ملة الإسلام

السورة 15 · 99 آية · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

سورة الحجر باللغة الشيشيوا

السورة بالعربية مع التفسير استمع إلى سورة الحجر (1,272 قارئاً)
مكيةسورة الحجر٩٩ آية

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

الٓرۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ وَقُرۡءَانٍ مُّبِينٍ ١Alif Lam Ra. Awa ndi mavesi a Buku, ndipo ndi Korani yofotokoza bwino رُّبَمَا يَوَدُّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَوۡ كَانُواْ مُسۡلِمِينَ ٢Mwina iwo amene sakhulupirira adzafuna kuti akadakhala Asilamu ذَرۡهُمۡ يَأۡكُلُواْ وَيَتَمَتَّعُواْ وَيُلۡهِهِمُ ٱلۡأَمَلُۖ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ ٣Alekeni kuti adye, ndi kuti asangalale ndipo alekeni kuti atangwanike ndi chikhulupiriro chabodza. Iwo adzadziwa posachedwapa وَمَآ أَهۡلَكۡنَا مِن قَرۡيَةٍ إِلَّا وَلَهَا كِتَابٌ مَّعۡلُومٌ ٤Ndipo Ife sitinaonongepo mzinda wina uliwonse, kupatula pamene nthawi yake itakwana مَّا تَسۡبِقُ مِنۡ أُمَّةٍ أَجَلَهَا وَمَا يَسۡتَـٔۡخِرُونَ ٥Anthu sangathe kufulumizitsa chionongeko chawo kapena kuchichedwetsa ayi وَقَالُواْ يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِي نُزِّلَ عَلَيۡهِ ٱلذِّكۡرُ إِنَّكَ لَمَجۡنُونٌ ٦Iwo amati, “Iwe, amene Korani yavumbulutsidwa kwa iwe! Ndithudi ndiwe munthu wa misala.” لَّوۡمَا تَأۡتِينَا بِٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ ٧“Bwanji siutibweretsera angelo ngati iweyo uli mmodzi mwa onena zoona?” مَا نُنَزِّلُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَمَا كَانُوٓاْ إِذًا مُّنظَرِينَ ٨Ife sitimatsitsa pansi angelo, kupatula ndi choonadi ndipo zitatero iwo sadzapatsidwa nthawi إِنَّا نَحۡنُ نَزَّلۡنَا ٱلذِّكۡرَ وَإِنَّا لَهُۥ لَحَٰفِظُونَ ٩Ndithudi ndife amene tidatsitsa Korani ndipo, ndithudi, Ife ndife amene tidzaiteteza وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ فِي شِيَعِ ٱلۡأَوَّلِينَ ١٠Ndithudi Ife tidatumizapo, iwe usanadze, Atumwi ena pakati pa mibadwo yakale وَمَا يَأۡتِيهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ ١١Ndipo sikunadze kwa iwo Mtumwi, amene iwo sanamuchite chipongwe كَذَٰلِكَ نَسۡلُكُهُۥ فِي قُلُوبِ ٱلۡمُجۡرِمِينَ ١٢Kotero timalowetsa chisokonezo m’mitima ya anthu ochita zoipa لَا يُؤۡمِنُونَ بِهِۦ وَقَدۡ خَلَتۡ سُنَّةُ ٱلۡأَوَّلِينَ ١٣Iwo sangakhulupirire mu uthenga wa Korani ndipo ndi chizolowezi cha anthu amene adalipo kale وَلَوۡ فَتَحۡنَا عَلَيۡهِم بَابًا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ فَظَلُّواْ فِيهِ يَعۡرُجُونَ ١٤Ndipo ngati Ife tikadatsekula khomo lakumwamba, iwo ndi kumakwera kumwamba mosalekeza لَقَالُوٓاْ إِنَّمَا سُكِّرَتۡ أَبۡصَٰرُنَا بَلۡ نَحۡنُ قَوۡمٌ مَّسۡحُورُونَ ١٥Iwo akadakanabe kuti, “Maso athu athobwa. Ndithudi ife talodzedwa.” وَلَقَدۡ جَعَلۡنَا فِي ٱلسَّمَآءِ بُرُوجًا وَزَيَّنَّٰهَا لِلنَّٰظِرِينَ ١٦Ndithudi Ife taika nyenyezi zikuluzikulu kumwamba ndipo tazikongoletsa kuti zizikondweretsa anthu oyang’ana وَحَفِظۡنَٰهَا مِن كُلِّ شَيۡطَٰنٍ رَّجِيمٍ ١٧Ndipo tawateteza malo a kumwamba kwa Satana wotembereredwa إِلَّا مَنِ ٱسۡتَرَقَ ٱلسَّمۡعَ فَأَتۡبَعَهُۥ شِهَابٌ مُّبِينٌ ١٨Kupatula iye amene amamvetsera mwakuba, iye amatsatiridwa ndi malawi a moto وَٱلۡأَرۡضَ مَدَدۡنَٰهَا وَأَلۡقَيۡنَا فِيهَا رَوَٰسِيَ وَأَنۢبَتۡنَا فِيهَا مِن كُلِّ شَيۡءٍ مَّوۡزُونٍ ١٩Ife tidatambasula dziko lapansi ndi kuikamo mapiri ndipo tameletsa mu ilo zinthu zosiyanasiyana chilichonse chili ndi muyeso wake وَجَعَلۡنَا لَكُمۡ فِيهَا مَعَٰيِشَ وَمَن لَّسۡتُمۡ لَهُۥ بِرَٰزِقِينَ ٢٠Ndipo takupatsani mu ilo njira zopezela chakudya chanu ndi cha izo zimene inu simungathe kuzidyetsa وَإِن مِّن شَيۡءٍ إِلَّا عِندَنَا خَزَآئِنُهُۥ وَمَا نُنَزِّلُهُۥٓ إِلَّا بِقَدَرٍ مَّعۡلُومٍ ٢١Palibe chilichonse, chimene nkhokwe yake siili ndi Ife ndipo sititumiza kupatula m’muyeso wodziwika وَأَرۡسَلۡنَا ٱلرِّيَٰحَ لَوَٰقِحَ فَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءً فَأَسۡقَيۡنَٰكُمُوهُ وَمَآ أَنتُمۡ لَهُۥ بِخَٰزِنِينَ ٢٢Ndipo Ife timatumiza mphepo yobereketsa ndipo timatsitsa madzi kuchokera kumwamba ndipo timakupatsani kuti mumwe; ndipo inu si ndinu osunga nkhokwe zake وَإِنَّا لَنَحۡنُ نُحۡيِۦ وَنُمِيتُ وَنَحۡنُ ٱلۡوَٰرِثُونَ ٢٣Ndipo, ndithudi, Ife ndife amene timapereka moyo ndi imfa ndipo zinthu zonse ndi zathu وَلَقَدۡ عَلِمۡنَا ٱلۡمُسۡتَقۡدِمِينَ مِنكُمۡ وَلَقَدۡ عَلِمۡنَا ٱلۡمُسۡتَـٔۡخِرِينَ ٢٤Ndipo, ndithudi, Ife timadziwa onse amene adalipo kale inu musanadze ndipo timadziwa mibadwo yanu yatsopano ndi iwo amene adzadza m’tsogolo وَإِنَّ رَبَّكَ هُوَ يَحۡشُرُهُمۡۚ إِنَّهُۥ حَكِيمٌ عَلِيمٌ ٢٥Ndipo, ndithudi, Ambuye wako adzasonkhanitsa onse pamodzi. Zoonadi Iye ndi Wanzeru ndi Wodziwa chilichonse وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِن صَلۡصَٰلٍ مِّنۡ حَمَإٍ مَّسۡنُونٍ ٢٦Ndipo, ndithudi, Ife tidamulenga munthu kuchokera ku dothi lotulutsa mawu, losinthidwa m’matope akuda osalala وَٱلۡجَآنَّ خَلَقۡنَٰهُ مِن قَبۡلُ مِن نَّارِ ٱلسَّمُومِ ٢٧Tidapanga mtundu wa majini poyamba kuchokera ku mphepo ya moto وَإِذۡ قَالَ رَبُّكَ لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِنِّي خَٰلِقُۢ بَشَرًا مِّن صَلۡصَٰلٍ مِّنۡ حَمَإٍ مَّسۡنُونٍ ٢٨Ndipo pamene Ambuye wako adati kwa angelo, “Ine ndilenga munthu kuchokera ku dothi lotulutsa mawu losinthidwa matope akuda osalala.” فَإِذَا سَوَّيۡتُهُۥ وَنَفَخۡتُ فِيهِ مِن رُّوحِي