Millat al-Islam

Chapter 86 · 17 verses · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

Surah At-Tariq in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah At-Tariq (1312 reciters)
Meccanسورة الطارق17 verses

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

وَٱلسَّمَآءِ وَٱلطَّارِقِ ١Pali kumwamba ndi pali Nyenyezi yowala وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلطَّارِقُ ٢Kodi chidzakudziwitsa kuti Nyenyezi yowala ndi chiani ٱلنَّجۡمُ ٱلثَّاقِبُ ٣Ndi Nyenyezi yowala kothobwetsa maso إِن كُلُّ نَفۡسٍ لَّمَّا عَلَيۡهَا حَافِظٌ ٤Ndithudi moyo uliwonse uli ndi mtetezi wake فَلۡيَنظُرِ ٱلۡإِنسَٰنُ مِمَّ خُلِقَ ٥Tamulekani munthu kuti aganize kuti adalengedwa kuchokera ku chiyani خُلِقَ مِن مَّآءٍ دَافِقٍ ٦Iye adalengedwa kuchokera ku madzi otuluka يَخۡرُجُ مِنۢ بَيۡنِ ٱلصُّلۡبِ وَٱلتَّرَآئِبِ ٧Amene amatuluka kuchokera pakati pa pfupa la munsana ndi nthiti إِنَّهُۥ عَلَىٰ رَجۡعِهِۦ لَقَادِرٌ ٨Ndithudi Iye ali ndi mphamvu zomudzutsa يَوۡمَ تُبۡلَى ٱلسَّرَآئِرُ ٩Pa tsiku limene zinthu zobisika zidzayesedwa فَمَا لَهُۥ مِن قُوَّةٍ وَلَا نَاصِرٍ ١٠Ndipo adzakhala wopanda mphamvu kapena womuthandiza وَٱلسَّمَآءِ ذَاتِ ٱلرَّجۡعِ ١١Pali mtambo umene umapereka mvula kawiri kawiri وَٱلۡأَرۡضِ ذَاتِ ٱلصَّدۡعِ ١٢Ndi pali dziko lapansi limene limang’ambika إِنَّهُۥ لَقَوۡلٌ فَصۡلٌ ١٣Ndithudi! Awa ndi mawu amene amasiyanitsa وَمَا هُوَ بِٱلۡهَزۡلِ ١٤Si nthabwala ayi إِنَّهُمۡ يَكِيدُونَ كَيۡدًا ١٥Ndithudi iwo Al-A’la 649 ali kukonza chiwembu وَأَكِيدُ كَيۡدًا ١٦Ndipo Inenso ndili kukonza chiwembu فَمَهِّلِ ٱلۡكَٰفِرِينَ أَمۡهِلۡهُمۡ رُوَيۡدَۢا ١٧Motero apatse nthawi anthu osakhulupirira. Ndipo chita nawo mwamtendere pa kanthawi kochepa

Translation: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.