بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَجَعَلَ ٱلظُّلُمَٰتِ وَٱلنُّورَۖ ثُمَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِرَبِّهِمۡ يَعۡدِلُونَ ١Kuyamikidwa ndi kwa Mulungu amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi kukhazikitsa mdima ndi kuwala, komabe anthu osakhulupirira amakhazikitsa milungu ina kuti ndi yolingana ndi Ambuye wawo هُوَ ٱلَّذِي خَلَقَكُم مِّن طِينٍ ثُمَّ قَضَىٰٓ أَجَلًاۖ وَأَجَلٌ مُّسَمًّى عِندَهُۥۖ ثُمَّ أَنتُمۡ تَمۡتَرُونَ ٢Iye ndiye amene adakulengani inu kuchokera ku dothi ndipo Iye adakhazikitsa nthawi. Ndipo Iye adakhazikitsanso nthawi ina, komabe inu mumakaika وَهُوَ ٱللَّهُ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَفِي ٱلۡأَرۡضِ يَعۡلَمُ سِرَّكُمۡ وَجَهۡرَكُمۡ وَيَعۡلَمُ مَا تَكۡسِبُونَ ٣Iye ndi Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi. Iye amadziwa zonse zimene mumabisa ndi zonse zimene mumaulula. Ndipo amadziwa zimene mumachita وَمَا تَأۡتِيهِم مِّنۡ ءَايَةٍ مِّنۡ ءَايَٰتِ رَبِّهِمۡ إِلَّا كَانُواْ عَنۡهَا مُعۡرِضِينَ ٤Ndipo chizindikiro sichidza kwa iwo kuchokera ku zizindikiro za Ambuye wawo, chimene iwo amachivomereza فَقَدۡ كَذَّبُواْ بِٱلۡحَقِّ لَمَّا جَآءَهُمۡ فَسَوۡفَ يَأۡتِيهِمۡ أَنۢبَٰٓؤُاْ مَا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ ٥Ndithudi iwo adakana choonadi pamene chidadza kwa iwo; koma kudzadza kwa iwo nkhani za zimene adali kuchita chipongwe أَلَمۡ يَرَوۡاْ كَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِن قَبۡلِهِم مِّن قَرۡنٍ مَّكَّنَّٰهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ مَا لَمۡ نُمَكِّن لَّكُمۡ وَأَرۡسَلۡنَا ٱلسَّمَآءَ عَلَيۡهِم مِّدۡرَارًا وَجَعَلۡنَا ٱلۡأَنۡهَٰرَ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهِمۡ فَأَهۡلَكۡنَٰهُم بِذُنُوبِهِمۡ وَأَنشَأۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِمۡ قَرۡنًا ءَاخَرِينَ ٦Kodi iwo sadaone kuti kodi ndi mibadwo ingati, iwo asanabadwe, imene Ife tidawononga imene tidakhazikitsa pa dziko kukhala ya mphamvu kwambiri kuposa inu? Ndipo timawatumizira mvula yochuluka kuchokera kumwamba ndi kuipanga mitsinje yamadzi kuyenda pansi pawo. Komabe tidawawononga chifukwa cha machimo awo ndipo tidalenganso, pambuyo pa iwo, mibadwo ina وَلَوۡ نَزَّلۡنَا عَلَيۡكَ كِتَٰبًا فِي قِرۡطَاسٍ فَلَمَسُوهُ بِأَيۡدِيهِمۡ لَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا سِحۡرٌ مُّبِينٌ ٧Ngakhale Ife tikadakutumizira iwe uthenga wolembedwa kale papepala kuti alikhudze ndi manja awo, anthu osakhulupirira akadanena kuti: “Ichi si china ayi koma matsenga enieni.” وَقَالُواْ لَوۡلَآ أُنزِلَ عَلَيۡهِ مَلَكٌۖ وَلَوۡ أَنزَلۡنَا مَلَكًا لَّقُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ ثُمَّ لَا يُنظَرُونَ ٨Iwo adati: Kodi ndi chifukwa chiyani mngelo sadatumizidwe kwa iye? Ife tikadatumiza mngelo, nkhani ikanaweruzidwa nthawi yomweyo, ndipo sakadapatsidwa mpata وَلَوۡ جَعَلۡنَٰهُ مَلَكًا لَّجَعَلۡنَٰهُ رَجُلًا وَلَلَبَسۡنَا عَلَيۡهِم مَّا يَلۡبِسُونَ ٩Ndipo ngati Ife tikadamupanga iye kukhala mngelo, ndithudi Ife tikadamupanga iye kuti azioneka ngati munthu ndipo tikadawasokoneza ndi zimene iwo adasokonezeka nazo kale وَلَقَدِ ٱسۡتُهۡزِئَ بِرُسُلٍ مِّن قَبۡلِكَ فَحَاقَ بِٱلَّذِينَ سَخِرُواْ مِنۡهُم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ ١٠Ndipo, ndithudi, Atumwi ena adasekedwa iwe usadadze, koma amene anali kuwaseka anazungulilidwa ndi zinthu zomwe iwo anali kuseka قُلۡ سِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ ثُمَّ ٱنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُكَذِّبِينَ ١١Nena: “Yendani pa dziko lapansi ndipo muone mapeto a anthu amene anakana choonadi.” قُل لِّمَن مَّا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ قُل لِّلَّهِۚ كَتَبَ عَلَىٰ نَفۡسِهِ ٱلرَّحۡمَةَۚ لَيَجۡمَعَنَّكُمۡ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ لَا رَيۡبَ فِيهِۚ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ فَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ ١٢Nena: “Kodi mwini wa chilichonse chimene chili kumwamba ndi dziko lapansi ndani?” Nena: “Mwini wake ndi Mulungu” ndipo Iye adadzilamula yekha kuti azionetsa chifundo. Ndipo, ndithudi, Iye adzakusonkhanitsani nonse pa tsiku la kuuka kwa akufa, tsiku lopanda chikaiko. Iwo amene asochera sadzakhulupirira ۞ وَلَهُۥ مَا سَكَنَ فِي ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِۚ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ ١٣Ndipo zake ndi zonse zimene zimapezeka usiku ndi usana ndipo Iye ndi Wakumva ndi Wozindikira قُلۡ أَغَيۡرَ ٱللَّهِ أَتَّخِذُ وَلِيًّا فَاطِرِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَهُوَ يُطۡعِمُ وَلَا يُطۡعَمُۗ قُلۡ إِنِّيٓ أُمِرۡتُ أَنۡ أَكُونَ أَوَّلَ مَنۡ أَسۡلَمَۖ وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ ١٤Nena: “Kodi ine nditenge wina aliyense osati Mulungu kuti akhale Mtetezi wanga, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi? Iye ndiye amene amadyetsa pamene Iye sadyetsedwa.” Nena: “Ndithudi ine ndalamulidwa kukhala woyamba wa anthu ogonjera kwa Mulungu.” Iwe usadzakhale mmodzi wa iwo amene amapembedza mafano قُلۡ إِنِّيٓ أَخَافُ إِنۡ عَصَيۡتُ رَبِّي عَذَابَ يَوۡمٍ عَظِيمٍ ١٥Nena: “Ine ndikuopa, ngati nditanyoza Ambuye wanga, chilango cha tsiku lalikulu.” مَّن يُصۡرَفۡ عَنۡهُ يَوۡمَئِذٍ فَقَدۡ رَحِمَهُۥۚ وَذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡمُبِينُ ١٦Aliyense amene adzapulumutsidwa ku mazunzo a tsiku limeneli adzakhala atalandira chifundo cha Mulungu. Kumeneko ndiko kudzakhala kupambana kwenikweni koonekeratu وَإِن يَمۡسَسۡكَ ٱللَّهُ بِضُرٍّ فَلَا كَاشِفَ لَهُۥٓ إِلَّا هُوَۖ وَإِن يَمۡسَسۡكَ بِخَيۡرٍ فَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ قَدِيرٌ ١٧Ndipo ngati Mulungu akupatsa mavuto, palibe wina amene angachotse mavutowo koma Iye yekha; ndipo ngati Iye akupatsa zinthu zabwino, Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse وَهُوَ ٱلۡقَاهِرُ فَوۡقَ عِبَادِهِۦۚ وَهُوَ ٱلۡحَكِيمُ ٱلۡخَبِيرُ ١٨Iye ali ndi mphamvu pa akapolo ake ndipo Iye ndiye Wanzeru ndi Wodziwa zonse قُلۡ أَيُّ شَيۡءٍ أَكۡبَرُ شَهَٰدَةًۖ قُلِ ٱللَّهُۖ شَهِيدُۢ بَيۡنِي وَبَيۡنَكُمۡۚ وَأُوحِيَ إِلَيَّ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانُ لِأُنذِرَكُم بِهِۦ وَمَنۢ بَلَغَۚ أَئِنَّكُمۡ لَتَشۡهَدُونَ أَنَّ مَعَ ٱللَّهِ ءَالِهَةً أُخۡرَىٰۚ قُل لَّآ أَشۡهَدُۚ قُلۡ إِنَّمَا هُوَ إِلَٰهٌ وَٰحِدٌ وَإِنَّنِي بَرِيٓءٌ مِّمَّا تُشۡرِكُونَ ١٩Nena: “Kodi ndi chiani chili chachikulu mu umboni?” Nena: “Mulungu ndiye mboni pakati pa ine ndi inu. Buku la Korani lavumbulutsidwa kwa ine kuti ndikuchenjezeni inu ndi ena onse amene angalandire chivumbulutsochi. Kodi inu mungachitire umboni kuti pali milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni?” Nena: “Ine sindingaikire umboni pa nkhani yotere.” Nena: “Iye ndi Mulungu mmodzi yekha. Ndipo, ndithudi, ine ndili kutali ndi milungu imene inu muli kupembedza powonjezera pa Iye.” ٱلَّذِينَ ءَاتَيۡنَٰهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ يَعۡرِفُونَهُۥ كَمَا يَعۡرِفُونَ أَبۡنَآءَهُمُۘ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ فَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ ٢٠Kwa iwo amene tidawapatsa Buku amamudziwa Iye mongamomweamadziwiraanaawo. Komaiwoameneataya mizimu yawo sadzakhulupirira وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا أَوۡ كَذَّبَ بِـَٔايَٰتِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلظَّٰلِمُونَ ٢١Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu kapena amakana chivumbulutso chake? Ndithudi anthu ochita zoipa sadzapambana ayi وَيَوۡمَ نَحۡشُرُهُمۡ جَمِيعًا ثُمَّ نَقُولُ لِلَّذِينَ أَشۡرَكُوٓاْ أَيۡنَ شُرَكَآؤُكُمُ ٱلَّذِينَ كُنتُمۡ تَزۡعُمُونَ ٢٢Ndipo patsiku limene tidzawasonkhanitsa onse pamodzi, Ife tidzati kwa anthu opembedza mafano: “Kodi ali kuti mafano anu aja munkawadalira?” ثُمَّ لَمۡ تَكُن فِتۡنَتُهُمۡ إِلَّآ أَن قَالُواْ وَٱللَّهِ رَبِّنَا مَا كُنَّا مُشۡرِكِينَ ٢٣Iwo sadzawiringula china chili chonse koma adzati: “Tilumbira pali Mulungu, Ambuye wathu, kuti ife sitidali kupembedza mafano pambali pa Mulungu.” ٱنظُرۡ كَيۡفَ كَذَبُواْ عَلَىٰٓ أَنفُسِهِمۡۚ وَضَلَّ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ ٢٤Taona mmene iwo ali kudzinamiza okha! Koma bodza limene anali kupeka lidzawathawira وَمِنۡهُم مَّن يَسۡتَمِعُ إِلَيۡكَۖ وَجَعَلۡنَا عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ أَكِنَّةً أَن يَفۡقَهُوهُ وَفِيٓ ءَاذَانِهِمۡ وَقۡرًاۚ وَإِن يَرَوۡاْ كُلَّ ءَايَةٍ لَّا يُؤۡمِنُواْ بِهَاۖ حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءُوكَ يُجَٰدِلُونَكَ يَقُولُ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّآ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ ٢٥Ndipo ena a iwo amamvetsera kwa iwe koma Ife taika tchingo m’mitima mwawo kuti asazindikire ndipo m’makutu mwawo ndi mogontha ndipo iwo akaona chizindikiro chilichonse, sadzachikhulupirira ndipo amadza kwa iwe kudzatsutsana nawe, ndipo anthu osakhulupirira amati: “Ichi sichina chilichonse koma nkhani zopeka za anthu a kale kwambiri.” وَهُمۡ يَنۡهَوۡنَ عَنۡهُ وَيَنۡـَٔوۡنَ عَنۡهُۖ وَإِن يُهۡلِكُونَ إِلَّآ أَنفُسَهُمۡ وَمَا يَشۡعُرُونَ ٢٦Ndipo iwo amaletsa anthu kumvetsera ndipo iwo amadzitalikitsa okha kwa Iye. Koma iwo sali kuwononga wina aliyense koma akudziononga okha. Koma iwo sazindikira وَلَوۡ تَرَىٰٓ إِذۡ وُقِفُواْ عَلَى ٱلنَّارِ فَقَالُواْ يَٰلَيۡتَنَا نُرَدُّ وَلَا نُكَذِّبَ بِـَٔايَٰتِ رَبِّنَا وَنَكُونَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٢٧Koma iwe ukadawaona pamene iwo adzaimitsidwe moyandikira moto! Iwo adzati: “Zikadakhala kuti tinabwezedwa! Ife sitikadakana chivumbulutso cha Ambuye wathu ndipo tikadakakhala anthu okhulupirira.” بَلۡ بَدَا لَهُم مَّا كَانُواْ يُخۡفُونَ مِن قَبۡلُۖ وَلَوۡ رُدُّواْ لَعَادُواْ لِمَا نُهُواْ عَنۡهُ وَإِنَّهُمۡ لَكَٰذِبُونَ ٢٨Koma zonse zimene adali kuzibisa kale zidzaonekera poyera kwa iwo. Komabe akadabwezedwa, iwo akadakabwerera ku zinthu zimene adaletsedwa. Ndithudi iwo ndi anthu a bodza وَقَالُوٓاْ إِنۡ هِيَ إِلَّا حَيَاتُنَا ٱلدُّنۡيَا وَمَا نَحۡنُ بِمَبۡعُوثِينَ ٢٩Iwo adanenetsa kuti: “Kulibenso moyo wina uliwonse kupatula moyo wathu wadziko lapansi ndiponso ife sitidzaukitsidwa kwa akufa.” وَلَوۡ تَرَىٰٓ إِذۡ وُقِفُواْ عَلَىٰ رَبِّهِمۡۚ قَالَ أَلَيۡسَ هَٰذَا بِٱلۡحَقِّۚ قَالُواْ بَلَىٰ وَرَبِّنَاۚ قَالَ فَذُوقُواْ ٱلۡعَذَابَ بِمَا كُنتُمۡ تَكۡفُرُونَ ٣٠Ndipo iwe ukadawaona pamene ali kusonkhanitsidwa kuima pamaso pa Ambuye wawo! Iye adzati: “Kodi izi sizoona?” Iwo adzayankha: “Ndi zoona pali Ambuye wathu.” Ndipo Iye adzati: “Motero lawani chilango chifukwa inu simunali okhulupilira.” قَدۡ خَسِرَ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِلِقَآءِ ٱللَّهِۖ حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَتۡهُمُ ٱلسَّاعَةُ بَغۡتَةً قَالُواْ يَٰحَسۡرَتَنَا عَلَىٰ مَا فَرَّطۡنَا فِيهَا وَهُمۡ يَحۡمِلُونَ أَوۡزَارَهُمۡ عَلَىٰ ظُهُورِهِمۡۚ أَلَا سَآءَ مَا يَزِرُونَ ٣١Ndithudi iwo ndi olephera kwambiri amene amakana kuti adzakumana ndi Ambuye wawo mpaka pamene ola loopsa lidza pa iwo mwadzidzidzi ndipo iwo adzafuula kuti: “Kalanga ife tidali kunyalanyaza kwambiri!” Iwo adzanyamula katundu wawo pa misana yawo ndipo zoipa kwambirizimeneadzasenza وَمَا ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَآ إِلَّا لَعِبٌ وَلَهۡوٌۖ وَلَلدَّارُ ٱلۡأٓخِرَةُ خَيۡرٌ لِّلَّذِينَ يَتَّقُونَۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ ٣٢Ndipomoyowapadzikolino lapansi siuli kanthu konse koma masewera ndi nthabwala. Koma yabwino kwambiri ndi nyumba m’moyo umene uli nkudza kwa amene amaopa. Kodi simungazindikire قَدۡ نَعۡلَمُ إِنَّهُۥ لَيَحۡزُنُكَ ٱلَّذِي يَقُولُونَۖ فَإِنَّهُمۡ لَا يُكَذِّبُونَكَ وَلَٰكِنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ يَجۡحَدُونَ ٣٣Ife tili kudziwa kuti zonse zimene ali kunena zili kukukhumudwitsa. Sindiwe amene iwo ali kukana koma ndi chivumbulutso cha Mulungu chimene anthu ochita zoipa ali kukana وَلَقَدۡ كُذِّبَتۡ رُسُلٌ مِّن قَبۡلِكَ فَصَبَرُواْ عَلَىٰ مَا كُذِّبُواْ وَأُوذُواْ حَتَّىٰٓ أَتَىٰهُمۡ نَصۡرُنَاۚ وَلَا مُبَدِّلَ لِكَلِمَٰتِ ٱللَّهِۚ وَلَقَدۡ جَآءَكَ مِن نَّبَإِيْ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ٣٤Ndithudi Atumwi ena adakanidwa iwe usanadze koma iwo adapilira pa zimene adali kuwanena ndipo anazunzidwa mpaka pamene thandizo lathu lidadza kwa iwo ndipo palibe amene angasinthe chilamulo cha Mulungu. Ndithudi iwe udamva nkhani zaAtumwi وَإِن كَانَ كَبُرَ عَلَيۡكَ إِعۡرَاضُهُمۡ فَإِنِ ٱسۡتَطَعۡتَ أَن تَبۡتَغِيَ نَفَقًا فِي ٱلۡأَرۡضِ أَوۡ سُلَّمًا فِي ٱلسَّمَآءِ فَتَأۡتِيَهُم بِـَٔايَةٍۚ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَجَمَعَهُمۡ عَلَى ٱلۡهُدَىٰۚ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡجَٰهِلِينَ ٣٥Ngati uona kuti kukana kwawo kwanyanya ndipo kuti sungathe kupirira, peza ngati ungathe, njira yapansi pa nthaka kapena makwerero oti ukwere kumwamba, kuti ukhoza kuwabweretsera chizindikiro. Ngati Mulungu akadafuna, Iye akadawasonkhanitsa onse ku chilangizo choona ndipo iwe usakhale mmodzi wa mbuli ۞ إِنَّمَا يَسۡتَجِيبُ ٱلَّذِينَ يَسۡمَعُونَۘ وَٱلۡمَوۡتَىٰ يَبۡعَثُهُمُ ٱللَّهُ ثُمَّ إِلَيۡهِ يُرۡجَعُونَ ٣٦Ndi okhawo amene amamva, amene adzapindula koma anthu akufa Mulungu adzawadzutsa kwa akufa ndipo kwa Iye adzabwerera وَقَالُواْ لَوۡلَا نُزِّلَ عَلَيۡهِ ءَايَةٌ مِّن رَّبِّهِۦۚ قُلۡ إِنَّ ٱللَّهَ قَادِرٌ عَلَىٰٓ أَن يُنَزِّلَ ءَايَةً وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ ٣٧Iwo amafunsa: “Kodi ndi chifukwa chiyani chizindikiro sichinadze kwa iye kuchokera kwa Ambuye wake?” Nena: “Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu zotumiza chizindikiro koma ambiri a iwo sazindikira.” وَمَا مِن دَآبَّةٍ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا طَٰٓئِرٍ يَطِيرُ بِجَنَاحَيۡهِ إِلَّآ أُمَمٌ أَمۡثَالُكُمۚ مَّا فَرَّطۡنَا فِي ٱلۡكِتَٰبِ مِن شَيۡءٍۚ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّهِمۡ يُحۡشَرُونَ ٣٨Palibe chinthu cha moyo padziko lapansi kapena mbalame imene imauluka ndi mapiko ake awiri imene ndi zosiyana ndi inu. Ife sitidasiye china chilichonse m’Buku ndipo kwa Ambuye wawo iwo adzasonkhanitsidwa وَٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا صُمٌّ وَبُكۡمٌ فِي ٱلظُّلُمَٰتِۗ مَن يَشَإِ ٱللَّهُ يُضۡلِلۡهُ وَمَن يَشَأۡ يَجۡعَلۡهُ عَلَىٰ صِرَٰطٍ مُّسۡتَقِيمٍ ٣٩Koma iwo amene amakana zizindikiro zathu, ndi agonthi m’khutu ndi abububu mu mdima. Mulungu amasocheza aliyense amene Iye wamufuna ndipo amatsogolera, kunjira yoyenera, aliyense amene Iye wamufuna قُلۡ أَرَءَيۡتَكُمۡ إِنۡ أَتَىٰكُمۡ عَذَابُ ٱللَّهِ أَوۡ أَتَتۡكُمُ ٱلسَّاعَةُ أَغَيۡرَ ٱللَّهِ تَدۡعُونَ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ ٤٠Nena: “Ndiuzeni, ngati chilango cha Mulungu chitadza pa inu kapena ola loopsa lidza pa inu, kodi inu mudzapempha wina amene sali Mulungu kuti akuthandizeni inu? Yankhani ngati mukunena zoona.” بَلۡ إِيَّاهُ تَدۡعُونَ فَيَكۡشِفُ مَا تَدۡعُونَ إِلَيۡهِ إِن شَآءَ وَتَنسَوۡنَ مَا تُشۡرِكُونَ ٤١Iyayi! Ndi kwa Iye yekha kumene inu mumapempha ndipo ngati Iye atafuna akhoza kukuchotserani zovuta zanu, ndipo inu pa nthawi imeneyi mudzaiwala mafano anu وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَآ إِلَىٰٓ أُمَمٍ مِّن قَبۡلِكَ فَأَخَذۡنَٰهُم بِٱلۡبَأۡسَآءِ وَٱلضَّرَّآءِ لَعَلَّهُمۡ يَتَضَرَّعُونَ ٤٢Ndithudi Ife tidatumiza, iwe usanadze, Atumwi ku mitundu ina. Ndipo tidawagwetsera umphawi, matenda ndi matsoka ochuluka kuti akhoza kukhulupilira modzichepetsa فَلَوۡلَآ إِذۡ جَآءَهُم بَأۡسُنَا تَضَرَّعُواْ وَلَٰكِن قَسَتۡ قُلُوبُهُمۡ وَزَيَّنَ لَهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ٤٣Nanga ndi chifukwa chiyani iwo sadadzichepetse pamene mazunzo athu adadza pa iwo? Koma mitima yawo inalimba ndipo Satana adawakongoletsera zochita zawo zoipa zimene adali kuchita فَلَمَّا نَسُواْ مَا ذُكِّرُواْ بِهِۦ فَتَحۡنَا عَلَيۡهِمۡ أَبۡوَٰبَ كُلِّ شَيۡءٍ حَتَّىٰٓ إِذَا فَرِحُواْ بِمَآ أُوتُوٓاْ أَخَذۡنَٰهُم بَغۡتَةً فَإِذَا هُم مُّبۡلِسُونَ ٤٤Ndipo pamene iwo adaiwala zimene adachenjezedwa, Ife tidawatsegulira makomo a zinthu zonse zabwino mpaka pamene adasangalala ndi zimene adapatsidwa, mwadzidzidzi Ife tidawalanga ndipo ah! Iwo adalowa m’chionongeko wokhumudwa ndi a chisoni فَقُطِعَ دَابِرُ ٱلۡقَوۡمِ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْۚ وَٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٤٥Motero maziko a anthu ochimwa adaonongedwa. Ndipo kutamandidwa konse kukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengezedwa zonse قُلۡ أَرَءَيۡتُمۡ إِنۡ أَخَذَ ٱللَّهُ سَمۡعَكُمۡ وَأَبۡصَٰرَكُمۡ وَخَتَمَ عَلَىٰ قُلُوبِكُم مَّنۡ إِلَٰهٌ غَيۡرُ ٱللَّهِ يَأۡتِيكُم بِهِۗ ٱنظُرۡ كَيۡفَ نُصَرِّفُ ٱلۡأٓيَٰتِ ثُمَّ هُمۡ يَصۡدِفُونَ ٤٦Nena: “Tandiuzani! Ngati Mulungu akadakulandani kumva kwanu, kuona kwanu ndi kutseka mitima yanu, kodi pali mulungu wina, woonjezera pa Mulungu weniweni, amene angakubwezereni zimenezi?” Taonani mmene tifotokozera chivumbulutso chathu ndi mmene iwo sakhulupilira قُلۡ أَرَءَيۡتَكُمۡ إِنۡ أَتَىٰكُمۡ عَذَابُ ٱللَّهِ بَغۡتَةً أَوۡ جَهۡرَةً هَلۡ يُهۡلَكُ إِلَّا ٱلۡقَوۡمُ ٱلظَّٰلِمُونَ ٤٧Nena: “Ndiuzeni, ngati chilango cha Mulungu chitadza mwadzidzidzi kapena moonekera, kodi ndani angaonongeke kupatula anthu ochita zoipa?” وَمَا نُرۡسِلُ ٱلۡمُرۡسَلِينَ إِلَّا مُبَشِّرِينَ وَمُنذِرِينَۖ فَمَنۡ ءَامَنَ وَأَصۡلَحَ فَلَا خَوۡفٌ عَلَيۡهِمۡ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ ٤٨Ndipo Ife sititumiza Aneneri koma kuti azikawauza anthu nkhani yabwino ndi kuwachenjeza. Motero aliyense amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, iye sadzakhala ndi nkhawa kapena kudandaula وَٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يَمَسُّهُمُ ٱلۡعَذَابُ بِمَا كَانُواْ يَفۡسُقُونَ ٤٩Koma iwo amene akana chivumbulutso chathu, chilango chidzawapeza chifukwa cha kusakhulupilira kwawo قُل لَّآ أَقُولُ لَكُمۡ عِندِي خَزَآئِنُ ٱللَّهِ وَلَآ أَعۡلَمُ ٱلۡغَيۡبَ وَلَآ أَقُولُ لَكُمۡ إِنِّي مَلَكٌۖ إِنۡ أَتَّبِعُ إِلَّا مَا يُوحَىٰٓ إِلَيَّۚ قُلۡ هَلۡ يَسۡتَوِي ٱلۡأَعۡمَىٰ وَٱلۡبَصِيرُۚ أَفَلَا تَتَفَكَّرُونَ ٥٠Nena: “Ine sindili kukuuzani kuti ndili ndi chuma cha Mulungu kapena kuti ndimadziwa zinthu zobisika kapena kuti ine ndine mngelo. Ine sinditsatira china chilichonse kupatula zokhazo zimene zavumbulutsidwa kwa ine.” Nena: “Kodi munthu wakhungu ndi munthu openya angafanane? Kodi inu simungaganize?” وَأَنذِرۡ بِهِ ٱلَّذِينَ يَخَافُونَ أَن يُحۡشَرُوٓاْ إِلَىٰ رَبِّهِمۡ لَيۡسَ لَهُم مِّن دُونِهِۦ وَلِيٌّ وَلَا شَفِيعٌ لَّعَلَّهُمۡ يَتَّقُونَ ٥١Ndipo achenjeze iwo amene amaopa kuti adzasonkhanitsidwa kupita kwa Ambuye wawo, amene alibe wowasamalira kapena mkhalapakati woonjezera pa Mulungu, kuti akhoza kumalewa zoipa وَلَا تَطۡرُدِ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ رَبَّهُم بِٱلۡغَدَوٰةِ وَٱلۡعَشِيِّ يُرِيدُونَ وَجۡهَهُۥۖ مَا عَلَيۡكَ مِنۡ حِسَابِهِم مِّن شَيۡءٍ وَمَا مِنۡ حِسَابِكَ عَلَيۡهِم مِّن شَيۡءٍ فَتَطۡرُدَهُمۡ فَتَكُونَ مِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ ٥٢Ndipo usawathamangitse iwo amene amapembedza Ambuye wawo m’mawa ndi madzulo pofuna chisangalalo chake. Iwe siudzaimbidwa mlandu pa zochita zawo ndipo nawonso sadzaimbidwa mlandu pa zochita zako ndipo ngati iwe uwathamangitsa udzakhala mugulu la anthu opanda chilungamo وَكَذَٰلِكَ فَتَنَّا بَعۡضَهُم بِبَعۡضٍ لِّيَقُولُوٓاْ أَهَٰٓؤُلَآءِ مَنَّ ٱللَّهُ عَلَيۡهِم مِّنۢ بَيۡنِنَآۗ أَلَيۡسَ ٱللَّهُ بِأَعۡلَمَ بِٱلشَّٰكِرِينَ ٥٣Motero ife tinawayesa ena a iwo kupyolera mwa anzawo kuti akhoza kunena, “Kodi awa ndiwo amene Mulungu wawadalitsa pakati pathu?” Kodi Mulungu sazindikira anthu othokoza وَإِذَا جَآءَكَ ٱلَّذِينَ يُؤۡمِنُونَ بِـَٔايَٰتِنَا فَقُلۡ سَلَٰمٌ عَلَيۡكُمۡۖ كَتَبَ رَبُّكُمۡ عَلَىٰ نَفۡسِهِ ٱلرَّحۡمَةَ أَنَّهُۥ مَنۡ عَمِلَ مِنكُمۡ سُوٓءَۢا بِجَهَٰلَةٍ ثُمَّ تَابَ مِنۢ بَعۡدِهِۦ وَأَصۡلَحَ فَأَنَّهُۥ غَفُورٌ رَّحِيمٌ ٥٤Ngati atadza kwa iwe anthu amene amakhulupirira chivumbulutso chathu. Nena, “Mtendere ukhale pa inu.” Ambuye wanu adadzilamulira yekha kuti azionetsa chisoni kuti ngati wina wa inu achita choipa chifukwa chosadziwa ndipo alapa pambuyo pake ndipo achita ntchito zabwino, ndithudi Iye ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha وَكَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ وَلِتَسۡتَبِينَ سَبِيلُ ٱلۡمُجۡرِمِينَ ٥٥Motero Ife timafotokoza chivulumbutso chathu poyera kuti njira ya anthu ochita zoipa ionekere poyera قُلۡ إِنِّي نُهِيتُ أَنۡ أَعۡبُدَ ٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِۚ قُل لَّآ أَتَّبِعُ أَهۡوَآءَكُمۡ قَدۡ ضَلَلۡتُ إِذًا وَمَآ أَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُهۡتَدِينَ ٥٦Nena, “Ine ndaletsedwa kupembedza milungu imene inumumaipembedzapowonjezerapa Mulungu.” Nena,“Ine sindidzatsatira zilakolako zanu zachabe. Ngati nditatero ndiye kuti ndasochera ndipo ine sindikhala mugulu la anthu otsogozedwa bwino.” قُلۡ إِنِّي عَلَىٰ بَيِّنَةٍ مِّن رَّبِّي وَكَذَّبۡتُم بِهِۦۚ مَا عِندِي مَا تَسۡتَعۡجِلُونَ بِهِۦٓۚ إِنِ ٱلۡحُكۡمُ إِلَّا لِلَّهِۖ يَقُصُّ ٱلۡحَقَّۖ وَهُوَ خَيۡرُ ٱلۡفَٰصِلِينَ ٥٧Nena, “Ine ndalandira umboni wokwana kuchokera kwa Ambuye wanga komabe inu muli kuukana. Ine ndilibe mphamvu yobweretsa msangamsanga chilango chimene mufuna. Chiweruzo chili m’manja mwa Mulungu yekha, Iye amanena zoona ndipo ndi yekhayo amene ali wabwino poweruza.” قُل لَّوۡ أَنَّ عِندِي مَا تَسۡتَعۡجِلُونَ بِهِۦ لَقُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ بَيۡنِي وَبَيۡنَكُمۡۗ وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِٱلظَّٰلِمِينَ ٥٨Nena, “Ine ndikadakhala nacho chimene mufuna mwamsanga msanga, mkangano wa pakati pa inu ndi ine ukadaweruzidwa kalekale koma Mulungu amadziwa anthu onse ochita zoipa.” ۞ وَعِندَهُۥ مَفَاتِحُ ٱلۡغَيۡبِ لَا يَعۡلَمُهَآ إِلَّا هُوَۚ وَيَعۡلَمُ مَا فِي ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِۚ وَمَا تَسۡقُطُ مِن وَرَقَةٍ إِلَّا يَعۡلَمُهَا وَلَا حَبَّةٍ فِي ظُلُمَٰتِ ٱلۡأَرۡضِ وَلَا رَطۡبٍ وَلَا يَابِسٍ إِلَّا فِي كِتَٰبٍ مُّبِينٍ ٥٩Iye ali ndi makiyi a zinthu zonse zobisika, palibe wina amene azidziwa koma Iye yekha. Iye amadziwa zonse zimene zili m’nthaka ndiponso m’nyanja; ndipo lisadagwe tsamba Iye amalidziwa. Palibe mbewu mu mdima wa nthaka kapena china chilichonse cha chiwisi kapena chouma koma zonsezo zidalembedwa mu Buku looneka bwino وَهُوَ ٱلَّذِي يَتَوَفَّىٰكُم بِٱلَّيۡلِ وَيَعۡلَمُ مَا جَرَحۡتُم بِٱلنَّهَارِ ثُمَّ يَبۡعَثُكُمۡ فِيهِ لِيُقۡضَىٰٓ أَجَلٌ مُّسَمًّىۖ ثُمَّ إِلَيۡهِ مَرۡجِعُكُمۡ ثُمَّ يُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ ٦٠Iye ndiye amene amachotsa mizimu yanu nthawi yausiku ndipo amadziwa zonse zimene mwachita masana ndipo amakudzutsani kuti mukwaniritse nthawi imene idaperekedwa pa moyo wanu ndipo pambuyo pake nonse mudzabwerera kwa Iye. Ndipo Iye adzakuuzani zonse zimene mumachita وَهُوَ ٱلۡقَاهِرُ فَوۡقَ عِبَادِهِۦۖ وَيُرۡسِلُ عَلَيۡكُمۡ حَفَظَةً حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَ أَحَدَكُمُ ٱلۡمَوۡتُ تَوَفَّتۡهُ رُسُلُنَا وَهُمۡ لَا يُفَرِّطُونَ ٦١Iye ndi wamphamvu pa akapolo ake ndipo amatumiza atetezi amene amakuyang’anirani inu mpaka pamene mmodzi wa inu imufikira imfa; Atumiki athu amachotsa moyo wake ndipo iwo sanyoza zimene alamulidwa ثُمَّ رُدُّوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ مَوۡلَىٰهُمُ ٱلۡحَقِّۚ أَلَا لَهُ ٱلۡحُكۡمُ وَهُوَ أَسۡرَعُ ٱلۡحَٰسِبِينَ ٦٢Ndipo iwo amabwerera kwa Mulungu, Ambuye wawo woona. Ndithudi Iye ndiye muweruzi ndipo Iye ndi wachangu powerengera zochita zanu قُلۡ مَن يُنَجِّيكُم مِّن ظُلُمَٰتِ ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِ تَدۡعُونَهُۥ تَضَرُّعًا وَخُفۡيَةً لَّئِنۡ أَنجَىٰنَا مِنۡ هَٰذِهِۦ لَنَكُونَنَّ مِنَ ٱلشَّٰكِرِينَ ٦٣Nena, “Kodi ndani amakupulumutsani m’mavuto a pa mtunda ndi a pa nyanja ndi pamene inu mumamupempha Iye modzichepetsa ndi mwamseri, ponena kuti: ‘Ngati Iye atipulumutsa ife pa mavuto awa, ndithudi, ife tidzakhala othokoza.” قُلِ ٱللَّهُ يُنَجِّيكُم مِّنۡهَا وَمِن كُلِّ كَرۡبٍ ثُمَّ أَنتُمۡ تُشۡرِكُونَ ٦٤Nena, “Mulungu amakupulumutsani inu ku zovuta izi ndi kumavuto ena onse, komabe inu mumapembedzabe mafano mowonjezera pa Iye.” قُلۡ هُوَ ٱلۡقَادِرُ عَلَىٰٓ أَن يَبۡعَثَ عَلَيۡكُمۡ عَذَابًا مِّن فَوۡقِكُمۡ أَوۡ مِن تَحۡتِ أَرۡجُلِكُمۡ أَوۡ يَلۡبِسَكُمۡ شِيَعًا وَيُذِيقَ بَعۡضَكُم بَأۡسَ بَعۡضٍۗ ٱنظُرۡ كَيۡفَ نُصَرِّفُ ٱلۡأٓيَٰتِ لَعَلَّهُمۡ يَفۡقَهُونَ ٦٥Nena, “Iye ali ndi mphamvu yotumiza chilango chake pa inu kuchokerapamutupanukapenapansipamapazianukapena kukugawani inu kukhala m’magulu a anthu osagwirizana ndi kukulawitsani mazunzo ochokera kwa anzanu. Taonani mmene timaonetsera poyera chivumbulutso chathu kuti akhale ozindikira.” وَكَذَّبَ بِهِۦ قَوۡمُكَ وَهُوَ ٱلۡحَقُّۚ قُل لَّسۡتُ عَلَيۡكُم بِوَكِيلٍ ٦٦Koma anthu ako alikana ili ngakhale lili choonadi chenicheni. Nena: “Ine sindine Msungi wanu ayi.” لِّكُلِّ نَبَإٍ مُّسۡتَقَرٌّۚ وَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ ٦٧Nkhani iliyonse ili ndi nthawi yake ndipo posachedwapa mudzazindikira وَإِذَا رَأَيۡتَ ٱلَّذِينَ يَخُوضُونَ فِيٓ ءَايَٰتِنَا فَأَعۡرِضۡ عَنۡهُمۡ حَتَّىٰ يَخُوضُواْ فِي حَدِيثٍ غَيۡرِهِۦۚ وَإِمَّا يُنسِيَنَّكَ ٱلشَّيۡطَٰنُ فَلَا تَقۡعُدۡ بَعۡدَ ٱلذِّكۡرَىٰ مَعَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ ٦٨Ndipo pamene iwe uwaona iwo amene amanyoza chivumbulutso chathu, usakhale nawo pamodzi mpaka pokhapokha akamba nkhani ina. Ngati satana akuiwalitsa, ndipo pambuyo pake ukumbukira usakhale mgulu la anthu ochita zoipa وَمَا عَلَى ٱلَّذِينَ يَتَّقُونَ مِنۡ حِسَابِهِم مِّن شَيۡءٍ وَلَٰكِن ذِكۡرَىٰ لَعَلَّهُمۡ يَتَّقُونَ ٦٩Iwo amene amaopa Mulungu alibe udindo pa iwo koma kungowakumbutsa kuti apewe kunyoza وَذَرِ ٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ دِينَهُمۡ لَعِبًا وَلَهۡوًا وَغَرَّتۡهُمُ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَاۚ وَذَكِّرۡ بِهِۦٓ أَن تُبۡسَلَ نَفۡسُۢ بِمَا كَسَبَتۡ لَيۡسَ لَهَا مِن دُونِ ٱللَّهِ وَلِيٌّ وَلَا شَفِيعٌ وَإِن تَعۡدِلۡ كُلَّ عَدۡلٍ لَّا يُؤۡخَذۡ مِنۡهَآۗ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ أُبۡسِلُواْ بِمَا كَسَبُواْۖ لَهُمۡ شَرَابٌ مِّنۡ حَمِيمٍ وَعَذَابٌ أَلِيمُۢ بِمَا كَانُواْ يَكۡفُرُونَ ٧٠Apewe iwo amene amasandutsa chipembedzo chawo kukhala masewera kapena nthabwala ndipo asokonezeka ndi zokoma za moyo wa dziko lapansi. Koma achenjeze ndi ilo kuti ungadzaonongeke mzimu wawo chifukwa cha zimene udachita pamene siudzakhala ndi wousamalira kapena kuwuteteza kupatula Mulungu, ndipo ngakhale iwo apereka chuma chopepesera, sichidzalandiridwa konse. Otere ndiwo amene aonongedwa chifukwa cha zimene anachita. Iwo adzalandira zakumwa zowira ndi chilango chowawa chifukwa cha zinthu zimene sadakhulupirire قُلۡ أَنَدۡعُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَنفَعُنَا وَلَا يَضُرُّنَا وَنُرَدُّ عَلَىٰٓ أَعۡقَابِنَا بَعۡدَ إِذۡ هَدَىٰنَا ٱللَّهُ كَٱلَّذِي ٱسۡتَهۡوَتۡهُ ٱلشَّيَٰطِينُ فِي ٱلۡأَرۡضِ حَيۡرَانَ لَهُۥٓ أَصۡحَٰبٌ يَدۡعُونَهُۥٓ إِلَى ٱلۡهُدَى ٱئۡتِنَاۗ قُلۡ إِنَّ هُدَى ٱللَّهِ هُوَ ٱلۡهُدَىٰۖ وَأُمِرۡنَا لِنُسۡلِمَ لِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٧١Nena, “Kodi ife tizipembedza ena powonjezera pa Mulungu amene sangathe kutithandiza kapena kutiwononga ndipo kodi ife tibwerere m’mbuyo pamene Mulungu watitsogolera? Monga ngati munthu amene alodzedwa ndi Satana, kumangoyenda uku ndi uku ngakhale kuti abwenzi ake ali kumuitana kuti atsatire njira yoyenera, ponena: Bwerani kuno?” Nena, “Ndithudi utsogoleri wa Mulungu ndiwo utsogoleri weniweni ndipo Ife talamulidwa kugonjera Mulungu Ambuye wa zolengedwa zonse.” وَأَنۡ أَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَٱتَّقُوهُۚ وَهُوَ ٱلَّذِيٓ إِلَيۡهِ تُحۡشَرُونَ ٧٢Ndi kuti muzipemphera moyenera, kumvera Mulungu ndi kumuopa Iye ndipo ndi kwa Iye kumene nonse mudzasonkhanitsidwa وَهُوَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِٱلۡحَقِّۖ وَيَوۡمَ يَقُولُ كُن فَيَكُونُۚ قَوۡلُهُ ٱلۡحَقُّۚ وَلَهُ ٱلۡمُلۡكُ يَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِۚ عَٰلِمُ ٱلۡغَيۡبِ وَٱلشَّهَٰدَةِۚ وَهُوَ ٱلۡحَكِيمُ ٱلۡخَبِيرُ ٧٣Iye ndiye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi ndipo patsikuli Iye adzati: “Khala” ndipo chidzakhala. Liwu lake ndi loonadi. Wake udzakhala Ufumu pa tsiku limene lipenga lidzaombedwa. Iye amadziwa zonse zosaoneka ndi zooneka. Iye ndi wanzeru ndi wodziwa zinthu zonse ۞ وَإِذۡ قَالَ إِبۡرَٰهِيمُ لِأَبِيهِ ءَازَرَ أَتَتَّخِذُ أَصۡنَامًا ءَالِهَةً إِنِّيٓ أَرَىٰكَ وَقَوۡمَكَ فِي ضَلَٰلٍ مُّبِينٍ ٧٤Ndi pamene Abrahamu adati kwa abambo ake a Uzar: “Kodi inu muzipembedza mafano ngati milungu yanu? Ndithudi ine ndili kuona kuti inu pamodzi ndi anthu anu mwasochera moonekera.” وَكَذَٰلِكَ نُرِيٓ إِبۡرَٰهِيمَ مَلَكُوتَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَلِيَكُونَ مِنَ ٱلۡمُوقِنِينَ ٧٥Motero tidamuonetsa Abrahamu Ufumu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi kuti akhale mmodzi wa wokhulupirira kweniweni فَلَمَّا جَنَّ عَلَيۡهِ ٱلَّيۡلُ رَءَا كَوۡكَبًاۖ قَالَ هَٰذَا رَبِّيۖ فَلَمَّآ أَفَلَ قَالَ لَآ أُحِبُّ ٱلۡأٓفِلِينَ ٧٦Ndipo pamene usiku udamukuta ndi mdima, iye adaona nyenyezi. Iye adati: “Iyo ndiyo Ambuye wanga.” Koma pamene iyo idalowa, iye adati: “Ine sindikonda zimene zimalowa.” فَلَمَّا رَءَا ٱلۡقَمَرَ بَازِغًا قَالَ هَٰذَا رَبِّيۖ فَلَمَّآ أَفَلَ قَالَ لَئِن لَّمۡ يَهۡدِنِي رَبِّي لَأَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلضَّآلِّينَ ٧٧Ndipo pamene iye adaona mwezi uli kutuluka, iye adati: “Uwo ndiwo Ambuye wanga.” Koma pamene iwo unalowa, Iye adati: “Ngati Ambuye wanga sanditsogolera ine, ndithudi, ine ndidzakhala m’gulu la anthu osochera.” فَلَمَّا رَءَا ٱلشَّمۡسَ بَازِغَةً قَالَ هَٰذَا رَبِّي هَٰذَآ أَكۡبَرُۖ فَلَمَّآ أَفَلَتۡ قَالَ يَٰقَوۡمِ إِنِّي بَرِيٓءٌ مِّمَّا تُشۡرِكُونَ ٧٨Ndipo pamene adaona dzuwa lili kutuluka, iye adati: “Ili ndilo Ambuye wanga. Ndipo ilo ndi lalikulu koposa.” Koma pamene ilo lidalowa, iye adati: “oh inu anthu anga! Ine ndatalikirana ndi zimene inu mukusakaniza popembedza Mulungu.” إِنِّي وَجَّهۡتُ وَجۡهِيَ لِلَّذِي فَطَرَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ حَنِيفًاۖ وَمَآ أَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ ٧٩Ndithudi ine ndayang’anitsa nkhope yanga kwa Iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Ine sindine mmodzi wa iwo opembedza mafano وَحَآجَّهُۥ قَوۡمُهُۥۚ قَالَ أَتُحَٰٓجُّوٓنِّي فِي ٱللَّهِ وَقَدۡ هَدَىٰنِۚ وَلَآ أَخَافُ مَا تُشۡرِكُونَ بِهِۦٓ إِلَّآ أَن يَشَآءَ رَبِّي شَيۡـًٔاۚ وَسِعَ رَبِّي كُلَّ شَيۡءٍ عِلۡمًاۚ أَفَلَا تَتَذَكَّرُونَ ٨٠Anthu ake adatsutsana naye ndipo iye adati: “Kodi inu mukutsutsana ndi ine za Mulungu pamene Iye wanditsogolera? Ndipo ine sindiopa mafano anu kupatula ngati Ambuye wanga atafuna chilichonse. Ambuye wanga amadziwa bwino chilichonse. Kodi inu simungakumbukire وَكَيۡفَ أَخَافُ مَآ أَشۡرَكۡتُمۡ وَلَا تَخَافُونَ أَنَّكُمۡ أَشۡرَكۡتُم بِٱللَّهِ مَا لَمۡ يُنَزِّلۡ بِهِۦ عَلَيۡكُمۡ سُلۡطَٰنًاۚ فَأَيُّ ٱلۡفَرِيقَيۡنِ أَحَقُّ بِٱلۡأَمۡنِۖ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ ٨١Ndipo kodi ine ndingaope bwanji milungu yanu yabodza pamene inuyo mulibe mantha pomapembedza mafano amene Mulungu sadakupatseniumboniwake? Kodindaniwamaguluawiriwa amene afuna chitetezo ngati inu mumadziwa?” ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَلَمۡ يَلۡبِسُوٓاْ إِيمَٰنَهُم بِظُلۡمٍ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمُ ٱلۡأَمۡنُ وَهُم مُّهۡتَدُونَ ٨٢Ndiwo amene ali okhulupirira ndipo sasakaniza chikhulupiriro chawo pochita ntchito zoipa, kwa iwo kuli mtendere ndipo ndi otsogozedwa وَتِلۡكَ حُجَّتُنَآ ءَاتَيۡنَٰهَآ إِبۡرَٰهِيمَ عَلَىٰ قَوۡمِهِۦۚ نَرۡفَعُ دَرَجَٰتٍ مَّن نَّشَآءُۗ إِنَّ رَبَّكَ حَكِيمٌ عَلِيمٌ ٨٣Chimenechi chinali chizindikiro chathu chimene tidamupatsa Abrahamu kuti agonjetsere anthu ake. Ife timakweza wina aliyense amene tamufuna. Ndithudi Ambuye wako ndi wanzeru ndi wodziwa zinthu zonse وَوَهَبۡنَا لَهُۥٓ إِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَۚ كُلًّا هَدَيۡنَاۚ وَنُوحًا هَدَيۡنَا مِن قَبۡلُۖ وَمِن ذُرِّيَّتِهِۦ دَاوُۥدَ وَسُلَيۡمَٰنَ وَأَيُّوبَ وَيُوسُفَ وَمُوسَىٰ وَهَٰرُونَۚ وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ ٨٤Ndipo tidamupatsa iye Isake ndi Yakobo, aliyense tidamutsogolera ndipo iye asanadze, tidatsogolera Nowa ndipo pakati pa adzukulu wake Davide, Solomoni, Yobu, Yosefe, Mose ndi Aroni. Motero ndi mmene timalipirira anthu ochita abwino وَزَكَرِيَّا وَيَحۡيَىٰ وَعِيسَىٰ وَإِلۡيَاسَۖ كُلٌّ مِّنَ ٱلصَّٰلِحِينَ ٨٥Ndi Zakariya, Yohane, Yesu, ndi Eliya, aliyense adali wangwiro وَإِسۡمَٰعِيلَ وَٱلۡيَسَعَ وَيُونُسَ وَلُوطًاۚ وَكُلًّا فَضَّلۡنَا عَلَى ٱلۡعَٰلَمِينَ ٨٦Ndi Ishimayeli, Elisa, Yona ndi Loti, onsewa tidawalemekeza pakati pa zolengedwa zonse وَمِنۡ ءَابَآئِهِمۡ وَذُرِّيَّٰتِهِمۡ وَإِخۡوَٰنِهِمۡۖ وَٱجۡتَبَيۡنَٰهُمۡ وَهَدَيۡنَٰهُمۡ إِلَىٰ صِرَٰطٍ مُّسۡتَقِيمٍ ٨٧Ndiponso makolo awo, ana awo, ndi abale awo Ife tidawasankha ndi kuwatsogolera ku njira yoyenera ذَٰلِكَ هُدَى ٱللَّهِ يَهۡدِي بِهِۦ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦۚ وَلَوۡ أَشۡرَكُواْ لَحَبِطَ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ٨٨Ichi ndi chilangizo cha Mulungu chimene amalangiza nacho aliyense amene wamufuna wa akapolo ake. Koma iwo akadatumikira milungu ina yoonjezera pa Mulungu m’modzi, ntchito zawo zonse zikadakhala zopanda phindu أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ ءَاتَيۡنَٰهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡحُكۡمَ وَٱلنُّبُوَّةَۚ فَإِن يَكۡفُرۡ بِهَا هَٰٓؤُلَآءِ فَقَدۡ وَكَّلۡنَا بِهَا قَوۡمًا لَّيۡسُواْ بِهَا بِكَٰفِرِينَ ٨٩Awa ndi amene tidawapatsa Buku, chiweruzo ndi Utumwi. Koma ngati awa sakhulupirira mwa ilo, ndithudi Ife tawapatsa iwo amene akhulupilira mwa ilo أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ هَدَى ٱللَّهُۖ فَبِهُدَىٰهُمُ ٱقۡتَدِهۡۗ قُل لَّآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ أَجۡرًاۖ إِنۡ هُوَ إِلَّا ذِكۡرَىٰ لِلۡعَٰلَمِينَ ٩٠Amenewa ndi anthu amene Mulungu adawatsogolera. Choncho tsatira chilangizo chawo. Nena, “Ine sindili kufuna malipiro chifukwa cha ntchito iyi ayi. Ili ndi chenjezo kwa zolengedwa zonse.” وَمَا قَدَرُواْ ٱللَّهَ حَقَّ قَدۡرِهِۦٓ إِذۡ قَالُواْ مَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ عَلَىٰ بَشَرٍ مِّن شَيۡءٍۗ قُلۡ مَنۡ أَنزَلَ ٱلۡكِتَٰبَ ٱلَّذِي جَآءَ بِهِۦ مُوسَىٰ نُورًا وَهُدًى لِّلنَّاسِۖ تَجۡعَلُونَهُۥ قَرَاطِيسَ تُبۡدُونَهَا وَتُخۡفُونَ كَثِيرًاۖ وَعُلِّمۡتُم مَّا لَمۡ تَعۡلَمُوٓاْ أَنتُمۡ وَلَآ ءَابَآؤُكُمۡۖ قُلِ ٱللَّهُۖ ثُمَّ ذَرۡهُمۡ فِي خَوۡضِهِمۡ يَلۡعَبُونَ ٩١Iwo sadapereke ulemu woyenera Mulungu pamene adati: “Mulungu sadavumbulutse china chilichonse kwa munthu.” Nena, “Kodi ndani yemwe adavumbulutsa Buku limene Mose anabwera nalo, muuni ndi chilangizo kwa