ملة الإسلام

السورة 50 · 45 آية · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

سورة ق باللغة الشيشيوا

السورة بالعربية مع التفسير استمع إلى سورة ق (1,405 قارئاً)
مكيةسورة ق٤٥ آية

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

قٓۚ وَٱلۡقُرۡءَانِ ٱلۡمَجِيدِ ١Qaf. Pali Buku lolemekezeka la Korani بَلۡ عَجِبُوٓاْ أَن جَآءَهُم مُّنذِرٌ مِّنۡهُمۡ فَقَالَ ٱلۡكَٰفِرُونَ هَٰذَا شَيۡءٌ عَجِيبٌ ٢Koma iwo alikudabwa kuti kwa iwo kwadza mchenjezi wochokera pakati pawo. Motero anthu osakhulupirira amati, “chimenechi ndi chinthu chachilendo!” أَءِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابًاۖ ذَٰلِكَ رَجۡعُۢ بَعِيدٌ ٣“Pamene ife tafa ndi kusanduka dothi, kubwerera kotero ndi kosatheka.” قَدۡ عَلِمۡنَا مَا تَنقُصُ ٱلۡأَرۡضُ مِنۡهُمۡۖ وَعِندَنَا كِتَٰبٌ حَفِيظُۢ ٤Ife timadziwa onse amene adamezedwa ndi nthaka ndipo Ife tili ndi Buku la mbiri yawo بَلۡ كَذَّبُواْ بِٱلۡحَقِّ لَمَّا جَآءَهُمۡ فَهُمۡ فِيٓ أَمۡرٍ مَّرِيجٍ ٥Iyayi, koma iwo adakana choonadi pamene chidadza kwa iwo. Kotero iwo, tsopano, asokonezeka أَفَلَمۡ يَنظُرُوٓاْ إِلَى ٱلسَّمَآءِ فَوۡقَهُمۡ كَيۡفَ بَنَيۡنَٰهَا وَزَيَّنَّٰهَا وَمَا لَهَا مِن فُرُوجٍ ٦Kodi iwo sayang’ana kumwamba ndi kuona mmene tidakukonzera ndi kukukongoletsera ndi kuona kuti kulibe mipata وَٱلۡأَرۡضَ مَدَدۡنَٰهَا وَأَلۡقَيۡنَا فِيهَا رَوَٰسِيَ وَأَنۢبَتۡنَا فِيهَا مِن كُلِّ زَوۡجِۭ بَهِيجٍ ٧Ndipo dziko lapansi Ife talipanga kukhala losalala ndi kuikamo mapiri ndipo tidameretsa mu dzikolo mbewu zokongola zosiyanasiyana تَبۡصِرَةً وَذِكۡرَىٰ لِكُلِّ عَبۡدٍ مُّنِيبٍ ٨Choonetsa ndi chikumbutso kwa kapolo aliyense amene amatembenukira nthawi zonse kwa Mulungu وَنَزَّلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءً مُّبَٰرَكًا فَأَنۢبَتۡنَا بِهِۦ جَنَّٰتٍ وَحَبَّ ٱلۡحَصِيدِ ٩Ndipo timatumiza kuchokera ku mitambo mvula yodalitsika ndipo timameretsa m’minda mbewu zimene zimakololedwa وَٱلنَّخۡلَ بَاسِقَٰتٍ لَّهَا طَلۡعٌ نَّضِيدٌ ١٠Ndi mitengo italiitali ya tende yolemedwa ndi zipatso رِّزۡقًا لِّلۡعِبَادِۖ وَأَحۡيَيۡنَا بِهِۦ بَلۡدَةً مَّيۡتًاۚ كَذَٰلِكَ ٱلۡخُرُوجُ ١١Chakudya cha akapolo. Ndipo Ife timapereka moyo kunthaka imene idali yakufa. Kumeneko ndiko kuuka kwa akufa كَذَّبَتۡ قَبۡلَهُمۡ قَوۡمُ نُوحٍ وَأَصۡحَٰبُ ٱلرَّسِّ وَثَمُودُ ١٢Adakana iwo asanadze, anthu a Nowa ndi iwo amene anali kukhala ku Ar-rass ndi Thamoud وَعَادٌ وَفِرۡعَوۡنُ وَإِخۡوَٰنُ لُوطٍ ١٣Anthu a mtundu wa Aad ndi Farawo ndi abale ake a Loti وَأَصۡحَٰبُ ٱلۡأَيۡكَةِ وَقَوۡمُ تُبَّعٍۚ كُلٌّ كَذَّبَ ٱلرُّسُلَ فَحَقَّ وَعِيدِ ١٤Ndi iwo amene anali kukhala m’nkhalango ndi anthu a ku Tuba, aliyense wa iwo adakana Atumwi ndipo chenjezo langa lidakwaniritsidwa أَفَعَيِينَا بِٱلۡخَلۡقِ ٱلۡأَوَّلِۚ بَلۡ هُمۡ فِي لَبۡسٍ مِّنۡ خَلۡقٍ جَدِيدٍ ١٥Kodi Ife tidatopa ndi chilengedwe choyamba? Iyayi. Iwo asokonezeka ndi nkhani zokhudza chilengedwe chatsopano وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ وَنَعۡلَمُ مَا تُوَسۡوِسُ بِهِۦ نَفۡسُهُۥۖ وَنَحۡنُ أَقۡرَبُ إِلَيۡهِ مِنۡ حَبۡلِ ٱلۡوَرِيدِ ١٦Ndithudi Ife tidamulenga munthu ndipo timadziwa zimene mtima wake umamuuza. Ndipo Ife tili pafupi ndi iye kuposa mtsempha wa moyo wake إِذۡ يَتَلَقَّى ٱلۡمُتَلَقِّيَانِ عَنِ ٱلۡيَمِينِ وَعَنِ ٱلشِّمَالِ قَعِيدٌ ١٧Pamene asungi awiri amulandira, wina atakhala kudzanja lamanja ndi wina ku dzanja lamanzere مَّا يَلۡفِظُ مِن قَوۡلٍ إِلَّا لَدَيۡهِ رَقِيبٌ عَتِيدٌ ١٨Palibe mawu amene amayankhula amene samveka kwa Msungi wa tcheru وَجَآءَتۡ سَكۡرَةُ ٱلۡمَوۡتِ بِٱلۡحَقِّۖ ذَٰلِكَ مَا كُنتَ مِنۡهُ تَحِيدُ ١٩Ndipo ululu wa imfa udzadza pa iye mwachoonadi. Ichi ndicho chimene iwe unali kuyesetsa kuchithawa وَنُفِخَ فِي ٱلصُّورِۚ ذَٰلِكَ يَوۡمُ ٱلۡوَعِيدِ ٢٠Ndipo lipenga lidzaombedwa ndipo limeneli lidzakhala tsiku loopseza وَجَآءَتۡ كُلُّ نَفۡسٍ مَّعَهَا سَآئِقٌ وَشَهِيدٌ ٢١Ndipo mzimu uliwonse udzadza pamodzi ndi mngelo wouyendetsa ndi mngelo wochitira umboni لَّقَدۡ كُنتَ فِي غَفۡلَةٍ مِّنۡ هَٰذَا فَكَشَفۡنَا عَنكَ غِطَآءَكَ فَبَصَرُكَ ٱلۡيَوۡمَ حَدِيدٌ ٢٢(Ndipo kudzanenedwa kwa anthu ochimwa) kuti, “Ndithudi inu simudafune kuchenjezedwa za chimenechi ndipotsopano Ifetavundukulachimenechimakuphimbani. Ndipo lero maso anu ali kuona zenizeni.” وَقَالَ قَرِينُهُۥ هَٰذَا مَا لَدَيَّ عَتِيدٌ ٢٣Ndipo mnzake adzati, “Uwu ndi umboni umene ndili nawo.” أَلۡقِيَا فِي جَهَنَّمَ كُلَّ كَفَّارٍ عَنِيدٍ ٢٤“Ponyani ku Gahena aliyense wosathokoza ndiponso wosamvera.” مَّنَّاعٍ لِّلۡخَيۡرِ مُعۡتَدٍ مُّرِيبٍ ٢٥“Woletsa kuchita ntchito zabwino, woswa malamulo ndiponso wokayika.” ٱلَّذِي جَعَلَ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ فَأَلۡقِيَاهُ فِي ٱلۡعَذَابِ ٱلشَّدِيدِ ٢٦“Iye amene anali kukhazikitsa milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni, motero mponyeni ku chilango chowawa.” ۞ قَالَ قَرِينُهُۥ رَبَّنَا مَآ أَطۡغَيۡتُهُۥ وَلَٰكِن كَانَ فِي ضَلَٰلِۭ بَعِيدٍ ٢٧Mnzake adzanena kuti, “Ambuye wathu! Ine sindidamuuze kuti aziswa malamulo ayi koma iye adadzisocheretsa yekha.” قَالَ لَا تَخۡتَصِمُواْ لَدَيَّ وَقَدۡ قَدَّمۡتُ إِلَيۡكُم بِٱلۡوَعِيدِ ٢٨Mulungu adzati, “Musakangane pamaso panga. Ine ndidakutumizirani chenjezo lokwanira.” مَا يُبَدَّلُ ٱلۡقَوۡلُ لَدَيَّ وَمَآ أَنَا۠ بِظَلَّٰمٍ لِّلۡعَبِيدِ ٢٩Chilango sichisintha ayi ndipo Ine sindionetsa chinyengo kwa akapolo anga يَوۡمَ نَقُولُ لِجَهَنَّمَ هَلِ ٱمۡتَلَأۡتِ وَتَقُولُ هَلۡ مِن مَّزِيدٍ ٣٠Patsiku limene Ife tidzaifunsa Gahena kuti, “Kodi mwadzadza?” Ndipo iyo idzati, “Kodi akanalipobe ena?” وَأُزۡلِفَتِ ٱلۡجَنَّةُ لِلۡمُتَّقِينَ غَيۡرَ بَعِيدٍ ٣١Ndipo Paradiso idzabweretsedwa