Millat al-Islam

Chapter 56 · 96 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Waqi'a in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah Al-Waqi'a (1348 reciters)

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

إِذَا وَقَعَتِ ٱلۡوَاقِعَةُ ١Pamene ola la chiweruzo lidza لَيۡسَ لِوَقۡعَتِهَا كَاذِبَةٌ ٢Ndipo palibe mzimu umene udzakana kudza kwake خَافِضَةٌ رَّافِعَةٌ ٣Kutsitsa gulu lina ndikukweza gulu linzake إِذَا رُجَّتِ ٱلۡأَرۡضُ رَجًّا ٤Pamene dziko lidzagwedezeka ndi chigwedezo choopsya وَبُسَّتِ ٱلۡجِبَالُ بَسًّا ٥Ndi pamene mapiri adzafumbutuka kukhala fumbi lokhalokha فَكَانَتۡ هَبَآءً مُّنۢبَثًّا ٦Motero iwo adzakhala fumbi louluzika paliponse وَكُنتُمۡ أَزۡوَٰجًا ثَلَٰثَةً ٧Ndipo inu mudzagawidwa m’magulu atatu فَأَصۡحَٰبُ ٱلۡمَيۡمَنَةِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَيۡمَنَةِ ٨Iwo a ku dzanja la manja. Kodi a ku dzanja la manja adzakhala ndani وَأَصۡحَٰبُ ٱلۡمَشۡـَٔمَةِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡمَشۡـَٔمَةِ ٩Iwo akudzanja la mazere. Kodi akudzanja la mazere adzakhala ndani وَٱلسَّٰبِقُونَ ٱلسَّٰبِقُونَ ١٠Ndipo gulu la iwo amene adzakhala kutsogolo m’chikhulupiriro adzakhala kutsogolo m’moyo umene uli nkudza أُوْلَٰٓئِكَ ٱلۡمُقَرَّبُونَ ١١Awa ndiwo amene adzakhala kufupi ndi Mulungu فِي جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ ١٢M’minda ya Paradiso ثُلَّةٌ مِّنَ ٱلۡأَوَّلِينَ ١٣Gulu lalikulu lidzachokera ku mibadwo ya kale وَقَلِيلٌ مِّنَ ٱلۡأٓخِرِينَ ١٤Ndi gulu lochepa lidzachokera ku mibadwo ya m’mbuyo mwake عَلَىٰ سُرُرٍ مَّوۡضُونَةٍ ١٥Iwo adzakhala pa mipando yawofowofo yomatidwa golide ndi miyala ya mtengo wapatali مُّتَّكِـِٔينَ عَلَيۡهَا مُتَقَٰبِلِينَ ١٦Atakhala pa iyo ndi kumayang’anizana يَطُوفُ عَلَيۡهِمۡ وِلۡدَٰنٌ مُّخَلَّدُونَ ١٧Iwo adzatumikiridwa ndi anyamata a muyaya بِأَكۡوَابٍ وَأَبَارِيقَ وَكَأۡسٍ مِّن مَّعِينٍ ١٨Ndi mabakuli, miphika ndi zikho za vinyo wabwino لَّا يُصَدَّعُونَ عَنۡهَا وَلَا يُنزِفُونَ ١٩Amene sadzawawitsa mitu yawo kapena kuwatopetsa وَفَٰكِهَةٍ مِّمَّا يَتَخَيَّرُونَ ٢٠Ndi zipatso zimene adzasankhepo وَلَحۡمِ طَيۡرٍ مِّمَّا يَشۡتَهُونَ ٢١Ndi nyama ya nkhuku imene angafune وَحُورٌ عِينٌ ٢٢Ndipo padzakhala anzawo okongola, a maso akulu ndi ochititsa kaso كَأَمۡثَٰلِ ٱللُّؤۡلُوِٕ ٱلۡمَكۡنُونِ ٢٣Monga ndolo zosamalidwa bwino جَزَآءَۢ بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ٢٤Malipiro a ntchito zimene adachita kale لَا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوًا