ملة الإسلام

السورة 23 · 118 آية · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

سورة المؤمنون باللغة الشيشيوا

السورة بالعربية مع التفسير استمع إلى سورة المؤمنون (1,265 قارئاً)
مكيةسورة المؤمنون١١٨ آية

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

قَدۡ أَفۡلَحَ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ ١Anthu okhulupirira ndiwo opambana ٱلَّذِينَ هُمۡ فِي صَلَاتِهِمۡ خَٰشِعُونَ ٢Iwo amene amadzichepetsa akamapemphera وَٱلَّذِينَ هُمۡ عَنِ ٱللَّغۡوِ مُعۡرِضُونَ ٣Ndi iwo amene amalewa nkhani zabodza وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِلزَّكَوٰةِ فَٰعِلُونَ ٤Ndipo amapereka zaulere kwa anthu osauka وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِفُرُوجِهِمۡ حَٰفِظُونَ ٥Ndi iwo amene amadziteteza ku chiwerewere إِلَّا عَلَىٰٓ أَزۡوَٰجِهِمۡ أَوۡ مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُهُمۡ فَإِنَّهُمۡ غَيۡرُ مَلُومِينَ ٦Kupatula kwa akazi awo kapena akapolo awo akazi, chifukwa iwo sangadzudzulidwe فَمَنِ ٱبۡتَغَىٰ وَرَآءَ ذَٰلِكَ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡعَادُونَ ٧Koma amene angafune zina pamwamba pa zimene tawaloleza anthu otere ndi ochimwa وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِأَمَٰنَٰتِهِمۡ وَعَهۡدِهِمۡ رَٰعُونَ ٨Amene amakwaniritsa malonjezo ndi mapangano awo وَٱلَّذِينَ هُمۡ عَلَىٰ صَلَوَٰتِهِمۡ يُحَافِظُونَ ٩Ndi iwo amene amasunga mapemphero awo أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡوَٰرِثُونَ ١٠Amenewa ndithudi ndiwo amene adzalowa ٱلَّذِينَ يَرِثُونَ ٱلۡفِرۡدَوۡسَ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ ١١Iwo adzalowa ku Paradiso ya pamwamba ndipo adzakhalamo mpaka kalekale وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِن سُلَٰلَةٍ مِّن طِينٍ ١٢Ndithudi Ife tidapanga munthu kuchokera ku dothi labwino ثُمَّ جَعَلۡنَٰهُ نُطۡفَةً فِي قَرَارٍ مَّكِينٍ ١٣Titatero tidamukonza iye kukhala dontho la umuna m’malo otetezedwa mu msana ثُمَّ خَلَقۡنَا ٱلنُّطۡفَةَ عَلَقَةً فَخَلَقۡنَا ٱلۡعَلَقَةَ مُضۡغَةً فَخَلَقۡنَا ٱلۡمُضۡغَةَ عِظَٰمًا فَكَسَوۡنَا ٱلۡعِظَٰمَ لَحۡمًا ثُمَّ أَنشَأۡنَٰهُ خَلۡقًا ءَاخَرَۚ فَتَبَارَكَ ٱللَّهُ أَحۡسَنُ ٱلۡخَٰلِقِينَ ١٤dontho la umunali tidalipanga kukhala dontho la magazi ndipo dontho lamagazili tidalipanga kukhala m’bulu wa mnofu. Ndipo mnofu umenewu tidaukonza kukhala mafupa ndipo tidakuta mafupa ndi mnofu. Kotero tidamupanga iye kukhala chilengedwe china. odalitsa akhale Mulungu, Namalenga wabwino kwambiri mwa onse ثُمَّ إِنَّكُم بَعۡدَ ذَٰلِكَ لَمَيِّتُونَ ١٥Ndipo pambuyo pake inu nonse mudzafa ثُمَّ إِنَّكُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ تُبۡعَثُونَ ١٦Ndipo mudzapatsidwanso moyo patsiku la kuuka kwa akufa وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا فَوۡقَكُمۡ سَبۡعَ طَرَآئِقَ وَمَا كُنَّا عَنِ ٱلۡخَلۡقِ غَٰفِلِينَ ١٧Ife tidalenga miyamba isanu ndi iwiri pamwamba panu ndipo kwa zolengedwa zathu. Ndipo Ife sitikhala osalabadira ayi وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءَۢ بِقَدَرٍ فَأَسۡكَنَّٰهُ فِي ٱلۡأَرۡضِۖ وَإِنَّا عَلَىٰ ذَهَابِۭ بِهِۦ لَقَٰدِرُونَ ١٨Ife