ملة الإسلام

السورة 11 · 123 آية · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

سورة هود باللغة الشيشيوا

السورة بالعربية مع التفسير استمع إلى سورة هود (1,270 قارئاً)
مكيةسورة هود١٢٣ آية

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

الٓرۚ كِتَٰبٌ أُحۡكِمَتۡ ءَايَٰتُهُۥ ثُمَّ فُصِّلَتۡ مِن لَّدُنۡ حَكِيمٍ خَبِيرٍ ١Alif Lam Ra. Ndi Buku limene mavesi ake akonzedwa bwino. Ndipo adafotokozedwa mwatsatane tsatane kuchokera kwa Mwini nzeru ndi wodziwa أَلَّا تَعۡبُدُوٓاْ إِلَّا ٱللَّهَۚ إِنَّنِي لَكُم مِّنۡهُ نَذِيرٌ وَبَشِيرٌ ٢Kuti musapembedze wina aliyense koma Mulungu. Ndithudi ine ndine wochokera kwa Iye wochenjeza ndi wobweretsa nkhani zabwino وَأَنِ ٱسۡتَغۡفِرُواْ رَبَّكُمۡ ثُمَّ تُوبُوٓاْ إِلَيۡهِ يُمَتِّعۡكُم مَّتَٰعًا حَسَنًا إِلَىٰٓ أَجَلٍ مُّسَمًّى وَيُؤۡتِ كُلَّ ذِي فَضۡلٍ فَضۡلَهُۥۖ وَإِن تَوَلَّوۡاْ فَإِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُمۡ عَذَابَ يَوۡمٍ كَبِيرٍ ٣Ndikuti mupemphe chikhululukiro kwa Ambuye wanu ndipo lapani kwa Iye yekha kuti Iye akupatseni zinthu zabwino mpaka pa nthawi yoikidwa. Ndi kupereka kwa aliyense wochita zabwino chisomo chake chomuyenera. Ndipo ngati inu mukana, ine ndichita mantha ndi chilango chimene chingadze pa inu patsiku lalikulu إِلَى ٱللَّهِ مَرۡجِعُكُمۡۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ قَدِيرٌ ٤Ndi kwa Mulungu kumene nonse mudzabwerera ndipo Iye ali ndi mphamvu pa zinthu zonse أَلَآ إِنَّهُمۡ يَثۡنُونَ صُدُورَهُمۡ لِيَسۡتَخۡفُواْ مِنۡهُۚ أَلَا حِينَ يَسۡتَغۡشُونَ ثِيَابَهُمۡ يَعۡلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعۡلِنُونَۚ إِنَّهُۥ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ ٥Zoonadi! Iwo amakuta mitima yawo kuti akhoza kubisala kwa Iye. Ndithudi ngakhale pamene iwo avala zovala zawo, Iye amadziwa zonse zimene akubisa ndi zimene akuulula. Iye amadziwa zonse zimene zili m’mitima mwawo

الجزء الثاني عشر

۞ وَمَا مِن دَآبَّةٍ فِي ٱلۡأَرۡضِ إِلَّا عَلَى ٱللَّهِ رِزۡقُهَا وَيَعۡلَمُ مُسۡتَقَرَّهَا وَمُسۡتَوۡدَعَهَاۚ كُلٌّ فِي كِتَٰبٍ مُّبِينٍ ٦Ndipo palibe cholengedwa padziko lapansi chimene chakudya chake sichichokera kwa Mulungu. Ndipo Iye amadziwa malo ake okhala ndi malo ake a mpumulo. Zonse zili m’Buku lofotokozera bwino zinthu وَهُوَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ فِي سِتَّةِ أَيَّامٍ وَكَانَ عَرۡشُهُۥ عَلَى ٱلۡمَآءِ لِيَبۡلُوَكُمۡ أَيُّكُمۡ أَحۡسَنُ عَمَلًاۗ وَلَئِن قُلۡتَ إِنَّكُم مَّبۡعُوثُونَ مِنۢ بَعۡدِ ٱلۡمَوۡتِ لَيَقُولَنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا سِحۡرٌ مُّبِينٌ ٧Iye ndi amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi m’masiku asanu ndi limodzi ndipo Mpando wake udali pamwamba pa madzi kuti akuyeseni kuti ndani wa inu amene ali ndi ntchito zabwino. Ndipo iwe ukadanena kuti: “Inu ndithudi mudzaukitsidwa pambuyo pa kufa,” anthu osakhulupirira akadanena kuti: “Ichi si china chilichonse koma matsenga enieni.” وَلَئِنۡ أَخَّرۡنَا عَنۡهُمُ ٱلۡعَذَابَ إِلَىٰٓ أُمَّةٍ مَّعۡدُودَةٍ لَّيَقُولُنَّ مَا يَحۡبِسُهُۥٓۗ أَلَا يَوۡمَ يَأۡتِيهِمۡ لَيۡسَ مَصۡرُوفًا عَنۡهُمۡ وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ ٨Ndipo ngati Ife titachedwetsa chilango chawo mpaka pa tsiku lokhazikitsidwa, iwo adzafunsa kuti: “Nanga ndi chifukwa chiyani tsikulo lili kuchedwa?” Ndithudi pa tsiku limene izi zidzachitika, palibe chilichonse chimene chingadzapirikitse chilangocho ndipo zoopsa zimene iwo ali kuseka zidzawazungulira iwo onse وَلَئِنۡ أَذَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِنَّا رَحۡمَةً ثُمَّ نَزَعۡنَٰهَا مِنۡهُ إِنَّهُۥ لَيَـُٔوسٌ كَفُورٌ ٩Ndipo ngati Ife timulawitsa munthu chifundo chathu kenaka ndi kumulanda, ndithudi, iye amadandaula ndiponso amakhala osuliza وَلَئِنۡ أَذَقۡنَٰهُ نَعۡمَآءَ بَعۡدَ ضَرَّآءَ مَسَّتۡهُ لَيَقُولَنَّ ذَهَبَ ٱلسَّيِّـَٔاتُ عَنِّيٓۚ إِنَّهُۥ لَفَرِحٌ فَخُورٌ ١٠Koma ngati Ife titamuonetsa munthu chisoni chathu, pambuyo pa mavuto amene adapeza, iye adzati: “Mavuto atha kwa ine” Ndithudi iye amakhala mosalabadira ndiponso modzikweza kwambiri إِلَّا ٱلَّذِينَ صَبَرُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ أُوْلَٰٓئِكَ لَهُم مَّغۡفِرَةٌ وَأَجۡرٌ كَبِيرٌ ١١Kupatula iwo amene amapirira ndi kuchita ntchito zabwino. Iwo adzakhala ndi chikhululukiro ndi malipiro akulu فَلَعَلَّكَ تَارِكُۢ بَعۡضَ مَا يُوحَىٰٓ إِلَيۡكَ وَضَآئِقُۢ بِهِۦ صَدۡرُكَ أَن يَقُولُواْ لَوۡلَآ أُنزِلَ عَلَيۡهِ كَنزٌ أَوۡ جَآءَ مَعَهُۥ مَلَكٌۚ إِنَّمَآ أَنتَ نَذِيرٌۚ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ وَكِيلٌ ١٢Mwina iwe ukhoza kusiya kunena zina za zimene zavumbulutsidwa kwa iwe ndi kukhala ovutika mu mtima chifukwa chakuti iwo amanena kuti, “Bwanji chuma sichidatumizidwe kwa iye kapena bwanji Mngelo sadadze pamodzi ndi iye?” Komatu iwe ndiwe wochenjeza. Ndipo Mulungu ndiye Msungi wa zinthu zonse أَمۡ يَقُولُونَ ٱفۡتَرَىٰهُۖ قُلۡ فَأۡتُواْ بِعَشۡرِ سُوَرٍ مِّثۡلِهِۦ مُفۡتَرَيَٰتٍ وَٱدۡعُواْ مَنِ ٱسۡتَطَعۡتُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ ١٣Kapena iwo akunena kuti: “Iye wapeka yekha!” Nena, “Nanunso bweretsani mitu khumi yofanana ndi yopekedwayi. Ndipo itananiwinaamenemungathekumuitanakupatulaMulungu ngati muli kunena zoona.” فَإِلَّمۡ يَسۡتَجِيبُواْ لَكُمۡ فَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّمَآ أُنزِلَ بِعِلۡمِ ٱللَّهِ وَأَن لَّآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ فَهَلۡ أَنتُم مُّسۡلِمُونَ ١٤Akapanda kukuyankha, dziwa