Millat al-Islam

Chapter 85 · 22 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah Al-Burooj in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah Al-Burooj (1318 reciters)
Meccanسورة البروج22 verses

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

وَٱلسَّمَآءِ ذَاتِ ٱلۡبُرُوجِ ١Pali kumwamba kumene kuli nyenyezi zikulu zikulu وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡمَوۡعُودِ ٢Pali tsiku lolonjezedwa وَشَاهِدٍ وَمَشۡهُودٍ ٣Pali tsiku la umboni ndi tsiku loperekedwa umboni قُتِلَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡأُخۡدُودِ ٤wotembereredwa anali anthu amene anakumba ngalande ٱلنَّارِ ذَاتِ ٱلۡوَقُودِ ٥Imene munali moto woyaka إِذۡ هُمۡ عَلَيۡهَا قُعُودٌ ٦Pamene akhala moizungulira وَهُمۡ عَلَىٰ مَا يَفۡعَلُونَ بِٱلۡمُؤۡمِنِينَ شُهُودٌ ٧Ndipo iwo adachitira umboni pa zomwe amachitira anthu okhulupirira وَمَا نَقَمُواْ مِنۡهُمۡ إِلَّآ أَن يُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَمِيدِ ٨Iwo analibe mlandu wina uliwonse ndi anthuwa kupatula kuti anali kukhulupirira mwa Mulungu mmodzi yekha, Mwini mphamvu zonse, Mwini kuyamikidwa ٱلَّذِي لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ شَهِيدٌ ٩Mwini Ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi! Ndipo Mulungu ndi mboni pa chilichonse إِنَّ ٱلَّذِينَ فَتَنُواْ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ ثُمَّ لَمۡ يَتُوبُواْ فَلَهُمۡ عَذَابُ جَهَنَّمَ وَلَهُمۡ عَذَابُ ٱلۡحَرِيقِ ١٠Ndithudi onse amene adazunza amuna okhulupirira, ndi akazi okhulupilira ndipo salapa machimo awo, adzalandira chilango chowawa cha moto woyaka wa ku Gahena إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَهُمۡ جَنَّٰتٌ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۚ ذَٰلِكَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡكَبِيرُ ١١Ndithu onse amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino adzakhala m’minda imene ili ndi mitsinje ya madzi oyenda. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu إِنَّ بَطۡشَ رَبِّكَ لَشَدِيدٌ ١٢Ndithudi chilango cha Ambuye wako ndi chowawa إِنَّهُۥ هُوَ يُبۡدِئُ وَيُعِيدُ ١٣Ndithudi Iye ndiye amene amayambitsa chilengedwe ndipo adzachibwereza patsiku louka kwa akufa وَهُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلۡوَدُودُ ١٤Ndipo Iye ndi wokhululuka ndi wachikondi chodzadza ذُو ٱلۡعَرۡشِ ٱلۡمَجِيدُ ١٥Mwini wake wa Mpando wachifumu, Wolemekezeka فَعَّالٌ لِّمَا يُرِيدُ ١٦Iye amachita chimene afuna هَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ ٱلۡجُنُودِ ١٧Kodi iwe siudamve za asirikali فِرۡعَوۡنَ وَثَمُودَ ١٨A Farao ndi a Thamoud بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فِي تَكۡذِيبٍ ١٩Iyayi! Koma anthu osakhulupirira amazikana وَٱللَّهُ مِن وَرَآئِهِم مُّحِيطُۢ ٢٠Ndipo Mulungu amawazungulira onse بَلۡ هُوَ قُرۡءَانٌ مَّجِيدٌ ٢١Iyayi! Ili ndi Buku loyera la Korani فِي لَوۡحٍ مَّحۡفُوظِۭ ٢٢Lolembedwa m’Buku lotetezedwa

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.