Millat al-Islam

Chapter 10 · 109 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Yunus in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah Yunus (1195 reciters)
Meccanسورة يونس109 verses

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

الٓرۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡحَكِيمِ ١Alif Lam Ra. Awa ndi mavesi a Buku la zinthu zanzeru zenizeni أَكَانَ لِلنَّاسِ عَجَبًا أَنۡ أَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ رَجُلٍ مِّنۡهُمۡ أَنۡ أَنذِرِ ٱلنَّاسَ وَبَشِّرِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَنَّ لَهُمۡ قَدَمَ صِدۡقٍ عِندَ رَبِّهِمۡۗ قَالَ ٱلۡكَٰفِرُونَ إِنَّ هَٰذَا لَسَٰحِرٌ مُّبِينٌ ٢Kodi n’chodabwitsa kwa anthu kuti Ife tidavumbulutsa chivumbulutso kwa mmodzi wa iwo ponena, “Pereka chenjezo kwa anthu ndipo uwauze nkhani zabwino anthu okhulupirira kuti adzakhala ndi mpando wapamwamba kwa Ambuye wawo?” Anthu osakhulupirira adati: “Ndithudi uyu ndi wamatsenga enieni.” إِنَّ رَبَّكُمُ ٱللَّهُ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ فِي سِتَّةِ أَيَّامٍ ثُمَّ ٱسۡتَوَىٰ عَلَى ٱلۡعَرۡشِۖ يُدَبِّرُ ٱلۡأَمۡرَۖ مَا مِن شَفِيعٍ إِلَّا مِنۢ بَعۡدِ إِذۡنِهِۦۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُوهُۚ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ ٣Ndithudi Ambuye wanu ndi Mulungu, amene m’masiku asanu ndi limodzi adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo anabuka pamwamba pa Mpando wachifumu, nalamula zinthu zonse. Palibe wina amene adzalandira ulamuliro wopepesa kwa Mulungu pokhapokha atalandira chilolezo cha Mulungu. Ameneyo ndiye Mulungu Ambuye wanu, mpembedzeni Iye. Kodi simudzakumbukira إِلَيۡهِ مَرۡجِعُكُمۡ جَمِيعًاۖ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقًّاۚ إِنَّهُۥ يَبۡدَؤُاْ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥ لِيَجۡزِيَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ بِٱلۡقِسۡطِۚ وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَهُمۡ شَرَابٌ مِّنۡ حَمِيمٍ وَعَذَابٌ أَلِيمُۢ بِمَا كَانُواْ يَكۡفُرُونَ ٤Kwa Iye nonse mudzabwerera. Lonjezo la Mulungu ndi loona. Iye ndiye adayamba kulenga zolengedwa zonse ndipo pomaliza adzazipatsanso moyo kuti adzawalipire mwa chilungamo onse amene adakhulupirira mwa Iye ndipo ankachita ntchito zabwino. Anthu osakhulupirira adzamwa zakumwa zamadzi ogaduka ndi kulandira chilango chowawa chifukwa chosakhulupirira هُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ ٱلشَّمۡسَ ضِيَآءً وَٱلۡقَمَرَ نُورًا وَقَدَّرَهُۥ مَنَازِلَ لِتَعۡلَمُواْ عَدَدَ ٱلسِّنِينَ وَٱلۡحِسَابَۚ مَا خَلَقَ ٱللَّهُ ذَٰلِكَ إِلَّا بِٱلۡحَقِّۚ يُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٍ يَعۡلَمُونَ ٥Iye ndiye amene adalipanga dzuwa kukhala muuni ndi mwezi kukhala wowala ndipo adazikonzera modutsa kuti inu muzidziwa kuchuluka kwa zaka ndi chiwerengero. Iye sadazilenge chabe izo koma mu choonadi. Iye amafotokoza mawu ake momveka kwa anthu ake ozindikira إِنَّ فِي ٱخۡتِلَٰفِ ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ وَمَا خَلَقَ ٱللَّهُ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ لَأٓيَٰتٍ لِّقَوۡمٍ يَتَّقُونَ ٦Ndithudi mukasinthidwe ka usiku ndi usana ndi zimene Mulungu walenga kumwamba ndi dziko lapansi, muli zizindikiro kwa anthu okana uchimo إِنَّ ٱلَّذِينَ لَا يَرۡجُونَ لِقَآءَنَا وَرَضُواْ بِٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَٱطۡمَأَنُّواْ بِهَا وَٱلَّذِينَ هُمۡ عَنۡ ءَايَٰتِنَا غَٰفِلُونَ ٧Ndithudi iwo ndi anthu amene sayembekeza kuti adzakumana nafe ndipo amasangalala ndi moyo wa m’dziko lapansi ndi kukhutitsidwa nawo ndiponso amene salabadira mawu أُوْلَٰٓئِكَ مَأۡوَىٰهُمُ ٱلنَّارُ بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ ٨Iwo malo awo okhala ndi kumoto chifukwa cha zoipa zimene anali kuchita إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ يَهۡدِيهِمۡ رَبُّهُم بِإِيمَٰنِهِمۡۖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهِمُ ٱلۡأَنۡهَٰرُ فِي جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ ٩Ndithudi iwo amene akhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, Ambuye wawo adzawatsogolera m’chikhulupiriro chawo. Mitsinje idzakhala ili kuyenda pansi pawo m’minda ya mtendere دَعۡوَىٰهُمۡ فِيهَا سُبۡحَٰنَكَ ٱللَّهُمَّ وَتَحِيَّتُهُمۡ فِيهَا سَلَٰمٌۚ وَءَاخِرُ دَعۡوَىٰهُمۡ أَنِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ١٠Pemphero lawo mmenemo lidzakhala loti; “Ndinu Woyera Ambuye!” Ndipo kulonjerana kwawo kudzakhala koti: “Mtendere” ndipo kumapeto kwa pempho lawo adzati: “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu, Ambuye wa chilengedwe.” ۞ وَلَوۡ يُعَجِّلُ ٱللَّهُ لِلنَّاسِ ٱلشَّرَّ ٱسۡتِعۡجَالَهُم بِٱلۡخَيۡرِ لَقُضِيَ إِلَيۡهِمۡ أَجَلُهُمۡۖ فَنَذَرُ ٱلَّذِينَ لَا يَرۡجُونَ لِقَآءَنَا فِي طُغۡيَٰنِهِمۡ يَعۡمَهُونَ ١١Akadakhala kuti Mulungu amabweretsa msanga chilango kwa anthu monga momwe iwo amafunira zabwino kuti zidze mwansanga, nthawi yawo yofera ikadakwaniritsidwa. Kwa iwo amene saopa kukumana ndi Ife tidzawasiya mukusochera kwawo, akusowa chochita وَإِذَا مَسَّ ٱلۡإِنسَٰنَ ٱلضُّرُّ دَعَانَا لِجَنۢبِهِۦٓ أَوۡ قَاعِدًا أَوۡ قَآئِمًا فَلَمَّا كَشَفۡنَا عَنۡهُ ضُرَّهُۥ مَرَّ كَأَن لَّمۡ يَدۡعُنَآ إِلَىٰ ضُرٍّ مَّسَّهُۥۚ كَذَٰلِكَ زُيِّنَ لِلۡمُسۡرِفِينَ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ١٢Pamene mavuto amadza pa munthu, iye amapemphera kwa Ifemogonachanthiti, mokhalapansikapenamoimirira. Koma tikangomuchotsera mavuto ake, iye amatsatila njira zake kukhala ngati sadatipemphe kuti timuchotsere mavuto omwe adamupeza. Kotero zidakongoletsedwa kwa anthu oononga zimene anali kuchita وَلَقَدۡ أَهۡلَكۡنَا ٱلۡقُرُونَ مِن قَبۡلِكُمۡ لَمَّا ظَلَمُواْ وَجَآءَتۡهُمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ وَمَا كَانُواْ لِيُؤۡمِنُواْۚ كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلۡمُجۡرِمِينَ ١٣Zoonadi Ife tidaononga mibadwo imene idalipo inu musanadze, pamene iwo adachita zoipa, anawafikira Atumwi awo ndi umboni weniweni koma iwo sadakhulupilire, motero tidzawalipira anthu ochita zoipa ثُمَّ جَعَلۡنَٰكُمۡ خَلَٰٓئِفَ فِي ٱلۡأَرۡضِ مِنۢ بَعۡدِهِمۡ لِنَنظُرَ كَيۡفَ تَعۡمَلُونَ ١٤Ndipo Ife tidakupangani kukhala alowa mmalo awo m’dziko lawo pambuyo pawo, kuti tione mmene inu mungachitire وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَاتُنَا بَيِّنَٰتٍ قَالَ ٱلَّذِينَ لَا يَرۡجُونَ لِقَآءَنَا ٱئۡتِ بِقُرۡءَانٍ غَيۡرِ هَٰذَآ أَوۡ بَدِّلۡهُۚ قُلۡ مَا يَكُونُ لِيٓ أَنۡ أُبَدِّلَهُۥ مِن تِلۡقَآيِٕ نَفۡسِيٓۖ إِنۡ أَتَّبِعُ إِلَّا مَا يُوحَىٰٓ إِلَيَّۖ إِنِّيٓ أَخَافُ إِنۡ عَصَيۡتُ رَبِّي عَذَابَ يَوۡمٍ عَظِيمٍ ١٥Ndi pamene Mau athu awerengedwa kwa iwo momveka, anthu amene salabadira zakukumana nafe amanena kuti, “Bweretsa Buku la Korani losiyana ndi ili kapena ulisinthe.” Nena, “Siudindo wanga kusintha Buku ili mwa chifuniro changa. Ndithudi ine ndimangotsatira zokhazo zimene zavumbulutsidwa kwa ine. Ndithudi ine ndimaopa chilango cha tsiku lalikulu ngati nditanyoza Ambuye wanga.” قُل لَّوۡ شَآءَ ٱللَّهُ مَا تَلَوۡتُهُۥ عَلَيۡكُمۡ وَلَآ أَدۡرَىٰكُم بِهِۦۖ فَقَدۡ لَبِثۡتُ فِيكُمۡ عُمُرًا مِّن قَبۡلِهِۦٓۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ ١٦Nena, “Mulungu akadafuna, ine sindikadawerengailokwainundiponsoIyesakadakupatsani inu nzeru zoti mulidziwe. Ndithu moyo wanga wonse ndakhala ndili pakati panu, Bukuli lisadavumbulutsidwe. Kodi simungathe kuzindikira?” فَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا أَوۡ كَذَّبَ بِـَٔايَٰتِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلۡمُجۡرِمُونَ ١٧Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu kapena amene amakana Mau ake? Ndithudi anthu ochita zoipa sadzapambana ayi وَيَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَضُرُّهُمۡ وَلَا يَنفَعُهُمۡ وَيَقُولُونَ هَٰٓؤُلَآءِ شُفَعَٰٓؤُنَا عِندَ ٱللَّهِۚ قُلۡ أَتُنَبِّـُٔونَ ٱللَّهَ بِمَا لَا يَعۡلَمُ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَلَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ ١٨Iwo amapembedza zinthu zina, osati Mulungu, zimene sizingathe kuwapweteka kapena kuwathandiza ndipo amati,“Izi zidzatilankhuliraifekwa Mulungu.” Nena,“Kodi inu mukumuuza Mulungu za zinthu zimene Iye sazidziwa zomwe zili kumwamba kapena pa dziko lapansi? Iye ndi Woyera ndipo akhale wa pamwamba kuposa mafano awo.” وَمَا كَانَ ٱلنَّاسُ إِلَّآ أُمَّةً وَٰحِدَةً فَٱخۡتَلَفُواْۚ وَلَوۡلَا كَلِمَةٌ سَبَقَتۡ مِن رَّبِّكَ لَقُضِيَ بَيۡنَهُمۡ فِيمَا فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ ١٩Mtundu wa anthu unali umodzi koma anasemphana pambuyo pake. Ndipo kukanapanda kuti Mau a Ambuye wako ananenedwa kale, mkangano wawo ukanathetsedwa وَيَقُولُونَ لَوۡلَآ أُنزِلَ عَلَيۡهِ ءَايَةٌ مِّن رَّبِّهِۦۖ فَقُلۡ إِنَّمَا ٱلۡغَيۡبُ لِلَّهِ فَٱنتَظِرُوٓاْ إِنِّي مَعَكُم مِّنَ ٱلۡمُنتَظِرِينَ ٢٠Anthu osakhulupirira amanena kuti: “Kodi chifukwa ninji chizindikiro sichinaperekedwe kwa iye kuchokera kwa Ambuye wake?” Nena, “Mulungu yekha ndiye amene amadziwa chilichonse chobisika. Dikirani, nanenso ndili mmodzi mwa odikira.” وَإِذَآ أَذَقۡنَا ٱلنَّاسَ رَحۡمَةً مِّنۢ بَعۡدِ ضَرَّآءَ مَسَّتۡهُمۡ إِذَا لَهُم مَّكۡرٌ فِيٓ ءَايَاتِنَاۚ قُلِ ٱللَّهُ أَسۡرَعُ مَكۡرًاۚ إِنَّ رُسُلَنَا يَكۡتُبُونَ مَا تَمۡكُرُونَ ٢١Ndipo tikawalawitsa anthu mtendere pambuyo pa mavuto amene anawapeza, iwo amayamba kukonza chiwembu chotsutsa chivumbulutso chathu. Nena: “Mulungu ndi wa changu pokonza chiwembu. Ndithudi Angelo athu ali kulemba zonse zimene mumapanga za chiwembu.” هُوَ ٱلَّذِي يُسَيِّرُكُمۡ فِي ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِۖ حَتَّىٰٓ إِذَا كُنتُمۡ فِي ٱلۡفُلۡكِ وَجَرَيۡنَ بِهِم بِرِيحٍ طَيِّبَةٍ وَفَرِحُواْ بِهَا جَآءَتۡهَا رِيحٌ عَاصِفٌ وَجَآءَهُمُ ٱلۡمَوۡجُ مِن كُلِّ مَكَانٍ وَظَنُّوٓاْ أَنَّهُمۡ أُحِيطَ بِهِمۡ دَعَوُاْ ٱللَّهَ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ لَئِنۡ أَنجَيۡتَنَا مِنۡ هَٰذِهِۦ لَنَكُونَنَّ مِنَ ٱلشَّٰكِرِينَ ٢٢Iyendiyeameneamakuyendetsanipamtundandiponso pa nyanja mpaka pamene inu muli m’ngalawa ndipo izo zimayendetsedwa ndi mphepo yabwino imene iwo amasangalala nayo. Koma mphepo ya mkuntho imawafikira ndipo mafunde amadza kwa iwo kuchokera ku mbali zonse ndipo iwo amaganiza kuti yawapeza ndipo amapemphera kwa Mulungu momuyeretsera chipembedzo chake. “Ngati mutipulumutse ku mavuto awa, ife tidzakhala othokoza.” فَلَمَّآ أَنجَىٰهُمۡ إِذَا هُمۡ يَبۡغُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّۗ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِنَّمَا بَغۡيُكُمۡ عَلَىٰٓ أَنفُسِكُمۖ مَّتَٰعَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۖ ثُمَّ إِلَيۡنَا مَرۡجِعُكُمۡ فَنُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ ٢٣Ndipo pamene Mulungu adawapulumutsa, iwo adayamba kuchita zoipa pa dziko mopanda chilungamo. Oh inu anthu! Zoipa zanu simuchitira wina aliyense koma inu nokha. Chimenecho ndicho chisangalalo cha moyo wa pa dziko lapansi ndipo pambuyo pake inu mudzabwerera kwa Ife ndipo tidzakuuzani zonse zomwe mumachita إِنَّمَا مَثَلُ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا كَمَآءٍ أَنزَلۡنَٰهُ مِنَ ٱلسَّمَآءِ فَٱخۡتَلَطَ بِهِۦ نَبَاتُ ٱلۡأَرۡضِ مِمَّا يَأۡكُلُ ٱلنَّاسُ وَٱلۡأَنۡعَٰمُ حَتَّىٰٓ إِذَآ أَخَذَتِ ٱلۡأَرۡضُ زُخۡرُفَهَا وَٱزَّيَّنَتۡ وَظَنَّ أَهۡلُهَآ أَنَّهُمۡ قَٰدِرُونَ عَلَيۡهَآ أَتَىٰهَآ أَمۡرُنَا لَيۡلًا أَوۡ نَهَارًا فَجَعَلۡنَٰهَا حَصِيدًا كَأَن لَّمۡ تَغۡنَ بِٱلۡأَمۡسِۚ كَذَٰلِكَ نُفَصِّلُ ٱلۡأٓيَٰتِ لِقَوۡمٍ يَتَفَكَّرُونَ ٢٤Ndithudi chitsanzo cha moyo wadziko lapansi chili ngati mvula imene timatsitsa kuchokera kumwamba ndipo imameretsa zomera za pa dziko zimene amadya anthu ndi nyama mpaka pamene dziko likongola ndi zomerazo. Ndipo anthu ake amakhulupirira kuti amalipambana ndipo lamulo lathu limadza pa izo nthawi ya usiku kapena ya masana ndipo timaichita kukhala ngati mbewu yokololedwa imene kunalibe dzulo. Mmenemo ndi mmene timaululira chivumbulutso chathu kwa anthu oganiza وَٱللَّهُ يَدۡعُوٓاْ إِلَىٰ دَارِ ٱلسَّلَٰمِ وَيَهۡدِي مَن يَشَآءُ إِلَىٰ صِرَٰطٍ مُّسۡتَقِيمٍ ٢٥Mulungu ali kuitanira ku Nyumba ya mtendere, ndi kumutsogolera yemwe wamufuna kunjira yoyenera ۞ لِّلَّذِينَ أَحۡسَنُواْ ٱلۡحُسۡنَىٰ وَزِيَادَةٌۖ وَلَا يَرۡهَقُ وُجُوهَهُمۡ قَتَرٌ وَلَا ذِلَّةٌۚ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ ٢٦Kwa iwo onse amene amachita zabwino adzapeza zabwino ndi zoonjezerapo. Ndipo nkhope zawo sizidzakutidwa ndi fumbi kapena kunyozedwa. Iwo ndi anthu a ku Paradiso, komwe adzakhala mpaka kalekale وَٱلَّذِينَ كَسَبُواْ ٱلسَّيِّـَٔاتِ جَزَآءُ سَيِّئَةِۭ بِمِثۡلِهَا وَتَرۡهَقُهُمۡ ذِلَّةٌۖ مَّا لَهُم مِّنَ ٱللَّهِ مِنۡ عَاصِمٍۖ كَأَنَّمَآ أُغۡشِيَتۡ وُجُوهُهُمۡ قِطَعًا مِّنَ ٱلَّيۡلِ مُظۡلِمًاۚ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ ٢٧Ndipo iwo amene amachitazoipa, malipiroawondioipamofananandizimene adachita. Mnyozo udzawakuta ndipo iwo sadzakhala ndi wina aliyense wowateteza ku chilango chochokera kwa Mulungu. Ndipo nkhope zawo zidzaoneka ngati kuti zidakutidwa ndi mbali ya mdima wa usiku. Iwo adzakhala anthu a kumoto ndipo adzakhala kumeneko nthawi zonse وَيَوۡمَ نَحۡشُرُهُمۡ جَمِيعًا ثُمَّ نَقُولُ لِلَّذِينَ أَشۡرَكُواْ مَكَانَكُمۡ أَنتُمۡ وَشُرَكَآؤُكُمۡۚ فَزَيَّلۡنَا بَيۡنَهُمۡۖ وَقَالَ شُرَكَآؤُهُم مَّا كُنتُمۡ إِيَّانَا تَعۡبُدُونَ ٢٨Tsiku limene tidzawasonkhanitsa onse, Ife tidzati kwa anthu opembedza mafano: “Khalani m’malo mwanu, inu pamodzi ndi mafano anu.” Ife tidzawasiyanitsa wina ndi mnzake ndipo mafano awo adzati kwa iwo: “Sindife amene inu munali kupembedza ayi.” فَكَفَىٰ بِٱللَّهِ شَهِيدَۢا بَيۡنَنَا وَبَيۡنَكُمۡ إِن كُنَّا عَنۡ عِبَادَتِكُمۡ لَغَٰفِلِينَ ٢٩“Akukwanira Mulungu kukhala mboni pakati pa ife ndi inu. Ife sitidziwa kuti munali kutipembedza!” هُنَالِكَ تَبۡلُواْ كُلُّ نَفۡسٍ مَّآ أَسۡلَفَتۡۚ وَرُدُّوٓاْ إِلَى ٱللَّهِ مَوۡلَىٰهُمُ ٱلۡحَقِّۖ وَضَلَّ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ ٣٠Kumeneko mzimu uliwonse udzadziwa chimene unatsogoza. Iwo adzabwezedwa kwa Mulungu, Ambuye wawo woona ndipo zidzawasokonekera iwo zimene anali kupeka قُلۡ مَن يَرۡزُقُكُم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِ أَمَّن يَمۡلِكُ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡأَبۡصَٰرَ وَمَن يُخۡرِجُ ٱلۡحَيَّ مِنَ ٱلۡمَيِّتِ وَيُخۡرِجُ ٱلۡمَيِّتَ مِنَ ٱلۡحَيِّ وَمَن يُدَبِّرُ ٱلۡأَمۡرَۚ فَسَيَقُولُونَ ٱللَّهُۚ فَقُلۡ أَفَلَا تَتَّقُونَ ٣١Nena, “Kodi ndani amakupatsani zinthu kuchokera kumwamba ndi padziko lapansi? Kodi ndani amene amapereka mphamvu yakumva ndi kuona? Kodi ndani amatulutsa cha moyo kuchokera ku chakufa ndi kutulutsa chakufa kuchokera mu chamoyo? Ndani amene amalamulira zinthu zonse?” Onse adzanena kuti, “Ndi Mulungu.” Nena, “Kodi inu simungaope Mulungu?” فَذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمُ ٱلۡحَقُّۖ فَمَاذَا بَعۡدَ ٱلۡحَقِّ إِلَّا ٱلضَّلَٰلُۖ فَأَنَّىٰ تُصۡرَفُونَ ٣٢Ameneyondiye Mulungu,Ambuyewanuwoona. Kupatula choonadi, kodi ndi chiyani chimene chingakhalepo osati chisokonekero? Nanga ndi chifukwa chiyani inu muli kusocheretsedwa كَذَٰلِكَ حَقَّتۡ كَلِمَتُ رَبِّكَ عَلَى ٱلَّذِينَ فَسَقُوٓاْ أَنَّهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ ٣٣Kotero ndi mmene liwu la Ambuye wako latsimikizidwira kwa anthu ochita zoipa ndipo iwo sadzakhulupirira قُلۡ هَلۡ مِن شُرَكَآئِكُم مَّن يَبۡدَؤُاْ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥۚ قُلِ ٱللَّهُ يَبۡدَؤُاْ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥۖ فَأَنَّىٰ تُؤۡفَكُونَ ٣٤Nena, “Kodi ena a mafano anu angalenge china chake ndi