Millat al-Islam

Chapter 65 · 12 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah At-Talaq in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah At-Talaq (1112 reciters)
Medinanسورة الطلاق12 verses

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّبِيُّ إِذَا طَلَّقۡتُمُ ٱلنِّسَآءَ فَطَلِّقُوهُنَّ لِعِدَّتِهِنَّ وَأَحۡصُواْ ٱلۡعِدَّةَۖ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ رَبَّكُمۡۖ لَا تُخۡرِجُوهُنَّ مِنۢ بُيُوتِهِنَّ وَلَا يَخۡرُجۡنَ إِلَّآ أَن يَأۡتِينَ بِفَٰحِشَةٍ مُّبَيِّنَةٍۚ وَتِلۡكَ حُدُودُ ٱللَّهِۚ وَمَن يَتَعَدَّ حُدُودَ ٱللَّهِ فَقَدۡ ظَلَمَ نَفۡسَهُۥۚ لَا تَدۡرِي لَعَلَّ ٱللَّهَ يُحۡدِثُ بَعۡدَ ذَٰلِكَ أَمۡرًا ١Oh iwe Mtumwi! Ngati usudzula akazi ako, asudzule potsatira nthawi zawo. Ndipo werenga bwino bwino masiku awo. Ndipo opani Mulungu Ambuye wanu ndipo musawapirikitse m’nyumba zawo ndipo iwo asachoke pokhapokha ngati iwo apalamula mlandu wachigololo. Amenewa ndiwo malamulo amene akhazikitsidwa ndi Mulungu. Ndipo aliyense amene aphwanya malamulo a Mulungu, ndithudi, amapondereza mzimu wake. Inu Al Talaq 605 simudziwa kuti, mwina, Mulungu adzakukumanizaninso فَإِذَا بَلَغۡنَ أَجَلَهُنَّ فَأَمۡسِكُوهُنَّ بِمَعۡرُوفٍ أَوۡ فَارِقُوهُنَّ بِمَعۡرُوفٍ وَأَشۡهِدُواْ ذَوَيۡ عَدۡلٍ مِّنكُمۡ وَأَقِيمُواْ ٱلشَّهَٰدَةَ لِلَّهِۚ ذَٰلِكُمۡ يُوعَظُ بِهِۦ مَن كَانَ يُؤۡمِنُ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِۚ وَمَن يَتَّقِ ٱللَّهَ يَجۡعَل لَّهُۥ مَخۡرَجًا ٢Ndipo ngati iwo ali pafupi kukwaniritsa nthawi yawo, mukhoza kuwasunga mwaubwino kapena kuwasiya mwaulemu. Ndipo itanani mboni ziwiri za chilungamo kuchokera pakati panu. Ndipo perekani umboni wanu chifukwa cha Mulungu. Limeneli ndi langizo limene laperekedwa kwa iye amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza. Ndipo aliyense amene aopa Mulungu, Iye adzamupulumutsa وَيَرۡزُقۡهُ مِنۡ حَيۡثُ لَا يَحۡتَسِبُۚ وَمَن يَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱللَّهِ فَهُوَ حَسۡبُهُۥٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ بَٰلِغُ أَمۡرِهِۦۚ قَدۡ جَعَلَ ٱللَّهُ لِكُلِّ شَيۡءٍ قَدۡرًا ٣Ndipo Iye adzamupatsa zinthu kuchokera ku mbali imene sanali kuyembekeza. Ndipo aliyense amene amakhulupirira mwa Mulungu, Iye adzamupatsa chili chonse. Mulungu, ndithudi, adzamupatsa iye zofuna zake zonse. Ndithudi Mulungu adakhazikitsa muyeso wa chilichonse وَٱلَّٰٓـِٔي يَئِسۡنَ مِنَ ٱلۡمَحِيضِ مِن نِّسَآئِكُمۡ إِنِ ٱرۡتَبۡتُمۡ فَعِدَّتُهُنَّ ثَلَٰثَةُ أَشۡهُرٍ وَٱلَّٰٓـِٔي لَمۡ يَحِضۡنَۚ وَأُوْلَٰتُ ٱلۡأَحۡمَالِ أَجَلُهُنَّ أَن يَضَعۡنَ حَمۡلَهُنَّۚ وَمَن يَتَّقِ ٱللَّهَ يَجۡعَل لَّهُۥ مِنۡ أَمۡرِهِۦ يُسۡرًا ٤Ndipo ena akazi anu amene adasiya kupita kumwezi, kwa iwo nthawi yawo yodikira, ngati inu mukaika, ndi miyezi itatu ndipo iwo amene anasiyiratu, nthawi yawo idzakhala chimodzimodzi. Ndipo iwo amene ali ndi akazi odwala pakati, nthawi yawo idzakhala mpaka pamene abereka. Ndipo aliyense amene amaopa Mulungu, Iye adzamuchepetsera mavuto ake ذَٰلِكَ أَمۡرُ ٱللَّهِ أَنزَلَهُۥٓ إِلَيۡكُمۡۚ وَمَن يَتَّقِ ٱللَّهَ يُكَفِّرۡ عَنۡهُ سَيِّـَٔاتِهِۦ وَيُعۡظِمۡ لَهُۥٓ أَجۡرًا ٥Uwu ndi ulamuliro wa Mulungu umene wakutumizirani inu. Ndipo aliyense amene aopa Mulungu, Iye adzamuchotsera zoipa zake. Ndipo Iye adzamuchulukitsira mphotho yake أَسۡكِنُوهُنَّ مِنۡ حَيۡثُ سَكَنتُم مِّن وُجۡدِكُمۡ وَلَا تُضَآرُّوهُنَّ لِتُضَيِّقُواْ عَلَيۡهِنَّۚ وَإِن كُنَّ أُوْلَٰتِ حَمۡلٍ فَأَنفِقُواْ عَلَيۡهِنَّ حَتَّىٰ يَضَعۡنَ حَمۡلَهُنَّۚ فَإِنۡ أَرۡضَعۡنَ لَكُمۡ فَـَٔاتُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ وَأۡتَمِرُواْ بَيۡنَكُم بِمَعۡرُوفٍۖ وَإِن تَعَاسَرۡتُمۡ فَسَتُرۡضِعُ لَهُۥٓ أُخۡرَىٰ ٦Khalani nawo monga momwe inu muli kukhalira, molingana ndi kupeza kwanu. Musawazunze ndi cholinga chowasowetsa mtendere. Ngati iwo ali ndi pakati, asamalireni mpaka pamene iwo abereka. Ndipo ngati iwo ali kuyamwitsa, apatseni malipiro awo ndipo lemekezanani. Ndipo ngati pali mavuto oti simuli kugwirizana m’banja, pezani Mayi wina kuti ayamwitse mwana m’malo mwake لِيُنفِقۡ ذُو سَعَةٍ مِّن سَعَتِهِۦۖ وَمَن قُدِرَ عَلَيۡهِ رِزۡقُهُۥ فَلۡيُنفِقۡ مِمَّآ ءَاتَىٰهُ ٱللَّهُۚ لَا يُكَلِّفُ ٱللَّهُ نَفۡسًا إِلَّا مَآ ءَاتَىٰهَاۚ سَيَجۡعَلُ ٱللَّهُ بَعۡدَ عُسۡرٍ يُسۡرًا ٧Mulekeni munthu wolemera kuti apereke molingana ndi chuma chake ndipo munthu wosauka molingana ndi mmene Mulungu adamupatsira iye. Mulungu sakhazika mtulo wolemera pa munthu umene sangathe kuunyamula. Mulungu adzapereka mtendere mavuto akatha وَكَأَيِّن مِّن قَرۡيَةٍ عَتَتۡ عَنۡ أَمۡرِ رَبِّهَا وَرُسُلِهِۦ فَحَاسَبۡنَٰهَا حِسَابًا شَدِيدًا وَعَذَّبۡنَٰهَا عَذَابًا نُّكۡرًا ٨Ndipo ndi mizinda yambiri imene idaukira malamulo a Mulungu ndi Atumwi ndipo Ife tidayilanga iyo ndipo tidzailanga ndi chilango choopsa zedi فَذَاقَتۡ وَبَالَ أَمۡرِهَا وَكَانَ عَٰقِبَةُ أَمۡرِهَا خُسۡرًا ٩Motero iyo idalawa mphotho ya kusakhulupilira kwake ndipo mapeto a kusakhulupilira adali chionongeko أَعَدَّ ٱللَّهُ لَهُمۡ عَذَابًا شَدِيدًاۖ فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ يَٰٓأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْۚ قَدۡ أَنزَلَ ٱللَّهُ إِلَيۡكُمۡ ذِكۡرًا ١٠Mulungu wawakonzeraiwochilangochoopsa. Moteroopani Mulungu oh inu anthu ozindikira! Inu amene mwakhulupirira, ndithudi, Mulungu watumiza chikumbutso kwa inu رَّسُولًا يَتۡلُواْ عَلَيۡكُمۡ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ مُبَيِّنَٰتٍ لِّيُخۡرِجَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ مِنَ ٱلظُّلُمَٰتِ إِلَى ٱلنُّورِۚ وَمَن يُؤۡمِنۢ بِٱللَّهِ وَيَعۡمَلۡ صَٰلِحًا يُدۡخِلۡهُ جَنَّٰتٍ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدًاۖ قَدۡ أَحۡسَنَ ٱللَّهُ لَهُۥ رِزۡقًا ١١Mtumwi amene ali kukuuzani zizindikiro zooneka za Mulungu ndi cholinga choti atsogolere onse amene akhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino kuchokera ku mdima kupita kowala. Ndipo aliyense amene amakhulupirira mwa Mulungu ndipo amachita ntchito zabwino, Iye adzamulowetsa m’minda imene pansi pake pamayenda mitsinje kuti adzakhaleko mpaka kalekale. Ndithudi Mulungu wawapatsa iwo mphotho yabwino kwambiri ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَ سَبۡعَ سَمَٰوَٰتٍ وَمِنَ ٱلۡأَرۡضِ مِثۡلَهُنَّۖ يَتَنَزَّلُ ٱلۡأَمۡرُ بَيۡنَهُنَّ لِتَعۡلَمُوٓاْ أَنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ قَدِيرٌ وَأَنَّ ٱللَّهَ قَدۡ أَحَاطَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عِلۡمَۢا ١٢Ndi Mulungu amene adalenga miyamba isanu ndi iwiri ndi dziko lapansi lolingana nayo. Malamulo ake amatsatiridwa ndi izo kuti inu mukhoza kudziwa kuti Mulungu ali ndi mphamvu pa zinthu zonse ndipo kuti Mulungu amadziwa chilichonse

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.