ملة الإسلام

السورة 4 · 176 آية · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

سورة النساء باللغة الشيشيوا

السورة بالعربية مع التفسير استمع إلى سورة النساء (1,273 قارئاً)
مدنيةسورة النساء١٧٦ آية

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ ٱتَّقُواْ رَبَّكُمُ ٱلَّذِي خَلَقَكُم مِّن نَّفۡسٍ وَٰحِدَةٍ وَخَلَقَ مِنۡهَا زَوۡجَهَا وَبَثَّ مِنۡهُمَا رِجَالًا كَثِيرًا وَنِسَآءًۚ وَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ ٱلَّذِي تَسَآءَلُونَ بِهِۦ وَٱلۡأَرۡحَامَۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلَيۡكُمۡ رَقِيبًا ١oh inu anthu! Muopeni Ambuye wanu amene anakulengani inu kuchokera kwa munthu mmodzi ndipo kuchokera kwa munthu ameneyu, Iye analenga mkazi wake. Ndipo kudzera mwa iwo, Iye adadzadza dziko lonse lapansi ndi anthu amuna ndi akazi osawerengeka. Opani Mulungu, dzina limene mumadandaulirana wina ndi mnzake. Ndipo lemekezani chibale. Ndithudi Mulungu amakuyang’anirani nthawi zonse وَءَاتُواْ ٱلۡيَتَٰمَىٰٓ أَمۡوَٰلَهُمۡۖ وَلَا تَتَبَدَّلُواْ ٱلۡخَبِيثَ بِٱلطَّيِّبِۖ وَلَا تَأۡكُلُوٓاْ أَمۡوَٰلَهُمۡ إِلَىٰٓ أَمۡوَٰلِكُمۡۚ إِنَّهُۥ كَانَ حُوبًا كَبِيرًا ٢Apatseni ana a masiye chuma chawo akafika msinkhu woyenera. Musasinthitse choipa ndi chabwino ndipo musadye chuma chawo pamodzi ndi chanu chifukwa kutero, ndithudi, ndi tchimo lalikulu وَإِنۡ خِفۡتُمۡ أَلَّا تُقۡسِطُواْ فِي ٱلۡيَتَٰمَىٰ فَٱنكِحُواْ مَا طَابَ لَكُم مِّنَ ٱلنِّسَآءِ مَثۡنَىٰ وَثُلَٰثَ وَرُبَٰعَۖ فَإِنۡ خِفۡتُمۡ أَلَّا تَعۡدِلُواْ فَوَٰحِدَةً أَوۡ مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُكُمۡۚ ذَٰلِكَ أَدۡنَىٰٓ أَلَّا تَعُولُواْ ٣Ngati inu muopa kuti simungathe kuchita chilungamo ndi ana a masiye, kwatirani mkazi amene mungamukonde awiri, atatu kapena anayi. Koma ngati inu muopa kuti simudzatha kuchita chilungamo, kukwaniritsa zonse bwinobwino, kwatirani mmodzi yekha kapena wina wa a kapolo a chitsikana amene muli nawo. Chimenechi chidzakhala chapafupi kwa inu kuti musalephere kutsata njira ya chilungamo وَءَاتُواْ ٱلنِّسَآءَ صَدُقَٰتِهِنَّ نِحۡلَةًۚ فَإِن طِبۡنَ لَكُمۡ عَن شَيۡءٍ مِّنۡهُ نَفۡسًا فَكُلُوهُ هَنِيٓـًٔا مَّرِيٓـًٔا ٤Apatseni akazi mphatso yawo monga mphatso yaulere. Koma ngati iwo, mwa chifuniro chawo, asankha kukugawiraniko gawo la mphatsoyi, idyani mosangalala ndi mwa ubwino وَلَا تُؤۡتُواْ ٱلسُّفَهَآءَ أَمۡوَٰلَكُمُ ٱلَّتِي جَعَلَ ٱللَّهُ لَكُمۡ قِيَٰمًا وَٱرۡزُقُوهُمۡ فِيهَا وَٱكۡسُوهُمۡ وَقُولُواْ لَهُمۡ قَوۡلًا مَّعۡرُوفًا ٥Musawapatse anthu ozerezeka katundu amene Mulungu wakupatsani kuti muziwathandizira, koma inu muyenera kuwasamala ndi kuwaveka kuchokera ku phindu la katunduyu ndipo lankhulani nawo mawu abwino a chifundo وَٱبۡتَلُواْ ٱلۡيَتَٰمَىٰ حَتَّىٰٓ إِذَا بَلَغُواْ ٱلنِّكَاحَ فَإِنۡ ءَانَسۡتُم مِّنۡهُمۡ رُشۡدًا فَٱدۡفَعُوٓاْ إِلَيۡهِمۡ أَمۡوَٰلَهُمۡۖ وَلَا تَأۡكُلُوهَآ إِسۡرَافًا وَبِدَارًا أَن يَكۡبَرُواْۚ وَمَن كَانَ غَنِيًّا فَلۡيَسۡتَعۡفِفۡۖ وَمَن كَانَ فَقِيرًا فَلۡيَأۡكُلۡ بِٱلۡمَعۡرُوفِۚ فَإِذَا دَفَعۡتُمۡ إِلَيۡهِمۡ أَمۡوَٰلَهُمۡ فَأَشۡهِدُواْ عَلَيۡهِمۡۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ حَسِيبًا ٦Aikeni ana a masiye pa mayesero mpakana pamene afika poti atha msinkhu. Ngati inu muona kuti ndi a maganizo okhazikika, apatseni chuma chawo ndipo musawaonongere iwo chuma chawo asanathe msinkhu. Munthu amene ali olemera asagwiritse ntchito katundu wa ana a masiye amene ali kumuyang’anira ndipo munthu osauka agwiritse ntchito chuma cha ana a masiye mosamala ndi mwa chilungamo. Pamene inu muwapatsa chuma chawo, itanani ena kuti akhale mboni; Mulungu ndi wokwana kukhala mboni pa zonse zimene muchita لِّلرِّجَالِ نَصِيبٌ مِّمَّا تَرَكَ ٱلۡوَٰلِدَانِ وَٱلۡأَقۡرَبُونَ وَلِلنِّسَآءِ نَصِيبٌ مِّمَّا تَرَكَ ٱلۡوَٰلِدَانِ وَٱلۡأَقۡرَبُونَ مِمَّا قَلَّ مِنۡهُ أَوۡ كَثُرَۚ نَصِيبًا مَّفۡرُوضًا ٧Amuna adzakhala ndi gawo mu katundu amene makolo ndi abale awo asiya ndipo akazi adzakhala ndi gawo mu katunduamenemakolondiabaleawoasiya. Kayakatunduyo ndi wochepa kapena wambiri, onse ayenera kulandira gawo lawo malinga ndi malamulo وَإِذَا حَضَرَ ٱلۡقِسۡمَةَ أُوْلُواْ ٱلۡقُرۡبَىٰ وَٱلۡيَتَٰمَىٰ وَٱلۡمَسَٰكِينُ فَٱرۡزُقُوهُم مِّنۡهُ وَقُولُواْ لَهُمۡ قَوۡلًا مَّعۡرُوفًا ٨Ngati a chibale, a masiye kapena osauka alipo pamene ali kugawa chuma cha masiye, agawireniko nawonso ndipo alankhuleni ndi mawu abwino وَلۡيَخۡشَ ٱلَّذِينَ لَوۡ تَرَكُواْ مِنۡ خَلۡفِهِمۡ ذُرِّيَّةً ضِعَٰفًا خَافُواْ عَلَيۡهِمۡ فَلۡيَتَّقُواْ ٱللَّهَ وَلۡيَقُولُواْ قَوۡلًا سَدِيدًا ٩Alekeni iwo amene amafunira zabwino ana awo, pamene iwo akufa, kuti asamale posawalakwira ana amasiye. Alekeni kuti aope Mulungu ndi kunena zinthu zokhazikitsa choonadi إِنَّ ٱلَّذِينَ يَأۡكُلُونَ أَمۡوَٰلَ ٱلۡيَتَٰمَىٰ ظُلۡمًا إِنَّمَا يَأۡكُلُونَ فِي بُطُونِهِمۡ نَارًاۖ وَسَيَصۡلَوۡنَ سَعِيرًا ١٠Kwa iwo amene amadya chuma cha ana a masiye mopanda chilungamo amameza moto m’mimba mwawo ndipo iwo adzalowa m’malawi a moto wa ku Gahena يُوصِيكُمُ ٱللَّهُ فِيٓ أَوۡلَٰدِكُمۡۖ لِلذَّكَرِ مِثۡلُ حَظِّ ٱلۡأُنثَيَيۡنِۚ فَإِن كُنَّ نِسَآءً فَوۡقَ ٱثۡنَتَيۡنِ فَلَهُنَّ ثُلُثَا مَا تَرَكَۖ وَإِن كَانَتۡ وَٰحِدَةً فَلَهَا ٱلنِّصۡفُۚ وَلِأَبَوَيۡهِ لِكُلِّ وَٰحِدٍ مِّنۡهُمَا ٱلسُّدُسُ مِمَّا تَرَكَ إِن كَانَ لَهُۥ وَلَدٌۚ فَإِن لَّمۡ يَكُن لَّهُۥ وَلَدٌ وَوَرِثَهُۥٓ أَبَوَاهُ فَلِأُمِّهِ ٱلثُّلُثُۚ فَإِن كَانَ لَهُۥٓ إِخۡوَةٌ فَلِأُمِّهِ ٱلسُّدُسُۚ مِنۢ بَعۡدِ وَصِيَّةٍ يُوصِي بِهَآ أَوۡ دَيۡنٍۗ ءَابَآؤُكُمۡ وَأَبۡنَآؤُكُمۡ لَا تَدۡرُونَ أَيُّهُمۡ أَقۡرَبُ لَكُمۡ نَفۡعًاۚ فَرِيضَةً مِّنَ ٱللَّهِۗ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلِيمًا حَكِيمًا ١١Mulungu wakulamulirani motere pankhani za ana anu: Mwana wa mwamuma adzalandira magawo awiri kuposa mwana wa mkazi. Ndipo ngati ana a akazi apitirira awiri, iwo adzalandira magawo awiri pa magawo atatu a katundu wosiyidwa koma ngati alipo mwana mmodzi yekha wamkazi, adzalandila theka ndipo makolo ake awiri, aliyense mwa iwo adzalandira gawo limodzi la magawo asanu ndi limodzi – muzimene adasiya malemuyo ngati malemuyo ali ndi mwana. Koma ngati alibe mwana ndipo makolo ake ndiwo amene ayenera kulandira katundu wake, amayi ake adzalandira gawo limodzi la magawo atatu. Ngati iye ali ndi abale ake, amayi ake adzalandira gawo limodzi la magawo asanu ndi limodzi atatha kukwaniritsa lonjezo la malemu ndiponso kubweza ngongole. Inu simudziwa kuti pakati pa makolo anu ndi ana anu amene ali wa phindu ndi inu. Ili ndi lamulo la Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi wanzeru ndi wodziwa chilichonse ۞ وَلَكُمۡ نِصۡفُ مَا تَرَكَ أَزۡوَٰجُكُمۡ إِن لَّمۡ يَكُن لَّهُنَّ وَلَدٌۚ فَإِن كَانَ لَهُنَّ وَلَدٌ فَلَكُمُ ٱلرُّبُعُ مِمَّا تَرَكۡنَۚ مِنۢ بَعۡدِ وَصِيَّةٍ يُوصِينَ بِهَآ أَوۡ دَيۡنٍۚ وَلَهُنَّ ٱلرُّبُعُ مِمَّا تَرَكۡتُمۡ إِن لَّمۡ يَكُن لَّكُمۡ وَلَدٌۚ فَإِن كَانَ لَكُمۡ وَلَدٌ فَلَهُنَّ ٱلثُّمُنُ مِمَّا تَرَكۡتُمۚ مِّنۢ بَعۡدِ وَصِيَّةٍ تُوصُونَ بِهَآ أَوۡ دَيۡنٍۗ وَإِن كَانَ رَجُلٌ يُورَثُ كَلَٰلَةً أَوِ ٱمۡرَأَةٌ وَلَهُۥٓ أَخٌ أَوۡ أُخۡتٌ فَلِكُلِّ وَٰحِدٍ مِّنۡهُمَا ٱلسُّدُسُۚ فَإِن كَانُوٓاْ أَكۡثَرَ مِن ذَٰلِكَ فَهُمۡ شُرَكَآءُ فِي ٱلثُّلُثِۚ مِنۢ بَعۡدِ وَصِيَّةٍ يُوصَىٰ بِهَآ أَوۡ دَيۡنٍ غَيۡرَ مُضَآرٍّۚ وَصِيَّةً مِّنَ ٱللَّهِۗ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَلِيمٌ ١٢Inu mudzalandira theka la chuma chimene akazi anu adasiya, ngati iwo alibe mwana. Ngati ali ndi mwana, inu mudzalandira gawo limodzi la magawo anayi la zimene mkaziyo wasiya pambuyo popereka zimene analonjeza ndi kubwezera ngongole. Nawo akazi anu adzapeza gawo limodzi m’magawo anayi muzimene mwasiya ngati mulibe mwana. Koma ngati muli ndi mwana, iwo, akaziwo, adzapeza gawo limodzi la magawo asanu ndi atatu a zimene mwasiya, pambuyo popereka zimene mudalonjeza ndi kubwezera ngongole. Ngati mwamuna kapena mkazi ndi yemwe wasiya katundu ndipo alibe mwana kapena mdzukulu, koma ali ndi mchimwene wake kapena mchemwali wake, aliyense wa iwo adzapeza gawo limodzi m’magawo asanu ndi limodzi, ndipo ngati adali ambiri koposa apo adzagawana gawo limodzi la magawo atatu pambuyo popereka zimene analonjeza kapena kubwezera ngongole mosabweretsa mavuto. Limeneli ndi lamulo lochokera kwa Mulungu, Mulungu ndi wodziwa ndi woleza mtima تِلۡكَ حُدُودُ ٱللَّهِۚ وَمَن يُطِعِ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ يُدۡخِلۡهُ جَنَّٰتٍ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ وَذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ ١٣Awa ndi malire a Mulungu. Ndipo aliyense amene amvera Mulungu ndi Mtumwi wake adzaikidwa m’minda yoyenda mitsinje pansi pake kumene adzakhalako nthawi zonse. Ndipo kumeneko ndiko kupambana kwakukulu وَمَن يَعۡصِ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ وَيَتَعَدَّ حُدُودَهُۥ يُدۡخِلۡهُ نَارًا خَٰلِدًا فِيهَا وَلَهُۥ عَذَابٌ مُّهِينٌ ١٤Koma iye amene amanyoza Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo amalumpha malire ake, adzamuponya ku moto wa ku Gahena ndipo adzakhala komweko mpaka kalekale ndipo iye adzalandira chilango chochititsa manyazi وَٱلَّٰتِي يَأۡتِينَ ٱلۡفَٰحِشَةَ مِن نِّسَآئِكُمۡ فَٱسۡتَشۡهِدُواْ عَلَيۡهِنَّ أَرۡبَعَةً مِّنكُمۡۖ فَإِن شَهِدُواْ فَأَمۡسِكُوهُنَّ فِي ٱلۡبُيُوتِ حَتَّىٰ يَتَوَفَّىٰهُنَّ ٱلۡمَوۡتُ أَوۡ يَجۡعَلَ ٱللَّهُ لَهُنَّ سَبِيلًا ١٥Ndipo iwo, mwa akazi anu, amene achita chigololo, pezani mboni zokwanira zinayi zochokera pakati panu ndipo ngati iwo apereka umboni wotsimikiza, asungeni kunyumba zawo mpaka pamene imfa iwapeza kapena mpaka pamene Mulungu alamula kwa iwo njira ina وَٱلَّذَانِ يَأۡتِيَٰنِهَا مِنكُمۡ فَـَٔاذُوهُمَاۖ فَإِن تَابَا وَأَصۡلَحَا فَأَعۡرِضُواْ عَنۡهُمَآۗ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ تَوَّابًا رَّحِيمًا ١٦Ndipo ngati anthu awiri achita chigololo pakati panu, alangeni onse awiri. Ngati iwo alapa ndi kusiya njira zawo zoipa, asiyeni. