Millat al-Islam

Chapter 20 · 135 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Ta-ha in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah Ta-ha (1340 reciters)
Meccanسورة طه135 verses

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

طه ١Ta Ha مَآ أَنزَلۡنَا عَلَيۡكَ ٱلۡقُرۡءَانَ لِتَشۡقَىٰٓ ٢Ife sitidavumbulutse Korani ino kwa iwe ndi cholinga choti uvutike إِلَّا تَذۡكِرَةً لِّمَن يَخۡشَىٰ ٣Koma kuti chikhale chilangizo kwa anthu oopa Mulungu تَنزِيلًا مِّمَّنۡ خَلَقَ ٱلۡأَرۡضَ وَٱلسَّمَٰوَٰتِ ٱلۡعُلَى ٤Ndi chivumbulutso chochokera kwa Iye amene adalenga dziko lapansi ndi kumwamba kwenikweniko ٱلرَّحۡمَٰنُ عَلَى ٱلۡعَرۡشِ ٱسۡتَوَىٰ ٥Mwini chisoni chosatha amene adaoneka ali pamwamba pa Mpando wa Chifumu لَهُۥ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا وَمَا تَحۡتَ ٱلثَّرَىٰ ٦Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zonse zimene zimakhala m’menemo ndiponso zimene zili pansi pa nthaka وَإِن تَجۡهَرۡ بِٱلۡقَوۡلِ فَإِنَّهُۥ يَعۡلَمُ ٱلسِّرَّ وَأَخۡفَى ٧Ngati iwe utchula mawu mokweza, ndithudi Iye amadziwa chinsinsi ndiponso chobisika ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ لَهُ ٱلۡأَسۡمَآءُ ٱلۡحُسۡنَىٰ ٨Mulungu! Kulibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye yekha. Ake ndi mayina okongola وَهَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ مُوسَىٰٓ ٩Kodi udamva za mbiri ya Mose إِذۡ رَءَا نَارًا فَقَالَ لِأَهۡلِهِ ٱمۡكُثُوٓاْ إِنِّيٓ ءَانَسۡتُ نَارًا لَّعَلِّيٓ ءَاتِيكُم مِّنۡهَا بِقَبَسٍ أَوۡ أَجِدُ عَلَى ٱلنَّارِ هُدًى ١٠Pamene iye adaona moto adawauza abale ake kuti, “Dikirani! Ndithudi ine ndaona moto. Mwina ndikubweretserani muuni kuti ndipeze ulangizi pa motopo.” فَلَمَّآ أَتَىٰهَا نُودِيَ يَٰمُوسَىٰٓ ١١Pamene iye adafika pafupi ndi moto, adaitanidwa pomutchula dzina lake kuti, “Oh Mose!” إِنِّيٓ أَنَا۠ رَبُّكَ فَٱخۡلَعۡ نَعۡلَيۡكَ إِنَّكَ بِٱلۡوَادِ ٱلۡمُقَدَّسِ طُوًى ١٢“Ndithudi, Ine ndine Ambuye wako! Motero chotsa nsapato zako. Ndithudi iwe uli m’dambo lodalitsika la Tuwa.” وَأَنَا ٱخۡتَرۡتُكَ فَٱسۡتَمِعۡ لِمَا يُوحَىٰٓ ١٣“Ndipo Ine ndakusankha iwe. Kotero mvetsera chimene chikuvumbulutsidwa kwa iwe.” إِنَّنِيٓ أَنَا ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّآ أَنَا۠ فَٱعۡبُدۡنِي وَأَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ لِذِكۡرِيٓ ١٤Ndithudi Ine ndine Mulungu. Palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine ndekha motero ndipembedze Ine ndipo pitiriza mapemphero pondikumbukira Ine.” إِنَّ ٱلسَّاعَةَ ءَاتِيَةٌ أَكَادُ أُخۡفِيهَا لِتُجۡزَىٰ كُلُّ نَفۡسِۭ بِمَا تَسۡعَىٰ ١٥“Ndithudi ola lili nkudza ndipo cholinga changa ndi kulibisa kuti mzimu ulionse udzalipidwe malipiro molingana ndi ntchito zake.” فَلَا يَصُدَّنَّكَ عَنۡهَا مَن لَّا يُؤۡمِنُ بِهَا وَٱتَّبَعَ هَوَىٰهُ فَتَرۡدَىٰ ١٦“Ndipo usalole kuti munthu amene sakhulupirira za olali ndipo yemwe amachita zimene mtima wake umafuna kuti akusocheretse chifukwa ukhoza kuonongeka.” وَمَا تِلۡكَ بِيَمِينِكَ يَٰمُوسَىٰ ١٧“Kodi ndi chiyani chimene chili m’dzanja lako la manja iwe Mose?” قَالَ هِيَ عَصَايَ أَتَوَكَّؤُاْ عَلَيۡهَا وَأَهُشُّ بِهَا عَلَىٰ غَنَمِي وَلِيَ فِيهَا مَـَٔارِبُ أُخۡرَىٰ ١٨Iye adati, “Iyi ndi ndodo yanga, ndi iyoyi ine ndimayedzamira ndipo ndimagwetsera masamba akudya nyama zanga. Imeneyi imandithandiza pa ntchito zambiri kuonjezera pa zimenezi.” قَالَ أَلۡقِهَا يَٰمُوسَىٰ ١٩Mulungu adati, “Ndodoyo iponye pansi iwe Mose.” فَأَلۡقَىٰهَا فَإِذَا هِيَ حَيَّةٌ تَسۡعَىٰ ٢٠Mose adaiponya pansi, ndipo taonani! Iyo idasanduka njoka yoyenda mwaliwiro قَالَ خُذۡهَا وَلَا تَخَفۡۖ سَنُعِيدُهَا سِيرَتَهَا ٱلۡأُولَىٰ ٢١Mulungu adati, “Igwire ndipo usachite mantha ayi. Ife tidzaibwezera monga momwe idalili poyamba.” وَٱضۡمُمۡ يَدَكَ إِلَىٰ جَنَاحِكَ تَخۡرُجۡ بَيۡضَآءَ مِنۡ غَيۡرِ سُوٓءٍ ءَايَةً