timatumiza madzi kuchokera kumwamba m’muyeso wokwana ndipo timawalowetsa pansi pa nthaka. Ndipo Ife tili ndi mphamvu yowachotsa madziwo فَأَنشَأۡنَا لَكُم بِهِۦ جَنَّٰتٍ مِّن نَّخِيلٍ وَأَعۡنَٰبٍ لَّكُمۡ فِيهَا فَوَٰكِهُ كَثِيرَةٌ وَمِنۡهَا تَأۡكُلُونَ ١٩Ndipo Ife timakutulutsirani mmenemo minda ya tende ndi mphesa, m’mene muli zipatso zanu zambiri zimene zina mwa izo mumadya وَشَجَرَةً تَخۡرُجُ مِن طُورِ سَيۡنَآءَ تَنۢبُتُ بِٱلدُّهۡنِ وَصِبۡغٍ لِّلۡأٓكِلِينَ ٢٠Mtengo umene umamera pa phiri la Sinai, umapereka mafuta ndiponso ndiwo kwa anthu وَإِنَّ لَكُمۡ فِي ٱلۡأَنۡعَٰمِ لَعِبۡرَةًۖ نُّسۡقِيكُم مِّمَّا فِي بُطُونِهَا وَلَكُمۡ فِيهَا مَنَٰفِعُ كَثِيرَةٌ وَمِنۡهَا تَأۡكُلُونَ ٢١M’nyama namonso muli chizindikiro choonetsa mphamvu zathu. Inu timakumwetsani zimene zili m’mimba mwake ndipo mumadya nyama yake ndiponso mumapeza phindu lambiri وَعَلَيۡهَا وَعَلَى ٱلۡفُلۡكِ تُحۡمَلُونَ ٢٢Ndipo pa izo ndi m’zombo zimene zimayenda pa nyanja, inu mumanyamulidwa وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوۡمِهِۦ فَقَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥٓۚ أَفَلَا تَتَّقُونَ ٢٣Tidamutumiza Nowa kwa anthu ake ndipo iye adati, “Tumikirani Mulungu anthu anga chifukwa mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kodi simungamuope Iye?” فَقَالَ ٱلۡمَلَؤُاْ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن قَوۡمِهِۦ مَا هَٰذَآ إِلَّا بَشَرٌ مِّثۡلُكُمۡ يُرِيدُ أَن يَتَفَضَّلَ عَلَيۡكُمۡ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَأَنزَلَ مَلَٰٓئِكَةً مَّا سَمِعۡنَا بِهَٰذَا فِيٓ ءَابَآئِنَا ٱلۡأَوَّلِينَ ٢٤Akuluakulu osakhulupirira a anthu ake adati, “Munthu uyu ndi wolingana ndi inu, iye ali kungodziyenereza kuti ndi wopambana pakati panu.” Mulungu akadafuna, akadatumiza angelo. Ndiponso zinthu za mtundu uwu sitidamvepo kuchokera kwa makolo athu akalekale إِنۡ هُوَ إِلَّا رَجُلُۢ بِهِۦ جِنَّةٌ فَتَرَبَّصُواْ بِهِۦ حَتَّىٰ حِينٍ ٢٥Ndithudi ameneyu ndi wopenga, ndipo mumuyang’anire pa kanthawi.” قَالَ رَبِّ ٱنصُرۡنِي بِمَا كَذَّبُونِ ٢٦Iye adati, “Ambuye! Ndithandizeni ine chifukwa iwo ali kundikana.” فَأَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡهِ أَنِ ٱصۡنَعِ ٱلۡفُلۡكَ بِأَعۡيُنِنَا وَوَحۡيِنَا فَإِذَا جَآءَ أَمۡرُنَا وَفَارَ ٱلتَّنُّورُ فَٱسۡلُكۡ فِيهَا مِن كُلٍّ زَوۡجَيۡنِ ٱثۡنَيۡنِ وَأَهۡلَكَ إِلَّا مَن سَبَقَ عَلَيۡهِ ٱلۡقَوۡلُ مِنۡهُمۡۖ وَلَا تُخَٰطِبۡنِي فِي ٱلَّذِينَ ظَلَمُوٓاْ إِنَّهُم مُّغۡرَقُونَ ٢٧Ife tidavumbulutsa chifuniro chathu kwa iye ponena kuti, “Khoma chombo chimene Ife tidzayang’anira molingana ndi chilangizo chathu. Pamene chiweruzo chathu chidza ndipo madzi asefukira kuchokera ku ng’anjo, utenge zolengedwa ziwiriziwiri, zazimuna ndi zazikazi ndiponso kuchokera kwa iwo a m’nyumba mwako kupatula okhawo amene adanenedwa kuti adzaonongeka. Usandipemphe kuti ndipulumutse iwo amene adachita zoipa chifukwa iwo adzamizidwa.” فَإِذَا ٱسۡتَوَيۡتَ أَنتَ وَمَن مَّعَكَ عَلَى ٱلۡفُلۡكِ فَقُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي نَجَّىٰنَا مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ ٢٨Ndipo pamene iwe ndi iwo