Millat al-Islam

Chapter 30 · 60 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Ar-Rum in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah Ar-Rum (1233 reciters)
Meccanسورة الروم60 verses

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

الٓمٓ ١Alif Lam Mim غُلِبَتِ ٱلرُّومُ ٢Aroma agonjetsedwa فِيٓ أَدۡنَى ٱلۡأَرۡضِ وَهُم مِّنۢ بَعۡدِ غَلَبِهِمۡ سَيَغۡلِبُونَ ٣M’dziko loyandikana nalo ndipo iwo atagonja, pambuyo pake adzapambana فِي بِضۡعِ سِنِينَۗ لِلَّهِ ٱلۡأَمۡرُ مِن قَبۡلُ وَمِنۢ بَعۡدُۚ وَيَوۡمَئِذٍ يَفۡرَحُ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ ٤M’zaka zowerengeka. Mulungu ndiye Mwini ulamuliro ndipo pa tsiku limeneli onse okhulupirira adzakondwera بِنَصۡرِ ٱللَّهِۚ يَنصُرُ مَن يَشَآءُۖ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ٥Ndi chithandizo cha Mulungu. Iye amathandiza aliyense amene wamufuna. Iye ndi wamphamvu, ndiponso Mwini chisoni chosatha وَعۡدَ ٱللَّهِۖ لَا يُخۡلِفُ ٱللَّهُ وَعۡدَهُۥ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ ٦Ili ndi lonjezo la Mulungu. Mulungu saphwanya lonjezo lake ndipo anthu ambiri sadziwa يَعۡلَمُونَ ظَٰهِرًا مِّنَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَهُمۡ عَنِ ٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ غَٰفِلُونَ ٧Iwo amangodziwa zokhazo zimene amaziona za m’moyo uno koma za m’moyo umene uli nkudza, iwo safuna kumva china chilichonse cha izo أَوَلَمۡ يَتَفَكَّرُواْ فِيٓ أَنفُسِهِمۗ مَّا خَلَقَ ٱللَّهُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَآ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَأَجَلٍ مُّسَمًّىۗ وَإِنَّ كَثِيرًا مِّنَ ٱلنَّاسِ بِلِقَآيِٕ رَبِّهِمۡ لَكَٰفِرُونَ ٨Kodi iwo saganizira pa okha kuti Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zinthu zonse zimene zikhala m’menemo mwachoonadi ndi mwa kanthawi yokhazikitsidwa? Ndipo, ndithudi, anthu ambiri amakana zoti adzakumana ndi Ambuye wawo أَوَلَمۡ يَسِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَيَنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۚ كَانُوٓاْ أَشَدَّ مِنۡهُمۡ قُوَّةً وَأَثَارُواْ ٱلۡأَرۡضَ وَعَمَرُوهَآ أَكۡثَرَ مِمَّا عَمَرُوهَا وَجَآءَتۡهُمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِۖ فَمَا كَانَ ٱللَّهُ لِيَظۡلِمَهُمۡ وَلَٰكِن كَانُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ ٩Kodi iwo sadayende pa dziko ndi kuona zimene zidawaonekera anthu amene adalipo kale? Iwo adali ndi mphamvu zambiri kuposa awa, ndipo adakumba nthaka ndiponso adamanga pa nthakayo nyumba zambiri kuposa zimene awa amanga. Ndipo kudadza kwa iwo Atumwi awo ndi chiphunzitso chomveka ndipo sikudali koyenera kuti Mulungu awachitire zinthu zosalungama koma kuti iwo adalakwira mizimu yawo ثُمَّ كَانَ عَٰقِبَةَ ٱلَّذِينَ أَسَٰٓـُٔواْ ٱلسُّوٓأَىٰٓ أَن كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَكَانُواْ بِهَا يَسۡتَهۡزِءُونَ ١٠Choipa chidatsata