Millat al-Islam

Chapter 17 · 111 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Israa in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah Al-Israa (1338 reciters)
Meccanسورة الإسراء111 verses

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

سُبۡحَٰنَ ٱلَّذِيٓ أَسۡرَىٰ بِعَبۡدِهِۦ لَيۡلًا مِّنَ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِ إِلَى ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡأَقۡصَا ٱلَّذِي بَٰرَكۡنَا حَوۡلَهُۥ لِنُرِيَهُۥ مِنۡ ءَايَٰتِنَآۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡبَصِيرُ ١Ulemerero ukhale kwa Iye amene adayendetsa kapolo wake nthawi ya usiku kuchoka ku Mzikiti Wolemekezeka kupita ku Mzikiti wakutali umene malo ake ozungulira tidawadalitsa; kuti timuonetse zina za zizindikiro zathu. Ndithudi Iye ndiwakumva ndipo woona zonse وَءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ وَجَعَلۡنَٰهُ هُدًى لِّبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ أَلَّا تَتَّخِذُواْ مِن دُونِي وَكِيلًا ٢Ndipo Ife tidamupatsa Mose Buku ndipo tidalipanga ilo kukhala chilangizo cha ana a Israyeli ponena kuti, “Musasankhe wina aliyense kupatula Ine kukhala wokutetezani.” ذُرِّيَّةَ مَنۡ حَمَلۡنَا مَعَ نُوحٍۚ إِنَّهُۥ كَانَ عَبۡدًا شَكُورًا ٣oh inu ana a iwo amene tidawanyamula pamodzi ndi Nowa! Ndithudi Iye adali kapolo wothokoza kwambiri وَقَضَيۡنَآ إِلَىٰ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ فِي ٱلۡكِتَٰبِ لَتُفۡسِدُنَّ فِي ٱلۡأَرۡضِ مَرَّتَيۡنِ وَلَتَعۡلُنَّ عُلُوًّا كَبِيرًا ٤Ife tidavumbulutsa kwa ana a Israyeli, m’Buku kuti, mosakayika, inu mudzabweretsa chisokonezo padziko kachiwiri ndipo mudzakhala ankhanza ndi odzikweza kwambiri فَإِذَا جَآءَ وَعۡدُ أُولَىٰهُمَا بَعَثۡنَا عَلَيۡكُمۡ عِبَادًا لَّنَآ أُوْلِي بَأۡسٍ شَدِيدٍ فَجَاسُواْ خِلَٰلَ ٱلدِّيَارِۚ وَكَانَ وَعۡدًا مَّفۡعُولًا ٥Ndipo litadza pangano loyamba, Ife tidzakutumizirani akapolo athu a gulu la nkhondo ankhongono zedi. Iwo amalowa m’katikati mwa nyumba zanu. Ndipo linali lonjezo limene linakwaniritsidwa ثُمَّ رَدَدۡنَا لَكُمُ ٱلۡكَرَّةَ عَلَيۡهِمۡ وَأَمۡدَدۡنَٰكُم بِأَمۡوَٰلٍ وَبَنِينَ وَجَعَلۡنَٰكُمۡ أَكۡثَرَ نَفِيرًا ٦Titatero tidakupatsani mphamvu powagonjetsa iwo. Ndipo tidakuonjezerani chuma ndi ana ndipo tidakupangani kukhala anthu ambiri amphamvu إِنۡ أَحۡسَنتُمۡ أَحۡسَنتُمۡ لِأَنفُسِكُمۡۖ وَإِنۡ أَسَأۡتُمۡ فَلَهَاۚ فَإِذَا جَآءَ وَعۡدُ ٱلۡأٓخِرَةِ لِيَسُـُٔواْ وُجُوهَكُمۡ وَلِيَدۡخُلُواْ ٱلۡمَسۡجِدَ كَمَا دَخَلُوهُ أَوَّلَ مَرَّةٍ وَلِيُتَبِّرُواْ مَا عَلَوۡاْ تَتۡبِيرًا ٧Ngati inu muchita zabwino, mukudzichitira nokha ubwinowo, koma ngati muchita zoipa, mukudzichitiranso nokha. Ndipo pamene pangano lomaliza lidza, Ife tidzalola adani anu kuti akumvetseni chisoni ndi kulowa mu Mzikiti wanu monga momwe adaloweramo koyamba ndi kukantha kwenikweni onse amene adawapeza عَسَىٰ رَبُّكُمۡ أَن يَرۡحَمَكُمۡۚ وَإِنۡ عُدتُّمۡ عُدۡنَاۚ وَجَعَلۡنَا جَهَنَّمَ لِلۡكَٰفِرِينَ حَصِيرًا ٨Mwina Ambuye wanu adzakuchitirani chifundo koma ngati inu mubwerera kuuchimo, nafenso tidzabwezera kukanthani. Ife takonza Gahena kukhala ndende ya anthu osakhulupirira إِنَّ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانَ يَهۡدِي لِلَّتِي هِيَ أَقۡوَمُ وَيُبَشِّرُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٱلَّذِينَ يَعۡمَلُونَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ أَنَّ لَهُمۡ أَجۡرًا كَبِيرًا ٩Ndithudi Korani ino imatsogolera ku zinthu zabwino ndipo imawauza anthu okhulupirira, amene amachita zabwino, kuti adzakhala ndi malipiro aakulu وَأَنَّ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ أَعۡتَدۡنَا لَهُمۡ عَذَابًا أَلِيمًا ١٠Ndipo iwo amene sakhulupirira za tsiku lotsiriza Ife tawakonzera chilango chowawa وَيَدۡعُ ٱلۡإِنسَٰنُ بِٱلشَّرِّ دُعَآءَهُۥ بِٱلۡخَيۡرِۖ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ عَجُولًا ١١Ndipo munthu amapempha zoipa monga momwe amapemphera zabwino ndipo munthu ndi wopupuluma وَجَعَلۡنَا ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ ءَايَتَيۡنِۖ فَمَحَوۡنَآ ءَايَةَ ٱلَّيۡلِ وَجَعَلۡنَآ ءَايَةَ ٱلنَّهَارِ مُبۡصِرَةً لِّتَبۡتَغُواْ فَضۡلًا مِّن رَّبِّكُمۡ وَلِتَعۡلَمُواْ عَدَدَ ٱلسِّنِينَ وَٱلۡحِسَابَۚ وَكُلَّ شَيۡءٍ فَصَّلۡنَٰهُ تَفۡصِيلًا ١٢Ndipo tidapanga usiku ndi usana kukhala zizindikiro zathu ziwiri. Ndipo tidakuta chizindikiro chausiku ndi mdima pamene tidaika chizindikiro chamasana kukhala chooneka kuti inu muzifunafuna zabwino zochokera kwa Ambuye wanu, komanso kuti mudziwe kuchuluka kwa zaka ndi chiwerengero. Ndipo zinthu zonse tazifotokoza momveka وَكُلَّ إِنسَٰنٍ أَلۡزَمۡنَٰهُ طَٰٓئِرَهُۥ فِي عُنُقِهِۦۖ وَنُخۡرِجُ لَهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ كِتَٰبًا يَلۡقَىٰهُ مَنشُورًا ١٣Ndipo Ife tidamangirira ntchito za munthu aliyense pakhosi lake ndipo patsiku lachiweruzo tidzamutulutsira buku limene adzalipeze lili lotsekulidwa ٱقۡرَأۡ كِتَٰبَكَ كَفَىٰ بِنَفۡسِكَ ٱلۡيَوۡمَ عَلَيۡكَ حَسِيبًا ١٤werenga Buku lako. Lero pakwana kuti mzimu wako udziwerengere wokha zonse zimene unkachita مَّنِ ٱهۡتَدَىٰ فَإِنَّمَا يَهۡتَدِي لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن ضَلَّ فَإِنَّمَا يَضِلُّ عَلَيۡهَاۚ وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٌ وِزۡرَ أُخۡرَىٰۗ وَمَا كُنَّا مُعَذِّبِينَ حَتَّىٰ نَبۡعَثَ رَسُولًا ١٥Aliyense amene achita zabwino atero podzipulumutsa yekha. Ndipo aliyense amene achita zoipa, atero podzipweteka yekha. Palibe amene adzanyamula katundu wa mnzake. Ndipo Ife sitilanga pokhapokha ngati tatumiza Mtumwi وَإِذَآ أَرَدۡنَآ أَن نُّهۡلِكَ قَرۡيَةً أَمَرۡنَا مُتۡرَفِيهَا فَفَسَقُواْ فِيهَا فَحَقَّ عَلَيۡهَا ٱلۡقَوۡلُ فَدَمَّرۡنَٰهَا تَدۡمِيرًا ١٦Ndipo pamene Ife tifuna kuononga Mzinda, poyamba timatumiza ulamuliro wathu kwa anthu ake opeza bwino. Ndipo iwo amauphwanya, ndipo motero liwu la chilango limatsimikiza pa iwo. Ndipo Ife timauononga kwambiri وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِنَ ٱلۡقُرُونِ مِنۢ بَعۡدِ نُوحٍۗ وَكَفَىٰ بِرَبِّكَ بِذُنُوبِ عِبَادِهِۦ خَبِيرَۢا بَصِيرًا ١٧Kodi ndi mibadwo ingati ya anthu imene taononga pambuyo pa Nowa? Ambuye wako wakwana kukhala Wozindikira ndi woona zolakwa za akapolo ake مَّن كَانَ يُرِيدُ ٱلۡعَاجِلَةَ عَجَّلۡنَا لَهُۥ فِيهَا مَا نَشَآءُ لِمَن نُّرِيدُ ثُمَّ جَعَلۡنَا لَهُۥ جَهَنَّمَ يَصۡلَىٰهَا مَذۡمُومًا مَّدۡحُورًا ١٨Aliyense amene afuna chisangalalo cha msanga Ife timapereka msanga chimene Ife tifuna kwa amene Ife tamufuna. Ndipo pambuyo pake tamukonzera iye Gahena, imene adzalowa monyozedwa ndi mokankhidwa وَمَنۡ أَرَادَ ٱلۡأٓخِرَةَ وَسَعَىٰ لَهَا سَعۡيَهَا وَهُوَ مُؤۡمِنٌ فَأُوْلَٰٓئِكَ كَانَ سَعۡيُهُم مَّشۡكُورًا ١٩Ndipo yense amene afuna moyo umene uli nkudza, ndi kumaugwirira ntchito zake molimbika, ndipo ndi wokhulupirira, amenewo ndi amene ntchito zawo zidzakhala zoyamikidwa كُلًّا نُّمِدُّ هَٰٓؤُلَآءِ وَهَٰٓؤُلَآءِ مِنۡ عَطَآءِ رَبِّكَۚ وَمَا كَانَ عَطَآءُ رَبِّكَ مَحۡظُورًا ٢٠Ife timapereka kuchokera ku mphatso za Ambuye wako. Ndipo mphatso za Ambuye wako sizokanizidwa kwa aliyense ٱنظُرۡ كَيۡفَ فَضَّلۡنَا بَعۡضَهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٍۚ وَلَلۡأٓخِرَةُ أَكۡبَرُ دَرَجَٰتٍ وَأَكۡبَرُ تَفۡضِيلًا ٢١Taona mmene tawalemekezera ena kuposa anzawo ndipo, ndithudi, moyo umene uli nkudza uli ndi ulemu wambiri ndipo ndi waukulu poyerekeza لَّا تَجۡعَلۡ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ فَتَقۡعُدَ مَذۡمُومًا مَّخۡذُولًا ٢٢Musasankhe mulungu wina ndi kumuphatikiza ndi Mulungu weniweni chifukwa mungadzakhale ndi manyazi ndi wopanda wokuthandizani ۞ وَقَضَىٰ رَبُّكَ أَلَّا تَعۡبُدُوٓاْ إِلَّآ إِيَّاهُ وَبِٱلۡوَٰلِدَيۡنِ إِحۡسَٰنًاۚ إِمَّا يَبۡلُغَنَّ عِندَكَ ٱلۡكِبَرَ أَحَدُهُمَآ أَوۡ كِلَاهُمَا فَلَا تَقُل لَّهُمَآ أُفٍّ وَلَا تَنۡهَرۡهُمَا وَقُل لَّهُمَا قَوۡلًا كَرِيمًا ٢٣Ndipo Ambuye wako walamula kuti musapembedze wina aliyense koma Iye yekha. Ndipo kuti muwachitire makolo anu zabwino. Ngati wina wa iwo kapena onse akalamba ali kukhala nanu, musawakalipire ayi, koma muziwayankhula ndi mawu aulemu وَٱخۡفِضۡ لَهُمَا جَنَاحَ ٱلذُّلِّ مِنَ ٱلرَّحۡمَةِ وَقُل رَّبِّ ٱرۡحَمۡهُمَا كَمَا رَبَّيَانِي صَغِيرًا ٢٤Onetsani kudzichepetsa ndi chisoni ndipo munene kuti, “Ambuye wanga! Achitireni chifundo monga momwe iwo adandilerera pamene ine ndidali wamng’ono.” رَّبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِمَا فِي نُفُوسِكُمۡۚ إِن تَكُونُواْ صَٰلِحِينَ فَإِنَّهُۥ كَانَ لِلۡأَوَّٰبِينَ غَفُورًا ٢٥Ambuye wanu amadziwa kwambiri zonse zimene zili m’mitima mwanu. Ngati muli abwino ndithudi Iye ali wokhululukira kwa anthu amene amadza kwa Iye nthawi zonse modzichepetsa ndi kulapa وَءَاتِ ذَا ٱلۡقُرۡبَىٰ حَقَّهُۥ وَٱلۡمِسۡكِينَ وَٱبۡنَ ٱلسَّبِيلِ وَلَا تُبَذِّرۡ تَبۡذِيرًا ٢٦Ndipo apatseni abale anu ndi anthu ovutika gawo lawo lowayenera ndiponso a paulendo amene avutika. Ndipo musapereke chuma chanu moononga إِنَّ ٱلۡمُبَذِّرِينَ كَانُوٓاْ إِخۡوَٰنَ ٱلشَّيَٰطِينِۖ وَكَانَ ٱلشَّيۡطَٰنُ لِرَبِّهِۦ كَفُورًا ٢٧Ndithudi anthu oononga ndi abale a Satana ndipo Satana, kwa Ambuye