أُخۡرَىٰ ٢٢“Tsopano kanikiza dzanja lako m’khwapa mwako. Ilo lidzasanduka loyera lopanda matenda ngati chizindikiro china.” لِنُرِيَكَ مِنۡ ءَايَٰتِنَا ٱلۡكُبۡرَى ٢٣“Kuti tikusonyeze zizindikiro zathu zazikulu.” ٱذۡهَبۡ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ إِنَّهُۥ طَغَىٰ ٢٤“Pita kwa Farawo! Ndithudi iye wadumpha malire onse.” قَالَ رَبِّ ٱشۡرَحۡ لِي صَدۡرِي ٢٥Mose adati, “Ambuye tsekulani chifuwa changa” وَيَسِّرۡ لِيٓ أَمۡرِي ٢٦“Ndipo pepukitsani ntchito yanga.” وَٱحۡلُلۡ عُقۡدَةً مِّن لِّسَانِي ٢٧“Masulani lilime langa ku chibwibwi.” يَفۡقَهُواْ قَوۡلِي ٢٨“Kuti anthu azindikire zonena zanga.” وَٱجۡعَل لِّي وَزِيرًا مِّنۡ أَهۡلِي ٢٩“Ndipo ndisankhileni munthu wondithandiza kuchokera ku banja langa.” هَٰرُونَ أَخِي ٣٠“Aroni m’bale wanga.” ٱشۡدُدۡ بِهِۦٓ أَزۡرِي ٣١“Onjezereni mphamvu zanga ndi iye.” وَأَشۡرِكۡهُ فِيٓ أَمۡرِي ٣٢“Ndipo muloleni nayenso kugwira ntchito yanga.” كَيۡ نُسَبِّحَكَ كَثِيرًا ٣٣“Kuti tizikulemekezani kwambiri.” وَنَذۡكُرَكَ كَثِيرًا ٣٤“Ndi kukukumbukirani kwambiri.” إِنَّكَ كُنتَ بِنَا بَصِيرًا ٣٥“Ndithudi! Inu muli kutiona nthawi zonse.” قَالَ قَدۡ أُوتِيتَ سُؤۡلَكَ يَٰمُوسَىٰ ٣٦Mulungu adati, “Pempho lako lalandiridwa, iwe Mose.” وَلَقَدۡ مَنَنَّا عَلَيۡكَ مَرَّةً أُخۡرَىٰٓ ٣٧“Ndithudi Ife tidakuonetsa chifundo chathu nthawi ina.” إِذۡ أَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰٓ أُمِّكَ مَا يُوحَىٰٓ ٣٨“Pamene tidawauza Amayi ako mawu athu.” أَنِ ٱقۡذِفِيهِ فِي ٱلتَّابُوتِ فَٱقۡذِفِيهِ فِي ٱلۡيَمِّ فَلۡيُلۡقِهِ ٱلۡيَمُّ بِٱلسَّاحِلِ يَأۡخُذۡهُ عَدُوٌّ لِّي وَعَدُوٌّ لَّهُۥۚ وَأَلۡقَيۡتُ عَلَيۡكَ مَحَبَّةً مِّنِّي وَلِتُصۡنَعَ عَلَىٰ عَيۡنِيٓ ٣٩Ponena kuti, “Ika mwana wako m’bokosi ndipo umuponye mu mtsinje ndipo mtsinje udzamulavula iye pa mtunda ndipo adzatoledwa ndi mdani wanga ndiponso ndi mdani wake. Ndipo Ine ndidaonetsa chikondi changa pa iwe kuti uleredwa moyang’aniridwa ndi Ine.” إِذۡ تَمۡشِيٓ أُخۡتُكَ فَتَقُولُ هَلۡ أَدُلُّكُمۡ عَلَىٰ مَن يَكۡفُلُهُۥۖ فَرَجَعۡنَٰكَ إِلَىٰٓ أُمِّكَ كَيۡ تَقَرَّ عَيۡنُهَا وَلَا تَحۡزَنَۚ وَقَتَلۡتَ نَفۡسًا فَنَجَّيۡنَٰكَ مِنَ ٱلۡغَمِّ وَفَتَنَّٰكَ فُتُونًاۚ فَلَبِثۡتَ سِنِينَ فِيٓ أَهۡلِ مَدۡيَنَ ثُمَّ جِئۡتَ عَلَىٰ قَدَرٍ يَٰمُوسَىٰ ٤٠“Ndipo pamene mlongo wako adapita kwa iwo ndi kunena kuti, Kodi ndikusonyezeni Mayi amene akhoza kumusamala iye? M’menemo ndi mmene tidakubwezera kwa Amayi ako kuti mtima wawo ukhoza kukhazikika ndipo kuti asakhumudwe. Ndipo pamene iwe udapha munthu, Ife tidakupulumutsa ku mavuto ako, ndipo tidakuyesa ndi mayeso ena. Iwe udakhala pakati pa anthu a ku Midiyani zaka zambiri ndipo pomaliza, iwe Mose, udabwera kuno monga momwe zidakonzedwera.” وَٱصۡطَنَعۡتُكَ لِنَفۡسِي ٤١“Ine ndakusankha iwe kuti unditumikire Ine.” ٱذۡهَبۡ أَنتَ وَأَخُوكَ بِـَٔايَٰتِي وَلَا تَنِيَا فِي ذِكۡرِي ٤٢“Pita iwe ndi m’bale wako ndi zizindikiro zanga ndipo musatope pondikumbukira Ine.” ٱذۡهَبَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ إِنَّهُۥ طَغَىٰ ٤٣“Pitani, nonsenu, kwa Farawo yemwe wadumpha malire.” فَقُولَا لَهُۥ قَوۡلًا لَّيِّنًا لَّعَلَّهُۥ يَتَذَكَّرُ أَوۡ يَخۡشَىٰ ٤٤“Ndipo mukayankhule naye ndi mawu oleza kuti mwina akhoza kumva chenjezo kapena kuopa Mulungu.” قَالَا رَبَّنَآ إِنَّنَا نَخَافُ أَن يَفۡرُطَ عَلَيۡنَآ أَوۡ أَن يَطۡغَىٰ ٤٥Iwo adati, “Ambuye wathu! Ndithudi! Ife tiopa kuti abweretsa chilango chake msanga kapena achita zoipa zambiri kwa ife.” قَالَ لَا تَخَافَآۖ إِنَّنِي مَعَكُمَآ أَسۡمَعُ وَأَرَىٰ ٤٦Iye adati, “Musaope! Ndithudi! Ine ndili pamodzi ndi inu. Ine ndimamva zonse ndipo ndimaona.” فَأۡتِيَاهُ فَقُولَآ إِنَّا رَسُولَا رَبِّكَ فَأَرۡسِلۡ مَعَنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَلَا تُعَذِّبۡهُمۡۖ قَدۡ جِئۡنَٰكَ بِـَٔايَةٍ مِّن رَّبِّكَۖ وَٱلسَّلَٰمُ عَلَىٰ مَنِ ٱتَّبَعَ ٱلۡهُدَىٰٓ ٤٧“Motero pitani nonse kwa iye