Millat al-Islam

Chapter 84 · 25 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Inshiqaq in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah Al-Inshiqaq (1262 reciters)

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

إِذَا ٱلسَّمَآءُ ٱنشَقَّتۡ ١Pamene thambo lidzang’ambika وَأَذِنَتۡ لِرَبِّهَا وَحُقَّتۡ ٢Ndipo limva ndi kumvera Ambuye wake ndipo ling’ambikadi وَإِذَا ٱلۡأَرۡضُ مُدَّتۡ ٣Pamene nthaka idzatambasulidwa وَأَلۡقَتۡ مَا فِيهَا وَتَخَلَّتۡ ٤Ndi kutulutsa zonse zimene zinakwiriridwa m’kati mwake ndi kukhala yopanda kanthu وَأَذِنَتۡ لِرَبِّهَا وَحُقَّتۡ ٥Ndipo limva ndi kumvera Ambuye wake ndipo ling’ambikadi يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡإِنسَٰنُ إِنَّكَ كَادِحٌ إِلَىٰ رَبِّكَ كَدۡحًا فَمُلَٰقِيهِ ٦oh iwe munthu! Ndithudi iwe uli kubwerera kupita kwa Ambuye wako ndi ntchito zako. Kubwerera kotsimikizidwa. Motero udzakumana nazo فَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِيَمِينِهِۦ ٧Koma Iye amene adzapatsidwa Buku lake m’dzanja lamanja فَسَوۡفَ يُحَاسَبُ حِسَابًا يَسِيرًا ٨Adzawerengedwa mosavuta وَيَنقَلِبُ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ مَسۡرُورًا ٩Ndipo adzabwerera kwa anthu ake ndi chisangalalo وَأَمَّا مَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ وَرَآءَ ظَهۡرِهِۦ ١٠Koma iye amene adzapatsidwa buku lake kumbuyo kwake فَسَوۡفَ يَدۡعُواْ ثُبُورًا ١١Iye adzalira وَيَصۡلَىٰ سَعِيرًا ١٢Ndipo akalowa ku moto walawi – lawi ku Gahena إِنَّهُۥ كَانَ فِيٓ أَهۡلِهِۦ مَسۡرُورًا ١٣Ndithudi iye adali wansangala pakati pa anthu ake إِنَّهُۥ ظَنَّ أَن لَّن يَحُورَ ١٤Ndithudi iye anali kuganiza kuti sadzabwerera kwa Mulungu بَلَىٰٓۚ إِنَّ رَبَّهُۥ كَانَ بِهِۦ بَصِيرًا ١٥Inde! Ndithudi Ambuye wake anali kuona zonse zimene iye ankachita فَلَآ أُقۡسِمُ بِٱلشَّفَقِ ١٦Ine ndilumbira pali kufiira kwa kulowa kwa dzuwa وَٱلَّيۡلِ وَمَا وَسَقَ ١٧Ndi pali usiku ndi zonse zimene umabweretsa mu mdima وَٱلۡقَمَرِ إِذَا ٱتَّسَقَ ١٨Ndi pali mwezi pamene ufika pa chimake penipeni لَتَرۡكَبُنَّ طَبَقًا عَن طَبَقٍ ١٩Ndipo inu, ndithudi, mudzayenda kupita kutsogolo, kuchoka apa ndi kufika apo فَمَا لَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ ٢٠Kodi ndi chifukwa chiyani choti iwo alibe chikhulupiriro وَإِذَا قُرِئَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡقُرۡءَانُ لَا يَسۡجُدُونَۤ ۩ ٢١Ndipo pamene Korani ili kuwerengedwa kwa iwo sagwa pansi. Al-Buruj بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يُكَذِّبُونَ ٢٢Iyayi! Koma anthu osakhulupirira amalikana وَٱللَّهُ أَعۡلَمُ بِمَا يُوعُونَ ٢٣Ndipo Mulungu amadziwa zinthu zonse zimene amasonkhanitsa فَبَشِّرۡهُم بِعَذَابٍ أَلِيمٍ ٢٤Choncho auze iwo za chilango chowawa إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُمۡ أَجۡرٌ غَيۡرُ مَمۡنُونِۭ ٢٥Kupatula okhawo amene akhulupirira ndi kumachita ntchito zabwino, chifukwa iwo ali ndi malipiro opanda malire

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.