Millat al-Islam

Chapter 32 · 30 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah As-Sajda in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah As-Sajda (1273 reciters)
Meccanسورة السجدة30 verses

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

الٓمٓ ١Alif Lam Mim تَنزِيلُ ٱلۡكِتَٰبِ لَا رَيۡبَ فِيهِ مِن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٢Ichi ndi chivumbulutso cha Buku Lopatulika limene mulibe zokayikitsa ndi chochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse أَمۡ يَقُولُونَ ٱفۡتَرَىٰهُۚ بَلۡ هُوَ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَ لِتُنذِرَ قَوۡمًا مَّآ أَتَىٰهُم مِّن نَّذِيرٍ مِّن قَبۡلِكَ لَعَلَّهُمۡ يَهۡتَدُونَ ٣Kodi kapena iwo amati wapeka yekha? Iyayi, ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wake kuti uchenjeze anthu amene kuyambira kale mchenjezi sanadze kwa iwo, kuti iwo akhoza kutsatira njira yoyenera ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا فِي سِتَّةِ أَيَّامٍ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ مَا لَكُم مِّن دُونِهِۦ مِن وَلِيٍّ وَلَا شَفِيعٍۚ أَفَلَا تَتَذَكَّرُونَ ٤Mulungu ndiye amene adalenga kumwamba ndi dziko Sajda 439 lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo m’masiku asanu ndi limodzi. Ndipo atatero Iye adabuka pa mpando wake wachifumu. Inu mulibe wokuyang’anirani kapena wokuthandizani kupatula Iye yekha. Kodi simungaganize يُدَبِّرُ ٱلۡأَمۡرَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ إِلَى ٱلۡأَرۡضِ ثُمَّ يَعۡرُجُ إِلَيۡهِ فِي يَوۡمٍ كَانَ مِقۡدَارُهُۥٓ أَلۡفَ سَنَةٍ مِّمَّا تَعُدُّونَ ٥Iye amalamulira zinthu kuchokera kumwamba mpaka pa dziko lapansi ndipo zidzakwera kudza kwa Iye m’tsiku limene muyeso wake ungathe kuyerekezedwa ndi zaka chikwi chimodzi mwa chiwerengero chomwe inu mumachidziwa ذَٰلِكَ عَٰلِمُ ٱلۡغَيۡبِ وَٱلشَّهَٰدَةِ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ٦Uyundiyewodziwazobisikandizooneka, Mwini mphamvu, ndi Mwini chisoni chosatha ٱلَّذِيٓ أَحۡسَنَ كُلَّ شَيۡءٍ خَلَقَهُۥۖ وَبَدَأَ خَلۡقَ ٱلۡإِنسَٰنِ مِن طِينٍ ٧Amene adalenga chilichonse m’maonekedwe abwino. Ndipo adalenga munthu kuchokera ku dothi ثُمَّ جَعَلَ نَسۡلَهُۥ مِن سُلَٰلَةٍ مِّن مَّآءٍ مَّهِينٍ ٨Ndipo adalenga ana ake kuchokera ku dontho lamadzi onyozeka ثُمَّ سَوَّىٰهُ وَنَفَخَ فِيهِ مِن رُّوحِهِۦۖ وَجَعَلَ لَكُمُ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡأَبۡصَٰرَ وَٱلۡأَفۡـِٔدَةَۚ قَلِيلًا مَّا تَشۡكُرُونَ ٩Ndipo iye adamuumba munthu mwaubwino ndipo adamuuzira Mzimu wake. Ndipo Iye adakupatsani inu makutu, maso ndi mitima, inu simuthokoza nthawi zambiri وَقَالُوٓاْ أَءِذَا ضَلَلۡنَا فِي ٱلۡأَرۡضِ أَءِنَّا لَفِي خَلۡقٍ جَدِيدِۭۚ بَلۡ هُم بِلِقَآءِ رَبِّهِمۡ كَٰفِرُونَ ١٠Iwo adati, “Chiyani! Pamene ife taikidwa m’manda, kodi tingadzalengedwenso?” Ndithudi iwo adakana kuti adzakumana ndi Ambuye wawo ۞ قُلۡ يَتَوَفَّىٰكُم مَّلَكُ ٱلۡمَوۡتِ ٱلَّذِي وُكِّلَ بِكُمۡ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُمۡ تُرۡجَعُونَ ١١Nena “Mngelo wa imfa, amene adasankhidwa kukuyang’anirani inu, adzakupangitsani kuti mufe. Kotero inu mudzabwerera kwa Ambuye wanu.” وَلَوۡ تَرَىٰٓ إِذِ ٱلۡمُجۡرِمُونَ نَاكِسُواْ رُءُوسِهِمۡ عِندَ رَبِّهِمۡ رَبَّنَآ أَبۡصَرۡنَا وَسَمِعۡنَا فَٱرۡجِعۡنَا نَعۡمَلۡ صَٰلِحًا إِنَّا مُوقِنُونَ ١٢Iwe ukadangodzaona mmene anthu ochimwa adzagwetsera mitu yawo pamaso pa Ambuye wawo nati, “Ambuye wathu! Ife taona ndipo tamva. Tsopano tibwezereni pa dziko lapansi ndipo ife tidzagwira ntchito zachilungamo chifukwa ife, ndithudi, takhulupirira.” وَلَوۡ شِئۡنَا لَأٓتَيۡنَا كُلَّ نَفۡسٍ هُدَىٰهَا وَلَٰكِنۡ حَقَّ ٱلۡقَوۡلُ مِنِّي لَأَمۡلَأَنَّ جَهَنَّمَ مِنَ ٱلۡجِنَّةِ وَٱلنَّاسِ أَجۡمَعِينَ ١٣Ife tikadafuna, ndithudi, tikadatsogolera mzimu uliwonse ku njira yoyenera. Koma kuti mawu ochokera kwa Ine adakwanitsidwa. “Ine ndidzadzadza Gahena ndi majini pamodzi ndi anthu.” فَذُوقُواْ بِمَا نَسِيتُمۡ لِقَآءَ يَوۡمِكُمۡ هَٰذَآ إِنَّا نَسِينَٰكُمۡۖ وَذُوقُواْ عَذَابَ ٱلۡخُلۡدِ بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ ١٤Lawani chilango tsopano, chifukwa inu mudaiwala za tsikuli. Ndipo nafenso takuiwalani. Kotero inu lawani chilango chosatha chifukwa cha ntchito zanu zoipa إِنَّمَا يُؤۡمِنُ بِـَٔايَٰتِنَا ٱلَّذِينَ إِذَا ذُكِّرُواْ بِهَا خَرُّواْۤ سُجَّدًاۤ وَسَبَّحُواْ بِحَمۡدِ رَبِّهِمۡ وَهُمۡ لَا يَسۡتَكۡبِرُونَ ۩ ١٥Ndi okhawo amene amakhulupirira chiphunzitso chathu amene chiphunzitsocho chimati chikaphunzitsidwa, amagwa pansi kupembedza ndipo amayamikandikulemekeza Mulunguwawomodzichepetsa تَتَجَافَىٰ جُنُوبُهُمۡ عَنِ ٱلۡمَضَاجِعِ يَدۡعُونَ رَبَّهُمۡ خَوۡفًا وَطَمَعًا وَمِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ يُنفِقُونَ ١٦Iwo amasiya makama awo ndi cholinga chopempha kwa Ambuye wawo mwamantha ndi mwa chikhulupiriro. Ndipo amapereka zaulere kuchokera ku chuma chimene tidawapatsa فَلَا تَعۡلَمُ نَفۡسٌ مَّآ أُخۡفِيَ لَهُم مِّن قُرَّةِ أَعۡيُنٍ جَزَآءَۢ بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ١٧Tsopano palibe munthu amene amadziwa madalitso amene ali kuwasungira m’nkhokwe ngati malipiro a ntchito zawo zabwino أَفَمَن كَانَ مُؤۡمِنًا كَمَن كَانَ فَاسِقًاۚ لَّا يَسۡتَوُۥنَ ١٨Kodi munthu wokhulupirira angafanane ndi munthu woswa malamulo ndi woipa? Iyayi, sangafanane أَمَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَلَهُمۡ جَنَّٰتُ ٱلۡمَأۡوَىٰ نُزُلَۢا بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ١٩Iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, adzalandira minda ngati malo awo okhala chifukwa cha ntchito zawo zabwino zimene anachita وَأَمَّا ٱلَّذِينَ فَسَقُواْ فَمَأۡوَىٰهُمُ ٱلنَّارُۖ كُلَّمَآ أَرَادُوٓاْ أَن يَخۡرُجُواْ مِنۡهَآ أُعِيدُواْ فِيهَا وَقِيلَ لَهُمۡ ذُوقُواْ عَذَابَ ٱلنَّارِ ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تُكَذِّبُونَ ٢٠Ndipo iwo amene amaswa malamulo, malo awo okhala ndi kumoto ndipo nthawi zonse zimene iwo adzafuna kuchokako, adzabwezedwanso komweko. Ndipo kudzanenedwa