بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
عَمَّ يَتَسَآءَلُونَ ١Kodi akufunsana nkhani zotani عَنِ ٱلنَّبَإِ ٱلۡعَظِيمِ ٢Ali kufunsana za nkhani ija yaikulu ٱلَّذِي هُمۡ فِيهِ مُخۡتَلِفُونَ ٣Nkhani imene akusiyana maganizo pakati pawo كـَلَّا سَيَعۡلَمُونَ ٤Iyayi, iwo adzadziwa posachedwa ثُمَّ كـَلَّا سَيَعۡلَمُونَ ٥Iyayi, iwo adzadziwa posachedwapa أَلَمۡ نَجۡعَلِ ٱلۡأَرۡضَ مِهَٰدًا ٦Kodi Ife sitidapange dziko lapansi monga ngati kama وَٱلۡجِبَالَ أَوۡتَادًا ٧Ndi mapiri ngati zikhomo وَخَلَقۡنَٰكُمۡ أَزۡوَٰجًا ٨Ndipo Ife tidakulengani inu awiri awiri وَجَعَلۡنَا نَوۡمَكُمۡ سُبَاتًا ٩Ndipo tidapanga tulo kukhala ngati mpumulo wanu وَجَعَلۡنَا ٱلَّيۡلَ لِبَاسًا ١٠Ndipo tidapanga usiku kukhala chophimba وَجَعَلۡنَا ٱلنَّهَارَ مَعَاشًا ١١Ndipo tinapanga usana kukhala kopezera zofuna zanu وَبَنَيۡنَا فَوۡقَكُمۡ سَبۡعًا شِدَادًا ١٢Ndipo tidamanga mlengalenga miyamba isanu ndi iwiri وَجَعَلۡنَا سِرَاجًا وَهَّاجًا ١٣Ndipo tidakhazikitsa mmenemo nyali yowala وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلۡمُعۡصِرَٰتِ مَآءً ثَجَّاجًا ١٤Ndipo tidatumiza mvula yambiri kuchokera ku mitambo ya mvula لِّنُخۡرِجَ بِهِۦ حَبًّا وَنَبَاتًا ١٥Kuti timeretse chakudya ndi mbewu وَجَنَّٰتٍ أَلۡفَافًا ١٦Ndipo minda ya zomera zothinana إِنَّ يَوۡمَ ٱلۡفَصۡلِ كَانَ مِيقَٰتًا ١٧Ndithudi tsiku la chiweruzo lidakhazikitsidwa kale يَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِ فَتَأۡتُونَ أَفۡوَاجًا ١٨Tsiku limene lipenga lidzalira ndipo inu mudzadza mu magulumagulu وَفُتِحَتِ ٱلسَّمَآءُ فَكَانَتۡ أَبۡوَٰبًا ١٩Ndipomumlengalengamudzatsegulidwa ndipo mudzakhala ngati makomo وَسُيِّرَتِ ٱلۡجِبَالُ فَكَانَتۡ سَرَابًا ٢٠Ndipo mapiri onse adzayendetsedwa ndi kukhala ngati nthunzi yamadzi إِنَّ جَهَنَّمَ كَانَتۡ مِرۡصَادًا ٢١Ndithudi Gahena ili kuwayembekezera لِّلطَّٰغِينَ مَـَٔابًا ٢٢Mudzi wa anthu ophwanya malamulo لَّٰبِثِينَ فِيهَآ أَحۡقَابًا ٢٣Kumeneko ndiko kumene adzakhale mpaka kalekale لَّا يَذُوقُونَ فِيهَا بَرۡدًا وَلَا شَرَابًا ٢٤Kumeneko sadzalawa chozizira kapena kumwa china chilichonse إِلَّا حَمِيمًا وَغَسَّاقًا ٢٥Kupatula Al-Naba 637 madzi owira ndi mafinya جَزَآءً وِفَاقًا ٢٦Mphotho yoyeneradi إِنَّهُمۡ كَانُواْ لَا يَرۡجُونَ حِسَابًا ٢٧Chifukwa, ndithudi, iwo sanali kuopa chidzudzulo chathu وَكَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا كِذَّابًا ٢٨Ndipo iwo moyerekedwa anali kukana chivumbulutso chathu وَكُلَّ شَيۡءٍ أَحۡصَيۡنَٰهُ كِتَٰبًا ٢٩Ndipo Ife tidalemba m’Buku zonse zimene anali kuchita فَذُوقُواْ فَلَن نَّزِيدَكُمۡ إِلَّا عَذَابًا ٣٠Motero inu lawani! Inu simudzalandira china chilichonse koma manzunzo ochuluka إِنَّ لِلۡمُتَّقِينَ مَفَازًا ٣١Ndithudi kwa anthu oopa Mulungu kudzakhala kupambana حَدَآئِقَ وَأَعۡنَٰبًا ٣٢Minda ndi m’minda ya mphesa وَكَوَاعِبَ أَتۡرَابًا ٣٣Ndi a namwali akulu akulu ofanana zaka وَكَأۡسًا دِهَاقًا ٣٤Ndi chikho chodzadza لَّا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوًا وَلَا كِذَّٰبًا ٣٥Kumeneko iwo sadzamva mawu opanda pake kapena nkhani zabodza جَزَآءً مِّن رَّبِّكَ عَطَآءً حِسَابًا ٣٦Imeneyi ndiyo mphotho yochokera kwa Ambuye wako ndipo ndi mphotho yokwanira رَّبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا ٱلرَّحۡمَٰنِۖ لَا يَمۡلِكُونَ مِنۡهُ خِطَابًا ٣٧Ambuye wa Kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo, Mwini chisoni chosatha ndipo iwo sadzatha kulankhula naye يَوۡمَ يَقُومُ ٱلرُّوحُ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ صَفًّاۖ لَّا يَتَكَلَّمُونَ إِلَّا مَنۡ أَذِنَ لَهُ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَقَالَ صَوَابًا ٣٨Patsiku limene Mzimu ndi angelo adzaima pa mizere ndipo palibe amene adzalankhula kupatula yekhayo amene adzalandira chilolezo cha Mwini chifundo chosatha ndipo adzanena chinthu chimene chili choona ذَٰلِكَ ٱلۡيَوۡمُ ٱلۡحَقُّۖ فَمَن شَآءَ ٱتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ مَـَٔابًا ٣٩Ndithudi tsiku limeneli ndi loona, motero iye amene afuna, mulekeni atsatire njira yobwerera kwa Ambuye wake إِنَّآ أَنذَرۡنَٰكُمۡ عَذَابًا قَرِيبًا يَوۡمَ يَنظُرُ ٱلۡمَرۡءُ مَا قَدَّمَتۡ يَدَاهُ وَيَقُولُ ٱلۡكَافِرُ يَٰلَيۡتَنِي كُنتُ تُرَٰبَۢا ٤٠Ndithudi takuchenjezani za chilango chowawa chimene chili nkudza posachedwa. Tsiku limene munthu adzayang’ana ntchito zimene manja ake adatsogoza, ndipo osakhulupirira adzati: “Kalanga ine, ndikanakhala dothi.”