munthu amene anali kuchita zoipa chifukwa iwo adakana chiphunzitso cha Mulungu ndipo anali kuwaseka iwo ٱللَّهُ يَبۡدَؤُاْ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥ ثُمَّ إِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ ١١Mulungu ndiye amene amalenga zolengedwa ndipo adzazibwereza ndipo ndi kwa Iye kumene mudzabwerera وَيَوۡمَ تَقُومُ ٱلسَّاعَةُ يُبۡلِسُ ٱلۡمُجۡرِمُونَ ١٢Ndipo pa nthawi imene ola lidzadza, anthu onse ochita zoipa adzakhala ndi nkhawa وَلَمۡ يَكُن لَّهُم مِّن شُرَكَآئِهِمۡ شُفَعَٰٓؤُاْ وَكَانُواْ بِشُرَكَآئِهِمۡ كَٰفِرِينَ ١٣Ndipo iwo sadzakhala ndi ena alionse owathandiza ochokera pakati pa milungu yawo imene anali kupembedza kuonjezera pa Mulungu weniweni ndipo iwo adzakhala okana milungu yawo وَيَوۡمَ تَقُومُ ٱلسَّاعَةُ يَوۡمَئِذٍ يَتَفَرَّقُونَ ١٤Ndipo pa nthawi imene ola lidzadza, pa nthawi imeneyi, iwo adzasiyanitsidwa wina ndi mnzake فَأَمَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَهُمۡ فِي رَوۡضَةٍ يُحۡبَرُونَ ١٥Ndipo onse amene adakhulupirira ndipo adachita ntchito zabwino, iwo adzasangalatsidwa m’munda wa Paradiso وَأَمَّا ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَلِقَآيِٕ ٱلۡأٓخِرَةِ فَأُوْلَٰٓئِكَ فِي ٱلۡعَذَابِ مُحۡضَرُونَ ١٦Iwo amene sadakhulupirire ndipo adakana chiphunzitso chathu ndi kukumana kwa m’moyo umene uli nkudza, awa ndiwo amene adzatengedwa kupita ku chilango فَسُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ حِينَ تُمۡسُونَ وَحِينَ تُصۡبِحُونَ ١٧Kotero lemekezani Mulungu pamene mulowa nthawi ya madzulo ndi pamene mulowa nthawi ya m’mawa وَلَهُ ٱلۡحَمۡدُ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَعَشِيًّا وَحِينَ تُظۡهِرُونَ ١٨Inde. Kwa Iye kukhale kuyamikidwa kumwamba ndi padziko lapansi ndiponso pa nthawi yamasana ndi yamadzulo يُخۡرِجُ ٱلۡحَيَّ مِنَ ٱلۡمَيِّتِ وَيُخۡرِجُ ٱلۡمَيِّتَ مِنَ ٱلۡحَيِّ وَيُحۡيِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَاۚ وَكَذَٰلِكَ تُخۡرَجُونَ ١٩Iye ndiye amene amadzutsa anthu kuchokera ku anthu akufa ndipo amadzutsa anthu akufa kuchokera ku anthu amoyo ndiponso amapereka moyo ku nthaka ikafa. Ndipo mmenemo ndi mmene mudzaukitsidwire وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦٓ أَنۡ خَلَقَكُم مِّن تُرَابٍ ثُمَّ إِذَآ أَنتُم بَشَرٌ تَنتَشِرُونَ ٢٠Ndipo chimodzi cha zizindikiro zake ndi chakuti Iye adakulengani inu kuchokera ku fumbi, ndipo inu, ndinudi, anthu amene mudamwazidwa وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦٓ أَنۡ خَلَقَ لَكُم مِّنۡ أَنفُسِكُمۡ أَزۡوَٰجًا لِّتَسۡكُنُوٓاْ إِلَيۡهَا وَجَعَلَ بَيۡنَكُم مَّوَدَّةً وَرَحۡمَةًۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّقَوۡمٍ يَتَفَكَّرُونَ ٢١Ndipo pakati pa zizindikiro china ndi chakuti Iye adalenga akazi kuchokera mwa inu kuti mukhoza kupeza mpumulo mwa iwo ndipo adaika pakati panu chikondi ndi chisoni. Ndithudi muli phunziro muichi kwa anthu amene amaganiza bwino وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦ خَلۡقُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَٱخۡتِلَٰفُ أَلۡسِنَتِكُمۡ وَأَلۡوَٰنِكُمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّلۡعَٰلِمِينَ ٢٢Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi kalengedwe ka kumwamba ndi dziko lapansi ndi kusiyana kwa zilankhulo zanu ndiponso maonekedwe a makungu anu. Ndithudi mu chimenechimulizizindikirokwaanthuophunzira وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦ مَنَامُكُم بِٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ وَٱبۡتِغَآؤُكُم مِّن فَضۡلِهِۦٓۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّقَوۡمٍ يَسۡمَعُونَ ٢٣Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi kugona kumene mumagona usiku ndi usana kufunafuna chisomo chake. Ndithudi mu chimenechi muli chizindikiro kwa anthu amene amatha kumva وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦ يُرِيكُمُ ٱلۡبَرۡقَ خَوۡفًا وَطَمَعًا وَيُنَزِّلُ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءً فَيُحۡيِۦ بِهِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَآۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّقَوۡمٍ يَعۡقِلُونَ ٢٤Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi chakuti Iye amakuonetsani mphezi imene imakuchititsani mantha ndiponso kukupatsani chikhulupiriro. Ndipo amatumiza mvula kuchokera ku mitambo ndiponso amapereka moyo ku nthaka ikafa. Ndithudi mu chimenechi muli zizndikiro kwa anthu ozindikira وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦٓ أَن تَقُومَ ٱلسَّمَآءُ وَٱلۡأَرۡضُ بِأَمۡرِهِۦۚ ثُمَّ إِذَا دَعَاكُمۡ دَعۡوَةً مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ إِذَآ أَنتُمۡ تَخۡرُجُونَ ٢٥Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi chakuti kumwamba ndi dziko lapansi zimadzichepetsa potsatira malamulo ake ndipo pamene Iye akuitanani inu kamodzi kokha kuchokera m’nthaka, Taonani inu mudzadza mwamsanga msanga وَلَهُۥ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ كُلٌّ لَّهُۥ قَٰنِتُونَ ٢٦Ndipo chilichonse chimene chili kumwamba ndi padziko lapansi ndi chake ndipo zonse zimamumvera Iye وَهُوَ ٱلَّذِي يَبۡدَؤُاْ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥ وَهُوَ أَهۡوَنُ عَلَيۡهِۚ وَلَهُ ٱلۡمَثَلُ ٱلۡأَعۡلَىٰ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ ٢٧Ndipo Iye ndiye amene amayambitsa chilengedwe ndipo adzachibwerezanso ndipo zimenezi ndi zapafupi kwa Iye. Ndipo wake ndi ulemerero kumwamba ndi padziko lapansi. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse ضَرَبَ لَكُم مَّثَلًا مِّنۡ أَنفُسِكُمۡۖ هَل لَّكُم مِّن مَّا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُكُم مِّن شُرَكَآءَ فِي مَا رَزَقۡنَٰكُمۡ فَأَنتُمۡ فِيهِ سَوَآءٌ تَخَافُونَهُمۡ كَخِيفَتِكُمۡ أَنفُسَكُمۡۚ كَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٍ يَعۡقِلُونَ ٢٨Iye ali kupereka chitsanzo chokhudza inu nomwe. Kodi inu muli nawo akapolo amene amakhala anzanu pa zinthu zimene takupatsani ndipo kuti mumagawana nawo zinthuzo mofanana ndiponso mumawaopa iwo monga momwe mumaoperana? Mmenemo ndi mmene timasiyanitsira chiphunzitso chathu kwa anthu amene amazindikira بَلِ ٱتَّبَعَ ٱلَّذِينَ ظَلَمُوٓاْ أَهۡوَآءَهُم بِغَيۡرِ عِلۡمٍۖ فَمَن يَهۡدِي مَنۡ أَضَلَّ ٱللَّهُۖ وَمَا لَهُم مِّن نَّٰصِرِينَ ٢٩Iyayi! onse osalungama amatsatira zilakolako zawo mosadziwa. Kotero ndani angatsogolere iye amene Mulungu wamusocheretsa? Ndipo iwo sadzakhala ndi wowathandiza فَأَقِمۡ وَجۡهَكَ لِلدِّينِ حَنِيفًاۚ فِطۡرَتَ ٱللَّهِ ٱلَّتِي فَطَرَ ٱلنَّاسَ عَلَيۡهَاۚ لَا تَبۡدِيلَ لِخَلۡقِ ٱللَّهِۚ ذَٰلِكَ ٱلدِّينُ ٱلۡقَيِّمُ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ ٣٠Kotero dzipereke kwathunthu ku chipembedzo choonadi, chipembedzo, chenicheni, chimene Mulungu adalamula kuti munthu ayenera kutsatira. Chilengedwe chimene Mulungu adalenga mtundu wa anthu sichingasinthidwe. Ndithudi pali Mulungu, icho ndicho chipembedzo choona. Koma ambiri a mtundu wa anthu sadziwa ۞ مُنِيبِينَ إِلَيۡهِ وَٱتَّقُوهُ وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَلَا تَكُونُواْ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ ٣١Lapani kwa Iye ndiponso muopeni Iye. Pitirizani kupemphera nthawi zonse ndipo musakhale inu pakati pa iwo amene amafanizira milungu ina ndi Mulungu weniweni مِنَ ٱلَّذِينَ فَرَّقُواْ دِينَهُمۡ وَكَانُواْ شِيَعًاۖ كُلُّ حِزۡبِۭ بِمَا لَدَيۡهِمۡ فَرِحُونَ ٣٢Pali anthu amene amagawa chipembedzo chawo ndi kukhala mipingo yosiyanasiyana ndipo mpingo uliwonse umasangalala ndi zimene uli nazo وَإِذَا مَسَّ ٱلنَّاسَ ضُرٌّ دَعَوۡاْ رَبَّهُم مُّنِيبِينَ إِلَيۡهِ ثُمَّ إِذَآ أَذَاقَهُم مِّنۡهُ رَحۡمَةً إِذَا فَرِيقٌ مِّنۡهُم بِرَبِّهِمۡ يُشۡرِكُونَ ٣٣Ndipo pamene mavuto adza pa anthu, iwo amalira kwa Ambuye wawo ndi kudza kwa Iye modzichepetsa. Koma pamene Mulungu awaonetsa gawo lachisoni chochokera kwa Iye Mwini, ena a iwo amayamba kupembedza milungu ina yoonjezera pa Ambuye wawo لِيَكۡفُرُواْ بِمَآ ءَاتَيۡنَٰهُمۡۚ فَتَمَتَّعُواْ فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ ٣٤Akhala ngati ali kuonetsakusathokozapazimenetawachitira. Basangalalani mwa kanthawi kochepa ndipo posachedwapa mudzadziwa kupusa kwanu أَمۡ أَنزَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ سُلۡطَٰنًا فَهُوَ يَتَكَلَّمُ بِمَا كَانُواْ بِهِۦ يُشۡرِكُونَ ٣٥Kodi kapena Ife tidawatumizira lamulo limene limanena za zinthu zimene iwo amazipembedza zoonjezera pa Mulungu وَإِذَآ أَذَقۡنَا ٱلنَّاسَ رَحۡمَةً فَرِحُواْ بِهَاۖ وَإِن تُصِبۡهُمۡ سَيِّئَةُۢ بِمَا قَدَّمَتۡ أَيۡدِيهِمۡ إِذَا هُمۡ يَقۡنَطُونَ ٣٦Ndipo pamene tiwaonetsera anthu chifundo chathu, iwo amasangalala kwambiri chifukwa cha chifundocho ndipo ngati choipa chidza pa iwo