kwa iwo kuti, “Lawani ululu wa moto umene munkati ndi bodza.” وَلَنُذِيقَنَّهُم مِّنَ ٱلۡعَذَابِ ٱلۡأَدۡنَىٰ دُونَ ٱلۡعَذَابِ ٱلۡأَكۡبَرِ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ ٢١Ndipo, ndithudi, Ife tidzawalawitsa, chilango cha m’moyo uno chisanadze, chilango choyamba kuti mwina akhoza kutembenuka وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّن ذُكِّرَ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِۦ ثُمَّ أَعۡرَضَ عَنۡهَآۚ إِنَّا مِنَ ٱلۡمُجۡرِمِينَ مُنتَقِمُونَ ٢٢Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amati akakumbutsidwa chiphunzitso cha Ambuye wake, iye amabwerera m’mbuyo? Ndithudi Ife tidzalanga anthu ochimwa وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ فَلَا تَكُن فِي مِرۡيَةٍ مِّن لِّقَآئِهِۦۖ وَجَعَلۡنَٰهُ هُدًى لِّبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٢٣Ndipo, ndithudi, Ife tidamupatsa Buku Mose ndipo musakayike za kulandira kwake ndipo tidalipanga ilo kukhala chotsogolera ana a Israyeli وَجَعَلۡنَا مِنۡهُمۡ أَئِمَّةً يَهۡدُونَ بِأَمۡرِنَا لَمَّا صَبَرُواْۖ وَكَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يُوقِنُونَ ٢٤Ndipo tidasankha pakati pawo, atsogoleri amene amapereka malangizo potsatira malamulo athu, pamene iwo anali kupirira ndi kukhulupirira mu chiphunzitso chathu إِنَّ رَبَّكَ هُوَ يَفۡصِلُ بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فِيمَا كَانُواْ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ ٢٥Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo pa tsiku louka kwa akufa pa nkhani zimene anali kutsutsana أَوَلَمۡ يَهۡدِ لَهُمۡ كَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِن قَبۡلِهِم مِّنَ ٱلۡقُرُونِ يَمۡشُونَ فِي مَسَٰكِنِهِمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍۚ أَفَلَا يَسۡمَعُونَ ٢٦Kodi icho sichiwaphunzitsa phunziro kuti kodi ndi mibadwo ingati imene tidaononga iwo asanadze, m’nyumba zawo zimene amalowa ndi kutulukamo? Ndithudi mu izo muli chiphunzitso. Kodi iwo sangamve أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّا نَسُوقُ ٱلۡمَآءَ إِلَى ٱلۡأَرۡضِ ٱلۡجُرُزِ فَنُخۡرِجُ بِهِۦ زَرۡعًا تَأۡكُلُ مِنۡهُ أَنۡعَٰمُهُمۡ وَأَنفُسُهُمۡۚ أَفَلَا يُبۡصِرُونَ ٢٧Kodi iwo saona kuti Ife timagwetsa mvula panthaka youma ndi kumeretsa mbewu zimene iwo ndi ziweto zawo zimadya? Kodi alibe maso oti angaone وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡفَتۡحُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ ٢٨Iwo amafunsa kuti “Kodi chiweruzo chimenechi chidzachitika liti ngati zimene munenazi ndi zoona?” قُلۡ يَوۡمَ ٱلۡفَتۡحِ لَا يَنفَعُ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِيمَٰنُهُمۡ وَلَا هُمۡ يُنظَرُونَ ٢٩Nena, “Pa tsiku lachiweruzo, chikhulupiriro cha iwo amene sakhulupirira sichidzawathandiza ndiponso sadzapeza mpumulo.” فَأَعۡرِضۡ عَنۡهُمۡ وَٱنتَظِرۡ إِنَّهُم مُّنتَظِرُونَ ٣٠Kotero asiye okha ndipo dikira ndithudi nawonso ali kudikira

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.