ملة الإسلام

السورة 61 · 14 آية · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

سورة الصف باللغة الشيشيوا

السورة بالعربية مع التفسير استمع إلى سورة الصف (1,188 قارئاً)
مدنيةسورة الصف١٤ آية

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

سَبَّحَ لِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۖ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ ١Chilichonse chimene chili mlengalenga ndi padziko lapansi, chimalemekeza Mulungu. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لِمَ تَقُولُونَ مَا لَا تَفۡعَلُونَ ٢oh inu okhulupirira! Kodi bwanji mumanena zinthu zimene simuchita كَبُرَ مَقۡتًا عِندَ ٱللَّهِ أَن تَقُولُواْ مَا لَا تَفۡعَلُونَ ٣Ndithudi ndi chinthu chonyansa kwambiri pamaso pa Mulungu kuti muzinena chinthu chimene simuchita إِنَّ ٱللَّهَ يُحِبُّ ٱلَّذِينَ يُقَٰتِلُونَ فِي سَبِيلِهِۦ صَفًّا كَأَنَّهُم بُنۡيَٰنٌ مَّرۡصُوصٌ ٤Ndithudi Mulungu amakonda iwo amene amamenya nkhondo ndi cholinga chokhazikitsa ulamuliro wake molimba, m’magulu, ngati chipupa cha miyala وَإِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِۦ يَٰقَوۡمِ لِمَ تُؤۡذُونَنِي وَقَد تَّعۡلَمُونَ أَنِّي رَسُولُ ٱللَّهِ إِلَيۡكُمۡۖ فَلَمَّا زَاغُوٓاْ أَزَاغَ ٱللَّهُ قُلُوبَهُمۡۚ وَٱللَّهُ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلۡفَٰسِقِينَ ٥Ndi pamene Mose adanena ndi anthu ake: “oh inu anthu anga! Kodi bwanji mukundikwiyitsa pamene muli kudziwa kuti ine ndine Mtumwi wa Mulungu kwa inuyo?” Ndipo pamene iwo adalakwa, Mulungu adalola kuti mitima yawo ilakwe. Ndipo Mulungu satsogolera anthu ophwanya malamulo وَإِذۡ قَالَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَ يَٰبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ إِنِّي رَسُولُ ٱللَّهِ إِلَيۡكُم مُّصَدِّقًا لِّمَا بَيۡنَ يَدَيَّ مِنَ ٱلتَّوۡرَىٰةِ وَمُبَشِّرَۢا بِرَسُولٍ يَأۡتِي مِنۢ بَعۡدِي ٱسۡمُهُۥٓ أَحۡمَدُۖ فَلَمَّا جَآءَهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ قَالُواْ هَٰذَا سِحۡرٌ مُّبِينٌ ٦Ndi pamene Yesu, mwana wa mwamuna wa Maria, adati: “oh inu ana a Israyeli! Ine ndine Mtumwi wa Mulungu amene ndatumidwa kwa inu, kutsimikizira za Buku la Chipangano chakale limene lidadza ine ndisanadze, ndi kuulula nkhani yabwino ya Mtumwi Ahmad amene adzabwera ine nditachoka.” Koma pamene iye adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka, iwo adati: “Awa ndiwo matsenga enieni.” وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ ٱلۡكَذِبَ وَهُوَ يُدۡعَىٰٓ إِلَى ٱلۡإِسۡلَٰمِۚ وَٱللَّهُ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ ٧Kodi amalakwa kwambiri ndani kuposa As-Saff 597 iye amene amapeka bodza lokhudza Mulungu ngakhale pamene ali kuitanidwa kuti alowe Chisilamu? Ndipo Mulungu satsogolera iwo amene amachita zoipa يُرِيدُونَ لِيُطۡفِـُٔواْ نُورَ ٱللَّهِ بِأَفۡوَٰهِهِمۡ وَٱللَّهُ مُتِمُّ نُورِهِۦ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡكَٰفِرُونَ ٨Cholinga chawo ndikufuna kuzimitsa nyali ya Mulungu ndi milomo yawo. Koma Mulungu adzateteza nyali yake ngakhale kuti anthu osakhulupirira sakondwera nazo هُوَ ٱلَّذِيٓ أَرۡسَلَ رَسُولَهُۥ بِٱلۡهُدَىٰ وَدِينِ ٱلۡحَقِّ لِيُظۡهِرَهُۥ عَلَى ٱلدِّينِ كُلِّهِۦ وَلَوۡ كَرِهَ ٱلۡمُشۡرِكُونَ ٩Ndiye amene watumiza Mtumwi wake ndi ulangizi ndiponso chipembedzo choonadi kuti chikhale chapamwamba pa zipembedzo zina zonse ngakhale kuti anthu osakhulupirira sakondwera nazo يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ هَلۡ أَدُلُّكُمۡ عَلَىٰ تِجَٰرَةٍ تُنجِيكُم مِّنۡ عَذَابٍ أَلِيمٍ ١٠Oh inu anthu okhulupirira! Kodi ndikulangizeni malonda apafupi amene angakuomboleni ku chilango choopsa تُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَتُجَٰهِدُونَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ بِأَمۡوَٰلِكُمۡ وَأَنفُسِكُمۡۚ ذَٰلِكُمۡ خَيۡرٌ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ ١١Kuti mukhulupirire mwa Mulungu ndi mwa Mtumwi wake, kuti mudzipereke kwathunthu mu njira ya Mulungu pogwiritsa ntchito chuma chanu ndi inu eni ake. Chimenechi ndicho chinthu chabwino kwa inu ngati inu mukadadziwa يَغۡفِرۡ لَكُمۡ ذُنُوبَكُمۡ وَيُدۡخِلۡكُمۡ جَنَّٰتٍ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ وَمَسَٰكِنَ طَيِّبَةً فِي جَنَّٰتِ عَدۡنٍۚ ذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ ١٢Iyeadzakukhululukiraniinumachimoanu ndi kukulandirani m’minda imene pansi pake pamayenda mitsinje, ndipo adzakulowetsani m’nyumba zokongola ndi zaulemu za m’Paradiso. Kumeneko, ndithudi, ndiko kupambana kwenikweni وَأُخۡرَىٰ تُحِبُّونَهَاۖ نَصۡرٌ مِّنَ ٱللَّهِ وَفَتۡحٌ قَرِيبٌۗ وَبَشِّرِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ١٣Ndipo Iye adzakupatsani madalitso ena amene mumakonda. Chithandizo chochokera kwa Mulungu ndi kupambana mwamsanga. Kotero auze nkhani yabwino anthu okhulupirira يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ كُونُوٓاْ أَنصَارَ ٱللَّهِ كَمَا قَالَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَ لِلۡحَوَارِيِّـۧنَ مَنۡ أَنصَارِيٓ إِلَى ٱللَّهِۖ قَالَ ٱلۡحَوَارِيُّونَ نَحۡنُ أَنصَارُ ٱللَّهِۖ فَـَٔامَنَت طَّآئِفَةٌ مِّنۢ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَكَفَرَت طَّآئِفَةٌۖ فَأَيَّدۡنَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ عَلَىٰ عَدُوِّهِمۡ فَأَصۡبَحُواْ ظَٰهِرِينَ ١٤oh inu okhulupirira! Khalani otumikira Mulungu monga momwe ananenera Yesu, mwana wa mwamuna wa Maria, kwa ophunzira ake: “Kodi ndani andithandiza ine potumikira Mulungu?” Iwo adayankha: “Ife ndife othandiza Mulungu.” Kotero ena mwa ana a Israyeli adakhulupirira pamene ena sadakhulupirire. Motero Ife tidawapatsa mphamvu iwo amene adakhulupirira zopambana adani awo ndipo iwo adapambanadi

الترجمة: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.