بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
تَبَارَكَ ٱلَّذِي نَزَّلَ ٱلۡفُرۡقَانَ عَلَىٰ عَبۡدِهِۦ لِيَكُونَ لِلۡعَٰلَمِينَ نَذِيرًا ١Alemekezeke Iye amene adavumbulutsa Korani kwa Mtumwi wake kuti akhoza kuchenjeza mitundu ya anthu ٱلَّذِي لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَلَمۡ يَتَّخِذۡ وَلَدًا وَلَمۡ يَكُن لَّهُۥ شَرِيكٌ فِي ٱلۡمُلۡكِ وَخَلَقَ كُلَّ شَيۡءٍ فَقَدَّرَهُۥ تَقۡدِيرًا ٢Iye ndiye Mfumu ya kumwamba ndi dziko lapansi. Iye ndiye amene sadabereke mwana ndipo alibe wothandizana naye mu Ufumu wake. Iye ndiye amene adalenga zinthu zonse ndipo adakhazikitsa mmene zili ndi mapeto ake وَٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ ءَالِهَةً لَّا يَخۡلُقُونَ شَيۡـًٔا وَهُمۡ يُخۡلَقُونَ وَلَا يَمۡلِكُونَ لِأَنفُسِهِمۡ ضَرًّا وَلَا نَفۡعًا وَلَا يَمۡلِكُونَ مَوۡتًا وَلَا حَيَوٰةً وَلَا نُشُورًا ٣Komabe anthu osakhulupirira amapembedza milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni imene siingathe kulenga china chilichonse chifukwa chakuti nayonso idachita kulengedwa. Ndi imene singathe kuwathandiza kapena kuwaononga ndiponso imene ilibe mphamvu pa nkhani zokhudza imfa kapena moyo kapena kuukitsa anthu akufa وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّآ إِفۡكٌ ٱفۡتَرَىٰهُ وَأَعَانَهُۥ عَلَيۡهِ قَوۡمٌ ءَاخَرُونَۖ فَقَدۡ جَآءُو ظُلۡمًا وَزُورًا ٤Anthu osakhulupirira amanena kuti, “Zonsezi ndi zinthu zabodza zimene wapeka yekha, ndiponso anthu ena amamuthandiza. Zonse zimene watulutsa ndi zopanda pake ndipo zabodza وَقَالُوٓاْ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ ٱكۡتَتَبَهَا فَهِيَ تُمۡلَىٰ عَلَيۡهِ بُكۡرَةً وَأَصِيلًا ٥Ndipo iwo amati, “Izi ndi nkhani zopanda pake za anthu amakedzana zimene iye walemba. Izo zimalembetsedwa kwa Iye m’mawa ndi masana aliwonse.” قُلۡ أَنزَلَهُ ٱلَّذِي يَعۡلَمُ ٱلسِّرَّ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ إِنَّهُۥ كَانَ غَفُورًا رَّحِيمًا ٦Nena, “Wavumbulutsa ndiye amene amadziwa zinsinsi za kumwamba ndi za padziko lapansi. Iye amakhululukira ndipo ndi Mwini chisoni chosatha.” وَقَالُواْ مَالِ هَٰذَا ٱلرَّسُولِ يَأۡكُلُ ٱلطَّعَامَ وَيَمۡشِي فِي ٱلۡأَسۡوَاقِ لَوۡلَآ أُنزِلَ إِلَيۡهِ مَلَكٌ فَيَكُونَ مَعَهُۥ نَذِيرًا ٧Iwo amanena kuti, “Uyu, ndi Mtumwi wotani amene amadya ndipo amayendayenda ku msika? Kodi bwanji mngelo sanathe kutumizidwa pansi pamodzi ndi iye kudzatichenjeza ife?” أَوۡ يُلۡقَىٰٓ إِلَيۡهِ كَنزٌ أَوۡ تَكُونُ لَهُۥ جَنَّةٌ يَأۡكُلُ مِنۡهَاۚ وَقَالَ ٱلظَّٰلِمُونَ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا رَجُلًا مَّسۡحُورًا ٨“Nanga ndi chifukwa chiyani