بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
يسٓ ١Ya seen وَٱلۡقُرۡءَانِ ٱلۡحَكِيمِ ٢Ndili kulumbira pali Buku la nzeru la Korani إِنَّكَ لَمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ٣Ndithudi iwe ndiwe mmodzi mwa amene adatumizidwa عَلَىٰ صِرَٰطٍ مُّسۡتَقِيمٍ ٤Pa njira yoyenera تَنزِيلَ ٱلۡعَزِيزِ ٱلرَّحِيمِ ٥Ichi ndi chivumbulutso cha Mwini mphamvu ndi Mwini chisoni لِتُنذِرَ قَوۡمًا مَّآ أُنذِرَ ءَابَآؤُهُمۡ فَهُمۡ غَٰفِلُونَ ٦Kuti uwachenjeze anthu amene makolo awo sadachenjezedwe, kotero iwo ndi osamvera لَقَدۡ حَقَّ ٱلۡقَوۡلُ عَلَىٰٓ أَكۡثَرِهِمۡ فَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ ٧Ndithudi liwu la chilango latsimikizidwa kwa ambiri a iwo koma iwo sali okhulupirira إِنَّا جَعَلۡنَا فِيٓ أَعۡنَٰقِهِمۡ أَغۡلَٰلًا فَهِيَ إِلَى ٱلۡأَذۡقَانِ فَهُم مُّقۡمَحُونَ ٨Ife taika magoli m’makosi mwawo, amene afika m’zigama ndipo mitu yawo yanyamulidwa وَجَعَلۡنَا مِنۢ بَيۡنِ أَيۡدِيهِمۡ سَدًّا وَمِنۡ خَلۡفِهِمۡ سَدًّا فَأَغۡشَيۡنَٰهُمۡ فَهُمۡ لَا يُبۡصِرُونَ ٩Ife taika chotchinga kutsogolo kwawo ndiponso kumbuyo kwawo ndipo tawakuta maso awo kuti asaone وَسَوَآءٌ عَلَيۡهِمۡ ءَأَنذَرۡتَهُمۡ أَمۡ لَمۡ تُنذِرۡهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ ١٠Ndi chimodzimodzi kaya uwachenjeza kapena ayi ndipo iwo sadzakhulupirira إِنَّمَا تُنذِرُ مَنِ ٱتَّبَعَ ٱلذِّكۡرَ وَخَشِيَ ٱلرَّحۡمَٰنَ بِٱلۡغَيۡبِۖ فَبَشِّرۡهُ بِمَغۡفِرَةٍ وَأَجۡرٍ كَرِيمٍ ١١Ukhoza kumuchenjeza yekhayo amene watsatira chikumbutso ndi kuopa Mwini Chisoni ngakhale kuti iye sangamuone. Kwa iye umuuze nkhani yabwino ya chikhululukiro ndi mphotho yopambana إِنَّا نَحۡنُ نُحۡيِ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَنَكۡتُبُ مَا قَدَّمُواْ وَءَاثَٰرَهُمۡۚ وَكُلَّ شَيۡءٍ أَحۡصَيۡنَٰهُ فِيٓ إِمَامٍ مُّبِينٍ ١٢Ndife amene tidzadzutsa anthu akufa ndi kulemba ntchito zonse za anthu ndi zizindikiro zimene asiya m’mbuyo: Talemba zonse mooneka bwino kwambiri m’buku وَٱضۡرِبۡ لَهُم مَّثَلًا أَصۡحَٰبَ ٱلۡقَرۡيَةِ إِذۡ جَآءَهَا ٱلۡمُرۡسَلُونَ ١٣Apatse chitsanzo cha anthu a mu mzinda umene mudadza Atumwi إِذۡ أَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡهِمُ ٱثۡنَيۡنِ فَكَذَّبُوهُمَا فَعَزَّزۡنَا بِثَالِثٍ فَقَالُوٓاْ إِنَّآ إِلَيۡكُم مُّرۡسَلُونَ ١٤Pamene Ife tidawatumizira iwo awiri, iwo adawakana. Motero Ife