ndipo mukati, ‘Ndithudi ife ndife Atumwi Ambuye wako motero aleke ana a Israyeli kuti apite ndi ife ndipo usawazunzenso ayi. Ndithudi ife takubweretsera zizindikiro zochokera kwa Ambuye wako! Ndipo mtendere udzakhala kwa iye amene atsatira langizo.” إِنَّا قَدۡ أُوحِيَ إِلَيۡنَآ أَنَّ ٱلۡعَذَابَ عَلَىٰ مَن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ ٤٨“Ndithudi zavumbulutsidwa kwa ife kuti chilango chake chidzagwa pa iye amene amakana zizindikiro zake ndipo sazimvera ayi.” قَالَ فَمَن رَّبُّكُمَا يَٰمُوسَىٰ ٤٩Farawo adati, “Kodi Mose, Ambuye wanu ndani?” قَالَ رَبُّنَا ٱلَّذِيٓ أَعۡطَىٰ كُلَّ شَيۡءٍ خَلۡقَهُۥ ثُمَّ هَدَىٰ ٥٠Iye adati, “Ambuye wathu ndiye amene adapereka maonekedwe osiyanasiyana ku zolengedwa zake ndipo adazilangiza bwinobwino.” قَالَ فَمَا بَالُ ٱلۡقُرُونِ ٱلۡأُولَىٰ ٥١Farawo adati, “Nanga zinali bwanji ndi anthu a masiku akale?” قَالَ عِلۡمُهَا عِندَ رَبِّي فِي كِتَٰبٍۖ لَّا يَضِلُّ رَبِّي وَلَا يَنسَى ٥٢Iye adati, “Ambuye wanga yekha ndiye amene adziwa zimenezo ndipo zidalembedwa mu Buku lake. Iye salakwa ndiponso saiwala.” ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ مَهۡدًا وَسَلَكَ لَكُمۡ فِيهَا سُبُلًا وَأَنزَلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءً فَأَخۡرَجۡنَا بِهِۦٓ أَزۡوَٰجًا مِّن نَّبَاتٍ شَتَّىٰ ٥٣Amene adakupangirani dziko lapansi kukhala ngati kama ndipo adakhazikitsa njira zoti inu muziyendamo ndipo watumiza mvula kuchokera kumwamba. Ndipo ameretsa ndi iyo mitundu yosiyanasiyana ya mbewu كُلُواْ وَٱرۡعَوۡاْ أَنۡعَٰمَكُمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّأُوْلِي ٱلنُّهَىٰ ٥٤Idyani ndiponso dyetsani ziweto zanu. Ndithudi muzimenezi muli zizindikiro kwa anthu ozindikira ۞ مِنۡهَا خَلَقۡنَٰكُمۡ وَفِيهَا نُعِيدُكُمۡ وَمِنۡهَا نُخۡرِجُكُمۡ تَارَةً أُخۡرَىٰ ٥٥Kuchokera ku dothi tidakulengani inu ndipo ndi ku nthaka kumene tidzakubwezerani ndipo kuchoka ku iyo tidzakuutsani kuti mukhalenso ndi moyo kachiwiri وَلَقَدۡ أَرَيۡنَٰهُ ءَايَٰتِنَا كُلَّهَا فَكَذَّبَ وَأَبَىٰ ٥٦Ndithudi tidamulangiza Farawo zizindikiro ndi umboni wathu koma iye adazikana zonse ndipo sadamvere ayi قَالَ أَجِئۡتَنَا لِتُخۡرِجَنَا مِنۡ أَرۡضِنَا بِسِحۡرِكَ يَٰمُوسَىٰ ٥٧Iye adati, “Kodi iwe Mose wadza kudzatichotsa m’dziko lathu ndi matsenga ako?” فَلَنَأۡتِيَنَّكَ بِسِحۡرٍ مِّثۡلِهِۦ فَٱجۡعَلۡ بَيۡنَنَا وَبَيۡنَكَ مَوۡعِدًا لَّا نُخۡلِفُهُۥ نَحۡنُ وَلَآ أَنتَ مَكَانًا سُوًى ٥٨“Ndithudi ife tikhoza kukubweretsera matsenga olingana ndi ako. Motero sankha tsiku limene ife kapena iwe siudzalephera kusunga loti tidzakumane iwe ndi ife, pa bwalo pamene tonse tidzakhala ndi mwai wofanana.” قَالَ مَوۡعِدُكُمۡ يَوۡمُ ٱلزِّينَةِ وَأَن يُحۡشَرَ ٱلنَّاسُ ضُحًى ٥٩Mose adati, “Tsiku lokumana lidzakhale tsiku la chisangalalo ndipo anthu adzasonkhanitsidwe nthawi ya ku m’mawa dzuwa litakwera pang’ono.” فَتَوَلَّىٰ فِرۡعَوۡنُ فَجَمَعَ كَيۡدَهُۥ ثُمَّ أَتَىٰ ٦٠Farawo adachokapo ndipo adasonkhanitsa a matsenga ake ndipo adadza nawo kwa Mose قَالَ لَهُم مُّوسَىٰ وَيۡلَكُمۡ لَا تَفۡتَرُواْ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا فَيُسۡحِتَكُم بِعَذَابٍۖ وَقَدۡ خَابَ مَنِ ٱفۡتَرَىٰ ٦١Mose adati kwa iwo, “Tsoka kwa inu! Musapeke mabodza okhudza Mulungu chifukwa akhoza kukuonongani ndi chilango. Ndipo, ndithudi, aliyense amene apeka bodza adzalephera mochititsa manyazi فَتَنَٰزَعُوٓاْ أَمۡرَهُم بَيۡنَهُمۡ وَأَسَرُّواْ ٱلنَّجۡوَىٰ ٦٢Anthu a matsenga adakambirana wina ndi mnzake pa zimene angachite ndipo adasunga zokambirana zawo قَالُوٓاْ إِنۡ هَٰذَٰنِ لَسَٰحِرَٰنِ يُرِيدَانِ أَن يُخۡرِجَاكُم مِّنۡ أَرۡضِكُم بِسِحۡرِهِمَا وَيَذۡهَبَا بِطَرِيقَتِكُمُ ٱلۡمُثۡلَىٰ ٦٣Iwo adati, “Anthu awiriwa ndi anthu a matsenga amene afuna kuti akuchotseni m’dziko lanu pogwiritsa ntchito matsenga awo ndikugonjetsa mafumu ndi anthu anu aulemu