wake, ndi wosayamika وَإِمَّا تُعۡرِضَنَّ عَنۡهُمُ ٱبۡتِغَآءَ رَحۡمَةٍ مِّن رَّبِّكَ تَرۡجُوهَا فَقُل لَّهُمۡ قَوۡلًا مَّيۡسُورًا ٢٨Ndipo ngati iwe siuwathandiza ndipo uli kuyembekezera chisomo chochokera kwa Ambuye wako, yankhula nawo mwachifundo ndi mawu oleza وَلَا تَجۡعَلۡ يَدَكَ مَغۡلُولَةً إِلَىٰ عُنُقِكَ وَلَا تَبۡسُطۡهَا كُلَّ ٱلۡبَسۡطِ فَتَقۡعُدَ مَلُومًا مَّحۡسُورًا ٢٩Ndipo musakhale oumira kapena opereka moononga chifukwa mungadzudzulidwe kapena kukhala osauka kwambiri إِنَّ رَبَّكَ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ وَيَقۡدِرُۚ إِنَّهُۥ كَانَ بِعِبَادِهِۦ خَبِيرَۢا بَصِيرًا ٣٠Ndithudi Ambuye wako amapereka zambiri kwa aliyense amene wamufuna ndipo amanyalapsa. Ndithudi Iye, kwa akapolo ake, ndi wodziwa ndi woona وَلَا تَقۡتُلُوٓاْ أَوۡلَٰدَكُمۡ خَشۡيَةَ إِمۡلَٰقٍۖ نَّحۡنُ نَرۡزُقُهُمۡ وَإِيَّاكُمۡۚ إِنَّ قَتۡلَهُمۡ كَانَ خِطۡـًٔا كَبِيرًا ٣١Ndipo musawaphe ana anu chifukwa choopa umphawi. Ife timawapatsa zosowa zawo ndi inu nomwe. Ndithudi kuwapha iwo ndi tchimo lalikulu وَلَا تَقۡرَبُواْ ٱلزِّنَىٰٓۖ إِنَّهُۥ كَانَ فَٰحِشَةً وَسَآءَ سَبِيلًا ٣٢Ndipo musayandikire chigololo. Ndithudi icho ndi chonyansa ndiponso njira yoipa وَلَا تَقۡتُلُواْ ٱلنَّفۡسَ ٱلَّتِي حَرَّمَ ٱللَّهُ إِلَّا بِٱلۡحَقِّۗ وَمَن قُتِلَ مَظۡلُومًا فَقَدۡ جَعَلۡنَا لِوَلِيِّهِۦ سُلۡطَٰنًا فَلَا يُسۡرِف فِّي ٱلۡقَتۡلِۖ إِنَّهُۥ كَانَ مَنصُورًا ٣٣Ndipo musaphe wina aliyense amene Mulungu waletsa pokhapokha ngati pali chifukwa chololedwa. Ndipo aliyense amene waphedwa mopanda chilungamo, Ife tamupatsa m’bale wake mphamvu zobwezera kapena kukhululuka pa imfa yake. Koma m’bale wakeyo asapyole muyeso pa kubwezeraku. Ndithudi iye ndi wotetezedwa وَلَا تَقۡرَبُواْ مَالَ ٱلۡيَتِيمِ إِلَّا بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ حَتَّىٰ يَبۡلُغَ أَشُدَّهُۥۚ وَأَوۡفُواْ بِٱلۡعَهۡدِۖ إِنَّ ٱلۡعَهۡدَ كَانَ مَسۡـُٔولًا ٣٤Ndipo musachiyandikire chuma cha mwana wamasiye kupatula ngati muli ndi cholinga chochisamala mpaka pamene mwini wake adzafike pa msinkhu woti akhoza kuchisamalira yekha. Ndipo kwaniritsani lonjezo lililonse. Ndithudi! mudzafunsidwa za lonjezoli وَأَوۡفُواْ ٱلۡكَيۡلَ إِذَا كِلۡتُمۡ وَزِنُواْ بِٱلۡقِسۡطَاسِ ٱلۡمُسۡتَقِيمِۚ ذَٰلِكَ خَيۡرٌ وَأَحۡسَنُ تَأۡوِيلًا ٣٥Ndipo kwaniritsani muyeso pamene muyesa zinthu ndipo yesani mwachilungamo polinga zinthu pa sikelo. Zimenezo ndizo zabwino ndipo ndi mapeto abwino kwambiri وَلَا تَقۡفُ مَا لَيۡسَ لَكَ بِهِۦ عِلۡمٌۚ إِنَّ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡبَصَرَ وَٱلۡفُؤَادَ كُلُّ أُوْلَٰٓئِكَ كَانَ عَنۡهُ مَسۡـُٔولًا ٣٦Ndipo musatsatire zinthu zimene simuzidziwa. Ndithudi kumvera kapena kuyang’ana kapenanso kuganizira kwa mumtima mwa munthu kudzafufuzidwa pa tsiku lachiweruzo وَلَا تَمۡشِ فِي ٱلۡأَرۡضِ مَرَحًاۖ إِنَّكَ لَن تَخۡرِقَ ٱلۡأَرۡضَ وَلَن تَبۡلُغَ ٱلۡجِبَالَ طُولًا ٣٧Ndipo musayende modzitukumula pa dziko lapansi, ndithudi, inu simungathe kuboola nthaka ndi kufika kutalika kwa mapiri كُلُّ ذَٰلِكَ كَانَ سَيِّئُهُۥ عِندَ رَبِّكَ مَكۡرُوهًا ٣٨Kuipa kwa zonsezi sikukondweretsa Ambuye wako ذَٰلِكَ مِمَّآ أَوۡحَىٰٓ إِلَيۡكَ رَبُّكَ مِنَ ٱلۡحِكۡمَةِۗ وَلَا تَجۡعَلۡ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ فَتُلۡقَىٰ فِي جَهَنَّمَ مَلُومًا مَّدۡحُورًا ٣٩Ili ndi gawo la luntha limene Ambuye wako wakuuza iwe. Ndipo usatumikire mulungu wina kuonjezera pa Mulungu weniweni chifukwa mwina iwe ungaponyedwe ku Gahena, modzudzulidwa ndi mokankhidwa أَفَأَصۡفَىٰكُمۡ رَبُّكُم بِٱلۡبَنِينَ وَٱتَّخَذَ مِنَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِنَٰثًاۚ إِنَّكُمۡ لَتَقُولُونَ قَوۡلًا عَظِيمًا ٤٠Kodi Ambuye wanu wakusankhirani inu ana aamuna ndipo wadzisankhira Iye mwini ana aakazi kuchokera kwa Angelo? Ndithudi! Inu mukuyankhula mawu oopsa وَلَقَدۡ صَرَّفۡنَا فِي هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ لِيَذَّكَّرُواْ وَمَا يَزِيدُهُمۡ إِلَّا نُفُورًا ٤١Ndithudi Ife tafotokoza chinthu chilichonse m’Korani iyi kuti iwo achenjezedwe, koma iyo siili kuonjezera chilichonse koma kuipidwa قُل لَّوۡ كَانَ مَعَهُۥٓ ءَالِهَةٌ كَمَا يَقُولُونَ إِذًا لَّٱبۡتَغَوۡاْ إِلَىٰ ذِي ٱلۡعَرۡشِ سَبِيلًا ٤٢Nena, “Kukadakhala kuti kuli milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni, monga momwe akunenera, iyo ikadapeza njira yoti ikhale pafupi ndi Mulungu.” سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يَقُولُونَ عُلُوًّا كَبِيرًا ٤٣Kuyamikidwa ndi kukhala pamwamba, kukhale kwake! Kuchokera ku bodza lalikulu limene iwo ali nkunena