tidatumizanso wina wachitatu, ndipo iwo adati, “Ndithudi ife tatumizidwa kwa inu.” قَالُواْ مَآ أَنتُمۡ إِلَّا بَشَرٌ مِّثۡلُنَا وَمَآ أَنزَلَ ٱلرَّحۡمَٰنُ مِن شَيۡءٍ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا تَكۡذِبُونَ ١٥Iwo adati, “Inu ndinu anthu ngati ife tomwe. Mwini chisoni sadavumbulutse china chilichonse! Inu muli kunama basi.” قَالُواْ رَبُّنَا يَعۡلَمُ إِنَّآ إِلَيۡكُمۡ لَمُرۡسَلُونَ ١٦Iwo adati, “Ambuye wathu akudziwa kuti ife tatumidwa.” وَمَا عَلَيۡنَآ إِلَّا ٱلۡبَلَٰغُ ٱلۡمُبِينُ ١٧“Udindo wathu ndi wongokuchenjezani basi.” قَالُوٓاْ إِنَّا تَطَيَّرۡنَا بِكُمۡۖ لَئِن لَّمۡ تَنتَهُواْ لَنَرۡجُمَنَّكُمۡ وَلَيَمَسَّنَّكُم مِّنَّا عَذَابٌ أَلِيمٌ ١٨Anthu adati, “Tili kuona malodza. Ngati mupitiriza tikuponyani miyala ndipo chilango chowawa chizadza pa inu.” قَالُواْ طَٰٓئِرُكُم مَّعَكُمۡ أَئِن ذُكِّرۡتُمۚ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٌ مُّسۡرِفُونَ ١٩Iwo adati, “Malodza anu akhale ndi inu! Kodi chifukwa chakuti mwachenjezedwa? Iyayi koma inu ndinu anthu ochimwa kwambiri وَجَآءَ مِنۡ أَقۡصَا ٱلۡمَدِينَةِ رَجُلٌ يَسۡعَىٰ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱتَّبِعُواْ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ٢٠Nthawi yomweyo munthu wina adadza ali kuthamanga kuchokera kumbali ina ya mzinda. Iye adati, “Anthu anga! Tsatirani iwo amene atumidwa ndi Mulungu.” ٱتَّبِعُواْ مَن لَّا يَسۡـَٔلُكُمۡ أَجۡرًا وَهُم مُّهۡتَدُونَ ٢١“Atsatireni iwo amene safuna malipiro kuchokera kwa inu pokukumbutsani mawu a Mulungu ndipo ndi otsogozedwa bwino.” وَمَالِيَ لَآ أَعۡبُدُ ٱلَّذِي فَطَرَنِي وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ ٢٢“Kodi pali chifukwa chotani chimene chingandilepheretse ine kuti ndim’pembedze Iye amene adandilenga popeza ndi kwa Iye kumene nonse mudzabwerera?” ءَأَتَّخِذُ مِن دُونِهِۦٓ ءَالِهَةً إِن يُرِدۡنِ ٱلرَّحۡمَٰنُ بِضُرٍّ لَّا تُغۡنِ عَنِّي شَفَٰعَتُهُمۡ شَيۡـًٔا وَلَا يُنقِذُونِ ٢٣“Kodi ine ndizipembedza milungu ina osati Iyeyo? Ngati ndi chifuniro cha Mwini chisoni kundizunza, kukhala pakati kwawo sikudzandithandiza ndipo iwo sadzandipulumutsa ayi.” إِنِّيٓ إِذًا لَّفِي ضَلَٰلٍ مُّبِينٍ ٢٤“Ndithudi ine ndikadatero, ndikadakhala mu chisokonezo choonekeratu.” إِنِّيٓ ءَامَنتُ بِرَبِّكُمۡ فَٱسۡمَعُونِ ٢٥Ndithudi ine ndakhulupirira mwa Ambuye wanu choncho ndimvereni.” قِيلَ ٱدۡخُلِ ٱلۡجَنَّةَۖ قَالَ يَٰلَيۡتَ قَوۡمِي يَعۡلَمُونَ ٢٦Kudanenedwa kwa iye kuti, “Lowa mu Paradiso.” Iye adafuula kuti, “Akadakhala kuti anthu anga adadziwa.” بِمَا غَفَرَ لِي رَبِّي وَجَعَلَنِي مِنَ ٱلۡمُكۡرَمِينَ ٢٧“Mmene Ambuye wanga wandionetsera chifundo chake kundiika mugulu la olemekezeka.”
