ملة الإسلام

السورة 71 · 28 آية · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

سورة نوح باللغة الشيشيوا

السورة بالعربية مع التفسير استمع إلى سورة نوح (1,290 قارئاً)
مكيةسورة نوح٢٨ آية

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

إِنَّآ أَرۡسَلۡنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوۡمِهِۦٓ أَنۡ أَنذِرۡ قَوۡمَكَ مِن قَبۡلِ أَن يَأۡتِيَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٌ ١Ndithudi tidatumiza Nowa kwa anthu ake: “Chenjeza anthu ako chilango chowawa chisadafike pa iwo.” قَالَ يَٰقَوۡمِ إِنِّي لَكُمۡ نَذِيرٌ مُّبِينٌ ٢Iye adati: “oh inu anthu anga! Ndithudi ine, ndine Mchenjezi wooneka kwa inu.” أَنِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ وَٱتَّقُوهُ وَأَطِيعُونِ ٣“Kuti muzipembedza Mulungu ndi kumuopa Iye ndipo mundimvere ine.” يَغۡفِرۡ لَكُم مِّن ذُنُوبِكُمۡ وَيُؤَخِّرۡكُمۡ إِلَىٰٓ أَجَلٍ مُّسَمًّىۚ إِنَّ أَجَلَ ٱللَّهِ إِذَا جَآءَ لَا يُؤَخَّرُۚ لَوۡ كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ ٤“Iye adzakukhululukirani machimo anu ndi kukusungani bwino mpaka nthawi ya imfa yanu. Ndithudi nthawi ya Mulungu ikakwana, palibe wina aliyense amene angaibwezere m’mbuyo inu mukadadziwa.” قَالَ رَبِّ إِنِّي دَعَوۡتُ قَوۡمِي لَيۡلًا وَنَهَارًا ٥Iye adati: “oh Ambuye! Ndithudi usana ndi usiku ndakhala ndiri kuwaitana anthu anga.” فَلَمۡ يَزِدۡهُمۡ دُعَآءِيٓ إِلَّا فِرَارًا ٦“Koma kuitana kwanga kwangoonjezera kusamvera kwawo.” وَإِنِّي كُلَّمَا دَعَوۡتُهُمۡ لِتَغۡفِرَ لَهُمۡ جَعَلُوٓاْ أَصَٰبِعَهُمۡ فِيٓ ءَاذَانِهِمۡ وَٱسۡتَغۡشَوۡاْ ثِيَابَهُمۡ وَأَصَرُّواْ وَٱسۡتَكۡبَرُواْ ٱسۡتِكۡبَارًا ٧“Ndipo, ndithudi, nthawi yonse imene ndiitana kuti Inu muwakhululukire, iwo amatenga zala zawo ndi kutseka m’makutu mwawo ndipo amatenga mikhanjo yawo ndi kufunditsa kumutu kwawo ndipo amapitirirabe kuchita zoipa monyada.” ثُمَّ إِنِّي دَعَوۡتُهُمۡ جِهَارًا ٨“Ndipo, ndithudi, ine ndidalalikira mokweza kwa iwo.” ثُمَّ إِنِّيٓ أَعۡلَنتُ لَهُمۡ وَأَسۡرَرۡتُ لَهُمۡ إِسۡرَارًا ٩“Ndipo, ndithudi, ndidawalankhula pagulu ndi mwamseri.” فَقُلۡتُ ٱسۡتَغۡفِرُواْ رَبَّكُمۡ إِنَّهُۥ كَانَ غَفَّارًا ١٠Ndidawauza: “Funsani chikhululukiro cha Ambuye wanu. Ndithudi Iye amakhululukira nthawi zonse.” يُرۡسِلِ ٱلسَّمَآءَ عَلَيۡكُم مِّدۡرَارًا ١١“Iye adzakutumizirani Nuh 621 mvula yochuluka.” وَيُمۡدِدۡكُم بِأَمۡوَٰلٍ وَبَنِينَ وَيَجۡعَل لَّكُمۡ جَنَّٰتٍ وَيَجۡعَل لَّكُمۡ أَنۡهَٰرًا ١٢“Ndikukupatsani inu chuma, ana, minda ndi mitsinje.” مَّا لَكُمۡ لَا تَرۡجُونَ لِلَّهِ وَقَارًا ١٣Kodi mwatani, inu simuyembekeza mphotho وَقَدۡ خَلَقَكُمۡ أَطۡوَارًا ١٤Pamene Iye adakulengani inu m’nthawi zosiyana siyana أَلَمۡ تَرَوۡاْ كَيۡفَ خَلَقَ ٱللَّهُ سَبۡعَ سَمَٰوَٰتٍ طِبَاقًا ١٥Kodi inu simuona mmene Mulungu adalengera miyamba isanu ndi iwiri, wina pamwamba pa unzake وَجَعَلَ ٱلۡقَمَرَ فِيهِنَّ نُورًا وَجَعَلَ ٱلشَّمۡسَ سِرَاجًا ١٦Ndipo anapanga mwezi ngati muuni ndi dzuwa ngati nyali وَٱللَّهُ أَنۢبَتَكُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ نَبَاتًا ١٧Mulungu adakulengani inu kuchokera ku nthaka ثُمَّ يُعِيدُكُمۡ فِيهَا وَيُخۡرِجُكُمۡ إِخۡرَاجًا ١٨Ndipo ku nthaka komweko adzakubwezerani inu ndi kukudzutsaninso وَٱللَّهُ جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ بِسَاطًا ١٩Ndipo Mulungu adalenga dziko kukhala lalikulu kwa inu لِّتَسۡلُكُواْ مِنۡهَا سُبُلًا فِجَاجًا ٢٠Kuti muziyenda m’njira zambiri za zikuluzikulu قَالَ نُوحٌ رَّبِّ إِنَّهُمۡ عَصَوۡنِي وَٱتَّبَعُواْ مَن لَّمۡ يَزِدۡهُ مَالُهُۥ وَوَلَدُهُۥٓ إِلَّا خَسَارًا ٢١Nowa adati: “oh Ambuye! Anthu anga sali kundimvera ine koma mmalo mwake ali kutsatira amene sangawaonjezere chuma ndi ana koma mavuto.” وَمَكَرُواْ مَكۡرًا كُبَّارًا ٢٢Ndipo iwo akonza chiwembu champhamvu وَقَالُواْ لَا تَذَرُنَّ ءَالِهَتَكُمۡ وَلَا تَذَرُنَّ وَدًّا وَلَا سُوَاعًا وَلَا يَغُوثَ وَيَعُوقَ وَنَسۡرًا ٢٣Ndipo ati: “Mwanjira ina iliyonse inu musaleke kupembedza milungu yanu. Musaleke kupembedza Wadd, Suwa, Yaghuth, Yauq kapena Nasr.” وَقَدۡ أَضَلُّواْ كَثِيرًاۖ وَلَا تَزِدِ ٱلظَّٰلِمِينَ إِلَّا ضَلَٰلًا ٢٤“Ndipo, ndithudi, iwo asocheza anthu ambiri. Ndipo Inu musaonjeze china chili chonse kwa anthu ochita zoipa chifukwa apitirizabe kuchita zoipa.” مِّمَّا خَطِيٓـَٰٔتِهِمۡ أُغۡرِقُواْ فَأُدۡخِلُواْ نَارًا فَلَمۡ يَجِدُواْ لَهُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ أَنصَارًا ٢٥Chifukwa cha machimo awo iwo anamizidwa ndipo adaponyedwa ku moto ndipo iwo sanapeze wina aliyense kuti awathandize, m’malo mwa Mulungu وَقَالَ نُوحٌ رَّبِّ لَا تَذَرۡ عَلَى ٱلۡأَرۡضِ مِنَ ٱلۡكَٰفِرِينَ دَيَّارًا ٢٦Ndipo Nowa adati: Ambuye wanga! Musasiye munthu aliyense padziko lapansi mwa anthu osakhulupirira إِنَّكَ إِن تَذَرۡهُمۡ يُضِلُّواْ عِبَادَكَ وَلَا يَلِدُوٓاْ إِلَّا فَاجِرًا كَفَّارًا ٢٧“Ngati Inu muwasiya iwo adzasocheretsa akapolo anu okhulupirira ndipo iwo adzabereka anthu ochita zoipa ndi osakhulupirira.” رَّبِّ ٱغۡفِرۡ لِي وَلِوَٰلِدَيَّ وَلِمَن دَخَلَ بَيۡتِيَ مُؤۡمِنًا وَلِلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِۖ وَلَا تَزِدِ ٱلظَّٰلِمِينَ إِلَّا تَبَارَۢا ٢٨“Ambuye wanga! Ndikhululukireni ine ndi makolo anga ndi iye amene alowa mnyumba yanga ngati wokhulupirira ndiponso okhulupirira onse amuna ndi akazi. Ndipo kwa anthu osakhulupilira, Inu musawaonjezere china koma chionongeko

الترجمة: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.