Millat al-Islam

Chapter 70 · 44 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Maarij in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah Al-Maarij (1275 reciters)

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

سَأَلَ سَآئِلُۢ بِعَذَابٍ وَاقِعٍ ١Wofunsa adafunsa za chilango chimene chichitike لِّلۡكَٰفِرِينَ لَيۡسَ لَهُۥ دَافِعٌ ٢Pa anthu onse osakhulupirira, chimene wina sangachiletse مِّنَ ٱللَّهِ ذِي ٱلۡمَعَارِجِ ٣Kuchokera kwa Ambuye, Mwini njira zokwerera kumwamba تَعۡرُجُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ وَٱلرُّوحُ إِلَيۡهِ فِي يَوۡمٍ كَانَ مِقۡدَارُهُۥ خَمۡسِينَ أَلۡفَ سَنَةٍ ٤Angelo ndi Mzimu amakwera kupita kwa Iye mtsiku limodzi limene lingafanizidwe ndi zaka zikwi makumi asanu فَٱصۡبِرۡ صَبۡرًا جَمِيلًا ٥Kotero pirira kupilira kwabwino إِنَّهُمۡ يَرَوۡنَهُۥ بَعِيدًا ٦Ndithudi! Iwo amaona kuti ili patali وَنَرَىٰهُ قَرِيبًا ٧Koma Ife tili kuliona lili pafupi يَوۡمَ تَكُونُ ٱلسَّمَآءُ كَٱلۡمُهۡلِ ٨Tsiku limene kumwamba kudzaoneka ngati mkuwa wachiphalaphala وَتَكُونُ ٱلۡجِبَالُ كَٱلۡعِهۡنِ ٩Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya wouluka وَلَا يَسۡـَٔلُ حَمِيمٌ حَمِيمًا ١٠Ndipo palibe bwenzi amene adzafunse za bwenzi lake يُبَصَّرُونَهُمۡۚ يَوَدُّ ٱلۡمُجۡرِمُ لَوۡ يَفۡتَدِي مِنۡ عَذَابِ يَوۡمِئِذِۭ بِبَنِيهِ ١١Iwo azidzawaona iwo. Munthu wochita zoipa adzafunitsitsa kuti mwina akhoza kudzipulumutsa ku chilango cha tsikuli popereka ana ake وَصَٰحِبَتِهِۦ وَأَخِيهِ ١٢Ndi mkazi wake ndi m’bale wake وَفَصِيلَتِهِ ٱلَّتِي تُـٔۡوِيهِ ١٣Ndi anansi ake amene adamusunga وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ جَمِيعًا ثُمَّ يُنجِيهِ ١٤Ndipo zonse zimene zili padziko lapansi kuti mwina zikhoza kumupulumutsa كـَلَّآۖ إِنَّهَا لَظَىٰ ١٥Kosatheka! Ndithudi udzakhala moto wa lawilawi wa ku Gahena نَزَّاعَةً لِّلشَّوَىٰ ١٦wotentha mutu wonse تَدۡعُواْ مَنۡ أَدۡبَرَ وَتَوَلَّىٰ ١٧Udzaitana aliyense amene amakana choonadi وَجَمَعَ فَأَوۡعَىٰٓ ١٨Ndipo amangopanga chuma ndi kuchisunga ۞ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ خُلِقَ هَلُوعًا ١٩Ndithudi Munthu adalengedwa kukhala wosapirira إِذَا مَسَّهُ ٱلشَّرُّ جَزُوعًا ٢٠Amakhala modandaula ngati mavuto amupeza وَإِذَا مَسَّهُ ٱلۡخَيۡرُ مَنُوعًا ٢١Ndipo amachita mwano ngati apeza zabwino إِلَّا ٱلۡمُصَلِّينَ ٢٢Kupatula okhawo amene amapemphera Al Ma’arij 619 nthawi zonse ٱلَّذِينَ هُمۡ عَلَىٰ صَلَاتِهِمۡ دَآئِمُونَ ٢٣Iwo amene amapemphera mowirikiza وَٱلَّذِينَ فِيٓ أَمۡوَٰلِهِمۡ حَقٌّ مَّعۡلُومٌ ٢٤Ndi iwo amene m’chuma chawo muli gawo limene amasiya padera لِّلسَّآئِلِ وَٱلۡمَحۡرُومِ ٢٥Kuti apereke kwa anthu opempha ndi amene ali pa mavuto وَٱلَّذِينَ يُصَدِّقُونَ بِيَوۡمِ ٱلدِّينِ ٢٦Ndi iwo amene