Millat al-Islam

Chapter 51 · 60 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Adh-Dhariyat in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah Adh-Dhariyat (1246 reciters)

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

وَٱلذَّٰرِيَٰتِ ذَرۡوًا ١Pali mphepo imene imamwaza fumbi فَٱلۡحَٰمِلَٰتِ وِقۡرًا ٢Ndi mitambo imene ili yolemedwa ndi madzi فَٱلۡجَٰرِيَٰتِ يُسۡرًا ٣Ndi zombo zimene zimayenda mosavutika ndi mwabata فَٱلۡمُقَسِّمَٰتِ أَمۡرًا ٤Ndipo pali iwo amene amagawa madalitso ndi chilolezo chathu إِنَّمَا تُوعَدُونَ لَصَادِقٌ ٥Ndithudi chimene mwalonjezedwa, ndithudi, ndi choona وَإِنَّ ٱلدِّينَ لَوَٰقِعٌ ٦Ndithudi chiweruzo chidzakwaniritsidwa وَٱلسَّمَآءِ ذَاتِ ٱلۡحُبُكِ ٧Pali kumwamba kumene kuli njira zambiri إِنَّكُمۡ لَفِي قَوۡلٍ مُّخۡتَلِفٍ ٨Ndithudi inu muli ndi maganizo osiyana يُؤۡفَكُ عَنۡهُ مَنۡ أُفِكَ ٩Amene abwezedwa ku icho ndiye amene wabwezedwa قُتِلَ ٱلۡخَرَّٰصُونَ ١٠wotembereredwa akhale amene amanama ٱلَّذِينَ هُمۡ فِي غَمۡرَةٍ سَاهُونَ ١١Amene akutidwa ndi kusamvera يَسۡـَٔلُونَ أَيَّانَ يَوۡمُ ٱلدِّينِ ١٢Iwo amafunsa kuti, “Kodi tsiku lachiweruzo lidzadza liti?” يَوۡمَ هُمۡ عَلَى ٱلنَّارِ يُفۡتَنُونَ ١٣Tsiku limene iwo adzaweruzidwa ndi kuponyedwa ku Zariat 559 moto ذُوقُواْ فِتۡنَتَكُمۡ هَٰذَا ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تَسۡتَعۡجِلُونَ ١٤Lawani chilango chanu! Ichi ndicho chimene munali kufuna kuti chidze msanga إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي جَنَّٰتٍ وَعُيُونٍ ١٥Ndithudi iwo amene amalewa machimo adzakhala m’minda imene ili ndi a kasupe ءَاخِذِينَ مَآ ءَاتَىٰهُمۡ رَبُّهُمۡۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَبۡلَ ذَٰلِكَ مُحۡسِنِينَ ١٦Kulandira zimene Ambuye wawo awapatsa. Ndithudi kale iwo anali kuchita zinthu zabwino كَانُواْ قَلِيلًا مِّنَ ٱلَّيۡلِ مَا يَهۡجَعُونَ ١٧Iwo anali kugona nthawi yochepa usiku وَبِٱلۡأَسۡحَارِ هُمۡ يَسۡتَغۡفِرُونَ ١٨Ndipo m’bandakucha anali kupempha chikhululukiro وَفِيٓ أَمۡوَٰلِهِمۡ حَقٌّ لِّلسَّآئِلِ وَٱلۡمَحۡرُومِ ١٩Ndipo mu chuma chawo mudali gawo limene linali kuperekedwa kwa anthu opempha ndi osowa وَفِي ٱلۡأَرۡضِ ءَايَٰتٌ لِّلۡمُوقِنِينَ ٢٠Ndipo m’dziko muli zizindikiro kwa iwo okhulupirira وَفِيٓ أَنفُسِكُمۡۚ أَفَلَا تُبۡصِرُونَ ٢١Ndi mizimu yanu kodi simungaone وَفِي ٱلسَّمَآءِ رِزۡقُكُمۡ وَمَا تُوعَدُونَ ٢٢Ndipo kumwamba ndiko kuli chakudya chanu ndi zimene muli kulonjezedwa فَوَرَبِّ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِ إِنَّهُۥ لَحَقٌّ مِّثۡلَ مَآ أَنَّكُمۡ تَنطِقُونَ ٢٣Ndiye, pali Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chimenechi ndi cholinga ndi choonadi chomwe inu mumayankhula هَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ ضَيۡفِ إِبۡرَٰهِيمَ ٱلۡمُكۡرَمِينَ ٢٤Kodi udamva nkhani ya alendo olemekezeka a Abrahamu إِذۡ دَخَلُواْ عَلَيۡهِ فَقَالُواْ سَلَٰمًاۖ قَالَ سَلَٰمٌ قَوۡمٌ مُّنكَرُونَ ٢٥Pamene iwo adadza kwa iye, iwo adati, “Mtendere.” Ndipo iye adati, “Mtendere.” Ndipo iye adati, “Inu ndinu alendo kwa ine.” فَرَاغَ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ فَجَآءَ بِعِجۡلٍ سَمِينٍ ٢٦Ndipo iye atapita ku banja lake adabweretsa nyama ya ng’ombe yowotcha فَقَرَّبَهُۥٓ إِلَيۡهِمۡ قَالَ أَلَا تَأۡكُلُونَ ٢٧Motero iye adadza nayo kwa iwo nati, “Kodi simufuna kudya?” فَأَوۡجَسَ مِنۡهُمۡ خِيفَةًۖ قَالُواْ لَا تَخَفۡۖ وَبَشَّرُوهُ بِغُلَٰمٍ عَلِيمٍ ٢٨Motero iye adayamba kuchita mantha mu mtima mwake. Ndipo iwo adati, “Usaope.” Ndipo iwo adamuuza nkhani yabwino yakubadwa kwa mwana wamwamuna yemwe adzakhala wanzeru kwambiri فَأَقۡبَلَتِ ٱمۡرَأَتُهُۥ فِي صَرَّةٍ فَصَكَّتۡ وَجۡهَهَا وَقَالَتۡ عَجُوزٌ عَقِيمٌ ٢٩Ndipo mkazi wake adadza modzichepetsa ndipo adamenya pa mphumi pake nati, “Nkhalamba yaikazi yosaberekapo!” قَالُواْ كَذَٰلِكِ قَالَ رَبُّكِۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡحَكِيمُ ٱلۡعَلِيمُ ٣٠Iwo adati, “Ngakhale ndi choncho, Ambuye wako wayankhula. Iye ndi wodzala ndi luntha ndiponso nzeru.”

