Millat al-Islam

Chapter 21 · 112 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Anbiyaa in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah Al-Anbiyaa (1271 reciters)

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

ٱقۡتَرَبَ لِلنَّاسِ حِسَابُهُمۡ وَهُمۡ فِي غَفۡلَةٍ مُّعۡرِضُونَ ١Chayandikira kwa anthu chiweruzo cha ntchito yawo ndi pamene iwo abwerera m’mbuyo monyoza مَا يَأۡتِيهِم مِّن ذِكۡرٍ مِّن رَّبِّهِم مُّحۡدَثٍ إِلَّا ٱسۡتَمَعُوهُ وَهُمۡ يَلۡعَبُونَ ٢Palibe chenjezo limene limadza kuchokera kwa Ambuye wawo limene iwo amalimvera kupatula pamene iwo ali kusewera لَاهِيَةً قُلُوبُهُمۡۗ وَأَسَرُّواْ ٱلنَّجۡوَى ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ هَلۡ هَٰذَآ إِلَّا بَشَرٌ مِّثۡلُكُمۡۖ أَفَتَأۡتُونَ ٱلسِّحۡرَ وَأَنتُمۡ تُبۡصِرُونَ ٣Ndi mitima yotangwanika, iwo amene amachita zoipa amauzana mwamseri kuti, “Kodi uyu si munthu ngati inu? Kodi inu mukutsatira matsenga pamene muli kuona?” قَالَ رَبِّي يَعۡلَمُ ٱلۡقَوۡلَ فِي ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِۖ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ ٤Iye adati: “Ambuye wanga amadziwa chilichonse chimene chimanenedwa kumwamba ndi pa dziko lapansi ndipo Iye amamva zonse ndiponso amadziwa chinthu china chilichonse.” بَلۡ قَالُوٓاْ أَضۡغَٰثُ أَحۡلَٰمِۭ بَلِ ٱفۡتَرَىٰهُ بَلۡ هُوَ شَاعِرٌ فَلۡيَأۡتِنَا بِـَٔايَةٍ كَمَآ أُرۡسِلَ ٱلۡأَوَّلُونَ ٥Koma ena amati, “Ichi si china koma maloto a bodza! Iyayi! Iye walipeka. Iyayi, iye ndi mlakatuli! Ndipo mulekeni atilangize ife chizindikiro china monga momwe Atumwi akale ankachitira.” مَآ ءَامَنَتۡ قَبۡلَهُم مِّن قَرۡيَةٍ أَهۡلَكۡنَٰهَآۖ أَفَهُمۡ يُؤۡمِنُونَ ٦Palibe umodzi wa mizinda imene tidaononga imene idakhulupirira iwo asanadze. Kodi iwo adzakhulupirira وَمَآ أَرۡسَلۡنَا قَبۡلَكَ إِلَّا رِجَالًا نُّوحِيٓ إِلَيۡهِمۡۖ فَسۡـَٔلُوٓاْ أَهۡلَ ٱلذِّكۡرِ إِن كُنتُمۡ لَا تَعۡلَمُونَ ٧Ndipo Ife, iwe usadabwere sitidatumize ena, koma amuna omwe timawapatsa chivumbulutso. Motero afunse anthu ozindikira ngati iwe siudziwa وَمَا جَعَلۡنَٰهُمۡ جَسَدًا لَّا يَأۡكُلُونَ ٱلطَّعَامَ وَمَا كَانُواْ خَٰلِدِينَ ٨Ife sitidawapange iwo ndi matupi amene samadya chakudya kapena amuyaya ayi ثُمَّ صَدَقۡنَٰهُمُ ٱلۡوَعۡدَ فَأَنجَيۡنَٰهُمۡ وَمَن نَّشَآءُ وَأَهۡلَكۡنَا ٱلۡمُسۡرِفِينَ ٩Ndipo Ife tidakwaniritsa lonjezo lathu kwa iwo, ndipo tidawapulumutsa iwo pamodzi ndi ena amene Ife tidawafuna koma tidaonongeratu anthu onse ochimwa لَقَدۡ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكُمۡ كِتَٰبًا فِيهِ ذِكۡرُكُمۡۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ ١٠Ndithudi tavumbulutsa Buku m’mene muli chikumbutso kwa inu. Kodi mulibe nzeru وَكَمۡ قَصَمۡنَا مِن قَرۡيَةٍ كَانَتۡ ظَالِمَةً وَأَنشَأۡنَا بَعۡدَهَا قَوۡمًا ءَاخَرِينَ ١١Kodi ndi mizinda ingati imene tidaononga imene idali yochita zoipa, ndipo m’malo mwawo tidaikamo anthu ena فَلَمَّآ أَحَسُّواْ بَأۡسَنَآ إِذَا هُم مِّنۡهَا يَرۡكُضُونَ ١٢Ndipo pamene iwo adaona chilango chathu iwo adayesa kuthawa m’mizinda yawo لَا تَرۡكُضُواْ وَٱرۡجِعُوٓاْ إِلَىٰ مَآ أُتۡرِفۡتُمۡ فِيهِ وَمَسَٰكِنِكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تُسۡـَٔلُونَ ١٣“Musathawe koma bwererani kumene mumakhala moyo wa chisangalalo ndi ku nyumba zanu kuti mukafunsidwe.” قَالُواْ يَٰوَيۡلَنَآ إِنَّا كُنَّا ظَٰلِمِينَ ١٤Iwo anati, “Tsoka kwa ife! Ndithudi tinali kuchita zoipa.” فَمَا زَالَت تِّلۡكَ دَعۡوَىٰهُمۡ حَتَّىٰ جَعَلۡنَٰهُمۡ حَصِيدًا خَٰمِدِينَ ١٥Koma kulira kwawo sikunathe mpaka pamene Ife tidawaononga ndi kukhala ngati munda umene wakololedwa وَمَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَآءَ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا لَٰعِبِينَ ١٦Sitidalengemwamasewerakumwambandidzikolapansi ndi zonse zimene zili pakati pake لَوۡ أَرَدۡنَآ أَن نَّتَّخِذَ لَهۡوًا لَّٱتَّخَذۡنَٰهُ مِن لَّدُنَّآ إِن كُنَّا فَٰعِلِينَ ١٧Ife tikadafuna kuti tisangalale tikadadzipangira tokha, ngati Ife tikadafunadi kutero بَلۡ نَقۡذِفُ بِٱلۡحَقِّ عَلَى ٱلۡبَٰطِلِ فَيَدۡمَغُهُۥ فَإِذَا هُوَ زَاهِقٌۚ وَلَكُمُ ٱلۡوَيۡلُ مِمَّا تَصِفُونَ ١٨Iyayi! Ife timatumiza choonadi kuti chilimbane ndi bodza ndipo chimaliononga. Taonani, ilo latha. Ndipo tsoka kwa inu chifukwa cha zimene mumanena وَلَهُۥ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَمَنۡ عِندَهُۥ لَا يَسۡتَكۡبِرُونَ عَنۡ عِبَادَتِهِۦ وَلَا يَسۡتَحۡسِرُونَ ١٩Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi. Ndipo onse amene ali pafupi pake sanyozera kumupembedza Iye ndipo satopa ayi يُسَبِّحُونَ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ لَا يَفۡتُرُونَ ٢٠Iwo amamutamanda Iye masana ndi usiku ndipo sachita ulesi أَمِ ٱتَّخَذُوٓاْ ءَالِهَةً مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ هُمۡ يُنشِرُونَ ٢١Kodi iwo asankha milungu ya pa dziko lapansi imene imadzutsa anthu akufa لَوۡ كَانَ فِيهِمَآ ءَالِهَةٌ إِلَّا ٱللَّهُ لَفَسَدَتَاۚ فَسُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ رَبِّ ٱلۡعَرۡشِ عَمَّا يَصِفُونَ ٢٢Kukadakhala milungu ina kumeneko yoonjezera pa Mulungu weniweni, ndithudi, konse kukadaonongeka. Alemekezeke Mulungu, Mwini wa Mpando wa Chifumu, mu zimene akumunenera لَا يُسۡـَٔلُ عَمَّا يَفۡعَلُ وَهُمۡ يُسۡـَٔلُونَ ٢٣Iye sangafunsidwe pa ntchito zimene amachita pamene iwo adzafunsidwa أَمِ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ ءَالِهَةًۖ قُلۡ هَاتُواْ بُرۡهَٰنَكُمۡۖ هَٰذَا ذِكۡرُ مَن مَّعِيَ وَذِكۡرُ مَن قَبۡلِيۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ ٱلۡحَقَّۖ فَهُم مُّعۡرِضُونَ ٢٤Kodi kapena iwo asankha milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni? Nena, “Bweretsani umboni wanu”. Ichi ndi chikumbutso cha amene ndili nawo ndiponso iwo amakedzana. Koma ambiri a iwo sadziwa choonadi motero salabadira وَمَآ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ مِن رَّسُولٍ إِلَّا نُوحِيٓ إِلَيۡهِ أَنَّهُۥ لَآ إِلَٰهَ إِلَّآ أَنَا۠ فَٱعۡبُدُونِ ٢٥Ndipo Ife sitidatumize iwe usadabadwe, Mtumwi wina aliyense amene sitinamuuze kuti, “Kulibe Mulungu wina koma Ine ndekha, kotero ndi pembedzeni Ine.” وَقَالُواْ ٱتَّخَذَ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَلَدًاۗ سُبۡحَٰنَهُۥۚ بَلۡ عِبَادٌ مُّكۡرَمُونَ ٢٦Iwo amati, “Mwini chisoni chosatha wabereka mwana wamwamuna.” Iye alemekezedwe! Amenewo si ena ayi koma akapolo ake olemekezeka لَا يَسۡبِقُونَهُۥ بِٱلۡقَوۡلِ وَهُم بِأَمۡرِهِۦ يَعۡمَلُونَ ٢٧Iwo sayankhula pokhapokha Iye atayankhula, ndipo amachita zinthu potsatira malamulo ake يَعۡلَمُ مَا بَيۡنَ أَيۡدِيهِمۡ وَمَا خَلۡفَهُمۡ وَلَا يَشۡفَعُونَ إِلَّا لِمَنِ ٱرۡتَضَىٰ وَهُم مِّنۡ خَشۡيَتِهِۦ مُشۡفِقُونَ ٢٨Iye amadziwa zonse zimene zili patsogolo pawo ndiponso zimene zili m’mbuyo mwawo ndipo iwo sangalankhulire wina aliyense chipulumutso kupatula amene Iye wamukonda ndipo iwo amanjenjemera chifukwa cha mantha pomuona Iye ۞ وَمَن يَقُلۡ مِنۡهُمۡ إِنِّيٓ إِلَٰهٌ مِّن دُونِهِۦ فَذَٰلِكَ نَجۡزِيهِ جَهَنَّمَۚ كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلظَّٰلِمِينَ ٢٩Ndipo ngati wina wa iwo atanena kuti, “Ndithudi ine ndine mulungu kuonjezera pa Iye.” Oteroyo adzalangidwa ndi moto wa ku Gahena. Mmenemo ndi mmene timalipirira anthu olakwa أَوَلَمۡ يَرَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ أَنَّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ كَانَتَا رَتۡقًا فَفَتَقۡنَٰهُمَاۖ وَجَعَلۡنَا مِنَ ٱلۡمَآءِ كُلَّ شَيۡءٍ حَيٍّۚ أَفَلَا يُؤۡمِنُونَ ٣٠Kodi anthu osakhulupirira sadziwa kuti kumwamba ndi dziko lapansi chidali chinthu chimodzi chogwirana chimene tidachisiyanitsa? Ndipo tidapanga, chilichonse chamoyo, kuchokera ku madzi. Kodi iwo sangakhulupirire وَجَعَلۡنَا فِي ٱلۡأَرۡضِ رَوَٰسِيَ أَن تَمِيدَ بِهِمۡ وَجَعَلۡنَا فِيهَا فِجَاجًا سُبُلًا لَّعَلَّهُمۡ يَهۡتَدُونَ ٣١Ndipo Ife tidakhazikitsa mapiri pa dziko lapansi molimba kuti asagwedezeke pamodzi ndi iwo ndipo tidakhazikitsa misewu pa miyala kuti mwina atsogozedwe وَجَعَلۡنَا ٱلسَّمَآءَ سَقۡفًا مَّحۡفُوظًاۖ وَهُمۡ عَنۡ ءَايَٰتِهَا مُعۡرِضُونَ ٣٢Ndipo tidapanga kumwamba denga losungika bwino limene silingagwe. Komabe iwo amakana zizindikiro zake وَهُوَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ وَٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَۖ كُلٌّ فِي فَلَكٍ يَسۡبَحُونَ ٣٣Iye ndiye amene adalenga usiku ndi usana, dzuwa ndi mwezi ndi china chilichonse chimene chimayenda mlengalenga وَمَا جَعَلۡنَا لِبَشَرٍ مِّن قَبۡلِكَ ٱلۡخُلۡدَۖ أَفَإِيْن مِّتَّ فَهُمُ ٱلۡخَٰلِدُونَ ٣٤Palibe munthu, pambuyo pako amene tidamulenga kuti sadzafa. Ngati iweyo udzafa, kodi iwo adzakhala ndi moyo mpaka kalekale كُلُّ نَفۡسٍ ذَآئِقَةُ ٱلۡمَوۡتِۗ وَنَبۡلُوكُم بِٱلشَّرِّ وَٱلۡخَيۡرِ فِتۡنَةًۖ وَإِلَيۡنَا تُرۡجَعُونَ ٣٥Chilichonse cholengedwa chidzalawa imfa ndipo Ife tidzakuyesani ndi zinthu zoipa ndi zabwino ndipo ndi kwa Ife kumene nonse mudzabwerera وَإِذَا رَءَاكَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِن يَتَّخِذُونَكَ إِلَّا هُزُوًا أَهَٰذَا ٱلَّذِي يَذۡكُرُ ءَالِهَتَكُمۡ وَهُم بِذِكۡرِ ٱلرَّحۡمَٰنِ هُمۡ كَٰفِرُونَ ٣٦Pamene anthu osakhulupirira amakuona iwe, sakuganizira zabwino koma chipongwe ndipo amati, “Kodi uyu ndiye munthu amene amayankhula zoipa za milungu yanu?” Pamene iwo amakana zonse zokhudza Mwini chisoni chosatha خُلِقَ ٱلۡإِنسَٰنُ مِنۡ عَجَلٍۚ سَأُوْرِيكُمۡ ءَايَٰتِي فَلَا تَسۡتَعۡجِلُونِ ٣٧Munthu adalengedwa kukhala opupuluma pochita zinthu. Ine ndidzakusonyezani zizindikiro zanga. Motero musandifulumizitse وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ ٣٨Iwo amati, “Kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa liti ngati zimene uli kunena ndi zoona?” لَوۡ يَعۡلَمُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ حِينَ لَا يَكُفُّونَ عَن وُجُوهِهِمُ ٱلنَّارَ وَلَا عَن ظُهُورِهِمۡ وَلَا هُمۡ يُنصَرُونَ ٣٩Akadakhala kuti anthu osakhulupirira akudziwa tsiku limene iwo sadzakhala ndi mphamvu zophimba nkhope kapena misana yawo kudziteteza ku moto ndipo iwo sangathandizike بَلۡ تَأۡتِيهِم بَغۡتَةً فَتَبۡهَتُهُمۡ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ رَدَّهَا وَلَا هُمۡ يُنظَرُونَ ٤٠Iyayi. Ilo lidzadza kwa iwo mwadzidzidzi ndipo adzadodoma ndi kusokonezeka ndipo iwo sadzatha kulibweza ndiponso sadzapatsidwa nthawi yopuma وَلَقَدِ ٱسۡتُهۡزِئَ بِرُسُلٍ مِّن قَبۡلِكَ فَحَاقَ بِٱلَّذِينَ سَخِرُواْ مِنۡهُم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ ٤١Ndithudi Atumwi ena, adachitidwa chipongwe kale, koma anthu a chipongwe adafafanizidwa ndi chilango chimene iwo adachichitira chipongwe قُلۡ مَن يَكۡلَؤُكُم بِٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ مِنَ ٱلرَّحۡمَٰنِۚ بَلۡ هُمۡ عَن ذِكۡرِ رَبِّهِم مُّعۡرِضُونَ ٤٢Nena, “Kodi ndani adzakutetezani inu nthawi ya usiku ndi nthawi ya masana ku mkwiyo wa Mwini chisoni?” Komabe iwo salabadira zokumbukira Ambuye wawo أَمۡ لَهُمۡ ءَالِهَةٌ تَمۡنَعُهُم مِّن دُونِنَاۚ لَا يَسۡتَطِيعُونَ نَصۡرَ أَنفُسِهِمۡ وَلَا هُم مِّنَّا يُصۡحَبُونَ ٤٣Kapena iwo ali ndi milungu ina yoti ingawateteze kwa Ife? Iyo siingathe kudziteteza yokha; ndiponso iwo sangatetezedwe kuchilango chathu بَلۡ مَتَّعۡنَا هَٰٓؤُلَآءِ وَءَابَآءَهُمۡ حَتَّىٰ طَالَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡعُمُرُۗ أَفَلَا يَرَوۡنَ أَنَّا نَأۡتِي ٱلۡأَرۡضَ نَنقُصُهَا مِنۡ أَطۡرَافِهَآۚ أَفَهُمُ ٱلۡغَٰلِبُونَ ٤٤Koma Ife tidapereka zokoma za m’moyo uno kwa anthuwa pamodzi ndi makolo awo mpaka pamene nthawi idawatalikira iwo. Kodi iwo saona kuti Ife timachepetsa dziko lawo kuchokera m’malire mwake? Kodi iwo ndiwo adzapambane قُلۡ إِنَّمَآ أُنذِرُكُم بِٱلۡوَحۡيِۚ وَلَا يَسۡمَعُ ٱلصُّمُّ ٱلدُّعَآءَ إِذَا مَا يُنذَرُونَ ٤٥Nena, “Ine ndili kukuchenjezani ndi chivumbulutso, koma agonthi sadzamva kuitana pamene achenjezedwa وَلَئِن مَّسَّتۡهُمۡ نَفۡحَةٌ مِّنۡ عَذَابِ رَبِّكَ لَيَقُولُنَّ يَٰوَيۡلَنَآ إِنَّا كُنَّا ظَٰلِمِينَ ٤٦Koma ngati katsoka kakang’ono kochokera kwa Ambuye wako kagwa pa iwo, ndithudi, iwo adzalira, “Tsoka kwa ife; ndithudi tidali anthu ochita zoipa.” وَنَضَعُ ٱلۡمَوَٰزِينَ ٱلۡقِسۡطَ لِيَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ فَلَا تُظۡلَمُ نَفۡسٌ شَيۡـًٔاۖ وَإِن كَانَ مِثۡقَالَ حَبَّةٍ مِّنۡ خَرۡدَلٍ أَتَيۡنَا بِهَاۗ وَكَفَىٰ بِنَا حَٰسِبِينَ ٤٧Ndipo Ife tidzakhazikitsa miyeso yoyenera pa tsiku la kuuka kwa akufa ndipo aliyense sadzaponderezedwa pa china chilichonse. Ngakhale patakhala ntchito zazing’ono zolingana ngati kanthangala kakang’ono tidzazitulutsa kuti ziyesedwe. Ndipo Ife ndife okwana kuwerengera ntchito zonse وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ ٱلۡفُرۡقَانَ وَضِيَآءً وَذِكۡرًا لِّلۡمُتَّقِينَ ٤٨Ndithudi Ife tidamupatsa Mose ndi Aroni muyeso ndi muuni wowala ndi chikumbutso kwa anthu angwiro ٱلَّذِينَ يَخۡشَوۡنَ رَبَّهُم بِٱلۡغَيۡبِ وَهُم مِّنَ ٱلسَّاعَةِ مُشۡفِقُونَ ٤٩Iwo amene amaopa Ambuye kuchokera m’maganizo a pansi penipeni pa mtima ndipo amaopa tsiku louka kwa akufa وَهَٰذَا ذِكۡرٌ مُّبَارَكٌ أَنزَلۡنَٰهُۚ أَفَأَنتُمۡ لَهُۥ مُنكِرُونَ ٥٠Ndipo ichi ndi chivumbulutso chodalitsika chimene tatumiza. Kodi mudzachikana ۞ وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَآ إِبۡرَٰهِيمَ رُشۡدَهُۥ مِن قَبۡلُ وَكُنَّا بِهِۦ عَٰلِمِينَ ٥١Ndithudi Ife tidamupatsa kale chilangizo Abrahamu ndipo tinali kumudziwa bwino إِذۡ قَالَ لِأَبِيهِ وَقَوۡمِهِۦ مَا هَٰذِهِ ٱلتَّمَاثِيلُ ٱلَّتِيٓ أَنتُمۡ لَهَا عَٰكِفُونَ ٥٢Pamene Iye adawauza abambo ake ndiponso anthu ake kuti, “Kodi mafano amene muli kuwapembedzawa ndi chiyani?” قَالُواْ وَجَدۡنَآ ءَابَآءَنَا لَهَا عَٰبِدِينَ ٥٣Iwo adati, “Ife tidapeza makolo athu ali kuwapembedza.” قَالَ لَقَدۡ كُنتُمۡ أَنتُمۡ وَءَابَآؤُكُمۡ فِي ضَلَٰلٍ مُّبِينٍ ٥٤Iye adati, “Ndithudi inu ndiponso makolo anu mwakhala muli kuchimwa kwambiri.” قَالُوٓاْ أَجِئۡتَنَا بِٱلۡحَقِّ أَمۡ أَنتَ مِنَ ٱللَّٰعِبِينَ ٥٥Iwo adati, “Kodi ndi zoona zimene wadza nazo kwa ife kapena ndi nthabwala chabe?” قَالَ بَل رَّبُّكُمۡ رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ ٱلَّذِي فَطَرَهُنَّ وَأَنَا۠ عَلَىٰ ذَٰلِكُم مِّنَ ٱلشَّٰهِدِينَ ٥٦Iye adati, “Iyayi. Ambuye wanu ndi amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndipo muzimenezo ine ndichitira umboni.” وَتَٱللَّهِ لَأَكِيدَنَّ أَصۡنَٰمَكُم بَعۡدَ أَن تُوَلُّواْ مُدۡبِرِينَ ٥٧“Ndilumbira pali Mulungu kuti ine ndidzachita chiwembu pa mafano anu inu mukangochoka.” فَجَعَلَهُمۡ جُذَٰذًا إِلَّا كَبِيرًا لَّهُمۡ لَعَلَّهُمۡ إِلَيۡهِ يَرۡجِعُونَ ٥٨Motero iye adaziphwanya zonse kukhala tizidutswa kupatula fano lalikulu kuti akhoza kudzalifunsa قَالُواْ مَن فَعَلَ هَٰذَا بِـَٔالِهَتِنَآ إِنَّهُۥ لَمِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ ٥٩Iwo adati: “Kodi ndani amene wachita izi kwa milungu yathu? Ndithudi iye ali oipitsitsa.” قَالُواْ سَمِعۡنَا فَتًى يَذۡكُرُهُمۡ يُقَالُ لَهُۥٓ إِبۡرَٰهِيمُ ٦٠Iwo adati, “Ife tinamva mnyamata wotchedwa Abrahamu akunena za milunguyo.” قَالُواْ فَأۡتُواْ بِهِۦ عَلَىٰٓ أَعۡيُنِ ٱلنَّاسِ لَعَلَّهُمۡ يَشۡهَدُونَ ٦١Iwo adati, “Mubweretseni pamaso pa anthu onse kuti achitire umboni.” قَالُوٓاْ ءَأَنتَ فَعَلۡتَ هَٰذَا بِـَٔالِهَتِنَا يَٰٓإِبۡرَٰهِيمُ ٦٢Iwo adati, “Kodi iwe ndi amene wachita izi ku milungu yathu? Oh Abrahamu!” قَالَ بَلۡ فَعَلَهُۥ كَبِيرُهُمۡ هَٰذَا فَسۡـَٔلُوهُمۡ إِن كَانُواْ يَنطِقُونَ ٦٣Iye adati, “Iyayi. Ndi uyu, wamkulu kuposa zonse amene waziphwanya. Afunseni, ngati angayankhule” فَرَجَعُوٓاْ إِلَىٰٓ أَنفُسِهِمۡ فَقَالُوٓاْ إِنَّكُمۡ أَنتُمُ ٱلظَّٰلِمُونَ ٦٤Pamenepo iwo adayang’anizana okha nati, “Ndithudi inu ndinu anthu ochimwa kwambiri.” ثُمَّ نُكِسُواْ عَلَىٰ رُءُوسِهِمۡ لَقَدۡ عَلِمۡتَ مَا هَٰٓؤُلَآءِ يَنطِقُونَ ٦٥Ndipo adayang’anizananso nati, “Ndithudi iwe uli kudziwa kuti milungu iyi siiyankhula.” قَالَ أَفَتَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَنفَعُكُمۡ شَيۡـًٔا وَلَا يَضُرُّكُمۡ ٦٦Abrahamu adati, “Kodi inu mumapembedza mowonjezera pa Mulungu zinthu zimene sizingathe kukuthandizani chilichonse kapena kukuonongani?” أُفٍّ لَّكُمۡ وَلِمَا تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ ٦٧“Tsoka likhale pa inu ndi pa mafano anu amene mumapembedza kuonjezera pa Mulungu! Kodi mulibe nzeru?” قَالُواْ حَرِّقُوهُ وَٱنصُرُوٓاْ ءَالِهَتَكُمۡ إِن كُنتُمۡ فَٰعِلِينَ ٦٨Onse adati, “Mutentheni kuti muteteze milungu yanu ngati mufuna kuchita china chilichonse.” قُلۡنَا يَٰنَارُ كُونِي بَرۡدًا وَسَلَٰمًا عَلَىٰٓ إِبۡرَٰهِيمَ ٦٩Ife tidati, “Iwe moto khala wozizira ndi wamtendere kwa Abrahamu.” وَأَرَادُواْ بِهِۦ كَيۡدًا فَجَعَلۡنَٰهُمُ ٱلۡأَخۡسَرِينَ ٧٠Ndipo iwo adafuna kumuononga Iye koma Ife tidawapanga iwo kukhala olephera وَنَجَّيۡنَٰهُ وَلُوطًا إِلَى ٱلۡأَرۡضِ ٱلَّتِي بَٰرَكۡنَا فِيهَا لِلۡعَٰلَمِينَ ٧١Koma Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi Loti ndipo tidawaika ku dziko limene tidalidalitsa kuti zolengedwa zonse zikhalemo وَوَهَبۡنَا لَهُۥٓ إِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَ نَافِلَةًۖ وَكُلًّا جَعَلۡنَا صَٰلِحِينَ ٧٢Ndipo Ife tidamupatsa Isake ndi Yakobo ngati chidzukulu chake ndipo tidawapanga onse kukhala anthu angwiro وَجَعَلۡنَٰهُمۡ أَئِمَّةً يَهۡدُونَ بِأَمۡرِنَا وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡهِمۡ فِعۡلَ ٱلۡخَيۡرَٰتِ وَإِقَامَ ٱلصَّلَوٰةِ وَإِيتَآءَ ٱلزَّكَوٰةِۖ وَكَانُواْ لَنَا عَٰبِدِينَ ٧٣Ndipo Ife tidawasankha iwo kukhala atsogoleri olangiza anthu ku ulamuliro wathu ndipo tidawalamulira kuti azigwira ntchito zabwino ndipo, azipitiriza kupemphera ndi kupereka zothandizira osauka. Ndipo iwo anali kutitumikira Ife nthawi zonse وَلُوطًا ءَاتَيۡنَٰهُ حُكۡمًا وَعِلۡمًا وَنَجَّيۡنَٰهُ مِنَ ٱلۡقَرۡيَةِ ٱلَّتِي كَانَت تَّعۡمَلُ ٱلۡخَبَٰٓئِثَۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمَ سَوۡءٍ فَٰسِقِينَ ٧٤Ndi Loti tidamupatsa luntha, utumiki ndi nzeru za chipembedzo ndipo tidamupulumutsa ku mzinda umene anthu ake anali kuchita zoipa. Ndithudi, iwo anali anthu ochita zoipa ndipo anali osamvera Mulungu وَأَدۡخَلۡنَٰهُ فِي رَحۡمَتِنَآۖ إِنَّهُۥ مِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ ٧٥Ndipo Ife tidamulowetsa m’chisomo chathu, ndithudi, iye adali mmodzi wa anthu olungama وَنُوحًا إِذۡ نَادَىٰ مِن قَبۡلُ فَٱسۡتَجَبۡنَا لَهُۥ فَنَجَّيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥ مِنَ ٱلۡكَرۡبِ ٱلۡعَظِيمِ ٧٦Ndi pamene Nowa adatipempha poyamba, Ife tidamva pempho lake ndipo tidamupulumutsa iye pamodzi ndi anthu ake ku chilango choopsa وَنَصَرۡنَٰهُ مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَآۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمَ سَوۡءٍ فَأَغۡرَقۡنَٰهُمۡ أَجۡمَعِينَ ٧٧Ndiponso Ife tidamupulumutsa ku gulu la anthu amene adakana chivumbulutso chathu. Ndithudi iwo anali anthu oipa ndipo onse tidawamiza m’madzi وَدَاوُۥدَ وَسُلَيۡمَٰنَ إِذۡ يَحۡكُمَانِ فِي ٱلۡحَرۡثِ إِذۡ نَفَشَتۡ فِيهِ غَنَمُ ٱلۡقَوۡمِ وَكُنَّا لِحُكۡمِهِمۡ شَٰهِدِينَ ٧٨Pamene Davide ndi Solomoni adaweruza mulandu wa munda umene nkhosa zosochera za anthu ena zidadya nthawiyausiku. Ndipo Ifetidalimbonipachiweruzochawo فَفَهَّمۡنَٰهَا سُلَيۡمَٰنَۚ وَكُلًّا ءَاتَيۡنَا حُكۡمًا وَعِلۡمًاۚ وَسَخَّرۡنَا مَعَ دَاوُۥدَ ٱلۡجِبَالَ يُسَبِّحۡنَ وَٱلطَّيۡرَۚ وَكُنَّا فَٰعِلِينَ ٧٩Ife tidapatsa Solomoni nzeru zoweruzira nkhaniyi ndipo aliyense wa iwo tidamupatsa luntha, utumwi ndi nzeru. Tinalamula mapiri ndi mbalame kuti zikhale pamodzi ndi Davide pomutamanda Mulungu. Ndife amene tidachita zonsezi وَعَلَّمۡنَٰهُ صَنۡعَةَ لَبُوسٍ لَّكُمۡ لِتُحۡصِنَكُم مِّنۢ بَأۡسِكُمۡۖ فَهَلۡ أَنتُمۡ شَٰكِرُونَ ٨٠Ndipo tidamuphunzitsa luso lopanga zovala za nkhondo kuti zizikutetezani pa nthawi ya nkhondo, Kodi ndinu othokoza وَلِسُلَيۡمَٰنَ ٱلرِّيحَ عَاصِفَةً تَجۡرِي بِأَمۡرِهِۦٓ إِلَى ٱلۡأَرۡضِ ٱلَّتِي بَٰرَكۡنَا فِيهَاۚ وَكُنَّا بِكُلِّ شَيۡءٍ عَٰلِمِينَ ٨١Ndi Solomoni, Ife tidampeputsira mphamvu ya mphepo. Iyo inali kuomba potsatira malamulo ake kupita kudziko limene Ife tidalidalitsa. Ndipo Ife timadziwa zinthu zonse وَمِنَ ٱلشَّيَٰطِينِ مَن يَغُوصُونَ لَهُۥ وَيَعۡمَلُونَ عَمَلًا دُونَ ذَٰلِكَۖ وَكُنَّا لَهُمۡ حَٰفِظِينَ ٨٢Ndipo pakati pa a Satana padali ena omwe amaimira m’malo mwa iye ndipo amachitanso ntchito zina. Kuonjezera apa ndipo ndife amene timawayang’anira iwo ۞ وَأَيُّوبَ إِذۡ نَادَىٰ رَبَّهُۥٓ أَنِّي مَسَّنِيَ ٱلضُّرُّ وَأَنتَ أَرۡحَمُ ٱلرَّٰحِمِينَ ٨٣Ndi Yobu pamene adaitana Ambuye wake nati, “Ine, ndithudi, mavuto andikuta ndipo Inu ndinu wachisoni kuposa achisoni onse.” فَٱسۡتَجَبۡنَا لَهُۥ فَكَشَفۡنَا مَا بِهِۦ مِن ضُرٍّۖ وَءَاتَيۡنَٰهُ أَهۡلَهُۥ وَمِثۡلَهُم مَّعَهُمۡ رَحۡمَةً مِّنۡ عِندِنَا وَذِكۡرَىٰ لِلۡعَٰبِدِينَ ٨٤Motero Ife timamuyankha pempho lake ndipo tidamuchotsera