sadapatsidwe chuma ndipo alibe munda woti azipezako chakudya?” Ndipo anthu ochita zoipa amati, “Ndithudi munthu amene muli kumutsatira ndi wolodzedwa.” ٱنظُرۡ كَيۡفَ ضَرَبُواْ لَكَ ٱلۡأَمۡثَٰلَ فَضَلُّواْ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ سَبِيلًا ٩Taona mafanizo amene amakupatsa iwe! Iwo asochera ndipo sangathe kubwerera kunjira yoyenera تَبَارَكَ ٱلَّذِيٓ إِن شَآءَ جَعَلَ لَكَ خَيۡرًا مِّن ذَٰلِكَ جَنَّٰتٍ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ وَيَجۡعَل لَّكَ قُصُورَۢا ١٠Alemekezeke Iye amene, ngati afuna akhoza kukupatsa iwe zinthu zabwino kuposa zimenezi monga minda yothiriridwa ndi madzi a m’mitsinje ndi nyumba zachifumu بَلۡ كَذَّبُواْ بِٱلسَّاعَةِۖ وَأَعۡتَدۡنَا لِمَن كَذَّبَ بِٱلسَّاعَةِ سَعِيرًا ١١Iyayi. Iwo amakana ola lachiweruzo, ndipo iwo amene amakana olali, Ife tawakonzera moto woyaka إِذَا رَأَتۡهُم مِّن مَّكَانِۭ بَعِيدٍ سَمِعُواْ لَهَا تَغَيُّظًا وَزَفِيرًا ١٢Pamene idzawaona iwo kuchokera kutali, iwo adzamva mkokomo wake وَإِذَآ أُلۡقُواْ مِنۡهَا مَكَانًا ضَيِّقًا مُّقَرَّنِينَ دَعَوۡاْ هُنَالِكَ ثُبُورًا ١٣Ndipo onse akadzamangidwa limodzi, adzaponyedwa kumalo opanikizika. Ndithudi iwo adzafuna imfa itadza pa iwo لَّا تَدۡعُواْ ٱلۡيَوۡمَ ثُبُورًا وَٰحِدًا وَٱدۡعُواْ ثُبُورًا كَثِيرًا ١٤Lero musaitane imfa imodzi yokha ayi koma itanani imfa zambiri قُلۡ أَذَٰلِكَ خَيۡرٌ أَمۡ جَنَّةُ ٱلۡخُلۡدِ ٱلَّتِي وُعِدَ ٱلۡمُتَّقُونَۚ كَانَتۡ لَهُمۡ جَزَآءً وَمَصِيرًا ١٥Nena, “Kodi chimenecho ndi chabwino kapena Paradiso yosatha imene anthu angwiro adalonjezedwa?” Imeneyo ndiyo mphotho yawo ndi kobwerera kwawo لَّهُمۡ فِيهَا مَا يَشَآءُونَ خَٰلِدِينَۚ كَانَ عَلَىٰ رَبِّكَ وَعۡدًا مَّسۡـُٔولًا ١٦Iwo adzapeza m’menemo zonse zimene anali kufuna ndi kukhala momwemo. Limenelo ndilo lonjezo limene ndi lofunika kumapempha pafupipafupi kuchokera kwa Ambuye wako وَيَوۡمَ يَحۡشُرُهُمۡ وَمَا يَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ فَيَقُولُ ءَأَنتُمۡ أَضۡلَلۡتُمۡ عِبَادِي هَٰٓؤُلَآءِ أَمۡ هُمۡ ضَلُّواْ ٱلسَّبِيلَ ١٧Patsiku limene Iye adzawasonkhanitsa onse ndi zomwe amapembedza kuonjezera pa Mulungu weniweni ndipo Iye adzati, “Kodi ndinu amene munasocheza akapolo anga kapena ndi iwo okha anasochera ku njira yoyenera?” قَالُواْ سُبۡحَٰنَكَ مَا كَانَ يَنۢبَغِي لَنَآ أَن نَّتَّخِذَ مِن دُونِكَ مِنۡ أَوۡلِيَآءَ وَلَٰكِن مَّتَّعۡتَهُمۡ وَءَابَآءَهُمۡ حَتَّىٰ نَسُواْ ٱلذِّكۡرَ وَكَانُواْ قَوۡمَۢا بُورًا ١٨Iwo adzati, “Ulemerero ukhale kwa Inu! Si koyenera kwa ife kuti tisankhe otisamalira ena oonjezera pa Inu. Koma Inu mudawapatsa iwo ndi makolo awo zinthu zokoma za dziko, kotero