amene akutsata iwe mulowa m’chombo, nena, “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu amene watipulumutsa ife kuchoka ku mtundu wa anthu oipa.” وَقُل رَّبِّ أَنزِلۡنِي مُنزَلًا مُّبَارَكًا وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلۡمُنزِلِينَ ٢٩Ndipo nena: “Ambuye wanga! Ndithandizeni kuti ndikafike pamalo podalitsika chifukwa Inu ndinu wabwino wa onse amene amafikitsa pamalo okocheza.” إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ وَإِن كُنَّا لَمُبۡتَلِينَ ٣٠Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro zooneka. Ndithudi Ife timawaika anthu m’mayesero ثُمَّ أَنشَأۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِمۡ قَرۡنًا ءَاخَرِينَ ٣١Potero Ife tidapanga mtundu wa anthu a tsopano pambuyo pawo فَأَرۡسَلۡنَا فِيهِمۡ رَسُولًا مِّنۡهُمۡ أَنِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥٓۚ أَفَلَا تَتَّقُونَ ٣٢Ndipo tidatumiza kwa iwo Mtumwi wa mtundu wawo amene adati, “Tumikirani Mulungu chifukwa inu mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kodi simungamuope Mulungu?” وَقَالَ ٱلۡمَلَأُ مِن قَوۡمِهِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَكَذَّبُواْ بِلِقَآءِ ٱلۡأٓخِرَةِ وَأَتۡرَفۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا مَا هَٰذَآ إِلَّا بَشَرٌ مِّثۡلُكُمۡ يَأۡكُلُ مِمَّا تَأۡكُلُونَ مِنۡهُ وَيَشۡرَبُ مِمَّا تَشۡرَبُونَ ٣٣Koma akuluakulu a anthu osakhulupirira a anthu ake, amene adakana za moyo umene uli nkudza ndi amene tidawapatsa zinthu zabwino za m’moyo uno adati, “Munthu uyu ndi munthu monga inu nomwe amene akudya zimene mumadya inu ndi kumwa zimene inu mumamwa.” وَلَئِنۡ أَطَعۡتُم بَشَرًا مِّثۡلَكُمۡ إِنَّكُمۡ إِذًا لَّخَٰسِرُونَ ٣٤“Ngati inu mumvera munthu wonga inu nomwe, ndithudi, inu mudzatayika.” أَيَعِدُكُمۡ أَنَّكُمۡ إِذَا مِتُّمۡ وَكُنتُمۡ تُرَابًا وَعِظَٰمًا أَنَّكُم مُّخۡرَجُونَ ٣٥“Kodi iye ali kukuopsezani kuti pamene inu mutafa ndi kusanduka dothi ndi mafupa mudzadzuka ndi kukhalanso ndi moyo?” ۞ هَيۡهَاتَ هَيۡهَاتَ لِمَا تُوعَدُونَ ٣٦“Zimene inu muli kuopsezedwa nazo zili kutali.” إِنۡ هِيَ إِلَّا حَيَاتُنَا ٱلدُّنۡيَا نَمُوتُ وَنَحۡيَا وَمَا نَحۡنُ بِمَبۡعُوثِينَ ٣٧“Kulibenso moyo wina koma moyo wathu wapadziko lapansi basi. Ife timafa ndi kukhala ndi moyo ndipo ife sitidzadzukanso ayi.” إِنۡ هُوَ إِلَّا رَجُلٌ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا وَمَا نَحۡنُ لَهُۥ بِمُؤۡمِنِينَ ٣٨“Munthu uyu ndi odziyenereza amene ali kunena za Mulungu zimene sizili zoona ayi. Ife sitidzamukhulupirira.” قَالَ رَبِّ ٱنصُرۡنِي بِمَا كَذَّبُونِ ٣٩Iye adati, “Ambuye! Ndithandizeni ine chifukwa iwo ali kunditsutsa.” قَالَ عَمَّا قَلِيلٍ لَّيُصۡبِحُنَّ نَٰدِمِينَ ٤٠Iye adati, “Posachedwapa iwo adzanong’oneza bombono.” فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّيۡحَةُ بِٱلۡحَقِّ فَجَعَلۡنَٰهُمۡ غُثَآءًۚ فَبُعۡدًا لِّلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ ٤١Chilango chathu chidawapeza mwachilungamo ndipo tidawafafaniza monga zinyalala. Chionongeko kwa anthu onse ochimwa ثُمَّ أَنشَأۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِمۡ قُرُونًا ءَاخَرِينَ ٤٢Atapita awa tidalenganso mitundu ina ya anthu مَا تَسۡبِقُ مِنۡ أُمَّةٍ أَجَلَهَا وَمَا يَسۡتَـٔۡخِرُونَ ٤٣Palibeanthuameneangafulumizitsekapenakuchedwetsa chionongeko chawo ثُمَّ أَرۡسَلۡنَا رُسُلَنَا تَتۡرَاۖ كُلَّ مَا جَآءَ أُمَّةً رَّسُولُهَا كَذَّبُوهُۖ فَأَتۡبَعۡنَا بَعۡضَهُم بَعۡضًا وَجَعَلۡنَٰهُمۡ أَحَادِيثَۚ فَبُعۡدًا لِّقَوۡمٍ لَّا يُؤۡمِنُونَ ٤٤Ndipo Ife tidatumiza Atumwi ena motsagana ndipo nthawi iliyonse Mtumwi amadza kwa iwo ndipo amamukana nati ndi wabodza. Ndipo Ife tidawaononga ena pambuyo pawo ndipo tidawapanga iwo kukhala chitsanzo cha mbiri ya anthu olakwa. Ichi chidali chionongeko cha anthu osakhulupirira ثُمَّ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ وَأَخَاهُ هَٰرُونَ بِـَٔايَٰتِنَا وَسُلۡطَٰنٍ مُّبِينٍ ٤٥Ndipo Ife tidamutumiza Mose pamodzi ndi m’bale wake Aroni ndi zizindikiro ndiponso ulamuliro wathu إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ فَٱسۡتَكۡبَرُواْ وَكَانُواْ قَوۡمًا عَالِينَ ٤٦Kwa Farawo ndi nduna zake ndipo iwo adawalandira mwamwano chifukwa iwo adali anthu a chipongwe فَقَالُوٓاْ أَنُؤۡمِنُ لِبَشَرَيۡنِ مِثۡلِنَا وَقَوۡمُهُمَا لَنَا عَٰبِدُونَ ٤٧Ndipo iwo adati, “Kodi ife tikhulupirire anthu awiri olingana ndi ife amene anthu awo ndi akapolo athu?” فَكَذَّبُوهُمَا فَكَانُواْ مِنَ ٱلۡمُهۡلَكِينَ ٤٨Iwo adawakana iwo kotero iwo adalandira chionongeko وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ لَعَلَّهُمۡ يَهۡتَدُونَ ٤٩Ndipo Ife tidamupatsa Mose Buku la Chipangano Chakale kuti anthu ake akhoza kutsogozedwa bwino وَجَعَلۡنَا ٱبۡنَ مَرۡيَمَ وَأُمَّهُۥٓ ءَايَةً وَءَاوَيۡنَٰهُمَآ إِلَىٰ رَبۡوَةٍ ذَاتِ قَرَارٍ وَمَعِينٍ ٥٠Ife tidamupanga mwana wamwamuna wa Maria pamodzi ndi amayi ake kukhala chizindikiro kwa anthu onse ndipo tidawapatsa mnthunzi pa malo okwera ndi malo a mtendere amene anali kuthiriridwa ndi madzi a pa kasupe يَٰٓأَيُّهَا ٱلرُّسُلُ كُلُواْ مِنَ ٱلطَّيِّبَٰتِ وَٱعۡمَلُواْ صَٰلِحًاۖ إِنِّي بِمَا تَعۡمَلُونَ عَلِيمٌ ٥١Oh Atumwi! Idyani zinthu zabwino ndipo muzichita ntchito zabwino. Ndithudi Ine ndimadziwa zonse zimene mumachita وَإِنَّ هَٰذِهِۦٓ أُمَّتُكُمۡ أُمَّةً وَٰحِدَةً وَأَنَا۠ رَبُّكُمۡ فَٱتَّقُونِ ٥٢Ndithudi chipembedzo chanu ndi chimodzi ndipo Ine ndine Ambuye wanu. Kotero ndiopeni Ine فَتَقَطَّعُوٓاْ أَمۡرَهُم بَيۡنَهُمۡ زُبُرًاۖ كُلُّ حِزۡبِۭ بِمَا لَدَيۡهِمۡ فَرِحُونَ ٥٣Koma anthu adagawanika m’magulu osiyanasiyana, gulu lililonse limasangalala ndi ziphunzitso zawo فَذَرۡهُمۡ فِي غَمۡرَتِهِمۡ حَتَّىٰ حِينٍ ٥٤Alekeni ayambe achimwa mpaka pamene imfa iwapeza أَيَحۡسَبُونَ أَنَّمَا نُمِدُّهُم بِهِۦ مِن مَّالٍ وَبَنِينَ ٥٥Kodi iwo amaganiza kuti popeza tawapatsa chuma ndi ana نُسَارِعُ لَهُمۡ فِي ٱلۡخَيۡرَٰتِۚ بَل لَّا يَشۡعُرُونَ ٥٦Ndiye kuti Ife tili kuwafunira zabwino? Iyayi. Iwo sadziwa kanthu ayi إِنَّ ٱلَّذِينَ هُم مِّنۡ خَشۡيَةِ رَبِّهِم مُّشۡفِقُونَ ٥٧Ndithudi iwo ndi anthu amene amaopa Ambuye wawo وَٱلَّذِينَ هُم بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِمۡ يُؤۡمِنُونَ ٥٨Amene amakhulupirira zizindikiro za Ambuye wawo وَٱلَّذِينَ هُم بِرَبِّهِمۡ لَا يُشۡرِكُونَ ٥٩Amene