mavuto ake ndipo tidamubwezeranso banja lake ndi zinthu zambiri zimene tidamupatsa ngati chisomo chochokera kwa Ife ndi chikumbutso kwa onse amene amatipembedza Ife وَإِسۡمَٰعِيلَ وَإِدۡرِيسَ وَذَا ٱلۡكِفۡلِۖ كُلٌّ مِّنَ ٱلصَّٰبِرِينَ ٨٥Ndipo Ishimayeli, Idris ndi dhulkifl, onse adali anthu opirira وَأَدۡخَلۡنَٰهُمۡ فِي رَحۡمَتِنَآۖ إِنَّهُم مِّنَ ٱلصَّٰلِحِينَ ٨٦Ndipo Ife tidawalowetsa m’chisomo chathu. Ndithudi iwo adali anthu olungama وَذَا ٱلنُّونِ إِذ ذَّهَبَ مُغَٰضِبًا فَظَنَّ أَن لَّن نَّقۡدِرَ عَلَيۡهِ فَنَادَىٰ فِي ٱلظُّلُمَٰتِ أَن لَّآ إِلَٰهَ إِلَّآ أَنتَ سُبۡحَٰنَكَ إِنِّي كُنتُ مِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ ٨٧Ndi dhan-Nun pamene adachoka mokwiya kwambiri chifukwa iye adali kuganiza kuti Ife sitingamulenge iye. Koma mu mdima iye adaitana, “Kulibe Mulungu wina koma Inu nokha. Ulemerero ukhale kwa Inu! Ndithudi ine ndidali mmodzi mwa anthu olakwa!” فَٱسۡتَجَبۡنَا لَهُۥ وَنَجَّيۡنَٰهُ مِنَ ٱلۡغَمِّۚ وَكَذَٰلِكَ نُـۨجِي ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٨٨Motero Ife tidayankha pempho lake ndipo tidamupulumutsa ku mavuto ake. Motero ndimo mmene timapulumutsira anthu okhulupirira وَزَكَرِيَّآ إِذۡ نَادَىٰ رَبَّهُۥ رَبِّ لَا تَذَرۡنِي فَرۡدًا وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلۡوَٰرِثِينَ ٨٩Ndi Zakariya pamene anaitana Ambuye wake nati, “Ambuye wanga! Musandileke ndekha. Ndipo Inu ndinu wabwinomwaokhalitsaonse.” فَٱسۡتَجَبۡنَا لَهُۥ وَوَهَبۡنَا لَهُۥ يَحۡيَىٰ وَأَصۡلَحۡنَا لَهُۥ زَوۡجَهُۥٓۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ يُسَٰرِعُونَ فِي ٱلۡخَيۡرَٰتِ وَيَدۡعُونَنَا رَغَبًا وَرَهَبًاۖ وَكَانُواْ لَنَا خَٰشِعِينَ ٩٠Motero Ifetidamuyankha pempho lake ndipo tidamupatsa Yohane ndipo tidathetsa uchumba wa mkazi wake. Ndithudi iwo adali ofulumira pochita ntchito zabwino ndipo amatipempha Ife ndi chikhulupiriro ndi mantha ndiponso amadzichepetsa kwa Ife وَٱلَّتِيٓ أَحۡصَنَتۡ فَرۡجَهَا فَنَفَخۡنَا فِيهَا مِن رُّوحِنَا وَجَعَلۡنَٰهَا وَٱبۡنَهَآ ءَايَةً لِّلۡعَٰلَمِينَ ٩١Adali mkazi amene adasunga unamwali wake. Ife tidauzira mwa iye ndipo tidamupanga iye pamodzi ndi mwana wake wa mwamuna kukhala chizindikiro kwa zolengedwa zonse إِنَّ هَٰذِهِۦٓ أُمَّتُكُمۡ أُمَّةً وَٰحِدَةً وَأَنَا۠ رَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُونِ ٩٢Ndithudi! Ichi ndi chipembedzo chanu ndipo ndi chipembedzo chimodzi, ndipo Ine ndine Ambuye wanu motero ndipembedzeni Ine ndekha وَتَقَطَّعُوٓاْ أَمۡرَهُم بَيۡنَهُمۡۖ كُلٌّ إِلَيۡنَا رَٰجِعُونَ ٩٣Ndipo iwo adapatukana ndi kugawa chipembedzo chawo pakati pawo ndipo ndi kwa Ife kumene adzabwerera فَمَن يَعۡمَلۡ مِنَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَهُوَ مُؤۡمِنٌ فَلَا كُفۡرَانَ لِسَعۡيِهِۦ وَإِنَّا لَهُۥ كَٰتِبُونَ ٩٤Motero aliyense amene achita ntchito zabwino ndipo ndi wokhulupirira moona ntchito zake sizidzakanidwa ayi. Ndithudi Ife timazilemba zonse m’Buku la chiwerengero وَحَرَٰمٌ عَلَىٰ قَرۡيَةٍ أَهۡلَكۡنَٰهَآ أَنَّهُمۡ لَا يَرۡجِعُونَ ٩٥Ndipo ndi koletsedwa kuti mudzi umene tidawuwononga kuti ubwererenso حَتَّىٰٓ إِذَا فُتِحَتۡ يَأۡجُوجُ وَمَأۡجُوجُ وَهُم مِّن كُلِّ حَدَبٍ يَنسِلُونَ ٩٦Mpaka pamene anthu a Ya-juj ndi Majuj adzamasulidwa ndipo iwo adzakhala akutsika kuchokera kumalo aliwonse wokwera وَٱقۡتَرَبَ ٱلۡوَعۡدُ ٱلۡحَقُّ فَإِذَا هِيَ شَٰخِصَةٌ أَبۡصَٰرُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يَٰوَيۡلَنَا قَدۡ كُنَّا فِي غَفۡلَةٍ مِّنۡ هَٰذَا بَلۡ كُنَّا ظَٰلِمِينَ ٩٧Ndipo pamene lonjezo loona lidzafika, maso a anthu onse osakhulupirira adzapenyetsetsa mwamantha nati “Tsoka kwa ife! Ndithudi ife tidali osalabadira zimenezi. Zoonadi ife tidali ochita zoipa.” إِنَّكُمۡ وَمَا تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ حَصَبُ جَهَنَّمَ أَنتُمۡ لَهَا وَٰرِدُونَ ٩٨Ndithudi! Inu pamodzi ndi zimene mukupembedza kuonjezera pa Mulungu, mudzakhala nkhuni za ku Gahena! Kumeneko nonse mudzalowako لَوۡ كَانَ هَٰٓؤُلَآءِ ءَالِهَةً مَّا وَرَدُوهَاۖ وَكُلٌّ فِيهَا خَٰلِدُونَ ٩٩Iyo ikadakhala milungu, siikadalowa kumeneko ndipo onse adzakhala kumeneko لَهُمۡ فِيهَا زَفِيرٌ وَهُمۡ فِيهَا لَا يَسۡمَعُونَ ١٠٠Kumeneko iwo adzalira ndipo adzakhala osamva إِنَّ ٱلَّذِينَ سَبَقَتۡ لَهُم مِّنَّا ٱلۡحُسۡنَىٰٓ أُوْلَٰٓئِكَ عَنۡهَا مُبۡعَدُونَ ١٠١Ndithudi iwo amene tawaonetsera chifundo chathu, iwo adzakhala kutali ndi moto لَا يَسۡمَعُونَ حَسِيسَهَاۖ وَهُمۡ فِي مَا ٱشۡتَهَتۡ أَنفُسُهُمۡ خَٰلِدُونَ ١٠٢Iwo sadzamva mkokomo wake pamene iwo ali kumene mitima yawo imafuna mpaka kalekale لَا يَحۡزُنُهُمُ ٱلۡفَزَعُ ٱلۡأَكۡبَرُ وَتَتَلَقَّىٰهُمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ هَٰذَا يَوۡمُكُمُ ٱلَّذِي كُنتُمۡ تُوعَدُونَ ١٠٣Zoopsa sizidzawadandaulitsa ayi ndipo Angelo adzawalandira iwo nati,“Ili ndi tsiku lanu limene inu mudalonjezedwa.” يَوۡمَ نَطۡوِي ٱلسَّمَآءَ كَطَيِّ ٱلسِّجِلِّ لِلۡكُتُبِۚ كَمَا بَدَأۡنَآ أَوَّلَ خَلۡقٍ نُّعِيدُهُۥۚ وَعۡدًا عَلَيۡنَآۚ إِنَّا كُنَّا فَٰعِلِينَ ١٠٤Tsiku limene tidzapinde thambo monga momwe timapindira tsamba la Buku. Monga momwe tidayamba chilengedwe choyamba momwemonso tidzachibwezeranso. Ili, ndithudi, ndi lonjezo kwa Ife. Ndithudi, Ife, tidzachita motero وَلَقَدۡ كَتَبۡنَا فِي ٱلزَّبُورِ مِنۢ بَعۡدِ ٱلذِّكۡرِ أَنَّ ٱلۡأَرۡضَ يَرِثُهَا عِبَادِيَ ٱلصَّٰلِحُونَ ١٠٥Ndipo, ndithudi, Ife tidalemba m’Buku la Masalimo, motsatira chikumbutso kuti akapolo anga angwiro adzakhala ku dziko lapansi إِنَّ فِي هَٰذَا لَبَلَٰغًا لِّقَوۡمٍ عَٰبِدِينَ ١٠٦Ndithudi mu ili muli Uthenga womveka kwa anthu amene amapembedza Mulungu وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا رَحۡمَةً لِّلۡعَٰلَمِينَ ١٠٧Ndipo sitidakutumize iwe pa chifukwa china koma ngati madalitso kwa zolengedwa zonse قُلۡ إِنَّمَا يُوحَىٰٓ إِلَيَّ أَنَّمَآ إِلَٰهُكُمۡ إِلَٰهٌ وَٰحِدٌۖ فَهَلۡ أَنتُم مُّسۡلِمُونَ ١٠٨Nena, “Zavumbulutsidwa kwa ine kuti Mulungu wanu ndi mmodzi yekha. Kodi inu mudzadzipereka kwa Iye?” فَإِن تَوَلَّوۡاْ فَقُلۡ ءَاذَنتُكُمۡ عَلَىٰ سَوَآءٍۖ وَإِنۡ أَدۡرِيٓ أَقَرِيبٌ أَم بَعِيدٌ مَّا تُوعَدُونَ ١٠٩Koma ngati iwo safuna kumvera nena, “Ine ndili kukuchenjezani kuti tonse tidziwe. Ine sindidziwa kuti chimene mwalonjezedwa chidza msanga kapena chikadali patali.” إِنَّهُۥ يَعۡلَمُ ٱلۡجَهۡرَ مِنَ ٱلۡقَوۡلِ وَيَعۡلَمُ مَا تَكۡتُمُونَ ١١٠Ndithudi Mulungu amadziwa zonse zimene mumayankhula mokweza ndipo amadziwanso zimene mubisa وَإِنۡ أَدۡرِي لَعَلَّهُۥ فِتۡنَةٌ لَّكُمۡ وَمَتَٰعٌ إِلَىٰ حِينٍ ١١١Ndipo ine sindidziwa ngati awa ndi mayeso kwa inu ndi chisangalalo cha kanthawi kochepa قَٰلَ رَبِّ ٱحۡكُم بِٱلۡحَقِّۗ وَرَبُّنَا ٱلرَّحۡمَٰنُ ٱلۡمُسۡتَعَانُ عَلَىٰ مَا تَصِفُونَ ١١٢Iye anati, “Ambuye wanga! Weruzani mwachilungamo! Ambuye wathu ndi Mwini chisoni chosatha amene chithandizo chake chimafunika pa zimene inu muonjezera.”

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.