kuti iwo adaiwala chenjezo lanu ndipo adali anthu oonongeka.” فَقَدۡ كَذَّبُوكُم بِمَا تَقُولُونَ فَمَا تَسۡتَطِيعُونَ صَرۡفًا وَلَا نَصۡرًاۚ وَمَن يَظۡلِم مِّنكُمۡ نُذِقۡهُ عَذَابًا كَبِيرًا ١٩Kotero iwo adatsutsa mawu anu ndipo inu simungathe kuthawa kapena kupeza chithandizo ndipo aliyense amene ndi wosalungama pakati panu, Ife tidzamupatsa chilango chachikulu وَمَآ أَرۡسَلۡنَا قَبۡلَكَ مِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ إِلَّآ إِنَّهُمۡ لَيَأۡكُلُونَ ٱلطَّعَامَ وَيَمۡشُونَ فِي ٱلۡأَسۡوَاقِۗ وَجَعَلۡنَا بَعۡضَكُمۡ لِبَعۡضٍ فِتۡنَةً أَتَصۡبِرُونَۗ وَكَانَ رَبُّكَ بَصِيرًا ٢٠Ife sitidatumizepo Atumwi kale amene sanali kudya ndi kuyenda m’misika. Ife tidakupangani ena a inu kukhala mayesero a ena. Kodi simungapirire? Ambuye wanu amaona chilichonse
۞ وَقَالَ ٱلَّذِينَ لَا يَرۡجُونَ لِقَآءَنَا لَوۡلَآ أُنزِلَ عَلَيۡنَا ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ أَوۡ نَرَىٰ رَبَّنَاۗ لَقَدِ ٱسۡتَكۡبَرُواْ فِيٓ أَنفُسِهِمۡ وَعَتَوۡ عُتُوًّا كَبِيرًا ٢١Iwo amene alibe chikhulupiriro choti adzakumana ndi Ife amati, “Kodi ndi chifukwa chiyani angelo sadatumizidwe kwa ife? Kapena ndi chifukwa chiyani kuti ife sitingaone Ambuye wathu?” Ndithudi iwo adadzikweza kwambiri يَوۡمَ يَرَوۡنَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ لَا بُشۡرَىٰ يَوۡمَئِذٍ لِّلۡمُجۡرِمِينَ وَيَقُولُونَ حِجۡرًا مَّحۡجُورًا ٢٢Patsiku limene iwo adzaona angelo, anthu ochita zoipa sadzasangalala ayi ndipo iwo adzati, “Ambuye wathu! Ikani malire pakati pa ife ndi iwo.” وَقَدِمۡنَآ إِلَىٰ مَا عَمِلُواْ مِنۡ عَمَلٍ فَجَعَلۡنَٰهُ هَبَآءً مَّنثُورًا ٢٣Ndipo Ife tidzabweretsa zonse zimene adachita ndikuzionetsa kuti ndi zinthu zopanda ntchito ngati fumbi louluka أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِ يَوۡمَئِذٍ خَيۡرٌ مُّسۡتَقَرًّا وَأَحۡسَنُ مَقِيلًا ٢٤Anthu okhala ku Paradiso, adzakhala kumalo abwino patsiku limeneli ndiponso malo abwino opumulako وَيَوۡمَ تَشَقَّقُ ٱلسَّمَآءُ بِٱلۡغَمَٰمِ وَنُزِّلَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ تَنزِيلًا ٢٥Patsiku limeneli kumwamba pamodzi ndi mitambo yake idzagawanika pakati ndipo angelo adzatumizidwa pansi pano m’maudindo awo ٱلۡمُلۡكُ يَوۡمَئِذٍ ٱلۡحَقُّ لِلرَّحۡمَٰنِۚ وَكَانَ يَوۡمًا عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ عَسِيرًا ٢٦Patsiku limeneli ufumu wonse udzakhala wa Mwini chisoni chosatha. Limeneli lidzakhala tsiku lovuta kwambiri kwa anthu osakhulupirira وَيَوۡمَ يَعَضُّ ٱلظَّالِمُ عَلَىٰ يَدَيۡهِ يَقُولُ يَٰلَيۡتَنِي ٱتَّخَذۡتُ مَعَ ٱلرَّسُولِ سَبِيلًا ٢٧Patsiku limeneli munthu ochita zoipa