sapembedza wina aliyense poonjezera pa Ambuye wawo وَٱلَّذِينَ يُؤۡتُونَ مَآ ءَاتَواْ وَّقُلُوبُهُمۡ وَجِلَةٌ أَنَّهُمۡ إِلَىٰ رَبِّهِمۡ رَٰجِعُونَ ٦٠Amene amapereka chaulere mitima ili yoopa Ambuye wawo chifukwa chakuti adzabwerera kwa Iye أُوْلَٰٓئِكَ يُسَٰرِعُونَ فِي ٱلۡخَيۡرَٰتِ وَهُمۡ لَهَا سَٰبِقُونَ ٦١Awa ndiwo amene amapikisana wina ndi mnzake pochita zabwino ndipo amakhala oyamba pozindikira وَلَا نُكَلِّفُ نَفۡسًا إِلَّا وُسۡعَهَاۚ وَلَدَيۡنَا كِتَٰبٌ يَنطِقُ بِٱلۡحَقِّ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ ٦٢Ife sitinyamulitsa mzimu wina uliwonse katundu amene iwo sangathe kunyamula. M’buku lathu mudalembedwa zoona zokhazokha. Ndipo palibe munthu amene adzaponderezedwa بَلۡ قُلُوبُهُمۡ فِي غَمۡرَةٍ مِّنۡ هَٰذَا وَلَهُمۡ أَعۡمَٰلٌ مِّن دُونِ ذَٰلِكَ هُمۡ لَهَا عَٰمِلُونَ ٦٣Koma mitima ya anthu osakhulupirira siyizidziwa zimenezi ayi. Iwo ali ndi ntchito zina zoipa kupatula zimene iwo amachita حَتَّىٰٓ إِذَآ أَخَذۡنَا مُتۡرَفِيهِم بِٱلۡعَذَابِ إِذَا هُمۡ يَجۡـَٔرُونَ ٦٤Koma pamene chilango chathu chidza pa iwo amene amakhala mu mtendere, iwo adzafuula kufuna chithandizo لَا تَجۡـَٔرُواْ ٱلۡيَوۡمَۖ إِنَّكُم مِّنَّا لَا تُنصَرُونَ ٦٥Musalire tsiku la lero chifukwa inu simudzalandira chithandizo china chilichonse kuchokera kwa Ife قَدۡ كَانَتۡ ءَايَٰتِي تُتۡلَىٰ عَلَيۡكُمۡ فَكُنتُمۡ عَلَىٰٓ أَعۡقَٰبِكُمۡ تَنكِصُونَ ٦٦Chivumbulutso changa chinali kulakatulidwa kwa inu nthawi zambiri koma inu munali kuthawa ndi kuchikana mwamwano مُسۡتَكۡبِرِينَ بِهِۦ سَٰمِرًا تَهۡجُرُونَ ٦٧Inu mumachinyoza usana ndi usiku uliwonse أَفَلَمۡ يَدَّبَّرُواْ ٱلۡقَوۡلَ أَمۡ جَآءَهُم مَّا لَمۡ يَأۡتِ ءَابَآءَهُمُ ٱلۡأَوَّلِينَ ٦٨Kodi iwo sangathe kulingalira mozama pa mawu a Mulungu kapena pali china chake chimene chidavumbulutsidwa kwa iwo chimene sichidavumbulutsidwe kwa makolo awo أَمۡ لَمۡ يَعۡرِفُواْ رَسُولَهُمۡ فَهُمۡ لَهُۥ مُنكِرُونَ ٦٩Kapena iwo sadziwa kuti akukana Mtumwi wawo أَمۡ يَقُولُونَ بِهِۦ جِنَّةُۢۚ بَلۡ جَآءَهُم بِٱلۡحَقِّ وَأَكۡثَرُهُمۡ لِلۡحَقِّ كَٰرِهُونَ ٧٠Kapena iwo akuti Iye ndi wopenga? Koma iye wawabweretsera iwo onse zoonadi. Koma ambiri amakana choonadi وَلَوِ ٱتَّبَعَ ٱلۡحَقُّ أَهۡوَآءَهُمۡ لَفَسَدَتِ ٱلسَّمَٰوَٰتُ وَٱلۡأَرۡضُ وَمَن فِيهِنَّۚ بَلۡ أَتَيۡنَٰهُم بِذِكۡرِهِمۡ فَهُمۡ عَن ذِكۡرِهِم مُّعۡرِضُونَ ٧١Kukadakhala kuti choonadi chimatsatira zofuna zawo, ndithudi, kumwamba, dziko lapansi ndi onse okhala m’menemo akadaonongeka. Ife tawapatsa chikumbutso komabe iwo safuna kumvera chikumbutsocho أَمۡ تَسۡـَٔلُهُمۡ خَرۡجًا فَخَرَاجُ رَبِّكَ خَيۡرٌۖ وَهُوَ خَيۡرُ ٱلرَّٰزِقِينَ ٧٢Kapena iwe uli kuwapemphera mphotho? Chithandizo cha Ambuye wawo ndicho chabwino. Ndipo Iye ndiye wopereka moolowa manja kuposa onse amene amapereka وَإِنَّكَ لَتَدۡعُوهُمۡ إِلَىٰ صِرَٰطٍ مُّسۡتَقِيمٍ ٧٣Ndithudi iwe uli kuwaitana kuti adze kunjira yoyenera وَإِنَّ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ عَنِ ٱلصِّرَٰطِ لَنَٰكِبُونَ ٧٤Ndithudi iwo amene amakana moyo umene uli nkudza adzakhala ali kusochera ku njira yoyenerayi ۞ وَلَوۡ رَحِمۡنَٰهُمۡ وَكَشَفۡنَا مَا بِهِم مِّن