wawo.” فَأَجۡمِعُواْ كَيۡدَكُمۡ ثُمَّ ٱئۡتُواْ صَفًّاۚ وَقَدۡ أَفۡلَحَ ٱلۡيَوۡمَ مَنِ ٱسۡتَعۡلَىٰ ٦٤“Motero konzekani ndipo muime mu mzere. Iwo amene apambane lero, ndithudi, adzakhala opambanadi.” قَالُواْ يَٰمُوسَىٰٓ إِمَّآ أَن تُلۡقِيَ وَإِمَّآ أَن نَّكُونَ أَوَّلَ مَنۡ أَلۡقَىٰ ٦٥Iwo adati, “Iwe Mose! Kodi udzayamba ndiwe kuponya ndodo yako kapena tiyambe ndife kuponya ndodo zathu?” قَالَ بَلۡ أَلۡقُواْۖ فَإِذَا حِبَالُهُمۡ وَعِصِيُّهُمۡ يُخَيَّلُ إِلَيۡهِ مِن سِحۡرِهِمۡ أَنَّهَا تَسۡعَىٰ ٦٦Iye adati, “Iyayi. Ponyani zanu poyamba.” Ndipo taona ndi mphamvu ya matsenga awo, zingwe ndi ndodo zawo zidaoneka, m’maso mwa Mose, kuti zinali kuyenda mofulumira فَأَوۡجَسَ فِي نَفۡسِهِۦ خِيفَةً مُّوسَىٰ ٦٧Motero Mose adachita mantha mu mtima mwake قُلۡنَا لَا تَخَفۡ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡأَعۡلَىٰ ٦٨Koma Ife tidamuuza kuti, “Usaope! Ndithudi iwe udzapambana.” وَأَلۡقِ مَا فِي يَمِينِكَ تَلۡقَفۡ مَا صَنَعُوٓاْۖ إِنَّمَا صَنَعُواْ كَيۡدُ سَٰحِرٍۖ وَلَا يُفۡلِحُ ٱلسَّاحِرُ حَيۡثُ أَتَىٰ ٦٩“Ndipo ponya chimene chili m’dzanja lako la manja. Icho chidzameza zinthu zimene iwo akonza chimene ndi chinyengo cha matsenga ndipo munthu wa matsenga sadzapambana ngakhale atakhala odziwa chotani.” فَأُلۡقِيَ ٱلسَّحَرَةُ سُجَّدًا قَالُوٓاْ ءَامَنَّا بِرَبِّ هَٰرُونَ وَمُوسَىٰ ٧٠Anthu a matsenga adagwa pansi kulambira nati, “Ife takhulupirira mwa Ambuye wa Aroni ndi Mose.” قَالَ ءَامَنتُمۡ لَهُۥ قَبۡلَ أَنۡ ءَاذَنَ لَكُمۡۖ إِنَّهُۥ لَكَبِيرُكُمُ ٱلَّذِي عَلَّمَكُمُ ٱلسِّحۡرَۖ فَلَأُقَطِّعَنَّ أَيۡدِيَكُمۡ وَأَرۡجُلَكُم مِّنۡ خِلَٰفٍ وَلَأُصَلِّبَنَّكُمۡ فِي جُذُوعِ ٱلنَّخۡلِ وَلَتَعۡلَمُنَّ أَيُّنَآ أَشَدُّ عَذَابًا وَأَبۡقَىٰ ٧١Farawo adati, “Kodi inu mukumukhulupirira iye wopanda chilolezo changa? Ndithudi munthu uyu ayenera kukhala mkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga. Ndithudi ine ndidzadula manja anu ndi miyendo yanu mosiyanitsa ndipo, ndithudi, ine ndidzakupachikani pa thunthu la mtengo wa mgwalangwa. Ndipo, ndithudi, inu mudzadziwa kuti ndani mwa ife amene akhoza kupereka chilango chowawa kwambiri ndiponso chosatha.” قَالُواْ لَن نُّؤۡثِرَكَ عَلَىٰ مَا جَآءَنَا مِنَ ٱلۡبَيِّنَٰتِ وَٱلَّذِي فَطَرَنَاۖ فَٱقۡضِ مَآ أَنتَ قَاضٍۖ إِنَّمَا تَقۡضِي هَٰذِهِ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَآ ٧٢Iwo adati, “Ife sitifuna iwe kuposa zizindikiro zimene zadza kwa ife ndi Iye amene adatilenga ife. Kotero iwe chita chimene ufuna kuchita chifukwa iwe ukhoza kulamulira za m’moyo uno zokha.” إِنَّآ ءَامَنَّا بِرَبِّنَا لِيَغۡفِرَ لَنَا خَطَٰيَٰنَا وَمَآ أَكۡرَهۡتَنَا عَلَيۡهِ مِنَ ٱلسِّحۡرِۗ وَٱللَّهُ خَيۡرٌ وَأَبۡقَىٰٓ ٧٣“Ndithudi ife taika chikhulupiriro chathumwaAmbuyewathukutiatikhululukireifemachimo athu ndiponso pa matsenga amene udatikakamiza kuti tichite ndipo malipiro a Mulungu ndi abwino ndiponso osatha pofanizira ndi malipiro ako.” إِنَّهُۥ مَن يَأۡتِ رَبَّهُۥ مُجۡرِمًا فَإِنَّ لَهُۥ جَهَنَّمَ لَا يَمُوتُ فِيهَا وَلَا يَحۡيَىٰ ٧٤Ndithudi! Aliyense amene adza pamaso pa Ambuye wake ali wamachimo, ndithudi, iye adzaponyedwa ku Gahena kumene sadzakhala ndi moyo kapena imfa وَمَن يَأۡتِهِۦ مُؤۡمِنًا قَدۡ عَمِلَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَأُوْلَٰٓئِكَ لَهُمُ ٱلدَّرَجَٰتُ ٱلۡعُلَىٰ ٧٥Koma iye amene adza kwa Iye ndi chikhulupiriro choonadi ndiponso ntchito zabwino, adzakhala ndi ulemerero wapamwamba zedi جَنَّٰتُ عَدۡنٍ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ وَذَٰلِكَ جَزَآءُ مَن تَزَكَّىٰ ٧٦Minda yamuyaya yomwe pansi pake pamayenda mitsinje m’menemo iwo adzakhalamo nthawi zonse. Amenewa ndiwo malipiro a iwo amene amadziyeretsa وَلَقَدۡ أَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ أَنۡ أَسۡرِ بِعِبَادِي فَٱضۡرِبۡ لَهُمۡ طَرِيقًا فِي ٱلۡبَحۡرِ يَبَسًا لَّا تَخَٰفُ دَرَكًا وَلَا تَخۡشَىٰ ٧٧Ndithudi Ife tidamuuza Mose kuti, “Nyamuka nthawi yausiku pamodzi ndi akapolo anga ndipo uwatsekulire njira pakati pa nyanja ndipo usaope kuti akupeza, kapena kumira m’nyanja.” فَأَتۡبَعَهُمۡ فِرۡعَوۡنُ بِجُنُودِهِۦ فَغَشِيَهُم مِّنَ ٱلۡيَمِّ مَا غَشِيَهُمۡ ٧٨Ndipo Farawo adawatsatira ndi asirikali ake koma madzi adawamiza onse وَأَضَلَّ فِرۡعَوۡنُ قَوۡمَهُۥ وَمَا هَدَىٰ ٧٩Farawo adasocheretsa anthu ake ndipo sadawatsogolere ayi يَٰبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ قَدۡ أَنجَيۡنَٰكُم مِّنۡ عَدُوِّكُمۡ وَوَٰعَدۡنَٰكُمۡ جَانِبَ ٱلطُّورِ ٱلۡأَيۡمَنَ وَنَزَّلۡنَا عَلَيۡكُمُ ٱلۡمَنَّ وَٱلسَّلۡوَىٰ ٨٠oh Inu ana a Israyeli! Ife tidakupulumutsani inu kwa adani anu ndipo tidachita lonjezo ndi inu pambali yakumanja kwa Phiri ndipo tidakutsitsirani manna ndi mbalame zokoma كُلُواْ مِن طَيِّبَٰتِ مَا رَزَقۡنَٰكُمۡ وَلَا تَطۡغَوۡاْ فِيهِ فَيَحِلَّ عَلَيۡكُمۡ غَضَبِيۖ وَمَن يَحۡلِلۡ عَلَيۡهِ غَضَبِي فَقَدۡ هَوَىٰ ٨١Idyani zinthu zabwino zimene tidakupatsani ndipo musaswe malamulo chifukwa mkwiyo wanga ungagwe pa inu. Ndipo yense amene umpeza mkwiyo wanga ndithudi watha وَإِنِّي لَغَفَّارٌ لِّمَن تَابَ وَءَامَنَ وَعَمِلَ صَٰلِحًا ثُمَّ ٱهۡتَدَىٰ ٨٢Ndipo, ndithudi, Ine ndimakhululukira aliyense amene alapa, akhulupirira ndipo achita ntchito zabwino ndiponso apitiriza kuzichita ۞ وَمَآ أَعۡجَلَكَ عَن قَوۡمِكَ يَٰمُوسَىٰ ٨٣“Kodi Mose chakufulumizitsa kubwera kuno ndi kusiya anthu ako ndi chiyani?” قَالَ هُمۡ أُوْلَآءِ عَلَىٰٓ أَثَرِي وَعَجِلۡتُ إِلَيۡكَ رَبِّ لِتَرۡضَىٰ ٨٤Mose adati, “Iwo ali kumbuyo kwangaku akunditsatira. Ndadza mofulumira kwa Inu, Ambuye, kuti musangalale.” قَالَ فَإِنَّا قَدۡ فَتَنَّا قَوۡمَكَ مِنۢ بَعۡدِكَ وَأَضَلَّهُمُ ٱلسَّامِرِيُّ ٨٥Mulungu adati, “Ndithudi! Ife tawayesa mayeso anthu ako popembedza ng’ombe pamene iwe unachoka ndipo Msamiri wawasocheretsa.” فَرَجَعَ مُوسَىٰٓ إِلَىٰ قَوۡمِهِۦ غَضۡبَٰنَ أَسِفًاۚ قَالَ يَٰقَوۡمِ أَلَمۡ يَعِدۡكُمۡ رَبُّكُمۡ وَعۡدًا حَسَنًاۚ أَفَطَالَ عَلَيۡكُمُ ٱلۡعَهۡدُ أَمۡ أَرَدتُّمۡ أَن يَحِلَّ عَلَيۡكُمۡ غَضَبٌ مِّن رَّبِّكُمۡ فَأَخۡلَفۡتُم مَّوۡعِدِي ٨٦Mose adabwerera kwa anthu ake ndi mkwiyo ndiponso mwachisoni. Iye adati, “Anthu anga! Kodi Ambuye wanu sadakulonjezeni lonjezo labwino? Kodi munaona nthawi ya lonjezo kutalika? Kapena chinali cholinga chanu kuti mkwiyo wa Ambuye wanu udze pa inu ndipo inu muphwanye lonjezo lanu kwa ine?” قَالُواْ مَآ أَخۡلَفۡنَا مَوۡعِدَكَ بِمَلۡكِنَا وَلَٰكِنَّا حُمِّلۡنَآ أَوۡزَارًا مِّن زِينَةِ ٱلۡقَوۡمِ فَقَذَفۡنَٰهَا فَكَذَٰلِكَ أَلۡقَى ٱلسَّامِرِيُّ ٨٧Iwo adati, “Ife sitinaphwanye lonjezo lako pa chifukwa chathu ayi. Koma ife anatinyamulitsa katundu wa anthu, ndolo, ndipo tinaziponya pa moto. Zimenezo ndizo zimene Msamiri anatiuza.” فَأَخۡرَجَ لَهُمۡ عِجۡلًا جَسَدًا لَّهُۥ خُوَارٌ فَقَالُواْ هَٰذَآ إِلَٰهُكُمۡ وَإِلَٰهُ مُوسَىٰ فَنَسِيَ ٨٨Ndipo iye adawatulutsira iwo chifanizo cha thupi la ng’ombe chimene chidali ndi mawu. Iwo adati, “Uyu ndi mulungu wanu ndi mulungu wa Mose yemwe adamuiwala.” أَفَلَا يَرَوۡنَ أَلَّا يَرۡجِعُ إِلَيۡهِمۡ قَوۡلًا وَلَا يَمۡلِكُ لَهُمۡ ضَرًّا وَلَا نَفۡعًا ٨٩Kodi iwo sanaone kuti sichidawayankhe china chilichonse ndipo kuti chinalibe mphamvu yowapweteka kapena kuwathandiza iwo وَلَقَدۡ قَالَ لَهُمۡ هَٰرُونُ مِن قَبۡلُ يَٰقَوۡمِ إِنَّمَا فُتِنتُم بِهِۦۖ وَإِنَّ رَبَّكُمُ ٱلرَّحۡمَٰنُ فَٱتَّبِعُونِي وَأَطِيعُوٓاْ أَمۡرِي ٩٠Ndithudi Aroni adawauza iwo poyamba kuti, “Oh Anthu anga! Inu muli kungoyesedwa nacho ichi koma, ndithudi, Ambuye wanu ndiye Mwini chisoni chosatha motero tsatireni ine ndipo mverani malamulo anga.” قَالُواْ لَن نَّبۡرَحَ عَلَيۡهِ عَٰكِفِينَ حَتَّىٰ يَرۡجِعَ إِلَيۡنَا مُوسَىٰ ٩١Iwo adati, “Ife sitidzasiya kuchipembedza ichi mpaka pamene Mose adza kwa ife.” قَالَ يَٰهَٰرُونُ مَا مَنَعَكَ إِذۡ رَأَيۡتَهُمۡ ضَلُّوٓاْ ٩٢Mose adati, “oh Aroni! Kodi chidakuletsa ndi chiyani kuwatsutsa iwo pamene udaona kuti ali kusochera?” أَلَّا تَتَّبِعَنِۖ أَفَعَصَيۡتَ أَمۡرِي ٩٣“Kuti siunanditsatire ine. Kodi waswa lamulo langa?” قَالَ يَبۡنَؤُمَّ لَا تَأۡخُذۡ بِلِحۡيَتِي وَلَا بِرَأۡسِيٓۖ إِنِّي خَشِيتُ أَن تَقُولَ فَرَّقۡتَ بَيۡنَ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ وَلَمۡ تَرۡقُبۡ قَوۡلِي ٩٤Aroni adati, “Mwana wa Amayi anga! Usandikoke ndevu zanga kapena tsitsi langa! Ndithudi! Ine ndidali ndi mantha kuti mwina iwe ukhoza kudzanena kuti, iwe wabzala mpatuko pakati pa ana a Israyeli ndipo siunalemekeze mau anga.” قَالَ فَمَا خَطۡبُكَ يَٰسَٰمِرِيُّ ٩٥Mose adati, “Iwe Msamiri, kodi chifukwa chiyani udachita izi?” قَالَ بَصُرۡتُ بِمَا لَمۡ يَبۡصُرُواْ بِهِۦ فَقَبَضۡتُ قَبۡضَةً مِّنۡ أَثَرِ ٱلرَّسُولِ فَنَبَذۡتُهَا وَكَذَٰلِكَ سَوَّلَتۡ لِي نَفۡسِي ٩٦Iye adati, “Ine ndidaona zimene iwo sanali kuona. Motero ine ndidatenga dothi lodzala m’manja kuchokera ku fumbi lochokera ku phazi la Mtumwi ndi kulitaya. Kotero mzimu wanga udandikakamiza.” قَالَ فَٱذۡهَبۡ فَإِنَّ لَكَ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ أَن تَقُولَ لَا مِسَاسَۖ وَإِنَّ لَكَ مَوۡعِدًا لَّن تُخۡلَفَهُۥۖ وَٱنظُرۡ إِلَىٰٓ إِلَٰهِكَ ٱلَّذِي ظَلۡتَ عَلَيۡهِ عَاكِفًاۖ لَّنُحَرِّقَنَّهُۥ ثُمَّ لَنَنسِفَنَّهُۥ فِي ٱلۡيَمِّ نَسۡفًا ٩٧Mose adati, “Choka! Ndithudi chilango chako m’moyo uno ndi chakuti udzanena kuti, ‘Musandikhudze.’ Ndithudi iwe uli ndi lonjezo limene siliphwanyidwa ayi. Taona mulungu wako amene wamutumikira ndi mtima wako wonse. Ife tidzaliotcha m’moto ndipo tidzamwaza phulusa lake pa nyanja.” إِنَّمَآ إِلَٰهُكُمُ ٱللَّهُ ٱلَّذِي لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۚ وَسِعَ كُلَّ شَيۡءٍ عِلۡمًا ٩٨Mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi yekha. Iye amadziwa chilichonse كَذَٰلِكَ نَقُصُّ عَلَيۡكَ مِنۡ أَنۢبَآءِ مَا قَدۡ سَبَقَۚ وَقَدۡ ءَاتَيۡنَٰكَ مِن لَّدُنَّا ذِكۡرًا ٩٩Kotero Ife tili kukufotokozerani mbiri ya zinthu zimene zidachitika kale. Ndithudi takupatsa chikumbutso مَّنۡ أَعۡرَضَ عَنۡهُ فَإِنَّهُۥ يَحۡمِلُ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ وِزۡرًا ١٠٠Iwo amene adzachikana ndithudi adzanyamula katundu wolemera wamachimo pa tsiku la kuuka kwa akufa خَٰلِدِينَ فِيهِۖ وَسَآءَ لَهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ حِمۡلًا ١٠١Iwo adzakhala m’menemo mpaka kalekale ndipo zidzakhala zoipa kwambiri kwa iwo osenza katundu wotereyu tsiku la kuuka kwa kufa يَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِۚ وَنَحۡشُرُ ٱلۡمُجۡرِمِينَ يَوۡمَئِذٍ زُرۡقًا ١٠٢Tsiku limene lipenga lidzaimbidwa, patsiku limene Ife tidzasonkhanitsa anthu onse ochimwa, maso awo adzakhala obiriwira ndi nkhope zakuda يَتَخَٰفَتُونَ بَيۡنَهُمۡ إِن لَّبِثۡتُمۡ إِلَّا عَشۡرًا ١٠٣Monong’onezana adzakhala ali nkuyankhulana nati, “Inu simunakhale padziko lapansi kupatula masiku khumi okha.” نَّحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَا يَقُولُونَ إِذۡ يَقُولُ أَمۡثَلُهُمۡ طَرِيقَةً إِن لَّبِثۡتُمۡ إِلَّا يَوۡمًا ١٠٤Ife tili kudziwa kwambiri zimene adzayankhula, pamene anthu awo angwiro ndi anzeru adzati, “Inu simunakhale padziko kupatula tsiku limodzi lokha.” وَيَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلۡجِبَالِ فَقُلۡ يَنسِفُهَا رَبِّي نَسۡفًا ١٠٥“Ndipo iwo ali kukufunsa za mapiri. Nena, “Ambuye wanga adzawachotsa iwo ndi kuwamwaza ngati fumbi la dothi.” فَيَذَرُهَا قَاعًا صَفۡصَفًا ١٠٦“Ndipo iye adzawasiya kukhala ngati bwalo lasesese.” لَّا تَرَىٰ فِيهَا عِوَجًا وَلَآ أَمۡتًا ١٠٧“M’menemo sudzaona malo otsika kapena okwera.” يَوۡمَئِذٍ يَتَّبِعُونَ ٱلدَّاعِيَ لَا عِوَجَ لَهُۥۖ وَخَشَعَتِ ٱلۡأَصۡوَاتُ لِلرَّحۡمَٰنِ فَلَا تَسۡمَعُ إِلَّا هَمۡسًا ١٠٨Pa tsiku limeneli, anthu adzatsatira woitana wa Mulungu, mopanda chinyengo. Ndipo mawu onse