فَقَعُواْ لَهُۥ سَٰجِدِينَ ٢٩“Motero ndikatha kumukonza ndi kuuzira mpweya umene ndidalenga chifukwa cha iye ndipo nonse gwadani kumulambira iye.” فَسَجَدَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ كُلُّهُمۡ أَجۡمَعُونَ ٣٠Motero Angelo onse adagwada ndi kumulambira إِلَّآ إِبۡلِيسَ أَبَىٰٓ أَن يَكُونَ مَعَ ٱلسَّٰجِدِينَ ٣١Kupatula Satanaadakanakukhalammodzimwaolambira قَالَ يَٰٓإِبۡلِيسُ مَا لَكَ أَلَّا تَكُونَ مَعَ ٱلسَّٰجِدِينَ ٣٢Mulungu adati, “oh iwe Satana! Kodi ndi chifukwa chiyani siuli pamodzi ndi olambira?” قَالَ لَمۡ أَكُن لِّأَسۡجُدَ لِبَشَرٍ خَلَقۡتَهُۥ مِن صَلۡصَٰلٍ مِّنۡ حَمَإٍ مَّسۡنُونٍ ٣٣Satana adati, “Ine sindingagwadire munthu amene Inu mwamulenga kuchokera ku dothi lotulutsa mawu losinthidwa matope akuda osalala.” قَالَ فَٱخۡرُجۡ مِنۡهَا فَإِنَّكَ رَجِيمٌ ٣٤Mulungu adati: “Motero choka kuno chifukwa ndithudi iwe ndiwe wotembereredwa.” وَإِنَّ عَلَيۡكَ ٱللَّعۡنَةَ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلدِّينِ ٣٥Ndipo, ndithudi, temberero lidzakhala pa iwe mpaka pa tsiku lachiweruzo.” قَالَ رَبِّ فَأَنظِرۡنِيٓ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ ٣٦Satana adati, “oh Ambuye wanga! Bandisungani mpaka patsiku louka kwa akufa.” قَالَ فَإِنَّكَ مِنَ ٱلۡمُنظَرِينَ ٣٧Mulungu adati, “Ndithudi iwe uli m’gulu la anthu amene apatsidwa nthawi.” إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡوَقۡتِ ٱلۡمَعۡلُومِ ٣٨“Mpaka pa nthawi ya tsiku lotsimikizika.” قَالَ رَبِّ بِمَآ أَغۡوَيۡتَنِي لَأُزَيِّنَنَّ لَهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَأُغۡوِيَنَّهُمۡ أَجۡمَعِينَ ٣٩Satana adati, “Oh Ambuye wanga! Popeza Inuyo mwandisocheretsa ine, ndithudi, ndidzawasalalitsira njira yautchimo anthu onse padziko lapansi, ndithudi onse ndidzawasocheretsa إِلَّا عِبَادَكَ مِنۡهُمُ ٱلۡمُخۡلَصِينَ ٤٠Kupatula akapolo anu osankhidwa amene ali pakati pawo.” قَالَ هَٰذَا صِرَٰطٌ عَلَيَّ مُسۡتَقِيمٌ ٤١Mulungu adati, “Imeneyi ndiyo njira imene idzalondola mwachindunji kwa Ine.” إِنَّ عِبَادِي لَيۡسَ لَكَ عَلَيۡهِمۡ سُلۡطَٰنٌ إِلَّا مَنِ ٱتَّبَعَكَ مِنَ ٱلۡغَاوِينَ ٤٢“Ndithudi iwe siudzakhala ndi mphamvu pa akapolo anga, kupatula anthu ochita zoipa amene amakutsatira iweyo.” وَإِنَّ جَهَنَّمَ لَمَوۡعِدُهُمۡ أَجۡمَعِينَ ٤٣“Ndipo, ndithudi, Gahena ndi malo olonjezedwa kwa iwo onse.” لَهَا سَبۡعَةُ أَبۡوَٰبٍ لِّكُلِّ بَابٍ مِّنۡهُمۡ جُزۡءٌ مَّقۡسُومٌ ٤٤“Iyo ili ndi makomo asanu ndi awiri, ndipo chipata chilichonse chidzakhala ndi anthu ake olowapo.” إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي جَنَّٰتٍ وَعُيُونٍ ٤٥“Ndithudi! Onse oopa Mulungu adzakhala m’kati mwa minda ndi m’kati mwa a kasupe.” ٱدۡخُلُوهَا بِسَلَٰمٍ ءَامِنِينَ ٤٦“Lowanimo mwamtendere mopanda mavuto.” وَنَزَعۡنَا مَا فِي صُدُورِهِم مِّنۡ غِلٍّ إِخۡوَٰنًا عَلَىٰ سُرُرٍ مُّتَقَٰبِلِينَ ٤٧“Ndipo Ife tidzachotsa m’mitima yawo mkwiyo uliwonse kuti akhoza kukhala pachibale ndi kupumula m’mipando yawofowofo moyang’anizana.” لَا يَمَسُّهُمۡ فِيهَا نَصَبٌ وَمَا هُم مِّنۡهَا بِمُخۡرَجِينَ ٤٨“Ndipo iwo sadzatopa kumeneko ndipo sadzafunsidwa kuti achoke ku Paradiso.” ۞ نَبِّئۡ عِبَادِيٓ أَنِّيٓ أَنَا ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ ٤٩Auze akapolo anga kuti ndithudi Ine ndimakhululukira ndipo ndine wachisoni ۞ وَأَنَّ عَذَابِي هُوَ ٱلۡعَذَابُ ٱلۡأَلِيمُ ٥٠Ndiponso kuti chilango changa, ndithudi, ndi chilango chowawa koposa وَنَبِّئۡهُمۡ عَن ضَيۡفِ إِبۡرَٰهِيمَ ٥١Auze za alendo a Abrahamu إِذۡ دَخَلُواْ عَلَيۡهِ فَقَالُواْ سَلَٰمًا قَالَ إِنَّا مِنكُمۡ وَجِلُونَ ٥٢Pamene iwo adadza kwa iye ndi kumuuza kuti, “Mtendere ukhale kwa iwe.’ Koma iye adawayankha kuti, “Ndili ndi mantha ndi inu.” قَالُواْ لَا تَوۡجَلۡ إِنَّا نُبَشِّرُكَ بِغُلَٰمٍ عَلِيمٍ ٥٣Iwo adati, “Usaope! Ife tadza kwa iwe ndi nkhani yabwino ya mwana wamwamuna amene adzakhala wodziwa zambiri.” قَالَ أَبَشَّرۡتُمُونِي عَلَىٰٓ أَن مَّسَّنِيَ ٱلۡكِبَرُ فَبِمَ تُبَشِّرُونَ ٥٤Iye adati, “Kodi inu muli kudzandiuza nkhani yabwino pamene ine nditakalamba kale? “Kodi nkhani yanu ndi yotani?” قَالُواْ بَشَّرۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ فَلَا تَكُن مِّنَ ٱلۡقَٰنِطِينَ ٥٥Iwo adati, “Ife tili kukuuza nkhani yabwinoyi mwachoonadi. Kotero usakhale wotaya mtima.” قَالَ وَمَن يَقۡنَطُ مِن رَّحۡمَةِ رَبِّهِۦٓ إِلَّا ٱلضَّآلُّونَ ٥٦Iye adati, “Ndani amene angataye mtima ndi chifundo cha Mulungu, kupatula osochera?” قَالَ فَمَا خَطۡبُكُمۡ أَيُّهَا ٱلۡمُرۡسَلُونَ ٥٧Iye adatinso, “Kodi cholinga chanu ndi chiyani, inu otumidwa?” قَالُوٓاْ إِنَّآ أُرۡسِلۡنَآ إِلَىٰ قَوۡمٍ مُّجۡرِمِينَ ٥٨Iwo adati, “Ife tatumidwa kwa anthu oipa.” إِلَّآ ءَالَ لُوطٍ إِنَّا لَمُنَجُّوهُمۡ أَجۡمَعِينَ ٥٩“onse kupatula anthu otsatira Loti okha. Ife, ndithudi, tidzawapulumutsa iwo okha.” إِلَّا ٱمۡرَأَتَهُۥ قَدَّرۡنَآ إِنَّهَا لَمِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ ٦٠“Kupatula mkazi wake amene ife talamulidwa kuti akhalire m’mbuyo pamodzi ndi iwo amene anali kukhalira m’mbuyo.” فَلَمَّا جَآءَ ءَالَ لُوطٍ ٱلۡمُرۡسَلُونَ ٦١Ndipo pamene a Kazembe athu adadza ku nyumba ya Loti قَالَ إِنَّكُمۡ قَوۡمٌ مُّنكَرُونَ ٦٢Loti adati, “Ndithudi inu ndinu anthu omwe sindikudziwani.” قَالُواْ بَلۡ جِئۡنَٰكَ بِمَا كَانُواْ فِيهِ يَمۡتَرُونَ ٦٣Iwo adati, “Iyayi. Ife takubweretsera iweyo zinthu zimene iwo anali kukayika.” وَأَتَيۡنَٰكَ بِٱلۡحَقِّ وَإِنَّا