ضُرٍّ لَّلَجُّواْ فِي طُغۡيَٰنِهِمۡ يَعۡمَهُونَ ٧٥Ngati Ife tikadawalangiza chisoni chathu ndi kuwachotsera mavuto, iwo akadakhala ali kulakwabe m’njira zawo zoipa ndi kusokonezeka ndi zoipazo وَلَقَدۡ أَخَذۡنَٰهُم بِٱلۡعَذَابِ فَمَا ٱسۡتَكَانُواْ لِرَبِّهِمۡ وَمَا يَتَضَرَّعُونَ ٧٦Ndithudi tidawalanga kale koma iwo sadafunefune Ambuye wawo kapena kukhala odzichepetsa pamaso pake حَتَّىٰٓ إِذَا فَتَحۡنَا عَلَيۡهِم بَابًا ذَا عَذَابٍ شَدِيدٍ إِذَا هُمۡ فِيهِ مُبۡلِسُونَ ٧٧Mpaka pamene tidzawatsekulira khomo la chilango chowawa, iwo adzakhala okhumudwa وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَنشَأَ لَكُمُ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡأَبۡصَٰرَ وَٱلۡأَفۡـِٔدَةَۚ قَلِيلًا مَّا تَشۡكُرُونَ ٧٨Iye ndiye amene adakupatsani makutu, maso ndi mitima. Komabe inu simuthokoza mokwanira وَهُوَ ٱلَّذِي ذَرَأَكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَإِلَيۡهِ تُحۡشَرُونَ ٧٩Iye ndiye amene adakulengani ndi kukuchulukitsani padziko lapansi ndipo nonsenu mudzasonkhanitsidwa kudza pamaso pake وَهُوَ ٱلَّذِي يُحۡيِۦ وَيُمِيتُ وَلَهُ ٱخۡتِلَٰفُ ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ ٨٠Iye ndiye amene amapereka moyo ndiponso imfa ndipo ndi Iyenso amene amasithanitsa usiku ndi usana. Kodi simungazindikire بَلۡ قَالُواْ مِثۡلَ مَا قَالَ ٱلۡأَوَّلُونَ ٨١Iwo amanena zimene anthu akale ankanena قَالُوٓاْ أَءِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابًا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ ٨٢Iwo amati, “Pamene ife tafa ndi kusanduka dothi ndi mafupa, kodi tidzadzukanso ndi kukhala ndi moyo?” لَقَدۡ وُعِدۡنَا نَحۡنُ وَءَابَآؤُنَا هَٰذَا مِن قَبۡلُ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّآ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ ٨٣Ndithudi ife tidalonjedzedwa zimenezi kale pamodzi ndi makolo athu. Izi si zina ayi koma nkhani zabodza za anthu a makedzana قُل لِّمَنِ ٱلۡأَرۡضُ وَمَن فِيهَآ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ ٨٤Nena, “Kodi Mwini wake wa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo ndani? Ndiuzeni ngati mumudziwa.” سَيَقُولُونَ لِلَّهِۚ قُلۡ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ ٨٥Iwo adzati, “Mwini wake ndi Mulungu.” Nena, “Kodi inu simungachenjezedwe?” قُلۡ مَن رَّبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ ٱلسَّبۡعِ وَرَبُّ ٱلۡعَرۡشِ ٱلۡعَظِيمِ ٨٦Nena, “Kodi Ambuye wa miyamba isanu ndi iwiri ndiponso Mwini Ufumu ndani?” سَيَقُولُونَ لِلَّهِۚ قُلۡ أَفَلَا تَتَّقُونَ ٨٧Iwo adzati, “Mwini wake ndi Mulungu.” Nena, “Nanga kodi simungasiye kuchita zoipa?” قُلۡ مَنۢ بِيَدِهِۦ مَلَكُوتُ كُلِّ شَيۡءٍ وَهُوَ يُجِيرُ وَلَا يُجَارُ عَلَيۡهِ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ ٨٨Nena, “Kodi ulamuliro wa zinthu zonse zili m’manja mwa yani? Kodi ndani amene amaziteteza zonse pamene Iye safuna chitetezo cha wina aliyense ngati inu mukudziwa?” سَيَقُولُونَ لِلَّهِۚ قُلۡ فَأَنَّىٰ تُسۡحَرُونَ ٨٩Iwo adzati, “M’manja mwa Mulungu.” Nena, “Nanga ndi chifukwa chiyani inu mwanyengedwa?” بَلۡ أَتَيۡنَٰهُم بِٱلۡحَقِّ وَإِنَّهُمۡ لَكَٰذِبُونَ ٩٠Iyayi, Ife tawavumbulutsira choonadi. Koma onsewa ndi anthu abodza مَا ٱتَّخَذَ ٱللَّهُ مِن وَلَدٍ وَمَا كَانَ مَعَهُۥ مِنۡ إِلَٰهٍۚ إِذًا لَّذَهَبَ كُلُّ إِلَٰهِۭ بِمَا خَلَقَ وَلَعَلَا بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٍۚ سُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ عَمَّا يَصِفُونَ ٩١Palibe nthawi imene Mulungu adabala mwana ndipo kulibe Mulungu wina woonjezera pa Iye. Ngati izi zikadakhala choncho, bwezi Mulungu aliyense akumatenga zolengedwa zake zokha ndi kumaziika pamwamba pa zolengedwa za Mulungu wina. Ulemerero ukhale kwa Mulungu woposa zina zilizonse عَٰلِمِ ٱلۡغَيۡبِ وَٱلشَّهَٰدَةِ فَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ ٩٢Iye amadziwa zonse zooneka ndiponso zobisika. Mulungu akhale wopambana milungu ina imene iwo amaitumikira قُل رَّبِّ إِمَّا تُرِيَنِّي مَا يُوعَدُونَ ٩٣Nena, “Ambuye wanga! Ngati Inu mukadandionetsa chilango chimene muli kuwopseza رَبِّ فَلَا تَجۡعَلۡنِي فِي ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ ٩٤Ambuye wanga! Pulumutsani ndipo musandisiye ine pakati pa mtundu wa anthu oipawu.” وَإِنَّا عَلَىٰٓ أَن نُّرِيَكَ مَا نَعِدُهُمۡ لَقَٰدِرُونَ ٩٥Ndithudi, Ife tili ndi mphamvu zoti ukhoza kuona chilango chimene tawaopseza ٱدۡفَعۡ بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ ٱلسَّيِّئَةَۚ نَحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَا يَصِفُونَ ٩٦Dzitetezeni ndi chabwino pothamangitsa choipa. Ife tili kudziwa zonse zimene ali kukunamizirani وَقُل رَّبِّ أَعُوذُ بِكَ مِنۡ هَمَزَٰتِ ٱلشَّيَٰطِينِ ٩٧Ndipo iwe unene kuti, “Ambuye wanga, Ine ndili kufuna chitetezo chanu pothawa zoipa za Satana.” وَأَعُوذُ بِكَ رَبِّ أَن يَحۡضُرُونِ ٩٨“Ambuye! Ine ndili kupempha chitetezo chanu kuti asabwere kumene ndili ine.” حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَ أَحَدَهُمُ ٱلۡمَوۡتُ قَالَ رَبِّ ٱرۡجِعُونِ ٩٩Mpaka pamene imfa idza kwa munthu wolakwa iye adzati, “Ambuye wanga! Bwezeni.” لَعَلِّيٓ أَعۡمَلُ صَٰلِحًا فِيمَا تَرَكۡتُۚ كـَلَّآۚ إِنَّهَا كَلِمَةٌ هُوَ قَآئِلُهَاۖ وَمِن وَرَآئِهِم بَرۡزَخٌ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ ١٠٠“Kuti ndikachite ntchitozabwinozimenendidalepherakuchita.” Kosatheka! Amenewa ndiwo mawu chabe amene akungolankhula. Kumbuyo kwawo kudzakhala chipupa mpaka pa tsiku la kuuka kwa akufa فَإِذَا نُفِخَ فِي ٱلصُّورِ فَلَآ أَنسَابَ بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَئِذٍ وَلَا يَتَسَآءَلُونَ ١٠١Ndipo pamene lipenga lidzaombedwa, pa tsiku limeneli, ubale wawo wonse udzathera pomwepo ndiponso sadzafunsana chithandizo chochokera kwa wina ndi mnzake فَمَن ثَقُلَتۡ مَوَٰزِينُهُۥ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ ١٠٢Aliyense amene muyeso wake udzakhala wolemera, adzapambana وَمَنۡ خَفَّتۡ مَوَٰزِينُهُۥ فَأُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ فِي جَهَنَّمَ خَٰلِدُونَ ١٠٣Koma aliyense amene muyeso wake udzakhala wopepuka adzataya moyo wake ndipo adzakhala ku Gahena nthawi zonse تَلۡفَحُ وُجُوهَهُمُ ٱلنَّارُ وَهُمۡ فِيهَا كَٰلِحُونَ ١٠٤Moto udzatentha nkhope zawo ndipo izo zidzakwinyikakwinyika