السورة بالعربية مع التفسير
استمع إلى سورة الزلزلة (1,320 قارئاً)
بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
إِذَا زُلۡزِلَتِ ٱلۡأَرۡضُ زِلۡزَالَهَا ١Pamene dziko lidzagwedezeka ndi chivomerezi chomaliza وَأَخۡرَجَتِ ٱلۡأَرۡضُ أَثۡقَالَهَا ٢Ndipo pamene nthaka idzatulutsa katundu amene ali m’kati mwake وَقَالَ ٱلۡإِنسَٰنُ مَا لَهَا ٣Ndipo munthu adzafunsa: “Kodi yatani?” يَوۡمَئِذٍ تُحَدِّثُ أَخۡبَارَهَا ٤Pa tsikuli nthaka idzaulula zonse بِأَنَّ رَبَّكَ أَوۡحَىٰ لَهَا ٥Chifukwa Ambuye wako wayiuza kuti itero يَوۡمَئِذٍ يَصۡدُرُ ٱلنَّاسُ أَشۡتَاتًا لِّيُرَوۡاْ أَعۡمَٰلَهُمۡ ٦Pa tsikuli mtundu wa anthu udzadza m’magulu osiyana siyana kudzalangizidwa ntchito zawo فَمَن يَعۡمَلۡ مِثۡقَالَ ذَرَّةٍ خَيۡرًا يَرَهُۥ ٧Motero aliyense amene amachita chabwino cholemera ngati njere ya mpiru, adzachiona وَمَن يَعۡمَلۡ مِثۡقَالَ ذَرَّةٍ شَرًّا يَرَهُۥ ٨Ndipo aliyense amene amachita choipa cholemera ngati njere ya mpiru, adzachiona
الترجمة: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.