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wa chisoni chosatha إِنَّمَا ٱلتَّوۡبَةُ عَلَى ٱللَّهِ لِلَّذِينَ يَعۡمَلُونَ ٱلسُّوٓءَ بِجَهَٰلَةٍ ثُمَّ يَتُوبُونَ مِن قَرِيبٍ فَأُوْلَٰٓئِكَ يَتُوبُ ٱللَّهُ عَلَيۡهِمۡۗ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلِيمًا حَكِيمًا ١٧Mulungu amavomera kulapa kwa amene achita zoipa mosazindikira ngati alapa mwamsanga. Ndi iwo amene Mulungu adzawakhululukira ndipo Mulungu ndi wodziwa ndiponso wanzeru وَلَيۡسَتِ ٱلتَّوۡبَةُ لِلَّذِينَ يَعۡمَلُونَ ٱلسَّيِّـَٔاتِ حَتَّىٰٓ إِذَا حَضَرَ أَحَدَهُمُ ٱلۡمَوۡتُ قَالَ إِنِّي تُبۡتُ ٱلۡـَٰٔنَ وَلَا ٱلَّذِينَ يَمُوتُونَ وَهُمۡ كُفَّارٌۚ أُوْلَٰٓئِكَ أَعۡتَدۡنَا لَهُمۡ عَذَابًا أَلِيمًا ١٨Kulibe phindu kulapa kwa iwo amene amachita zinthu zoipa mpaka pamene imfa imupeza wina wa iwo ndipo ati: “Tsopano ndalapa,” kapena kwa iwo amene amafa ali osakhulupirira. Kwa iwo Ife tawakonzera chilango chowawa يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا يَحِلُّ لَكُمۡ أَن تَرِثُواْ ٱلنِّسَآءَ كَرۡهًاۖ وَلَا تَعۡضُلُوهُنَّ لِتَذۡهَبُواْ بِبَعۡضِ مَآ ءَاتَيۡتُمُوهُنَّ إِلَّآ أَن يَأۡتِينَ بِفَٰحِشَةٍ مُّبَيِّنَةٍۚ وَعَاشِرُوهُنَّ بِٱلۡمَعۡرُوفِۚ فَإِن كَرِهۡتُمُوهُنَّ فَعَسَىٰٓ أَن تَكۡرَهُواْ شَيۡـًٔا وَيَجۡعَلَ ٱللَّهُ فِيهِ خَيۡرًا كَثِيرًا ١٩oh inu anthu okhulupirira! Inu simuloledwa kulowa chokolo chokakamiza ndipo musawazunze ndi cholinga choti muwalande zina zimene mudawapatsa pokhapokha ngati achita chigololo. Ndipo khalani nawo mwa mtendere. Ngati simukuwafuna, mwina mungachide chinthu chimene Mulungu waikamo zabwino zambiri وَإِنۡ أَرَدتُّمُ ٱسۡتِبۡدَالَ زَوۡجٍ مَّكَانَ زَوۡجٍ وَءَاتَيۡتُمۡ إِحۡدَىٰهُنَّ قِنطَارًا فَلَا تَأۡخُذُواْ مِنۡهُ شَيۡـًٔاۚ أَتَأۡخُذُونَهُۥ بُهۡتَٰنًا وَإِثۡمًا مُّبِينًا ٢٠Koma ngati inu mufuna kusudzula mkazi ndi cholinga chokwatira mkazi wina ndipo mutampatsa mmodzi mwa iwo chuma chochuluka, ngati mphatso ya ukwati, musatenge chilichonse mwa chumacho. Kodi inu mungakhale mopanda chilungamo ndikuwonetsa kuchimwa poyera وَكَيۡفَ تَأۡخُذُونَهُۥ وَقَدۡ أَفۡضَىٰ بَعۡضُكُمۡ إِلَىٰ بَعۡضٍ وَأَخَذۡنَ مِنكُم مِّيثَٰقًا غَلِيظًا ٢١Kodi inu mungalande bwanji chuma pamene munali kugonera limodzi, ndipo iwo adakupatsani chipangano chotsimikizika وَلَا تَنكِحُواْ مَا نَكَحَ ءَابَآؤُكُم مِّنَ ٱلنِّسَآءِ إِلَّا مَا قَدۡ سَلَفَۚ إِنَّهُۥ كَانَ فَٰحِشَةً وَمَقۡتًا وَسَآءَ سَبِيلًا ٢٢Ndipo musakwatire mkazi amene adakwatiwapo ndi abambo anu, kupatula zimene zidatha kale. Ndithudi zinali zochititsa manyazi; zonyansa ndiponso njira yauchimo حُرِّمَتۡ عَلَيۡكُمۡ أُمَّهَٰتُكُمۡ وَبَنَاتُكُمۡ وَأَخَوَٰتُكُمۡ وَعَمَّٰتُكُمۡ وَخَٰلَٰتُكُمۡ وَبَنَاتُ ٱلۡأَخِ وَبَنَاتُ ٱلۡأُخۡتِ وَأُمَّهَٰتُكُمُ ٱلَّٰتِيٓ أَرۡضَعۡنَكُمۡ وَأَخَوَٰتُكُم مِّنَ ٱلرَّضَٰعَةِ وَأُمَّهَٰتُ نِسَآئِكُمۡ وَرَبَٰٓئِبُكُمُ ٱلَّٰتِي فِي حُجُورِكُم مِّن نِّسَآئِكُمُ ٱلَّٰتِي دَخَلۡتُم بِهِنَّ فَإِن لَّمۡ تَكُونُواْ دَخَلۡتُم بِهِنَّ فَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ وَحَلَٰٓئِلُ أَبۡنَآئِكُمُ ٱلَّذِينَ مِنۡ أَصۡلَٰبِكُمۡ وَأَن تَجۡمَعُواْ بَيۡنَ ٱلۡأُخۡتَيۡنِ إِلَّا مَا قَدۡ سَلَفَۗ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ غَفُورًا رَّحِيمًا ٢٣Inu mwaletsedwa kukwatira awa: Amayi anu, ana anu a akazi, alongo anu, azakhali anu, achemwali amayi anu, ana akazi achimwene anu, ana akazi a alongo anu, amayi amene adakuyamwitsani, akazi amene mudayamwitsidwa nawo bere limodzi, apongozi anu, ndi ana a akazi owapeza amene muli kuwasunga amene anabereka akazi amene mwawakwatira. Koma ngati simunagonepo ndi amai awo palibe choletsa kwa inu kuwakwatira atsikanawo. Kukwatiraakaziaanaanuamunaamenemudaberekainundi akazi awiri amimba imodzi nthawi imodzi ndi koletsedwa kupatula zimene zinachitika kale. Ndithudi Mulungu ndi okhululukira ndi wa chisoni chosatha

الجزء الخامس

۞ وَٱلۡمُحۡصَنَٰتُ مِنَ ٱلنِّسَآءِ إِلَّا مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُكُمۡۖ كِتَٰبَ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡۚ وَأُحِلَّ لَكُم مَّا وَرَآءَ ذَٰلِكُمۡ أَن تَبۡتَغُواْ بِأَمۡوَٰلِكُم مُّحۡصِنِينَ غَيۡرَ مُسَٰفِحِينَۚ فَمَا ٱسۡتَمۡتَعۡتُم بِهِۦ مِنۡهُنَّ فَـَٔاتُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ فَرِيضَةًۚ وَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ فِيمَا تَرَٰضَيۡتُم بِهِۦ مِنۢ بَعۡدِ ٱلۡفَرِيضَةِۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلِيمًا حَكِيمًا ٢٤Ndipo ndikoletsedwa kukwatira akazi okwatiwa kupatula amene ali m’manja mwanu ngati akapolo. Limeneli ndi lamulo la Mulungu kwa inu. Ndipo ndi kololedwa kwa inu kukwatira wina aliyense amene sanatchulidwe pamwambapa ngati inu muwapatsa mphatso ya ukwati kuchokera ku chuma chanu mu njira yabwino osati ya chiwerewere. Amene muwakwatira , apatseni mphatso yawo ya ukwati motsatira malamulo. Koma pamene mphatso itchulidwa, sizolakwika kwa inu ngati mugwirizana. Ndithudi Mulungu ndi wodziwa, ndi Waluntha وَمَن لَّمۡ يَسۡتَطِعۡ مِنكُمۡ طَوۡلًا أَن يَنكِحَ ٱلۡمُحۡصَنَٰتِ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ فَمِن مَّا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُكُم مِّن فَتَيَٰتِكُمُ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتِۚ وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِإِيمَٰنِكُمۚ بَعۡضُكُم مِّنۢ بَعۡضٍۚ فَٱنكِحُوهُنَّ بِإِذۡنِ أَهۡلِهِنَّ وَءَاتُوهُنَّ أُجُورَهُنَّ بِٱلۡمَعۡرُوفِ مُحۡصَنَٰتٍ غَيۡرَ مُسَٰفِحَٰتٍ وَلَا مُتَّخِذَٰتِ أَخۡدَانٍۚ فَإِذَآ أُحۡصِنَّ فَإِنۡ أَتَيۡنَ بِفَٰحِشَةٍ فَعَلَيۡهِنَّ نِصۡفُ مَا عَلَى ٱلۡمُحۡصَنَٰتِ مِنَ ٱلۡعَذَابِۚ ذَٰلِكَ لِمَنۡ خَشِيَ ٱلۡعَنَتَ مِنكُمۡۚ وَأَن تَصۡبِرُواْ خَيۡرٌ لَّكُمۡۗ وَٱللَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ ٢٥Ndipo ngati wina wa inu alibe mwayi woti nkukwatira mkazi wokhulupirira amene ndi mfulu, mukhoza kukwatira mwa atsikana anu wokhulupirira kuchokera kugulu la akapolo amene muli nawo, ndipo Mulungu amadziwa zonse za chikhulupiriro chanu ndipo inu ndinu amodzi. Akwatitseni ndi chilolezo cha ambuye awo ndipo muwapatse mphatso yawo ya ukwati mwa chilungamo. Iwo ayenera kudzisunga, osati a chiwerewere kapena wochita chibwenzi. Ndipo ngati akwatiwa ndipo achita chigololo, chilango chawo ndi theka la chilango chimene mfulu ya ikazi ingalandire. Ichi chikhudza iye amene aopa kupwetekeka pakati pa inu. Koma ndi kwabwino ngati inu mudziletsa ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha يُرِيدُ ٱللَّهُ لِيُبَيِّنَ لَكُمۡ وَيَهۡدِيَكُمۡ سُنَنَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِكُمۡ وَيَتُوبَ عَلَيۡكُمۡۗ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ ٢٦Mulungu afuna kuti akufotokozereni inu ndi kukutsogolerani ku njira za iwo amene adalipo inu musanadze ndi kukukhululukirani inu. Ndipo Mulungu ndi wodziwa ndi wanzeru وَٱللَّهُ يُرِيدُ أَن يَتُوبَ عَلَيۡكُمۡ وَيُرِيدُ ٱلَّذِينَ يَتَّبِعُونَ ٱلشَّهَوَٰتِ أَن تَمِيلُواْ مَيۡلًا عَظِيمًا ٢٧Mulungu afuna kukukhululukirani inu koma iwo amene amatsatira zilakolako zawo amafunisitsa mutasiya njira yoyenera يُرِيدُ ٱللَّهُ أَن يُخَفِّفَ عَنكُمۡۚ وَخُلِقَ ٱلۡإِنسَٰنُ ضَعِيفًا ٢٨Mulungu afuna kukupeputsirani malamulo ake chifukwa munthu analengedwa wofoka يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَأۡكُلُوٓاْ أَمۡوَٰلَكُم بَيۡنَكُم بِٱلۡبَٰطِلِ إِلَّآ أَن تَكُونَ تِجَٰرَةً عَن تَرَاضٍ مِّنكُمۡۚ وَلَا تَقۡتُلُوٓاْ أَنفُسَكُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ بِكُمۡ رَحِيمًا ٢٩oh inu anthu okhulupirira! Musadye chuma cha anzanu mopanda chilungamo ngakhale kuti ndi malonda amene mwagwirizana pakati panu. Ndipo musawonongane wina ndi mzake. Ndithudi Mulungu ndi wa chifundo chosatha kwa inu وَمَن يَفۡعَلۡ ذَٰلِكَ عُدۡوَٰنًا وَظُلۡمًا فَسَوۡفَ نُصۡلِيهِ نَارًاۚ وَكَانَ ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ يَسِيرًا ٣٠Ndipo aliyense amene achita izi mwamtopola kapena mwakusowa chilungamo, Ife tidzamulowetsa kumoto ndipo kutero si chinthu chovuta kwa Mulungu إِن تَجۡتَنِبُواْ كَبَآئِرَ مَا تُنۡهَوۡنَ عَنۡهُ نُكَفِّرۡ عَنكُمۡ سَيِّـَٔاتِكُمۡ وَنُدۡخِلۡكُم مُّدۡخَلًا كَرِيمًا ٣١Ngati inu mupewa machimo akuluakulu amene mukuletsedwa, Ife tidzakukhululukirani machimo anu ndipo tidzakulowetsani kukhomo lolemekezeka وَلَا تَتَمَنَّوۡاْ مَا فَضَّلَ ٱللَّهُ بِهِۦ بَعۡضَكُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٍۚ لِّلرِّجَالِ نَصِيبٌ مِّمَّا ٱكۡتَسَبُواْۖ وَلِلنِّسَآءِ نَصِيبٌ مِّمَّا ٱكۡتَسَبۡنَۚ وَسۡـَٔلُواْ ٱللَّهَ مِن فَضۡلِهِۦٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمًا ٣٢Ndipo musasirire zokoma zimene Mulungu wawapatsa ena a inu kuposa anzawo. Kwa amuna kuli gawo kuzimene amachita, nawonso akazi ali ndi gawo muzimene amachita ndipo mupempheni Mulungu kuti akupatseni zabwino zake. Ndithudi Mulungu amadziwa chinthu chilichonse وَلِكُلٍّ جَعَلۡنَا مَوَٰلِيَ مِمَّا تَرَكَ ٱلۡوَٰلِدَانِ وَٱلۡأَقۡرَبُونَۚ وَٱلَّذِينَ عَقَدَتۡ أَيۡمَٰنُكُمۡ فَـَٔاتُوهُمۡ نَصِيبَهُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ شَهِيدًا ٣٣Ndipo kwa aliyense tamuikira abale olandira chuma chimene chasiyidwa ndi makolo ndi abale. Ndipo iwo amene mwachita nawo chipangano, apatseni gawo lawo nawonso kuti alandire. Ndithudi Mulungu ndi mboni pa zinthu zonse ٱلرِّجَالُ قَوَّٰمُونَ عَلَى ٱلنِّسَآءِ بِمَا فَضَّلَ ٱللَّهُ بَعۡضَهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٍ وَبِمَآ أَنفَقُواْ مِنۡ أَمۡوَٰلِهِمۡۚ فَٱلصَّٰلِحَٰتُ قَٰنِتَٰتٌ حَٰفِظَٰتٌ لِّلۡغَيۡبِ بِمَا حَفِظَ ٱللَّهُۚ وَٱلَّٰتِي تَخَافُونَ نُشُوزَهُنَّ فَعِظُوهُنَّ وَٱهۡجُرُوهُنَّ فِي ٱلۡمَضَاجِعِ وَٱضۡرِبُوهُنَّۖ فَإِنۡ أَطَعۡنَكُمۡ فَلَا تَبۡغُواْ عَلَيۡهِنَّ سَبِيلًاۗ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلِيًّا كَبِيرًا ٣٤Anthu amuna ndi atetezi ndi osamala anthu akazi chifukwa Mulungu wawalemekeza ena kuposa anzawo ndiponso chifukwa cha chuma chawo chimene amagwiritsa ntchito. Motero akazi ochita zabwino ndipo amene amamvera, amasunga pamene amuna awo palibe, ndi zimene Mulungu awalamulira kuti azisunge. Ndipo akazi amene mukuona kuti samvera achenjezeni ndipo ngati iwo sasintha asiyeni agone pa okha ndipo ngati sasinthabe amenyeni. Koma ngati iwo akumverani, musawafunire njira yachabe. Ndithudi Mulungu ndi wapamwamba ndi wamkulu وَإِنۡ خِفۡتُمۡ شِقَاقَ بَيۡنِهِمَا فَٱبۡعَثُواْ حَكَمًا مِّنۡ أَهۡلِهِۦ وَحَكَمًا مِّنۡ أَهۡلِهَآ إِن يُرِيدَآ إِصۡلَٰحًا يُوَفِّقِ ٱللَّهُ بَيۡنَهُمَآۗ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلِيمًا خَبِيرًا ٣٥Ndipo ngati inu muopa kuti asiyana, sankhani nkhoswe kuchokera kwa m’bale wa mwamuna ndiponso nkhoswe kuchokera kwa m’bale wa mkazi ngati iwo akufuna kuyanjanitsidwa, ndipo Mulungu adzawayanjanitsa pakati pawo. Ndithudi Mulungu ndi wodziwa ndi wozindikira ۞ وَٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ وَلَا تُشۡرِكُواْ بِهِۦ شَيۡـًٔاۖ وَبِٱلۡوَٰلِدَيۡنِ إِحۡسَٰنًا وَبِذِي ٱلۡقُرۡبَىٰ وَٱلۡيَتَٰمَىٰ وَٱلۡمَسَٰكِينِ وَٱلۡجَارِ ذِي ٱلۡقُرۡبَىٰ وَٱلۡجَارِ ٱلۡجُنُبِ وَٱلصَّاحِبِ بِٱلۡجَنۢبِ وَٱبۡنِ ٱلسَّبِيلِ وَمَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُكُمۡۗ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُحِبُّ مَن كَانَ مُخۡتَالًا فَخُورًا ٣٦Pembedzani Mulungu ndipo musamuphatikize Iye ndi china chilichonse ndipo chitani zabwino kwa makolo anu ndi achibale, kwa a masiye ndi kwa osauka, ndi kwa anzanu amene muli nawo pafupi kapena kutali ndi anzanu okhala nawo pafupi, ndi kwa a paulendo ndi kwa akapolo anu. Ndithudi Mulungu sakonda anthu a mtudzu ndi odzikundikira ٱلَّذِينَ يَبۡخَلُونَ وَيَأۡمُرُونَ ٱلنَّاسَ بِٱلۡبُخۡلِ وَيَكۡتُمُونَ مَآ ءَاتَىٰهُمُ ٱللَّهُ مِن فَضۡلِهِۦۗ وَأَعۡتَدۡنَا لِلۡكَٰفِرِينَ عَذَابًا مُّهِينًا ٣٧Iwo amene ndi