chifukwa cha zimene iwo achita ndi manja awo, taonani! Iwo amadandaula kwambiri أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّ ٱللَّهَ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ وَيَقۡدِرُۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّقَوۡمٍ يُؤۡمِنُونَ ٣٧Kodi iwo saona kuti Mulungu amapereka moolowa manja kwa aliyense amene Iye wamufuna ndiponso zomupatsazochepa munthu yemwe wamufuna. Ndithudi mu chimenechi muli phunziro kwa anthu okhulupirira فَـَٔاتِ ذَا ٱلۡقُرۡبَىٰ حَقَّهُۥ وَٱلۡمِسۡكِينَ وَٱبۡنَ ٱلسَّبِيلِۚ ذَٰلِكَ خَيۡرٌ لِّلَّذِينَ يُرِيدُونَ وَجۡهَ ٱللَّهِۖ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ ٣٨Kotero apatseni zosowa zawo abale anu, anthu osauka ndi a paulendo. Ichi ndicho chinthu chabwino kwambiri kwa iwo amene afuna chisangalalo cha Mulungu ndipo awa ndiwo amene ali opambana وَمَآ ءَاتَيۡتُم مِّن رِّبًا لِّيَرۡبُوَاْ فِيٓ أَمۡوَٰلِ ٱلنَّاسِ فَلَا يَرۡبُواْ عِندَ ٱللَّهِۖ وَمَآ ءَاتَيۡتُم مِّن زَكَوٰةٍ تُرِيدُونَ وَجۡهَ ٱللَّهِ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُضۡعِفُونَ ٣٩Chimene mumapereka ngati chiongoladzanja kuti chionjezere chuma cha anthu, sichidzakhala ndi chionjezero kwa Mulungu. Koma zopereka zimene mupereka ngati chaulere ndi cholinga chopeza madalitso a Mulungu ndi chimenechi chimene chidzaonjezeredwa kwambirimbiri ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَكُمۡ ثُمَّ رَزَقَكُمۡ ثُمَّ يُمِيتُكُمۡ ثُمَّ يُحۡيِيكُمۡۖ هَلۡ مِن شُرَكَآئِكُم مَّن يَفۡعَلُ مِن ذَٰلِكُم مِّن شَيۡءٍۚ سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ ٤٠Ndi Mulungu amene anakulengani inu amene amakupatsani zofuna zanu. Iye adzakonza kuti mufe patsogolopakepanondipokenakaadzakupatsaninsomoyo. Kodi chilipo china chilichonse chimene mungachifanizire ndi chimene chingachite zimenezi? Ulemerero ukhale kwa Iye ndipo Iye akhale zopambana kuposa zonse zimene amazifanizira ndi Iye ظَهَرَ ٱلۡفَسَادُ فِي ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِ بِمَا كَسَبَتۡ أَيۡدِي ٱلنَّاسِ لِيُذِيقَهُم بَعۡضَ ٱلَّذِي عَمِلُواْ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ ٤١Zinthu zoipa zalowa m’dziko ndiponso m’nyanja chifukwa cha ntchito za anthu zimene amachita ndi manja awo. Mulungu akhoza kuwalawitsa chilango chifukwa cha ntchito zawo kuti mwina athe kutembenuka قُلۡ سِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَٱنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلُۚ كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّشۡرِكِينَ ٤٢Nena “Pitani paliponse pa dziko ndi kuona zimene zidawaonekera anthu amene adalipo kale. Ambiri a iwo adali opembedza mafano.” فَأَقِمۡ وَجۡهَكَ لِلدِّينِ ٱلۡقَيِّمِ مِن قَبۡلِ أَن يَأۡتِيَ يَوۡمٌ لَّا مَرَدَّ لَهُۥ مِنَ ٱللَّهِۖ يَوۡمَئِذٍ يَصَّدَّعُونَ ٤٣Kotero dziperekeni kwathunthu ku chipembedzo choona lisanadze tsiku loopsa kuchokera kwa Mulungu