۞ وَمَآ أَنزَلۡنَا عَلَىٰ قَوۡمِهِۦ مِنۢ بَعۡدِهِۦ مِن جُندٍ مِّنَ ٱلسَّمَآءِ وَمَا كُنَّا مُنزِلِينَ ٢٨Ndipo Ife sitidatumize padziko lapansi, kwa anthu ake, gulu lochokera kumwamba kuti lilimbane nawo ndipo sikudali koyenera kuti Ife tichite choncho إِن كَانَتۡ إِلَّا صَيۡحَةً وَٰحِدَةً فَإِذَا هُمۡ خَٰمِدُونَ ٢٩Udali mkuwo umodzi ndipo Oh! Onse adaonongedwa يَٰحَسۡرَةً عَلَى ٱلۡعِبَادِۚ مَا يَأۡتِيهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ ٣٠Kalanga akapolo anga! Iwo amaseka pofuna kunyoza Mtumwi aliyense amene adadza kwa iwo أَلَمۡ يَرَوۡاْ كَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّنَ ٱلۡقُرُونِ أَنَّهُمۡ إِلَيۡهِمۡ لَا يَرۡجِعُونَ ٣١Kodi iwo sadaone mibadwo yakale imene tidaiononga zaka zikwizikwi iwo asanabadwe? Ndipo iwo sadzabwereranso وَإِن كُلٌّ لَّمَّا جَمِيعٌ لَّدَيۡنَا مُحۡضَرُونَ ٣٢onse, popanda opatuka, adzadza kwa Ife وَءَايَةٌ لَّهُمُ ٱلۡأَرۡضُ ٱلۡمَيۡتَةُ أَحۡيَيۡنَٰهَا وَأَخۡرَجۡنَا مِنۡهَا حَبًّا فَمِنۡهُ يَأۡكُلُونَ ٣٣Chizindikiro kwa iwo ndi nthaka yakufa imene tidaidzutsa ndipo timatulutsa m’nthakamo nthangala zomwe iwo amadya وَجَعَلۡنَا فِيهَا جَنَّٰتٍ مِّن نَّخِيلٍ وَأَعۡنَٰبٍ وَفَجَّرۡنَا فِيهَا مِنَ ٱلۡعُيُونِ ٣٤Taika m’nthakamo minda ya mitengo ya tende ndi ya mphesa ndipo timathirira ndi madzi a m’kasupe لِيَأۡكُلُواْ مِن ثَمَرِهِۦ وَمَا عَمِلَتۡهُ أَيۡدِيهِمۡۚ أَفَلَا يَشۡكُرُونَ ٣٥Moti akhoza kumadya zipatso zake. Si manja awo amene adapanga zimenezi ayi. Kodi sangathokoze سُبۡحَٰنَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلۡأَزۡوَٰجَ كُلَّهَا مِمَّا تُنۢبِتُ ٱلۡأَرۡضُ وَمِنۡ أَنفُسِهِمۡ وَمِمَّا لَا يَعۡلَمُونَ ٣٦Ulemerero ukhale kwa Iye amene adalenga zinthu ziwiriziwiri, (chachimuna ndi chachikazi) zimene zimamera m’nthaka ndi zina za mtundu wawo ndi zinanso zimene sazidziwa وَءَايَةٌ لَّهُمُ ٱلَّيۡلُ نَسۡلَخُ مِنۡهُ ٱلنَّهَارَ فَإِذَا هُم مُّظۡلِمُونَ ٣٧Chizindikiro cha kwa iwo ndi usiku. Kuchokera ku iwo timachotsa usana ndipo iwo amakhala