kuchibwezeranso?” Nena, “Mulungu anayambitsa chilengedwendipoadzachibwezeranso.Nangandichifukwa chiyani mukusocheretsedwa?” قُلۡ هَلۡ مِن شُرَكَآئِكُم مَّن يَهۡدِيٓ إِلَى ٱلۡحَقِّۚ قُلِ ٱللَّهُ يَهۡدِي لِلۡحَقِّۗ أَفَمَن يَهۡدِيٓ إِلَى ٱلۡحَقِّ أَحَقُّ أَن يُتَّبَعَ أَمَّن لَّا يَهِدِّيٓ إِلَّآ أَن يُهۡدَىٰۖ فَمَا لَكُمۡ كَيۡفَ تَحۡكُمُونَ ٣٥Nena, “Kodi mafano anu angakulondolereni ku choonadi?” Nena, “Mulungu yekha ndiye amene angakulondolereni ku choonadi. Kodi ndani amene ayenera kutsatidwa? Iye amene amakulondolerani ku choonadi kapena iye amene sangathe chifukwa chakuti nayenso afuna kuti atsogozedwe? Kodi mukusiyanitsa bwanji?” وَمَا يَتَّبِعُ أَكۡثَرُهُمۡ إِلَّا ظَنًّاۚ إِنَّ ٱلظَّنَّ لَا يُغۡنِي مِنَ ٱلۡحَقِّ شَيۡـًٔاۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلِيمُۢ بِمَا يَفۡعَلُونَ ٣٦Ambiri a iwo satsatira china chilichonse koma zongoganiza. Komatu nkhani zongoganiza sizithandiza mu choonadi chilichonse. Ndithu Mulungu amadziwa zonse zimene iwo amachita وَمَا كَانَ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانُ أَن يُفۡتَرَىٰ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَلَٰكِن تَصۡدِيقَ ٱلَّذِي بَيۡنَ يَدَيۡهِ وَتَفۡصِيلَ ٱلۡكِتَٰبِ لَا رَيۡبَ فِيهِ مِن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٣٧Sizingatheke kuti Korani iyi ikhale yopeka ndiponso kuti siinachokere kwa Mulungu. Koma iyo imatsimikiza zinthu zonse zimene zidavumbulutsidwa kale ndi kufotokoza Mau a m’buku la Mulungu. Ilo ndi losakaikitsa ndipo ndi lochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse أَمۡ يَقُولُونَ ٱفۡتَرَىٰهُۖ قُلۡ فَأۡتُواْ بِسُورَةٍ مِّثۡلِهِۦ وَٱدۡعُواْ مَنِ ٱسۡتَطَعۡتُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ ٣٨Kapena iwo amati “Iye walipeka!” Nena: “Nanunso pekani mutu umodzi wolingana nalo ndipo itanani amene mungathe kuwaitana osakhala Mulungu ngati muli angwiro!” بَلۡ كَذَّبُواْ بِمَا لَمۡ يُحِيطُواْ بِعِلۡمِهِۦ وَلَمَّا يَأۡتِهِمۡ تَأۡوِيلُهُۥۚ كَذَٰلِكَ كَذَّبَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلظَّٰلِمِينَ ٣٩Iyayi. Iwo ali kutsutsa zinthu zimene sadziwa chilichonse cha izo pamene choona chake chisanafike kwa iwo. Mmenemonso ndi mmene anthu akale adakanira. Taonani zidali bwanji zotsatira za anthu ochita zoipa وَمِنۡهُم مَّن يُؤۡمِنُ بِهِۦ وَمِنۡهُم مَّن لَّا يُؤۡمِنُ بِهِۦۚ وَرَبُّكَ أَعۡلَمُ بِٱلۡمُفۡسِدِينَ ٤٠Ena a iwo amakhulupirira mu ilo pamene ena sakhulupirira ayi. Ndipo Ambuye wako amawadziwa kwambiri anthu owononga وَإِن كَذَّبُوكَ فَقُل لِّي عَمَلِي وَلَكُمۡ عَمَلُكُمۡۖ أَنتُم بَرِيٓـُٔونَ مِمَّآ أَعۡمَلُ وَأَنَا۠ بَرِيٓءٌ مِّمَّا تَعۡمَلُونَ ٤١Ngati iwo akukana iwe, nena: “Ine ndili ndi ntchito zanga ndipo nanunso muli ndi ntchito zanu. Inu muli kutali ndi zimene ndikuchita ndipo nanenso ndili kutali ndi zimene mukuchita.” وَمِنۡهُم مَّن يَسۡتَمِعُونَ إِلَيۡكَۚ أَفَأَنتَ تُسۡمِعُ ٱلصُّمَّ وَلَوۡ كَانُواْ لَا يَعۡقِلُونَ ٤٢Ena a iwo amakumvera iwe. Kodi iwe ungawapangitse agonthi kuti amve ngakhale kuti safuna kuzindikira وَمِنۡهُم مَّن يَنظُرُ إِلَيۡكَۚ أَفَأَنتَ تَهۡدِي ٱلۡعُمۡيَ وَلَوۡ كَانُواْ لَا يُبۡصِرُونَ ٤٣Ena a iwo amakuyang’ana iwe. Kodi iwe ungalangize njira kwa anthu a khungu pamene saona china chilichonse إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَظۡلِمُ ٱلنَّاسَ شَيۡـًٔا وَلَٰكِنَّ ٱلنَّاسَ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ ٤٤Ndithudi Mulungu salakwira anthu koma kuti anthu eni ake amadzipondereza okha وَيَوۡمَ يَحۡشُرُهُمۡ كَأَن لَّمۡ يَلۡبَثُوٓاْ إِلَّا سَاعَةً مِّنَ ٱلنَّهَارِ يَتَعَارَفُونَ بَيۡنَهُمۡۚ قَدۡ خَسِرَ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِلِقَآءِ ٱللَّهِ وَمَا كَانُواْ مُهۡتَدِينَ ٤٥Akumbutseni zatsiku limene adzawasonkhanitsa onse. Tsiku limeneli adzaona ngati kuti adangokhala ora limodzi lamasana. Iwo adzazindikirana wina ndi mnzake. Ndithudi olephera adzakhala iwo amene adakana za kukumana ndi Mulungu ndipo sanali otsogozedwa وَإِمَّا نُرِيَنَّكَ بَعۡضَ ٱلَّذِي نَعِدُهُمۡ أَوۡ نَتَوَفَّيَنَّكَ فَإِلَيۡنَا مَرۡجِعُهُمۡ ثُمَّ ٱللَّهُ شَهِيدٌ عَلَىٰ مَا يَفۡعَلُونَ ٤٦Kaya tikuonetsa zina za zimene tawalonjeza kapena kukuchititsa kuti ufe, ndi kwa Ife kumene onse adzabwerera ndipo Mulungu ndi mboni pa zimene akuchita وَلِكُلِّ أُمَّةٍ رَّسُولٌۖ فَإِذَا جَآءَ رَسُولُهُمۡ قُضِيَ بَيۡنَهُم بِٱلۡقِسۡطِ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ ٤٧Ndithudi m’mbadwo uliwonse uli ndi Mtumwi wake ndipo pamene Mtumwi wawo adza, nkhani yawo idzaweruzidwa mwa chilungamo pakati pawo ndipo sadzaponderezedwa وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ ٤٨Iwo amanena: “Kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa liti ngati ukunena zoona?” قُل لَّآ أَمۡلِكُ لِنَفۡسِي ضَرًّا وَلَا نَفۡعًا إِلَّا مَا شَآءَ ٱللَّهُۗ لِكُلِّ أُمَّةٍ أَجَلٌۚ إِذَا جَآءَ أَجَلُهُمۡ فَلَا يَسۡتَـٔۡخِرُونَ سَاعَةً وَلَا يَسۡتَقۡدِمُونَ ٤٩Nena, “Ine ndilibe mphamvu yopeza zabwino kapena kupewa choipa chimene chingadze pa ine kupatula ndi chifuniro cha Mulungu. M’badwo uliwonse uli ndi nthawi imene idakhazikitsidwa kale. Ndipo pamene nthawi yawo idza, iwo sadzatha kuichedwetsa kapena kuifulumizitsa.” قُلۡ أَرَءَيۡتُمۡ إِنۡ أَتَىٰكُمۡ عَذَابُهُۥ بَيَٰتًا أَوۡ نَهَارًا مَّاذَا يَسۡتَعۡجِلُ مِنۡهُ ٱلۡمُجۡرِمُونَ ٥٠Nena “Ndiuzeni! Ngati chilango chake chitadza pa inu nthawi ya usiku kapena masana kodi ndi gawo liti limene anthu ochita zoipa angalifulumize?” أَثُمَّ إِذَا مَا وَقَعَ ءَامَنتُم بِهِۦٓۚ ءَآلۡـَٰٔنَ وَقَدۡ كُنتُم بِهِۦ تَسۡتَعۡجِلُونَ ٥١Kodi inu mudzakhulupirira pamene chidza pa inu? Nanga! Tsopano siuja munali kuchifulumizitsa ثُمَّ قِيلَ لِلَّذِينَ ظَلَمُواْ ذُوقُواْ عَذَابَ ٱلۡخُلۡدِ هَلۡ تُجۡزَوۡنَ إِلَّا بِمَا كُنتُمۡ تَكۡسِبُونَ ٥٢Ndipo kudzanenedwa kwa anthu ochita zoipa! “Lawani chilango chosatha! Inu simudzalipidwa china chilichonse kupatula zimene munali kuchita.” ۞ وَيَسۡتَنۢبِـُٔونَكَ أَحَقٌّ هُوَۖ قُلۡ إِي وَرَبِّيٓ إِنَّهُۥ لَحَقٌّۖ وَمَآ أَنتُم بِمُعۡجِزِينَ ٥٣Ndipo amakufunsa kuti uwauze: “Kodi ndizoona?” Nena, “Indedi, pali Ambuye. Zimenezo ndi zoonadi ndipo inu simungazithawe ayi.” وَلَوۡ أَنَّ لِكُلِّ نَفۡسٍ ظَلَمَتۡ مَا فِي ٱلۡأَرۡضِ لَٱفۡتَدَتۡ بِهِۦۗ وَأَسَرُّواْ ٱلنَّدَامَةَ لَمَّا رَأَوُاْ ٱلۡعَذَابَۖ وَقُضِيَ بَيۡنَهُم بِٱلۡقِسۡطِ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ ٥٤Kukadakhala kuti munthu aliyense wochita zoipa anali ndi zinthu zonse zimene zili padziko lapansi ndipo amafuna kuzipereka ngati dipo loti adziombolere, ndipo iwo akanamva chisoni m’mitima yawo pamene akadaona chilango ndipo iwo adzaweruzidwa mwachilungamo ndiponso sadzaponderezedwa ai أَلَآ إِنَّ لِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۗ أَلَآ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقٌّ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ ٥٥Ndithudi mosakaika Mulungu ndiye Mwini wa chilichonse chimene chili mlengalenga ndi padziko lapansi. Ndithudi mosakaika lonjezo la Mulungu ndi loona. Koma ambiri a iwo sadziwa هُوَ يُحۡيِۦ وَيُمِيتُ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ ٥٦Iye ndiye amene amapereka moyo ndipo amaperekanso imfa, ndipo ndi kwa Iye kumene inu nonse mudzabwerera يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ قَدۡ جَآءَتۡكُم مَّوۡعِظَةٌ مِّن رَّبِّكُمۡ وَشِفَآءٌ لِّمَا فِي ٱلصُّدُورِ وَهُدًى وَرَحۡمَةٌ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ ٥٧Oh inu anthu! Chilangizo chabwino chadza kwa inu kuchokera kwa Ambuye wanu, chochiritsa zimene zili m’mitima mwanu, utsogoleri ndi madalitso kwa anthu okhulupirira m’choonadi قُلۡ بِفَضۡلِ ٱللَّهِ وَبِرَحۡمَتِهِۦ فَبِذَٰلِكَ فَلۡيَفۡرَحُواْ هُوَ خَيۡرٌ مِّمَّا يَجۡمَعُونَ ٥٨Nena, “M’chisomo ndi M’chisoni cha Mulungu asiyeni asangalale. Chifukwa izi ndi zabwino kuposa zimene akusonkhanitsa.” قُلۡ أَرَءَيۡتُم مَّآ أَنزَلَ ٱللَّهُ لَكُم مِّن رِّزۡقٍ فَجَعَلۡتُم مِّنۡهُ حَرَامًا وَحَلَٰلًا قُلۡ ءَآللَّهُ أَذِنَ لَكُمۡۖ أَمۡ عَلَى ٱللَّهِ تَفۡتَرُونَ ٥٩Ndiuzeni kodi Mulungu wakufulumizirani chiani? Ndipo mwazisandutsa zina kukhala zololedwa ndi zina zoletsedwa. Nena, Kodi Mulungu wakulolani kapena mukumpekera zabodza وَمَا ظَنُّ ٱلَّذِينَ يَفۡتَرُونَ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۗ إِنَّ ٱللَّهَ لَذُو فَضۡلٍ عَلَى ٱلنَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَشۡكُرُونَ ٦٠Kodi anthu amene amapeka mabodza okhudza Mulungu amaganiza chiyani za tsiku la kuuka kwa akufa? Ndithudi Mulungu ndi wabwino kwa anthu koma ambiri a iwo sathokoza ayi وَمَا تَكُونُ فِي شَأۡنٍ وَمَا تَتۡلُواْ مِنۡهُ مِن قُرۡءَانٍ وَلَا تَعۡمَلُونَ مِنۡ عَمَلٍ إِلَّا كُنَّا عَلَيۡكُمۡ شُهُودًا إِذۡ تُفِيضُونَ فِيهِۚ وَمَا يَعۡزُبُ عَن رَّبِّكَ مِن مِّثۡقَالِ ذَرَّةٍ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا فِي ٱلسَّمَآءِ وَلَآ أَصۡغَرَ مِن ذَٰلِكَ وَلَآ أَكۡبَرَ إِلَّا فِي كِتَٰبٍ مُّبِينٍ ٦١Chilichonse chimene uzichita ndiponso gawo lililonse limene uzilakatula la Korani ndipo chilichonse chimene muzichita, Ife ndife mboni pa icho pamene muli kuchichita. Palibe chobisika kwa Ambuye wanu, ngakhale chochepa ngati nyerere padziko lapansi kapena kumwamba. Palibe chaching’ono choposa ichi kapena chachikulu choposa ichi chimene sichilembedwa mu Buku أَلَآ إِنَّ أَوۡلِيَآءَ ٱللَّهِ لَا خَوۡفٌ عَلَيۡهِمۡ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ ٦٢Mosakaika! Ndithudi abwenzi a Mulungu ndipo amamukonda Iye kwambiri, sadzakhala ndi mantha ndiponso sadzadandaula ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَكَانُواْ يَتَّقُونَ ٦٣Iwo amene adakhulupirira ndipo anali kuopa Mulungu لَهُمُ ٱلۡبُشۡرَىٰ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَفِي ٱلۡأٓخِرَةِۚ لَا تَبۡدِيلَ لِكَلِمَٰتِ ٱللَّهِۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ ٦٤Kwa iwo ndi chisangalalo m’dziko lino ndiponso m’dziko limene lili n’kudza. Palibe kusintha kulikonse m’Mau a Mulungu. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu وَلَا يَحۡزُنكَ قَوۡلُهُمۡۘ إِنَّ ٱلۡعِزَّةَ لِلَّهِ جَمِيعًاۚ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ ٦٥Ndipo mawu awo asakukhumudwitse iwe. Ndithudi mphamvu zonse Mwini wake ndi Mulungu. Iye ndi wakumva ndi wodziwa أَلَآ إِنَّ لِلَّهِ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِۗ وَمَا يَتَّبِعُ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ شُرَكَآءَۚ إِن يَتَّبِعُونَ إِلَّا ٱلظَّنَّ وَإِنۡ هُمۡ إِلَّا يَخۡرُصُونَ ٦٦Mosakaika! Ndithudi Mulungu ndiye mwini wa zimene zili kumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo onse amene amapembedza milungu yabodza satsatira china chilichonse koma zinthu zopanda pake ndipo iwo amangopeka mabodza هُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلَّيۡلَ لِتَسۡكُنُواْ فِيهِ وَٱلنَّهَارَ مُبۡصِرًاۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّقَوۡمٍ يَسۡمَعُونَ ٦٧Iye ndiye amene adakupangirani usiku kuti muzipumula ndi usana kuti muziona. Ndithudi mu izi muli zizindikiro kwa anthu amene amamva قَالُواْ ٱتَّخَذَ ٱللَّهُ وَلَدًاۗ سُبۡحَٰنَهُۥۖ هُوَ ٱلۡغَنِيُّۖ لَهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ إِنۡ عِندَكُم مِّن سُلۡطَٰنِۭ بِهَٰذَآۚ أَتَقُولُونَ عَلَى ٱللَّهِ مَا لَا تَعۡلَمُونَ ٦٨Iwo amanena kuti: “Mulungu wabereka mwana wamwamuna.” Mulungu ayeretsedwe ndi zimenezo. “Iye ndi Wolemera. Zake ndi zonse zimene zili m’lengalenga ndi padzikolapansi. Paichiinumulibeumboni. Kodimukunena zinthu zokhudza Mulungu zimene simuzidziwa?” قُلۡ إِنَّ ٱلَّذِينَ يَفۡتَرُونَ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَ لَا يُفۡلِحُونَ ٦٩Nena, “Ndithudi iwo amene amapeka bodza lokhudza Mulungu sadzapambana ayi.” مَتَٰعٌ فِي ٱلدُّنۡيَا ثُمَّ إِلَيۡنَا مَرۡجِعُهُمۡ ثُمَّ نُذِيقُهُمُ ٱلۡعَذَابَ ٱلشَّدِيدَ بِمَا كَانُواْ يَكۡفُرُونَ ٧٠Chisangalalo cha kanthawi kochepa ka m’dziko lapansi ndipo ndi kwa Ife kumene adzabwerera ndipo Ife tidzawalawitsa chilango chowawa chifukwa cha kukana kwawo ۞ وَٱتۡلُ عَلَيۡهِمۡ نَبَأَ نُوحٍ إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِۦ يَٰقَوۡمِ إِن كَانَ كَبُرَ عَلَيۡكُم مَّقَامِي وَتَذۡكِيرِي بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ فَعَلَى ٱللَّهِ تَوَكَّلۡتُ فَأَجۡمِعُوٓاْ أَمۡرَكُمۡ وَشُرَكَآءَكُمۡ ثُمَّ لَا يَكُنۡ أَمۡرُكُمۡ عَلَيۡكُمۡ غُمَّةً ثُمَّ ٱقۡضُوٓاْ إِلَيَّ وَلَا تُنظِرُونِ ٧١Ndipo awerengere iwo za nkhani ya Nowa pamene iye adanena kwa anthu ake kuti: “oh! Inu anthu anga! Ngati muli kuipidwa ndi kukhala kwanga pakati panu ndi kukukumbutsani mawu a Mulungu, dziwani kuti ine ndaika chikhulupiliro changa mwa Mulungu motero inu musonkhanitse zopanga zanu ndi mafano anu ndipo inu musapange chiwembu mseri ayi. Gamulani chiweruzo chanu pa ine ndipo musandipatse nthawi ayi.” فَإِن تَوَلَّيۡتُمۡ فَمَا سَأَلۡتُكُم مِّنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَى ٱللَّهِۖ وَأُمِرۡتُ أَنۡ أَكُونَ مِنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ ٧٢“Ndipo ngati muyamba kusakhulupirira ine sindidakupempheni mphotho. Mphotho yanga ili ndi Mulungu ndiponso ndalamulidwa kuti ndikhale mmodzi mwa ogonjera malamulo a Mulungu.” فَكَذَّبُوهُ فَنَجَّيۡنَٰهُ وَمَن مَّعَهُۥ فِي ٱلۡفُلۡكِ وَجَعَلۡنَٰهُمۡ خَلَٰٓئِفَ وَأَغۡرَقۡنَا ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَاۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُنذَرِينَ ٧٣Koma iwo adamukana. Ife tidamupulumutsa Nowa pamodzi ndi iwo amene adali naye m’chombo ndipo tinawapanga iwo kukhala olowa m’malo padziko ndipo tidamiza onse amene adakana zonena zathu. Ona, adali bwanji mapeto a anthu ochenjezedwa ثُمَّ بَعَثۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِۦ رُسُلًا إِلَىٰ قَوۡمِهِمۡ فَجَآءُوهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَمَا كَانُواْ لِيُؤۡمِنُواْ بِمَا كَذَّبُواْ بِهِۦ مِن قَبۡلُۚ كَذَٰلِكَ نَطۡبَعُ عَلَىٰ قُلُوبِ ٱلۡمُعۡتَدِينَ ٧٤Zitatha izi, tidatumiza Atumwi ena kwa anthu awo. Iwo adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka koma iwo sanali okhulupirira mzimene adazikana kale. Mmenemo ndi mmene timadindira zidindo mitima ya anthu ochita zinthu mopyora muyeso ثُمَّ بَعَثۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِم مُّوسَىٰ وَهَٰرُونَ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ بِـَٔايَٰتِنَا فَٱسۡتَكۡبَرُواْ وَكَانُواْ قَوۡمًا مُّجۡرِمِينَ ٧٥Pambuyo pake tinatumiza Mose ndi Aroni ndi zizindikiro zathu kwa Farawo ndi nduna zake. Koma iwo adadzikweza ndipo anali anthu oipa فَلَمَّا جَآءَهُمُ ٱلۡحَقُّ مِنۡ عِندِنَا قَالُوٓاْ إِنَّ هَٰذَا لَسِحۡرٌ مُّبِينٌ ٧٦Pamene chidadza choonadi kwa iwo kuchokera kwa Ife, iwo adati: “Ndithudi awa ndi matsenga woonekereratu.” قَالَ مُوسَىٰٓ أَتَقُولُونَ لِلۡحَقِّ لَمَّا جَآءَكُمۡۖ أَسِحۡرٌ هَٰذَا وَلَا يُفۡلِحُ ٱلسَّٰحِرُونَ ٧٧Mose adati: “Kodi inu mukunena choona pamene chakufikani kuti ndi matsenga? Wamatsenga sapambana ai.” قَالُوٓاْ أَجِئۡتَنَا لِتَلۡفِتَنَا عَمَّا وَجَدۡنَا عَلَيۡهِ ءَابَآءَنَا وَتَكُونَ لَكُمَا ٱلۡكِبۡرِيَآءُ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا نَحۡنُ لَكُمَا بِمُؤۡمِنِينَ ٧٨Iwo adati: “Kodi iwe wadza kuti utitembenuze m’zimene tidapeza makolo athu akuchita ndi cholinga chakuti inu anthu awiri, mukhale akuluakulu m’dziko? Ife sitikukhulupirirani anthu awirinu.” وَقَالَ فِرۡعَوۡنُ ٱئۡتُونِي بِكُلِّ سَٰحِرٍ عَلِيمٍ ٧٩Ndipo Farawo adati: “Bweretsani wa amatsenga aliyense wodziwa kwa ine.” فَلَمَّا جَآءَ ٱلسَّحَرَةُ قَالَ لَهُم مُّوسَىٰٓ أَلۡقُواْ مَآ أَنتُم مُّلۡقُونَ ٨٠Pamene amatsenga adadza, Mose adati kwa izo: “Ponyani zonse zimene mufuna kuponya.” فَلَمَّآ أَلۡقَوۡاْ قَالَ مُوسَىٰ مَا جِئۡتُم بِهِ ٱلسِّحۡرُۖ إِنَّ ٱللَّهَ سَيُبۡطِلُهُۥٓ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُصۡلِحُ عَمَلَ ٱلۡمُفۡسِدِينَ ٨١Ndipo pamene adaponya pansi ndodo zawo Mose adati: “Amenewa ndi matsenga ndipo Mulungu, ndithudi, adzagonjetsa matsenga anu. Ndithudi Mulungu savomera ntchito za anthu ochita zoipa kuti zipambane.” وَيُحِقُّ ٱللَّهُ ٱلۡحَقَّ بِكَلِمَٰتِهِۦ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡمُجۡرِمُونَ ٨٢Mulungu, ndi Mau ake, amakhazikitsa choonadi ngakhale kuti anthu oipa sakondwera فَمَآ ءَامَنَ لِمُوسَىٰٓ إِلَّا ذُرِّيَّةٌ مِّن قَوۡمِهِۦ عَلَىٰ خَوۡفٍ مِّن فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِمۡ أَن يَفۡتِنَهُمۡۚ وَإِنَّ فِرۡعَوۡنَ لَعَالٍ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَإِنَّهُۥ لَمِنَ ٱلۡمُسۡرِفِينَ ٨٣Palibe amene adamukhulupirira Mose kupatula ana a anthu ake chifukwa chomuopa Farawo ndi nduna zake kuti angawavutitse. Ndithudi Farawo adali wokakala moyo m’dzikomo ndiponso adali m’modzi wa anthu oononga وَقَالَ مُوسَىٰ يَٰقَوۡمِ إِن كُنتُمۡ ءَامَنتُم بِٱللَّهِ فَعَلَيۡهِ تَوَكَّلُوٓاْ إِن كُنتُم مُّسۡلِمِينَ ٨٤Mose adati: “oh inu anthu anga! Ngati inu mwakhulupirira mwa Mulungu, mudalire mwa Iye yekha, ngatiinumulianthuokhulupirira.” فَقَالُواْ عَلَى ٱللَّهِ تَوَكَّلۡنَا رَبَّنَا لَا تَجۡعَلۡنَا فِتۡنَةً لِّلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ ٨٥Iwoadati:“Timadalira mwa Mulungu. oh Ambuye wathu! Musalole kuti ife tizunzike m’manja mwa anthu oipa.” وَنَجِّنَا بِرَحۡمَتِكَ مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلۡكَٰفِرِينَ ٨٦“Tipulumutseni mwa chisomo chanu kwa anthu osakhulupirira.” وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰ وَأَخِيهِ أَن تَبَوَّءَا لِقَوۡمِكُمَا بِمِصۡرَ بُيُوتًا وَٱجۡعَلُواْ بُيُوتَكُمۡ قِبۡلَةً وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَۗ وَبَشِّرِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٨٧Tidavumbulutsa Mau athu kwa Mose ndi m’bale wake ponena kuti: “Amangireni nyumba anthu anu m’dziko la Aiguputo ndipo mupange nyumba zanu kukhala malo opemphereramo. Pitirizani mapemphero ndipo muwauze nkhani yabwino anthu okhulupirira.” وَقَالَ مُوسَىٰ رَبَّنَآ إِنَّكَ ءَاتَيۡتَ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَأَهُۥ زِينَةً وَأَمۡوَٰلًا فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا رَبَّنَا لِيُضِلُّواْ عَن سَبِيلِكَۖ رَبَّنَا ٱطۡمِسۡ عَلَىٰٓ أَمۡوَٰلِهِمۡ وَٱشۡدُدۡ عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ فَلَا يُؤۡمِنُواْ حَتَّىٰ يَرَوُاْ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَلِيمَ ٨٨Ndipo Mose adati: “Ambuye wathu! Inu mwamupatsa Farao ndi anthu ake zinthu zabwino ndi chuma m’moyo uno, Ambuye wathu, kuti asocheretse anthu ku njira yanu. Ambuye wathu! onongani chuma chawo ndipo limbitsani mitima yawo, kuti iwo asadzakhulupirire mpaka pamene aona chilango chowawa.” قَالَ قَدۡ أُجِيبَت دَّعۡوَتُكُمَا فَٱسۡتَقِيمَا وَلَا تَتَّبِعَآنِّ سَبِيلَ ٱلَّذِينَ لَا يَعۡلَمُونَ ٨٩Mulungu adati: “Pempho lanu layankhidwa. Kotero pitirizani kuyenda m’njira yoyenera nonse awiri ndipo musatsatire njira ya anthu osadziwa.” ۞ وَجَٰوَزۡنَا بِبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱلۡبَحۡرَ فَأَتۡبَعَهُمۡ فِرۡعَوۡنُ وَجُنُودُهُۥ بَغۡيًا وَعَدۡوًاۖ حَتَّىٰٓ إِذَآ أَدۡرَكَهُ ٱلۡغَرَقُ قَالَ ءَامَنتُ أَنَّهُۥ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا ٱلَّذِيٓ ءَامَنَتۡ بِهِۦ بَنُوٓاْ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَأَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ ٩٠Ife tidatsogolera ana a Israyeli kuoloka nyanja. Farawo, pamodzi ndi magulu ake a nkhondo, adawatsatira ndi chiwembu ndiponso udani. Kufikira pamene anali kumira, Farawo adati: “Ndikhulupirira kuti kulibe mulungu koma Iye amene ana a Israyeli amamukhulupirira. Ndipo ine ndili m’modzi wa odzipereka pogonjera.” ءَآلۡـَٰٔنَ وَقَدۡ عَصَيۡتَ قَبۡلُ وَكُنتَ مِنَ ٱلۡمُفۡسِدِينَ ٩١“Chiyani? Tsopano ndiye ukukhulupirira pamene iwe udanyoza kale ndipo udali mmodzi wa anthu oononga?” فَٱلۡيَوۡمَ نُنَجِّيكَ بِبَدَنِكَ لِتَكُونَ لِمَنۡ خَلۡفَكَ ءَايَةًۚ وَإِنَّ كَثِيرًا مِّنَ ٱلنَّاسِ عَنۡ ءَايَٰتِنَا لَغَٰفِلُونَ ٩٢“Lero, Ife tidzasunga thupi lako, kuti ukhale chizindikiro kwa onse amene adza m’mbuyo mwako. Ndithudi anthu ambiri ndi oiwala zizindikiro zathu.” وَلَقَدۡ بَوَّأۡنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ مُبَوَّأَ صِدۡقٍ وَرَزَقۡنَٰهُم مِّنَ ٱلطَّيِّبَٰتِ فَمَا ٱخۡتَلَفُواْ حَتَّىٰ جَآءَهُمُ ٱلۡعِلۡمُۚ إِنَّ رَبَّكَ يَقۡضِي بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فِيمَا كَانُواْ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ ٩٣Ndithudi Ife tidawakhazika ana a Israyeli malo abwino ndipo tidawapatsa zinthu zabwino. Ndipo iwo sadatsutsane mpaka pamene nzeru zinadza kwa iwo. Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo pa zinthu zimene amasiyana pa tsiku la kuuka kwa akufa فَإِن كُنتَ فِي شَكٍّ مِّمَّآ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكَ فَسۡـَٔلِ ٱلَّذِينَ يَقۡرَءُونَ ٱلۡكِتَٰبَ مِن قَبۡلِكَۚ لَقَدۡ جَآءَكَ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُمۡتَرِينَ ٩٤Ngati ukaika pa zimene tavumbulutsa kwa iwe, afunse iwo amene adawerenga Buku la kale iwe usanadze. Ndithudi, choonadi chadza kwa iwe kuchokera kwa Ambuyewakokoterousakhalemmodziwaokaika وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ فَتَكُونَ مِنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ ٩٥Ndipo usakhale mmodzi wa anthu amene adakana chivumbulutso cha Mulungu chifukwa ngati utero udzakhala mmodzi olephera إِنَّ ٱلَّذِينَ حَقَّتۡ عَلَيۡهِمۡ كَلِمَتُ رَبِّكَ لَا يُؤۡمِنُونَ ٩٦Ndithudi iwo amene Mau a Ambuye wawo akwaniritsidwa, sadzakhulupirira وَلَوۡ جَآءَتۡهُمۡ كُلُّ ءَايَةٍ حَتَّىٰ يَرَوُاْ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَلِيمَ ٩٧Ngakhale atalandira chizindikiro china chilichonse mpaka pamene adzaone chilango chowawa فَلَوۡلَا كَانَتۡ قَرۡيَةٌ ءَامَنَتۡ فَنَفَعَهَآ إِيمَٰنُهَآ إِلَّا قَوۡمَ يُونُسَ لَمَّآ ءَامَنُواْ كَشَفۡنَا عَنۡهُمۡ عَذَابَ ٱلۡخِزۡيِ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا وَمَتَّعۡنَٰهُمۡ إِلَىٰ حِينٍ ٩٨Kodi padalinso mzinda wina umene unakhulupirira ndipo kuti chikhulupiriro chake chinaupulumutsa kupatula anthu a Yona, pamene iwo adakhulupirira? Ife tidawachotsera chilango chochititsa manyazi m’moyo uno ndi kuwalola kusangalala pa kanthawi kochepa وَلَوۡ شَآءَ رَبُّكَ لَأٓمَنَ مَن فِي ٱلۡأَرۡضِ كُلُّهُمۡ جَمِيعًاۚ أَفَأَنتَ تُكۡرِهُ ٱلنَّاسَ حَتَّىٰ يَكُونُواْ مُؤۡمِنِينَ ٩٩Ngati Ambuye wako akadafuna, anthu onse a pa dziko lapansi akanakhulupirira mwa Iye yekha. Kodi iwe ungakakamize anthu kuti akhale okhulupirira وَمَا كَانَ لِنَفۡسٍ أَن تُؤۡمِنَ إِلَّا بِإِذۡنِ ٱللَّهِۚ وَيَجۡعَلُ ٱلرِّجۡسَ عَلَى ٱلَّذِينَ لَا يَعۡقِلُونَ ١٠٠Palibe munthu angakhulupirire pokhapokha m’chifuniro cha Mulungu. Iye adzagwetsa mkwiyo wake pa anthu opanda nzeru قُلِ ٱنظُرُواْ مَاذَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَمَا تُغۡنِي ٱلۡأٓيَٰتُ وَٱلنُّذُرُ عَن قَوۡمٍ لَّا يُؤۡمِنُونَ ١٠١Nena, “Taonani zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi!” Koma zizindikiro ndiponso anthu opereka chenjezo, siaphindu kwa anthu osakhulupirira فَهَلۡ يَنتَظِرُونَ إِلَّا مِثۡلَ أَيَّامِ ٱلَّذِينَ خَلَوۡاْ مِن قَبۡلِهِمۡۚ قُلۡ فَٱنتَظِرُوٓاْ إِنِّي مَعَكُم مِّنَ ٱلۡمُنتَظِرِينَ ١٠٢Kodi pali chimene akudikira kupatula zimene zinaoneka m’masiku a anthu omwe analipo iwo asanadze? Nena, “Dikirani, ine ndili nanu ngati mmodzi mwa odikira.” ثُمَّ نُنَجِّي رُسُلَنَا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْۚ كَذَٰلِكَ حَقًّا عَلَيۡنَا نُنجِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ١٠٣Pambuyo pake tinawapulumutsa Atumwi athu pamodzi ndi amene amakhulupirira. Kotero ndi koyenera kwa Ife kupulumutsa anthu okhulupirira قُلۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ إِن كُنتُمۡ فِي شَكٍّ مِّن دِينِي فَلَآ أَعۡبُدُ ٱلَّذِينَ تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَلَٰكِنۡ أَعۡبُدُ ٱللَّهَ ٱلَّذِي يَتَوَفَّىٰكُمۡۖ وَأُمِرۡتُ أَنۡ أَكُونَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ١٠٤Nena, “oh inu anthu! Ngati inu muli ndi chikaiko pa chipembedzo changa, dziwani kuti ine sindidzapembedza zomwe mukuzipembedza kuonjezera pa Mulungu weniweni. Koma ine ndikupembedza Mulungu amene amakuphani nonse ndipo ndalamulidwa kuti ndikhale mmodzi wa anthu okhulupirira.” وَأَنۡ أَقِمۡ وَجۡهَكَ لِلدِّينِ حَنِيفًا وَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ ١٠٥Ine ndidalamulidwa kuti, “Tsatira chipempedzo chopembedza Mulungu mmodzi ndipo usakhale mmodzi mwa anthu opembedza mafano.” وَلَا تَدۡعُ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَنفَعُكَ وَلَا يَضُرُّكَۖ فَإِن فَعَلۡتَ فَإِنَّكَ إِذًا مِّنَ ٱلظَّٰلِمِينَ ١٠٦Ndipo usapembedze wina aliyense yemwe si Mulungu, amene sangathe kukuthandiza kapena kukuononga chifukwa, utatero, udzakhala mmodzi wa wochita zoipa وَإِن يَمۡسَسۡكَ ٱللَّهُ بِضُرٍّ فَلَا كَاشِفَ لَهُۥٓ إِلَّا هُوَۖ وَإِن يُرِدۡكَ بِخَيۡرٍ فَلَا رَآدَّ لِفَضۡلِهِۦۚ يُصِيبُ بِهِۦ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦۚ وَهُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ ١٠٧Ngati Mulungu akupatsa mavuto palibe wina amene angawachotse kupatula Iye yekha ndipo ngati Iye akufunira zabwino, palibe wina amene angabweze zokoma zake zimene Iye amapereka kwa kapolo wake amene Iye wamufuna. Ndipo Iye ndi wokhululukira ndiponso Mwini chisoni chosatha قُلۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ قَدۡ جَآءَكُمُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكُمۡۖ فَمَنِ ٱهۡتَدَىٰ فَإِنَّمَا يَهۡتَدِي لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن ضَلَّ فَإِنَّمَا يَضِلُّ عَلَيۡهَاۖ وَمَآ أَنَا۠ عَلَيۡكُم بِوَكِيلٍ ١٠٨Nena, “Oh inu anthu! Choonadi chadza kwa inu kuchokerakwaAmbuyewanu.Aliyenseameneatsogozedwa atero podzithandiza iye mwini ndipo aliyense amene asochera adzisocheretsa yekha. Ine sindili wokusamalirani inu.” وَٱتَّبِعۡ مَا يُوحَىٰٓ إِلَيۡكَ وَٱصۡبِرۡ حَتَّىٰ يَحۡكُمَ ٱللَّهُۚ وَهُوَ خَيۡرُ ٱلۡحَٰكِمِينَ ١٠٩Tsatira zimene zikuvumbulutsidwa kwa iwe ndipo pirira mpaka pamene Mulungu aweruza. Iye ndi Muweruzi wodziwa kuposa aweruzi ena onse

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.