amakhulupirira kuti kudzakhala tsiku lachiweruzo وَٱلَّذِينَ هُم مِّنۡ عَذَابِ رَبِّهِم مُّشۡفِقُونَ ٢٧Ndi iwo amene amachita mantha ndi chilango cha Ambuye wawo إِنَّ عَذَابَ رَبِّهِمۡ غَيۡرُ مَأۡمُونٍ ٢٨Ndithudi chilango cha Ambuye ndi chosatetezeka وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِفُرُوجِهِمۡ حَٰفِظُونَ ٢٩Ndi iwo amene amadzisunga إِلَّا عَلَىٰٓ أَزۡوَٰجِهِمۡ أَوۡ مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُهُمۡ فَإِنَّهُمۡ غَيۡرُ مَلُومِينَ ٣٠Kupatula akazi awo ndi akapolo awo chifukwa iwo sadzadzudzulidwa فَمَنِ ٱبۡتَغَىٰ وَرَآءَ ذَٰلِكَ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡعَادُونَ ٣١Koma aliyense amene afuna kuposa awa, ndi wophwanya malamulo وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِأَمَٰنَٰتِهِمۡ وَعَهۡدِهِمۡ رَٰعُونَ ٣٢Ndi iwo amene amasunga malonjezo ndi malamulo awo وَٱلَّذِينَ هُم بِشَهَٰدَٰتِهِمۡ قَآئِمُونَ ٣٣Ndi iwo amene amapereka umboni woona nthawi zonse وَٱلَّذِينَ هُمۡ عَلَىٰ صَلَاتِهِمۡ يُحَافِظُونَ ٣٤Ndi iwo amene amalabadira mapemphero awo أُوْلَٰٓئِكَ فِي جَنَّٰتٍ مُّكۡرَمُونَ ٣٥Awa ndiwo amene adzalemekezeka m’minda ya Paradiso فَمَالِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ قِبَلَكَ مُهۡطِعِينَ ٣٦Kodi chachitika ndi chiyani kwa anthu osakhulupirira kuti azibwera mwaliwiro kudza kwa iwe عَنِ ٱلۡيَمِينِ وَعَنِ ٱلشِّمَالِ عِزِينَ ٣٧Kuchokera kumbali ya dzanja lamanja ndi mbali yakumanzere mu unyinji wawo أَيَطۡمَعُ كُلُّ ٱمۡرِيٍٕ مِّنۡهُمۡ أَن يُدۡخَلَ جَنَّةَ نَعِيمٍ ٣٨Kodi aliyense wa iwo amayembekeza kukalowa m’munda wa chisangalalo كـَلَّآۖ إِنَّا خَلَقۡنَٰهُم مِّمَّا يَعۡلَمُونَ ٣٩Kosatheka! Ndithudi Ife tawalenga kuchokera ku chinthu chimene sachidziwa فَلَآ أُقۡسِمُ بِرَبِّ ٱلۡمَشَٰرِقِ وَٱلۡمَغَٰرِبِ إِنَّا لَقَٰدِرُونَ ٤٠Motero, Ine ndilumbira pa Ambuye wa malo onse a kum’mawa ndi kumadzulo kuti Ife tikhoza عَلَىٰٓ أَن نُّبَدِّلَ خَيۡرًا مِّنۡهُمۡ وَمَا نَحۡنُ بِمَسۡبُوقِينَ ٤١Kuika anthu ena abwino m’malo mwawo ndipo palibe chinthu chimene chingatiletse kutero فَذَرۡهُمۡ يَخُوضُواْ وَيَلۡعَبُواْ حَتَّىٰ يُلَٰقُواْ يَوۡمَهُمُ ٱلَّذِي يُوعَدُونَ ٤٢Motero asiye ayambe adzinyenga ndi chisangalalo mpaka pamene adzakumana ndi tsiku lawo limene adalonjezedwa يَوۡمَ يَخۡرُجُونَ مِنَ ٱلۡأَجۡدَاثِ سِرَاعًا كَأَنَّهُمۡ إِلَىٰ نُصُبٍ يُوفِضُونَ ٤٣Tsiku limene adzatuluka mwansanga m’manda mwawo ngati anthu a pa mpikisano umene amalandirirapo mphotho خَٰشِعَةً أَبۡصَٰرُهُمۡ تَرۡهَقُهُمۡ ذِلَّةٌۚ ذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمُ ٱلَّذِي كَانُواْ يُوعَدُونَ ٤٤Atayang’ana maso awo pansi ndipo adzachititsidwa manyazi. Limeneli ndilo tsiku limene analonjezedwa

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.