oumira ndipo amauza anzawo kuti akhalenso oumira, amene amabisa chuma chimene Mulungu adawapatsa mwachifundo chake. Ndipo Ife tawakonzera anthu osakhulupirira chilango chochititsa manyazi وَٱلَّذِينَ يُنفِقُونَ أَمۡوَٰلَهُمۡ رِئَآءَ ٱلنَّاسِ وَلَا يُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَلَا بِٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِۗ وَمَن يَكُنِ ٱلشَّيۡطَٰنُ لَهُۥ قَرِينًا فَسَآءَ قَرِينًا ٣٨Ndi iwo amene amaononga chuma chawo modzionetsera kwa anthu, ndipo sakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku la chiweruzo; ndipo aliyense amene asankha Satana kukhala bwenzi lake, wasankha bwenzi loopsya وَمَاذَا عَلَيۡهِمۡ لَوۡ ءَامَنُواْ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِ وَأَنفَقُواْ مِمَّا رَزَقَهُمُ ٱللَّهُۚ وَكَانَ ٱللَّهُ بِهِمۡ عَلِيمًا ٣٩Kodi iwo akadataya chiyani ngati akadakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku la chiweruzo ndi kupereka muzinthu zimene Mulungu adawapatsa iwo kuti ziziwathandiza? Mulungu amawadziwa onse إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَظۡلِمُ مِثۡقَالَ ذَرَّةٍۖ وَإِن تَكُ حَسَنَةً يُضَٰعِفۡهَا وَيُؤۡتِ مِن لَّدُنۡهُ أَجۡرًا عَظِيمًا ٤٠Ndithudi! Mulungu sapondereza malipiro ngakhale a kanthu kochepa, ndipo ngati muli zabwino Iye adzakaonjezera malipiro ake ndipo amapereka kuchokera kwa Iye malipiro ochuluka فَكَيۡفَ إِذَا جِئۡنَا مِن كُلِّ أُمَّةِۭ بِشَهِيدٍ وَجِئۡنَا بِكَ عَلَىٰ هَٰٓؤُلَآءِ شَهِيدًا ٤١Kodi zidzakhala bwanji pamene tidzabweretsa mboni kuchokera ku anthu a mtundu uliwonse ndipo tikubweretsa iwe kuti uzakhale mboni yowatsutsa يَوۡمَئِذٍ يَوَدُّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَعَصَوُاْ ٱلرَّسُولَ لَوۡ تُسَوَّىٰ بِهِمُ ٱلۡأَرۡضُ وَلَا يَكۡتُمُونَ ٱللَّهَ حَدِيثًا ٤٢Patsikulo onse amene sadakhulupilire ndipo sanamvere Mtumwi adzafunitsitsa akadaundiridwa m’nthaka koma iwo sadzabisa china chilichonse kwa Mulungu يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَقۡرَبُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَأَنتُمۡ سُكَٰرَىٰ حَتَّىٰ تَعۡلَمُواْ مَا تَقُولُونَ وَلَا جُنُبًا إِلَّا عَابِرِي سَبِيلٍ حَتَّىٰ تَغۡتَسِلُواْۚ وَإِن كُنتُم مَّرۡضَىٰٓ أَوۡ عَلَىٰ سَفَرٍ أَوۡ جَآءَ أَحَدٌ مِّنكُم مِّنَ ٱلۡغَآئِطِ أَوۡ لَٰمَسۡتُمُ ٱلنِّسَآءَ فَلَمۡ تَجِدُواْ مَآءً فَتَيَمَّمُواْ صَعِيدًا طَيِّبًا فَٱمۡسَحُواْ بِوُجُوهِكُمۡ وَأَيۡدِيكُمۡۗ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَفُوًّا غَفُورًا ٤٣oh inu anthu okhulupirira! Musayandikire mapemphero pamene muli oledzera mpaka pamene mudziwa tanthauzo la zimene muli nkunena ndiponso pamene mwakhala malo ndi a kunyumba kwanu ndipo simunasambe kupatula pamene muli pa ulendo. Ndipo ngati muli nkudwala kapena muli pa ulendo kapena mmodzi mwa inu wachokera ku chimbudzi kapena mwagona limodzi ndi akazi anu, ndipo simudapeze madzi, tapani dothi labwino ndipo mupukute nkhope ndi manja anu. Ndithudi Mulungu ndi wa chifundo ndi okhululukira أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ أُوتُواْ نَصِيبًا مِّنَ ٱلۡكِتَٰبِ يَشۡتَرُونَ ٱلضَّلَٰلَةَ وَيُرِيدُونَ أَن تَضِلُّواْ ٱلسَّبِيلَ ٤٤Kodi iwe siunawaone iwo amene adapatsidwa gawo la Buku ali kusochera ndipo akufuna kuti iwe usochere ku njira yabwino وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِأَعۡدَآئِكُمۡۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ وَلِيًّا وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ نَصِيرًا ٤٥Mulungu amawadziwa bwino adani anu ndipo Mulungu ndi wokwana kukhala Mtetezi ndipo ndi wokwana kukhala Mthandizi مِّنَ ٱلَّذِينَ هَادُواْ يُحَرِّفُونَ ٱلۡكَلِمَ عَن مَّوَاضِعِهِۦ وَيَقُولُونَ سَمِعۡنَا وَعَصَيۡنَا وَٱسۡمَعۡ غَيۡرَ مُسۡمَعٍ وَرَٰعِنَا لَيَّۢا بِأَلۡسِنَتِهِمۡ وَطَعۡنًا فِي ٱلدِّينِۚ وَلَوۡ أَنَّهُمۡ قَالُواْ سَمِعۡنَا وَأَطَعۡنَا وَٱسۡمَعۡ وَٱنظُرۡنَا لَكَانَ خَيۡرًا لَّهُمۡ وَأَقۡوَمَ وَلَٰكِن لَّعَنَهُمُ ٱللَّهُ بِكُفۡرِهِمۡ فَلَا يُؤۡمِنُونَ إِلَّا قَلِيلًا ٤٦Pakati pa Ayuda pali ena amene amasinthitsa mawu m’malo mwake ndipo amati: “Ife tamva mau ako koma sitikumvera ndipo imva koma usamve chili chonse” ndipo amati: ‘Chenjera, timvere ife ndipo ife tidzakumvera’ ali kupotoza malirime awo ndi cholinga chotukwana chipembedzo. Koma iwo akadati: “Tamva ndipo tatsatira; tiphunzitse ife”; zikadawakhalira bwino kwambiri, koma Mulungu wawatemberera iwo chifukwa chosakhulupirira kwawo motero iwo sakhulupilira koma pang’ono يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ ءَامِنُواْ بِمَا نَزَّلۡنَا مُصَدِّقًا لِّمَا مَعَكُم مِّن قَبۡلِ أَن نَّطۡمِسَ وُجُوهًا فَنَرُدَّهَا عَلَىٰٓ أَدۡبَارِهَآ أَوۡ نَلۡعَنَهُمۡ كَمَا لَعَنَّآ أَصۡحَٰبَ ٱلسَّبۡتِۚ وَكَانَ أَمۡرُ ٱللَّهِ مَفۡعُولًا ٤٧oh inu anthu amene mudapatsidwa Buku! Khulupirirani zimene tavumbulutsa zimene zitsimikizira Maua Mulunguamenemulinawo, tisadatembenuzenkhope ndikuzibwezera kumbuyo kwake kapena kuwatemberera monga mmene tidawatemberera anthu ophwanya tsiku la Sabata. Ndipo lamulo la Mulungu limatsatidwa ndipo limakwaniritsidwa إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَغۡفِرُ أَن يُشۡرَكَ بِهِۦ وَيَغۡفِرُ مَا دُونَ ذَٰلِكَ لِمَن يَشَآءُۚ وَمَن يُشۡرِكۡ بِٱللَّهِ فَقَدِ ٱفۡتَرَىٰٓ إِثۡمًا عَظِيمًا ٤٨Ndithudi Mulungu sakhululukira kuti milungu izipembedzedwa yowonjezera pa Iye koma Iye amakhululukira aliyense amene wamufuna pa machimo ena. Ndipo aliyense amene amapembedza milungu ina yowonjezera pa Iye, iye, ndithudi, wapeka bodza loopsya أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ يُزَكُّونَ أَنفُسَهُمۚ بَلِ ٱللَّهُ يُزَكِّي مَن يَشَآءُ وَلَا يُظۡلَمُونَ فَتِيلًا ٤٩Kodi simunaone amene amadziyeretsa okha? Iyayi! Koma Mulungu amayeretsa aliyense amene Iye wamufuna ndipo iwo sadzaponderezedwa ngakhale ndi pang’ono pomwe ٱنظُرۡ كَيۡفَ يَفۡتَرُونَ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَۖ وَكَفَىٰ بِهِۦٓ إِثۡمًا مُّبِينًا ٥٠Taona mmene iwo amapekera bodza lokhudza Mulungu ndipo zimenezi zikukwanira kukhala tchimo looneka أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ أُوتُواْ نَصِيبًا مِّنَ ٱلۡكِتَٰبِ يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡجِبۡتِ وَٱلطَّٰغُوتِ وَيَقُولُونَ لِلَّذِينَ كَفَرُواْ هَٰٓؤُلَآءِ أَهۡدَىٰ مِنَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ سَبِيلًا ٥١Kodi siunaone iwo amene adapatsidwa gawo la Buku la Mulungu? Iwo amakhulupirira mafano ndi milungu yabodza ndipo amawauza osakhulupilira kuti ndi otsogozedwa bwino kuposa anthu okhulupirira أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ لَعَنَهُمُ ٱللَّهُۖ وَمَن يَلۡعَنِ ٱللَّهُ فَلَن تَجِدَ لَهُۥ نَصِيرًا ٥٢Amenewa ndiwo anthu amene Mulungu wawatemberera ndipo aliyense amene atembereredwa ndi Mulungu iwe siungamupezere womuthandiza أَمۡ لَهُمۡ نَصِيبٌ مِّنَ ٱلۡمُلۡكِ فَإِذًا لَّا يُؤۡتُونَ ٱلنَّاسَ نَقِيرًا ٥٣Kodi kapena iwo ali ndi gawo mu Ufumu? Zikadatero, iwo sakadawapatsa anthu ngakhale kanthu kakang’ono أَمۡ يَحۡسُدُونَ ٱلنَّاسَ عَلَىٰ مَآ ءَاتَىٰهُمُ ٱللَّهُ مِن فَضۡلِهِۦۖ فَقَدۡ ءَاتَيۡنَآ ءَالَ إِبۡرَٰهِيمَ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡحِكۡمَةَ وَءَاتَيۡنَٰهُم مُّلۡكًا عَظِيمًا ٥٤Kodi kapena iwo amachitira kaduka anthu mu zinthu zabwino zimene Mulungu wawapatsa? Ife tidawapatsa ana a Abrahamu Buku ndi luntha ndipo tidawapatsa Ufumu waukulu فَمِنۡهُم مَّنۡ ءَامَنَ بِهِۦ وَمِنۡهُم مَّن صَدَّ عَنۡهُۚ وَكَفَىٰ بِجَهَنَّمَ سَعِيرًا ٥٥Ena mwa iwo adakhulupirira iye koma ena a iwo anayang’ana kumbali ndipo Moto ukukwanira kukhala chilango chawo إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِنَا سَوۡفَ نُصۡلِيهِمۡ نَارًا كُلَّمَا نَضِجَتۡ جُلُودُهُم بَدَّلۡنَٰهُمۡ جُلُودًا غَيۡرَهَا لِيَذُوقُواْ ٱلۡعَذَابَۗ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَزِيزًا حَكِيمًا ٥٦Ndithudi iwo amene adakana zizindikiro zathu tidzawaotcha ku moto. Nthawi zonse pamene makungu awo azidzapsya, Ife tidzawapatsa makungu ena kuti iwo alawe chilango. Ndithudi Mulungu ndi wamphamvu nthawi zonse ndi Wanzeru وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ سَنُدۡخِلُهُمۡ جَنَّٰتٍ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدًاۖ لَّهُمۡ فِيهَآ أَزۡوَٰجٌ مُّطَهَّرَةٌۖ وَنُدۡخِلُهُمۡ ظِلًّا ظَلِيلًا ٥٧Koma iwo amene amakhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, Ife tidzawalowetsa m’minda yothiriridwa ndi mitsinje yoyenda pansi pake, ndipo adzakhalako mpaka kalekale. Ndipo kumeneko adzakhala ndi akazi oyera ndipo Ife tidzawalowetsa ku mthunzi wabwino kwambiri ۞ إِنَّ ٱللَّهَ يَأۡمُرُكُمۡ أَن تُؤَدُّواْ ٱلۡأَمَٰنَٰتِ إِلَىٰٓ أَهۡلِهَا وَإِذَا حَكَمۡتُم بَيۡنَ ٱلنَّاسِ أَن تَحۡكُمُواْ بِٱلۡعَدۡلِۚ إِنَّ ٱللَّهَ نِعِمَّا يَعِظُكُم بِهِۦٓۗ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ سَمِيعَۢا بَصِيرًا ٥٨Ndithudi Mulungu ali kukulamulirani kuti mubwezere katundu amene mwasunga kwa eni ake ndipo ngati muweruza pakati pa anthu, weruzani mwachilungamo. Ndithudi chilangizo chimene Mulungu akukulangizani ndi chabwino kwambiri. Ndithudi Mulungu amamva nthawi zonse ndipo amaona zinthu zonse يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَطِيعُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُواْ ٱلرَّسُولَ وَأُوْلِي ٱلۡأَمۡرِ مِنكُمۡۖ فَإِن تَنَٰزَعۡتُمۡ فِي شَيۡءٍ فَرُدُّوهُ إِلَى ٱللَّهِ وَٱلرَّسُولِ إِن كُنتُمۡ تُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِۚ ذَٰلِكَ خَيۡرٌ وَأَحۡسَنُ تَأۡوِيلًا ٥٩oh inu anthu okhulupirira! Mverani Mulungu ndipo mverani Mtumwi wake ndiponso iwo amene ali ndi udindo pakati panu. Ndipo ngati mutsutsana pa chinthu china chilichonse, chiperekeni icho kwa Mulungu ndi Mtumwi wake ngati inu mumakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza. Zimenezi zidzakhala zabwino ndi zolungama pomaliza أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ يَزۡعُمُونَ أَنَّهُمۡ ءَامَنُواْ بِمَآ أُنزِلَ إِلَيۡكَ وَمَآ أُنزِلَ مِن قَبۡلِكَ يُرِيدُونَ أَن يَتَحَاكَمُوٓاْ إِلَى ٱلطَّٰغُوتِ وَقَدۡ أُمِرُوٓاْ أَن يَكۡفُرُواْ بِهِۦۖ وَيُرِيدُ ٱلشَّيۡطَٰنُ أَن يُضِلَّهُمۡ ضَلَٰلَۢا بَعِيدًا ٦٠Kodi iwe wawaona amene amanena kuti amakhulupirira mu zimene zavumbulitsidwa kwa iwe ndi kwa Atumwi ena amene adalipo iwe usanadze ndipo iwo amafunafuna chiweruzo cha oweruza abodza, pamene iwo adalamulidwa kuti awakane iwo? Koma chofuna cha Satana ndi kuwasokeretsa iwo ku njira yoyenera وَإِذَا قِيلَ لَهُمۡ تَعَالَوۡاْ إِلَىٰ مَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ وَإِلَى ٱلرَّسُولِ رَأَيۡتَ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ يَصُدُّونَ عَنكَ صُدُودًا ٦١Ndipo pamene auzidwa “Bwerani ku zimene Mulungu wavumbulutsa ndiponso kwa Mtumwi,” iwe umaona anthu a chinyengo ali kukukana iwe mwamwano فَكَيۡفَ إِذَآ أَصَٰبَتۡهُم مُّصِيبَةُۢ بِمَا قَدَّمَتۡ أَيۡدِيهِمۡ ثُمَّ جَآءُوكَ يَحۡلِفُونَ بِٱللَّهِ إِنۡ أَرَدۡنَآ إِلَّآ إِحۡسَٰنًا وَتَوۡفِيقًا ٦٢Kodi bwanji, ngati vuto ligwa pa iwo chifukwa cha ntchito zimene adatsogoza manja awo, amadza kwa iwe, kulumbira m’dzina la Mulungu kuti: “Ife sitifuna china chilichonse koma zabwino ndi chigwirizano!” أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ يَعۡلَمُ ٱللَّهُ مَا فِي قُلُوبِهِمۡ فَأَعۡرِضۡ عَنۡهُمۡ وَعِظۡهُمۡ وَقُل لَّهُمۡ فِيٓ أَنفُسِهِمۡ قَوۡلَۢا بَلِيغًا ٦٣Awa ndiwo amene Mulungu amadziwa zimene zili m’mitima mwawo. Motero asiye koma uwachenjeze ndipo uwauze mawu ogwira mtima وَمَآ أَرۡسَلۡنَا مِن رَّسُولٍ إِلَّا لِيُطَاعَ بِإِذۡنِ ٱللَّهِۚ وَلَوۡ أَنَّهُمۡ إِذ ظَّلَمُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ جَآءُوكَ فَٱسۡتَغۡفَرُواْ ٱللَّهَ وَٱسۡتَغۡفَرَ لَهُمُ ٱلرَّسُولُ لَوَجَدُواْ ٱللَّهَ تَوَّابًا رَّحِيمًا ٦٤IfesitidatumizeMtumwialiyense,komakutiatsatiridwe mwa lamulo la Mulungu. Ngati iwo adadzilakwitsa, akanadza kwa iwe kupempha chikhululukiro cha Mulungu ndipo Mtumwi akadawapemphera chikhululukiro cha Mulungu. Iwo akadamupeza Iye wokhululuka ndi wa chisoni فَلَا وَرَبِّكَ لَا يُؤۡمِنُونَ حَتَّىٰ يُحَكِّمُوكَ فِيمَا شَجَرَ بَيۡنَهُمۡ ثُمَّ لَا يَجِدُواْ فِيٓ أَنفُسِهِمۡ حَرَجًا مِّمَّا قَضَيۡتَ وَيُسَلِّمُواْ تَسۡلِيمًا ٦٥Koma iyayi, pali Ambuye wako, iwo sadzakhala okhulupirira mpaka pamene akusankha iwe kukhala oweruza pa mikangano ya pakati pawo ndipo satsutsa chiweruzo chako, ndipo achivomeleza kwathunthu وَلَوۡ أَنَّا كَتَبۡنَا عَلَيۡهِمۡ أَنِ ٱقۡتُلُوٓاْ أَنفُسَكُمۡ أَوِ ٱخۡرُجُواْ مِن دِيَٰرِكُم مَّا فَعَلُوهُ إِلَّا قَلِيلٌ مِّنۡهُمۡۖ وَلَوۡ أَنَّهُمۡ فَعَلُواْ مَا يُوعَظُونَ بِهِۦ لَكَانَ خَيۡرًا لَّهُمۡ وَأَشَدَّ تَثۡبِيتًا ٦٦Zikadakhala kuti Ife tidawalamulira kuti: “Mudziphe nokha kapena tulukani m’nyumba zanu,” sakadachita kupatula owerengeka okha. Koma ngati iwo akadachita zimene auzidwa zikadakhala bwino kwa iwo, ndipo zikadaonjezera chikhulupiriro وَإِذًا لَّأٓتَيۡنَٰهُم مِّن لَّدُنَّآ أَجۡرًا عَظِيمًا ٦٧Ndipo ndithudi Ife tikadawapatsa iwo, kuchokera kwa Ife, dipo lalikulu وَلَهَدَيۡنَٰهُمۡ صِرَٰطًا مُّسۡتَقِيمًا ٦٨Ndithudi Ife tikadawatsogolera ku njira yoyenera وَمَن يُطِعِ ٱللَّهَ وَٱلرَّسُولَ فَأُوْلَٰٓئِكَ مَعَ ٱلَّذِينَ أَنۡعَمَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِم مِّنَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ وَٱلصِّدِّيقِينَ وَٱلشُّهَدَآءِ وَٱلصَّٰلِحِينَۚ وَحَسُنَ أُوْلَٰٓئِكَ رَفِيقًا ٦٩Ndipo aliyense amene amvera Mulungu ndi Mtumwi wake, ameneyo ndi amene ali pamodzi ndi anthu amene Mulungu wawadalitsa kuchokera ku gulu la Atumwi, anthu a chilungamo, anthu ofera ku nkhondo m’njira ya Mulungu ndi anthu ochita zabwino. Ati bwanji kukoma kukhala mgulu lotere ذَٰلِكَ ٱلۡفَضۡلُ مِنَ ٱللَّهِۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ عَلِيمًا ٧٠Ichi ndi chisomo chochokera kwa Mulungu, ndipo Mulungu ndi wokwanira kukhala wodziwa chili chonse يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ خُذُواْ حِذۡرَكُمۡ فَٱنفِرُواْ ثُبَاتٍ أَوِ ٱنفِرُواْ جَمِيعًا ٧١Oh inu anthu okhulupirira! Khalani okonzeka ndipo yendani m’magulu m’magulu kapena pa gulu limodzi lokha وَإِنَّ مِنكُمۡ لَمَن لَّيُبَطِّئَنَّ فَإِنۡ أَصَٰبَتۡكُم مُّصِيبَةٌ قَالَ قَدۡ أَنۡعَمَ ٱللَّهُ عَلَيَّ إِذۡ لَمۡ أَكُن مَّعَهُمۡ شَهِيدًا ٧٢Alipo wina pakati panu amene adzatsalira m’mbuyo. Amene ngati choipa chioneka kwa inu amanena kuti: “Ndithudi Mulungu wandionetsera ine chifundo chifukwa sindinali nawo.” وَلَئِنۡ أَصَٰبَكُمۡ فَضۡلٌ مِّنَ ٱللَّهِ لَيَقُولَنَّ كَأَن لَّمۡ تَكُنۢ بَيۡنَكُمۡ وَبَيۡنَهُۥ مَوَدَّةٌ يَٰلَيۡتَنِي كُنتُ مَعَهُمۡ فَأَفُوزَ فَوۡزًا عَظِيمًا ٧٣Koma ngati mtendere wochokera kwa Mulungu ukupezani, ndithudi iye adzanena ngati kuti padalibe ubwenzi pakati pa iye ndi inu ndipo iwo adzati: “Ndikadakhala nawo limodzi, ndithudi ndikadakhala ndi mwayi waukulu.” ۞ فَلۡيُقَٰتِلۡ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ ٱلَّذِينَ يَشۡرُونَ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا بِٱلۡأٓخِرَةِۚ وَمَن يُقَٰتِلۡ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ فَيُقۡتَلۡ أَوۡ يَغۡلِبۡ فَسَوۡفَ نُؤۡتِيهِ أَجۡرًا عَظِيمًا ٧٤Kotero alekeni iwo amene amagulitsa moyo uno ndi moyo umene uli nkudza kuti amenye nkhondo mu njira ya Mulungu. Aliyense amene amenya nkhondo m’njira ya Mulungu ndipo aphedwa kapena apambana, Ife tidzamupatsa dipo lalikulu وَمَا لَكُمۡ لَا تُقَٰتِلُونَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ وَٱلۡمُسۡتَضۡعَفِينَ مِنَ ٱلرِّجَالِ وَٱلنِّسَآءِ وَٱلۡوِلۡدَٰنِ ٱلَّذِينَ يَقُولُونَ رَبَّنَآ أَخۡرِجۡنَا مِنۡ هَٰذِهِ ٱلۡقَرۡيَةِ ٱلظَّالِمِ أَهۡلُهَا وَٱجۡعَل لَّنَا مِن لَّدُنكَ وَلِيًّا وَٱجۡعَل لَّنَا مِن لَّدُنكَ نَصِيرًا ٧٥Kodi ndi chifukwa chiyani inu simukumenya nkhondo m’njira ya Mulungu pamene anthu ofoka mwa anthu amuna, akazi ndi ana amati: “Ambuye wathu! Tipulumutseni kuchoka kumzinda uwu wa anthu wochita zoipa ndipo tidzutsireni mtetezi wochokera kwa Inu amene adzatithandiza ife.” ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ يُقَٰتِلُونَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِۖ وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يُقَٰتِلُونَ فِي سَبِيلِ ٱلطَّٰغُوتِ فَقَٰتِلُوٓاْ أَوۡلِيَآءَ ٱلشَّيۡطَٰنِۖ إِنَّ كَيۡدَ ٱلشَّيۡطَٰنِ كَانَ ضَعِيفًا ٧٦Iwo amene akhulupirira amamenya nkhondo m’njira ya Mulungu koma amene sakhulupilira amamenya mu njira ya Satana. Kotero inu menyanani ndi abwenzi a Satana, ndithudi chikonzero cha Satana ndi chopanda mphamvu أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ قِيلَ لَهُمۡ كُفُّوٓاْ أَيۡدِيَكُمۡ وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَ فَلَمَّا كُتِبَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡقِتَالُ إِذَا فَرِيقٌ مِّنۡهُمۡ يَخۡشَوۡنَ ٱلنَّاسَ كَخَشۡيَةِ ٱللَّهِ أَوۡ أَشَدَّ خَشۡيَةًۚ وَقَالُواْ رَبَّنَا لِمَ كَتَبۡتَ عَلَيۡنَا ٱلۡقِتَالَ لَوۡلَآ أَخَّرۡتَنَآ إِلَىٰٓ أَجَلٍ قَرِيبٍۗ قُلۡ مَتَٰعُ ٱلدُّنۡيَا قَلِيلٌ وَٱلۡأٓخِرَةُ خَيۡرٌ لِّمَنِ ٱتَّقَىٰ وَلَا تُظۡلَمُونَ فَتِيلًا ٧٧Kodi siunaone anthu amene amauzidwa kuti: “Musamenye nkhondo, pempherani mwandondomeko ndipo perekani msonkho wothandizira anthu osauka,” koma pamene iwo adalamulidwa kuti amenye nkhondo, taona; enaaiwoamaopaanthumongamomweamamuopera Mulungu kapenanso kuposa apa. Iwo amati: “Ambuye wathu! Kodi ndi chifukwa chiyani mwatilamula kuti timenye nkhondo? Kodi simungatipatse nthawi yopumula ngakhale yochepa” Nena: “Chisangalalo cha moyo uno ndi chochepa kwambiri. Moyo umene uli nkudza ndi wabwino kwambiri kwa iye amene amaopa Mulungu ndipo inu simudzaponderezedwa ndi pang’onong’ono pomwe.” أَيۡنَمَا تَكُونُواْ يُدۡرِككُّمُ ٱلۡمَوۡتُ وَلَوۡ كُنتُمۡ فِي بُرُوجٍ مُّشَيَّدَةٍۗ وَإِن تُصِبۡهُمۡ حَسَنَةٌ يَقُولُواْ هَٰذِهِۦ مِنۡ عِندِ ٱللَّهِۖ وَإِن تُصِبۡهُمۡ سَيِّئَةٌ يَقُولُواْ هَٰذِهِۦ مِنۡ عِندِكَۚ قُلۡ كُلٌّ مِّنۡ عِندِ ٱللَّهِۖ فَمَالِ هَٰٓؤُلَآءِ ٱلۡقَوۡمِ لَا يَكَادُونَ يَفۡقَهُونَ حَدِيثًا ٧٨Pali ponse pomwe mungakhale, imfa idzakupezani, ngakhale inu mutadzitsekera mkati mwa nsanja zolimba. Ndipo ngati zabwino ziwapeza, iwo amati: “Izi zachokera kwa Mulungu” koma ngati choipa chiwagwera, iwo amati: “Ichi ndi chochokera kwa iwe.” Nena: “Zinthu zonse zimachokera kwa Mulungu.” Kodi ndi chiani chawapeza anthu awa kuti sangathe kuzindikira china chiri chonse مَّآ أَصَابَكَ مِنۡ حَسَنَةٍ فَمِنَ ٱللَّهِۖ وَمَآ أَصَابَكَ مِن سَيِّئَةٍ فَمِن نَّفۡسِكَۚ وَأَرۡسَلۡنَٰكَ لِلنَّاسِ رَسُولًاۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ شَهِيدًا ٧٩Chilichonse chabwino chimene chidza pa iwe ndi chochokera kwa Mulungu, ndipo choipa chimene chikupeza ndi chochokera kwa iwe mwini. Ndipo Ife takutumiza iwe ngati Mtumwi kwa anthu onse. Ndipo Mulungu akwana kukhala mboni مَّن يُطِعِ ٱلرَّسُولَ فَقَدۡ أَطَاعَ ٱللَّهَۖ وَمَن تَوَلَّىٰ فَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ عَلَيۡهِمۡ حَفِيظًا ٨٠Aliyense amene amvera Mtumwi ndithudi amvera Mulungu ndipo iye amene safuna kukumvera iwe, Ife sitidakutumize kuti ukhale wowayang’anira ayi وَيَقُولُونَ طَاعَةٌ فَإِذَا بَرَزُواْ مِنۡ عِندِكَ بَيَّتَ طَآئِفَةٌ مِّنۡهُمۡ غَيۡرَ ٱلَّذِي تَقُولُۖ وَٱللَّهُ يَكۡتُبُ مَا يُبَيِّتُونَۖ فَأَعۡرِضۡ عَنۡهُمۡ وَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱللَّهِۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ وَكِيلًا ٨١Iwo amati: “Ife ndife omvera” koma iwo akangochoka kwa iwe, ambiri a iwo amachita chiwembu usiku pochita zinthu zimene siukunena. Koma Mulungu amalemba ziwembu zawo zonse zomwe amachita usiku. Kotero aleke okha ndipo ika chikhulupiliro chako mwa Mulungu. Ndipo Mulungu ndi okwana kukhala Mtetezi أَفَلَا يَتَدَبَّرُونَ ٱلۡقُرۡءَانَۚ وَلَوۡ كَانَ مِنۡ عِندِ غَيۡرِ ٱللَّهِ لَوَجَدُواْ فِيهِ ٱخۡتِلَٰفًا كَثِيرًا ٨٢Kodi iwo salingalira za Korani? Ilo likadakhala kuti silinachokere kwa Mulungu, iwo akadapeza mu ilo kusemphana kwambiri وَإِذَا جَآءَهُمۡ أَمۡرٌ مِّنَ ٱلۡأَمۡنِ أَوِ ٱلۡخَوۡفِ أَذَاعُواْ بِهِۦۖ وَلَوۡ رَدُّوهُ إِلَى ٱلرَّسُولِ وَإِلَىٰٓ أُوْلِي ٱلۡأَمۡرِ مِنۡهُمۡ لَعَلِمَهُ ٱلَّذِينَ يَسۡتَنۢبِطُونَهُۥ مِنۡهُمۡۗ وَلَوۡلَا فَضۡلُ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ وَرَحۡمَتُهُۥ لَٱتَّبَعۡتُمُ ٱلشَّيۡطَٰنَ إِلَّا قَلِيلًا ٨٣Pamene iwo amva nkhani iliyonse ya mtendere kapena yochititsa mantha, iwo amaiulutsa koma iwo akanaipereka kwa Mtumwi kapena kwa amene ali ndi udindo pakati pawo kapena anthu amene amafufuza bwino nkhani, akadadziwa. Ndipo pakadapanda chisomo ndi chisoni cha Mulungu pa inu, inu mukanatsatira Satana kupatula anthu ochepa okha فَقَٰتِلۡ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ لَا تُكَلَّفُ إِلَّا نَفۡسَكَۚ وَحَرِّضِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَۖ عَسَى ٱللَّهُ أَن يَكُفَّ بَأۡسَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْۚ وَٱللَّهُ أَشَدُّ بَأۡسًا وَأَشَدُّ تَنكِيلًا ٨٤Motero menya nkhondo mu njira ya Mulungu, iwe siudzafunsidwa za munthu wina ayi koma za iwe wekha ndipo alimbikitse okhulupirira kuti mwina Mulungu adzagonjetsa anthu osakhulupirira. Mulungu ndi wamphamvu kwambiri ndi Waukali polanga مَّن يَشۡفَعۡ شَفَٰعَةً حَسَنَةً يَكُن لَّهُۥ نَصِيبٌ مِّنۡهَاۖ وَمَن يَشۡفَعۡ شَفَٰعَةً سَيِّئَةً يَكُن لَّهُۥ كِفۡلٌ مِّنۡهَاۗ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ مُّقِيتًا ٨٥Aliyense amene amathandiza kuchita ntchito zabwino adzalandira gawo lake la ntchitoyo, ndipo aliyense amene amathandiza kuchita ntchito zoipa naye adzakhala ndi gawo la uchimo. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu yochita chinthu china chilichonse وَإِذَا حُيِّيتُم بِتَحِيَّةٍ فَحَيُّواْ بِأَحۡسَنَ مِنۡهَآ أَوۡ رُدُّوهَآۗ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ حَسِيبًا ٨٦Ngati munthu akulonjerani onetsetsani kuti malonje anu ndi abwino kuposa malonje ake kapena mumubwezere monga momwe wakulonjererani. Ndithudi Mulungu amasunga chiwerengero cha zinthu zonse ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۚ لَيَجۡمَعَنَّكُمۡ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ لَا رَيۡبَ فِيهِۗ وَمَنۡ أَصۡدَقُ مِنَ ٱللَّهِ حَدِيثًا ٨٧Mulungu! Kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Ndithudi Iye adzakusonkhanitsani nonse pamodzi patsiku louka kwa akufa, tsiku lopanda chikaiko. Kodi ndani amalankhula zoona kuposa Mulungu ۞ فَمَا لَكُمۡ فِي ٱلۡمُنَٰفِقِينَ فِئَتَيۡنِ وَٱللَّهُ أَرۡكَسَهُم بِمَا كَسَبُوٓاْۚ أَتُرِيدُونَ أَن تَهۡدُواْ مَنۡ أَضَلَّ ٱللَّهُۖ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَلَن تَجِدَ لَهُۥ سَبِيلًا ٨٨Kodi mwatani kuti mukhale ogawikana magulu awiri pa nkhani ya anthu a chinyengo? Mulungu, mwini wake wawataya chifukwa cha ntchito zawo zoipa. Kodi inu mufuna kumutsogolera iye amene Mulungu wamusokeretsa? Inu simudzapeza njira ina iliyonse وَدُّواْ لَوۡ تَكۡفُرُونَ كَمَا كَفَرُواْ فَتَكُونُونَ سَوَآءًۖ فَلَا تَتَّخِذُواْ مِنۡهُمۡ أَوۡلِيَآءَ حَتَّىٰ يُهَاجِرُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِۚ فَإِن تَوَلَّوۡاْ فَخُذُوهُمۡ وَٱقۡتُلُوهُمۡ حَيۡثُ وَجَدتُّمُوهُمۡۖ وَلَا تَتَّخِذُواْ مِنۡهُمۡ وَلِيًّا وَلَا نَصِيرًا ٨٩Iwo afuna kuti iwe usakhulupirire monga momwe iwo sadakhulupirire kuti mulingane. Iwe usapalane nawo ubwenzi ayi mpaka pamene asiya nyumba zawo chifukwa cha njira ya Mulungu. Koma ngati iwo akuthawani, agwireni ndipo muwaphe pali ponse pamene muwapeze ndipo musafune abwenzi kapena okuthandizani pakati pawo إِلَّا ٱلَّذِينَ يَصِلُونَ إِلَىٰ قَوۡمِۭ بَيۡنَكُمۡ وَبَيۡنَهُم مِّيثَٰقٌ أَوۡ جَآءُوكُمۡ حَصِرَتۡ صُدُورُهُمۡ أَن يُقَٰتِلُوكُمۡ أَوۡ يُقَٰتِلُواْ قَوۡمَهُمۡۚ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَسَلَّطَهُمۡ عَلَيۡكُمۡ فَلَقَٰتَلُوكُمۡۚ فَإِنِ ٱعۡتَزَلُوكُمۡ فَلَمۡ يُقَٰتِلُوكُمۡ وَأَلۡقَوۡاْ إِلَيۡكُمُ ٱلسَّلَمَ فَمَا جَعَلَ ٱللَّهُ لَكُمۡ عَلَيۡهِمۡ سَبِيلًا ٩٠Kupatula okhawo amene gulu lina limene liri pakati panu ndipo inu mwachita nawo pangano lokhazikitsa mtendere kapena adza kwa inu chifukwa mitima yawo yawaletsa kuti amenyane nanu kapena kumenyana ndi anthu a mtundu wawo. Mulungu akadafuna akadawapatsa iwo mphamvu zoti akugonjetseni inu, kotero akadamenyana nanu. Choncho ngati atalikirana nanu ndipo asiya kumenyana nanu ndi kukuonetsani mtendere, Mulungu wakulamulirani kuti musawaononge سَتَجِدُونَ ءَاخَرِينَ يُرِيدُونَ أَن يَأۡمَنُوكُمۡ وَيَأۡمَنُواْ قَوۡمَهُمۡ كُلَّ مَا رُدُّوٓاْ إِلَى ٱلۡفِتۡنَةِ أُرۡكِسُواْ فِيهَاۚ فَإِن لَّمۡ يَعۡتَزِلُوكُمۡ وَيُلۡقُوٓاْ إِلَيۡكُمُ ٱلسَّلَمَ وَيَكُفُّوٓاْ أَيۡدِيَهُمۡ فَخُذُوهُمۡ وَٱقۡتُلُوهُمۡ حَيۡثُ ثَقِفۡتُمُوهُمۡۚ وَأُوْلَٰٓئِكُمۡ جَعَلۡنَا لَكُمۡ عَلَيۡهِمۡ سُلۡطَٰنًا مُّبِينًا ٩١Mudzawapeza ena ali kufuna chitetezo chanu ndiponso chitetezo chochokera kwa anthu awo. Nthawi iliyonse akayesedwa iwo amapita mwamsangamsanga. Ngati iwo sachoka kwa inu ndiponso ngati iwo sakhazikitsa mtendere ndi inu kapena kusiya nkhondo ndi inu, agwireni ndi kuwapha pali ponse pamene muwapeza. Pa anthu otere, Ife takupatsani chilolezo chomenyana nawo وَمَا كَانَ لِمُؤۡمِنٍ أَن يَقۡتُلَ مُؤۡمِنًا إِلَّا خَطَـًٔاۚ وَمَن قَتَلَ مُؤۡمِنًا خَطَـًٔا فَتَحۡرِيرُ رَقَبَةٍ مُّؤۡمِنَةٍ وَدِيَةٌ مُّسَلَّمَةٌ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦٓ إِلَّآ أَن يَصَّدَّقُواْۚ فَإِن كَانَ مِن قَوۡمٍ عَدُوٍّ لَّكُمۡ وَهُوَ مُؤۡمِنٌ فَتَحۡرِيرُ رَقَبَةٍ مُّؤۡمِنَةٍۖ وَإِن كَانَ مِن قَوۡمِۭ بَيۡنَكُمۡ وَبَيۡنَهُم مِّيثَٰقٌ فَدِيَةٌ مُّسَلَّمَةٌ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ وَتَحۡرِيرُ رَقَبَةٍ مُّؤۡمِنَةٍۖ فَمَن لَّمۡ يَجِدۡ فَصِيَامُ شَهۡرَيۡنِ مُتَتَابِعَيۡنِ تَوۡبَةً مِّنَ ٱللَّهِۗ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلِيمًا حَكِيمًا ٩٢Ndi chinthu choletsedwa kuti munthu wokhulupirira aphe mzake wokhulupirira kupatula mwangozi. Ndipo aliyense amene, mwangozi, akupha munthu wokhulupirira ayenera kumasula kapolo wokhulupirira m’modzi ndi kulipira ndalama zopepesera ku banja la ophedwayo, kupatula ngati iwo asankha kuti amukhululukira munthu wakuphayo. Ngati malemuyo anali wochokera kwa adani anu ndipo anali wokhulupirira, chilango chake ndi kumasula kapolo m’modzi wa wokhulupirira. Koma ngati malemuyo anali ochokera ku mtundu wa athu ogwirizana nawo, ndalama za chipepeso ziyenera kuperekedwa kubanja la munthu wakufayo ndi kumasula kapolo mmodzi wa wokhulupirira. Ngati munthu sangathe kupeza izi, ayenera kusala miyezi iwiri motsatizana ndi cholinga chopeza chikhululukiro kwa Mulungu. Ndipo Mulungu ndi Wodziwa ndi Waluntha وَمَن يَقۡتُلۡ مُؤۡمِنًا مُّتَعَمِّدًا فَجَزَآؤُهُۥ جَهَنَّمُ خَٰلِدًا فِيهَا وَغَضِبَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِ وَلَعَنَهُۥ وَأَعَدَّ لَهُۥ عَذَابًا عَظِيمًا ٩٣Ndipo aliyense amene apha munthu wokhulupirira mwadala, mphotho yake ndi kupsya ku moto wa ku Gahena ndipo adzakhala komweko ndipo mkwiyo ndi temberero la Mulungu zili pa iye ndipo chilango chowawa chili kukonzedwa chifukwa cha iye يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِذَا ضَرَبۡتُمۡ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ فَتَبَيَّنُواْ وَلَا تَقُولُواْ لِمَنۡ أَلۡقَىٰٓ إِلَيۡكُمُ ٱلسَّلَٰمَ لَسۡتَ مُؤۡمِنًا تَبۡتَغُونَ عَرَضَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا فَعِندَ ٱللَّهِ مَغَانِمُ كَثِيرَةٌۚ كَذَٰلِكَ كُنتُم مِّن قَبۡلُ فَمَنَّ ٱللَّهُ عَلَيۡكُمۡ فَتَبَيَّنُوٓاْۚ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرًا ٩٤oh inu anthu okhulupirira! onetsetsani kuti pamene mupita kukamenya nkhondo m’njira ya Mulungu, kuti musanene kwa iwo amene akhulupirira kuti ndi osakhulupirira pofuna kuti mupeze katundu wosakhalitsa wa mdziko lino. Kwa Mulungu kuli zinthu zambiri zabwino. Monga mmene iye ali, nanunso mudali wosakhulupirira m’masiku adzana koma tsopano Mulungu wakupatsani chisomo chake pokutsogolerani ku njira yoyenera. Kotero musachite tsankho! Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita لَّا يَسۡتَوِي ٱلۡقَٰعِدُونَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ غَيۡرُ أُوْلِي ٱلضَّرَرِ وَٱلۡمُجَٰهِدُونَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ بِأَمۡوَٰلِهِمۡ وَأَنفُسِهِمۡۚ فَضَّلَ ٱللَّهُ ٱلۡمُجَٰهِدِينَ بِأَمۡوَٰلِهِمۡ وَأَنفُسِهِمۡ عَلَى ٱلۡقَٰعِدِينَ دَرَجَةًۚ وَكُلًّا وَعَدَ ٱللَّهُ ٱلۡحُسۡنَىٰۚ وَفَضَّلَ ٱللَّهُ ٱلۡمُجَٰهِدِينَ عَلَى ٱلۡقَٰعِدِينَ أَجۡرًا عَظِيمًا ٩٥Anthu okhulupirira amene akhala, safanana kupatula iwo amene ali ndi bvuto ndi amene amenyana nkhondo m’njira ya Mulungu ndi chuma chawo ndi iwo eni. Mulungu adawakweza pamwamba iwo amene amamenya nkhondo ndi chuma chawo pamodzi ndi iwo eni kuposa iwo amene akhala kunyumba. Kwa aliyense, Iye walonjeza malipiro abwino koma Mulungu wawapatsa mphotho yaikulu amene amalimbikira ndipo amamenya nkhondo m’njira ya Mulungu kuposa amene amakhala kunyumba دَرَجَٰتٍ مِّنۡهُ وَمَغۡفِرَةً وَرَحۡمَةًۚ وَكَانَ ٱللَّهُ غَفُورًا رَّحِيمًا ٩٦Adzapeza maudindo kuchokera kwa Iye, chikhululukiro ndi chisoni. Mulungu amakhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha إِنَّ ٱلَّذِينَ تَوَفَّىٰهُمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ ظَالِمِيٓ أَنفُسِهِمۡ قَالُواْ فِيمَ كُنتُمۡۖ قَالُواْ كُنَّا مُسۡتَضۡعَفِينَ فِي ٱلۡأَرۡضِۚ قَالُوٓاْ أَلَمۡ تَكُنۡ أَرۡضُ ٱللَّهِ وَٰسِعَةً فَتُهَاجِرُواْ فِيهَاۚ فَأُوْلَٰٓئِكَ مَأۡوَىٰهُمۡ جَهَنَّمُۖ وَسَآءَتۡ مَصِيرًا ٩٧Ndithudi! Iwo amene angelo amachotsa moyo wawo pamene ali ochimwa, adzafunsidwa kuti: “Mudali kuchita chiyani?” Iwo adzanena: “Tinali opanda mphamvu ndi oponderezedwa padziko lapansi.” Angelo adzati kwa iwo: “Kodi dziko la Mulungu silinali lotambasuka kuti inu mukadasamuka?” Iwo mudzi wawo ndi Gahena. Malo oipa kwambiri ofikirako إِلَّا ٱلۡمُسۡتَضۡعَفِينَ مِنَ ٱلرِّجَالِ وَٱلنِّسَآءِ وَٱلۡوِلۡدَٰنِ لَا يَسۡتَطِيعُونَ حِيلَةً وَلَا يَهۡتَدُونَ سَبِيلًا ٩٨Kupatula anthu ofoka pakati pa amuna, akazi ndi ana amene alibe mphamvu kapena njira zothawira فَأُوْلَٰٓئِكَ عَسَى ٱللَّهُ أَن يَعۡفُوَ عَنۡهُمۡۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَفُوًّا غَفُورًا ٩٩Kwa otere pali chikhulupiriro choti Mulungu adzawakhululukira ndipo Mulungu ndi wachisoni ndi wokhululuka nthawi zonse ۞ وَمَن يُهَاجِرۡ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ يَجِدۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُرَٰغَمًا كَثِيرًا وَسَعَةًۚ وَمَن يَخۡرُجۡ مِنۢ بَيۡتِهِۦ مُهَاجِرًا إِلَى ٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ ثُمَّ يُدۡرِكۡهُ ٱلۡمَوۡتُ فَقَدۡ وَقَعَ أَجۡرُهُۥ عَلَى ٱللَّهِۗ وَكَانَ ٱللَّهُ غَفُورًا رَّحِيمًا ١٠٠Iye amene asamuka kwawo mu njira ya Mulungu adzapeza padziko lapansi malo ochuluka othawirako ndi katundu wochuluka. Ndipo iye amene asamuka chifukwa cha Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo imfa impeza, ndithu malipiro ake ali ndi Mulungu. Ndipo Mulungu ndi wokhululuka ndi wachisoni chosatha وَإِذَا ضَرَبۡتُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَلَيۡسَ عَلَيۡكُمۡ جُنَاحٌ أَن تَقۡصُرُواْ مِنَ ٱلصَّلَوٰةِ إِنۡ خِفۡتُمۡ أَن يَفۡتِنَكُمُ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْۚ إِنَّ ٱلۡكَٰفِرِينَ كَانُواْ لَكُمۡ عَدُوًّا مُّبِينًا ١٠١Ndipo pamene inu muyenda padziko lapansi sikulakwa kwa inu kupungula mapemphero ngati muopa kuti anthu osakhulupirira akuvutitsani. Ndithudi anthu osakhulupirira ndi adani anu enieni وَإِذَا كُنتَ فِيهِمۡ فَأَقَمۡتَ لَهُمُ ٱلصَّلَوٰةَ فَلۡتَقُمۡ طَآئِفَةٌ مِّنۡهُم مَّعَكَ وَلۡيَأۡخُذُوٓاْ أَسۡلِحَتَهُمۡۖ فَإِذَا سَجَدُواْ فَلۡيَكُونُواْ مِن وَرَآئِكُمۡ وَلۡتَأۡتِ طَآئِفَةٌ أُخۡرَىٰ لَمۡ يُصَلُّواْ فَلۡيُصَلُّواْ مَعَكَ وَلۡيَأۡخُذُواْ حِذۡرَهُمۡ وَأَسۡلِحَتَهُمۡۗ وَدَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَوۡ تَغۡفُلُونَ عَنۡ أَسۡلِحَتِكُمۡ وَأَمۡتِعَتِكُمۡ فَيَمِيلُونَ عَلَيۡكُم مَّيۡلَةً وَٰحِدَةًۚ وَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ إِن كَانَ بِكُمۡ أَذًى مِّن مَّطَرٍ أَوۡ كُنتُم مَّرۡضَىٰٓ أَن تَضَعُوٓاْ أَسۡلِحَتَكُمۡۖ وَخُذُواْ حِذۡرَكُمۡۗ إِنَّ ٱللَّهَ أَعَدَّ لِلۡكَٰفِرِينَ عَذَابًا مُّهِينًا ١٠٢Pamene iwe uli pakati pawo ndipo uli kuwatsogolera pa mapemphero, lola gulu lina la iwo kuti liime pamodzi ndi iwe, atanyamula zida zawo za nkhondo. Akatha kugwetsa nkhope zawo pansi apite kumbuyo kwanu ndipo libwere gulu lina limene silinapemphere kuti lipemphere nawe, ayenera kukhala tcheru ndi kutenga zida zawo za nkhondo. Anthu osakhulupirira amafuna inu mutaiwala zida zanu ndi katundu wanu kuti akukantheni nthawi imodzi, koma palibe cholakwa ngati musiya zida zanu chifukwa cha mavuto