kufupi kwa anthu olungama هَٰذَا مَا تُوعَدُونَ لِكُلِّ أَوَّابٍ حَفِيظٍ ٣٢Ichi ndicho chimene mudalonjezedwa ndipo ndi mphotho kwa iye amene amadzipereka kwa Mulungu nthawi zonse nasunga malamulo ake مَّنۡ خَشِيَ ٱلرَّحۡمَٰنَ بِٱلۡغَيۡبِ وَجَآءَ بِقَلۡبٍ مُّنِيبٍ ٣٣Ndiponso kwa iye amene amaopa Mwini chisoni chosatha wosaoneka ndipo amadza kwa Iye ndi mtima wodzichepetsa ٱدۡخُلُوهَا بِسَلَٰمٍۖ ذَٰلِكَ يَوۡمُ ٱلۡخُلُودِ ٣٤Lowani m’menemo mwamtendere ndi mosaopa ayi. Ili ndi tsiku la moyo wosatha لَهُم مَّا يَشَآءُونَ فِيهَا وَلَدَيۡنَا مَزِيدٌ ٣٥M’menemo mudzakhala chilichonse chimene iwo adzafuna ndipo Ife tili ndi zinthu zambiri وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّن قَرۡنٍ هُمۡ أَشَدُّ مِنۡهُم بَطۡشًا فَنَقَّبُواْ فِي ٱلۡبِلَٰدِ هَلۡ مِن مَّحِيصٍ ٣٦Kodi ndi mibadwo ingati imene Ife tidaiononga iwo asanabadwe amene adali ndi mphamvu zoposa iwo ndipo iwo adafuna chitetezo padziko? Kodi iwo anali ndi kwina kothawira إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَذِكۡرَىٰ لِمَن كَانَ لَهُۥ قَلۡبٌ أَوۡ أَلۡقَى ٱلسَّمۡعَ وَهُوَ شَهِيدٌ ٣٧Ndithudi muli chikumbutso mu zimenezi kwa iye amene ali ndi mtima kapena amatchera khutu pamene achenjezedwa وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا فِي سِتَّةِ أَيَّامٍ وَمَا مَسَّنَا مِن لُّغُوبٍ ٣٨Ndithudi Ife tidalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo m’masiku asanu ndi limodzi ndipo sitidatope ayi فَٱصۡبِرۡ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ قَبۡلَ طُلُوعِ ٱلشَّمۡسِ وَقَبۡلَ ٱلۡغُرُوبِ ٣٩Kotero pirira pa zonse zimene amanena ndipo lemekeza Ambuye wako dzuwa lisanatuluke ndiponso lisanalowe وَمِنَ ٱلَّيۡلِ فَسَبِّحۡهُ وَأَدۡبَٰرَ ٱلسُّجُودِ ٤٠Ndipo mulemekeze Iye usiku ndipo utatha kupemphera وَٱسۡتَمِعۡ يَوۡمَ يُنَادِ ٱلۡمُنَادِ مِن مَّكَانٍ قَرِيبٍ ٤١Ndipo udzamve patsiku limene woitana adzaitana kuchokera pafupi يَوۡمَ يَسۡمَعُونَ ٱلصَّيۡحَةَ بِٱلۡحَقِّۚ ذَٰلِكَ يَوۡمُ ٱلۡخُرُوجِ ٤٢Tsiku limene iwo adzamva kulira kwa mfuwu woona. Limeneli lidzakhala tsiku louka kwa akufa إِنَّا نَحۡنُ نُحۡيِۦ وَنُمِيتُ وَإِلَيۡنَا ٱلۡمَصِيرُ ٤٣Ndithudi ndife amene timapereka moyo ndi imfa ndipo ndi kwa Ife kumene zonse zidzabwerera يَوۡمَ تَشَقَّقُ ٱلۡأَرۡضُ عَنۡهُمۡ سِرَاعًاۚ ذَٰلِكَ حَشۡرٌ عَلَيۡنَا يَسِيرٌ ٤٤Tsiku limene dziko lidzang’ambika ndipo iwo adzatuluka mofulumira. Kumeneko ndiko kudzakhala kusonkhanitsidwa pamodzi نَّحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَا يَقُولُونَۖ وَمَآ أَنتَ عَلَيۡهِم بِجَبَّارٍۖ فَذَكِّرۡ بِٱلۡقُرۡءَانِ مَن يَخَافُ وَعِيدِ ٤٥Ife timadziwa zonse zimene amanena ndipo iwe si ndiwe wankhanza ayi. Koma muchenjeze ndi Korani kwa aliyense amene aopa chilango changa

الترجمة: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.