تُسَبِّحُ لَهُ ٱلسَّمَٰوَٰتُ ٱلسَّبۡعُ وَٱلۡأَرۡضُ وَمَن فِيهِنَّۚ وَإِن مِّن شَيۡءٍ إِلَّا يُسَبِّحُ بِحَمۡدِهِۦ وَلَٰكِن لَّا تَفۡقَهُونَ تَسۡبِيحَهُمۡۚ إِنَّهُۥ كَانَ حَلِيمًا غَفُورًا ٤٤Miyamba isanu ndi iwiri, dziko lapansi ndi zonse zimene zimakhala m’menemo zimamulemekeza Iye ndipo palibe chinthu chomwe sichimulemekeza Mulungu. Koma inu simumva mayamiko. Ndithudi Iye ndi woleza mtima ndipo ndi wokhululukira nthawi zonse وَإِذَا قَرَأۡتَ ٱلۡقُرۡءَانَ جَعَلۡنَا بَيۡنَكَ وَبَيۡنَ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ حِجَابًا مَّسۡتُورًا ٤٥Pamene iwe umawerenga Korani, Ife timaika, pakati pa iwe ndi iwo amene sakhulupirira za moyo umene uli nkudza tchingo losaoneka وَجَعَلۡنَا عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ أَكِنَّةً أَن يَفۡقَهُوهُ وَفِيٓ ءَاذَانِهِمۡ وَقۡرًاۚ وَإِذَا ذَكَرۡتَ رَبَّكَ فِي ٱلۡقُرۡءَانِ وَحۡدَهُۥ وَلَّوۡاْ عَلَىٰٓ أَدۡبَٰرِهِمۡ نُفُورًا ٤٦Ndipo Ife taika zophimba m’mitima mwawo kuti mwina angaizindikire ndi m’makutu mwawo kuti asaimvetse. Ndipo pamene iwe utchula Ambuye wako yekha mu Korani iwo amatembenuka kuthawa mosangalala نَّحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَا يَسۡتَمِعُونَ بِهِۦٓ إِذۡ يَسۡتَمِعُونَ إِلَيۡكَ وَإِذۡ هُمۡ نَجۡوَىٰٓ إِذۡ يَقُولُ ٱلظَّٰلِمُونَ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا رَجُلًا مَّسۡحُورًا ٤٧Ife timadziwa kwambiri zimene iwo akumva ndi pamene amamvetsera kwa iwe. Ndipo pamene amanong’onezana, taona anthu oipa, amanena kuti: “Inu mukutsatira munthu wolodzedwa.” ٱنظُرۡ كَيۡفَ ضَرَبُواْ لَكَ ٱلۡأَمۡثَالَ فَضَلُّواْ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ سَبِيلًا ٤٨Taona mmene akuperekera zitsanzo zokhudza iwe. Motero iwo asochera ndipo sangathe kupeza njira وَقَالُوٓاْ أَءِذَا كُنَّا عِظَٰمًا وَرُفَٰتًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ خَلۡقًا جَدِيدًا ٤٩Ndipo iwo amati, “Kodi pamene ife tidzasanduka mafupa ndi zidutswa zopereseka kodi tidzaukitsidwanso kukhala chilengedwe chatsopano?” ۞ قُلۡ كُونُواْ حِجَارَةً أَوۡ حَدِيدًا ٥٠Nena, “Khalani miyala kapena zitsulo.” أَوۡ خَلۡقًا مِّمَّا يَكۡبُرُ فِي صُدُورِكُمۡۚ فَسَيَقُولُونَ مَن يُعِيدُنَاۖ قُلِ ٱلَّذِي فَطَرَكُمۡ أَوَّلَ مَرَّةٍۚ فَسَيُنۡغِضُونَ إِلَيۡكَ رُءُوسَهُمۡ وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هُوَۖ قُلۡ عَسَىٰٓ أَن يَكُونَ قَرِيبًا ٥١“Kapena cholengedwa china chimene ndi chachikulu m’mitima mwanu.” Iwo adzati, “Ndani amene adzatibwezeranso?” Nena, “Iye amene adakulengani poyamba.” Ndipo iwo adzapukusa mitu yawo ndipo kwa iwe adzafunsa kuti, “Kodi zimenezi zidzachitika liti?” Nena, “Mwina zili pafupi.” يَوۡمَ يَدۡعُوكُمۡ فَتَسۡتَجِيبُونَ بِحَمۡدِهِۦ وَتَظُنُّونَ إِن لَّبِثۡتُمۡ إِلَّا قَلِيلًا ٥٢Pa tsiku limene Iye adzakuitanani ndipo inu mudzamuyankha ndi matamando ake ndi kumvera, pamenepo inu mudzaganiza kuti simudakhale nthawi yaitali koma yochepa وَقُل لِّعِبَادِي يَقُولُواْ ٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُۚ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ يَنزَغُ بَيۡنَهُمۡۚ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ كَانَ لِلۡإِنسَٰنِ عَدُوًّا مُّبِينًا ٥٣Auze akapolo anga kuti aziyankhula zokhazo zimene zili zabwino. Ndithudi Satana amafesa chidani pakati pawo. Ndithudi Satana, kwa munthu, ndi mdani woonekeratu رَّبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِكُمۡۖ إِن يَشَأۡ يَرۡحَمۡكُمۡ أَوۡ إِن يَشَأۡ يُعَذِّبۡكُمۡۚ وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ عَلَيۡهِمۡ وَكِيلًا ٥٤Ambuye wanu amadziwa kwambiri za inu ndipo ngati Iye afuna adzakuchitirani chifundo kapena ngati Iye afuna adzakulangani. Ndipo Ife sitidakutumize iwe kuti ukhale wowayang’anira iwo ayi وَرَبُّكَ أَعۡلَمُ بِمَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۗ وَلَقَدۡ فَضَّلۡنَا بَعۡضَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ عَلَىٰ بَعۡضٍۖ وَءَاتَيۡنَا دَاوُۥدَ زَبُورًا ٥٥Ambuye wako amadziwa kwambiri zonse zimene zili kumwamba ndi padziko lapansi ndipo, ndithudi, Ife tidalemekeza Aneneri ena kuposa anzawo ndipo kwa Davide, Ife tidamupatsa Buku la Masalimo قُلِ ٱدۡعُواْ ٱلَّذِينَ زَعَمۡتُم مِّن دُونِهِۦ فَلَا يَمۡلِكُونَ كَشۡفَ ٱلضُّرِّ عَنكُمۡ وَلَا تَحۡوِيلًا ٥٦Nena, “Aitaneni onse amene mumadzinyengeza nawo mowonjezera pa Iye. Iwo alibe mphamvu zochotsa mavuto anu kapena kuwasintha ndi kupatsa munthu wina.” أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ يَبۡتَغُونَ إِلَىٰ رَبِّهِمُ ٱلۡوَسِيلَةَ أَيُّهُمۡ أَقۡرَبُ وَيَرۡجُونَ رَحۡمَتَهُۥ وَيَخَافُونَ عَذَابَهُۥٓۚ إِنَّ عَذَابَ رَبِّكَ كَانَ مَحۡذُورًا ٥٧Iwo amene amawapembedza nawonso amafunafuna njira yodziyandikiritsira kwa Ambuye wawo, kuti ndani amene angakhale pafupi kwambiri ndi Mulungu ndipo amafunafuna mtendere wa Mulungu ndikuopa chilango chake. Ndithudi chilango cha Ambuye wako ndi chofuna kuopedwa وَإِن مِّن قَرۡيَةٍ إِلَّا نَحۡنُ مُهۡلِكُوهَا قَبۡلَ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ أَوۡ مُعَذِّبُوهَا عَذَابًا شَدِيدًاۚ كَانَ ذَٰلِكَ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مَسۡطُورًا ٥٨Ndipo palibe mzinda umene Ife sitingauononge kapena kuulanga ndi chilango choopsa tsiku lachiweruzo lisanadze. Izi zidalembedwa m’Buku وَمَا مَنَعَنَآ أَن نُّرۡسِلَ بِٱلۡأٓيَٰتِ إِلَّآ أَن كَذَّبَ بِهَا ٱلۡأَوَّلُونَۚ وَءَاتَيۡنَا ثَمُودَ ٱلنَّاقَةَ مُبۡصِرَةً فَظَلَمُواْ بِهَاۚ وَمَا نُرۡسِلُ بِٱلۡأٓيَٰتِ إِلَّا تَخۡوِيفًا ٥٩Ndipo palibe chimene chimatiletsa Ife kutumiza zizindikiro kupatula kuti anthu a mvula zakale sadazikhulupirire izo. Ndipo kwa anthu a Thamoud, Ife tidawapatsa ngamira yaikazi kukhala chizindikiro chooneka ndi maso komabe iwo adaichitira zoipa. Ndipo Ife sititumiza zizindikiro kupatula ndi cholinga chofuna kuchenjeza ndi kuwachititsa mantha وَإِذۡ قُلۡنَا لَكَ إِنَّ رَبَّكَ أَحَاطَ بِٱلنَّاسِۚ وَمَا جَعَلۡنَا ٱلرُّءۡيَا ٱلَّتِيٓ أَرَيۡنَٰكَ إِلَّا فِتۡنَةً لِّلنَّاسِ وَٱلشَّجَرَةَ ٱلۡمَلۡعُونَةَ فِي ٱلۡقُرۡءَانِۚ وَنُخَوِّفُهُمۡ فَمَا يَزِيدُهُمۡ إِلَّا طُغۡيَٰنًا كَبِيرًا ٦٠Ndipo pamene tidakuuza kuti, “Ndithudi! Ambuye wako wawazungulira anthu. Ndipo Ife sitidapange masomphenya amene tidakuonetsa iwe koma kukhala mayeso kwa anthu chimodzimodzinso mtengo wotembereredwa umene watchulidwa m’Korani. Ife timawachenjeza ndi kuwachititsa mantha koma sizili kuwathandiza koma kuonjezera kusakhulupirira.” وَإِذۡ قُلۡنَا لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ ٱسۡجُدُواْ لِأٓدَمَ فَسَجَدُوٓاْ إِلَّآ إِبۡلِيسَ قَالَ ءَأَسۡجُدُ لِمَنۡ خَلَقۡتَ طِينًا ٦١Ndipo pamene ife tidawauza angelo kuti, “Mugwadireni Adamu.” Onse adamugwadira iye kupatula Satana. Iye adayankha kuti, “Kodi ine ndimugwadire iye amene Inu mudamupanga kuchokera ku dothi?” قَالَ أَرَءَيۡتَكَ هَٰذَا ٱلَّذِي كَرَّمۡتَ عَلَيَّ لَئِنۡ أَخَّرۡتَنِ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ لَأَحۡتَنِكَنَّ ذُرِّيَّتَهُۥٓ إِلَّا قَلِيلًا ٦٢Iye adati, “Mukumuona! Uyu ndiye amene mwamulemekeza kuposa ine ndipo ngati inu mundisunga ndi moyo mpaka patsiku louka kwa akufa, ine ndidzawasokoneza ana ake kupatula ochepa.” قَالَ ٱذۡهَبۡ فَمَن تَبِعَكَ مِنۡهُمۡ فَإِنَّ جَهَنَّمَ جَزَآؤُكُمۡ جَزَآءً مَّوۡفُورًا ٦٣Mulungu adati, “Pita, ndipo aliyense wa iwo amene adzakutsatira, ndithudi, Gahena ndiyo idzakhala malipiro ake ndipo ndi malipiro okwana.” وَٱسۡتَفۡزِزۡ مَنِ ٱسۡتَطَعۡتَ مِنۡهُم بِصَوۡتِكَ وَأَجۡلِبۡ عَلَيۡهِم بِخَيۡلِكَ وَرَجِلِكَ وَشَارِكۡهُمۡ فِي ٱلۡأَمۡوَٰلِ وَٱلۡأَوۡلَٰدِ وَعِدۡهُمۡۚ وَمَا يَعِدُهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ إِلَّا غُرُورًا ٦٤“Ndipo anyengerere amene ungawathe mwa iwo ndi mawu ako, ndipo menyana nawo ndi asirikali ako okwera akavalo ndi oyenda pansi, ndipo gawana nawo chuma ndi ana ndipo alonjeze.” Koma Satana sawalonjeza china chilichonse koma chinyengo إِنَّ عِبَادِي لَيۡسَ لَكَ عَلَيۡهِمۡ سُلۡطَٰنٌۚ وَكَفَىٰ بِرَبِّكَ وَكِيلًا ٦٥“Ndithudi pa akapolo anga angwiro, iwe siudzakhala ndi mphamvu ina iliyonse pa iwo yowasokoneza. Ambuye wako ndi wokwana kukhala Mtetezi.” رَّبُّكُمُ ٱلَّذِي يُزۡجِي لَكُمُ ٱلۡفُلۡكَ فِي ٱلۡبَحۡرِ لِتَبۡتَغُواْ مِن فَضۡلِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ كَانَ بِكُمۡ رَحِيمًا ٦٦Ambuye wanu ndiye amene amayendetsa zombo pa nyanja kuti mufunefune zokoma zake. Ndithudi Iye ali wachisoni ndi inu وَإِذَا مَسَّكُمُ ٱلضُّرُّ فِي ٱلۡبَحۡرِ ضَلَّ مَن تَدۡعُونَ إِلَّآ إِيَّاهُۖ فَلَمَّا نَجَّىٰكُمۡ إِلَى ٱلۡبَرِّ أَعۡرَضۡتُمۡۚ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ كَفُورًا ٦٧Ndipo akakupezani mavuto pamene mulipanyanja, iwoamenemumawapembedzamowonjezera pa Iye amakuthawirani kupatula Iye yekha. Koma ngati Iye akupulumutsani kufika pa mtunda, mumatembenuka. Ndithudi, munthu ndi wamwano أَفَأَمِنتُمۡ أَن يَخۡسِفَ بِكُمۡ جَانِبَ ٱلۡبَرِّ أَوۡ يُرۡسِلَ عَلَيۡكُمۡ حَاصِبًا ثُمَّ لَا تَجِدُواْ لَكُمۡ وَكِيلًا ٦٨Kodi inu muli ndi chikhulupiriro chakuti Iye sangakumizeni m’dera lililonse la pamtunda kapena kuti sangakutumizireni mphepo yamkuntho? Pamenepo inu simudzapeza wina aliyense wokuthandizani أَمۡ أَمِنتُمۡ أَن يُعِيدَكُمۡ فِيهِ تَارَةً أُخۡرَىٰ فَيُرۡسِلَ عَلَيۡكُمۡ قَاصِفًا مِّنَ ٱلرِّيحِ فَيُغۡرِقَكُم بِمَا كَفَرۡتُمۡ ثُمَّ لَا تَجِدُواْ لَكُمۡ عَلَيۡنَا بِهِۦ تَبِيعًا ٦٩Kapena inu mukukhulupirira kuti sangakubwezereninso m’nyanjamo kachiwiri ndi kukutumizirani mphepo yamkuntho, ndikukumizani chifukwa chakusakhulupirira kwanu ndipo kuti inu simudzapeza wokuthandizani polimbana ndi Ife ۞ وَلَقَدۡ كَرَّمۡنَا بَنِيٓ ءَادَمَ وَحَمَلۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِ وَرَزَقۡنَٰهُم مِّنَ ٱلطَّيِّبَٰتِ وَفَضَّلۡنَٰهُمۡ عَلَىٰ كَثِيرٍ مِّمَّنۡ خَلَقۡنَا تَفۡضِيلًا ٧٠Ndithudi Ife tawalemekeza ana a Adamu, ndipo Ife tawanyamula pamtunda ndi pa nyanja ndipo tawapatsa zinthu zabwino ndiponso tawalemekeza kuposa zina zimene talenga ndi ulemu wapadera يَوۡمَ نَدۡعُواْ كُلَّ أُنَاسِۭ بِإِمَٰمِهِمۡۖ فَمَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِيَمِينِهِۦ فَأُوْلَٰٓئِكَ يَقۡرَءُونَ كِتَٰبَهُمۡ وَلَا يُظۡلَمُونَ فَتِيلًا ٧١Ndipo kumbukira tsiku limene tidzaitana mtundu uliwonse wa anthu pamodzi ndi Atsogoleri awo. Ndipo yemwe adzapatsidwa Buku lake ku dzanja lamanja iwo adzawerenga Bukulo mwa chisangalalo ndipo sadzaponderezedwa ngakhale ndi pang’onong’ono pomwe وَمَن كَانَ فِي هَٰذِهِۦٓ أَعۡمَىٰ فَهُوَ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ أَعۡمَىٰ وَأَضَلُّ سَبِيلًا ٧٢Koma iye amene ali wakhungu m’moyo uno adzakhalanso wakhungu m’moyo umene uli nkudza ndipo adzasochera kwambiri وَإِن كَادُواْ لَيَفۡتِنُونَكَ عَنِ ٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ لِتَفۡتَرِيَ عَلَيۡنَا غَيۡرَهُۥۖ وَإِذًا لَّٱتَّخَذُوكَ خَلِيلًا ٧٣Ndithudi iwo adali pafupi kuti akusokoneze ku zimene takuvumbulutsira iwe kuti utinamizire zina ndipo zikadatero akadakupala ubwenzi وَلَوۡلَآ أَن ثَبَّتۡنَٰكَ لَقَدۡ كِدتَّ تَرۡكَنُ إِلَيۡهِمۡ شَيۡـًٔا قَلِيلًا ٧٤Ngati Ife tikadapanda kulimbikitsa chikhulupiriro chako, padatsala pang’ono kuti uwatsatire إِذًا لَّأَذَقۡنَٰكَ ضِعۡفَ ٱلۡحَيَوٰةِ وَضِعۡفَ ٱلۡمَمَاتِ ثُمَّ لَا تَجِدُ لَكَ عَلَيۡنَا نَصِيرًا ٧٥Ndipo zikadatero Ife tikadakulawitsa chilango chachikulu m’moyo uno ndi chilango chachikulu m’moyo umene uli nkudza. Kotero siukadapeza wina aliyense wokuthandiza ku mkwiyo wathu وَإِن كَادُواْ لَيَسۡتَفِزُّونَكَ مِنَ ٱلۡأَرۡضِ لِيُخۡرِجُوكَ مِنۡهَاۖ وَإِذًا لَّا يَلۡبَثُونَ خِلَٰفَكَ إِلَّا قَلِيلًا ٧٦Ndithudi adatsala pang’ono kukuchititsa mantha m’dziko ndi cholinga choti akuchotse m’menemo. Zikadatheka kutero iwo sakadakhala pambuyo pako, koma kwa kanthawi kochepa سُنَّةَ مَن قَدۡ أَرۡسَلۡنَا قَبۡلَكَ مِن رُّسُلِنَاۖ وَلَا تَجِدُ لِسُنَّتِنَا تَحۡوِيلًا ٧٧Umenewu ndiwo mwambo wa Atumwi amene tidatumiza iwe usanadze ndipo iwe siudzapeza kusintha kulikonse m’mwambo wathu أَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ لِدُلُوكِ ٱلشَّمۡسِ إِلَىٰ غَسَقِ ٱلَّيۡلِ وَقُرۡءَانَ ٱلۡفَجۡرِۖ إِنَّ قُرۡءَانَ ٱلۡفَجۡرِ كَانَ مَشۡهُودًا ٧٨Chita mapemphero kuyambira nthawi yopendekera dzuwakufikirausikundipowerenga Koranim’mapemphero a m’mbandakucha. Ndithudi kuwerenga Korani nthawi ya m’mbandakucha kumachitilidwa umboni وَمِنَ ٱلَّيۡلِ فَتَهَجَّدۡ بِهِۦ نَافِلَةً لَّكَ عَسَىٰٓ أَن يَبۡعَثَكَ رَبُّكَ مَقَامًا مَّحۡمُودًا ٧٩Ndipo m’kati mwa usiku, pemphera ndi kuwerenga Korani ndi mapemphero oonjezera kwa iwe. Mwina Ambuye wako angadzakuike pamalo wotamandika وَقُل رَّبِّ أَدۡخِلۡنِي مُدۡخَلَ صِدۡقٍ وَأَخۡرِجۡنِي مُخۡرَجَ صِدۡقٍ وَٱجۡعَل لِّي مِن لَّدُنكَ سُلۡطَٰنًا نَّصِيرًا ٨٠Nena, “Ambuye ndilowetseni kulowa kwa bwino ndipo nditulutseni mwaubwino. Ndipo ndipatseni kuchokera kwa Inu mphamvu yondithandiza.” وَقُلۡ جَآءَ ٱلۡحَقُّ وَزَهَقَ ٱلۡبَٰطِلُۚ إِنَّ ٱلۡبَٰطِلَ كَانَ زَهُوقًا ٨١Nena, “Choonadi chadza ndipo bodza latha. Ndithudi bodza liyenera kutha.” وَنُنَزِّلُ مِنَ ٱلۡقُرۡءَانِ مَا هُوَ شِفَآءٌ وَرَحۡمَةٌ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ وَلَا يَزِيدُ ٱلظَّٰلِمِينَ إِلَّا خَسَارًا ٨٢Ndipo titumiza kuchokera m’Korani mankhwala ochiza ndiponso chisoni kwa onse okhulupirira, ndipo imaonjezera kwa anthu osakhulupirira chionongeko وَإِذَآ أَنۡعَمۡنَا عَلَى ٱلۡإِنسَٰنِ أَعۡرَضَ وَنَـَٔا بِجَانِبِهِۦ وَإِذَا مَسَّهُ ٱلشَّرُّ كَانَ يَـُٔوسًا ٨٣Ndipo tikam’patsa munthu zokoma zathu, iye amatembenuka ndi kuchita mwano ndipo amakhala kutali ndi njira yoyenera. Ndipo zikam’peza zoipa amakhala wotaya mtima kwambiri قُلۡ كُلٌّ يَعۡمَلُ عَلَىٰ شَاكِلَتِهِۦ فَرَبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِمَنۡ هُوَ أَهۡدَىٰ سَبِيلًا ٨٤Nena, “Munthu aliyense amachita molingana ndi chikhalidwe chake koma Ambuye wanu amadziwa yemwe watsogozedwa bwino panjira yachilungamo.” وَيَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلرُّوحِۖ قُلِ ٱلرُّوحُ مِنۡ أَمۡرِ رَبِّي وَمَآ أُوتِيتُم مِّنَ ٱلۡعِلۡمِ إِلَّا قَلِيلًا ٨٥IwoakukufunsazaMzimu.Ndiponena,“Ambuyewanga ndiye amene adziwa za iwo. Ndipo inu simudapatsidwe nzeru koma pang’ono pokha.” وَلَئِن شِئۡنَا لَنَذۡهَبَنَّ بِٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ ثُمَّ لَا تَجِدُ لَكَ بِهِۦ عَلَيۡنَا وَكِيلًا ٨٦Ndithudi Ife tikadafuna, tikadakulanda chimene tavumbulutsa kwa iwe ndipo iwe siukadapeza wina aliyense wokuteteza kwa Ife m’malo mwako إِلَّا رَحۡمَةً مِّن رَّبِّكَۚ إِنَّ فَضۡلَهُۥ كَانَ عَلَيۡكَ كَبِيرًا ٨٧Kupatula chifundo chochokera kwa Ambuye wako, ndithudi ubwino wake pa iwe ndi waukulu zedi قُل لَّئِنِ ٱجۡتَمَعَتِ ٱلۡإِنسُ وَٱلۡجِنُّ عَلَىٰٓ أَن يَأۡتُواْ بِمِثۡلِ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ لَا يَأۡتُونَ بِمِثۡلِهِۦ وَلَوۡ كَانَ بَعۡضُهُمۡ لِبَعۡضٍ ظَهِيرًا ٨٨Nena, “Ngati anthu ndi majini akadagwirizana kubweretsa chofanana ndi Korani ino, iwo sakadabweretsa chofanana nayo ngakhale kuti iwo akadathandizana.” وَلَقَدۡ صَرَّفۡنَا لِلنَّاسِ فِي هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ مِن كُلِّ مَثَلٍ فَأَبَىٰٓ أَكۡثَرُ ٱلنَّاسِ إِلَّا كُفُورًا ٨٩Ndithudi talongosola kwa anthu mu Korani ino chitsanzo chilichonse. Komabe anthu ambiri akana choonadi ndi kukhala osakhulupirira وَقَالُواْ لَن نُّؤۡمِنَ لَكَ حَتَّىٰ تَفۡجُرَ لَنَا مِنَ ٱلۡأَرۡضِ يَنۢبُوعًا ٩٠Iwo amati, “Ife sitidzakukhulupirira iwe mpaka pamene utatitumphutsira kasupe kuchokera pansi.” أَوۡ تَكُونَ لَكَ جَنَّةٌ مِّن نَّخِيلٍ وَعِنَبٍ فَتُفَجِّرَ ٱلۡأَنۡهَٰرَ خِلَٰلَهَا تَفۡجِيرًا ٩١“Kapena utakhala ndi munda wa tende ndi mphesa ndipo m’kati mwake utumphutse mitsinjeyaikulu.” أَوۡ تُسۡقِطَ ٱلسَّمَآءَ كَمَا زَعَمۡتَ عَلَيۡنَا كِسَفًا أَوۡ تَأۡتِيَ بِٱللَّهِ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ قَبِيلًا ٩٢“Kapenaugwetsemtambopaifemonga momwe udatilonjezera kapena utibweretsere Mulungu pamodzi ndi angelo pamaso pathu.” أَوۡ يَكُونَ لَكَ بَيۡتٌ مِّن زُخۡرُفٍ أَوۡ تَرۡقَىٰ فِي ٱلسَّمَآءِ وَلَن نُّؤۡمِنَ لِرُقِيِّكَ حَتَّىٰ تُنَزِّلَ عَلَيۡنَا كِتَٰبًا نَّقۡرَؤُهُۥۗ قُلۡ سُبۡحَانَ رَبِّي هَلۡ كُنتُ إِلَّا بَشَرًا رَّسُولًا ٩٣“Kapena ukhale ndi nyumba yokongoletsedwa bwino kwambiri kapena ukwere kumwamba. Komabe ife sitidzakukhulupirira kukwera kwako mpaka pamene utatitsitsira ife Buku kuti tiziwerenga.” Nena, “Alemekezeke Ambuye wanga! Ndithudi ine sindine aliyense koma munthu amene watumizidwa ngati Mtumwi.” وَمَا مَنَعَ ٱلنَّاسَ أَن يُؤۡمِنُوٓاْ إِذۡ جَآءَهُمُ ٱلۡهُدَىٰٓ إِلَّآ أَن قَالُوٓاْ أَبَعَثَ ٱللَّهُ بَشَرًا رَّسُولًا ٩٤Ndipo palibe chimene chidawaletsa anthu kukhala okhulupirira pamene malangizo adadza kwa iwo koma mwano chifukwa iwo amati, “Kodi Mulungu watumiza munthu kukhala Mtumwi?” قُل لَّوۡ كَانَ فِي ٱلۡأَرۡضِ مَلَٰٓئِكَةٌ يَمۡشُونَ مُطۡمَئِنِّينَ لَنَزَّلۡنَا عَلَيۡهِم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ مَلَكًا رَّسُولًا ٩٥Nena, “Ngati angelo akadakhala pa dziko lapansi, namayenda mwamtendere, ndithudi, Ife tikadatumiza kwa iwo mngelo kuchoka kumwamba ngati Mtumwi.” قُلۡ كَفَىٰ بِٱللَّهِ شَهِيدَۢا بَيۡنِي وَبَيۡنَكُمۡۚ إِنَّهُۥ كَانَ بِعِبَادِهِۦ خَبِيرَۢا بَصِيرًا ٩٦Nena, “Mulungu ndi wokwana kukhala mboni pakati pa ine ndi inu. Ndithudi! Iye ndi wodziwa ndi woona zonse za akapolo ake.” وَمَن يَهۡدِ ٱللَّهُ فَهُوَ ٱلۡمُهۡتَدِۖ وَمَن يُضۡلِلۡ فَلَن تَجِدَ لَهُمۡ أَوۡلِيَآءَ مِن دُونِهِۦۖ وَنَحۡشُرُهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ عَلَىٰ وُجُوهِهِمۡ عُمۡيًا وَبُكۡمًا وَصُمًّاۖ مَّأۡوَىٰهُمۡ جَهَنَّمُۖ كُلَّمَا خَبَتۡ زِدۡنَٰهُمۡ سَعِيرًا ٩٧Ndipo aliyense amene Mulungu wamutsogolera , atsogozedwa bwino koma iye amene Iye amusocheza wotere iwe siungamupezere mtetezi wina aliyense kupatula Iye yekha. Ndipo Ife tidzawasonkhanitsa onse pa tsiku la kuuka kwa akufa, akuyenda pa nkhope zawo, akhungu, abububu ndi agonthi, malo awo adzakhala Gahena ndipo pamene malawi ake azikazima tizidzawaonjezera moto ذَٰلِكَ جَزَآؤُهُم بِأَنَّهُمۡ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَقَالُوٓاْ أَءِذَا كُنَّا عِظَٰمًا وَرُفَٰتًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ خَلۡقًا جَدِيدًا ٩٨Amenewo ndiwo malipiro awo chifukwa iwo sadakhulupirire mawu athu ndipo adati, “Pamene ife tidzasanduka mafupa ndi kufufutika, kodi tidzaukitsidwa