ena monga mvula kapena matenda koma khala tcheru. Ndithudi Mulungu wawakonzera anthu wosakhulupirira chilango chochititsa manyazi فَإِذَا قَضَيۡتُمُ ٱلصَّلَوٰةَ فَٱذۡكُرُواْ ٱللَّهَ قِيَٰمًا وَقُعُودًا وَعَلَىٰ جُنُوبِكُمۡۚ فَإِذَا ٱطۡمَأۡنَنتُمۡ فَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَۚ إِنَّ ٱلصَّلَوٰةَ كَانَتۡ عَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ كِتَٰبًا مَّوۡقُوتًا ١٠٣Pamene mumaliza mapemphero, kumbukirani Mulungu pamene muli choimirira, chokhala pansi kapena chogona. Koma pamene muli pabwino, pempherani nthawi zonse. Ndithudi mapemphero ndi udindo umene udaperekedwa kwa anthu okhulupirira kuti azichita pa nthawi zimene zidakhazikitsidwa وَلَا تَهِنُواْ فِي ٱبۡتِغَآءِ ٱلۡقَوۡمِۖ إِن تَكُونُواْ تَأۡلَمُونَ فَإِنَّهُمۡ يَأۡلَمُونَ كَمَا تَأۡلَمُونَۖ وَتَرۡجُونَ مِنَ ٱللَّهِ مَا لَا يَرۡجُونَۗ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلِيمًا حَكِيمًا ١٠٤Ndipo musafoke pofunafuna mdani. Ngati inu mumva kuwawa nawonso, ndithudi, akumva kuwawa monga mmene mukuonera kuwawa inu. Koma inu muli ndi chiyembekezo chochokera kwa Mulungu chimene iwo alibe. Ndipo Mulungu ndi wodziwa ndi wanzeru إِنَّآ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَ بِٱلۡحَقِّ لِتَحۡكُمَ بَيۡنَ ٱلنَّاسِ بِمَآ أَرَىٰكَ ٱللَّهُۚ وَلَا تَكُن لِّلۡخَآئِنِينَ خَصِيمًا ١٠٥Ndithudi Ife tavumbulutsa Buku kwa iwe mwachoonadi kuti uweruze pakati pa anthu pogwiritsa ntchito chimene Mulungu wakulangiza iwe. Motero iwe usawapemphere anthu oipa وَٱسۡتَغۡفِرِ ٱللَّهَۖ إِنَّ ٱللَّهَ كَانَ غَفُورًا رَّحِيمًا ١٠٦Ndipo pempha chikhululukiro cha Mulungu, ndithudi, Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni وَلَا تُجَٰدِلۡ عَنِ ٱلَّذِينَ يَخۡتَانُونَ أَنفُسَهُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يُحِبُّ مَن كَانَ خَوَّانًا أَثِيمًا ١٠٧Ndipo iwe usawaimire iwo amene amasokeretsa miyoyo yawo. Ndithudi Mulungu sakonda munthu wodzipondereza yekha amene amachita zoipa يَسۡتَخۡفُونَ مِنَ ٱلنَّاسِ وَلَا يَسۡتَخۡفُونَ مِنَ ٱللَّهِ وَهُوَ مَعَهُمۡ إِذۡ يُبَيِّتُونَ مَا لَا يَرۡضَىٰ مِنَ ٱلۡقَوۡلِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ بِمَا يَعۡمَلُونَ مُحِيطًا ١٠٨Iwo akhoza kudzibisa kwa anthu koma sangathe kudzibisa kwa Mulungu chifukwa Iye ali pamodzi ndi iwo pamene akonza chiwembu nthawi ya usiku ndi mawu amene samukondweretsa. Ndipo Mulungu amadziwa zimene iwo amachita هَٰٓأَنتُمۡ هَٰٓؤُلَآءِ جَٰدَلۡتُمۡ عَنۡهُمۡ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا فَمَن يُجَٰدِلُ ٱللَّهَ عَنۡهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ أَم مَّن يَكُونُ عَلَيۡهِمۡ وَكِيلًا ١٠٩Lo! Inu ndi amene mudawaimirira mu umoyo wa padzikolapansi.Nangakodindaniameneadzawadandaulire, kwa Mulungu pa tsiku la kuuka kwa akufa kapena ndani amene adzakhala mtetezi wawo وَمَن يَعۡمَلۡ سُوٓءًا أَوۡ يَظۡلِمۡ نَفۡسَهُۥ ثُمَّ يَسۡتَغۡفِرِ ٱللَّهَ يَجِدِ ٱللَّهَ غَفُورًا رَّحِيمًا ١١٠Ndipo iye amene achita choipa kapena achimwira mzimu wake koma pambuyo pake apempha chikhululukiro cha Mulungu, adzamupeza Mulungu ali Wokhululuka ndi Wachisoni وَمَن يَكۡسِبۡ إِثۡمًا فَإِنَّمَا يَكۡسِبُهُۥ عَلَىٰ نَفۡسِهِۦۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلِيمًا حَكِيمًا ١١١Ndipo aliyense amene achita zoipa akudzilakwira yekha. Ndipo Mulungu ndi Waluntha ndi Wanzeru وَمَن يَكۡسِبۡ خَطِيٓـَٔةً أَوۡ إِثۡمًا ثُمَّ يَرۡمِ بِهِۦ بَرِيٓـًٔا فَقَدِ ٱحۡتَمَلَ بُهۡتَٰنًا وَإِثۡمًا مُّبِينًا ١١٢Ndipo aliyense amene achita zoipa kapena tchimo koma anamizira munthu wina wopanda chifukwa, ndithudi, iye wadzisenzetsa bodza ndi tchimo limene lili loonekera وَلَوۡلَا فَضۡلُ ٱللَّهِ عَلَيۡكَ وَرَحۡمَتُهُۥ لَهَمَّت طَّآئِفَةٌ مِّنۡهُمۡ أَن يُضِلُّوكَ وَمَا يُضِلُّونَ إِلَّآ أَنفُسَهُمۡۖ وَمَا يَضُرُّونَكَ مِن شَيۡءٍۚ وَأَنزَلَ ٱللَّهُ عَلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡحِكۡمَةَ وَعَلَّمَكَ مَا لَمۡ تَكُن تَعۡلَمُۚ وَكَانَ فَضۡلُ ٱللَّهِ عَلَيۡكَ عَظِيمًا ١١٣Koma pakadapanda Chisomo ndi Chisoni cha Mulungu pa iwe gulu lina la iwo likadafuna kuti likusokeretse koma iwo sangasokeretse wina aliyense koma iwo okha, ndipo iwo sangakupweteke iwe ayi. Mulungu wavumbulutsa kwa iwe Buku la luntha ndi kukuphunzitsa iwe zinthu zimene siunali kuzidziwa. Ndipo ubwino wa Mulungu pa iwe ndi waukulu zedi ۞ لَّا خَيۡرَ فِي كَثِيرٍ مِّن نَّجۡوَىٰهُمۡ إِلَّا مَنۡ أَمَرَ بِصَدَقَةٍ أَوۡ مَعۡرُوفٍ أَوۡ إِصۡلَٰحِۭ بَيۡنَ ٱلنَّاسِۚ وَمَن يَفۡعَلۡ ذَٰلِكَ ٱبۡتِغَآءَ مَرۡضَاتِ ٱللَّهِ فَسَوۡفَ نُؤۡتِيهِ أَجۡرًا عَظِيمًا ١١٤Mulibe zabwino zambiri muzokambirana zawo za mseri kupatula mwa iye amene amalangiza za kupereka chaulere, kuonetsa chifundo ndi chiyanjanitso pakati pa anthu, ndipo iye amene amachita izi ndi cholinga chokondweretsa Mulungu, Ife tidzampatsa mphotho yaikulu وَمَن يُشَاقِقِ ٱلرَّسُولَ مِنۢ بَعۡدِ مَا تَبَيَّنَ لَهُ ٱلۡهُدَىٰ وَيَتَّبِعۡ غَيۡرَ سَبِيلِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ نُوَلِّهِۦ مَا تَوَلَّىٰ وَنُصۡلِهِۦ جَهَنَّمَۖ وَسَآءَتۡ مَصِيرًا ١١٥Ndipo aliyense amene amatsutsa ndi kutsutsana ndi Mtumwi, langizo lathu litaonetsedwa kwa iye ndipo atsatira njira imene siili ya anthu okhulupirira, Ife tidzamusunga mnjira imene wasankha ndipo tidzamuotcha iye ku Moto, malo onyansa kwambiri إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَغۡفِرُ أَن يُشۡرَكَ بِهِۦ وَيَغۡفِرُ مَا دُونَ ذَٰلِكَ لِمَن يَشَآءُۚ وَمَن يُشۡرِكۡ بِٱللَّهِ فَقَدۡ ضَلَّ ضَلَٰلَۢا بَعِيدًا ١١٦Ndithudi! Mulungu sadzakhululukira munthu wopembedza mafano. Iye adzakhululukira wina aliyense amene wamufuna pa machimo ena onse ndipo aliyense amene amalambira milungu ina osati Mulungu, iye wasochera kwambiri kuchokera ku choonadi إِن يَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦٓ إِلَّآ إِنَٰثًا وَإِن يَدۡعُونَ إِلَّا شَيۡطَٰنًا مَّرِيدًا ١١٧Iwo sapembedza china koma milungu ya ikazi m’malo mwa Iye ndipo iwo sapembedza wina koma Satana wogalukira لَّعَنَهُ ٱللَّهُۘ وَقَالَ لَأَتَّخِذَنَّ مِنۡ عِبَادِكَ نَصِيبًا مَّفۡرُوضًا ١١٨Mulungu anamutemberera iye ndipo iye adati: “Ine ndidzalanda gawo lina lokhazikika la akapolo ako.” وَلَأُضِلَّنَّهُمۡ وَلَأُمَنِّيَنَّهُمۡ وَلَأٓمُرَنَّهُمۡ فَلَيُبَتِّكُنَّ ءَاذَانَ ٱلۡأَنۡعَٰمِ وَلَأٓمُرَنَّهُمۡ فَلَيُغَيِّرُنَّ خَلۡقَ ٱللَّهِۚ وَمَن يَتَّخِذِ ٱلشَّيۡطَٰنَ وَلِيًّا مِّن دُونِ ٱللَّهِ فَقَدۡ خَسِرَ خُسۡرَانًا مُّبِينًا ١١٩“Ndithudi ine ndidzawasocheretsa ndipo, ndithudi, ndidzaukitsa zilakolako zawo zopanda pake ndipo, ndithudi, ndidzawalamula kuboola makutu a ng’ombe ndipo, ndithudi, ndidzawalamula kusintha zinthu zimene zinalengedwa ndi Mulungu.” Ndithudi aliyense amene asankha Satana m’malo mwa Mulungu ngati mtetezi wake, iye ndi wotayika kodziwikiratu يَعِدُهُمۡ وَيُمَنِّيهِمۡۖ وَمَا يَعِدُهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ إِلَّا غُرُورًا ١٢٠Iye akuwalonjeza ndi kuwakhulupiritsa zinthu zopanda pake ndipo malonjezo a Satana si ena koma chinyengo أُوْلَٰٓئِكَ مَأۡوَىٰهُمۡ جَهَنَّمُ وَلَا يَجِدُونَ عَنۡهَا مَحِيصًا ١٢١Malo a anthu otere ndi Gahena ndipo sadzapeza njira yothawira kumeneko وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ سَنُدۡخِلُهُمۡ جَنَّٰتٍ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدًاۖ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقًّاۚ وَمَنۡ أَصۡدَقُ مِنَ ٱللَّهِ قِيلًا ١٢٢Koma iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, tidzawalowetsa ku Minda yothiriridwa ndi mitsinje ya madzi yoyenda pansi pake ndipo kumeneko adzakhalako mpaka kalekale. Lonjezo la Mulungu ndi loona. Kodi ndani amene anganene zoona kuposa Mulungu لَّيۡسَ بِأَمَانِيِّكُمۡ وَلَآ أَمَانِيِّ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِۗ مَن يَعۡمَلۡ سُوٓءًا يُجۡزَ بِهِۦ وَلَا يَجِدۡ لَهُۥ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَلِيًّا وَلَا نَصِيرًا ١٢٣Sikudzakhala molingana ndi zilakolako zanu kapena za anthu a m’Buku. Iye amene achita zoipa adzalandira zoipa, ndipo sadzapeza wina kukhala omuteteza kapena kumuthandiza iye pambali pa Mulungu وَمَن يَعۡمَلۡ مِنَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ مِن ذَكَرٍ أَوۡ أُنثَىٰ وَهُوَ مُؤۡمِنٌ فَأُوْلَٰٓئِكَ يَدۡخُلُونَ ٱلۡجَنَّةَ وَلَا يُظۡلَمُونَ نَقِيرًا ١٢٤Ndipo aliyense amene amachita ntchito zabwino, mwamuna kapena mkazi, ndipo ndi wokhulupirira, ameneyo ndiye adzalowa ku Paradiso ndipo sadzaponderezedwa ngakhale pang’ono وَمَنۡ أَحۡسَنُ دِينًا مِّمَّنۡ أَسۡلَمَ وَجۡهَهُۥ لِلَّهِ وَهُوَ مُحۡسِنٌ وَٱتَّبَعَ مِلَّةَ إِبۡرَٰهِيمَ حَنِيفًاۗ وَٱتَّخَذَ ٱللَّهُ إِبۡرَٰهِيمَ خَلِيلًا ١٢٥Kodi ndani ali ndi chipembedzo chabwino kuposa munthu amene amadzipereka kwathunthu kwa Mulungu ndipo amachita ntchito zabwino ndipo amatsatira chikhulupiriro cha Abrahamu wangwiro? Ndipo Mulungu anamusankha Abrahamu kukhala bwenzi lake la pamtima وَلِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ بِكُلِّ شَيۡءٍ مُّحِيطًا ١٢٦Mwini wa chilichonse chimene chili mu mlengalenga ndi padziko lapansi ndi Mulungu. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse وَيَسۡتَفۡتُونَكَ فِي ٱلنِّسَآءِۖ قُلِ ٱللَّهُ يُفۡتِيكُمۡ فِيهِنَّ وَمَا يُتۡلَىٰ عَلَيۡكُمۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ فِي يَتَٰمَى ٱلنِّسَآءِ ٱلَّٰتِي لَا تُؤۡتُونَهُنَّ مَا كُتِبَ لَهُنَّ وَتَرۡغَبُونَ أَن تَنكِحُوهُنَّ وَٱلۡمُسۡتَضۡعَفِينَ مِنَ ٱلۡوِلۡدَٰنِ وَأَن تَقُومُواْ لِلۡيَتَٰمَىٰ بِٱلۡقِسۡطِۚ وَمَا تَفۡعَلُواْ مِنۡ خَيۡرٍ فَإِنَّ ٱللَّهَ كَانَ بِهِۦ عَلِيمًا ١٢٧Iwo amakufunsa malamulo okhudza akazi. Nena: “Mulungu ali kukuuzani za iwo ndi zomwe zikuwerengedwa m’buku zokhudza ana akazi a masiye amene simukuwapatsa zimene zidalamulidwa kwa iwo komabe inu mufuna kuwakwatira ndi ana opanda mphamvu ndi oponderezedwa ndipo kuti muonetse chilungamo kwa ana a masiye. Ndipo zilizonse zabwino zimene muchita, Mulungu amazidziwa.” وَإِنِ ٱمۡرَأَةٌ خَافَتۡ مِنۢ بَعۡلِهَا نُشُوزًا أَوۡ إِعۡرَاضًا فَلَا جُنَاحَ عَلَيۡهِمَآ أَن يُصۡلِحَا بَيۡنَهُمَا صُلۡحًاۚ وَٱلصُّلۡحُ خَيۡرٌۗ وَأُحۡضِرَتِ ٱلۡأَنفُسُ ٱلشُّحَّۚ وَإِن تُحۡسِنُواْ وَتَتَّقُواْ فَإِنَّ ٱللَّهَ كَانَ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرًا ١٢٨Ndipo ngati mkazi aopa kuzunzidwa kapena kusiyidwa ndi mwamuna wake, sichidzakhala chinthu cholakwa kwa iwo awiriwo ngati onse afuna kugwirizana pakati pawo chifukwa mgwirizano ndi wabwino. Ndipo umunthu umalamulidwa ndi umbombo. Koma ngati inu muchita chinthu chabwino ndi kulewa zoipa, ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene mukuchita وَلَن تَسۡتَطِيعُوٓاْ أَن تَعۡدِلُواْ بَيۡنَ ٱلنِّسَآءِ وَلَوۡ حَرَصۡتُمۡۖ فَلَا تَمِيلُواْ كُلَّ ٱلۡمَيۡلِ فَتَذَرُوهَا كَٱلۡمُعَلَّقَةِۚ وَإِن تُصۡلِحُواْ وَتَتَّقُواْ فَإِنَّ ٱللَّهَ كَانَ غَفُورًا رَّحِيمًا ١٢٩Inu simudzatha kuchita