chifukwa chaululu أَلَمۡ تَكُنۡ ءَايَٰتِي تُتۡلَىٰ عَلَيۡكُمۡ فَكُنتُم بِهَا تُكَذِّبُونَ ١٠٥“Kodi chivumbulutso chathu sichidalakatulidwe kwa inu? Kodi simudachikane?” قَالُواْ رَبَّنَا غَلَبَتۡ عَلَيۡنَا شِقۡوَتُنَا وَكُنَّا قَوۡمًا ضَآلِّينَ ١٠٦Iwo adzati, “Ambuye wathu! Zilakolako zathu zidatigonjetsa ife ndipo tidali anthu osochera.” رَبَّنَآ أَخۡرِجۡنَا مِنۡهَا فَإِنۡ عُدۡنَا فَإِنَّا ظَٰلِمُونَ ١٠٧“Ambuye wathu! tipulumutseni ife ku ichi. Ngati ife tidzabwereranso ku zoipa, ndithudi, ife tidzakhala anthu oipa kwambiri.” قَالَ ٱخۡسَـُٔواْ فِيهَا وَلَا تُكَلِّمُونِ ١٠٨Iye adzati, “Khalani mu icho mwamanyazi ndipo musandiyankhulitse Ine ayi.” إِنَّهُۥ كَانَ فَرِيقٌ مِّنۡ عِبَادِي يَقُولُونَ رَبَّنَآ ءَامَنَّا فَٱغۡفِرۡ لَنَا وَٱرۡحَمۡنَا وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلرَّٰحِمِينَ ١٠٩Ndithudi padali gulu la Atumiki anga amene adati, “Ambuye wathu! Ife timakhulupirira mwa inu. Tikhululukireni ndipo mutichitire chisoni. Inu ndinu wabwino pochita chisoni kuposa a chisoni onse.” فَٱتَّخَذۡتُمُوهُمۡ سِخۡرِيًّا حَتَّىٰٓ أَنسَوۡكُمۡ ذِكۡرِي وَكُنتُم مِّنۡهُمۡ تَضۡحَكُونَ ١١٠Koma inu munali kuwanyogodola mpaka pamene inu mudandiiwala Ine ndipo inu munali kuwaseka iwo إِنِّي جَزَيۡتُهُمُ ٱلۡيَوۡمَ بِمَا صَبَرُوٓاْ أَنَّهُمۡ هُمُ ٱلۡفَآئِزُونَ ١١١Ndithudi lero Ine ndawalipira chifukwa cha kupirira kwawo ndipo iwo ndi amene apambana قَٰلَ كَمۡ لَبِثۡتُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ عَدَدَ سِنِينَ ١١٢Ndipo Iye adzafunsa kuti, “Kodi inu munakhala padziko lapansi zaka zingati?” قَالُواْ لَبِثۡنَا يَوۡمًا أَوۡ بَعۡضَ يَوۡمٍ فَسۡـَٔلِ ٱلۡعَآدِّينَ ١١٣Iwo adzayankha kuti, “Takhala tsiku limodzi kapena mphindi zochepa zokha. Afunseni iwo amene amasunga chiwerengero.” قَٰلَ إِن لَّبِثۡتُمۡ إِلَّا قَلِيلًاۖ لَّوۡ أَنَّكُمۡ كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ ١١٤Iye adzawayankha kuti, “Inu mukadadziwa ndi nthawi yochepa kwambiri imene inu munakhala.” أَفَحَسِبۡتُمۡ أَنَّمَا خَلَقۡنَٰكُمۡ عَبَثًا وَأَنَّكُمۡ إِلَيۡنَا لَا تُرۡجَعُونَ ١١٥“Kodi inu mumaganiza kuti tidangokulengani inu opanda cholinga ndipo kuti simudzabwerera kwa Ife?” فَتَعَٰلَى ٱللَّهُ ٱلۡمَلِكُ ٱلۡحَقُّۖ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ رَبُّ ٱلۡعَرۡشِ ٱلۡكَرِيمِ ١١٦Motero alemekezeke Mulungu, Mfumu ya chilungamo. Palibe Mulungu wina koma Iye yekha, Ambuye wa Mpando wolemekezeka ndi Wachifumu وَمَن يَدۡعُ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ لَا بُرۡهَٰنَ لَهُۥ بِهِۦ فَإِنَّمَا حِسَابُهُۥ عِندَ رَبِّهِۦٓۚ إِنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلۡكَٰفِرُونَ ١١٧Aliyense amene apembedza mulungu wina woonjezera pa Mulungu, pamene Iye alibe umboni wa chimenecho, Ambuye wake adzamufunsa. Ndithudi anthu osakhulupirira sadzapambana ayi وَقُل رَّبِّ ٱغۡفِرۡ وَٱرۡحَمۡ وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلرَّٰحِمِينَ ١١٨Nena, “Ambuye wanga! Ndikhululukireni machimo anga ndipo mundichitire chisoni chifukwa Inu ndinu wachisoni choposa a chisoni onse.”

الترجمة: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.