anthu onse; amene mwalemba pa mipukutu ya mapepala, kuulula zina ndi kubisa zambiri? Ndipo mudaphunzitsidwa zimene inu ndiponso makolo anu sadazidziwe ndi kale lomwe.” Nena: “Ndi Mulungu.” Ndipo asiye okha kuti abadzisangalatsa ndi nkhani zopusa وَهَٰذَا كِتَٰبٌ أَنزَلۡنَٰهُ مُبَارَكٌ مُّصَدِّقُ ٱلَّذِي بَيۡنَ يَدَيۡهِ وَلِتُنذِرَ أُمَّ ٱلۡقُرَىٰ وَمَنۡ حَوۡلَهَاۚ وَٱلَّذِينَ يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ يُؤۡمِنُونَ بِهِۦۖ وَهُمۡ عَلَىٰ صَلَاتِهِمۡ يُحَافِظُونَ ٩٢Ndipo ili ndi Buku lodalitsika limene tavumbulutsa, kuchitira umboni zimene zinadza ilo lisadadze kuti uchenjeze Mzinda wa Makka ndi iwo amene amakhala mouzungulira. Iwo amene ali ndi chikhulupiriro mu zamoyo umene uli nkudza amakhulupirira ilo ndipo amasamala kwambiri m’mapemphero awo وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا أَوۡ قَالَ أُوحِيَ إِلَيَّ وَلَمۡ يُوحَ إِلَيۡهِ شَيۡءٌ وَمَن قَالَ سَأُنزِلُ مِثۡلَ مَآ أَنزَلَ ٱللَّهُۗ وَلَوۡ تَرَىٰٓ إِذِ ٱلظَّٰلِمُونَ فِي غَمَرَٰتِ ٱلۡمَوۡتِ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ بَاسِطُوٓاْ أَيۡدِيهِمۡ أَخۡرِجُوٓاْ أَنفُسَكُمُۖ ٱلۡيَوۡمَ تُجۡزَوۡنَ عَذَابَ ٱلۡهُونِ بِمَا كُنتُمۡ تَقُولُونَ عَلَى ٱللَّهِ غَيۡرَ ٱلۡحَقِّ وَكُنتُمۡ عَنۡ ءَايَٰتِهِۦ تَسۡتَكۡبِرُونَ ٩٣Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa iye amene amapeka bodza lonamizira Mulungu kapena amati: “Ine ndalandira chibvumbulutso pamene sichidavumbulutsidwe kwa iye chilichonse?” Kapena munthu amene amati: “Ine ndikhoza kuvumbulutsa zinthu zofanana ndi zimene Mulungu wavumbulutsa?” Ndipo iwe ukadangoona anthu ochimwa pamene ali kufa ndi pamene angelo ali kutambasula manja awo akuti: “Perekani mizimu yanu. Inu mudzalipidwa mphotho yochititsa manyazi lero chifukwa cha zimene munali kunena zabodza zokhudza Mulungu. Ndiponso inu munali kukana chivumbulutso chake mwa mwano.” وَلَقَدۡ جِئۡتُمُونَا فُرَٰدَىٰ كَمَا خَلَقۡنَٰكُمۡ أَوَّلَ مَرَّةٍ وَتَرَكۡتُم مَّا خَوَّلۡنَٰكُمۡ وَرَآءَ ظُهُورِكُمۡۖ وَمَا نَرَىٰ مَعَكُمۡ شُفَعَآءَكُمُ ٱلَّذِينَ زَعَمۡتُمۡ أَنَّهُمۡ فِيكُمۡ شُرَكَٰٓؤُاْۚ لَقَد تَّقَطَّعَ بَيۡنَكُمۡ وَضَلَّ عَنكُم مَّا كُنتُمۡ تَزۡعُمُونَ ٩٤“Ndipo, ndithudi, mwadza kwa Ife, nokha, monga momwe tidakulengerani inu poyamba. Inu mwasiya zonse zimene tidakupatsani kumbuyo kwanu. Ndiponso Ife sitili kuona pamodzi ndi inu zimene mumazipembedza, zija mumati ndi zofanana ndi Mulungu. Tsopano ubale wonse umene umakugwirizitsani waduka ndipo zonse zimene mumaziganizira kuti zingakuthandizeni zakuthawirani.” ۞ إِنَّ ٱللَّهَ فَالِقُ ٱلۡحَبِّ وَٱلنَّوَىٰۖ يُخۡرِجُ ٱلۡحَيَّ مِنَ ٱلۡمَيِّتِ وَمُخۡرِجُ ٱلۡمَيِّتِ مِنَ ٱلۡحَيِّۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُۖ فَأَنَّىٰ تُؤۡفَكُونَ ٩٥Ndithudi! Ndi Mulungu amene amasiyanitsa mbewu ndi khoko lake kuti imere. Iye amatulutsa chamoyo kuchokera mu chakufa ndipo ndiye amatulutsa chakufa kuchokera ku chamoyo. Ameneyo ndiye Mulungu, nanga ndi chifukwa chiyani mukusokera kusiya choonadi فَالِقُ ٱلۡإِصۡبَاحِ وَجَعَلَ ٱلَّيۡلَ سَكَنًا وَٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَ حُسۡبَانًاۚ ذَٰلِكَ تَقۡدِيرُ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡعَلِيمِ ٩٦Iye amadzetsa kuwala kwa m’mawa. Ndipo Iye waika usiku kuti ikhale nthawi yopumula, dzuwa ndi mwezi kuti zikhale zothandiza kuwerengera; umenewo ndiwo muyeso wa Mwini mphamvu zonse ndi wodziwa chilichonse وَهُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلنُّجُومَ لِتَهۡتَدُواْ بِهَا فِي ظُلُمَٰتِ ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِۗ قَدۡ فَصَّلۡنَا ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٍ يَعۡلَمُونَ ٩٧Iye ndiye amene adakulengerani nyenyezi kuti zizikutsogolerani mu mdima wa pa mtunda ndi pa nyanja. Ife tafotokoza chivumbulutso kwa anthu odziwa kwambiri وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَنشَأَكُم مِّن نَّفۡسٍ وَٰحِدَةٍ فَمُسۡتَقَرٌّ وَمُسۡتَوۡدَعٌۗ قَدۡ فَصَّلۡنَا ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٍ يَفۡقَهُونَ ٩٨Iye ndiye amene adakulengani inu kuchokera kwa munthu mmodzi ndipo adakupatsani malo okhalamo ndi osungidwa. Ife ndithudi tafotokoza chivumbulutso chathu kwa anthu omvetsa وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءً فَأَخۡرَجۡنَا بِهِۦ نَبَاتَ كُلِّ شَيۡءٍ فَأَخۡرَجۡنَا مِنۡهُ خَضِرًا نُّخۡرِجُ مِنۡهُ حَبًّا مُّتَرَاكِبًا وَمِنَ ٱلنَّخۡلِ مِن طَلۡعِهَا قِنۡوَانٌ دَانِيَةٌ وَجَنَّٰتٍ مِّنۡ أَعۡنَابٍ وَٱلزَّيۡتُونَ وَٱلرُّمَّانَ مُشۡتَبِهًا وَغَيۡرَ مُتَشَٰبِهٍۗ ٱنظُرُوٓاْ إِلَىٰ ثَمَرِهِۦٓ إِذَآ أَثۡمَرَ وَيَنۡعِهِۦٓۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكُمۡ لَأٓيَٰتٍ لِّقَوۡمٍ يُؤۡمِنُونَ ٩٩Iye ndiye amene amatumiza mvula kuchokera kumwamba ndipo ndi iyo, Ife timameretsa mbewu zosiyana siyana ndipo kuchokera ku izo timatulutsa mphesi za ziwisi zimene zimabereka mbeu mothinana. Ndipo kuchokera ku mitengo ya tende kumadza zipatso za tende zotsika pansi, minda ya mphesa ndi mitengo ya mafuta ya azitona, chimanga cha chizungu, zipatso zofanana koma zosiyanasiyana. Taonani zipatso zake pamene zili kubereka, kukhwima ndi kumapsya. Ndithudi! Mu izi muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira وَجَعَلُواْ لِلَّهِ شُرَكَآءَ ٱلۡجِنَّ وَخَلَقَهُمۡۖ وَخَرَقُواْ لَهُۥ بَنِينَ وَبَنَٰتِۭ بِغَيۡرِ عِلۡمٍۚ سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يَصِفُونَ ١٠٠Komabe iwo amasankha majini kukhala milungu kuonjezera pa Mulungu weniweni ngakhale kuti Iye ndiye amene anawalenga ndipo amamunamizira Mulungu kuti ali ndi ana amuna ndi akazi. Ulemerero ukhale kwa Iye! Alemekezeke Iye koposa zonse zimene akunena بَدِيعُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ أَنَّىٰ يَكُونُ لَهُۥ وَلَدٌ وَلَمۡ تَكُن لَّهُۥ صَٰحِبَةٌۖ وَخَلَقَ كُلَّ شَيۡءٍۖ وَهُوَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٌ ١٠١Iye ndi Namalenga wa kumwamba ndi dziko lapansi. Kodi Iye angakhale ndi ana bwanji pamene Iye alibe mkazi? Iye adalenga zinthu zonse ndipo amadziwa chilichonse ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمۡۖ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ خَٰلِقُ كُلِّ شَيۡءٍ فَٱعۡبُدُوهُۚ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ وَكِيلٌ ١٠٢Ameneyo ndiye Mulungu, Ambuye wanu. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha, Namalenga wa zinthu zonse. Motero mpembedzeni Iye yekha. Iye ndiye wosamalira zinthu zonse لَّا تُدۡرِكُهُ ٱلۡأَبۡصَٰرُ وَهُوَ يُدۡرِكُ ٱلۡأَبۡصَٰرَۖ وَهُوَ ٱللَّطِيفُ ٱلۡخَبِيرُ ١٠٣Palibe amene angamuone Iye koma Iye amaona chili chonse. Iye ndiye wachifundo ndipo amadziwa zonse قَدۡ جَآءَكُم بَصَآئِرُ مِن رَّبِّكُمۡۖ فَمَنۡ أَبۡصَرَ فَلِنَفۡسِهِۦۖ وَمَنۡ عَمِيَ فَعَلَيۡهَاۚ وَمَآ أَنَا۠ عَلَيۡكُم بِحَفِيظٍ ١٠٤Ndithudi zizindikiro zonse zadza kwa inu kuchokera kwa Ambuye wanu ndipo aliyense amene aona zidzampindulira iye koma aliyense amene ali wakhungu adzalephera yekha ndipo ine sindine wokuyang’anirani وَكَذَٰلِكَ نُصَرِّفُ ٱلۡأٓيَٰتِ وَلِيَقُولُواْ دَرَسۡتَ وَلِنُبَيِّنَهُۥ لِقَوۡمٍ يَعۡلَمُونَ ١٠٥Motero Ife timafotokoza chivumbulutso chathu, kuti iwo anene kuti: “Iwe waphunzira” ndi kuti tifotokoze momveka kwa anthu ozindikira ٱتَّبِعۡ مَآ أُوحِيَ إِلَيۡكَ مِن رَّبِّكَۖ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ وَأَعۡرِضۡ عَنِ ٱلۡمُشۡرِكِينَ ١٠٦Choncho tsatira zonse zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha ndipo alewe anthu osakhulupirira وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ مَآ أَشۡرَكُواْۗ وَمَا جَعَلۡنَٰكَ عَلَيۡهِمۡ حَفِيظًاۖ وَمَآ أَنتَ عَلَيۡهِم بِوَكِيلٍ ١٠٧Ngati Mulungu akadafuna, iwo sakanapembedza mafano. Ndipo Ife sitikadakusankha iwe kukhala owayang’anira ayi ndiponso iwe sindiwe wowasamalira wawo وَلَا تَسُبُّواْ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ فَيَسُبُّواْ ٱللَّهَ عَدۡوَۢا بِغَيۡرِ عِلۡمٍۗ كَذَٰلِكَ زَيَّنَّا لِكُلِّ أُمَّةٍ عَمَلَهُمۡ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّهِم مَّرۡجِعُهُمۡ فَيُنَبِّئُهُم بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ١٠٨Ndipo musatukwane iwo amene amapembedza mafano poonjezera pa Mulungu weniweni kuti mwina iwo angathe kutukwana Mulungu molakwa ndi mwa umbuli. Motero tazipanga zochita zawo kukhala zosangalatsa ndipo ndi kwa Ambuye wawo kumene onse adzabwerera ndipo Iye adzawauza iwo zonse zimene anali kuchita وَأَقۡسَمُواْ بِٱللَّهِ جَهۡدَ أَيۡمَٰنِهِمۡ لَئِن جَآءَتۡهُمۡ ءَايَةٌ لَّيُؤۡمِنُنَّ بِهَاۚ قُلۡ إِنَّمَا ٱلۡأٓيَٰتُ عِندَ ٱللَّهِۖ وَمَا يُشۡعِرُكُمۡ أَنَّهَآ إِذَا جَآءَتۡ لَا يُؤۡمِنُونَ ١٠٩Ndipo iwo amalumbira pali Mulungu motsindika kuti ngati chizindikiro chitaperekedwa kwa iwo, iwo adzachikhulupirira. Nena, “Ndithudi zizindikiro zonse zili ndi Mulungu ndipo kodi inu mungadziwe bwanji ngati chidza kwa iwo kuti iwo sadzachikhulupirira?” وَنُقَلِّبُ أَفۡـِٔدَتَهُمۡ وَأَبۡصَٰرَهُمۡ كَمَا لَمۡ يُؤۡمِنُواْ بِهِۦٓ أَوَّلَ مَرَّةٍ وَنَذَرُهُمۡ فِي طُغۡيَٰنِهِمۡ يَعۡمَهُونَ ١١٠Ndipo Ife tidzatembenuza mitima yawo ndi maso awo monga mmene adakana kukhulupirira nthawi yoyamba ndipo Ife tidzawasiya mukusochera kwawo akusowa chochita