chilungamo pakati pa akazi anu ngakhale mutafuna kutero. Motero musakondere mbali imodzi ndikumusiya winayo osadziwa chimene chili kuchitika. Ndipo ngati inu muchita chilungamo ndi kuchita chili chonse chabwino ndi kuopa Mulungu, ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha وَإِن يَتَفَرَّقَا يُغۡنِ ٱللَّهُ كُلًّا مِّن سَعَتِهِۦۚ وَكَانَ ٱللَّهُ وَٰسِعًا حَكِيمًا ١٣٠Koma ngati iwo asiyana, Mulungu adzapereka zochuluka kwa aliyense wa iwo kuchokera ku zinthu zake zambiri. Ndipo Mulungu ndi wopereka mowolowa manja kwa zolengedwa zake ndipo ndi Wanzeru وَلِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۗ وَلَقَدۡ وَصَّيۡنَا ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ مِن قَبۡلِكُمۡ وَإِيَّاكُمۡ أَنِ ٱتَّقُواْ ٱللَّهَۚ وَإِن تَكۡفُرُواْ فَإِنَّ لِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ غَنِيًّا حَمِيدًا ١٣١Ndipo mwini wake wa zonse za m’mlengalenga ndi za pa dziko lapansi ndi Mulungu. Ndipo, Ife tidawalangiza iwo amene analandira Buku inu musadadze ndiponso ndi inu nomwe kuti muziopa Mulungu. Koma ngati mukana, ndithudi, Mulungu ndiye mwini wa zonse zimene zili m’mlengalenga ndi padziko lapansi. Mulungu sasowa chilichonse ndipo ndi otamandidwa وَلِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ وَكِيلًا ١٣٢Ndipo mwini wake wa zonse zimene zili mlengalenga ndi padziko lapansi ndi Mulungu. Ndipo Mulungu ndi wokwanira kukhala Mtetezi wanu إِن يَشَأۡ يُذۡهِبۡكُمۡ أَيُّهَا ٱلنَّاسُ وَيَأۡتِ بِـَٔاخَرِينَۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلَىٰ ذَٰلِكَ قَدِيرًا ١٣٣Ngati Iye atafuna, akhoza kukuchotsani inu ndi kubweretsa ena. Ndipo Mulungu ali ndi mphamvu yotero مَّن كَانَ يُرِيدُ ثَوَابَ ٱلدُّنۡيَا فَعِندَ ٱللَّهِ ثَوَابُ ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ سَمِيعَۢا بَصِيرًا ١٣٤Aliyense amene afuna dipo la moyo uno ndi Mulungu yekha amene amasunga dipo la m’moyo uno ndi umoyo umene uli nkudza. Ndipo Mulungu amamva zonse ndipo amaona zonse ۞ يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ كُونُواْ قَوَّٰمِينَ بِٱلۡقِسۡطِ شُهَدَآءَ لِلَّهِ وَلَوۡ عَلَىٰٓ أَنفُسِكُمۡ أَوِ ٱلۡوَٰلِدَيۡنِ وَٱلۡأَقۡرَبِينَۚ إِن يَكُنۡ غَنِيًّا أَوۡ فَقِيرًا فَٱللَّهُ أَوۡلَىٰ بِهِمَاۖ فَلَا تَتَّبِعُواْ ٱلۡهَوَىٰٓ أَن تَعۡدِلُواْۚ وَإِن تَلۡوُۥٓاْ أَوۡ تُعۡرِضُواْ فَإِنَّ ٱللَّهَ كَانَ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرًا ١٣٥oh inu anthu okhulupirira! Khalani anthu ochita chilungamo ngati mboni za Mulungu ngakhale kuti umboniwo ndi wosakomera inu kapena makolo anu kapena abale anu, kaya iwo ndi wolemera kapena wosauka. Mulungu ndiye Mtetezi wa iwo onse. Motero musatsatire zilakolako zanu ndi kusiya kuchita chilungamo. Ndipo ngati mukapereka umboni wosayenera kapena kukana kupereka, ndithudi Mulungu ali kudziwa ntchito zanu zimene muchita يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ ءَامِنُواْ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَٱلۡكِتَٰبِ ٱلَّذِي نَزَّلَ عَلَىٰ رَسُولِهِۦ وَٱلۡكِتَٰبِ ٱلَّذِيٓ أَنزَلَ مِن قَبۡلُۚ وَمَن يَكۡفُرۡ بِٱللَّهِ وَمَلَٰٓئِكَتِهِۦ وَكُتُبِهِۦ وَرُسُلِهِۦ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِ فَقَدۡ ضَلَّ ضَلَٰلَۢا بَعِيدًا ١٣٦oh inu anthu okhulupirira! Khulupirirani mwa Mulungundi Mtumwiwakendi Bukulimenewavumbulutsa kwa Mtumwi wake ndi Buku limene Iye adavumbulutsa kale ndipo aliyense amene sakhulupirira Mulungu, Angelo ake, Mabuku ake, Atumwi ake ndi tsiku lomaliza ndithudi wasokera إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ثُمَّ كَفَرُواْ ثُمَّ ءَامَنُواْ ثُمَّ كَفَرُواْ ثُمَّ ٱزۡدَادُواْ كُفۡرًا لَّمۡ يَكُنِ ٱللَّهُ لِيَغۡفِرَ لَهُمۡ وَلَا لِيَهۡدِيَهُمۡ سَبِيلَۢا ١٣٧Ndithudi iwo amene akhulupirira ndipo kenaka akana ndipo akhulupirira ndipo akananso ndipo aonjezera kusakhulupirira, Mulungu sadzawakhululukira kapena kuwatsogolera kunjira ya choonadi بَشِّرِ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ بِأَنَّ لَهُمۡ عَذَابًا أَلِيمًا ١٣٨Achenjezeni anthu achinyengo kuti chilango chowawa chili kuwadikira ٱلَّذِينَ يَتَّخِذُونَ ٱلۡكَٰفِرِينَ أَوۡلِيَآءَ مِن دُونِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَۚ أَيَبۡتَغُونَ عِندَهُمُ ٱلۡعِزَّةَ فَإِنَّ ٱلۡعِزَّةَ لِلَّهِ جَمِيعًا ١٣٩Iwo amene amasankha anthu osakhulupirira kukhala atetezi awo m’malo mwa anthu okhulupirira, kodi iwo ali kufuna ulemerero kuchokera kwa iwo? Ndithudi ulemerero, mphamvu ndi kuyamikidwa, Mwini wake ndi Mulungu وَقَدۡ نَزَّلَ عَلَيۡكُمۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ أَنۡ إِذَا سَمِعۡتُمۡ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ يُكۡفَرُ بِهَا وَيُسۡتَهۡزَأُ بِهَا فَلَا تَقۡعُدُواْ مَعَهُمۡ حَتَّىٰ يَخُوضُواْ فِي حَدِيثٍ غَيۡرِهِۦٓ إِنَّكُمۡ إِذًا مِّثۡلُهُمۡۗ إِنَّ ٱللَّهَ جَامِعُ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ وَٱلۡكَٰفِرِينَ فِي جَهَنَّمَ جَمِيعًا ١٤٠Ndipo zavumbulutsidwa kale kwa inu m’Buku kuti pamene inu mukumva chivumbulutso cha Mulungu chili kukanidwa kapena kunyozedwa, inu musakhale pa malo amenewo mpaka pamene ayamba kukamba nkhani zina chifukwa mukakhala nawo, mudzakhala ngati iwo. Ndithudi Mulungu adzasonkhanitsa anthu a chinyengo ndi anthu osakhulupirira ku Gahena ٱلَّذِينَ يَتَرَبَّصُونَ بِكُمۡ فَإِن كَانَ لَكُمۡ فَتۡحٌ مِّنَ ٱللَّهِ قَالُوٓاْ أَلَمۡ نَكُن مَّعَكُمۡ وَإِن كَانَ لِلۡكَٰفِرِينَ نَصِيبٌ قَالُوٓاْ أَلَمۡ نَسۡتَحۡوِذۡ عَلَيۡكُمۡ وَنَمۡنَعۡكُم مِّنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَۚ فَٱللَّهُ يَحۡكُمُ بَيۡنَكُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ وَلَن يَجۡعَلَ ٱللَّهُ لِلۡكَٰفِرِينَ عَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ سَبِيلًا ١٤١Iwo amene amayembekezera ndi kuyang’ana; ndipo ngati Mulungu akupambanitsani, iwo amati: “Kodi ife sitinali kumbali yanu?” Ndipo ngati anthu osakhulupirira apambana, iwo amati kwa iwo: “Kodi ife sitidali ndi mphamvu zoposa inu ndiponso kodi ife sitidakutetezeni kwa anthu okhulupirira?” Mulungu adzaweruza, pakati panu, pa tsiku lakuuka kwa akufa. Ndipo Mulungu sadzawapatsa anthu osakhulupirira njira yoti apambane anthu okhulupirira إِنَّ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ يُخَٰدِعُونَ ٱللَّهَ وَهُوَ خَٰدِعُهُمۡ وَإِذَا قَامُوٓاْ إِلَى ٱلصَّلَوٰةِ قَامُواْ كُسَالَىٰ يُرَآءُونَ ٱلنَّاسَ وَلَا يَذۡكُرُونَ ٱللَّهَ إِلَّا قَلِيلًا ١٤٢Ndithudi anthu a chinyengo afuna kunyenga Mulungu koma ndi Mulungu amene amawanyenga iwo ndipo pamene iwo amaima pamapemphero, amaimirira mwaulesi kuti anthu awaone ndipo sakumbukira Mulungu ngakhale mwapang’ono مُّذَبۡذَبِينَ بَيۡنَ ذَٰلِكَ لَآ إِلَىٰ هَٰٓؤُلَآءِ وَلَآ إِلَىٰ هَٰٓؤُلَآءِۚ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَلَن تَجِدَ لَهُۥ سَبِيلًا ١٤٣Iwo ali kupita uku ndi uko, ndipo sali m’gulu ili ndipo aliyense amene Mulungu wamusocheretsa simungampezere iye njira يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَتَّخِذُواْ ٱلۡكَٰفِرِينَ أَوۡلِيَآءَ مِن دُونِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَۚ أَتُرِيدُونَ أَن تَجۡعَلُواْ لِلَّهِ عَلَيۡكُمۡ سُلۡطَٰنًا مُّبِينًا ١٤٤oh inu anthu okhulupirira! Musasankhe anthu osakhulupirira kuti akhale abwenzi anu mmalo mwa anthu okhulupirira. Kodi mukufuna kuika umboni woonekera kwa Mulungu wokutsutsani inu إِنَّ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ فِي ٱلدَّرۡكِ ٱلۡأَسۡفَلِ مِنَ ٱلنَّارِ وَلَن تَجِدَ لَهُمۡ نَصِيرًا ١٤٥Ndithudi anthu achinyengo adzaponyedwa ku malo apansipansi a ku Moto. Inu simudzawapezera wowathandiza إِلَّا ٱلَّذِينَ تَابُواْ وَأَصۡلَحُواْ وَٱعۡتَصَمُواْ بِٱللَّهِ وَأَخۡلَصُواْ دِينَهُمۡ لِلَّهِ فَأُوْلَٰٓئِكَ مَعَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَۖ وَسَوۡفَ يُؤۡتِ ٱللَّهُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ أَجۡرًا عَظِيمًا ١٤٦Kupatula iwo amene alapa zoipa zawo ndi kuchita ntchito zabwino ndipo ayeretsa chipembedzo chawo. Iwo adzakhala pamodzi ndi anthu okhulupirira. Ndipo Mulungu adzawapatsa anthu okhulupirira mphotho yaikulu مَّا يَفۡعَلُ ٱللَّهُ بِعَذَابِكُمۡ إِن شَكَرۡتُمۡ وَءَامَنتُمۡۚ وَكَانَ ٱللَّهُ شَاكِرًا عَلِيمًا ١٤٧Kodi Mulungu angakulangeni bwanji inu ngati muthokoza ndi kukhulupirira mwa Iye? Ndithudi Mulungu amayamika, ndipo ndi Wodziwa zonse

الجزء السادس

۞ لَّا يُحِبُّ ٱللَّهُ ٱلۡجَهۡرَ بِٱلسُّوٓءِ مِنَ ٱلۡقَوۡلِ إِلَّا مَن ظُلِمَۚ وَكَانَ ٱللَّهُ سَمِيعًا عَلِيمًا ١٤٨Mulungu sakondwera ndi kuyankhula mawu oipa pagulu kupatula kuchokera kwa amene waponderezedwa. Ndipo Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa zonse إِن تُبۡدُواْ خَيۡرًا أَوۡ تُخۡفُوهُ أَوۡ تَعۡفُواْ عَن سُوٓءٍ فَإِنَّ ٱللَّهَ كَانَ عَفُوًّا قَدِيرًا ١٤٩Kaya inu muonetsera pochita zabwino kapena mubisa, kapena mukhululukira zoipa, ndithudi, Mulungu ndi wokhululukira ndi wamphamvu zonse إِنَّ ٱلَّذِينَ يَكۡفُرُونَ بِٱللَّهِ وَرُسُلِهِۦ وَيُرِيدُونَ أَن يُفَرِّقُواْ بَيۡنَ ٱللَّهِ وَرُسُلِهِۦ وَيَقُولُونَ نُؤۡمِنُ بِبَعۡضٍ وَنَكۡفُرُ بِبَعۡضٍ وَيُرِيدُونَ أَن يَتَّخِذُواْ بَيۡنَ ذَٰلِكَ سَبِيلًا ١٥٠Ndithudi iwo amene sakhulupirira Mulungu ndi Atumwi ake ndipo afuna kusiyanitsa pakati pa Mulungu ndi Atumwi ake ponena kuti: “Ife timakhulupirira mwa ena ndipo sitikhulupirira ena.” Ndipo amafuna kusankha njira yapakati ndi pakati أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡكَٰفِرُونَ حَقًّاۚ وَأَعۡتَدۡنَا لِلۡكَٰفِرِينَ عَذَابًا مُّهِينًا ١٥١Amenewa ndithudi ndi osakhulupirira enieni. Ndipo Ife tawakonzera anthu osakhulupirira chilango chochititsa manyazi وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِٱللَّهِ وَرُسُلِهِۦ وَلَمۡ يُفَرِّقُواْ بَيۡنَ أَحَدٍ مِّنۡهُمۡ أُوْلَٰٓئِكَ سَوۡفَ يُؤۡتِيهِمۡ أُجُورَهُمۡۚ وَكَانَ ٱللَّهُ غَفُورًا رَّحِيمًا ١٥٢Ndipo iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Atumwi ake ndipo sasiyanitsa pakati pa aliyense wa iwo, Ife tidzawapatsa mphotho zawo ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi wa chisoni chosatha يَسۡـَٔلُكَ أَهۡلُ ٱلۡكِتَٰبِ أَن تُنَزِّلَ عَلَيۡهِمۡ كِتَٰبًا مِّنَ ٱلسَّمَآءِۚ فَقَدۡ سَأَلُواْ مُوسَىٰٓ أَكۡبَرَ مِن ذَٰلِكَ فَقَالُوٓاْ أَرِنَا ٱللَّهَ جَهۡرَةً فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّٰعِقَةُ بِظُلۡمِهِمۡۚ ثُمَّ ٱتَّخَذُواْ ٱلۡعِجۡلَ مِنۢ بَعۡدِ مَا جَآءَتۡهُمُ ٱلۡبَيِّنَٰتُ فَعَفَوۡنَا عَن ذَٰلِكَۚ وَءَاتَيۡنَا مُوسَىٰ سُلۡطَٰنًا مُّبِينًا ١٥٣Anthu otsatira a m’Buku akukufunsa iwe kuti uwatsitsire buku kuchokera kumwamba. Ndithudi iwo adafunsa Mose zazikulu kuposa zimenezi pamene iwo adati: “Tionetse Mulungu poyera.” Koma iwo anakanthidwa ndi mphenzi chifukwa cha uchimo wawo. Ndipo iwo adapembedza mwana wa ng’ombe ngakhale analandira zizindikiro zathu. Komabe Ife tidawakhululukira zimenezo. Ndipo tidampatsa Mose mphamvu zooneka وَرَفَعۡنَا فَوۡقَهُمُ ٱلطُّورَ بِمِيثَٰقِهِمۡ وَقُلۡنَا لَهُمُ ٱدۡخُلُواْ ٱلۡبَابَ سُجَّدًا وَقُلۡنَا لَهُمۡ لَا تَعۡدُواْ فِي ٱلسَّبۡتِ وَأَخَذۡنَا مِنۡهُم مِّيثَٰقًا غَلِيظًا ١٥٤Pokwaniritsa lonjezo, Ife tidakweza pamwamba pawo phiri, ndipo tidati kwa iwo: “Lowani pa chipata mogwetsa nkhope ndi modzichepetsa.” Ndipo Ife tidawalamula kuti: “Musaswe malamulo a tsiku la Sabata.” Ndipo Ife tidatenga lonjezo lokhazikika kuchokera kwa iwo فَبِمَا نَقۡضِهِم مِّيثَٰقَهُمۡ وَكُفۡرِهِم بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَقَتۡلِهِمُ ٱلۡأَنۢبِيَآءَ بِغَيۡرِ حَقٍّ وَقَوۡلِهِمۡ قُلُوبُنَا غُلۡفُۢۚ بَلۡ طَبَعَ ٱللَّهُ عَلَيۡهَا بِكُفۡرِهِمۡ فَلَا يُؤۡمِنُونَ إِلَّا قَلِيلًا ١٥٥Chifukwa chakuphwanya pangano lawo ndi kukana zizindikiro za Mulungu ndi kupha Atumwi popanda chilungamo ndi kulankhula kwawo koti: Mitima yathu ndi yokutidwa. Iyayi, Mulungu wamata mitima yawo chifukwa chakusakhulupirira kwawo. Ndipo iwo sakhulupirira kwenikweni koma pang’ono وَبِكُفۡرِهِمۡ وَقَوۡلِهِمۡ عَلَىٰ مَرۡيَمَ بُهۡتَٰنًا عَظِيمًا ١٥٦Ndi chifukwa cha kusakhulupirira kwawo ndi kulankhula zoipa za Maria, tchimo lalikulu وَقَوۡلِهِمۡ إِنَّا قَتَلۡنَا ٱلۡمَسِيحَ عِيسَى ٱبۡنَ مَرۡيَمَ رَسُولَ ٱللَّهِ وَمَا قَتَلُوهُ وَمَا صَلَبُوهُ وَلَٰكِن شُبِّهَ لَهُمۡۚ وَإِنَّ ٱلَّذِينَ ٱخۡتَلَفُواْ فِيهِ لَفِي شَكٍّ مِّنۡهُۚ مَا لَهُم بِهِۦ مِنۡ عِلۡمٍ إِلَّا ٱتِّبَاعَ ٱلظَّنِّۚ وَمَا قَتَلُوهُ يَقِينَۢا ١٥٧Ndikulankhula kwawo koti: “Ife tidamupha Messiya, Yesu mwana wamwamuna wa Maria, Mthenga wa Mulungu,” koma iwo sadamuphe ayi ndipo sadampachike koma maonekedwe a Yesu anaikidwa pa munthu wina ndipo iwo amene amatsutsa za izo ndi okaika. Iwo sadziwa chili chonse, koma akutsatira nkhani za m’maluwa. Ndithudi iwo sadamuphe ayi بَل رَّفَعَهُ ٱللَّهُ إِلَيۡهِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَزِيزًا حَكِيمًا ١٥٨Koma Mulungu adamukweza kudza kwa Iye. Ndipo Mulungu ndi wa mphamvu ndi Wanzeru وَإِن مِّنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ إِلَّا لَيُؤۡمِنَنَّ بِهِۦ قَبۡلَ مَوۡتِهِۦۖ وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ يَكُونُ عَلَيۡهِمۡ شَهِيدًا ١٥٩Ndipo palibe mmodzi wa anthu a m’Buku amene angakhulupirire mwa iye, asadafe. Ndipo patsiku louka kwa akufa, iye adzakhala mboni yowatsutsa iwo فَبِظُلۡمٍ مِّنَ ٱلَّذِينَ هَادُواْ حَرَّمۡنَا عَلَيۡهِمۡ طَيِّبَٰتٍ أُحِلَّتۡ لَهُمۡ وَبِصَدِّهِمۡ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ كَثِيرًا ١٦٠Chifukwa chakulakwa kwa Ayuda, Ife tidawaletsa chakudya china chabwino chimene chidali chololedwa kwa iwo ndi chifukwa chotsekereza anthu ambiri mnjira ya Mulungu وَأَخۡذِهِمُ ٱلرِّبَوٰاْ وَقَدۡ نُهُواْ عَنۡهُ وَأَكۡلِهِمۡ أَمۡوَٰلَ ٱلنَّاسِ بِٱلۡبَٰطِلِۚ وَأَعۡتَدۡنَا لِلۡكَٰفِرِينَ مِنۡهُمۡ عَذَابًا أَلِيمًا ١٦١Ndi kulandira kwawo kwa katapira pamene iwo ataletsedwa kutero, ndi kudya kwawo kwa chuma cha anthu mwachinyengo. Ndipo Ife takonza chilango chowawa cha anthu osakhulupirira amene ali pakati pawo لَّٰكِنِ ٱلرَّٰسِخُونَ فِي ٱلۡعِلۡمِ مِنۡهُمۡ وَٱلۡمُؤۡمِنُونَ يُؤۡمِنُونَ بِمَآ أُنزِلَ إِلَيۡكَ وَمَآ أُنزِلَ مِن قَبۡلِكَۚ وَٱلۡمُقِيمِينَ ٱلصَّلَوٰةَۚ وَٱلۡمُؤۡتُونَ ٱلزَّكَوٰةَ وَٱلۡمُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِ أُوْلَٰٓئِكَ سَنُؤۡتِيهِمۡ أَجۡرًا عَظِيمًا ١٦٢Koma iwo ozindikira kwambiri amene ali pakati pawo ndi okhulupirira amene amakhulupirira mu zimene zavumbulutsidwa kwa iwe ndi zimene zidavumbulitsidwa iwe usanadze, ndipo amapemphera nthawi zonse ndikupereka msonkho wothandiza anthu osauka ndipo ali ndi chikhulupiriro mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza, awa ndiwo amene Ife tidzawapatsa mphotho yaikulu ۞ إِنَّآ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ كَمَآ أَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ نُوحٍ وَٱلنَّبِيِّـۧنَ مِنۢ بَعۡدِهِۦۚ وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰٓ إِبۡرَٰهِيمَ وَإِسۡمَٰعِيلَ وَإِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَ وَٱلۡأَسۡبَاطِ وَعِيسَىٰ وَأَيُّوبَ وَيُونُسَ وَهَٰرُونَ وَسُلَيۡمَٰنَۚ وَءَاتَيۡنَا دَاوُۥدَ زَبُورًا ١٦٣Ife tavumbulutsa kwa iwe monga momwe tidavumbulutsira kwa Nowa ndi kwa Atumwi ena amene anadza pambuyo pa iye. Ndipo tidavumbulutsa kwa Abrahamu, Ishimayeli, Isake, Yakobo ndi a mitundu, Yesu, Yobu, Yona, Aroni ndi Solomoni ndipo Davide tidamupatsa Buku la Masalimo وَرُسُلًا قَدۡ قَصَصۡنَٰهُمۡ عَلَيۡكَ مِن قَبۡلُ وَرُسُلًا لَّمۡ نَقۡصُصۡهُمۡ عَلَيۡكَۚ وَكَلَّمَ ٱللَّهُ مُوسَىٰ تَكۡلِيمًا ١٦٤Ndi Atumwi amene Ife takuuza kale mbiri yawo ndi Atumwi amene sitidakuuze ayi, ndipo ndi Mose Mulungu adalankhula naye mwachindunji رُّسُلًا مُّبَشِّرِينَ وَمُنذِرِينَ لِئَلَّا يَكُونَ لِلنَّاسِ عَلَى ٱللَّهِ حُجَّةُۢ بَعۡدَ ٱلرُّسُلِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَزِيزًا حَكِيمًا ١٦٥Atumwi ngati obweretsa nkhani zabwino kwa mitundu ya anthu ndipo chenjezo kuti iwo asadzakhale ndi chodandaula kwa Mulungu pambuyo pa Atumwi. Ndipo Mulungu ndi Wamphamvu nd Wanzeru لَّٰكِنِ ٱللَّهُ يَشۡهَدُ بِمَآ أَنزَلَ إِلَيۡكَۖ أَنزَلَهُۥ بِعِلۡمِهِۦۖ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ يَشۡهَدُونَۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ شَهِيدًا ١٦٦Koma Mulungu achitira umboni pa zimene wavumbulutsakwaiwe, Iyewalitumizandinzeruzakendipo angelo achitira umboni. Ndipo Mulungu ndi wokwana kukhalamboni إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَصَدُّواْ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ قَدۡ ضَلُّواْ ضَلَٰلَۢا بَعِيدًا ١٦٧Ndithudiiwoamenesakhulupirirandipo amaletsa ena kutsatira njira ya Mulungu, ndithudi, asochera kwenikweni إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَظَلَمُواْ لَمۡ يَكُنِ ٱللَّهُ لِيَغۡفِرَ لَهُمۡ وَلَا لِيَهۡدِيَهُمۡ طَرِيقًا ١٦٨Ndithudi iwo amene sakhulupirira ndipo adachita zosalungama, Mulungu sazawakhululukira ndipo sadzawatsogolera kunjira ina إِلَّا طَرِيقَ جَهَنَّمَ خَٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدًاۚ وَكَانَ ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ يَسِيرًا ١٦٩Kupatula njira ya ku Gahena, kuti adzakhaleko mpaka kalekale. Ndipo imeneyi ndi ntchito yopepuka kwa Mulungu يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ قَدۡ جَآءَكُمُ ٱلرَّسُولُ بِٱلۡحَقِّ مِن رَّبِّكُمۡ فَـَٔامِنُواْ خَيۡرًا لَّكُمۡۚ وَإِن تَكۡفُرُواْ فَإِنَّ لِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلِيمًا حَكِيمًا ١٧٠oh inu anthu! Ndithudi wadza kwa inu Mtumwi ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wanu, motero khulupirirani mwa iye ndipo zonse zidzakhala bwino kwa inu. Ngati inu simukhulupirira ndithudi mwini wa chilichonse chimene chili mlengalenga ndi padziko lapansi ndi Mulungu. Ndipo Mulungu ndi wodziwa chilichonse ndi Wanzeru يَٰٓأَهۡلَ ٱلۡكِتَٰبِ لَا تَغۡلُواْ فِي دِينِكُمۡ وَلَا تَقُولُواْ عَلَى ٱللَّهِ إِلَّا ٱلۡحَقَّۚ إِنَّمَا ٱلۡمَسِيحُ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَ رَسُولُ ٱللَّهِ وَكَلِمَتُهُۥٓ أَلۡقَىٰهَآ إِلَىٰ مَرۡيَمَ وَرُوحٌ مِّنۡهُۖ فَـَٔامِنُواْ بِٱللَّهِ وَرُسُلِهِۦۖ وَلَا تَقُولُواْ ثَلَٰثَةٌۚ ٱنتَهُواْ خَيۡرًا لَّكُمۡۚ إِنَّمَا ٱللَّهُ إِلَٰهٌ وَٰحِدٌۖ سُبۡحَٰنَهُۥٓ أَن يَكُونَ لَهُۥ وَلَدٌۘ لَّهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۗ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ وَكِيلًا ١٧١oh inu anthu a m’Buku! Musadutse malire a chipembedzo chanu kapena kunena zokhudza Mulungu kupatula choonadi. Messiya Yesu, mwana wa Maria, sadali wina aliyense koma Mtumwi wa Mulungu ndi Mawu ake amene adanena kwa Maria, ndi Mzimu wolengedwa ndi Iye. Kotero khulupirirani mwa Mulungu ndi Atumwi ake. Ndipo musanene kuti: “Atatu.” Siyani! Zidzakhala bwino kwa inu. Chifukwa Mulungu ndi mmodzi yekha. Ulemerero ukhale kwa Iye. Iye sangakhale ndi mwana. Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndipo Mulungu ndi okwana kukhala Mtetezi wodalirika لَّن يَسۡتَنكِفَ ٱلۡمَسِيحُ أَن يَكُونَ عَبۡدًا لِّلَّهِ وَلَا ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ ٱلۡمُقَرَّبُونَۚ وَمَن يَسۡتَنكِفۡ عَنۡ عِبَادَتِهِۦ وَيَسۡتَكۡبِرۡ فَسَيَحۡشُرُهُمۡ إِلَيۡهِ جَمِيعًا ١٧٢Messiya sangakane kukhala kapolo wa Mulungu ndiponso angelo amene ali kufupi ndi Mulungu. Ndipo aliyense amene amakana kumutumikira Mulungu chifukwa cha kudzikweza, Iye adzawasonkhanitsa onse kudza pamaso pake فَأَمَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَيُوَفِّيهِمۡ أُجُورَهُمۡ وَيَزِيدُهُم مِّن فَضۡلِهِۦۖ وَأَمَّا ٱلَّذِينَ ٱسۡتَنكَفُواْ وَٱسۡتَكۡبَرُواْ فَيُعَذِّبُهُمۡ عَذَابًا أَلِيمًا وَلَا يَجِدُونَ لَهُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ وَلِيًّا وَلَا نَصِيرًا ١٧٣Motero iwo amene ali ndi chikhulupiriro ndipo amachita ntchito zabwino, Iye adzawapatsa mphotho zawo mokwanira ndipo adzawalemeretsa iwo mwachisomo chake chochuluka. Koma iwo amene akana kupembedza kapena oyerekedwa, Iye adzawalanga ndi chilango chowawa. Ndipo iwo sadzapeza wina woposa Mulungu kuti awateteze kapena kuwathandiza يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ قَدۡ جَآءَكُم بُرۡهَٰنٌ مِّن رَّبِّكُمۡ وَأَنزَلۡنَآ إِلَيۡكُمۡ نُورًا مُّبِينًا ١٧٤oh inu anthu! Ndithudi wadza kwa inu umboni wooneka kuchokera kwa Ambuye wanu ndipo Ife takutumizirani Muuni woonekera فَأَمَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِٱللَّهِ وَٱعۡتَصَمُواْ بِهِۦ فَسَيُدۡخِلُهُمۡ فِي رَحۡمَةٍ مِّنۡهُ وَفَضۡلٍ وَيَهۡدِيهِمۡ إِلَيۡهِ صِرَٰطًا مُّسۡتَقِيمًا ١٧٥Motero iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndipo amadzipereka kwathunthu kwa Iye, adzawalowetsa ku chifundo ndi chisomo chake ndi kuwatsogolera kunjira yoyenera يَسۡتَفۡتُونَكَ قُلِ ٱللَّهُ يُفۡتِيكُمۡ فِي ٱلۡكَلَٰلَةِۚ إِنِ ٱمۡرُؤٌاْ هَلَكَ لَيۡسَ لَهُۥ وَلَدٌ وَلَهُۥٓ أُخۡتٌ فَلَهَا نِصۡفُ مَا تَرَكَۚ وَهُوَ يَرِثُهَآ إِن لَّمۡ يَكُن لَّهَا وَلَدٌۚ فَإِن كَانَتَا ٱثۡنَتَيۡنِ فَلَهُمَا ٱلثُّلُثَانِ مِمَّا تَرَكَۚ وَإِن كَانُوٓاْ إِخۡوَةً رِّجَالًا وَنِسَآءً فَلِلذَّكَرِ مِثۡلُ حَظِّ ٱلۡأُنثَيَيۡنِۗ يُبَيِّنُ ٱللَّهُ لَكُمۡ أَن تَضِلُّواْۗ وَٱللَّهُ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمُۢ ١٧٦Iwo amakufunsa za malamulo; Nena: “Mulungu akukuuzani za munthu amene alibe makolo kapena mwana. Ngati munthu wa mwamuna akufa, ndipo alibe mwana koma ali ndi mlongo wake, mlongo wake adzalandire theka la katundu amene asiya. Ndipo ngati mkazi sasiya mwana, mlongo wake adzatenga chuma chake. Koma ngati akhala ndi alongo ake awiri, iwo adzalandire magawo awiri a magawo atatu a katundu amene asiya. Ndipo ngati pali abale amuna ndi akazi, mwamuna adzalandira magawo amene angalandire akazi awiri. Mulungu akukulongosolerani kuti musasochere. Ndipo Mulungu ndi wodziwa chilichonse.”

الترجمة: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.