لَصَٰدِقُونَ ٦٤“Ndipo Ife tadza ndi choonadi kwa iwe ndipo, ndithudi, ife ndife onena zoona.” فَأَسۡرِ بِأَهۡلِكَ بِقِطۡعٍ مِّنَ ٱلَّيۡلِ وَٱتَّبِعۡ أَدۡبَٰرَهُمۡ وَلَا يَلۡتَفِتۡ مِنكُمۡ أَحَدٌ وَٱمۡضُواْ حَيۡثُ تُؤۡمَرُونَ ٦٥“Motero choka ndi abale ako pakati pa usiku, iwe uziyenda pambuyo pawo ndipo usalole wina aliyense kuti atembenuke. Kapita kumene walamulidwa kupita.” وَقَضَيۡنَآ إِلَيۡهِ ذَٰلِكَ ٱلۡأَمۡرَ أَنَّ دَابِرَ هَٰٓؤُلَآءِ مَقۡطُوعٌ مُّصۡبِحِينَ ٦٦Ndipo tidamuuza lamulo ili kuti mizu ya iwo idzazulidwa m’mawa وَجَآءَ أَهۡلُ ٱلۡمَدِينَةِ يَسۡتَبۡشِرُونَ ٦٧Ndipo anthu a mu Mzinda adadza ali osangala قَالَ إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ ضَيۡفِي فَلَا تَفۡضَحُونِ ٦٨Iye adati, “Ndithudi! Awa ndi alendo anga motero musandichititse manyazi ayi.” وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَلَا تُخۡزُونِ ٦٩“opani Mulungu ndipo musandipangitse manyazi.” قَالُوٓاْ أَوَلَمۡ نَنۡهَكَ عَنِ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٧٠Iwo adati, “Kodi ife sitidakuletse kuti uzichereza alendo?” قَالَ هَٰٓؤُلَآءِ بَنَاتِيٓ إِن كُنتُمۡ فَٰعِلِينَ ٧١Iye adati, “Awa ndi ana anga a aakazi; akwatireni ngati inu mufunadi kutero.” لَعَمۡرُكَ إِنَّهُمۡ لَفِي سَكۡرَتِهِمۡ يَعۡمَهُونَ ٧٢Ndithudi pali moyo wako! Iwo chifukwa chakuledzera anali kuyenda mwakhungu فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّيۡحَةُ مُشۡرِقِينَ ٧٣Ndipo chilango chidawapeza pamene dzuwa linkatuluka فَجَعَلۡنَا عَٰلِيَهَا سَافِلَهَا وَأَمۡطَرۡنَا عَلَيۡهِمۡ حِجَارَةً مِّن سِجِّيلٍ ٧٤Ndipo Ife tidaononga (mizinda yawo) zapansi kukhala pamwamba ndipo tidawagwetsera mvula ya miyala ya moto إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّلۡمُتَوَسِّمِينَ ٧٥Ndithudi! Mu izi muli zizindikiro kwa anthu omvetsa وَإِنَّهَا لَبِسَبِيلٍ مُّقِيمٍ ٧٦Ndipo, ndithudi, iyo ili m’mphepete mwa msewu umene umapitidwa إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةً لِّلۡمُؤۡمِنِينَ ٧٧Ndithudi! Muizimulizizindikirokwaanthuokhulupirira وَإِن كَانَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡأَيۡكَةِ لَظَٰلِمِينَ ٧٨Ngakhale anthu okhala m’nkhalango nawonso anali ochimwa فَٱنتَقَمۡنَا مِنۡهُمۡ وَإِنَّهُمَا لَبِإِمَامٍ مُّبِينٍ ٧٩Motero Ife tidawalanga. Ndipo iwo ali pamalo poonekera وَلَقَدۡ كَذَّبَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡحِجۡرِ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ٨٠Ndipo, ndithudi, anthu a ku Hijr adakana Atumwi وَءَاتَيۡنَٰهُمۡ ءَايَٰتِنَا فَكَانُواْ عَنۡهَا مُعۡرِضِينَ ٨١Ndipo Ife tidawapatsa zizindikiro zathu koma iwo adazikana وَكَانُواْ يَنۡحِتُونَ مِنَ ٱلۡجِبَالِ بُيُوتًا ءَامِنِينَ ٨٢Ndipo iwo anali kukumba mapiri kukhala nyumba zawo ndipo anali kukhala mosaopa فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّيۡحَةُ مُصۡبِحِينَ ٨٣Phokoso la chilango lidafika kwa iwo m’mawa فَمَآ أَغۡنَىٰ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ ٨٤Ndipo sizidawathandize zonse zimene anali kuchita وَمَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَآ إِلَّا بِٱلۡحَقِّۗ وَإِنَّ ٱلسَّاعَةَ لَأٓتِيَةٌۖ فَٱصۡفَحِ ٱلصَّفۡحَ ٱلۡجَمِيلَ ٨٥Ndipo Ife sitidalenge kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo kupatula ndi choonadi. Ndithudi popanda chikayiko tsiku lachiweruzo lidzadza; kotero akhululukireni, kukhululuka kwabwino إِنَّ رَبَّكَ هُوَ ٱلۡخَلَّٰقُ ٱلۡعَلِيمُ ٨٦Ndithudi Ambuye wako ndi Namalenga ndi wodziwa zinthu zonse وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَٰكَ سَبۡعًا مِّنَ ٱلۡمَثَانِي وَٱلۡقُرۡءَانَ ٱلۡعَظِيمَ ٨٧Ndipo, ndithudi, Ife tidakupatsa mavesi asanu ndi awiri amene amanenedwa kawirikawiri ndi Korani yolemekezeka لَا تَمُدَّنَّ عَيۡنَيۡكَ إِلَىٰ مَا مَتَّعۡنَا بِهِۦٓ أَزۡوَٰجًا مِّنۡهُمۡ وَلَا تَحۡزَنۡ عَلَيۡهِمۡ وَٱخۡفِضۡ جَنَاحَكَ لِلۡمُؤۡمِنِينَ ٨٨Usamayang’ane mwanjiru zinthu zokoma zimene tawapatsa ena a iwo kapena kumamva chisoni pa izo. Ndipo onetsani chifundo kwa anthu okhulupirira وَقُلۡ إِنِّيٓ أَنَا ٱلنَّذِيرُ ٱلۡمُبِينُ ٨٩Ndipo Nena, “Ine ndine Mchenjezi” كَمَآ أَنزَلۡنَا عَلَى ٱلۡمُقۡتَسِمِينَ ٩٠Monga tidatumiza kwa amene amagawanitsa ٱلَّذِينَ جَعَلُواْ ٱلۡقُرۡءَانَ عِضِينَ ٩١Amene apanga Buku la Korani kukhala magawo awiri فَوَرَبِّكَ لَنَسۡـَٔلَنَّهُمۡ أَجۡمَعِينَ ٩٢Kotero, pali Ambuye wako, tidzawafunsa عَمَّا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ٩٣Pa zonse zimene anali kuchita فَٱصۡدَعۡ بِمَا تُؤۡمَرُ وَأَعۡرِضۡ عَنِ ٱلۡمُشۡرِكِينَ ٩٤Motero lalikira poyera zonse zimene walamulidwa, ndipo choka pakati pa osakhulupirira إِنَّا كَفَيۡنَٰكَ ٱلۡمُسۡتَهۡزِءِينَ ٩٥Ndithudi Ife tidzakuteteza kwa onyoza ٱلَّذِينَ يَجۡعَلُونَ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَۚ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ ٩٦Iwo amene amatumikira mulungu wina kuonjezera pa Mulungu weniweni iwowo adzadziwa وَلَقَدۡ نَعۡلَمُ أَنَّكَ يَضِيقُ صَدۡرُكَ بِمَا يَقُولُونَ ٩٧Ndithudi Ife tilikudziwakutizimakupweteka mumtima mwako zinthu zimene amanena فَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ وَكُن مِّنَ ٱلسَّٰجِدِينَ ٩٨Motero lemekeza Ambuye wako ndipo khala mmodzi wa iwo amene amagwada pomulemekeza Iye وَٱعۡبُدۡ رَبَّكَ حَتَّىٰ يَأۡتِيَكَ ٱلۡيَقِينُ ٩٩Ndipo pembedza Ambuye wako mpaka pamene ola lotsimikizidwa likupeza

الترجمة: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.