kuti chivumbulutso chatumizidwa ndi nzeru ya Mulungu. Ndipo kuti kulibe wina woti apembedzedwe kupatula Iye yekha. Kodi tsopano mudzakhala ogonjera مَن كَانَ يُرِيدُ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا وَزِينَتَهَا نُوَفِّ إِلَيۡهِمۡ أَعۡمَٰلَهُمۡ فِيهَا وَهُمۡ فِيهَا لَا يُبۡخَسُونَ ١٥Aliyense amene afuna moyo wa m’dziko lino pamodzi ndi zokondweretsa zake, Ife tidzawalipira molingana ndi ntchito zawo , mopanda kuchotsera chilichonse أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ لَيۡسَ لَهُمۡ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ إِلَّا ٱلنَّارُۖ وَحَبِطَ مَا صَنَعُواْ فِيهَا وَبَٰطِلٌ مَّا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ١٦Awa ndiwo anthu amene sadzapeza chilichonse m’moyo umene uli nkudza kupatula moto ndipo zonse zimene amachita pa dziko lapansi zidzaonongeka ndiponso ntchito zawo zimene ankachita zidzakhala zopanda pake أَفَمَن كَانَ عَلَىٰ بَيِّنَةٍ مِّن رَّبِّهِۦ وَيَتۡلُوهُ شَاهِدٌ مِّنۡهُ وَمِن قَبۡلِهِۦ كِتَٰبُ مُوسَىٰٓ إِمَامًا وَرَحۡمَةًۚ أُوْلَٰٓئِكَ يُؤۡمِنُونَ بِهِۦۚ وَمَن يَكۡفُرۡ بِهِۦ مِنَ ٱلۡأَحۡزَابِ فَٱلنَّارُ مَوۡعِدُهُۥۚ فَلَا تَكُ فِي مِرۡيَةٍ مِّنۡهُۚ إِنَّهُ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّكَ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يُؤۡمِنُونَ ١٧Kodi iwo amene amadalira umboni wooneka wochokera kwa Ambuye wawo, umene mboni yochokera kwa Iye amautsatira, ndipo iwo usanadze, linadza Buku la Mose, ulangizi ndi chisomo, iwo amakhulupirira koma a mpatuko amene amalikana, kumoto ndiko kudzakhala malo awo okumana. Motero iwe usakaike za ilo. Ndithudi ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wako koma anthu ambiri sakhulupirira وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًاۚ أُوْلَٰٓئِكَ يُعۡرَضُونَ عَلَىٰ رَبِّهِمۡ وَيَقُولُ ٱلۡأَشۡهَٰدُ هَٰٓؤُلَآءِ ٱلَّذِينَ كَذَبُواْ عَلَىٰ رَبِّهِمۡۚ أَلَا لَعۡنَةُ ٱللَّهِ عَلَى ٱلظَّٰلِمِينَ ١٨Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu? Anthu otero adzaonetsedwa pamaso pa Ambuye wawo ndipo mboni zidzati: “Awa ndiwo amene anali kunamizira Ambuye wawo.” Mosakaika! Matemberero a Mulungu ali pa anthu ochita zoipa ٱلَّذِينَ يَصُدُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ وَيَبۡغُونَهَا عِوَجًا وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ كَٰفِرُونَ ١٩Iwo amene amaletsa anzawo kuti asatsatire njira ya Mulungu ndipo amafuna kuti njira ya Mulungu ikhale yopindika ndiponso amakana kuti kuli moyo wina umene uli nkudza أُوْلَٰٓئِكَ لَمۡ يَكُونُواْ مُعۡجِزِينَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا كَانَ لَهُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ مِنۡ أَوۡلِيَآءَۘ يُضَٰعَفُ لَهُمُ ٱلۡعَذَابُۚ مَا كَانُواْ يَسۡتَطِيعُونَ ٱلسَّمۡعَ وَمَا كَانُواْ يُبۡصِرُونَ ٢٠Wotere sadzathawa padziko lapansi ndiponso alibe owateteza kupatula Mulungu! Chilango chawo chidzaonjezeredwa chifukwa chakuti iwo samafuna kumva ndiponso samaona أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ وَضَلَّ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ ٢١Awa ndiwo amene ataya mizimu yawo ndipo zinthu zawo zonse zabodza zidzawathawira لَا جَرَمَ أَنَّهُمۡ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ هُمُ ٱلۡأَخۡسَرُونَ ٢٢Ndithudi iwo ndiwo amene sadzapindula zambiri mmoyo umene uli nkudza إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَأَخۡبَتُوٓاْ إِلَىٰ رَبِّهِمۡ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ ٢٣Ndithudi iwo amene akhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, ndipo amadzichepetsa kwambiri pamaso pa Ambuye wawo, iwo adzakhala eni ake a Paradiso ndipo kumeneko adzakhalako mpaka kalekale ۞ مَثَلُ ٱلۡفَرِيقَيۡنِ كَٱلۡأَعۡمَىٰ وَٱلۡأَصَمِّ وَٱلۡبَصِيرِ وَٱلسَّمِيعِۚ هَلۡ يَسۡتَوِيَانِ مَثَلًاۚ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ ٢٤Fanizo la magulu awiri a anthu lili ngati munthu wakhungu ndi wosamva, wopenya ndi wakumva. Kodi magulu awiriwa ndi ofanana? Kodi simungaganize pamenepa وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوۡمِهِۦٓ إِنِّي لَكُمۡ نَذِيرٌ مُّبِينٌ ٢٥Zoonadi tidamutumiza Nowa kwa anthu ake nati: “Ndithudi ine ndine mchenjezi wanu weniweni أَن لَّا تَعۡبُدُوٓاْ إِلَّا ٱللَّهَۖ إِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُمۡ عَذَابَ يَوۡمٍ أَلِيمٍ ٢٦Kuti musapembedze wina aliyense koma Mulungu, ndithudi, ine ndili kukuderani nkhawa pa chilango cha tsiku lowawa.” فَقَالَ ٱلۡمَلَأُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن قَوۡمِهِۦ مَا نَرَىٰكَ إِلَّا بَشَرًا مِّثۡلَنَا وَمَا نَرَىٰكَ ٱتَّبَعَكَ إِلَّا ٱلَّذِينَ هُمۡ أَرَاذِلُنَا بَادِيَ ٱلرَّأۡيِ وَمَا نَرَىٰ لَكُمۡ عَلَيۡنَا مِن فَضۡلِۭ بَلۡ نَظُنُّكُمۡ كَٰذِبِينَ ٢٧Akuluakulu osakhulupirira amene adali pakati pa anthu ake adati: “Ife tili kukuona iwe ngati munthu onga ife tomwe ndiponso tili kuona kuti onse amene ali kukutsatira kuti ndi anthu apansi kwambiri pakati pathu ndiponso iwo akutsatira iwe osaganiza. Ndipo ife sitili kuona china chilichonse mwa iwe chopambana ife ndipo, kunena moona, tikuganiza kuti inu ndinu abodza.” قَالَ يَٰقَوۡمِ أَرَءَيۡتُمۡ إِن كُنتُ عَلَىٰ بَيِّنَةٍ مِّن رَّبِّي وَءَاتَىٰنِي رَحۡمَةً مِّنۡ عِندِهِۦ فَعُمِّيَتۡ عَلَيۡكُمۡ أَنُلۡزِمُكُمُوهَا وَأَنتُمۡ لَهَا كَٰرِهُونَ ٢٨Iye adati: “Oh inu anthu anga! Mukuona bwanji? Ngati ine ndili ndi umboni wochokera kwa Ambuye wanga ndiponso wandipatsa chifundo kuchokera kwa Iye, ndipo