Juz 27

۞ قَالَ فَمَا خَطۡبُكُمۡ أَيُّهَا ٱلۡمُرۡسَلُونَ ٣١Iye adati, “Kodi inu Atumwi uthenga wanu ndi wotani?” قَالُوٓاْ إِنَّآ أُرۡسِلۡنَآ إِلَىٰ قَوۡمٍ مُّجۡرِمِينَ ٣٢Iwo adati, “Ife tatumidwa kwa anthu ochimwa.” لِنُرۡسِلَ عَلَيۡهِمۡ حِجَارَةً مِّن طِينٍ ٣٣“Kuti tigwetse pa iwo miyala yamakande.” مُّسَوَّمَةً عِندَ رَبِّكَ لِلۡمُسۡرِفِينَ ٣٤“Idakonzedwa ndi Ambuye wako kudza kwa anthu oswa malamulo.” فَأَخۡرَجۡنَا مَن كَانَ فِيهَا مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٣٥Ndipo Ife tidatulutsa anthu okhulupirira amene adali momwemo فَمَا وَجَدۡنَا فِيهَا غَيۡرَ بَيۡتٍ مِّنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ ٣٦Koma sitidapezemo mabanja a Chisilamu kupatula banja limodzi lokha basi وَتَرَكۡنَا فِيهَآ ءَايَةً لِّلَّذِينَ يَخَافُونَ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَلِيمَ ٣٧Ndipo Ife tidasiyamo chizindikiro kwa iwo amene amaopa chilango chowawa وَفِي مُوسَىٰٓ إِذۡ أَرۡسَلۡنَٰهُ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ بِسُلۡطَٰنٍ مُّبِينٍ ٣٨Ndi mwa Mose. Pamene tidamutumiza kwa Farawo ndi zizindikiro zooneka فَتَوَلَّىٰ بِرُكۡنِهِۦ وَقَالَ سَٰحِرٌ أَوۡ مَجۡنُونٌ ٣٩Koma Farawo adakana pamodzi ndi mafumu ake nati, “Ndiwe munthu wamatsenga kapena munthu wa misala.” فَأَخَذۡنَٰهُ وَجُنُودَهُۥ فَنَبَذۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡيَمِّ وَهُوَ مُلِيمٌ ٤٠Motero tidamugwira pamodzi ndi gulu la asirikali ake ndi kuwamiza onse m’nyanja pamene iye ndiye adali wolakwa وَفِي عَادٍ إِذۡ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمُ ٱلرِّيحَ ٱلۡعَقِيمَ ٤١Ndipo mwa a Aad pamene tidawatumizira mphepo yoononga مَا تَذَرُ مِن شَيۡءٍ أَتَتۡ عَلَيۡهِ إِلَّا جَعَلَتۡهُ كَٱلرَّمِيمِ ٤٢Imene sidasiye chilichonse chimene idalimbana nacho kupatula kuchiononga ndi kuchisandutsa phulusa وَفِي ثَمُودَ إِذۡ قِيلَ لَهُمۡ تَمَتَّعُواْ حَتَّىٰ حِينٍ ٤٣Ndipo mwa anthu a Thamoud. Pamene adauzidwa kuti, “Basangalalani kanthawi kochepa.” فَعَتَوۡاْ عَنۡ أَمۡرِ رَبِّهِمۡ فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّٰعِقَةُ وَهُمۡ يَنظُرُونَ ٤٤Koma iwo adaphwanya lamulo la Ambuye wawo mwamwano, kotero mabingu adawaononga iwo ali kuona فَمَا ٱسۡتَطَٰعُواْ مِن قِيَامٍ وَمَا كَانُواْ مُنتَصِرِينَ ٤٥Kotero iwo adalibe mphamvu zodzuka kapena zodzitetezera وَقَوۡمَ نُوحٍ مِّن قَبۡلُۖ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمًا فَٰسِقِينَ ٤٦Ndi anthu a Nowa iwo asanadze. Ndithudi iwo adali anthu oswa malamulo وَٱلسَّمَآءَ بَنَيۡنَٰهَا بِأَيۡيْدٍ وَإِنَّا لَمُوسِعُونَ ٤٧Ife tidakonza kumwamba mwamphamvu ndiponso mwaluso. Ndipo, ndithudi, ndife amene timapanga kukula kwa mlengalenga وَٱلۡأَرۡضَ فَرَشۡنَٰهَا فَنِعۡمَ ٱلۡمَٰهِدُونَ ٤٨Ndipo dziko, tidamwaza. Kodi ndife omwaza bwino bwanji وَمِن كُلِّ شَيۡءٍ خَلَقۡنَا زَوۡجَيۡنِ لَعَلَّكُمۡ تَذَكَّرُونَ ٤٩Ndipo zonse zimene tidalenga tidazilenga ziwiriziwiri kuti mukhoza kukumbukira فَفِرُّوٓاْ إِلَى ٱللَّهِۖ إِنِّي لَكُم مِّنۡهُ نَذِيرٌ مُّبِينٌ ٥٠Kotero thawirani kwa Mulungu. Ndithudi Ine ndine mchenjezi wooneka kwa inu wochokera kwa Iye وَلَا تَجۡعَلُواْ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَۖ إِنِّي لَكُم مِّنۡهُ نَذِيرٌ مُّبِينٌ ٥١Ndipo musapange fano kukhala lopembedzedwa pamodzi ndi Mulungu. Ndithudi ine ndine mchenjezi wooneka kwa inu wochokera kwa Iye كَذَٰلِكَ مَآ أَتَى ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا قَالُواْ سَاحِرٌ أَوۡ مَجۡنُونٌ ٥٢Chimodzimodzi palibe Mtumwi amene adadza kwa anthu amene sadamunenere mawu ofanana monga akuti: “Wamatsenga kapena munthu wopenga!” أَتَوَاصَوۡاْ بِهِۦۚ بَلۡ هُمۡ قَوۡمٌ طَاغُونَ ٥٣Kodi uwu ndi mwambo umene akhala ali kusiyirana wina ndi mnzake? Iyayi, iwo ndi anthu amene ali kuswa malamulo mopyola muyeso فَتَوَلَّ عَنۡهُمۡ فَمَآ أَنتَ بِمَلُومٍ ٥٤Kotero uwaleke chifukwa iwe ulibe mlandu وَذَكِّرۡ فَإِنَّ ٱلذِّكۡرَىٰ تَنفَعُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٥٥Ndipo kumbutsa chifukwa chikumbutso chimathandiza anthu okhulupirira وَمَا خَلَقۡتُ ٱلۡجِنَّ وَٱلۡإِنسَ إِلَّا لِيَعۡبُدُونِ ٥٦Ndipo Ine ndidalenga majini ndi anthu kuti azindipembedza Ine مَآ أُرِيدُ مِنۡهُم مِّن رِّزۡقٍ وَمَآ أُرِيدُ أَن يُطۡعِمُونِ ٥٧Ine sindiwapempha chakudya ndipo sindiwafunsa kuti azindidyetsa Ine إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلرَّزَّاقُ ذُو ٱلۡقُوَّةِ ٱلۡمَتِينُ ٥٨Ndithudi ndi Mulungu yekha amene amapereka chakudya chonse, Mwini mphamvu zonse ndi wolimba kwambiri فَإِنَّ لِلَّذِينَ ظَلَمُواْ ذَنُوبًا مِّثۡلَ ذَنُوبِ أَصۡحَٰبِهِمۡ فَلَا يَسۡتَعۡجِلُونِ ٥٩Ndithudi anthu onse olakwa adzalandira gawo longa limene anzawo olakwa akale adalandira, kotero asandifunse Ine kuchita mofulumira فَوَيۡلٌ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن يَوۡمِهِمُ ٱلَّذِي يُوعَدُونَ ٦٠Kotero tsoka kwa onse osakhulupirira kuchokera ku tsiku lomwe iwo alonjezedwa

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.