وَلَا تَأۡثِيمًا ٢٥Palibe nkhani zopanda pake kapena zolaula zimene adzamva إِلَّا قِيلًا سَلَٰمًا سَلَٰمًا ٢٦Kupatula mawu akuti Mtendere, Mtendere وَأَصۡحَٰبُ ٱلۡيَمِينِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلۡيَمِينِ ٢٧Iwo a kudzanja lamanja, kodi akudzanja lamanja adzakhala ndani فِي سِدۡرٍ مَّخۡضُودٍ ٢٨Iwo adzakhala pakati pa m’mithunzi ya mitengo ya Sidrah وَطَلۡحٍ مَّنضُودٍ ٢٩Ndi m’mapata a nthochi zokhala ndi mikoko wina pamwamba pa unzake وَظِلٍّ مَّمۡدُودٍ ٣٠M’mithunzi yotambasuka وَمَآءٍ مَّسۡكُوبٍ ٣١Pambali pa madzi osefukira وَفَٰكِهَةٍ كَثِيرَةٍ ٣٢Ndi zipatso zochuluka لَّا مَقۡطُوعَةٍ وَلَا مَمۡنُوعَةٍ ٣٣Zimene nyengo yake sikutha ndipo kuchuluka kwake kudzakhalabe وَفُرُشٍ مَّرۡفُوعَةٍ ٣٤Ndi pa mipando yawofowofo yokwezedwa إِنَّآ أَنشَأۡنَٰهُنَّ إِنشَآءً ٣٥Ndithudi Ife tawalenga iwo mu chilengedwe cha padera فَجَعَلۡنَٰهُنَّ أَبۡكَارًا ٣٦Ndi kuwapanga kukhala a Namwali abwino عُرُبًا أَتۡرَابًا ٣٧A chikondi pa anzawo olingana nawo zaka لِّأَصۡحَٰبِ ٱلۡيَمِينِ ٣٨A iwo amene adzakhala kudzanja lamanja ثُلَّةٌ مِّنَ ٱلۡأَوَّلِينَ ٣٩Gulu lochuluka lidzakhala lochokera ku mibadwo yoyamba, yakale وَثُلَّةٌ مِّنَ ٱلۡأٓخِرِينَ ٤٠Gulu lochuluka lidzakhala lochokera ku mibadwo ya pambuyo pake وَأَصۡحَٰبُ ٱلشِّمَالِ مَآ أَصۡحَٰبُ ٱلشِّمَالِ ٤١Gulu la anthu a kudzanja lamanzere. Kodi anthu a kudzanja la manzere adzakhala otani فِي سَمُومٍ وَحَمِيمٍ ٤٢M’katikati mwa malawi a moto ndi m’madzi ogaduka وَظِلٍّ مِّن يَحۡمُومٍ ٤٣Ndi m’mithunzi ya utsi wakuda لَّا بَارِدٍ وَلَا كَرِيمٍ ٤٤Yosazizira kapena yabwino إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَبۡلَ ذَٰلِكَ مُتۡرَفِينَ ٤٥Ndithudi iwo kale adali kukhala m’moyo wosavutika ndi opeza zinthu zambiri وَكَانُواْ يُصِرُّونَ عَلَى ٱلۡحِنثِ ٱلۡعَظِيمِ ٤٦Ndipo adapitirira kuchita zoipa zikulu zikulu وَكَانُواْ يَقُولُونَ أَئِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابًا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ ٤٧Ndipo iwo anali kukonda kunena kuti: “Pamene ife tafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, kodi tingadzaukitsidwenso?” أَوَءَابَآؤُنَا ٱلۡأَوَّلُونَ ٤٨“Ndi makolo athu a nthawi ya makedzana?” قُلۡ إِنَّ ٱلۡأَوَّلِينَ وَٱلۡأٓخِرِينَ ٤٩Nena: “Ndithudi onse oyambirira ndi otsiriza.” لَمَجۡمُوعُونَ إِلَىٰ مِيقَٰتِ يَوۡمٍ مَّعۡلُومٍ ٥٠“Ndithudi onse adzasonkhanitsidwa pamodzi pa tsiku lokhazikitsidwa.” ثُمَّ إِنَّكُمۡ أَيُّهَا ٱلضَّآلُّونَ ٱلۡمُكَذِّبُونَ ٥١“Kuphatikiza inu nonse amene muchimwa ndi