mu mdima وَٱلشَّمۡسُ تَجۡرِي لِمُسۡتَقَرٍّ لَّهَاۚ ذَٰلِكَ تَقۡدِيرُ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡعَلِيمِ ٣٨Dzuwa limayenda mofulumira kupita kumalo ake okapuma. Umenewu ndiwo ulamuliro wa Mwini Mphamvu zonse ndiponso Wodziwa chilichonse وَٱلۡقَمَرَ قَدَّرۡنَٰهُ مَنَازِلَ حَتَّىٰ عَادَ كَٱلۡعُرۡجُونِ ٱلۡقَدِيمِ ٣٩Ndipo mwezi tidaulamulira kuti uyende mumsewu wake mpaka pamene ukamabwerera ngati nthawi yoyamba m’maonekedwe لَا ٱلشَّمۡسُ يَنۢبَغِي لَهَآ أَن تُدۡرِكَ ٱلۡقَمَرَ وَلَا ٱلَّيۡلُ سَابِقُ ٱلنَّهَارِۚ وَكُلٌّ فِي فَلَكٍ يَسۡبَحُونَ ٤٠Dzuwa sililoledwa kupitirira mwezi ndipo usiku siupyola usana. Chilichonse chimayenda mumsewu wake وَءَايَةٌ لَّهُمۡ أَنَّا حَمَلۡنَا ذُرِّيَّتَهُمۡ فِي ٱلۡفُلۡكِ ٱلۡمَشۡحُونِ ٤١Ndipo chizindikiro china kwa iwo ndi chakuti tidanyamula makolo awo mu chombo chonyamula katundu وَخَلَقۡنَا لَهُم مِّن مِّثۡلِهِۦ مَا يَرۡكَبُونَ ٤٢Tidalenga zombo za mtundu umenewu kuti iwo azikweramo وَإِن نَّشَأۡ نُغۡرِقۡهُمۡ فَلَا صَرِيخَ لَهُمۡ وَلَا هُمۡ يُنقَذُونَ ٤٣Timawamiza tikafuna ndipo palibe amene angawathandize ndipo sangathe kupulumutsidwa إِلَّا رَحۡمَةً مِّنَّا وَمَتَٰعًا إِلَىٰ حِينٍ ٤٤Kupatula kudzera m’chifundo chathu ndi kuwapatsa chisangalalo cha kanthawi kochepa وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ٱتَّقُواْ مَا بَيۡنَ أَيۡدِيكُمۡ وَمَا خَلۡفَكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ ٤٥Pamene zinenedwa kwa iwo kuti, “Opani chinthu chimene chili patsogolo panu ndi pambuyo panu kuti mwina Mulungu angakuonetsereni chifundo” ndipo iwo samvera ayi وَمَا تَأۡتِيهِم مِّنۡ ءَايَةٍ مِّنۡ ءَايَٰتِ رَبِّهِمۡ إِلَّا كَانُواْ عَنۡهَا مُعۡرِضِينَ ٤٦Ndithudi palibe chizindikiro chochokera kwa Ambuye wawo chimene iwo amachivomera. Ndipo iwo salabadira وَإِذَا قِيلَ لَهُمۡ أَنفِقُواْ مِمَّا رَزَقَكُمُ ٱللَّهُ قَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَنُطۡعِمُ مَن لَّوۡ يَشَآءُ ٱللَّهُ أَطۡعَمَهُۥٓ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا فِي ضَلَٰلٍ مُّبِينٍ ٤٧Ndipo pamene auzidwa kuti, “Perekani gawo la chopereka chaulere pa zinthu zimene Mulungu wakupatsani.” Anthu osakhulupirira amanena kwa anthu okhulupirira kuti, “Kodi ife tizidyetsa iwo amene Mulungu atafuna akhoza kuwadyetsa? Ndithudi inu ndi osochera kwambiri.” وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ ٤٨Iwo amanenanso kuti, “Kodi lonjezo limeneli la tsiku lachiweruzo lidzatsimikizidwa liti, ngati zimene uli kunenazi ndi zoona?” مَا يَنظُرُونَ إِلَّا صَيۡحَةً وَٰحِدَةً تَأۡخُذُهُمۡ وَهُمۡ يَخِصِّمُونَ ٤٩Angodikira mkokomo umodzi wokha basi umene udzadza pa nthawi imene iwo ali kutsutsana فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ تَوۡصِيَةً وَلَآ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِمۡ يَرۡجِعُونَ ٥٠Iwo sadzakhala ndi mwayi wosiya mawu kapena kubwerera kwa abale awo وَنُفِخَ فِي ٱلصُّورِ فَإِذَا هُم مِّنَ ٱلۡأَجۡدَاثِ إِلَىٰ رَبِّهِمۡ يَنسِلُونَ ٥١Pamene lipenga lidzamveka, taona, kuchokera ku manda, anthu adzathamanga kupita kwa Ambuye wawo قَالُواْ يَٰوَيۡلَنَا مَنۢ بَعَثَنَا مِن مَّرۡقَدِنَاۜۗ هَٰذَا مَا وَعَدَ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَصَدَقَ ٱلۡمُرۡسَلُونَ ٥٢“Tsoka kwa ife!” Iwo adzatero. “Ndani amene watidzutsa kuchokera kumalo athu a mpumulo?” Ichi ndi chimene Ambuye wachifundo adalonjeza. “Atumwi adanenadi zoona!” إِن كَانَتۡ إِلَّا صَيۡحَةً وَٰحِدَةً فَإِذَا هُمۡ جَمِيعٌ لَّدَيۡنَا مُحۡضَرُونَ ٥٣Ndithudi ndi mfuwu umodzi wokha, onse panthawiyo, adzasonkhanitsidwa kwa Ife فَٱلۡيَوۡمَ لَا تُظۡلَمُ نَفۡسٌ شَيۡـًٔا وَلَا تُجۡزَوۡنَ إِلَّا مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ ٥٤Patsiku limeneli sipadzakhala mzimu umene siudzaweruzidwa ndipo inu mudzalandira mphotho molingana ndi ntchito zanu إِنَّ أَصۡحَٰبَ ٱلۡجَنَّةِ ٱلۡيَوۡمَ فِي شُغُلٍ فَٰكِهُونَ ٥٥Pa tsiku limeneli anthu okhala ku Paradiso adzakhala osangalala kwambiri هُمۡ وَأَزۡوَٰجُهُمۡ فِي ظِلَٰلٍ عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِ مُتَّكِـُٔونَ ٥٦Iwo pamodzi ndi akazi awo, adzakhala m’mithunzi ya nkhalango, pa mipando yawofowofo لَهُمۡ فِيهَا فَٰكِهَةٌ وَلَهُم مَّا يَدَّعُونَ ٥٧Iwo adzapeza m’menemo zipatso ndi zina zonse zimene adzafuna سَلَٰمٌ قَوۡلًا مِّن رَّبٍّ رَّحِيمٍ ٥٨“Mtendere” ndiwo mawu amene adzachokere kwa Mulungu, Mwini Chisoni وَٱمۡتَٰزُواْ ٱلۡيَوۡمَ أَيُّهَا ٱلۡمُجۡرِمُونَ ٥٩Ndipo Iye adzati, “Khalani kutali inu oipa tsiku lalero?” ۞ أَلَمۡ أَعۡهَدۡ إِلَيۡكُمۡ يَٰبَنِيٓ ءَادَمَ أَن لَّا تَعۡبُدُواْ ٱلشَّيۡطَٰنَۖ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوٌّ مُّبِينٌ ٦٠“Kodi Ine sindidakuchenjezeni, inu ana a