umboniwo wabisika kwa inu. Kodi ife tingakuumirizeni kuti mumvomere pamene mukunyansidwa nawo?” وَيَٰقَوۡمِ لَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مَالًاۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَى ٱللَّهِۚ وَمَآ أَنَا۠ بِطَارِدِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْۚ إِنَّهُم مُّلَٰقُواْ رَبِّهِمۡ وَلَٰكِنِّيٓ أَرَىٰكُمۡ قَوۡمًا تَجۡهَلُونَ ٢٩“oh inu anthu anga! Ine sindikukupemphani chuma chifukwa cha ichi, malipiro anga sali kwa wina koma Mulungu yekha. Ndipo ine sindiwathamangitsa amene akhulupirira. Ndithudi, iwo adzakumana ndi Ambuye wawo. Koma ine ndikukuonani kuti ndinu anthu osadziwa.” وَيَٰقَوۡمِ مَن يَنصُرُنِي مِنَ ٱللَّهِ إِن طَرَدتُّهُمۡۚ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ ٣٠“oh inu anthu anga! Ndani anganditeteze ine kwa Mulungu ngati nditawapitikitsa iwo? Kodi inu simungaganizire pamenepa?” وَلَآ أَقُولُ لَكُمۡ عِندِي خَزَآئِنُ ٱللَّهِ وَلَآ أَعۡلَمُ ٱلۡغَيۡبَ وَلَآ أَقُولُ إِنِّي مَلَكٌ وَلَآ أَقُولُ لِلَّذِينَ تَزۡدَرِيٓ أَعۡيُنُكُمۡ لَن يُؤۡتِيَهُمُ ٱللَّهُ خَيۡرًاۖ ٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا فِيٓ أَنفُسِهِمۡ إِنِّيٓ إِذًا لَّمِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ ٣١“Ine sindili kunena kwa inu kuti ndili ndi Nkhokwe za chuma cha Mulungu kapena kuti ndimadziwa zinthu zobisika. Ine sindili kunena kuti ndine Mngelo ayi ndiponso ine sindinena za iwo amene maso anu akuwanyoza kuti Mulungu sadzawapatsa zokoma zake. Mulungu amadziwa bwinobwino zonse zimene zili m’mitima mwawo, chifukwa nditatero, ndithudi, ine ndidzakhala m’modzi wa anthu olakwa.” قَالُواْ يَٰنُوحُ قَدۡ جَٰدَلۡتَنَا فَأَكۡثَرۡتَ جِدَٰلَنَا فَأۡتِنَا بِمَا تَعِدُنَآ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ ٣٢Iwo anati, “Iwe Nowa! Iwe watsutsana nafe kwambiri. Tsopano bweretsa msangamsanga chilango chimene uli nkutiopsyeza nacho ngati uli mmodzi wa anthu onena zoona!” قَالَ إِنَّمَا يَأۡتِيكُم بِهِ ٱللَّهُ إِن شَآءَ وَمَآ أَنتُم بِمُعۡجِزِينَ ٣٣Iye adati, “Mulungu yekha adzakubweretserani chilango chake pamene Iye afuna. Ndipo inu simudzathawa ai.” وَلَا يَنفَعُكُمۡ نُصۡحِيٓ إِنۡ أَرَدتُّ أَنۡ أَنصَحَ لَكُمۡ إِن كَانَ ٱللَّهُ يُرِيدُ أَن يُغۡوِيَكُمۡۚ هُوَ رَبُّكُمۡ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ ٣٤“Ndiponso ulangizi wanga siudzakuthandizani ngakhale nditafuna kukulangizani ngati chifuniro cha Mulungu ndi kukusocheretsani. Iye ndi Ambuye wanu ndipo ndi kwa Iye mudzabwerera.” أَمۡ يَقُولُونَ ٱفۡتَرَىٰهُۖ قُلۡ إِنِ ٱفۡتَرَيۡتُهُۥ فَعَلَيَّ إِجۡرَامِي وَأَنَا۠ بَرِيٓءٌ مِّمَّا تُجۡرِمُونَ ٣٥Kapena iwo akunena kuti, “Iye wapeka.” Nena, “Ngati ine ndapeka, tchimo ndi langa koma ine ndili nazo kutali zoipa zimene mukuchita.” وَأُوحِيَ إِلَىٰ نُوحٍ أَنَّهُۥ لَن يُؤۡمِنَ مِن قَوۡمِكَ إِلَّا مَن قَدۡ ءَامَنَ فَلَا تَبۡتَئِسۡ بِمَا كَانُواْ يَفۡعَلُونَ ٣٦Ndipo Mau a Mulungu adavumbulutsidwa kwa Nowa ponena kuti: “Palibe mmodzi mwa anthu ako amene adzakhulupirira kupatula okhawo amene akhulupirira kale. Motero usamve chisoni chifukwa cha zimene anali kuchita.” وَٱصۡنَعِ ٱلۡفُلۡكَ بِأَعۡيُنِنَا وَوَحۡيِنَا وَلَا تُخَٰطِبۡنِي فِي ٱلَّذِينَ ظَلَمُوٓاْ إِنَّهُم مُّغۡرَقُونَ ٣٧“Ndipo panga chombo pamaso pathu ndi chilamulo chathu ndipo usalankhule mmalo mwa anthu ochimwa. Ndithudi onse adzamizidwa m’madzi.” وَيَصۡنَعُ ٱلۡفُلۡكَ وَكُلَّمَا مَرَّ عَلَيۡهِ مَلَأٌ مِّن قَوۡمِهِۦ سَخِرُواْ مِنۡهُۚ قَالَ إِن تَسۡخَرُواْ مِنَّا فَإِنَّا نَسۡخَرُ مِنكُمۡ كَمَا تَسۡخَرُونَ ٣٨Pamene iye adayamba kupanga chombo, ndipo nthawi zonse pamene akuluakulu a anthu ake anali kudutsa pafupi ndi iye, iwo amamuchita chipongwe. Iye adati: “Ngati mukutichita chipongwe, nafenso tidzakubwezerani chipongwe monga mmene mukutichitira ife.” فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ مَن يَأۡتِيهِ عَذَابٌ يُخۡزِيهِ وَيَحِلُّ عَلَيۡهِ عَذَابٌ مُّقِيمٌ ٣٩“Ndipo inu mudzadziwa posachedwa yemwe chilango chochititsa manyazi chidzamfikira, ndiponso iwo amene adzalandira chilango chosatha.” حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَ أَمۡرُنَا وَفَارَ ٱلتَّنُّورُ قُلۡنَا ٱحۡمِلۡ فِيهَا مِن كُلٍّ زَوۡجَيۡنِ ٱثۡنَيۡنِ وَأَهۡلَكَ إِلَّا مَن سَبَقَ عَلَيۡهِ ٱلۡقَوۡلُ وَمَنۡ ءَامَنَۚ وَمَآ ءَامَنَ مَعَهُۥٓ إِلَّا قَلِيلٌ ٤٠Kufikira pamene chilamulo chathu chidadza, ndipo nthaka idayamba kutulutsa madzi. Ife tinati: “Lowetsa m’chombo zinthu ziwiriziwiri, (chachimuna ndi chachikazi), anthu a banja lako kupatula iye amene chiweruzo chaperekedwa kale ndi iwo amene akhulupilira. Koma si ambiri amene adali okhulupirira ndi iye kupatula ochepa okha ۞ وَقَالَ ٱرۡكَبُواْ فِيهَا بِسۡمِ ٱللَّهِ مَجۡر۪ىٰهَا وَمُرۡسَىٰهَآۚ إِنَّ رَبِّي لَغَفُورٌ رَّحِيمٌ ٤١Iye adati, “Kwerani m’menemo, M’dzina la Mulungu chidzayenda mnjira yake ndipo chidzaima pamalo pofunikira. Ndithudi Ambuye wanga ndi wokhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha.” وَهِيَ تَجۡرِي بِهِمۡ فِي مَوۡجٍ كَٱلۡجِبَالِ وَنَادَىٰ نُوحٌ ٱبۡنَهُۥ وَكَانَ فِي مَعۡزِلٍ يَٰبُنَيَّ ٱرۡكَب مَّعَنَا وَلَا تَكُن مَّعَ ٱلۡكَٰفِرِينَ ٤٢Motere icho chinayenda pa mafunde okhala ngati mapiri, ndipo Nowa adamuitana mwana wake amene adaima pambali. “oh mwana wanga! Kwerachombopamodzindiifendipousakhalepamodzindi anthu osakhulupirira.” قَالَ سَـَٔاوِيٓ إِلَىٰ جَبَلٍ يَعۡصِمُنِي مِنَ ٱلۡمَآءِۚ قَالَ لَا عَاصِمَ ٱلۡيَوۡمَ مِنۡ أَمۡرِ ٱللَّهِ إِلَّا مَن رَّحِمَۚ وَحَالَ بَيۡنَهُمَا