adzachepetsedwa chifukwa cha Mwini chisoni ndipo iwe siudzamva china kupatula mgugu wochepa wa mapazi awo يَوۡمَئِذٍ لَّا تَنفَعُ ٱلشَّفَٰعَةُ إِلَّا مَنۡ أَذِنَ لَهُ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَرَضِيَ لَهُۥ قَوۡلًا ١٠٩Patsiku limeneli, palibe wina amene adzakhala ndi mphamvu yoyankhula m’malo mwawo kupatula yekhayo amene adzalandire chilolezo cha Mwini chisoni ndiponso amene mawu ake ngolandiridwa kwa Iye يَعۡلَمُ مَا بَيۡنَ أَيۡدِيهِمۡ وَمَا خَلۡفَهُمۡ وَلَا يُحِيطُونَ بِهِۦ عِلۡمًا ١١٠Amadziwa zonse zimene zili kutsogolo kwawo ndiponso zimene zili kumbuyo kwawo ndi zimene zili nkudza pamene iwo sadziwa china chilichonse cha Iye ۞ وَعَنَتِ ٱلۡوُجُوهُ لِلۡحَيِّ ٱلۡقَيُّومِۖ وَقَدۡ خَابَ مَنۡ حَمَلَ ظُلۡمًا ١١١Ndipo nkhope zonse zidzachepetsedwa pamaso pa Mwini moyo wa nthawi zonse amene amateteza china chilichonse. Ndipo yense amene analakwa, ndithudi, ndi olephera وَمَن يَعۡمَلۡ مِنَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَهُوَ مُؤۡمِنٌ فَلَا يَخَافُ ظُلۡمًا وَلَا هَضۡمًا ١١٢Ndipo iye amene achita ntchito zabwino ndipo ndi munthu wokhulupirira, iye sadzaopa kuponderezedwa kapena kumanidwa malipiro وَكَذَٰلِكَ أَنزَلۡنَٰهُ قُرۡءَانًا عَرَبِيًّا وَصَرَّفۡنَا فِيهِ مِنَ ٱلۡوَعِيدِ لَعَلَّهُمۡ يَتَّقُونَ أَوۡ يُحۡدِثُ لَهُمۡ ذِكۡرًا ١١٣Motero Ife tidatumiza Korani mu Chiarabu ndipo tafotokoza m’menemo mowirikiza machenjezo kuti iwo akhale oopa Mulungu kapena kuti Koraniyo iwapatse chiphunzitso kuchokera mu ilo فَتَعَٰلَى ٱللَّهُ ٱلۡمَلِكُ ٱلۡحَقُّۗ وَلَا تَعۡجَلۡ بِٱلۡقُرۡءَانِ مِن قَبۡلِ أَن يُقۡضَىٰٓ إِلَيۡكَ وَحۡيُهُۥۖ وَقُل رَّبِّ زِدۡنِي عِلۡمًا ١١٤Wolemekezeka ndi Mulungu, Mfumu ya choonadi! Ndipo usafulumire kulakatula Korani, chivumbulutso chake chisanathe koma uyenera kunena kuti, “Ambuye ndionjezereni nzeru.” وَلَقَدۡ عَهِدۡنَآ إِلَىٰٓ ءَادَمَ مِن قَبۡلُ فَنَسِيَ وَلَمۡ نَجِدۡ لَهُۥ عَزۡمًا ١١٥Ndithudi IfetidachitalonjezondiAdamukalekomaiye adaiwala ndipo sitinapeze chipiriro kwa iye وَإِذۡ قُلۡنَا لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ ٱسۡجُدُواْ لِأٓدَمَ فَسَجَدُوٓاْ إِلَّآ إِبۡلِيسَ أَبَىٰ ١١٦Pamenepo Ife tidawauza angelo kuti, “Mugwadireni Adamu.” Ndipo onse adamugwadira koma Satana adakana فَقُلۡنَا يَٰٓـَٔادَمُ إِنَّ هَٰذَا عَدُوٌّ لَّكَ وَلِزَوۡجِكَ فَلَا يُخۡرِجَنَّكُمَا مِنَ ٱلۡجَنَّةِ فَتَشۡقَىٰٓ ١١٧Ife tidati, “oh iwe Adamu! Ndithudi uyu ndi mdani wako ndiponso mdani wa mkazi wako. Musalole kuti akutulutseni ku Paradiso ndi kukukhazikani m’mavuto.” إِنَّ لَكَ أَلَّا تَجُوعَ فِيهَا وَلَا تَعۡرَىٰ ١١٨Ndithudi muli ndi lonjezo lathu kuti kumeneko inu simudzamva njala kapena kukhala wamaliseche وَأَنَّكَ لَا تَظۡمَؤُاْ فِيهَا وَلَا تَضۡحَىٰ ١١٩Ndiponso inu simudzamva ludzu m’menemo kapena kutentha kwa dzuwa فَوَسۡوَسَ إِلَيۡهِ ٱلشَّيۡطَٰنُ قَالَ يَٰٓـَٔادَمُ هَلۡ أَدُلُّكَ عَلَىٰ شَجَرَةِ ٱلۡخُلۡدِ وَمُلۡكٍ لَّا يَبۡلَىٰ ١٢٠Koma Satana adamunong’oneza nati, “Oh iwe Adamu! Kodi ndingakulangize mtengo wa moyo wosatha ndiponso ufumu wosatha?” فَأَكَلَا مِنۡهَا فَبَدَتۡ لَهُمَا سَوۡءَٰتُهُمَا وَطَفِقَا يَخۡصِفَانِ عَلَيۡهِمَا مِن وَرَقِ ٱلۡجَنَّةِۚ وَعَصَىٰٓ ءَادَمُ رَبَّهُۥ فَغَوَىٰ ١٢١Ndipo onse adadya chipatso cha mumtengo uja kotero udaonekera umaliseche wawo ndipo adayamba kudziveka masamba a m’munda muja. Kotero Adamu adanyoza lamulo la Ambuye wake ndipo adasochera ثُمَّ ٱجۡتَبَٰهُ رَبُّهُۥ فَتَابَ عَلَيۡهِ وَهَدَىٰ ١٢٢Ndipo Ambuye wake adamusankha iye ndipo adamukhululukira ndi kumutsogolera kunjira yoyenera قَالَ ٱهۡبِطَا مِنۡهَا جَمِيعَۢاۖ بَعۡضُكُمۡ لِبَعۡضٍ عَدُوٌّۖ فَإِمَّا يَأۡتِيَنَّكُم مِّنِّي هُدًى فَمَنِ ٱتَّبَعَ هُدَايَ فَلَا يَضِلُّ وَلَا يَشۡقَىٰ ١٢٣Mulungu adati, “Chokani inu m’menemo, nonse awiri, ndipo inu mudzakhala adani a wina ndi mnzake. Pamene ulangizi wanga udzavumbulutsidwa kwa