Adamu, kuti musamagwadire Satana, chifukwa iyeyu ndi mdani wanu woonekeratu?” وَأَنِ ٱعۡبُدُونِيۚ هَٰذَا صِرَٰطٌ مُّسۡتَقِيمٌ ٦١“Ndi kuti muzindipembedza Ine? Ndithudi imeneyo ndiyo njira yoyenera.” وَلَقَدۡ أَضَلَّ مِنكُمۡ جِبِلًّا كَثِيرًاۖ أَفَلَمۡ تَكُونُواْ تَعۡقِلُونَ ٦٢Koma iye adasocheretsa anthu ambiri. Kodi mudalibe nzeru هَٰذِهِۦ جَهَنَّمُ ٱلَّتِي كُنتُمۡ تُوعَدُونَ ٦٣Imeneyi ndiyo Gahena imene munali kulonjezedwa ٱصۡلَوۡهَا ٱلۡيَوۡمَ بِمَا كُنتُمۡ تَكۡفُرُونَ ٦٤Lowani m’menemo tsiku lalero ngati chilango, chifukwa chakusakhulupirira kwanu ٱلۡيَوۡمَ نَخۡتِمُ عَلَىٰٓ أَفۡوَٰهِهِمۡ وَتُكَلِّمُنَآ أَيۡدِيهِمۡ وَتَشۡهَدُ أَرۡجُلُهُم بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ ٦٥Lero, Ife titseka pakamwa pawo, ndipo manja awo ndi amene ayankhule ndi Ife ndiponso miyendo yawo ichitira umboni pa ntchito zoipa zimene anali kuchita وَلَوۡ نَشَآءُ لَطَمَسۡنَا عَلَىٰٓ أَعۡيُنِهِمۡ فَٱسۡتَبَقُواْ ٱلصِّرَٰطَ فَأَنَّىٰ يُبۡصِرُونَ ٦٦Chikadakhala cholinga chathu, tikadawachititsa khungu kuti azivutika poyenda. Nanga akadaona bwanji machimo awo وَلَوۡ نَشَآءُ لَمَسَخۡنَٰهُمۡ عَلَىٰ مَكَانَتِهِمۡ فَمَا ٱسۡتَطَٰعُواْ مُضِيًّا وَلَا يَرۡجِعُونَ ٦٧Chikadakhala cholinga chathu, tikadawasintha kuti asanduke china chake pamalo pamene adaimirira, kuti asapite patsogolo kapena kubwerera m’mbuyo وَمَن نُّعَمِّرۡهُ نُنَكِّسۡهُ فِي ٱلۡخَلۡقِۚ أَفَلَا يَعۡقِلُونَ ٦٨Aliyense amene timamukalambitsa, timam’bwezera ku ubwana. Kodi iwo sangazindikire chimenechi وَمَا عَلَّمۡنَٰهُ ٱلشِّعۡرَ وَمَا يَنۢبَغِي لَهُۥٓۚ إِنۡ هُوَ إِلَّا ذِكۡرٌ وَقُرۡءَانٌ مُّبِينٌ ٦٩Ife sitidamuphunzitse iye ndakatulo ayi ndiponso si koyenera kuti akhale mlakatuli. Ichi si china koma chikumbutso ndi dongosolo la Korani لِّيُنذِرَ مَن كَانَ حَيًّا وَيَحِقَّ ٱلۡقَوۡلُ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ ٧٠Limene lichenjeza anthu a moyo ndi kupereka chiweruzo kwa anthu osakhulupirira أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّا خَلَقۡنَا لَهُم مِّمَّا عَمِلَتۡ أَيۡدِينَآ أَنۡعَٰمًا فَهُمۡ لَهَا مَٰلِكُونَ ٧١Kodi iwo saona kuti pakati pa zinthu zimene tidalenga ndi manja athu tidawalengera nyama zimene iwo amazilamulira وَذَلَّلۡنَٰهَا لَهُمۡ فَمِنۡهَا رَكُوبُهُمۡ وَمِنۡهَا يَأۡكُلُونَ ٧٢Tidalamula zimenezi kuti zizimvera malamulo awo kuti