ٱلۡمَوۡجُ فَكَانَ مِنَ ٱلۡمُغۡرَقِينَ ٤٣Iye adati: “Ine ndidzathawira ku phiri limene lidzanditeteza ku chigumula cha madzi.” Nowa adati, “Lero palibe woteteza wina ku lamulo la Mulungu kupatula yekhayo amene Mulungu adzamuonetsera chisomo chake.” Ndipo funde lidatchinga pakati pawo ndipo mwana wa Nowa anali mmodzi wa omizidwa وَقِيلَ يَٰٓأَرۡضُ ٱبۡلَعِي مَآءَكِ وَيَٰسَمَآءُ أَقۡلِعِي وَغِيضَ ٱلۡمَآءُ وَقُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ وَٱسۡتَوَتۡ عَلَى ٱلۡجُودِيِّۖ وَقِيلَ بُعۡدًا لِّلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ ٤٤Ndipo kudanenedwa: “Nthaka meza madzi ako! Ndi kumwamba siya kugwetsa mvula.” Chigumula chinasiya ndipo chifuniro cha Mulungu chinakwaniritsidwa. Ndipo chombo chinadzaima pa phiri la Al Judi ndipo panamveka mawu onena kuti: “Chionongeko chili kwa anthu ochita zoipa.” وَنَادَىٰ نُوحٌ رَّبَّهُۥ فَقَالَ رَبِّ إِنَّ ٱبۡنِي مِنۡ أَهۡلِي وَإِنَّ وَعۡدَكَ ٱلۡحَقُّ وَأَنتَ أَحۡكَمُ ٱلۡحَٰكِمِينَ ٤٥Ndipo Nowa adaitana kwa Ambuye wake nati: “Ambuye! Ndithudi mwana wanga ndi mmodzi wa anthu a banja langa. Lonjezo lanu, ndithudi, ndi loona. Inu ndinu oweruza bwino kuposa oweruza onse.” قَالَ يَٰنُوحُ إِنَّهُۥ لَيۡسَ مِنۡ أَهۡلِكَۖ إِنَّهُۥ عَمَلٌ غَيۡرُ صَٰلِحٍۖ فَلَا تَسۡـَٔلۡنِ مَا لَيۡسَ لَكَ بِهِۦ عِلۡمٌۖ إِنِّيٓ أَعِظُكَ أَن تَكُونَ مِنَ ٱلۡجَٰهِلِينَ ٤٦Mulungu adati: “Iwe Nowa! Ndithudi iye si wabanja lako ayi. Ndithudi ntchito zake si zabwino motero usandifunse zinthu zimene iwe siudziwa. Ndili kukuchenjeza kuti usakhale mugulu la mbuli ayi.” قَالَ رَبِّ إِنِّيٓ أَعُوذُ بِكَ أَنۡ أَسۡـَٔلَكَ مَا لَيۡسَ لِي بِهِۦ عِلۡمٌۖ وَإِلَّا تَغۡفِرۡ لِي وَتَرۡحَمۡنِيٓ أَكُن مِّنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ ٤٧Nowa adati: “Ine ndipempha chitetezo chanu, Ambuye, chifukwa chokupemphani zinthu zimene ine sindili kuzidziwa. Ndipo Inu ngati simundikhululukira ndi kundimvera ine chisoni, ndithudi, ine ndidzakhala mmodzi wa anthu olephera.” قِيلَ يَٰنُوحُ ٱهۡبِطۡ بِسَلَٰمٍ مِّنَّا وَبَرَكَٰتٍ عَلَيۡكَ وَعَلَىٰٓ أُمَمٍ مِّمَّن مَّعَكَۚ وَأُمَمٌ سَنُمَتِّعُهُمۡ ثُمَّ يَمَسُّهُم مِّنَّا عَذَابٌ أَلِيمٌ ٤٨Kudanenedwa: “Iwe Nowa! Tsika pa mtunda ndi mtendere wochokera kwa Ife ndi madalitso akhale kwa iwe ndi kugulu la anthu amene ali nawe, koma anthu onse tidzawasangalatsa pa kanthawi ndipo pambuyo pake chidzawapezanso chilango chowawa chochokera kwa Ife.” تِلۡكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ ٱلۡغَيۡبِ نُوحِيهَآ إِلَيۡكَۖ مَا كُنتَ تَعۡلَمُهَآ أَنتَ وَلَا قَوۡمُكَ مِن قَبۡلِ هَٰذَاۖ فَٱصۡبِرۡۖ إِنَّ ٱلۡعَٰقِبَةَ لِلۡمُتَّقِينَ ٤٩Zimenezi ndi nkhani zobisika zimene tikuvumbulutsa kwa iwe, zimene iwe kapena anthu ako samazidziwa chisanabwere chivumbulutso ichi. Motero pirira. Ndithudi mapeto abwino ndi a iwo amene amuopa Mulungu وَإِلَىٰ عَادٍ أَخَاهُمۡ هُودًاۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥٓۖ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا مُفۡتَرُونَ ٥٠Ndipo kwa mtundu wa Aad, tidatumiza m’bale wawo Hud. Iye adati: “Oh anthu anga! Pembedzani Mulungu. Inu mulibe mulungu wina kupatula Iye yekha. Ndithudi inu simuchita china chili chonse koma kupeka bodza basi.” يَٰقَوۡمِ لَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ أَجۡرًاۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَى ٱلَّذِي فَطَرَنِيٓۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ ٥١“oh anthu anga! Ine sindikukupemphani malipiro pazimenezi. Malipiro anga sali ndi wina koma ali ndi Iye amene adandilenga. Kodi simutha kumva zimenezi?” وَيَٰقَوۡمِ ٱسۡتَغۡفِرُواْ رَبَّكُمۡ ثُمَّ تُوبُوٓاْ إِلَيۡهِ يُرۡسِلِ ٱلسَّمَآءَ عَلَيۡكُم مِّدۡرَارًا وَيَزِدۡكُمۡ قُوَّةً إِلَىٰ قُوَّتِكُمۡ وَلَا تَتَوَلَّوۡاْ مُجۡرِمِينَ ٥٢“oh Anthu anga! Mpempheni Ambuye wanu chikhululukiro ndipo lapani kwa Iye chifukwa Iye adzakutumizirani mvula yambiri ndipo adzakuonjezerani mphamvu pamwamba pa mphamvu zanu. Kotero musatembenuke kukhala anthu oipa.” قَالُواْ يَٰهُودُ مَا جِئۡتَنَا بِبَيِّنَةٍ وَمَا نَحۡنُ بِتَارِكِيٓ ءَالِهَتِنَا عَن قَوۡلِكَ وَمَا نَحۡنُ لَكَ بِمُؤۡمِنِينَ ٥٣Iwo adati, “oh iwe Hud! Iwe siunatibweretsere umboni wokwana. Ndipo ife sitidzasiya kupembedza milungu yathu chifukwa cha mawu ako! Ndipo ife sitikukhulupirira iwe ayi.” إِن نَّقُولُ إِلَّا ٱعۡتَرَىٰكَ بَعۡضُ ءَالِهَتِنَا بِسُوٓءٍۗ قَالَ إِنِّيٓ أُشۡهِدُ ٱللَّهَ وَٱشۡهَدُوٓاْ أَنِّي بَرِيٓءٌ مِّمَّا تُشۡرِكُونَ ٥٤“Zimene tilikunena ndizakuti ina ya milungu yathu yakupatsa iwe tsoka.” Iye adati: “Ndithudi Mulungu ndiye mboni yanga ndipo nanunso chitirani umboni kuti ine ndatalikirana nazo zimene mukamapembedza mulikuonjezera.” مِن دُونِهِۦۖ فَكِيدُونِي جَمِيعًا ثُمَّ لَا تُنظِرُونِ ٥٥“Motero nonsenu konzani chiwembu chanu pa ine ndipo musandichedwetse.” إِنِّي تَوَكَّلۡتُ عَلَى ٱللَّهِ رَبِّي وَرَبِّكُمۚ مَّا مِن دَآبَّةٍ إِلَّا هُوَ ءَاخِذُۢ بِنَاصِيَتِهَآۚ إِنَّ رَبِّي عَلَىٰ صِرَٰطٍ مُّسۡتَقِيمٍ ٥٦“Ine ndaika chikhulupiliro changa mwa Mulungu, Ambuye wanga ndiponso Ambuye wanu. Palibe chinthu cha moyo pa dziko lapansi chimene tsogolo lake sililamulidwa ndi Iye. Ndithudi Ambuye wanga ndi amene ali pa njira yoyenera.” فَإِن تَوَلَّوۡاْ فَقَدۡ أَبۡلَغۡتُكُم مَّآ أُرۡسِلۡتُ بِهِۦٓ إِلَيۡكُمۡۚ وَيَسۡتَخۡلِفُ رَبِّي قَوۡمًا غَيۡرَكُمۡ وَلَا تَضُرُّونَهُۥ شَيۡـًٔاۚ إِنَّ رَبِّي عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ حَفِيظٌ ٥٧“Ndipo ngati mutembenuka, ine ndakuuzani Uthenga