adzanong’oneza bombono nati, “Oh zikadakhala bwino ndikadakhala kuti ndidatsatira zimene Mtumwi anali kunena!” يَٰوَيۡلَتَىٰ لَيۡتَنِي لَمۡ أَتَّخِذۡ فُلَانًا خَلِيلًا ٢٨“oh kalanga ine! Ndikadakhala kuti sindidasankhe a uje ndi a uje kuti akhale anzanga!” لَّقَدۡ أَضَلَّنِي عَنِ ٱلذِّكۡرِ بَعۡدَ إِذۡ جَآءَنِيۗ وَكَانَ ٱلشَّيۡطَٰنُ لِلۡإِنسَٰنِ خَذُولًا ٢٩“Mosakayika ndiwo amene adandisokoneza ine kuti ndisakhulupirire machenjezo a Mulungu pamene machenjezowo atandifika. Ndithudi Satana ndi wachinyengo nthawi zonse kwa munthu.” وَقَالَ ٱلرَّسُولُ يَٰرَبِّ إِنَّ قَوۡمِي ٱتَّخَذُواْ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانَ مَهۡجُورًا ٣٠Mtumwi adati, “Ambuye wanga! Ndithudi anthu anga alikana Buku la Korani.” وَكَذَٰلِكَ جَعَلۡنَا لِكُلِّ نَبِيٍّ عَدُوًّا مِّنَ ٱلۡمُجۡرِمِينَۗ وَكَفَىٰ بِرَبِّكَ هَادِيًا وَنَصِيرًا ٣١Motero Ife tapanga kwa Mtumwi aliyense mdani kuchokera kwa anthu ochimwa, anthu otsutsana naye, ndipo Ambuye wako ali wokwana kukhala wokutsogolera mu zabwino ndiponso ngati wokuthandiza wako وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَوۡلَا نُزِّلَ عَلَيۡهِ ٱلۡقُرۡءَانُ جُمۡلَةً وَٰحِدَةًۚ كَذَٰلِكَ لِنُثَبِّتَ بِهِۦ فُؤَادَكَۖ وَرَتَّلۡنَٰهُ تَرۡتِيلًا ٣٢Anthu osakhulupirira anati, “Kodi ndi chifukwa chiyani Korani yonse siidavumbulutsidwe kwa iye nthawi imodzi?” Ife talivumbulutsa kotero kuti tikhoza kulimbikitsa mtima wako ndipo takupatsa ilo kwa iwe mu chivumbulutso chapang’onopang’ono وَلَا يَأۡتُونَكَ بِمَثَلٍ إِلَّا جِئۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ وَأَحۡسَنَ تَفۡسِيرًا ٣٣Iwo sadzatha kubwera ndi mtsutso umene Ife sitidakonze yankho loona ndi kafotokozedwe kake ٱلَّذِينَ يُحۡشَرُونَ عَلَىٰ وُجُوهِهِمۡ إِلَىٰ جَهَنَّمَ أُوْلَٰٓئِكَ شَرٌّ مَّكَانًا وَأَضَلُّ سَبِيلًا ٣٤Iwo adzaduduluzidwa cha mphumi kupita ku Gahena ndipo iwo adzakhala ndi malo oipa okhalamo ndipo njira yawo ndi yosochera وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ وَجَعَلۡنَا مَعَهُۥٓ أَخَاهُ هَٰرُونَ وَزِيرًا ٣٥Ndithudi Ife tidavumbulutsa mawu a Mulungu kwa Mose ndipo tidamupatsa m’bale wake Aroni kuti akhale nduna yomuthandiza فَقُلۡنَا ٱذۡهَبَآ إِلَى ٱلۡقَوۡمِ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا فَدَمَّرۡنَٰهُمۡ تَدۡمِيرًا ٣٦Tidawauza iwo kuti, “Pitani nonse kwa anthu amene adakana zizindikiro zathu” ndipo pambuyo pake tidawaononga kotheratu وَقَوۡمَ نُوحٍ لَّمَّا كَذَّبُواْ ٱلرُّسُلَ أَغۡرَقۡنَٰهُمۡ وَجَعَلۡنَٰهُمۡ لِلنَّاسِ ءَايَةًۖ وَأَعۡتَدۡنَا لِلظَّٰلِمِينَ عَذَابًا أَلِيمًا ٣٧Akakhala anthu a Nowa, tidawamiza pamene iwo adakana Atumwi awo ndipo tidawapanga iwo kukhala phunziro kwa anthu a mitundu yonse. Ndipo anthu ochimwa tawakonzera chilango chowawa وَعَادًا وَثَمُودَاْ وَأَصۡحَٰبَ ٱلرَّسِّ وَقُرُونَۢا بَيۡنَ ذَٰلِكَ كَثِيرًا ٣٨Mitundu ya anthu a ku Thamoud ndi Aad nawonso tidawaononga ndiponso iwo amene anali kukhala ku Raas ndi mibadwo yochuluka imene idadza pakati pawo وَكُلًّا ضَرَبۡنَا لَهُ ٱلۡأَمۡثَٰلَۖ وَكُلًّا تَبَّرۡنَا تَتۡبِيرًا ٣٩Ndipo onsewa, tidawapatsa zitsanzo ndipo onse tidawaononga kotheratu وَلَقَدۡ أَتَوۡاْ عَلَى ٱلۡقَرۡيَةِ ٱلَّتِيٓ أُمۡطِرَتۡ مَطَرَ ٱلسَّوۡءِۚ أَفَلَمۡ يَكُونُواْ يَرَوۡنَهَاۚ بَلۡ كَانُواْ لَا يَرۡجُونَ نُشُورًا ٤٠Ndithudi anthu osakhulupirira adadutsa pa mzinda umene udaonongeka ndi madzi a mvula. Kodi iwo sadauone mzindawu? Komabe iwo adalibe chikhulupiriro mu kuukanso kwa akufa وَإِذَا رَأَوۡكَ إِن يَتَّخِذُونَكَ إِلَّا هُزُوًا أَهَٰذَا ٱلَّذِي بَعَثَ ٱللَّهُ رَسُولًا ٤١Nthawi zonse akakuona iwe amakunyoza ndipo amati, “Kodi uyu ndiye munthu amene akuti Mulungu wamutumiza ngati Mtumwi wake?” إِن كَادَ لَيُضِلُّنَا عَنۡ ءَالِهَتِنَا لَوۡلَآ أَن صَبَرۡنَا عَلَيۡهَاۚ وَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ حِينَ يَرَوۡنَ ٱلۡعَذَابَ مَنۡ أَضَلُّ سَبِيلًا ٤٢Ngati ife tikadapanda kulimba popembedza milungu yathu ndithudi iye akadatitembenuza ife kuti tisiye milungu yathu. Koma posakhalitsa iwo adzaona chilango ndipo adzadziwa kuti ndani amene adasochera kwambiri أَرَءَيۡتَ مَنِ ٱتَّخَذَ إِلَٰهَهُۥ هَوَىٰهُ أَفَأَنتَ تَكُونُ عَلَيۡهِ وَكِيلًا ٤٣Kodi wamuona iye amene amayesa zilakolako zake ngati milungu? Kodi iwe ungakhale munthu wosamalira munthu wotere أَمۡ تَحۡسَبُ أَنَّ أَكۡثَرَهُمۡ يَسۡمَعُونَ أَوۡ يَعۡقِلُونَۚ إِنۡ هُمۡ إِلَّا كَٱلۡأَنۡعَٰمِ بَلۡ هُمۡ أَضَلُّ سَبِيلًا ٤٤Kodi iwe umaganiza kuti ambiri a iwo angathe kumva kapena kuzindikira? Iwo si chinthu china chilichonse koma ali ngati nyama yosochera kwambiri أَلَمۡ تَرَ إِلَىٰ رَبِّكَ كَيۡفَ مَدَّ ٱلظِّلَّ وَلَوۡ شَآءَ لَجَعَلَهُۥ سَاكِنًا ثُمَّ جَعَلۡنَا ٱلشَّمۡسَ عَلَيۡهِ دَلِيلًا ٤٥Kodi iwe siuona mmeneAmbuye wako amatambasulira mthunzi? Mulungu akadafuna, akadaupanga kuti ukhale wokhazikika. Ndipo Ife tapanga dzuwa kukhala chizindikiro chake ثُمَّ قَبَضۡنَٰهُ إِلَيۡنَا قَبۡضًا يَسِيرًا ٤٦Ndipo timaubweretsa kwa Ife mwapang’onopang’onomosavuta وَهُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلَّيۡلَ لِبَاسًا وَٱلنَّوۡمَ سُبَاتًا وَجَعَلَ ٱلنَّهَارَ نُشُورًا ٤٧Ndiyeamenewapanga usiku kukhala chofunda ndi tulo kuti tikhale mpumulo, ndipo wapanga usana kuti uzikhala nthawi yodzuka ndi kumagwira ntchito وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَرۡسَلَ ٱلرِّيَٰحَ بُشۡرَۢا بَيۡنَ يَدَيۡ رَحۡمَتِهِۦۚ وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءً طَهُورًا ٤٨Ndiye amene amatumiza mphepo ngati mthenga wobweretsa chisomo chake ndipo timatumiza madzi abwino kuchokera kumwamba لِّنُحۡـِۧيَ بِهِۦ بَلۡدَةً مَّيۡتًا وَنُسۡقِيَهُۥ مِمَّا خَلَقۡنَآ أَنۡعَٰمًا وَأَنَاسِيَّ كَثِيرًا ٤٩Ndi cholinga choti tipereke moyo ku nthaka imene inali yakufa ndi kuti timwetse zinthu zimene talenga, nyama ndi anthu ambiri وَلَقَدۡ صَرَّفۡنَٰهُ بَيۡنَهُمۡ لِيَذَّكَّرُواْ فَأَبَىٰٓ أَكۡثَرُ ٱلنَّاسِ إِلَّا كُفُورًا ٥٠Ndithudi tawatumizira pakati pawo, kuti akhoza kukumbukira, chisomo cha Mulungu koma anthu ambiri amakana. Ndipo iwo amasankha kusakhulupirira وَلَوۡ شِئۡنَا لَبَعَثۡنَا فِي كُلِّ قَرۡيَةٍ نَّذِيرًا ٥١Chikadakhala chifuniro chathu, tikadautsa wowachenjeza ku mzinda uliwonse فَلَا تُطِعِ ٱلۡكَٰفِرِينَ وَجَٰهِدۡهُم بِهِۦ جِهَادًا كَبِيرًا ٥٢Iwe usawamvere anthu osakhulupirira koma limbana nawo kwambiri pogwiritsa ntchito Korani ino ۞ وَهُوَ ٱلَّذِي مَرَجَ ٱلۡبَحۡرَيۡنِ هَٰذَا عَذۡبٌ فُرَاتٌ وَهَٰذَا مِلۡحٌ أُجَاجٌ وَجَعَلَ بَيۡنَهُمَا بَرۡزَخًا وَحِجۡرًا مَّحۡجُورًا ٥٣Ndiye amene adatumiza nyanja ziwiri, ina yamadzi ozuna ndi abwino pamene ina ndi yamadzi a mchere ndi owawa ndipo adakhazikitsa malire olimba kwambiri pakati pa nyanjazi وَهُوَ ٱلَّذِي خَلَقَ مِنَ ٱلۡمَآءِ بَشَرًا فَجَعَلَهُۥ نَسَبًا وَصِهۡرًاۗ وَكَانَ رَبُّكَ قَدِيرًا ٥٤Ndiye amene adamulenga munthu kuchokera ku madzi ndipo adamupatsa abale chifukwa cha magazi amodzi ndiponso chifukwa cha ukwati. Ndipo Ambuye wako ndiye mwini mphamvu zonse ndipo amachita zimene afuna وَيَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَنفَعُهُمۡ وَلَا يَضُرُّهُمۡۗ وَكَانَ ٱلۡكَافِرُ عَلَىٰ رَبِّهِۦ ظَهِيرًا ٥٥Komabe anthu osakhulupirira amapembedza mafano moonjezerapa Mulungu Mafanowosangathekuwathandiza kapena kuwaononga. Munthu wosakhulupirira amathandiza Satana kuchita zoipa zosakomera Ambuye wake وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا مُبَشِّرًا وَنَذِيرًا ٥٦Ndipo takutumiza iwe ngati wobweretsa nkhani yabwino ndiponso munthu wopereka chenjezo قُلۡ مَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍ إِلَّا مَن شَآءَ أَن يَتَّخِذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ سَبِيلًا ٥٧Nena, “Ine sindili kukupemphani malipiro pa ntchito iyi ayi kupatula kuti iye amene afuna atsatire njira yoyenera yopita kwa Ambuye wake.” وَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱلۡحَيِّ ٱلَّذِي لَا يَمُوتُ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِهِۦۚ وَكَفَىٰ بِهِۦ بِذُنُوبِ عِبَادِهِۦ خَبِيرًا ٥٨Ndipo ika chikhulupiriro chako mwa Iye wa moyo amene sakufa ayi. Ndipo mulemekeze nthawi zonse. Iye ndi okwana chifukwa Iye amadziwa bwinobwino za machimo a akapolo ake ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا فِي سِتَّةِ أَيَّامٍ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ ٱلرَّحۡمَٰنُ فَسۡـَٔلۡ بِهِۦ خَبِيرًا ٥٩Iye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo masiku asanu ndi limodzi. Ndipo atatero adabuka pa chimpando chaufumu, Mwini Chisononi chosatha. Motero mufunse Iye chifukwa amadziwa china chili chonse وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ٱسۡجُدُواْۤ لِلرَّحۡمَٰنِ قَالُواْ وَمَا ٱلرَّحۡمَٰنُ أَنَسۡجُدُ لِمَا تَأۡمُرُنَا وَزَادَهُمۡ نُفُورًا ۩ ٦٠Pamene zimanenedwa kwa iwo kuti, “Lambirani Mwini chisoni chosatha,” Iwo amati; “Kodi Mwini chisoni chosatha ndani? Kodi iwe ufuna kuti ife tizipembedza chilichonse chimene iwe utilamula?” Mawu amenewa amaonjezera kukana kwawo تَبَارَكَ ٱلَّذِي جَعَلَ فِي ٱلسَّمَآءِ بُرُوجًا وَجَعَلَ فِيهَا سِرَٰجًا وَقَمَرًا مُّنِيرًا ٦١Alemekezeke Iye amene adalenga gulu la nyenyezi kumtambo ndipo adalenga dzuwa ndi mwezi wowala وَهُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ خِلۡفَةً لِّمَنۡ أَرَادَ أَن يَذَّكَّرَ أَوۡ أَرَادَ شُكُورًا ٦٢Ndipo ndiye amene amasinthanitsa usiku ndi usana chifukwa cha iye amene afuna kukumbukira kapena afuna kuonetsa kuyamika kwake وَعِبَادُ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلَّذِينَ يَمۡشُونَ عَلَى ٱلۡأَرۡضِ هَوۡنًا وَإِذَا خَاطَبَهُمُ ٱلۡجَٰهِلُونَ قَالُواْ سَلَٰمًا ٦٣Ndipo akapolo a Mwini Chisoni Chosatha ndi iwo amene amayenda modzichepetsa padziko lapansi ndipo ngati mbuli zikawayankhula mwachipongwe iwo amayankha mwaulemu وَٱلَّذِينَ يَبِيتُونَ لِرَبِّهِمۡ سُجَّدًا وَقِيَٰمًا ٦٤Ndipo iwo amene amachezera pamaso pa Ambuye wawo, amagwada ndi kuima وَٱلَّذِينَ يَقُولُونَ رَبَّنَا ٱصۡرِفۡ عَنَّا عَذَابَ جَهَنَّمَۖ إِنَّ عَذَابَهَا كَانَ غَرَامًا ٦٥Amene amanena kuti, “Ambuye wathu! Tichotsereni chilango cha ku Gahena.” Ndithudi chilango chake ndi chosatha إِنَّهَا سَآءَتۡ مُسۡتَقَرًّا وَمُقَامًا ٦٦Ndithudi kumeneko ndi malo wonyansa kupumirako ndiponso malo wonyansa kukhalako وَٱلَّذِينَ إِذَآ أَنفَقُواْ لَمۡ يُسۡرِفُواْ وَلَمۡ يَقۡتُرُواْ وَكَانَ بَيۡنَ ذَٰلِكَ قَوَامًا ٦٧Iwo akamapereka saononga chuma chawo moposa muyeso ndipo saumira koma amakhala pakatikati وَٱلَّذِينَ لَا يَدۡعُونَ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ وَلَا يَقۡتُلُونَ ٱلنَّفۡسَ ٱلَّتِي حَرَّمَ ٱللَّهُ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَلَا يَزۡنُونَۚ وَمَن يَفۡعَلۡ ذَٰلِكَ يَلۡقَ أَثَامًا ٦٨Ndipo anthu amene sapembedza mulungu wina kuonjezera pa Mulungu weniweni ndipo sakupha mzimu umene Mulungu waletsa kupatula mu njira yachilungamo ndipo sachita chigololo. Ndipo aliyense amene achita izi adzalandira chilango يُضَٰعَفۡ لَهُ ٱلۡعَذَابُ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ وَيَخۡلُدۡ فِيهِۦ مُهَانًا ٦٩Chilango chake chidzaonjezedwa kawiri patsiku la kuuka kwa akufa ndipo adzakhala ndi manyazi nthawi zonse إِلَّا مَن تَابَ وَءَامَنَ وَعَمِلَ عَمَلًا صَٰلِحًا فَأُوْلَٰٓئِكَ يُبَدِّلُ ٱللَّهُ سَيِّـَٔاتِهِمۡ حَسَنَٰتٍۗ وَكَانَ ٱللَّهُ غَفُورًا رَّحِيمًا ٧٠Kupatula okhawo amene alapa ndi kukhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, chifukwa potero Mulungu adzasintha zoipa zawo kukhala ntchito zabwino. Ndipo Mulungu amakhululukira ndi wachisoni chosatha وَمَن تَابَ وَعَمِلَ صَٰلِحًا فَإِنَّهُۥ يَتُوبُ إِلَى ٱللَّهِ مَتَابًا ٧١Iye amene alapa ndi kuchita ntchito zabwino, ndithudi, ndiye kuti wabwerera kwa Mulungu وَٱلَّذِينَ لَا يَشۡهَدُونَ ٱلزُّورَ وَإِذَا مَرُّواْ بِٱللَّغۡوِ مَرُّواْ كِرَامًا ٧٢Iwo amene sapereka umboni ku zinthu zabodza ndipo akamadutsa pamalo pamene pakuchitika zinthu zoipa kapena zoletsedwa, iwo amadutsa modzilemekeza وَٱلَّذِينَ إِذَا ذُكِّرُواْ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِمۡ لَمۡ يَخِرُّواْ عَلَيۡهَا صُمًّا وَعُمۡيَانًا ٧٣Amene sanyozera chivumbulutso cha Ambuye wawo ndipo pamene akumbutsidwa za icho sachita ngati kuti iwo ndi a gonthi kapena a khungu وَٱلَّذِينَ يَقُولُونَ رَبَّنَا هَبۡ لَنَا مِنۡ أَزۡوَٰجِنَا وَذُرِّيَّٰتِنَا قُرَّةَ أَعۡيُنٍ وَٱجۡعَلۡنَا لِلۡمُتَّقِينَ إِمَامًا ٧٤Ndipo anthu amene amanena kuti, “Ambuye wathu! Tipatseni chisangalalo mu akazi ndi ana athu ndipo tipangeni ife kukhala atsogoleri a iwo amene amakuopani Inu!” أُوْلَٰٓئِكَ يُجۡزَوۡنَ ٱلۡغُرۡفَةَ بِمَا صَبَرُواْ وَيُلَقَّوۡنَ فِيهَا تَحِيَّةً وَسَلَٰمًا ٧٥Amenewa adzalipidwa Paradiso wa pamwamba chifukwa cha kupirira kwawo. Kumeneko adzalandiridwa ndi malonje abwino mawu amtendere ndi aulemu خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ حَسُنَتۡ مُسۡتَقَرًّا وَمُقَامًا ٧٦Adzakhala kumeneko nthawi zonse ndipo ndi malo abwino kukhalako ndiponso ndi malo abwino opumirako قُلۡ مَا يَعۡبَؤُاْ بِكُمۡ رَبِّي لَوۡلَا دُعَآؤُكُمۡۖ فَقَدۡ كَذَّبۡتُمۡ فَسَوۡفَ يَكُونُ لِزَامَۢا ٧٧Nena “Ambuye wanga amakusamalani inu chifukwa cha mapempheroanuakwa Iyeyekha. Komatsopano, ndithudi, inu mwamukana Iye. Motero chilango chidzakhala chanu mpaka kalekale.”