۞ وَلَوۡ أَنَّنَا نَزَّلۡنَآ إِلَيۡهِمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ وَكَلَّمَهُمُ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَحَشَرۡنَا عَلَيۡهِمۡ كُلَّ شَيۡءٍ قُبُلًا مَّا كَانُواْ لِيُؤۡمِنُوٓاْ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ يَجۡهَلُونَ ١١١Ngakhale Ife tikadawatumizira iwo angelo ndi kupangaanthuakufakutialankhulenawondikusonkhanitsa zinthu zonse pamaso pawo, iwo sakadakhulupirirabe pokhapokha ngati Mulungu afuna koma ambiri a iwo ndi anthu osadziwa وَكَذَٰلِكَ جَعَلۡنَا لِكُلِّ نَبِيٍّ عَدُوًّا شَيَٰطِينَ ٱلۡإِنسِ وَٱلۡجِنِّ يُوحِي بَعۡضُهُمۡ إِلَىٰ بَعۡضٍ زُخۡرُفَ ٱلۡقَوۡلِ غُرُورًاۚ وَلَوۡ شَآءَ رَبُّكَ مَا فَعَلُوهُۖ فَذَرۡهُمۡ وَمَا يَفۡتَرُونَ ١١٢Kotero Ife tidakhazikitsa mdani kwa Mtumwi aliyense. A satana amene ali pakati pa anthu ndi majini, amene amauzana wina ndi mnzake mawu okoma ndiponso a chinyengo. Koma Ambuye wako akadafuna, iwo sakadachita zotero ayi motero asiyeni okha ndi zimene akupeka وَلِتَصۡغَىٰٓ إِلَيۡهِ أَفۡـِٔدَةُ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ وَلِيَرۡضَوۡهُ وَلِيَقۡتَرِفُواْ مَا هُم مُّقۡتَرِفُونَ ١١٣Kuti mitima ya anthu amene sakhulupirira m’moyo umene uli nkudza ipendekere kuzolankhula zawo ndipo kuti azitsatira zimene apeka okha ndi kumasangalala kuti mwina akhoza kuchita zimene ali nkuchita أَفَغَيۡرَ ٱللَّهِ أَبۡتَغِي حَكَمًا وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَنزَلَ إِلَيۡكُمُ ٱلۡكِتَٰبَ مُفَصَّلًاۚ وَٱلَّذِينَ ءَاتَيۡنَٰهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ يَعۡلَمُونَ أَنَّهُۥ مُنَزَّلٌ مِّن رَّبِّكَ بِٱلۡحَقِّۖ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُمۡتَرِينَ ١١٤“Kodi ine ndifune wina woweruza oposa Mulungu pamene ndiye amene adavumbulutsa Korani kwa inu ndi malamulo ofotokozedwa bwino?” Iwo amene tidawapatsa Mau athu amadziwa kuti lidavumbulutsidwa kuchokera kwa Ambuye wako mwa choonadi. Motero usakhale mmodzi wa anthu okaika وَتَمَّتۡ كَلِمَتُ رَبِّكَ صِدۡقًا وَعَدۡلًاۚ لَّا مُبَدِّلَ لِكَلِمَٰتِهِۦۚ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ ١١٥Ndipo Mau a Ambuye wako akwaniritsidwa moona ndi mwachilungamo. Palibe wina amene angasinthe Mau ake. Iye amamva ndipo ndi wozindikira chili chonse وَإِن تُطِعۡ أَكۡثَرَ مَن فِي ٱلۡأَرۡضِ يُضِلُّوكَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِۚ إِن يَتَّبِعُونَ إِلَّا ٱلظَّنَّ وَإِنۡ هُمۡ إِلَّا يَخۡرُصُونَ ١١٦Ndipo ngati iwe umvera zonena za anthu ambiri apa dziko lapansi iwo adzakusocheza ku njira ya Mulungu. Iwo satsatira chilichonse koma nkhani zongoganiza chabe ndipo sachita china chilichonse koma kunama إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعۡلَمُ مَن يَضِلُّ عَن سَبِيلِهِۦۖ وَهُوَ أَعۡلَمُ بِٱلۡمُهۡتَدِينَ ١١٧Ndithudi Ambuye wako! Ndiye amene amadziwa anthu onse amene amasochera ku njira yake ndiponso Iye amadziwa iwo amene atsogozedwa bwino bwino فَكُلُواْ مِمَّا ذُكِرَ ٱسۡمُ ٱللَّهِ عَلَيۡهِ إِن كُنتُم بِـَٔايَٰتِهِۦ مُؤۡمِنِينَ ١١٨Motero idyani nyama yokhayo imene yaphedwa m’dzina la Mulungu ngati inu mukhulupiriradi mu chivumbulutso chake وَمَا لَكُمۡ أَلَّا تَأۡكُلُواْ مِمَّا ذُكِرَ ٱسۡمُ ٱللَّهِ عَلَيۡهِ وَقَدۡ فَصَّلَ لَكُم مَّا حَرَّمَ عَلَيۡكُمۡ إِلَّا مَا ٱضۡطُرِرۡتُمۡ إِلَيۡهِۗ وَإِنَّ كَثِيرًا لَّيُضِلُّونَ بِأَهۡوَآئِهِم بِغَيۡرِ عِلۡمٍۚ إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعۡلَمُ بِٱلۡمُعۡتَدِينَ ١١٩Kodi inu simungadye bwanji nyama imene yaphedwa m’dzina la Mulungu pamene Iye adaulula poyera zimene adakuletsani pokhapokha ngati mwasimidwa? Ndithudi ambiri amasochera potsatira zilako lako zawo mwa umbuli. Ndithudi Ambuye wako amadziwa onse oswa malamulo وَذَرُواْ ظَٰهِرَ ٱلۡإِثۡمِ وَبَاطِنَهُۥٓۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ يَكۡسِبُونَ ٱلۡإِثۡمَ سَيُجۡزَوۡنَ بِمَا كَانُواْ يَقۡتَرِفُونَ ١٢٠Pewa machimo oonekera kapena obisika. Ndithudi iwo amene amachita zoipa adzalangidwa chifukwa cha zoipa zawo وَلَا تَأۡكُلُواْ مِمَّا لَمۡ يُذۡكَرِ ٱسۡمُ ٱللَّهِ عَلَيۡهِ وَإِنَّهُۥ لَفِسۡقٌۗ وَإِنَّ ٱلشَّيَٰطِينَ لَيُوحُونَ إِلَىٰٓ أَوۡلِيَآئِهِمۡ لِيُجَٰدِلُوكُمۡۖ وَإِنۡ أَطَعۡتُمُوهُمۡ إِنَّكُمۡ لَمُشۡرِكُونَ ١٢١Musadye nyama iliyonse imene sidaphedwe m’dzina la Mulungu chifukwa kutero ndi kulakwa. Ndithudi a Satana amaphunzitsa anthu awo kuti azikangana ndi inu ndipo ngati inu muwamvera, ndithudi, nanunso mudzakhala opembedza mafano أَوَمَن كَانَ مَيۡتًا فَأَحۡيَيۡنَٰهُ وَجَعَلۡنَا لَهُۥ نُورًا يَمۡشِي بِهِۦ فِي ٱلنَّاسِ كَمَن مَّثَلُهُۥ فِي ٱلظُّلُمَٰتِ لَيۡسَ بِخَارِجٍ مِّنۡهَاۚ كَذَٰلِكَ زُيِّنَ لِلۡكَٰفِرِينَ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ١٢٢Kodi munthu amene adafa, ndipo tamuukitsa kwa akufa ndipo wapatsidwa kuwala kumene kukhoza kumutsogolera pakati pa anthu, angafanizidwe ndi iye amene ali kusochera mumdima umene sadzatulukamo? Chomwecho zimakongoletsedwa kwa anthu osakhulupirira zimene adali kuchita وَكَذَٰلِكَ جَعَلۡنَا فِي كُلِّ قَرۡيَةٍ أَكَٰبِرَ مُجۡرِمِيهَا لِيَمۡكُرُواْ فِيهَاۖ وَمَا يَمۡكُرُونَ إِلَّا بِأَنفُسِهِمۡ وَمَا يَشۡعُرُونَ ١٢٣Motero Ife tidakhazikitsa mu Mzinda uliwonse atsogoleri a anthu olakwa kwambiri amene amakonza njira zoswera malamulo m’kati mwa Mzindawo. Koma iwo amakonza njira zoti zibweretse chiwonongeko pa iwo eni ndipo iwo sadziwa وَإِذَا جَآءَتۡهُمۡ ءَايَةٌ قَالُواْ لَن نُّؤۡمِنَ حَتَّىٰ نُؤۡتَىٰ مِثۡلَ مَآ أُوتِيَ رُسُلُ ٱللَّهِۘ ٱللَّهُ أَعۡلَمُ حَيۡثُ يَجۡعَلُ رِسَالَتَهُۥۗ سَيُصِيبُ ٱلَّذِينَ أَجۡرَمُواْ صَغَارٌ عِندَ ٱللَّهِ وَعَذَابٌ شَدِيدُۢ بِمَا كَانُواْ يَمۡكُرُونَ ١٢٤Ndipo pamene zizindikiro ziwafikira iwo amati: “Ife sitidzakhulupirira mu ichi pokhapokha ngati tipatsidwa chimene Atumwi a Mulungu adapatsidwa.” Mulungu amadziwa bwino ndani amene akhoza kumupatsa uthenga wake. Kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi kochokera kwa Mulungu ndiponso chilango chowawa chidzadza pa anthu oipa chifukwa cha zimene anali kuchita فَمَن يُرِدِ ٱللَّهُ أَن يَهۡدِيَهُۥ يَشۡرَحۡ صَدۡرَهُۥ لِلۡإِسۡلَٰمِۖ وَمَن يُرِدۡ أَن يُضِلَّهُۥ يَجۡعَلۡ صَدۡرَهُۥ ضَيِّقًا حَرَجًا كَأَنَّمَا يَصَّعَّدُ فِي ٱلسَّمَآءِۚ كَذَٰلِكَ يَجۡعَلُ ٱللَّهُ ٱلرِّجۡسَ عَلَى ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ ١٢٥Ndipo aliyense amene Mulungu afuna kumutsogolera, Iye amatsegula mtima wake kuti akhale Msilamu ndipo aliyense amene Iye afuna kumusocheretsa, Iye amachititsa mtima wake kukhala opapatizika ndi ovutika ngati kuti akukwera kumwamba. Mmenemo ndi mmene Mulungu amaikira mkwiyo pa anthu osakhulupirira وَهَٰذَا صِرَٰطُ رَبِّكَ مُسۡتَقِيمًاۗ قَدۡ فَصَّلۡنَا ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٍ يَذَّكَّرُونَ ١٢٦Iyi ndi njira ya Ambuye wako, yoyenera. Ife tafotokoza chivumbulutso kwa anthu oganizira ۞ لَهُمۡ دَارُ ٱلسَّلَٰمِ عِندَ رَبِّهِمۡۖ وَهُوَ وَلِيُّهُم بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ١٢٧Kwa iwo kudzakhala nyumba ya mtendere imene ili ndi Ambuye wawo. Iye adzakhala Mtetezi wawo chifukwa cha zimene anali kuchita وَيَوۡمَ يَحۡشُرُهُمۡ جَمِيعًا يَٰمَعۡشَرَ ٱلۡجِنِّ قَدِ ٱسۡتَكۡثَرۡتُم مِّنَ ٱلۡإِنسِۖ وَقَالَ أَوۡلِيَآؤُهُم مِّنَ ٱلۡإِنسِ رَبَّنَا ٱسۡتَمۡتَعَ بَعۡضُنَا بِبَعۡضٍ وَبَلَغۡنَآ أَجَلَنَا ٱلَّذِيٓ أَجَّلۡتَ لَنَاۚ قَالَ ٱلنَّارُ مَثۡوَىٰكُمۡ خَٰلِدِينَ فِيهَآ إِلَّا مَا شَآءَ ٱللَّهُۚ إِنَّ رَبَّكَ حَكِيمٌ عَلِيمٌ ١٢٨Ndipo patsiku limene adzawasonkhanitsa onse, ndi kuti: “oh inu gulu la majini! Inu mudali kusokeletsa anthu mu unyinji wawo.” Ndipo anzawo ochokera m’gulu la anthu adzati: “Ambuye ife tidapindula kuchokera kwa wina ndi mnzake, koma tsopano tafika pa mapeto ya nthawi yathu imene mudatikhazikitsira ife.” Mulungu adzati: “Kumoto ndiko kumalo kwanu ndipo kumeneko mukakhala mpaka kalekale kufikira pamene Mulungu adzafuna.” Ndithudi Ambuye wako ndi Wanzeru ndi Wozindikira وَكَذَٰلِكَ نُوَلِّي بَعۡضَ ٱلظَّٰلِمِينَ بَعۡضَۢا بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ ١٢٩Ndipo motero ndi mmene timapangira anthu olakwa kuthandizana wina ndi mzake chifukwa cha zimene anali kuchita يَٰمَعۡشَرَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِ أَلَمۡ يَأۡتِكُمۡ رُسُلٌ مِّنكُمۡ يَقُصُّونَ عَلَيۡكُمۡ ءَايَٰتِي وَيُنذِرُونَكُمۡ لِقَآءَ يَوۡمِكُمۡ هَٰذَاۚ قَالُواْ شَهِدۡنَا عَلَىٰٓ أَنفُسِنَاۖ وَغَرَّتۡهُمُ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَا وَشَهِدُواْ عَلَىٰٓ أَنفُسِهِمۡ أَنَّهُمۡ كَانُواْ كَٰفِرِينَ ١٣٠Inu gulu la majini ndi anthu! “Kodi sikudadze kwa inu Atumwi a mtundu wanu amene adali kukuuzani za zizindikiro zanga ndi kuchenjeza za kukumana kwa tsiku lanuli?” Iwo adzayankha, “Ife tidzichitira umboni wodzitsutsa tokha.” Ndi moyo wa dziko lino lapansi umene udawanyenga. Ndipo iwo adzadzichitira umboni okha kuti iwo adali osakhulupirira ذَٰلِكَ أَن لَّمۡ يَكُن رَّبُّكَ مُهۡلِكَ ٱلۡقُرَىٰ بِظُلۡمٍ وَأَهۡلُهَا غَٰفِلُونَ ١٣١Ichi ndi chifukwa chakuti Ambuye wako samaononga Mizinda chifukwa cha zochita zawo, pamene anthu ake sadali kudziwa وَلِكُلٍّ دَرَجَٰتٌ مِّمَّا عَمِلُواْۚ وَمَا رَبُّكَ بِغَٰفِلٍ عَمَّا يَعۡمَلُونَ ١٣٢Kwa aliyense kudzaperekedwa gawo molingana ndi zimene adachita. Sikuti Ambuye wako sadziwa zimene iwo achita وَرَبُّكَ ٱلۡغَنِيُّ ذُو ٱلرَّحۡمَةِۚ إِن يَشَأۡ يُذۡهِبۡكُمۡ وَيَسۡتَخۡلِفۡ مِنۢ بَعۡدِكُم مَّا يَشَآءُ كَمَآ أَنشَأَكُم مِّن ذُرِّيَّةِ قَوۡمٍ ءَاخَرِينَ ١٣٣Ambuye wako ndi wolemera ndiponso ndi wachisoni ndipo ngati Iye afuna, akhoza kukuonongani ndi kuika m’malo mwanu ena amene Iye wafuna monga momwe Iye adakulengerani inu kuchokera ku mbeu ya anthu ena إِنَّ مَا تُوعَدُونَ لَأٓتٍۖ وَمَآ أَنتُم بِمُعۡجِزِينَ ١٣٤Ndithudi chimene inu mukulonjezedwa chidzachitika ndipo inu simungachizembe ayi قُلۡ يَٰقَوۡمِ ٱعۡمَلُواْ عَلَىٰ مَكَانَتِكُمۡ إِنِّي عَامِلٌۖ فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ مَن تَكُونُ لَهُۥ عَٰقِبَةُ ٱلدَّارِۚ إِنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلظَّٰلِمُونَ ١٣٥Nena, “oh anthu anga! Chitani chimene mungachite, ndithudi, nanenso ndili kuchita chimene ndimachita ndipo inu mudzadziwa kuti ndani wa ife amene adzakhala ndi mapeto abwino m’moyo umene uli nkudza. Ndithudi anthu olakwa sadzapambana.” وَجَعَلُواْ لِلَّهِ مِمَّا ذَرَأَ مِنَ ٱلۡحَرۡثِ وَٱلۡأَنۡعَٰمِ نَصِيبًا فَقَالُواْ هَٰذَا لِلَّهِ بِزَعۡمِهِمۡ وَهَٰذَا لِشُرَكَآئِنَاۖ فَمَا كَانَ لِشُرَكَآئِهِمۡ فَلَا يَصِلُ إِلَى ٱللَّهِۖ وَمَا كَانَ لِلَّهِ فَهُوَ يَصِلُ إِلَىٰ شُرَكَآئِهِمۡۗ سَآءَ مَا يَحۡكُمُونَ ١٣٦Ndipo iwo amaika pa mbali gawo la mbewu ndi gawo la ziweto kuti ndi za Mulungu ndipo amati: “Izi ndi za Mulungu pamene izi ndi za mafano athu.” Koma gawo limene amati ndi la mafano awo silifika kwa Mulungu ayi pamene gawo la Mulungu limafika lonse kwa mafano awo! Chiweruzo chawo ndi choipa kwambiri وَكَذَٰلِكَ زَيَّنَ لِكَثِيرٍ مِّنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ قَتۡلَ أَوۡلَٰدِهِمۡ شُرَكَآؤُهُمۡ لِيُرۡدُوهُمۡ وَلِيَلۡبِسُواْ عَلَيۡهِمۡ دِينَهُمۡۖ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ مَا فَعَلُوهُۖ فَذَرۡهُمۡ وَمَا يَفۡتَرُونَ ١٣٧Motero kwa anthu opembedza mafano, mafano awo adapangitsa kupha ana awo kukhala chinthu chokondweretsa ndi cholinga chakuti awawononge iwo ndi kuwasokonezera chipembedzo chawo. Koma ngati Mulungu akadafuna, iwo sakadachita choncho. Motero asiyeni okha ndi zimene akupeka وَقَالُواْ هَٰذِهِۦٓ أَنۡعَٰمٌ وَحَرۡثٌ حِجۡرٌ لَّا يَطۡعَمُهَآ إِلَّا مَن نَّشَآءُ بِزَعۡمِهِمۡ وَأَنۡعَٰمٌ حُرِّمَتۡ ظُهُورُهَا وَأَنۡعَٰمٌ لَّا يَذۡكُرُونَ ٱسۡمَ ٱللَّهِ عَلَيۡهَا ٱفۡتِرَآءً عَلَيۡهِۚ سَيَجۡزِيهِم بِمَا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ ١٣٨Potsatira zofuna zawo, iwo amati: “Nyama izi ndiponso mbewu izi ndi zoletsedwa ndipo palibe munthu amene adye kupatula okhawo amene tawaloleza.” Ndipo pali nyama zina zimene amaletsa anthu kuti asakwere kapena kugwira ntchito, ndi zina zimene satchulapo dzina la Mulungu komwe ndi kumunamizira Iye. Mulungu adzawalipira chifukwa cha mabodza awo amene amapeka وَقَالُواْ مَا فِي بُطُونِ هَٰذِهِ ٱلۡأَنۡعَٰمِ خَالِصَةٌ لِّذُكُورِنَا وَمُحَرَّمٌ عَلَىٰٓ أَزۡوَٰجِنَاۖ وَإِن يَكُن مَّيۡتَةً فَهُمۡ فِيهِ شُرَكَآءُۚ سَيَجۡزِيهِمۡ وَصۡفَهُمۡۚ إِنَّهُۥ حَكِيمٌ عَلِيمٌ ١٣٩Ndipo iwo amati: “Zam’kati zanyamazi ndi zololedwa kudyedwa ndi anthu athu amuna okha ndipo ndi zoletsedwa kwa anthu a akazi koma ngati izo zibadwa zakufa onse amagawana. Mulungu adzawalanga chifukwa cha zonse zimene amamunamizira Iye. Ndithudi Iye ndi Wanzeru ndi Wodziwa.” قَدۡ خَسِرَ ٱلَّذِينَ قَتَلُوٓاْ أَوۡلَٰدَهُمۡ سَفَهَۢا بِغَيۡرِ عِلۡمٍ وَحَرَّمُواْ مَا رَزَقَهُمُ ٱللَّهُ ٱفۡتِرَآءً عَلَى ٱللَّهِۚ قَدۡ ضَلُّواْ وَمَا كَانُواْ مُهۡتَدِينَ ١٤٠Ndithudi olephera ndi amene, adapha ana awo mwaumbuli ndipo adaletsa zinthu zimene Mulungu adawapatsa iwo ndi kupeka bodza lokhudza Mulungu. Ndithudi iwo asokera ndipo siotsogozedwa ۞ وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَنشَأَ جَنَّٰتٍ مَّعۡرُوشَٰتٍ وَغَيۡرَ مَعۡرُوشَٰتٍ وَٱلنَّخۡلَ وَٱلزَّرۡعَ مُخۡتَلِفًا أُكُلُهُۥ وَٱلزَّيۡتُونَ وَٱلرُّمَّانَ مُتَشَٰبِهًا وَغَيۡرَ مُتَشَٰبِهٍۚ كُلُواْ مِن ثَمَرِهِۦٓ إِذَآ أَثۡمَرَ وَءَاتُواْ حَقَّهُۥ يَوۡمَ حَصَادِهِۦۖ وَلَا تُسۡرِفُوٓاْۚ إِنَّهُۥ لَا يُحِبُّ ٱلۡمُسۡرِفِينَ ١٤١Iye ndiye amene amapanga minda ya mbewu za mitundumitundu; zoyanga ndi zosayanga, mitengo ya tende ndi mbeu zosiyanasiyana kukoma kwake, azitona ndi chimanga cha chizungu zofanana ndi zosiyana. Idyani zipatso zake pamene zibereka ndipo perekani chaulere chake nthawi yake. Koma musawononge ayi. Ndithudi Mulungu sakonda anthu owononga وَمِنَ ٱلۡأَنۡعَٰمِ حَمُولَةً وَفَرۡشًاۚ كُلُواْ مِمَّا رَزَقَكُمُ ٱللَّهُ وَلَا تَتَّبِعُواْ خُطُوَٰتِ ٱلشَّيۡطَٰنِۚ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوٌّ مُّبِينٌ ١٤٢Ndipo pakati pa nyama, pali zina zonyamula katundu ndi zina zosanyamula katundu. Idyani zimene Mulungu wakupatsani ndipo musatsatire mapazi a Satana ayi. Ndithudi iye ndi mdani wooneka ثَمَٰنِيَةَ أَزۡوَٰجٍۖ مِّنَ ٱلضَّأۡنِ ٱثۡنَيۡنِ وَمِنَ ٱلۡمَعۡزِ ٱثۡنَيۡنِۗ قُلۡ ءَآلذَّكَرَيۡنِ حَرَّمَ أَمِ ٱلۡأُنثَيَيۡنِ أَمَّا ٱشۡتَمَلَتۡ عَلَيۡهِ أَرۡحَامُ ٱلۡأُنثَيَيۡنِۖ نَبِّـُٔونِي بِعِلۡمٍ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ ١٤٣Tengani ng’ombe zisanu ndi zitatu, ndi nkhosa ziwiri, ndi mbuzi ziwiri. Nena, “Kodi Iye adaletsa zazimuna ziwiri kapena zazikazi ziwiri kapena ana amene ali m’mimba? Ndiyankheni mozindikira ngati mukunena zoona.” وَمِنَ ٱلۡإِبِلِ ٱثۡنَيۡنِ وَمِنَ ٱلۡبَقَرِ ٱثۡنَيۡنِۗ قُلۡ ءَآلذَّكَرَيۡنِ حَرَّمَ أَمِ ٱلۡأُنثَيَيۡنِ أَمَّا ٱشۡتَمَلَتۡ عَلَيۡهِ أَرۡحَامُ ٱلۡأُنثَيَيۡنِۖ أَمۡ كُنتُمۡ شُهَدَآءَ إِذۡ وَصَّىٰكُمُ ٱللَّهُ بِهَٰذَاۚ فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا لِّيُضِلَّ ٱلنَّاسَ بِغَيۡرِ عِلۡمٍۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ ١٤٤Ndipo kuchokera ku ngamira, ziwiri ndi ng’ombe ziwiri. Nena, “Kodi Iye adaletsa zazimuna ziwiri kapena zazikazi ziwiri kapena ana amene ali m’mimba mwawo? Kodi mudalipo pamene Mulungu adakupatsani malamulo awa? Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu ndi kusocheretsa anthu popanda kuzindikira? Ndithudi Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa.” قُل لَّآ أَجِدُ فِي مَآ أُوحِيَ إِلَيَّ مُحَرَّمًا عَلَىٰ طَاعِمٍ يَطۡعَمُهُۥٓ إِلَّآ أَن يَكُونَ مَيۡتَةً أَوۡ دَمًا مَّسۡفُوحًا أَوۡ لَحۡمَ خِنزِيرٍ فَإِنَّهُۥ رِجۡسٌ أَوۡ فِسۡقًا أُهِلَّ لِغَيۡرِ ٱللَّهِ بِهِۦۚ فَمَنِ ٱضۡطُرَّ غَيۡرَ بَاغٍ وَلَا عَادٍ فَإِنَّ رَبَّكَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ ١٤٥Nena, “Ine sindipeza china chilichonse mu zimene zavumbulutsidwa kwa ine choletsa aliyense kudya chakudya china chilichonse kupatula nyama yofa yokha kapena liwende kapena nyama ya nkhumba, chifukwa zimenezo ndi zauve ndi zodetsedwa kapena nyama ina iliyonse imene yaphedwa osati mu dzina la Mulungu. Koma aliyense amene waumirizidwa kudya chilichonse cha izi, osati mokondweretsedwa kapena ndi cholinga chofuna kuswa malamulo, ndithudi, Ambuye wako ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha.” وَعَلَى ٱلَّذِينَ هَادُواْ حَرَّمۡنَا كُلَّ ذِي ظُفُرٍۖ وَمِنَ ٱلۡبَقَرِ وَٱلۡغَنَمِ حَرَّمۡنَا عَلَيۡهِمۡ شُحُومَهُمَآ إِلَّا مَا حَمَلَتۡ ظُهُورُهُمَآ أَوِ ٱلۡحَوَايَآ أَوۡ مَا ٱخۡتَلَطَ بِعَظۡمٍۚ ذَٰلِكَ جَزَيۡنَٰهُم بِبَغۡيِهِمۡۖ وَإِنَّا لَصَٰدِقُونَ ١٤٦Ife tidawaletsa Ayuda kudya nyama zonse zosabsyukula ndipo tinawaletsa mafuta a ng’ombe ndi a nkhosa kupatula amene ali pa msana ndi m’matumbo kapena amene adasakanizika ndi mafupa. Motero tidawapatsa chilango chifukwa cha kulakwa kwawo. Ndithudi Ife tili kunena zoonadi فَإِن كَذَّبُوكَ فَقُل رَّبُّكُمۡ ذُو رَحۡمَةٍ وَٰسِعَةٍ وَلَا يُرَدُّ بَأۡسُهُۥ عَنِ ٱلۡقَوۡمِ ٱلۡمُجۡرِمِينَ ١٤٧Ngati iwo akukunamizani, nena, “Ambuye wanu ndi Mwini chifundo chosatha koma mkwiyo wake siungachotsedwe pa anthu ochita zoipa.” سَيَقُولُ ٱلَّذِينَ أَشۡرَكُواْ لَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ مَآ أَشۡرَكۡنَا وَلَآ ءَابَآؤُنَا وَلَا حَرَّمۡنَا مِن شَيۡءٍۚ كَذَٰلِكَ كَذَّبَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ حَتَّىٰ ذَاقُواْ بَأۡسَنَاۗ قُلۡ هَلۡ عِندَكُم مِّنۡ عِلۡمٍ فَتُخۡرِجُوهُ لَنَآۖ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا ٱلظَّنَّ وَإِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا تَخۡرُصُونَ ١٤٨Anthu opembedza mafano adzati: “Mulungu akadafuna, ife kapena makolo athu, sitikadatumikira milungu ina yoonjezera pa Iye ndipo ife sitikadaletsa china chilichonse.” Mmenemu ndi mmene anthu amene adalipo kale adanamira mpaka pamene analawa mkwiyo wathu. Nena, “Kodi inu muli ndi umboni uliwonse umene mungatisonyeze Ife?” Ndithudi inu simutsatira china koma zinthu zongoganiza ndiponso simuchita china chilichonse koma bodza basi قُلۡ فَلِلَّهِ ٱلۡحُجَّةُ ٱلۡبَٰلِغَةُۖ فَلَوۡ شَآءَ لَهَدَىٰكُمۡ أَجۡمَعِينَ ١٤٩Nena, “Ndi Mulungu yekha amene ali ndi umboni weniweni ndipo Iye akadafuna akadakutsogolerani nonse.” قُلۡ هَلُمَّ شُهَدَآءَكُمُ ٱلَّذِينَ يَشۡهَدُونَ أَنَّ ٱللَّهَ حَرَّمَ هَٰذَاۖ فَإِن شَهِدُواْ فَلَا تَشۡهَدۡ مَعَهُمۡۚ وَلَا تَتَّبِعۡ أَهۡوَآءَ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ وَهُم بِرَبِّهِمۡ يَعۡدِلُونَ ١٥٠Nena, “Bweretsani mboni zanu zonse zimene zikhoza kuchitira umboni kuti Mulungu adakuletsani izi. Ngati iwo apereka umboni, iwe usapereke umboni wako. Ndipo usatsatire zilakolako za iwo amene amati chivumbulutso chathu ndi chabodza, amene sakhulupirira za m’moyo umene uli nkudza ndipo amapanga milungu ina kukhala yofanana ndi Ambuye wawo.” ۞ قُلۡ تَعَالَوۡاْ أَتۡلُ مَا حَرَّمَ رَبُّكُمۡ عَلَيۡكُمۡۖ أَلَّا تُشۡرِكُواْ بِهِۦ شَيۡـًٔاۖ وَبِٱلۡوَٰلِدَيۡنِ إِحۡسَٰنًاۖ وَلَا تَقۡتُلُوٓاْ أَوۡلَٰدَكُم مِّنۡ إِمۡلَٰقٍ نَّحۡنُ نَرۡزُقُكُمۡ وَإِيَّاهُمۡۖ وَلَا تَقۡرَبُواْ ٱلۡفَوَٰحِشَ مَا ظَهَرَ مِنۡهَا وَمَا بَطَنَۖ وَلَا تَقۡتُلُواْ ٱلنَّفۡسَ ٱلَّتِي حَرَّمَ ٱللَّهُ إِلَّا بِٱلۡحَقِّۚ ذَٰلِكُمۡ وَصَّىٰكُم بِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ ١٥١Nena, “Bwerani! Ine ndikuwerengerani zimene Ambuye wanu wakulamulani inu kuti musachite. Musapembedze milungu ina yowonjezera pa Iye; Muzionetsa chifundo kwa makolo anu; musaphe ana anu chifukwa chaumphawi, Ife timakudyetsani inu pamodzi ndi iwo; musayandikire zinthu zoipa zimene zili zoonekera kapena zili zobisika ndipo musaphe munthu amene Mulungu waletsa pokhapokha ngati pali chifukwa choyenera.” Ichi wakulamulani inu kuti muzindikire وَلَا تَقۡرَبُواْ مَالَ ٱلۡيَتِيمِ إِلَّا بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ حَتَّىٰ يَبۡلُغَ أَشُدَّهُۥۚ وَأَوۡفُواْ ٱلۡكَيۡلَ وَٱلۡمِيزَانَ بِٱلۡقِسۡطِۖ لَا نُكَلِّفُ نَفۡسًا إِلَّا وُسۡعَهَاۖ وَإِذَا قُلۡتُمۡ فَٱعۡدِلُواْ وَلَوۡ كَانَ ذَا قُرۡبَىٰۖ وَبِعَهۡدِ ٱللَّهِ أَوۡفُواْۚ ذَٰلِكُمۡ وَصَّىٰكُم بِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَذَكَّرُونَ ١٥٢“Ndipo musayandikire chuma cha ana a masiye kupatula m’njira yabwino yowakonzera tsogolo lawo mpaka pamene iwo akula msinkhu. Kwaniritsani muyeso woyenera ndipo muyese mwachilungamo. Ife sitinyamulitsa munthu wina aliyense katundu wolemera amene iye sangathe kunyamula. Ndipo mukamalankhula, muzilankhula mwachilungamo ngakhale kuti nkhanizo zikhudza abale anu ndipo kwaniritsani malonjezo a Mulungu. Ichi wakulamurani inu kuti mudzikumbukira.” وَأَنَّ هَٰذَا صِرَٰطِي مُسۡتَقِيمًا فَٱتَّبِعُوهُۖ وَلَا تَتَّبِعُواْ ٱلسُّبُلَ فَتَفَرَّقَ بِكُمۡ عَن سَبِيلِهِۦۚ ذَٰلِكُمۡ وَصَّىٰكُم بِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَتَّقُونَ ١٥٣Ndithu iyi ndi njira yanga yoyenera motero itsatireni ndipo musatsatire njira zina zake chifukwa izo zidzakusocheretsani inu ku njira yake. Ichi Iye wakulamulani kuti mukhale angwiro ثُمَّ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ تَمَامًا عَلَى ٱلَّذِيٓ أَحۡسَنَ وَتَفۡصِيلًا لِّكُلِّ شَيۡءٍ وَهُدًى وَرَحۡمَةً لَّعَلَّهُم بِلِقَآءِ رَبِّهِمۡ يُؤۡمِنُونَ ١٥٤Ndipo Ife tidamupatsa Mose Buku, kumaliza ubwino wathu kwa aliyense wochita zabwino ndiponso lofotokoza chinthu chilichonse, ulangizi ndi chisomo kuti akhulupirire mukukumana kwawo ndi Ambuye wawo وَهَٰذَا كِتَٰبٌ أَنزَلۡنَٰهُ مُبَارَكٌ فَٱتَّبِعُوهُ وَٱتَّقُواْ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ ١٥٥Ili ndi Buku lodalitsika limene talivumbulutsa, motero opani Mulungu kuti mulandire chisomo أَن تَقُولُوٓاْ إِنَّمَآ أُنزِلَ ٱلۡكِتَٰبُ عَلَىٰ طَآئِفَتَيۡنِ مِن قَبۡلِنَا وَإِن كُنَّا عَن دِرَاسَتِهِمۡ لَغَٰفِلِينَ ١٥٦Kuti inu musadzanene kuti: “Buku lidangovumbulutsidwa ku magulu awiri pambuyo pathu, ndipo ife sitidadziwe zimene adali kuwerenga.” أَوۡ تَقُولُواْ لَوۡ أَنَّآ أُنزِلَ عَلَيۡنَا ٱلۡكِتَٰبُ لَكُنَّآ أَهۡدَىٰ مِنۡهُمۡۚ فَقَدۡ جَآءَكُم بَيِّنَةٌ مِّن رَّبِّكُمۡ وَهُدًى وَرَحۡمَةٌۚ فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن كَذَّبَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَصَدَفَ عَنۡهَاۗ سَنَجۡزِي ٱلَّذِينَ يَصۡدِفُونَ عَنۡ ءَايَٰتِنَا سُوٓءَ ٱلۡعَذَابِ بِمَا كَانُواْ يَصۡدِفُونَ ١٥٧Kapena mukhoza kudzanena kuti: “Buku la Mulungu likanavumbulutsidwa kwa ife, ndithudi, tikadalangizidwa bwino kuposa iwo.” Ndithudi chizindikiro chosakaikitsa chadza tsopano kuchokera kwa a Ambuye wanu; chilangizo ndi madalitso. Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene akana chivumbulutso cha Mulungu ndipo safuna kuchitsatira? Ife tidzawalipira onse amene amakana zizindikiro zathu ndi chilango chowawa chifukwa chokana kwawo هَلۡ يَنظُرُونَ إِلَّآ أَن تَأۡتِيَهُمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ أَوۡ يَأۡتِيَ رَبُّكَ أَوۡ يَأۡتِيَ بَعۡضُ ءَايَٰتِ رَبِّكَۗ يَوۡمَ يَأۡتِي بَعۡضُ ءَايَٰتِ رَبِّكَ لَا يَنفَعُ نَفۡسًا إِيمَٰنُهَا لَمۡ تَكُنۡ ءَامَنَتۡ مِن قَبۡلُ أَوۡ كَسَبَتۡ فِيٓ إِيمَٰنِهَا خَيۡرًاۗ قُلِ ٱنتَظِرُوٓاْ إِنَّا مُنتَظِرُونَ ١٥٨Kodi iwo ali kudikira wina kupatula angelo kuti adze kwa iwo kapena kuti Ambuye wako adze kapena zina mwa zizindikiro za Ambuye wako zidze? Tsiku limene zina mwa zizindikiro za Ambuye wako zidzadza, chikhulupiriro sichidzathandiza mzimu umene unalibe chikhulupiriro kale kapena umene siudagwiritse ntchito bwino chikhulupiriro. Nena, “Dikirani! Nafenso tili kudikira.” إِنَّ ٱلَّذِينَ فَرَّقُواْ دِينَهُمۡ وَكَانُواْ شِيَعًا لَّسۡتَ مِنۡهُمۡ فِي شَيۡءٍۚ إِنَّمَآ أَمۡرُهُمۡ إِلَى ٱللَّهِ ثُمَّ يُنَبِّئُهُم بِمَا كَانُواْ يَفۡعَلُونَ ١٥٩Ndithudi iwo amene apatukana m’chipembedzo ndi kupanga mipingo yosiyanasiyana, iwe sizikukhudza zimenezo. Nkhani yawo adzathetsa ndi Mulungu ndipo Iye adzawauza zomwe amachita مَن جَآءَ بِٱلۡحَسَنَةِ فَلَهُۥ عَشۡرُ أَمۡثَالِهَاۖ وَمَن جَآءَ بِٱلسَّيِّئَةِ فَلَا يُجۡزَىٰٓ إِلَّا مِثۡلَهَا وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ ١٦٠Aliyense amene amachita ntchito yabwino adzalipidwa magawo khumi olingana ndi iyo ndipo aliyense amene amachita zoipa adzalandira choipa chomwecho ndipo iwo sadzaponderezedwa ayi قُلۡ إِنَّنِي هَدَىٰنِي رَبِّيٓ إِلَىٰ صِرَٰطٍ مُّسۡتَقِيمٍ دِينًا قِيَمًا مِّلَّةَ إِبۡرَٰهِيمَ حَنِيفًاۚ وَمَا كَانَ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ ١٦١Nena, “Ndithudi Ambuye wanga wanditsogolera ine ku njira yoyenera, ku chipembedzo changwiro, chikhulupiriro cha Abrahamu wangwiro chifukwa Abrahamu sadali mmodzi wa anthu opembedza mafano.” قُلۡ إِنَّ صَلَاتِي وَنُسُكِي وَمَحۡيَايَ وَمَمَاتِي لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ١٦٢Nena, “Ndithudi mapemphero anga, nsembe yanga, moyo wanga ndi imfa yanga zonse zili m’manja mwa Mulungu Ambuye wazolengedwa zonse.” لَا شَرِيكَ لَهُۥۖ وَبِذَٰلِكَ أُمِرۡتُ وَأَنَا۠ أَوَّلُ ٱلۡمُسۡلِمِينَ ١٦٣Iye alibe wothandizana naye. Pa izi ine ndalamulidwa ndipo ine ndine woyamba wa iwo ogonjera malamulo a Mulungu قُلۡ أَغَيۡرَ ٱللَّهِ أَبۡغِي رَبًّا وَهُوَ رَبُّ كُلِّ شَيۡءٍۚ وَلَا تَكۡسِبُ كُلُّ نَفۡسٍ إِلَّا عَلَيۡهَاۚ وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٌ وِزۡرَ أُخۡرَىٰۚ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُم مَّرۡجِعُكُمۡ فَيُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمۡ فِيهِ تَخۡتَلِفُونَ ١٦٤Nena, “Kodi ine ndifune Ambuye wina osati Mulungu pamene Iye ndi Ambuye wa zinthu zonse? Munthu aliyense adzakolola zipatso za ntchito yake ndipo palibe mzimu umene udzanyamula katundu wa wina wake. Pomaliza nonse mudzabwerera kwa Ambuye wanu; ndipo Iye adzakuuzani zomwe munali kutsutsana.” وَهُوَ ٱلَّذِي جَعَلَكُمۡ خَلَٰٓئِفَ ٱلۡأَرۡضِ وَرَفَعَ بَعۡضَكُمۡ فَوۡقَ بَعۡضٍ دَرَجَٰتٍ لِّيَبۡلُوَكُمۡ فِي مَآ ءَاتَىٰكُمۡۗ إِنَّ رَبَّكَ سَرِيعُ ٱلۡعِقَابِ وَإِنَّهُۥ لَغَفُورٌ رَّحِيمُۢ ١٦٥Ndipo ndiye amene anakulengani kukhala mibadwo yodza pambuyo pa mibadwo yina, kulowa m’malo mwa uzake padziko lapansi. Ndipo anakukwezani m’maudindo, ena kuposa anzawo kuti akhoza kukuyesani ndi zimene wakupatsani. Ndithudi Ambuye wanu ndi wachangu polanga koma ndithudi Iye amakhululuka, Mwini chisoni chosatha