umene ndatumizidwa kwa inu. Ambuye wanga adzaika, m’malo mwanu, anthu ena ndipo inu simungamuchite chinthu choipa chilichonse. Ndithudi Ambuye wanga ndi Msungi wa zinthu zonse.” وَلَمَّا جَآءَ أَمۡرُنَا نَجَّيۡنَا هُودًا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَهُۥ بِرَحۡمَةٍ مِّنَّا وَنَجَّيۡنَٰهُم مِّنۡ عَذَابٍ غَلِيظٍ ٥٨Ndipo pamene chiweruzo chathu chidadza, Ife tidamupulumutsa Hud, kudzera mu Chisomo chathu, pamodzi ndi amene adakhulupirira ndi iye. Ife tidawapulumutsa ku chilango chokhwima وَتِلۡكَ عَادٌۖ جَحَدُواْ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِمۡ وَعَصَوۡاْ رُسُلَهُۥ وَٱتَّبَعُوٓاْ أَمۡرَ كُلِّ جَبَّارٍ عَنِيدٍ ٥٩Amenewa anali anthu a Aad. Iwo adakana Mawu a Ambuye wawo, ndipo adanyoza Atumwi ake ndipo anatsata malamulo a atsogoleri awo a nkhanza ndi okana chilungamo وَأُتۡبِعُواْ فِي هَٰذِهِ ٱلدُّنۡيَا لَعۡنَةً وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۗ أَلَآ إِنَّ عَادًا كَفَرُواْ رَبَّهُمۡۗ أَلَا بُعۡدًا لِّعَادٍ قَوۡمِ هُودٍ ٦٠Ndipo iwo adatsatiridwa ndi temberero m’dziko lino ndipo adzakhala otembereredwa pa tsiku la chiweruzo. Mosakaika, ndithudi, anthu a Ad adamukana Ambuye wawo. Motero tinathana nawo Ad, anthu a Hud ۞ وَإِلَىٰ ثَمُودَ أَخَاهُمۡ صَٰلِحًاۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥۖ هُوَ أَنشَأَكُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ وَٱسۡتَعۡمَرَكُمۡ فِيهَا فَٱسۡتَغۡفِرُوهُ ثُمَّ تُوبُوٓاْ إِلَيۡهِۚ إِنَّ رَبِّي قَرِيبٌ مُّجِيبٌ ٦١Ndipo kwa Thamoud, tidatumiza m’bale wawo Saleh. Iye adati: “Oh anthu anga! Mpembedzeni Mulungu, chifukwa inu mulibe mulungu wina kupatula Iye yekha. Iye ndiye amene adakulengani inu kuchokera ku nthaka, ndipo adakupatsani inu malo okhala pa nthakayo. Motero funani chikhululukiro kwa Iye ndipo idzani kwa Iye ndi kulapa. Ndithudi Ambuye wanga ali pafupi nanu ndipo Iye adzamva mapemphero anu.” قَالُواْ يَٰصَٰلِحُ قَدۡ كُنتَ فِينَا مَرۡجُوًّا قَبۡلَ هَٰذَآۖ أَتَنۡهَىٰنَآ أَن نَّعۡبُدَ مَا يَعۡبُدُ ءَابَآؤُنَا وَإِنَّنَا لَفِي شَكٍّ مِّمَّا تَدۡعُونَآ إِلَيۡهِ مُرِيبٍ ٦٢Iwo adati: “Iwe Saleh! Ndithudi iwe wakhala pakati pathu ndipo udali chiyembekezo chathu. Kodi iwe utiletsa kupembedza zimene amapembedza makolo athu? Ndithudi ife tili ndi chikaiko chambiri ndi chipembedzo chimene uli kutiitanira.” قَالَ يَٰقَوۡمِ أَرَءَيۡتُمۡ إِن كُنتُ عَلَىٰ بَيِّنَةٍ مِّن رَّبِّي وَءَاتَىٰنِي مِنۡهُ رَحۡمَةً فَمَن يَنصُرُنِي مِنَ ٱللَّهِ إِنۡ عَصَيۡتُهُۥۖ فَمَا تَزِيدُونَنِي غَيۡرَ تَخۡسِيرٍ ٦٣Iye adati: “Oh anthu anga! Ndiuzeni ngati ine ndili ndi umboni wokwanira wochokera kwa Ambuye wanga ndipo Iye wandipatsa chisomo kuchokera kwa Iye, ndani angandipulumutse ine kuchokera ku chilango cha Mulungu ngati nditamunyoza? Inu simungaonjezere china chilichonse kwa ine koma kutayika.” وَيَٰقَوۡمِ هَٰذِهِۦ نَاقَةُ ٱللَّهِ لَكُمۡ ءَايَةًۖ فَذَرُوهَا تَأۡكُلۡ فِيٓ أَرۡضِ ٱللَّهِۖ وَلَا تَمَسُّوهَا بِسُوٓءٍ فَيَأۡخُذَكُمۡ عَذَابٌ قَرِيبٌ ٦٤“Oh Anthu anga! Iyi ndi Ngamira yaikazi, mwini wake ndi Mulungu, ndipo ndi chizindikiro chooneka kwa inu. Isiyeni kuti izidya mwachifuniro cha Mulungu m’dziko lake ndipo musaizunze chifukwa chilango chingadze pa inu mwamsanga.” فَعَقَرُوهَا فَقَالَ تَمَتَّعُواْ فِي دَارِكُمۡ ثَلَٰثَةَ أَيَّامٍۖ ذَٰلِكَ وَعۡدٌ غَيۡرُ مَكۡذُوبٍ ٦٥Koma iwo adaipha ngamirayo ndipo iye adati: “Inu basangalalani m’nyumba zanu masiku atatu. Chimenecho ndi chipangano chimene sichili chabodza.” فَلَمَّا جَآءَ أَمۡرُنَا نَجَّيۡنَا صَٰلِحًا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَهُۥ بِرَحۡمَةٍ مِّنَّا وَمِنۡ خِزۡيِ يَوۡمِئِذٍۚ إِنَّ رَبَّكَ هُوَ ٱلۡقَوِيُّ ٱلۡعَزِيزُ ٦٦Ndipo pamene chiweruzo chathu chimadza, Ife tinamupulumutsa Saleh pamodzi ndi amene adakhulupirira ndi iye kudzera m’Chisomo chathu, kuchokera m’masautso a tsiku limeneli. Ndithudi Ambuye wako ndi wanyonga, ndi wopambana وَأَخَذَ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ ٱلصَّيۡحَةُ فَأَصۡبَحُواْ فِي دِيَٰرِهِمۡ جَٰثِمِينَ ٦٧Ndipo mkuwo wowopsa udawaononga anthu ochita zoipa ndipo anthu onse adali lambilambi m’nyumba zawo atafa كَأَن لَّمۡ يَغۡنَوۡاْ فِيهَآۗ أَلَآ إِنَّ ثَمُودَاْ كَفَرُواْ رَبَّهُمۡۗ أَلَا بُعۡدًا لِّثَمُودَ ٦٨Kukhala ngati sadakhalepo pa malo amenewo. Mosakaika, ndithudi, a Thamoud sadakhulupirire mwa Ambuye wawo. Motero anatha anthu a Thamoud وَلَقَدۡ جَآءَتۡ رُسُلُنَآ إِبۡرَٰهِيمَ بِٱلۡبُشۡرَىٰ قَالُواْ سَلَٰمًاۖ قَالَ سَلَٰمٌۖ فَمَا لَبِثَ أَن جَآءَ بِعِجۡلٍ حَنِيذٍ ٦٩Ndithudi Atumwi athu adadza kwa Abrahamu ndi nkhani yabwino. Iwo adati: “Mtendere!” Iye anayankha: “Mtendere” ndipo posakhalitsa iye adabweretsa nyama ya ng’ombe yowotcha فَلَمَّا رَءَآ أَيۡدِيَهُمۡ لَا تَصِلُ إِلَيۡهِ نَكِرَهُمۡ وَأَوۡجَسَ مِنۡهُمۡ خِيفَةًۚ قَالُواْ لَا تَخَفۡ إِنَّآ أُرۡسِلۡنَآ إِلَىٰ قَوۡمِ لُوطٍ ٧٠Ndipo pamene iye adaona kuti manja awo sakukhudza nyamayo adawadabwa, nachita mantha. Iwo adati: “Usaope. Ife tatumidwa kwa anthu a Loti.” وَٱمۡرَأَتُهُۥ قَآئِمَةٌ فَضَحِكَتۡ فَبَشَّرۡنَٰهَا بِإِسۡحَٰقَ وَمِن وَرَآءِ إِسۡحَٰقَ يَعۡقُوبَ ٧١Ndipo mkazi wake adali chiimire pompo, naseka. Ife tidamuuza kuti adzabereka Isake ndipo kuti Isake adzabala Yakobo قَالَتۡ يَٰوَيۡلَتَىٰٓ ءَأَلِدُ وَأَنَا۠ عَجُوزٌ وَهَٰذَا بَعۡلِي شَيۡخًاۖ إِنَّ هَٰذَا لَشَيۡءٌ عَجِيبٌ ٧٢Iye adati: “Kalanga ine! Kodi ine ndingabereke pamene ndine wokalamba ndipo mwamuna wanga ndi wokalambanso? Ndithudi ichi ndi chinthu chododometsa.” قَالُوٓاْ أَتَعۡجَبِينَ مِنۡ أَمۡرِ ٱللَّهِۖ رَحۡمَتُ ٱللَّهِ وَبَرَكَٰتُهُۥ عَلَيۡكُمۡ أَهۡلَ ٱلۡبَيۡتِۚ إِنَّهُۥ حَمِيدٌ مَّجِيدٌ ٧٣Iwo adati: “Kodi iwe uli kuwadabwa malamulo a Mulungu? Madalitso ndi chisomo cha Mulungu chikhale pa inu a m’banja la Abrahamu. Ndithudi Iye ndi wotamandidwa ndiponso wolemekezeka.” فَلَمَّا ذَهَبَ عَنۡ إِبۡرَٰهِيمَ ٱلرَّوۡعُ وَجَآءَتۡهُ ٱلۡبُشۡرَىٰ يُجَٰدِلُنَا فِي قَوۡمِ لُوطٍ ٧٤Ndipo pamene Abrahamu adamuchoka mantha ndi kumfikirankhaniyabwino, iyeadatifunsa Ifezaanthua Loti إِنَّ إِبۡرَٰهِيمَ لَحَلِيمٌ أَوَّٰهٌ مُّنِيبٌ ٧٥Ndithudi Abrahamu anali woleza mtima, wodzichepetsa ndiponso munthu wodzipereka kwa Mulungu يَٰٓإِبۡرَٰهِيمُ أَعۡرِضۡ عَنۡ هَٰذَآۖ إِنَّهُۥ قَدۡ جَآءَ أَمۡرُ رَبِّكَۖ وَإِنَّهُمۡ ءَاتِيهِمۡ عَذَابٌ غَيۡرُ مَرۡدُودٍ ٧٦Angelo adati: “Iwe Abrahamu! Siya zimenezo. Ndithudi lamulo la Ambuye wako ladza. Ndithudi kudzadza chilango kwa iwo chimene sichingaletsedwe.” وَلَمَّا جَآءَتۡ رُسُلُنَا لُوطًا سِيٓءَ بِهِمۡ وَضَاقَ بِهِمۡ ذَرۡعًا وَقَالَ هَٰذَا يَوۡمٌ عَصِيبٌ ٧٧Ndipo pamene Atumwi athu adadza kwa Loti, iye adali wodandaula kwambiri ndi kubanika mumtima chifukwa cha iwo. Ndipo adati: “Ndithudi ili ndi tsiku loopsa.” وَجَآءَهُۥ قَوۡمُهُۥ يُهۡرَعُونَ إِلَيۡهِ وَمِن قَبۡلُ كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ٱلسَّيِّـَٔاتِۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ هَٰٓؤُلَآءِ بَنَاتِي هُنَّ أَطۡهَرُ لَكُمۡۖ فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَلَا تُخۡزُونِ فِي ضَيۡفِيٓۖ أَلَيۡسَ مِنكُمۡ رَجُلٌ رَّشِيدٌ ٧٨Anthu ake adadza kwa iye akuthamanga ndipo pambuyo adali kuchita zinthu zoipa. Iye adati: “Oh! Anthu anga, awa ndi ana anga akazi, amene ali oyera kwa inu. Opani Mulungu ndipo musandiyalutse kwa alendo anga. Kodi palibe pakati panu munthu mmodzi wangwiro?” قَالُواْ لَقَدۡ عَلِمۡتَ مَا لَنَا فِي بَنَاتِكَ مِنۡ حَقٍّ وَإِنَّكَ لَتَعۡلَمُ مَا نُرِيدُ ٧٩Iwo adati: “Iwe ukudziwa kuti tilibe khumbo mu ana ako akazi ayi. Ndiponso iwe ukudziwa zimene tikufuna.” قَالَ لَوۡ أَنَّ لِي بِكُمۡ قُوَّةً أَوۡ ءَاوِيٓ إِلَىٰ رُكۡنٍ شَدِيدٍ ٨٠Iye adati: “Ine ndikadakhala ndi mphamvu zoti ndikugonjetseni kapena ndikanapeza munthu wina wamphamvu zambiri ndikadamenyana nanu.” قَالُواْ يَٰلُوطُ إِنَّا رُسُلُ رَبِّكَ لَن يَصِلُوٓاْ إِلَيۡكَۖ فَأَسۡرِ بِأَهۡلِكَ بِقِطۡعٍ مِّنَ ٱلَّيۡلِ وَلَا يَلۡتَفِتۡ مِنكُمۡ أَحَدٌ إِلَّا ٱمۡرَأَتَكَۖ إِنَّهُۥ مُصِيبُهَا مَآ أَصَابَهُمۡۚ إِنَّ مَوۡعِدَهُمُ ٱلصُّبۡحُۚ أَلَيۡسَ ٱلصُّبۡحُ بِقَرِيبٍ ٨١Iwo adati: “Iwe Loti! Ndithudi ife ndife Atumwi Ambuye wako, iwo sakukhudza, choka pamodzi ndi anthu ako pakati pa usiku. Ndipo usalole wina wa inu kuti ayang’ane m’mbuyo kupatula mkazi wako, ndithudi, adzaona zonse zimene ena adzaone. Ndithudi lonjezo lawo ndi m’mamawa. Kodi m’mawa si pafupi?” فَلَمَّا جَآءَ أَمۡرُنَا جَعَلۡنَا عَٰلِيَهَا سَافِلَهَا وَأَمۡطَرۡنَا عَلَيۡهَا حِجَارَةً مِّن سِجِّيلٍ مَّنضُودٍ ٨٢Ndipo pamene chilamulo chathu chidadza, Ife tidatembenuza pamwamba pa Mzinda kukhala pansi ndipo tidagwetsa pa iwo miyala youmbidwa ndi nthaka ya makande younjikika مُّسَوَّمَةً عِندَ رَبِّكَۖ وَمَا هِيَ مِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ بِبَعِيدٍ ٨٣Yokhala ndi zizindikiro, yochokera kwa Ambuye wako ndipo iyo siili kutali ndi anthu wosalungama ۞ وَإِلَىٰ مَدۡيَنَ أَخَاهُمۡ شُعَيۡبًاۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥۖ وَلَا تَنقُصُواْ ٱلۡمِكۡيَالَ وَٱلۡمِيزَانَۖ إِنِّيٓ أَرَىٰكُم بِخَيۡرٍ وَإِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُمۡ عَذَابَ يَوۡمٍ مُّحِيطٍ ٨٤Ndipo kwa anthu a ku Midiyani tidawatumizira m’bale wawo Shoaib. Iye adati: “oh Anthu anga! Pembedzani Mulungu, chifukwa inu mulibe mulungu wina koma Mulungu mmodzi yekha ndipo musapungule miyeso ya zinthu. Ine ndikuona kuti inu ndinu anthu a chuma. Ine, ndithudi, ndili kuchita mantha ndi chilango cha tsiku limene lidzakuzungulirani inu.” وَيَٰقَوۡمِ أَوۡفُواْ ٱلۡمِكۡيَالَ وَٱلۡمِيزَانَ بِٱلۡقِسۡطِۖ وَلَا تَبۡخَسُواْ ٱلنَّاسَ أَشۡيَآءَهُمۡ وَلَا تَعۡثَوۡاْ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُفۡسِدِينَ ٨٥“Anthu anga! Kwaniritsani muyeso wa zinthu ndipo yesani mwachilungamo ndipo musawapungulire anthu katundu wawo ndipo musachite zoipa padziko ndikuyambitsa chisokonezo.” بَقِيَّتُ ٱللَّهِ خَيۡرٌ لَّكُمۡ إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَۚ وَمَآ أَنَا۠ عَلَيۡكُم بِحَفِيظٍ ٨٦“Zimene Mulungu wakusiyirani inu ndi zimene zili zabwino kwa inu ngati muli okhulupirira. Ndipo ine sindine wokuyang’anirani ayi.” قَالُواْ يَٰشُعَيۡبُ أَصَلَوٰتُكَ تَأۡمُرُكَ أَن نَّتۡرُكَ مَا يَعۡبُدُ ءَابَآؤُنَآ أَوۡ أَن نَّفۡعَلَ فِيٓ أَمۡوَٰلِنَا مَا نَشَٰٓؤُاْۖ إِنَّكَ لَأَنتَ ٱلۡحَلِيمُ ٱلرَّشِيدُ ٨٧Iwo adati: “Iwe Shoaib! Kodi mapemphero ako akulamulira kuti ife tiyenera kuleka kupembedza milungu ya makolo athu kapena kuti sitiyenera kuchita zimene tifuna ndi chuma chathu? Ndithudi iwe ndiwe wopirira ndiponso wa nzeru zokhazikika.” قَالَ يَٰقَوۡمِ أَرَءَيۡتُمۡ إِن كُنتُ عَلَىٰ بَيِّنَةٍ مِّن رَّبِّي وَرَزَقَنِي مِنۡهُ رِزۡقًا حَسَنًاۚ وَمَآ أُرِيدُ أَنۡ أُخَالِفَكُمۡ إِلَىٰ مَآ أَنۡهَىٰكُمۡ عَنۡهُۚ إِنۡ أُرِيدُ إِلَّا ٱلۡإِصۡلَٰحَ مَا ٱسۡتَطَعۡتُۚ وَمَا تَوۡفِيقِيٓ إِلَّا بِٱللَّهِۚ عَلَيۡهِ تَوَكَّلۡتُ وَإِلَيۡهِ أُنِيبُ ٨٨Iye adati: “Ndiuzeni! Ngati ine ndili ndi umboni woonekera wochokera kwa Ambuye wanga ndipo Iye wandipatsa gawo labwino. Ine sindifuna kusemphana nanu pochita chinthu chimene ndili kukuletsani. Palibe chilichonse chimene ndifuna koma kukonza mmene ndingathere. Ndipo ulangizi wanga siubwera kuchokera kwa wina aliyense kupatula Mulungu. Mwa Iye ndaika chikhulupiriro changa ndipo kwa Iye ndiko ndimalapa.” وَيَٰقَوۡمِ لَا يَجۡرِمَنَّكُمۡ شِقَاقِيٓ أَن يُصِيبَكُم مِّثۡلُ مَآ أَصَابَ قَوۡمَ نُوحٍ أَوۡ قَوۡمَ هُودٍ أَوۡ قَوۡمَ صَٰلِحٍۚ وَمَا قَوۡمُ لُوطٍ مِّنكُم بِبَعِيدٍ ٨٩“Oh anthu anga! Musalole kuti kusagwirizana kwanu ndi ine kuti kubweretse pa inu mavuto amene adadza pa anthu a Nowa, kapena pa anthu a Hud ndi Saleh ndiponso sikale pamene anthu a Loti adaonongeka.” وَٱسۡتَغۡفِرُواْ رَبَّكُمۡ ثُمَّ تُوبُوٓاْ إِلَيۡهِۚ إِنَّ رَبِّي رَحِيمٌ وَدُودٌ ٩٠“Ndipo funani chikhululukiro cha Ambuye wanu, ndiponso lapani kwa Iye. Ndithudi Ambuye wanga ndi wa Chisoni ndiponso wa Chikondi chosatha.” قَالُواْ يَٰشُعَيۡبُ مَا نَفۡقَهُ كَثِيرًا مِّمَّا تَقُولُ وَإِنَّا لَنَرَىٰكَ فِينَا ضَعِيفًاۖ وَلَوۡلَا رَهۡطُكَ لَرَجَمۡنَٰكَۖ وَمَآ أَنتَ عَلَيۡنَا بِعَزِيزٍ ٩١Iwo adati: “Oh Shoaib! Zambiri zimene unena ife sitili kuzizindikira ndipo ife tili kuona kuti ulibe mphamvu pakati pathu. Pakadapanda mtundu wako, ndithudi, ife tikadakuponya miyala ndiponso iwe ulibe mphamvu zoposa zathu.” قَالَ يَٰقَوۡمِ أَرَهۡطِيٓ أَعَزُّ عَلَيۡكُم مِّنَ ٱللَّهِ وَٱتَّخَذۡتُمُوهُ وَرَآءَكُمۡ ظِهۡرِيًّاۖ إِنَّ رَبِّي بِمَا تَعۡمَلُونَ مُحِيطٌ ٩٢Iye adati: “oh anthu anga! Kodi mtundu wanga ndi olemekezeka kwambiri kuposa Mulungu? Ndipo inu mwamuponya Iye kumbuyo kwanu? Ndithudi Ambuye wanga ndi wodziwa zonse zimene muchita.” وَيَٰقَوۡمِ ٱعۡمَلُواْ عَلَىٰ مَكَانَتِكُمۡ إِنِّي عَٰمِلٌۖ سَوۡفَ تَعۡلَمُونَ مَن يَأۡتِيهِ عَذَابٌ يُخۡزِيهِ وَمَنۡ هُوَ كَٰذِبٌۖ وَٱرۡتَقِبُوٓاْ إِنِّي مَعَكُمۡ رَقِيبٌ ٩٣“oh anthu anga! Chitani chimene mufuna kuti muchite, nanenso ndidzachita zanga. Inu mudzadziwa kuti ndani adzalangidwa ndi chilango chochititsa manyazi ndiponso kuti kodi ndani amene ali kunama! Ndithudi dikirani nanenso ndili kudikira pamodzi ndi inu.” وَلَمَّا جَآءَ أَمۡرُنَا نَجَّيۡنَا شُعَيۡبًا وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مَعَهُۥ بِرَحۡمَةٍ مِّنَّا وَأَخَذَتِ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ ٱلصَّيۡحَةُ فَأَصۡبَحُواْ فِي دِيَٰرِهِمۡ جَٰثِمِينَ ٩٤Ndipo pamene lamulo lathu lidadza tidamupulumutsa Shoaib, pamodzi ndi anzake onse amene anali wokhulupirira mwa chisomo chathu. Ndipo mkuwo waukulu udawaononga anthu onse ochita zoipa ndipo onse adali lambilambi m’nyumba zawo كَأَن لَّمۡ يَغۡنَوۡاْ فِيهَآۗ أَلَا بُعۡدًا لِّمَدۡيَنَ كَمَا بَعِدَتۡ ثَمُودُ ٩٥Kukhala ngati iwo sadakhalemo m’menemo! Motero adaonongeka anthu a ku Midiyani monga momwe adaonongekera anthu a ku Thamoud وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَا وَسُلۡطَٰنٍ مُّبِينٍ ٩٦Zoonadi tidamutumiza Mose ndi zizindikiro zathu ndiponso umboni wooneka إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ فَٱتَّبَعُوٓاْ أَمۡرَ فِرۡعَوۡنَۖ وَمَآ أَمۡرُ فِرۡعَوۡنَ بِرَشِيدٍ ٩٧Kwa Farao ndi nduna zake, iwo anatsatira malamulo a Farao ndipo malamulo a Farao sanali olungama يَقۡدُمُ قَوۡمَهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فَأَوۡرَدَهُمُ ٱلنَّارَۖ وَبِئۡسَ ٱلۡوِرۡدُ ٱلۡمَوۡرُودُ ٩٨Iye adzawatsogolera anthu ake pa tsiku la chiweruzo ndipo adzawalowetsa ku moto. Aipirenji malo omwe adatengedwerako وَأُتۡبِعُواْ فِي هَٰذِهِۦ لَعۡنَةً وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ بِئۡسَ ٱلرِّفۡدُ ٱلۡمَرۡفُودُ ٩٩Ndipo anatsatiridwa ndi matemberero m’moyo wa m’dziko lino ndi patsiku la chiweruzo. Iyipirenji mphotho yomwe adzapatsidwe ذَٰلِكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ ٱلۡقُرَىٰ نَقُصُّهُۥ عَلَيۡكَۖ مِنۡهَا قَآئِمٌ وَحَصِيدٌ ١٠٠Iyi ndi nkhani, ya m’mizinda imene tinaononga ndipo tili kukufotokozera iwe, ndipo ina mwa Mizindayo ilipo pamene ina idaonongeka وَمَا ظَلَمۡنَٰهُمۡ وَلَٰكِن ظَلَمُوٓاْ أَنفُسَهُمۡۖ فَمَآ أَغۡنَتۡ عَنۡهُمۡ ءَالِهَتُهُمُ ٱلَّتِي يَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مِن شَيۡءٍ لَّمَّا جَآءَ أَمۡرُ رَبِّكَۖ وَمَا زَادُوهُمۡ غَيۡرَ تَتۡبِيبٍ ١٠١Ife sitinawapondereze ayi koma adadzipondereza okha. Motero milungu yawo imene analikuipembedzakuonjezerapa Mulungusiidawathandize chilichonse pamene chiweruzo cha Ambuye wako chidadza ndiponso milungu yawo sidawaonjezere kalikonse koma chionongeko وَكَذَٰلِكَ أَخۡذُ رَبِّكَ إِذَآ أَخَذَ ٱلۡقُرَىٰ وَهِيَ ظَٰلِمَةٌۚ إِنَّ أَخۡذَهُۥٓ أَلِيمٌ شَدِيدٌ ١٠٢Chimenecho ndicho chilango cha Ambuye wako akafuna kulanga mzinda wa anthu ochita zoipa. Ndithudi chilango chake ndi chokhwima ndi chowawa kwambiri إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةً لِّمَنۡ خَافَ عَذَابَ ٱلۡأٓخِرَةِۚ ذَٰلِكَ يَوۡمٌ مَّجۡمُوعٌ لَّهُ ٱلنَّاسُ وَذَٰلِكَ يَوۡمٌ مَّشۡهُودٌ ١٠٣Ndithudi mu izo muli chizindikiro kwa iye amene aopa chilango cha moyo umene uli nkudza. Ndi tsiku limene anthu onse adzasonkhanitsidwa pamodzi ndiponso ili ndi tsiku lomwe chilichonse chidzakhalapo وَمَا نُؤَخِّرُهُۥٓ إِلَّا لِأَجَلٍ مَّعۡدُودٍ ١٠٤Ife tili kulichedwetsa mpaka pa nthawi yokhazikitsidwa يَوۡمَ يَأۡتِ لَا تَكَلَّمُ نَفۡسٌ إِلَّا بِإِذۡنِهِۦۚ فَمِنۡهُمۡ شَقِيٌّ وَسَعِيدٌ ١٠٥Ndipo pamene tsikuli lidza, palibe munthu amene adzalankhula opanda chilolezo cha Mulungu. Ena a iwo adzakhala a tsoka pamene ena adzakhala amwayi فَأَمَّا ٱلَّذِينَ شَقُواْ فَفِي ٱلنَّارِ لَهُمۡ فِيهَا زَفِيرٌ وَشَهِيقٌ ١٠٦Akhala iwo amene adzakhala