kukhala chilengedwe chatsopano?” ۞ أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّ ٱللَّهَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ قَادِرٌ عَلَىٰٓ أَن يَخۡلُقَ مِثۡلَهُمۡ وَجَعَلَ لَهُمۡ أَجَلًا لَّا رَيۡبَ فِيهِ فَأَبَى ٱلظَّٰلِمُونَ إِلَّا كُفُورًا ٩٩Kodi iwo saona kuti Mulungu amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ali ndi mphamvu yolenga zofanana ndi iwo? Ndipo Iye adawaikira iwo nthawi yosakayikitsa. Komabe anthu ochimwa amakana choonadi ndikusankha kusakhulupirira قُل لَّوۡ أَنتُمۡ تَمۡلِكُونَ خَزَآئِنَ رَحۡمَةِ رَبِّيٓ إِذًا لَّأَمۡسَكۡتُمۡ خَشۡيَةَ ٱلۡإِنفَاقِۚ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ قَتُورًا ١٠٠Nena, “Ngati mukadakhala ndi nkhokwe za chifundo cha Ambuye wanga, ndithudi, inu mukanazibisa poopa kuti zingathe.” Ndithudi munthu ndi waumbombo وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَىٰ تِسۡعَ ءَايَٰتِۭ بَيِّنَٰتٍۖ فَسۡـَٔلۡ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ إِذۡ جَآءَهُمۡ فَقَالَ لَهُۥ فِرۡعَوۡنُ إِنِّي لَأَظُنُّكَ يَٰمُوسَىٰ مَسۡحُورًا ١٠١Ndithudi Ife tidamupatsa Mose zizindikiro zisanu ndi zinayi zooneka. Afunse ana a Israyeli pamene iye adadza kwa iwo ndipo Farawo adati kwa iye, “Iwe Mose, ndithudi, ine ndili kukuganizira kuti ndiwe wolodzedwa.” قَالَ لَقَدۡ عَلِمۡتَ مَآ أَنزَلَ هَٰٓؤُلَآءِ إِلَّا رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ بَصَآئِرَ وَإِنِّي لَأَظُنُّكَ يَٰفِرۡعَوۡنُ مَثۡبُورًا ١٠٢Iye adati, “Ndithudi iwe uli kudziwa bwinobwino kuti zizindikiro izi sizinatumizidwe ndi wina koma Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ngati umboni wooneka ndi maso. Ndipo, ndithudi, ine ndiganiza kuti iwe, Farawo, ndiwe woonongeka.” فَأَرَادَ أَن يَسۡتَفِزَّهُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ فَأَغۡرَقۡنَٰهُ وَمَن مَّعَهُۥ جَمِيعًا ١٠٣Farawo anafunitsitsa kuti awapirikitse m’dziko. Koma Ife tidamumiza pamodzi ndi onse amene adali naye وَقُلۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِۦ لِبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱسۡكُنُواْ ٱلۡأَرۡضَ فَإِذَا جَآءَ وَعۡدُ ٱلۡأٓخِرَةِ جِئۡنَا بِكُمۡ لَفِيفًا ١٠٤Ndipo pambuyo pake Ife tidati kwa ana a Israyeli, “Khalani m’dziko ndipo pamene lonjezo lomaliza lidzadza, Ife tidzakusonkhanitsani kukhala malo amodzi.” وَبِٱلۡحَقِّ أَنزَلۡنَٰهُ وَبِٱلۡحَقِّ نَزَلَۗ وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا مُبَشِّرًا وَنَذِيرًا ١٠٥Ifetavumbulutsa Bukula Koranim’choonadindipondi m’choonadi latsika. Ndipo Ife takutumiza iwe osati wina kuti ukalalikire nkhani za bwino ndi kupereka chenjezo وَقُرۡءَانًا فَرَقۡنَٰهُ لِتَقۡرَأَهُۥ عَلَى ٱلنَّاسِ عَلَىٰ مُكۡثٍ وَنَزَّلۡنَٰهُ تَنزِيلًا ١٠٦Ndi Buku la Korani limene tagawa m’zigawo kuti iwe uwerenge kwa anthu mwakanthawi. Ife talivumbulutsa pang’onopang’ono قُلۡ ءَامِنُواْ بِهِۦٓ أَوۡ لَا تُؤۡمِنُوٓاْۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ مِن قَبۡلِهِۦٓ إِذَا يُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ يَخِرُّونَۤ لِلۡأَذۡقَانِۤ سُجَّدًاۤ ١٠٧Nena, “Zili kwa inu kulikhulupirira kapena kusalikhulupirira. Ndithudi! Iwo amene adapatsidwa nzeru ilo lisadadze, likamawerengedwa kwa iwo, amagwetsa mphumi zawo pansi.” وَيَقُولُونَ سُبۡحَٰنَ رَبِّنَآ إِن كَانَ وَعۡدُ رَبِّنَا لَمَفۡعُولًا ١٠٨Ndipo iwo amati, “Ulemerero ndi wa Ambuye wathu! Ndithudi lonjezo la Ambuye wathu likwaniritsidwe.” وَيَخِرُّونَ لِلۡأَذۡقَانِ يَبۡكُونَ وَيَزِيدُهُمۡ خُشُوعًا ۩ ١٠٩Ndipo iwo amagwa pansi pa zipumi zawo, ali kulira ndipo limawaonjezera kudzichepetsa قُلِ ٱدۡعُواْ ٱللَّهَ أَوِ ٱدۡعُواْ ٱلرَّحۡمَٰنَۖ أَيًّا مَّا تَدۡعُواْ فَلَهُ ٱلۡأَسۡمَآءُ ٱلۡحُسۡنَىٰۚ وَلَا تَجۡهَرۡ بِصَلَاتِكَ وَلَا تُخَافِتۡ بِهَا وَٱبۡتَغِ بَيۡنَ ذَٰلِكَ سَبِيلًا ١١٠Nena, “Muitaneni Mulungu kapena Mwini chifundo chosatha, m’dzina lililonse limene mungamuitanire, chifukwa Iye ali ndi mayina abwino. Ndipo musanene mapemphero anu mokweza kapena motsitsa koma sankhani mawu a pakati ndi pakati.” وَقُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي لَمۡ يَتَّخِذۡ وَلَدًا وَلَمۡ يَكُن لَّهُۥ شَرِيكٌ فِي ٱلۡمُلۡكِ وَلَمۡ يَكُن لَّهُۥ وَلِيٌّ مِّنَ ٱلذُّلِّۖ وَكَبِّرۡهُ تَكۡبِيرَۢا ١١١Nena, “Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu, amene sanabale mwana wamwamuna ndipo alibe mnzake womuthandiza mu Ufumu wake, ndipo Iye siwopanda mphamvu kuti angakhale ndi womuthandiza. Motero mulemekezeni Iye ndi ulemu woyenera Iye yekha.”

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.