kukana choonadi.” لَأٓكِلُونَ مِن شَجَرٍ مِّن زَقُّومٍ ٥٢“Ndithudi inu mudzadya zipatso za mtengo wa Zaqqoom.” فَمَالِـُٔونَ مِنۡهَا ٱلۡبُطُونَ ٥٣“Ndipo mudzakhutitsa mimba zanu ndi izo.” فَشَٰرِبُونَ عَلَيۡهِ مِنَ ٱلۡحَمِيمِ ٥٤“Ndi kumwa madzi ogaduka.” فَشَٰرِبُونَ شُرۡبَ ٱلۡهِيمِ ٥٥“Ndi kumwa monga momwe ngamira yodwala ndi yaludzu imamwera.” هَٰذَا نُزُلُهُمۡ يَوۡمَ ٱلدِّينِ ٥٦Kumeneko ndiko kudzakhala kusangalala kwawo patsiku lachiweruzo نَحۡنُ خَلَقۡنَٰكُمۡ فَلَوۡلَا تُصَدِّقُونَ ٥٧Ndife amene tidakulengani inu nanga ndi chifukwa chiyani simukhulupilira أَفَرَءَيۡتُم مَّا تُمۡنُونَ ٥٨Ndiuzeni za umuna umene mumatulutsa ءَأَنتُمۡ تَخۡلُقُونَهُۥٓ أَمۡ نَحۡنُ ٱلۡخَٰلِقُونَ ٥٩Kodi ndinu amene mumaulenga kapena Ife ndife timaulenga نَحۡنُ قَدَّرۡنَا بَيۡنَكُمُ ٱلۡمَوۡتَ وَمَا نَحۡنُ بِمَسۡبُوقِينَ ٦٠Ife tidalamulira imfa kukhala pakati panu ndipo Ife sitingagonjetsedwe ayi عَلَىٰٓ أَن نُّبَدِّلَ أَمۡثَٰلَكُمۡ وَنُنشِئَكُمۡ فِي مَا لَا تَعۡلَمُونَ ٦١Kukusinthani inu ndi kukulengani kukhala china chake chimene inu simuchidziwa وَلَقَدۡ عَلِمۡتُمُ ٱلنَّشۡأَةَ ٱلۡأُولَىٰ فَلَوۡلَا تَذَكَّرُونَ ٦٢Ndithudi inu mumadziwa za chilengedwe choyamba. Nanga ndi chifukwa chiyani simulabadira أَفَرَءَيۡتُم مَّا تَحۡرُثُونَ ٦٣Kodi mudayamba mwaganiza za mbewu imene mumabzala ءَأَنتُمۡ تَزۡرَعُونَهُۥٓ أَمۡ نَحۡنُ ٱلزَّٰرِعُونَ ٦٤Kodi ndinu amene mumaimeretsa kapena ndife amene timameretsa لَوۡ نَشَآءُ لَجَعَلۡنَٰهُ حُطَٰمًا فَظَلۡتُمۡ تَفَكَّهُونَ ٦٥Ngati titafuna, Ife tikadaiphwanya m’timagawomagawo touma ndipo inu mukadayamba kudandaula إِنَّا لَمُغۡرَمُونَ ٦٦Ndithudi ife tapatsidwa chingongole cholemera بَلۡ نَحۡنُ مَحۡرُومُونَ ٦٧Iyayi. Koma tamanidwa أَفَرَءَيۡتُمُ ٱلۡمَآءَ ٱلَّذِي تَشۡرَبُونَ ٦٨Kodi inu mumawaona madzi amene mumamwa ءَأَنتُمۡ أَنزَلۡتُمُوهُ مِنَ ٱلۡمُزۡنِ أَمۡ نَحۡنُ ٱلۡمُنزِلُونَ ٦٩Kodi ndinu amene mumawagwetsa kuchokera ku mitambo kapena ndife لَوۡ نَشَآءُ جَعَلۡنَٰهُ أُجَاجًا فَلَوۡلَا تَشۡكُرُونَ ٧٠Chikadakhala chifuniro chathu tikadawapanga iwo kukhala a mchere. Nanga ndi chifukwa chiyani simuthokoza أَفَرَءَيۡتُمُ ٱلنَّارَ ٱلَّتِي تُورُونَ ٧١Kodi inu mumaganizira za moto umene mumasonkha ءَأَنتُمۡ أَنشَأۡتُمۡ شَجَرَتَهَآ أَمۡ نَحۡنُ ٱلۡمُنشِـُٔونَ ٧٢Kodi ndinu amene mumameretsa mtengo umene umayaka moto kapena ndife amene timaumeretsa نَحۡنُ جَعَلۡنَٰهَا تَذۡكِرَةً وَمَتَٰعًا لِّلۡمُقۡوِينَ ٧٣Ife taupanga iwo kukhala chikumbutso ndi chinthu chothandiza anthu amene ali paulendo فَسَبِّحۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلۡعَظِيمِ ٧٤Kotero lemekezani dzina la Ambuye wanu Wamkulu ۞ فَلَآ أُقۡسِمُ بِمَوَٰقِعِ ٱلنُّجُومِ ٧٥Ndipo ndilumbira pali nyenyezi zimene zili kugwa وَإِنَّهُۥ لَقَسَمٌ لَّوۡ تَعۡلَمُونَ عَظِيمٌ ٧٦Ndithudi ili ndi lonjezo lalikulu inu mukadadziwa إِنَّهُۥ لَقُرۡءَانٌ كَرِيمٌ ٧٧Ndithudi ndi Buku lolemekezeka la Korani فِي كِتَٰبٍ مَّكۡنُونٍ ٧٨Limene lili m’Buku lotetezedwa لَّا يَمَسُّهُۥٓ إِلَّا ٱلۡمُطَهَّرُونَ ٧٩Palibe amene adzalikhudza kupatula oyeretsedwa okha تَنزِيلٌ مِّن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٨٠Chivumbulutso chochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse أَفَبِهَٰذَا ٱلۡحَدِيثِ أَنتُم مُّدۡهِنُونَ ٨١Kodi muli kunyozabe uthenga uwu وَتَجۡعَلُونَ رِزۡقَكُمۡ أَنَّكُمۡ تُكَذِّبُونَ ٨٢Mmalo mothokoza chifukwa cha zinthu zimene amakupatsani inu mumamukana Iye فَلَوۡلَآ إِذَا بَلَغَتِ ٱلۡحُلۡقُومَ ٨٣Nanga ndi chifukwa chiyani inu simuthandiza pamene mzimu wa munthu amene ali kufa ufika pa khosi pake وَأَنتُمۡ حِينَئِذٍ تَنظُرُونَ ٨٤Pamene panthawiyo, inu mumangoyang’ana وَنَحۡنُ أَقۡرَبُ إِلَيۡهِ مِنكُمۡ وَلَٰكِن لَّا تُبۡصِرُونَ ٨٥Koma Ife tili pafupi ndi iye kuposa inu koma inu simutiona فَلَوۡلَآ إِن كُنتُمۡ غَيۡرَ مَدِينِينَ ٨٦Nanga ndi chifukwa chiyani simutero ngati inu simudzaweruzidwa patsogolo pake تَرۡجِعُونَهَآ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ ٨٧Bwezerani mzimuwo ngati ndinu anthu a choonadi فَأَمَّآ إِن كَانَ مِنَ ٱلۡمُقَرَّبِينَ ٨٨Ndipo ngati iye ndi mmodzi wa anthu amene ali kufupi ndi Mulungu فَرَوۡحٌ وَرَيۡحَانٌ وَجَنَّتُ نَعِيمٍ ٨٩Iye adzapeza mpumulo ndi chakudya ndi munda wa chisangalalo وَأَمَّآ إِن كَانَ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلۡيَمِينِ ٩٠Ndipo ngati iye ndi wam’gulu la anthu akudzanja la manja فَسَلَٰمٌ لَّكَ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلۡيَمِينِ ٩١Kotero kuli mtendere kwa iwo a kudzanja lamanja وَأَمَّآ إِن كَانَ مِنَ ٱلۡمُكَذِّبِينَ ٱلضَّآلِّينَ ٩٢Ndipo ngati iye ndi mmodzi wa iwo okana choonadi ndi amene amalakwa فَنُزُلٌ مِّنۡ حَمِيمٍ ٩٣Motero kulandiridwa kwake kudzakhala kwa madzi otentha kwambiri وَتَصۡلِيَةُ جَحِيمٍ ٩٤Ndi kulowetsedwa ku Gahena إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ حَقُّ ٱلۡيَقِينِ ٩٥Ndithudi ichi ndi choonadi chosakayikitsa فَسَبِّحۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلۡعَظِيمِ ٩٦Motero lemekezani dzina la Ambuye wanu, Wamkulu

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.