a tsoka, iwo akakhala m’moto ali kubuula mokweza ndiponso motsitsa خَٰلِدِينَ فِيهَا مَا دَامَتِ ٱلسَّمَٰوَٰتُ وَٱلۡأَرۡضُ إِلَّا مَا شَآءَ رَبُّكَۚ إِنَّ رَبَّكَ فَعَّالٌ لِّمَا يُرِيدُ ١٠٧Iwo adzakhala komweko mpaka pamene kumwamba ndi dziko lapansi zidzakhale zilipobe kupatula ngati Ambuye wako afuna kusintha. Ndithudi Ambuye wako amachita zimene afuna ۞ وَأَمَّا ٱلَّذِينَ سُعِدُواْ فَفِي ٱلۡجَنَّةِ خَٰلِدِينَ فِيهَا مَا دَامَتِ ٱلسَّمَٰوَٰتُ وَٱلۡأَرۡضُ إِلَّا مَا شَآءَ رَبُّكَۖ عَطَآءً غَيۡرَ مَجۡذُوذٍ ١٠٨Akakhala anthu odala, iwo adzakhala ku Paradiso mpaka pamene kumwamba ndi dziko lapansi zidzakhale zilipobe kupatula ngati Ambuye wako afuna kusintha, mphatso yosatha mpaka kalekale فَلَا تَكُ فِي مِرۡيَةٍ مِّمَّا يَعۡبُدُ هَٰٓؤُلَآءِۚ مَا يَعۡبُدُونَ إِلَّا كَمَا يَعۡبُدُ ءَابَآؤُهُم مِّن قَبۡلُۚ وَإِنَّا لَمُوَفُّوهُمۡ نَصِيبَهُمۡ غَيۡرَ مَنقُوصٍ ١٠٩Motero usakaike pa zimene anthu awa apembedza. Iwo sali kupembedza koma kungotsatira mmene makolo awo amapembedzera kale. Ndipo ndithudi Ife tidzawalipira malipiro awo mopanda kuchepetsa وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ فَٱخۡتُلِفَ فِيهِۚ وَلَوۡلَا كَلِمَةٌ سَبَقَتۡ مِن رَّبِّكَ لَقُضِيَ بَيۡنَهُمۡۚ وَإِنَّهُمۡ لَفِي شَكٍّ مِّنۡهُ مُرِيبٍ ١١٠Ndithudi Ife tidamupatsa Mose Buku koma mikangano inabuka pakati pawo ndipo kukadapanda kuti liwu lochokera kwa Ambuye wako lidatsogola kale, lamulo likadadza pa iwo. Ndithudi iwo ndi okaika kwambiri za ili وَإِنَّ كُلًّا لَّمَّا لَيُوَفِّيَنَّهُمۡ رَبُّكَ أَعۡمَٰلَهُمۡۚ إِنَّهُۥ بِمَا يَعۡمَلُونَ خَبِيرٌ ١١١Ndithudi Ambuye wako adzalipira anthu molingana ndi ntchito zawo. Ndithudi Iye amadziwa zonse zimene akuchita فَٱسۡتَقِمۡ كَمَآ أُمِرۡتَ وَمَن تَابَ مَعَكَ وَلَا تَطۡغَوۡاْۚ إِنَّهُۥ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٌ ١١٢Motero pitiriza kukhala m’njira yoyenera monga momwe walamulidwira pamodzi ndi onse amene alapa pamodzi ndi iwe ndipo usapyole malire. Ndithudi Iye amaona zonse zimene mumachita وَلَا تَرۡكَنُوٓاْ إِلَى ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ فَتَمَسَّكُمُ ٱلنَّارُ وَمَا لَكُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ مِنۡ أَوۡلِيَآءَ ثُمَّ لَا تُنصَرُونَ ١١٣Ndipo usatsatire anthu ochita zoipa chifukwa moto ungakupezeni ndiponso palibe wina wokuthandizani kupatula Mulungu ndiponso palibe wokuthandizani وَأَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ طَرَفَيِ ٱلنَّهَارِ وَزُلَفًا مِّنَ ٱلَّيۡلِۚ إِنَّ ٱلۡحَسَنَٰتِ يُذۡهِبۡنَ ٱلسَّيِّـَٔاتِۚ ذَٰلِكَ ذِكۡرَىٰ لِلذَّٰكِرِينَ ١١٤Ndipo chita mapemphero ako nthawi ziwiri za masana ndi m’maola oyambirira a usiku. Ndithudi ntchito zabwino zimafafaniza machimo. Chimenechi ndi chikumbutso kwa anthu okumbukira وَٱصۡبِرۡ فَإِنَّ ٱللَّهَ لَا يُضِيعُ أَجۡرَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ ١١٥Kotero pirira. Ndithudi Mulungu sasokoneza mphotho ya ochita zabwino فَلَوۡلَا كَانَ مِنَ ٱلۡقُرُونِ مِن قَبۡلِكُمۡ أُوْلُواْ بَقِيَّةٍ يَنۡهَوۡنَ عَنِ ٱلۡفَسَادِ فِي ٱلۡأَرۡضِ إِلَّا قَلِيلًا مِّمَّنۡ أَنجَيۡنَا مِنۡهُمۡۗ وَٱتَّبَعَ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ مَآ أُتۡرِفُواْ فِيهِ وَكَانُواْ مُجۡرِمِينَ ١١٦Kukadakhala kuti pakati pa mibadwo imene inalipo kale, panali anthu a nzeru oletsa anthu kuchita zoipa padziko lapansi kupatula owerengeka amene Ife tidawapulumutsa pakati pawo. Iwo amene amachita zoipa anali kutsatira zokoma za m’moyo uno ndipo adali kupitiliza kuchita zoipa وَمَا كَانَ رَبُّكَ لِيُهۡلِكَ ٱلۡقُرَىٰ بِظُلۡمٍ وَأَهۡلُهَا مُصۡلِحُونَ ١١٧Ndipo sizinali koyenera kuti Ambuye wako aononge mizinda mwankhanza pamene anthu ake anali kuchita zabwino وَلَوۡ شَآءَ رَبُّكَ لَجَعَلَ ٱلنَّاسَ أُمَّةً وَٰحِدَةًۖ وَلَا يَزَالُونَ مُخۡتَلِفِينَ ١١٨Ndipo Ambuye wako akadafuna, ndithudi, akadawapanga anthu onse kukhala a chipembedzo chimodzi koma akadapitiriza kukhala osiyana إِلَّا مَن رَّحِمَ رَبُّكَۚ وَلِذَٰلِكَ خَلَقَهُمۡۗ وَتَمَّتۡ كَلِمَةُ رَبِّكَ لَأَمۡلَأَنَّ جَهَنَّمَ مِنَ ٱلۡجِنَّةِ وَٱلنَّاسِ أَجۡمَعِينَ ١١٩Kupatula yekhayo amene Ambuye wako wamuonetsera chisomo chake ndipo ndicho chifukwa chake chimene Mulungu adawalengera. Mawu a Ambuye wako adzakwaniritsidwa “Ndithudi Ine ndidzadzadza Gahena ndi Majini ndi anthu onse pamodzi.” وَكُلًّا نَّقُصُّ عَلَيۡكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ ٱلرُّسُلِ مَا نُثَبِّتُ بِهِۦ فُؤَادَكَۚ وَجَآءَكَ فِي هَٰذِهِ ٱلۡحَقُّ وَمَوۡعِظَةٌ وَذِكۡرَىٰ لِلۡمُؤۡمِنِينَ ١٢٠Ndipo zonse zimene tili kukuuza iwe za nkhani za Atumwi ndi kulimbikitsa mtima wako. Kudzera mu izi choonadi ndi ulangizi wadza kwa iwe ndiponso uthenga wa chikumbutso kwa anthu okhulupirira وَقُل لِّلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ ٱعۡمَلُواْ عَلَىٰ مَكَانَتِكُمۡ إِنَّا عَٰمِلُونَ ١٢١Auze anthu osakhulupirira kuti: “Chitani mmene mungathere, nafenso tidzachita chimodzimodzi.” وَٱنتَظِرُوٓاْ إِنَّا مُنتَظِرُونَ ١٢٢dikirani! Ndithudi nafenso tili kudikira وَلِلَّهِ غَيۡبُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَإِلَيۡهِ يُرۡجَعُ ٱلۡأَمۡرُ كُلُّهُۥ فَٱعۡبُدۡهُ وَتَوَكَّلۡ عَلَيۡهِۚ وَمَا رَبُّكَ بِغَٰفِلٍ عَمَّا تَعۡمَلُونَ ١٢٣Zobisika zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi za Mulungu ndipo zonse zimabwerera kwa Iye. Motero mpembedzeni Iye ndipo ika chikhulupiriro chako mwa Iye. Ambuye wako saiwala zimene mukuchita

الترجمة: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.