akhoza kumakwera ndi zina zoti azidya وَلَهُمۡ فِيهَا مَنَٰفِعُ وَمَشَارِبُۚ أَفَلَا يَشۡكُرُونَ ٧٣Ndipo amapezanso phindu lina lolekana. Iwo amamwa mkaka kuchokera ku izo. Kodi iwo sangathokoze وَٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ ءَالِهَةً لَّعَلَّهُمۡ يُنصَرُونَ ٧٤Iwo akhazikitsa milungu ina powonjezera pa Mulungu weniweni, poganiza kuti mwina akhoza kuthandizidwa لَا يَسۡتَطِيعُونَ نَصۡرَهُمۡ وَهُمۡ لَهُمۡ جُندٌ مُّحۡضَرُونَ ٧٥Milunguyo siingawathandize. Iwo adzatengedwa mwankhondo kunka ku chilango فَلَا يَحۡزُنكَ قَوۡلُهُمۡۘ إِنَّا نَعۡلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعۡلِنُونَ ٧٦Usalole kuti mawu awo akumvetse chisoni. Ife tikudziwa zonse zimene azibisa ndi zonse zimene akuzionetsa أَوَلَمۡ يَرَ ٱلۡإِنسَٰنُ أَنَّا خَلَقۡنَٰهُ مِن نُّطۡفَةٍ فَإِذَا هُوَ خَصِيمٌ مُّبِينٌ ٧٧Kodi munthu, sadziwa kuti tidamulenga kuchokera ku dontho la umuna? Koma iye ndi otsutsana ndi Ife poyera وَضَرَبَ لَنَا مَثَلًا وَنَسِيَ خَلۡقَهُۥۖ قَالَ مَن يُحۡيِ ٱلۡعِظَٰمَ وَهِيَ رَمِيمٌ ٧٨Iye amatifanizira Ife ndi zina zake ndipo amaiwala za chilengedwe chake. Iye amafunsa kuti, “Kodi ndani amene adzapereka moyo ku mafupa oola?” قُلۡ يُحۡيِيهَا ٱلَّذِيٓ أَنشَأَهَآ أَوَّلَ مَرَّةٍۖ وَهُوَ بِكُلِّ خَلۡقٍ عَلِيمٌ ٧٩Nena “Iye amene adawalenga poyamba adzawapatsa moyo. Iye amadziwa chilichonse cha zolengedwa zake.” ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُم مِّنَ ٱلشَّجَرِ ٱلۡأَخۡضَرِ نَارًا فَإِذَآ أَنتُم مِّنۡهُ تُوقِدُونَ ٨٠Iye amene amakupatsani moto kuchokera ku mtengo wauwisi umene inu mumawunikira أَوَلَيۡسَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِقَٰدِرٍ عَلَىٰٓ أَن يَخۡلُقَ مِثۡلَهُمۚ بَلَىٰ وَهُوَ ٱلۡخَلَّٰقُ ٱلۡعَلِيمُ ٨١Kodi Iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, alibe mphamvu zolenga china chake chofanana nazo? Ndithudi ali nazo. Iye ndi Mlengi amene amadziwa chinthu china chilichonse إِنَّمَآ أَمۡرُهُۥٓ إِذَآ أَرَادَ شَيۡـًٔا أَن يَقُولَ لَهُۥ كُن فَيَكُونُ ٨٢Ndithudi pamene Iye afuna chinthu amangonena kuti, “Chikhale” ndipo chimakhaladi فَسُبۡحَٰنَ ٱلَّذِي بِيَدِهِۦ مَلَكُوتُ كُلِّ شَيۡءٍ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ ٨٣Ulemerero ukhale kwa Iye amene ali ndi ulamuliro pa chinthu china chilichonse; ndipo ndi kwa Iye kumene nonse mudzabwerera