ملة الإسلام

السورة 96 · 19 آية · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

سورة العلق باللغة الشيشيوا

السورة بالعربية مع التفسير استمع إلى سورة العلق (1,283 قارئاً)
مكيةسورة العلق١٩ آية

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

ٱقۡرَأۡ بِٱسۡمِ رَبِّكَ ٱلَّذِي خَلَقَ ١Werenga! M’dzina la Ambuye wako amene analenga خَلَقَ ٱلۡإِنسَٰنَ مِنۡ عَلَقٍ ٢Yemwe adalenga munthu kuchokera ku kadontho kamagazi oundana ٱقۡرَأۡ وَرَبُّكَ ٱلۡأَكۡرَمُ ٣werenga! Ndipo Ambuye wako ndiye wopereka mowoolowa manja ٱلَّذِي عَلَّمَ بِٱلۡقَلَمِ ٤Amene anaphunzitsa ndi cholembera عَلَّمَ ٱلۡإِنسَٰنَ مَا لَمۡ يَعۡلَمۡ ٥Anaphunzitsa munthu chimene sanali kuchidziwa كـَلَّآ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لَيَطۡغَىٰٓ ٦Iyayi! Ndithudi, munthu amalakwa mopyola muyeso أَن رَّءَاهُ ٱسۡتَغۡنَىٰٓ ٧Chifukwa amaganiza kuti iye ndi oima payekha إِنَّ إِلَىٰ رَبِّكَ ٱلرُّجۡعَىٰٓ ٨Ndithudi! Nonse mudzabwerera kwa Ambuye wanu أَرَءَيۡتَ ٱلَّذِي يَنۡهَىٰ ٩Kodi mwamuona munthu amene amaletsa عَبۡدًا إِذَا صَلَّىٰٓ ١٠Kapolo pamene akupemphera أَرَءَيۡتَ إِن كَانَ عَلَى ٱلۡهُدَىٰٓ ١١Kodi mwamuona ngati iye alikutsatira chilangizo chabwino أَوۡ أَمَرَ بِٱلتَّقۡوَىٰٓ ١٢Kapena kulamulira machitidwe abwino أَرَءَيۡتَ إِن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰٓ ١٣Ndiuze ngati iye akana choonadi ndipo salabadira أَلَمۡ يَعۡلَم بِأَنَّ ٱللَّهَ يَرَىٰ ١٤Kodi iye sadziwa kuti Mulungu amaona zinthu zonse كـَلَّا لَئِن لَّمۡ يَنتَهِ لَنَسۡفَعَۢا بِٱلنَّاصِيَةِ ١٥Iyayi! Ngati iye sasiya, Ife tidzamududuluza pogwira tsitsi la pa mphumi pake نَاصِيَةٍ كَٰذِبَةٍ خَاطِئَةٍ ١٦Mphumi yabodza ndi yochimwa فَلۡيَدۡعُ نَادِيَهُۥ ١٧Ndipo mulekeni iye aitane anzake oti amuthandize سَنَدۡعُ ٱلزَّبَانِيَةَ ١٨Ife tidzaitana osunga Gahena كـَلَّا لَا تُطِعۡهُ وَٱسۡجُدۡۤ وَٱقۡتَرِب ۩ ١٩Iyayi! Usamumvere iye. Gunditsa mphumi yako pansi ndipo idza pafupi ndi Mulungu

الترجمة: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.