Millat al-Islam

Chapter 89 · 30 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Fajr in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah Al-Fajr (1331 reciters)
Meccanسورة الفجر30 verses

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

وَٱلۡفَجۡرِ ١Pali m’mbandakucha وَلَيَالٍ عَشۡرٍ ٢Ndi pali usiku khumi وَٱلشَّفۡعِ وَٱلۡوَتۡرِ ٣Pali chofanana ndi chosiyana وَٱلَّيۡلِ إِذَا يَسۡرِ ٤Pali usiku pamene uli nkutha هَلۡ فِي ذَٰلِكَ قَسَمٌ لِّذِي حِجۡرٍ ٥Ndithudi m’menemu muli umboni wokwanira kwa anthu a nzeru أَلَمۡ تَرَ كَيۡفَ فَعَلَ رَبُّكَ بِعَادٍ ٦Kodi iwe siudaone mmene Ambuye wako adakhaulitsira anthu a Aad إِرَمَ ذَاتِ ٱلۡعِمَادِ ٧Amene anali atali atali ngati nsanamila zitali zitali ٱلَّتِي لَمۡ يُخۡلَقۡ مِثۡلُهَا فِي ٱلۡبِلَٰدِ ٨wolingana nawo amene sanalengedwepo padziko وَثَمُودَ ٱلَّذِينَ جَابُواْ ٱلصَّخۡرَ بِٱلۡوَادِ ٩Ndi anthu a Thamoud, amene ankakumba nyumba zawo m’miyala ya m’dambo وَفِرۡعَوۡنَ ذِي ٱلۡأَوۡتَادِ ١٠Ndi Farao, amene anali ndi zichiri ٱلَّذِينَ طَغَوۡاْ فِي ٱلۡبِلَٰدِ ١١Amene anali kuphwanya malamulo paliponse m’dziko فَأَكۡثَرُواْ فِيهَا ٱلۡفَسَادَ ١٢Ndipo adachulukitsa chisokonezo فَصَبَّ عَلَيۡهِمۡ رَبُّكَ سَوۡطَ عَذَابٍ ١٣Motero Ambuye wako adabweretsa chilango chosiyana siyana chowawa pa iwo إِنَّ رَبَّكَ لَبِٱلۡمِرۡصَادِ ١٤Ndithudi Ambuye wako amaona فَأَمَّا ٱلۡإِنسَٰنُ إِذَا مَا ٱبۡتَلَىٰهُ رَبُّهُۥ فَأَكۡرَمَهُۥ وَنَعَّمَهُۥ فَيَقُولُ رَبِّيٓ أَكۡرَمَنِ ١٥Ndipo nthawi zonse munthu, pamene Ambuye wake amuyesa pomukweza ndi kumuonetsera chifundo chake, iye amati: “Ambuye wanga wandilemekeza ine.” وَأَمَّآ إِذَا مَا ٱبۡتَلَىٰهُ فَقَدَرَ عَلَيۡهِ رِزۡقَهُۥ فَيَقُولُ رَبِّيٓ أَهَٰنَنِ ١٦Koma akamuyesa pomumana zinthu, iye amati: “Ambuye wanga ali kundizunza ine.” كـَلَّاۖ بَل لَّا تُكۡرِمُونَ ٱلۡيَتِيمَ ١٧Iyayi! Koma inu simuonetsa chifundo kwa ana a masiye وَلَا تَحَٰٓضُّونَ عَلَىٰ طَعَامِ ٱلۡمِسۡكِينِ ١٨Ndi kuuzana kuti mudzidyetsa anthu osauka وَتَأۡكُلُونَ ٱلتُّرَاثَ أَكۡلًا لَّمًّا ١٩Inu mumalanda chuma cha anthu opanda mphamvu chifukwa cha umbombo وَتُحِبُّونَ ٱلۡمَالَ حُبًّا جَمًّا ٢٠Ndipo mumakonda chuma ndi mitima yanu yonse كـَلَّآۖ إِذَا دُكَّتِ ٱلۡأَرۡضُ دَكًّا دَكًّا ٢١Iyayi! Koma pamene dziko lidzasinjidwa kukhala ufa وَجَآءَ رَبُّكَ وَٱلۡمَلَكُ صَفًّا صَفًّا ٢٢Ndipo Ambuye wanu adzadza pamodzi ndi angelo ali pa mizere وَجِاْيٓءَ يَوۡمَئِذِۭ بِجَهَنَّمَۚ يَوۡمَئِذٍ يَتَذَكَّرُ ٱلۡإِنسَٰنُ وَأَنَّىٰ لَهُ ٱلذِّكۡرَىٰ ٢٣Ndipo Gahena idzabweretsedwa pafupi patsikuli. Ndipo patsikuli munthu adzakumbukira. Koma, kodi chikumbumtima chake chidzamuthandiza motani يَقُولُ يَٰلَيۡتَنِي قَدَّمۡتُ لِحَيَاتِي ٢٤Iye adzanena kuti: “Kalanga ine! Ndikanakhala ndinali kuchita zabwino pamene ndinali ndi moyo.” فَيَوۡمَئِذٍ لَّا يُعَذِّبُ عَذَابَهُۥٓ أَحَدٌ ٢٥Motero patsikuli, palibe wina amene adzalanga monga momwe Iye adzalangire وَلَا يُوثِقُ وَثَاقَهُۥٓ أَحَدٌ ٢٦Ndipo palibe wina amene adzamanga monga ngati momwe Iye adzamangire يَٰٓأَيَّتُهَا ٱلنَّفۡسُ ٱلۡمُطۡمَئِنَّةُ ٢٧oh! Iwe wokhutitsidwa ٱرۡجِعِيٓ إِلَىٰ رَبِّكِ رَاضِيَةً مَّرۡضِيَّةً ٢٨Bwerera kwa Ambuye wako mosangalala ndi Iye, ndi Iye mosangalala ndi iwe فَٱدۡخُلِي فِي عِبَٰدِي ٢٩Lowa m’gulu la akapolo anga wolemekezeka وَٱدۡخُلِي جَنَّتِي ٣٠Ndipo lowa mu Paradiso yanga

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.