inu, iye amene adzautsatira sadzasochera kapena kuona mavuto.” وَمَنۡ أَعۡرَضَ عَن ذِكۡرِي فَإِنَّ لَهُۥ مَعِيشَةً ضَنكًا وَنَحۡشُرُهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ أَعۡمَىٰ ١٢٤“Koma iye amene safuna kumvera machenjezo anga, ndithudi, adzakhala movutika ndipo tidzamuukitsa ali wakhungu pa tsiku louka kwa akufa.” قَالَ رَبِّ لِمَ حَشَرۡتَنِيٓ أَعۡمَىٰ وَقَدۡ كُنتُ بَصِيرًا ١٢٥Iye adzati, “Ambuye wanga! Bwanji mwandiukitsa wakhungu, pamene ine ndidali wopenya?” قَالَ كَذَٰلِكَ أَتَتۡكَ ءَايَٰتُنَا فَنَسِيتَهَاۖ وَكَذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمَ تُنسَىٰ ١٢٦Mulungu adzati, “Chifukwa chakuti pamene chivumbulutso chathu chinadza kwa iwe udachiiwala. Chimodzimodzi tsiku lino nawenso waiwalidwa.” وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي مَنۡ أَسۡرَفَ وَلَمۡ يُؤۡمِنۢ بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِۦۚ وَلَعَذَابُ ٱلۡأٓخِرَةِ أَشَدُّ وَأَبۡقَىٰٓ ١٢٧Mmenemundimmenetimalipiriramunthu oswa malamulo amene sakhulupirira chivumbulutso cha Ambuye wake. Koma chilango cha m’moyo umene uli nkudza ndi choopsa ndiponso chosatha أَفَلَمۡ يَهۡدِ لَهُمۡ كَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّنَ ٱلۡقُرُونِ يَمۡشُونَ فِي مَسَٰكِنِهِمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّأُوْلِي ٱلنُّهَىٰ ١٢٨Kodi iwo saona mibadwo ya anthu imene tidaiononga iwo asanadze? Iwo amayenda pakati pa nyumba zimene iwo anali kukhalamo. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu a nzeru وَلَوۡلَا كَلِمَةٌ سَبَقَتۡ مِن رَّبِّكَ لَكَانَ لِزَامًا وَأَجَلٌ مُّسَمًّى ١٢٩Akadakhala kuti Ambuye wako sadalonjeze ndi kukhazikitsa nthawi, chilango chawo chikanadza kale فَٱصۡبِرۡ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَسَبِّحۡ بِحَمۡدِ رَبِّكَ قَبۡلَ طُلُوعِ ٱلشَّمۡسِ وَقَبۡلَ غُرُوبِهَاۖ وَمِنۡ ءَانَآيِٕ ٱلَّيۡلِ فَسَبِّحۡ وَأَطۡرَافَ ٱلنَّهَارِ لَعَلَّكَ تَرۡضَىٰ ١٣٠Motero pirira pa zimene ali kunena ndipo lemekeza ndi kutamanda Ambuye wako dzuwa lisanatuluke ndiponso lisanalowe. Ndipo muyamike Iye nthawi yausiku ndi yausana kuti iwe udzasangalale وَلَا تَمُدَّنَّ عَيۡنَيۡكَ إِلَىٰ مَا مَتَّعۡنَا بِهِۦٓ أَزۡوَٰجًا مِّنۡهُمۡ زَهۡرَةَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا لِنَفۡتِنَهُمۡ فِيهِۚ وَرِزۡقُ رَبِّكَ خَيۡرٌ وَأَبۡقَىٰ ١٣١Usasirire zinthu zimene tawapatsa anthu chifukwa zimenezi ndi zosangalatsa za m’moyo uno. Ife tingofuna kuwayesa nazo. Koma mphotho ya Ambuye wako ndi yabwino ndipo ndi yosatha وَأۡمُرۡ أَهۡلَكَ بِٱلصَّلَوٰةِ وَٱصۡطَبِرۡ عَلَيۡهَاۖ لَا نَسۡـَٔلُكَ رِزۡقًاۖ نَّحۡنُ نَرۡزُقُكَۗ وَٱلۡعَٰقِبَةُ لِلتَّقۡوَىٰ ١٣٢Ndipo lamulira banja lako kupemphera ndipo ukhale wopirira pokwaniritsa mapemphero. Ife sitipempha zinthu kwa iwe koma Ife timakupatsa zofuna zako. Ndipo mapeto abwino ndi a anthu oopa Mulungu وَقَالُواْ لَوۡلَا يَأۡتِينَا بِـَٔايَةٍ مِّن رَّبِّهِۦٓۚ أَوَلَمۡ تَأۡتِهِم بَيِّنَةُ مَا فِي ٱلصُّحُفِ ٱلۡأُولَىٰ ١٣٣Iwo adati, “Bwanji iye satipatsa ife chizindikiro chochokera kwa Ambuye wake?” Kodi iwo sadapatsidwe zizindikiro zambiri zimene zili m’mabuku a kale a Mulungu وَلَوۡ أَنَّآ أَهۡلَكۡنَٰهُم بِعَذَابٍ مِّن قَبۡلِهِۦ لَقَالُواْ رَبَّنَا لَوۡلَآ أَرۡسَلۡتَ إِلَيۡنَا رَسُولًا فَنَتَّبِعَ ءَايَٰتِكَ مِن قَبۡلِ أَن نَّذِلَّ وَنَخۡزَىٰ ١٣٤Ngati Ife tikadawaononga iwo ndi chilango tisadawatumizire ichi, iwo akadati, “Ambuye wathu! Inu mukadatitumizira Mtumwi, ndithudi, ife tikadatsatira chivumbulutso chanu tisadanyozedwe ndi kuchititsidwa manyazi.” قُلۡ كُلٌّ مُّتَرَبِّصٌ فَتَرَبَّصُواْۖ فَسَتَعۡلَمُونَ مَنۡ أَصۡحَٰبُ ٱلصِّرَٰطِ ٱلسَّوِيِّ وَمَنِ ٱهۡتَدَىٰ ١٣٥Nena, “onse ali kudikira. Nanunso dikirani ndipo inu mudzadziwa kuti ndani amene adatsatira njira yoyenera ndiponso amene ali otsogozedwa.”

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.