limene silidzatheka kulizemba. Pa tsiku limeneli anthu adzagawidwa m’magulu مَن كَفَرَ فَعَلَيۡهِ كُفۡرُهُۥۖ وَمَنۡ عَمِلَ صَٰلِحًا فَلِأَنفُسِهِمۡ يَمۡهَدُونَ ٤٤onse osakhulupirira adzalangidwa chifukwa cha kusakhulupirira kwawo ndipo onse amene amachita ntchito zabwino adzadzisungira zinthu zabwino kumwamba لِيَجۡزِيَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ مِن فَضۡلِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ لَا يُحِبُّ ٱلۡكَٰفِرِينَ ٤٥Ndipo Iye adzawapatsa malipiro abwino onse amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino kuchokera ku zokoma zake. Ndipo Iye sakonda anthu osakhulupirira وَمِنۡ ءَايَٰتِهِۦٓ أَن يُرۡسِلَ ٱلرِّيَاحَ مُبَشِّرَٰتٍ وَلِيُذِيقَكُم مِّن رَّحۡمَتِهِۦ وَلِتَجۡرِيَ ٱلۡفُلۡكُ بِأَمۡرِهِۦ وَلِتَبۡتَغُواْ مِن فَضۡلِهِۦ وَلَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ ٤٦Ndipo chimodzi mwa zizindikiro zake ndi chakuti amatumiza mphepo imene imabweretsa zabwino ndi cholinga choti mulawe chisomo chake ndiponso kuti zombo ziyende mwamalamulo ake ndiponso kuti inu muzifunafuna chifundo chake ndi kumuthokoza وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ رُسُلًا إِلَىٰ قَوۡمِهِمۡ فَجَآءُوهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَٱنتَقَمۡنَا مِنَ ٱلَّذِينَ أَجۡرَمُواْۖ وَكَانَ حَقًّا عَلَيۡنَا نَصۡرُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٤٧Ndithudi Ife tidatumiza, Atumwi kwa anthu awo iwe usanabadwe ndipo iwo adadza kwa iwo ndi chiphunzitso choyenera. Ife tidapereka chilango kwa anthu ochimwa ndipo kuthandiza anthu okhulupirira ndi udindo wosatha kwa Ife ٱللَّهُ ٱلَّذِي يُرۡسِلُ ٱلرِّيَٰحَ فَتُثِيرُ سَحَابًا فَيَبۡسُطُهُۥ فِي ٱلسَّمَآءِ كَيۡفَ يَشَآءُ وَيَجۡعَلُهُۥ كِسَفًا فَتَرَى ٱلۡوَدۡقَ يَخۡرُجُ مِنۡ خِلَٰلِهِۦۖ فَإِذَآ أَصَابَ بِهِۦ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦٓ إِذَا هُمۡ يَسۡتَبۡشِرُونَ ٤٨Mulungu ndiye amene amatumiza mphepo kuti iyendetse mtambo ndipo amaumwaza mlengalenga monga momwe wafunira. Iye amauphwanya ndipo inu mumaona mvula ili kugwa kuchokera mu mtambowo. Iye amagwetsa mvula pa akapolo ake amene wawafuna. Taonani! Iwo amakhala osangalala وَإِن كَانُواْ مِن قَبۡلِ أَن يُنَزَّلَ عَلَيۡهِم مِّن قَبۡلِهِۦ لَمُبۡلِسِينَ ٤٩Ngakhale kuti, iyo isanadze, iwo anali kuda nkhawa فَٱنظُرۡ إِلَىٰٓ ءَاثَٰرِ رَحۡمَتِ ٱللَّهِ كَيۡفَ يُحۡيِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَآۚ إِنَّ ذَٰلِكَ لَمُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ قَدِيرٌ ٥٠Taonani zizindikiro za chisoni cha Mulungu mmene amaperekera moyo ku nthaka imene inali yakufa. Ndithudi Iye adzadzutsa zakufa kuti zikhale zamoyo. Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse وَلَئِنۡ أَرۡسَلۡنَا رِيحًا فَرَأَوۡهُ مُصۡفَرًّا لَّظَلُّواْ مِنۢ بَعۡدِهِۦ يَكۡفُرُونَ ٥١Ndipo ngati Ife tikatumiza mphepo imene imapangitsa mbewu zawo kusanduka za chikasu, iwo amakhala osathokoza فَإِنَّكَ لَا تُسۡمِعُ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَلَا تُسۡمِعُ ٱلصُّمَّ ٱلدُّعَآءَ إِذَا وَلَّوۡاْ مُدۡبِرِينَ ٥٢Ndithudi iwe siungathe kumupanga munthu wakufa kuti amve ndiponso siungathe kumupanga munthu wosamva kuti amve kuitana pamene iwo atembenuka ndi kuthawa وَمَآ أَنتَ بِهَٰدِ ٱلۡعُمۡيِ عَن ضَلَٰلَتِهِمۡۖ إِن تُسۡمِعُ إِلَّا مَن يُؤۡمِنُ بِـَٔايَٰتِنَا فَهُم مُّسۡلِمُونَ ٥٣Ndipo iwe siungathe kumutsogolera munthu wakhungu kuti asiye kulakwa kwake. Palibe amene adzakumvera kupatula okhawo amene amakhulupirira mu chiphunzitso chathu ۞ ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَكُم مِّن ضَعۡفٍ ثُمَّ جَعَلَ مِنۢ بَعۡدِ ضَعۡفٍ قُوَّةً ثُمَّ جَعَلَ مِنۢ بَعۡدِ قُوَّةٍ ضَعۡفًا وَشَيۡبَةًۚ يَخۡلُقُ مَا يَشَآءُۚ وَهُوَ ٱلۡعَلِيمُ ٱلۡقَدِيرُ ٥٤di Mulungu amene adakulengani inu ofoka ndipo adakupatsani mphamvu pambuyo pa kufoka. Ndipo atakupatsani mphamvu adakupatsani kufoka ndi imvi. Iye amalenga chilichonse chimene wafuna ndipo ndiye amene amadziwa zonse ndipo ndiye Mwini mphamvu وَيَوۡمَ تَقُومُ ٱلسَّاعَةُ يُقۡسِمُ ٱلۡمُجۡرِمُونَ مَا لَبِثُواْ غَيۡرَ سَاعَةٍۚ كَذَٰلِكَ كَانُواْ يُؤۡفَكُونَ ٥٥Ndipo pamene ola lidzadza, anthu ochimwa adzalumbira kuti adangokhala ola limodzi lokha. Kotero iwo amakhala onamizidwa وَقَالَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ وَٱلۡإِيمَٰنَ لَقَدۡ لَبِثۡتُمۡ فِي كِتَٰبِ ٱللَّهِ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡبَعۡثِۖ فَهَٰذَا يَوۡمُ ٱلۡبَعۡثِ وَلَٰكِنَّكُمۡ كُنتُمۡ لَا تَعۡلَمُونَ ٥٦Ndipo iwo amene adapatsidwa nzeru ndi chikhulupiriro adzati, “Ndithudi inu mwakhala molingana ndi malamulo a Mulungu mpaka pa tsiku louka kwa akufa. Kotero ili ndilo tsiku louka kwa akufa koma inu simunalidziwe ayi.” فَيَوۡمَئِذٍ لَّا يَنفَعُ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ مَعۡذِرَتُهُمۡ وَلَا هُمۡ يُسۡتَعۡتَبُونَ ٥٧Koma patsiku limeneli zodandaula zawo sizidzawathandiza anthu onse ochimwa ndipo sizidzamveka ayi وَلَقَدۡ ضَرَبۡنَا لِلنَّاسِ فِي هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ مِن كُلِّ مَثَلٍۚ وَلَئِن جِئۡتَهُم بِـَٔايَةٍ لَّيَقُولَنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا مُبۡطِلُونَ ٥٨Ndithudi m’Buku ili la Korani anthu tawaikiramo zitsanzo zambiri zosiyanasiyana ndipo ngati iwe utawabweretsera chiphunzitso iwo amene sakhulupirira adzati, “Iwe siuli kutsatira china chilichonse koma bodza ndi matsenga.” كَذَٰلِكَ يَطۡبَعُ ٱللَّهُ عَلَىٰ قُلُوبِ ٱلَّذِينَ لَا يَعۡلَمُونَ ٥٩Mmenemo ndi mmene Mulungu amatsekera mitima ya anthu osadziwa فَٱصۡبِرۡ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقٌّۖ وَلَا يَسۡتَخِفَّنَّكَ ٱلَّذِينَ لَا يُوقِنُونَ ٦٠Kotero pirirani. Lonjezo la Mulungu ndi loona ndipo usalole anthu opanda chikhulupiriro kuti akuderere iwe

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.