Millat al-Islam

Chapter 98 · 8 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Bayyina in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah Al-Bayyina (1270 reciters)
Medinanسورة البينة8 verses

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

لَمۡ يَكُنِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ وَٱلۡمُشۡرِكِينَ مُنفَكِّينَ حَتَّىٰ تَأۡتِيَهُمُ ٱلۡبَيِّنَةُ ١Iwo amene sakhulupirira a m’gulu la anthu a m’Buku ndi anthu opembedza mafano, sadzasiya kusakhulupilira mpaka pamene zizindikiro zooneka zitaperekedwa kwa iwo رَسُولٌ مِّنَ ٱللَّهِ يَتۡلُواْ صُحُفًا مُّطَهَّرَةً ٢Mtumwi wochokera kwa Mulungu amene ali kuwerenga kuchokera pa Masamba oyera فِيهَا كُتُبٌ قَيِّمَةٌ ٣Amene ali ndi malamulo angwiro ndi omveka bwino ochokera kwa Mulungu وَمَا تَفَرَّقَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ إِلَّا مِنۢ بَعۡدِ مَا جَآءَتۡهُمُ ٱلۡبَيِّنَةُ ٤Ndipo anthu okhulupirira Buku sanayambe kugawikana pakati pawo mpaka pamene zizindikiro zooneka zidaperekedwa kwa iwo وَمَآ أُمِرُوٓاْ إِلَّا لِيَعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ حُنَفَآءَ وَيُقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَيُؤۡتُواْ ٱلزَّكَوٰةَۚ وَذَٰلِكَ دِينُ ٱلۡقَيِّمَةِ ٥Ndipo Al-Zalzala 659 iwo sadalamulidwe koma kuti azipembedza Mulungu ndipo kuti asapembedze wina aliyense koma Iye yekha ndipo kuti adzipemphera pa nthawi yake ndi kupereka msonkho wothandiza anthu osauka. Ndipo chimenechi ndicho chipembedzo chabwino إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ وَٱلۡمُشۡرِكِينَ فِي نَارِ جَهَنَّمَ خَٰلِدِينَ فِيهَآۚ أُوْلَٰٓئِكَ هُمۡ شَرُّ ٱلۡبَرِيَّةِ ٦Ndithudi iwo amene sakhulupirira amene ali pakati pa anthu a m’Buku, ndi anthu opembedza mafano, adzakhala ku moto wa ku Gahena. Iwo ndiwo oipa zedi pa zolengedwa zonse إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ أُوْلَٰٓئِكَ هُمۡ خَيۡرُ ٱلۡبَرِيَّةِ ٧Ndithudi iwo amene atsatira chikhulupiriro choonadi ndipo amachita ntchito zabwino ndiwo olemekezeka pa zolengedwa zonse جَزَآؤُهُمۡ عِندَ رَبِّهِمۡ جَنَّٰتُ عَدۡنٍ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدًاۖ رَّضِيَ ٱللَّهُ عَنۡهُمۡ وَرَضُواْ عَنۡهُۚ ذَٰلِكَ لِمَنۡ خَشِيَ رَبَّهُۥ ٨Mphotho yawo imene ili ndi Ambuye wawo ndi kuwaika m’minda imene imathiriridwa ndi madzi ya m’mitsinje pansi pake, kumene adzakhalako nthawi zonse. Mulungu ndi wosangalala ndi iwo ndipo nawonso ndi osangalala ndi Iye. M’menemo ndi m’mene munthu oopa Mulungu adzalandirire mphotho yake

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.