بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
كٓهيعٓصٓ ١Kaf ha ya ain suad ذِكۡرُ رَحۡمَتِ رَبِّكَ عَبۡدَهُۥ زَكَرِيَّآ ٢Ichi ndi chikumbutso cha chifuniro cha Ambuye wako kwa kapolo wake Zakariya إِذۡ نَادَىٰ رَبَّهُۥ نِدَآءً خَفِيًّا ٣Pamene Iye adamupempha Ambuye wake motsitsa mawu قَالَ رَبِّ إِنِّي وَهَنَ ٱلۡعَظۡمُ مِنِّي وَٱشۡتَعَلَ ٱلرَّأۡسُ شَيۡبًا وَلَمۡ أَكُنۢ بِدُعَآئِكَ رَبِّ شَقِيًّا ٤Iye adati, “oh Ambuye wanga! Mafupa anga ndi ofoka ndipo mutu wanga uli ndi imvi chifukwa cha ukalamba. Komabe, Ambuye, ine sindidapemphe kwa Inu mopanda phindu.” وَإِنِّي خِفۡتُ ٱلۡمَوَٰلِيَ مِن وَرَآءِي وَكَانَتِ ٱمۡرَأَتِي عَاقِرًا فَهَبۡ لِي مِن لَّدُنكَ وَلِيًّا ٥“Ndithudi ine ndili ndi mantha ndi abale anga za amene adzalowe m’malo mwanga ndiponso mkazi wanga ndi chumba. Ndipatseni mwana wamwamuna.” يَرِثُنِي وَيَرِثُ مِنۡ ءَالِ يَعۡقُوبَۖ وَٱجۡعَلۡهُ رَبِّ رَضِيًّا ٦“Amene adzalowe m’malo mwanga ndi m’malo mwa ana a Yakobo, ndipo mpangeni, Ambuye wanga, kukhala mmodzi wa wokondedwa wanu.” يَٰزَكَرِيَّآ إِنَّا نُبَشِّرُكَ بِغُلَٰمٍ ٱسۡمُهُۥ يَحۡيَىٰ لَمۡ نَجۡعَل لَّهُۥ مِن قَبۡلُ سَمِيًّا ٧“Ee iwe Zakariya! Ife tili kukuuza nkhani yabwino yakuti iwe udzapatsidwa mwana wamwamuna ndipo adzatchedwa Yohane, dzina limene silidapatsidwe kwa aliyense kumbuyoku.” قَالَ رَبِّ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَٰمٌ وَكَانَتِ ٱمۡرَأَتِي عَاقِرًا وَقَدۡ بَلَغۡتُ مِنَ ٱلۡكِبَرِ عِتِيًّا ٨Zakariya adati, “Ambuye! Kodi ine ndingakhale ndi mwana wamwamuna bwanji, pamene mkazi wanga ndi chumba ndipo ine ndine wokalamba?” قَالَ كَذَٰلِكَ قَالَ رَبُّكَ هُوَ عَلَيَّ هَيِّنٌ وَقَدۡ خَلَقۡتُكَ مِن قَبۡلُ وَلَمۡ تَكُ شَيۡـًٔا ٩Iye adati, “Chimenechi, wanena Ambuye wako! Idzakhala ntchito yopepuka kwa Ine chifukwa Ine ndidakupanga kukhala munthu pamene iwe siunali chinthu china chilichonse chodziwika.” قَالَ رَبِّ ٱجۡعَل لِّيٓ ءَايَةًۖ قَالَ ءَايَتُكَ أَلَّا تُكَلِّمَ ٱلنَّاسَ ثَلَٰثَ لَيَالٍ سَوِيًّا ١٠Zakariya adati, “Ambuye, ndipatseni chizindikiro chokhudza zimene zidzachitike.” Iye adati, “Chizindikiro chako ndi chakuti siudzalankhula ndi anthu usiku utatu ngakhale ulibe chilema.” فَخَرَجَ عَلَىٰ قَوۡمِهِۦ مِنَ ٱلۡمِحۡرَابِ فَأَوۡحَىٰٓ إِلَيۡهِمۡ أَن سَبِّحُواْ بُكۡرَةً وَعَشِيًّا ١١Pamene Zakariya adadza kwa anthu ake kuchokera m’kachisi, adawauza anthuwo kuti, “Lemekezani Ambuye wanu m’mawa ndi madzulo.” يَٰيَحۡيَىٰ خُذِ ٱلۡكِتَٰبَ بِقُوَّةٍۖ وَءَاتَيۡنَٰهُ ٱلۡحُكۡمَ صَبِيًّا ١٢“Oh Yohane! Samala mawu a Mulungu kwambiri.” Ife tidamupatsa luntha pamene adali mwana وَحَنَانًا مِّن لَّدُنَّا وَزَكَوٰةًۖ وَكَانَ تَقِيًّا ١٣Ndiponso tidamupatsa mtima wachifundo ndi woyeretsedwa ndipo adali munthu opewa zoipa وَبَرَّۢا بِوَٰلِدَيۡهِ وَلَمۡ يَكُن جَبَّارًا عَصِيًّا ١٤Ndipo adali kulemekeza abambo ndi amayi ake. Iye sadali wodzikweza kapena wonyoza malamulo a Mulungu وَسَلَٰمٌ عَلَيۡهِ يَوۡمَ وُلِدَ وَيَوۡمَ يَمُوتُ وَيَوۡمَ يُبۡعَثُ حَيًّا ١٥Mtendere udali pa iye pa tsiku limene adabadwa ndi pa tsiku limene adafa ndipo mtendere ukhale pa iye pamene aukitsidwa kwa akufa وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مَرۡيَمَ إِذِ ٱنتَبَذَتۡ مِنۡ أَهۡلِهَا مَكَانًا شَرۡقِيًّا ١٦Ndipo kukumbukira nkhani ya Maria m’Buku! Pamene iye adasiya anthu ake ndi kupita kumalo a payekha kumbali ya ku m’mawa فَٱتَّخَذَتۡ مِن دُونِهِمۡ حِجَابًا فَأَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡهَا رُوحَنَا فَتَمَثَّلَ لَهَا بَشَرًا سَوِيًّا ١٧Ndipo iye adafunda nsalu kuti anthu asaone nkhope yake. Ife tidamutumizira iye Mzimu wathu umene udaoneka ngati munthu قَالَتۡ إِنِّيٓ أَعُوذُ بِٱلرَّحۡمَٰنِ مِنكَ إِن كُنتَ تَقِيًّا ١٨Maria adati, “Mwini chisoni anditeteze ine kwa iwe! Ngati iwe umaopa Ambuye, ndisiye ndekha, usandiyandikire ayi.” قَالَ إِنَّمَآ أَنَا۠ رَسُولُ رَبِّكِ لِأَهَبَ لَكِ غُلَٰمًا زَكِيًّا ١٩Mngelo adati, “Ine ndine Mthenga wa Ambuye wako ndipo ndadza kudzakupatsa mwana wamwamuna woyera.” قَالَتۡ أَنَّىٰ يَكُونُ لِي غُلَٰمٌ وَلَمۡ يَمۡسَسۡنِي بَشَرٌ وَلَمۡ أَكُ بَغِيًّا ٢٠Maria adati, “Kodi ine ndidzabereka mwana bwanji pamene ine ndine wosakhudzidwa ndi mwamuna ndiponso si ndine wachiwerewere ayi?” قَالَ كَذَٰلِكِ قَالَ رَبُّكِ هُوَ عَلَيَّ هَيِّنٌۖ وَلِنَجۡعَلَهُۥٓ ءَايَةً لِّلنَّاسِ وَرَحۡمَةً مِّنَّاۚ وَكَانَ أَمۡرًا مَّقۡضِيًّا ٢١Mngelo adati, “Ndi momwemo” Ambuye wako wanena kuti, “Zimenezo, kwa Ine, ndi zopepuka. Tidzamupanga iye kukhala chizindikiro kwa anthu ndi madalitso ochoka kwa Ife. Limeneli ndilo lamulo limene lalamulidwa.” ۞ فَحَمَلَتۡهُ فَٱنتَبَذَتۡ بِهِۦ مَكَانًا قَصِيًّا ٢٢Ndipo iye adakhala ndi pakati ndipo adapita kumalo akutali فَأَجَآءَهَا ٱلۡمَخَاضُ إِلَىٰ جِذۡعِ ٱلنَّخۡلَةِ قَالَتۡ يَٰلَيۡتَنِي مِتُّ قَبۡلَ هَٰذَا وَكُنتُ نَسۡيًا مَّنسِيًّا ٢٣Ndipo ululu wa kubereka udamubwerera pamene adali patsinde pa mtengo wa tende ndipo adalira nati, “Kalanga ine, bola ndikadangofa zisanachitike izi chifukwa ndikadakhala woiwalidwa.” فَنَادَىٰهَا مِن تَحۡتِهَآ أَلَّا تَحۡزَنِي قَدۡ جَعَلَ رَبُّكِ تَحۡتَكِ سَرِيًّا ٢٤Kudabwera mawu kuchokera pansi oti: “Usadandaule ayi. Ambuye wako wakukonzera ka mtsinje kamene kalikuyenda ku mapazi ako.” وَهُزِّيٓ إِلَيۡكِ بِجِذۡعِ ٱلنَّخۡلَةِ تُسَٰقِطۡ عَلَيۡكِ رُطَبًا جَنِيًّا ٢٥“Ndipo gwedeza mtengo watendewu, iwo udzagwetsa zipatso za tende zaziwisi ndi zakupsa.” فَكُلِي وَٱشۡرَبِي وَقَرِّي عَيۡنًاۖ فَإِمَّا تَرَيِنَّ مِنَ ٱلۡبَشَرِ أَحَدًا فَقُولِيٓ إِنِّي نَذَرۡتُ لِلرَّحۡمَٰنِ صَوۡمًا فَلَنۡ أُكَلِّمَ ٱلۡيَوۡمَ إِنسِيًّا ٢٦“Idya ndi umwe, kotero sangalala.” Ndipo ukakumana ndi munthu wina aliyense muuze kuti, “Ine ndalumbira kwa Mwini chisoni kusala chakudya ndipo sindidzayankhula ndi munthu wina aliyense lero.” فَأَتَتۡ بِهِۦ قَوۡمَهَا تَحۡمِلُهُۥۖ قَالُواْ يَٰمَرۡيَمُ لَقَدۡ جِئۡتِ شَيۡـًٔا فَرِيًّا ٢٧Ndipo iye adatenga mwana wake nanka naye kwa anthu ake amene adati kwa iye’ “Iwe Maria! Ndithudi iwe wabweretsa chinthu cha chilendo.” يَٰٓأُخۡتَ هَٰرُونَ مَا كَانَ أَبُوكِ ٱمۡرَأَ سَوۡءٍ وَمَا كَانَتۡ أُمُّكِ بَغِيًّا ٢٨“Iwe mlongo wake wa Aroni! Atate wako sanali munthu wochita zoipa ndiponso Amayi ako sadali a chiwerewere.” فَأَشَارَتۡ إِلَيۡهِۖ قَالُواْ كَيۡفَ نُكَلِّمُ مَن كَانَ فِي ٱلۡمَهۡدِ صَبِيًّا ٢٩Maria adamuloza iye. Koma iwo adati, “Kodi ife tingayankhule ndi mwana wam’chikuta bwanji?” قَالَ إِنِّي عَبۡدُ ٱللَّهِ ءَاتَىٰنِيَ ٱلۡكِتَٰبَ وَجَعَلَنِي نَبِيًّا ٣٠Mwanayo adati, “Ine ndine kapolo wa Mulungu. Iye wandipatsa ine Buku labwino ndipo wandisankha kukhala Mtumwi.” وَجَعَلَنِي مُبَارَكًا أَيۡنَ مَا كُنتُ وَأَوۡصَٰنِي بِٱلصَّلَوٰةِ وَٱلزَّكَوٰةِ مَا دُمۡتُ حَيًّا ٣١“Madalitso ake ali pa ine kulikonse kumene ndingapite ndipo wandilamulira kuti ndikhale wopemphera ndi kupereka chaulere kwa anthu osauka nthawi yonse ya moyo wanga.” وَبَرَّۢا بِوَٰلِدَتِي وَلَمۡ يَجۡعَلۡنِي جَبَّارًا شَقِيًّا ٣٢“Iye wandilamula kuti ndizilemekeza amayi anga ndipo sadandipange kukhala wamwano ndi woipa.” وَٱلسَّلَٰمُ عَلَيَّ يَوۡمَ وُلِدتُّ وَيَوۡمَ أَمُوتُ وَيَوۡمَ أُبۡعَثُ حَيًّا ٣٣Ndipo mtendere ukhale kwa ine patsiku limene ndidabadwa, ndi patsiku limene ndidzafa ndiponso pa tsiku limene ndidzaukitsidwa kwa akufa ذَٰلِكَ عِيسَى ٱبۡنُ مَرۡيَمَۖ قَوۡلَ ٱلۡحَقِّ ٱلَّذِي فِيهِ يَمۡتَرُونَ ٣٤Ameneyo ndiye Yesu, mwana wa Maria. Liwu loonadi limene iwo ali kukayika مَا كَانَ لِلَّهِ أَن يَتَّخِذَ مِن وَلَدٍۖ سُبۡحَٰنَهُۥٓۚ إِذَا قَضَىٰٓ أَمۡرًا فَإِنَّمَا يَقُولُ لَهُۥ كُن فَيَكُونُ ٣٥Sizili zoyenera kuti Mulungu akhale ndi mwana wamwamuna! Iye ayeretsedwe ku zimenezo. Ngati Iye afuna chinthu, Iye amangonena kuti, “Chikhale” ndipo chimakhaladi وَإِنَّ ٱللَّهَ رَبِّي وَرَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُوهُۚ هَٰذَا صِرَٰطٌ مُّسۡتَقِيمٌ ٣٦Ndithudi Mulungu ndi Ambuye wanga ndiponso Ambuye wanu. Kotero mpembedzeni Iye yekha. Imeneyo ndiyo njira فَٱخۡتَلَفَ ٱلۡأَحۡزَابُ مِنۢ بَيۡنِهِمۡۖ فَوَيۡلٌ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن مَّشۡهَدِ يَوۡمٍ عَظِيمٍ ٣٧Koma magulu a Akhirisitu adasemphana maganizo pakati pawo. Koma pamene tsiku loopsa lidza, tsoka kwa anthu osakhulupirira أَسۡمِعۡ بِهِمۡ وَأَبۡصِرۡ يَوۡمَ يَأۡتُونَنَا لَٰكِنِ ٱلظَّٰلِمُونَ ٱلۡيَوۡمَ فِي ضَلَٰلٍ مُّبِينٍ ٣٨Kodi iwo adzaona ndi kumva momveka bwanji pa tsiku limene adzaonekera pa maso pathu! Koma anthu ochita zoipa lero ali mu chisokonezo choonekeratu وَأَنذِرۡهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡحَسۡرَةِ إِذۡ قُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ وَهُمۡ فِي غَفۡلَةٍ وَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ ٣٩Achenjeze za tsiku limene adzanong’oneza bombono, pamene malamulo athu adzakwaniritsidwa ndipo pamene iwo ali nkuiwala ndi kusakhulupirira إِنَّا نَحۡنُ نَرِثُ ٱلۡأَرۡضَ وَمَنۡ عَلَيۡهَا وَإِلَيۡنَا يُرۡجَعُونَ ٤٠Ndithudi Ife tidzatenga dziko lapansi ndi onse amene amakhala m’menemo. Ndi kwa Ife kumene onse adzabwezedwa وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ إِبۡرَٰهِيمَۚ إِنَّهُۥ كَانَ صِدِّيقًا نَّبِيًّا ٤١Ndipo kumbukira nkhani ya Abrahamu imene ili m’Buku. Iye adali Mtumwi ndi munthu wangwiro إِذۡ قَالَ لِأَبِيهِ يَٰٓأَبَتِ لِمَ تَعۡبُدُ مَا لَا يَسۡمَعُ وَلَا يُبۡصِرُ وَلَا يُغۡنِي عَنكَ شَيۡـًٔا ٤٢Pamene iye adawauza bambo wake kuti, “Oh Abambo! Kodi inu mungalambire bwanji chinthu chimene sichingathe kumva, kuona kapena kukuthandizani pa chilichonse?” يَٰٓأَبَتِ إِنِّي قَدۡ جَآءَنِي مِنَ ٱلۡعِلۡمِ مَا لَمۡ يَأۡتِكَ فَٱتَّبِعۡنِيٓ أَهۡدِكَ صِرَٰطًا سَوِيًّا ٤٣“Ohabambo! Choonadichavumbulutsidwa kwa ine chimene sichinakufikireni inu. Kotero nditsatireni ine kuti ndikutsogolereni ku njira yoyenera.” يَٰٓأَبَتِ لَا تَعۡبُدِ ٱلشَّيۡطَٰنَۖ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ كَانَ لِلرَّحۡمَٰنِ عَصِيًّا ٤٤“oh abambo! Musamapembedze Satana. Ndithudi Satana adanyoza Ambuye wachisoni chosatha.” يَٰٓأَبَتِ إِنِّيٓ أَخَافُ أَن يَمَسَّكَ عَذَابٌ مِّنَ ٱلرَّحۡمَٰنِ فَتَكُونَ لِلشَّيۡطَٰنِ وَلِيًّا ٤٥“oh abambo! Ine ndili kuopa kuti chilango cha Mulungu chidzadza pa inu ndipo mudzakhala bwenzi la Satana.” قَالَ أَرَاغِبٌ أَنتَ عَنۡ ءَالِهَتِي يَٰٓإِبۡرَٰهِيمُۖ لَئِن لَّمۡ تَنتَهِ لَأَرۡجُمَنَّكَۖ وَٱهۡجُرۡنِي مَلِيًّا ٤٦Abambo ake adati, “Kodi ukudana ndi milungu yanga iwe Abrahamu? Ukapanda kusiya ndidzakuponya miyala ndipo unditalikire pa kanthawi kochepa.” قَالَ سَلَٰمٌ عَلَيۡكَۖ سَأَسۡتَغۡفِرُ لَكَ رَبِّيٓۖ إِنَّهُۥ كَانَ بِي حَفِيًّا ٤٧Abrahamu adati, “Mtendere ukhale kwa inu. Ine ndidzapempha Ambuye wanga kuti akukhululukireni popeza, Mulungu, kwa ine, ndi wokoma mtima.” وَأَعۡتَزِلُكُمۡ وَمَا تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَأَدۡعُواْ رَبِّي عَسَىٰٓ أَلَّآ أَكُونَ بِدُعَآءِ رَبِّي شَقِيًّا ٤٨“Ine ndikuchokerani ndi zimene mumapembedza kuonjezera pa Mulungu. Ine ndidzapempha kwa Ambuye wanga ndipo ndikhulupirira kuti popembedza Ambuye wanga ndisadzakhale watsoka فَلَمَّا ٱعۡتَزَلَهُمۡ وَمَا يَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَهَبۡنَا لَهُۥٓ إِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَۖ وَكُلًّا جَعَلۡنَا نَبِيًّا ٤٩Ndipo pamene Abrahamu adasiya anthu ake ndi mafano amene iwo anali kupembedza kuonjezera pa Mulungu, tidamupatsa Isake ndi Yakobo. Aliyense wa iwo tidamupanga kukhala Mtumwi وَوَهَبۡنَا لَهُم مِّن رَّحۡمَتِنَا وَجَعَلۡنَا لَهُمۡ لِسَانَ صِدۡقٍ عَلِيًّا ٥٠Ndipo tidawapatsa onse mituka kuchokera m’chifundo chathu ndipo tidawapanga iwo kukhala otchulidwa mwaulemu وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مُوسَىٰٓۚ إِنَّهُۥ كَانَ مُخۡلَصًا وَكَانَ رَسُولًا نَّبِيًّا ٥١Ndipo kumbukira nkhani ya Mose imene ili m’Buku, amene adali wosankhidwa ndiponso Mtumwi ndi Mneneri وَنَٰدَيۡنَٰهُ مِن جَانِبِ ٱلطُّورِ ٱلۡأَيۡمَنِ وَقَرَّبۡنَٰهُ نَجِيًّا ٥٢Ife tidamuitana kuchokera kumbali ya dzanja la manja la phiri la Sinai ndipo tinamuyandikitsa kukhala pafupi ndi Ife kuti tiyankhule naye mwamseri وَوَهَبۡنَا لَهُۥ مِن رَّحۡمَتِنَآ أَخَاهُ هَٰرُونَ نَبِيًّا ٥٣Tidamupatsa, mwachisoni chathu, m’bale wake Aroni kuti akhale Mtumwi وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ إِسۡمَٰعِيلَۚ إِنَّهُۥ كَانَ صَادِقَ ٱلۡوَعۡدِ وَكَانَ رَسُولًا نَّبِيًّا ٥٤Ndipo kumbukira nkhani ya Ishimayeli imene ili m’Buku. Iye adali wosunga pangano ndipo adali Mtumwi ndi Mneneri وَكَانَ يَأۡمُرُ أَهۡلَهُۥ بِٱلصَّلَوٰةِ وَٱلزَّكَوٰةِ وَكَانَ عِندَ رَبِّهِۦ مَرۡضِيًّا ٥٥Iye anali kulamula anthu ake kuchita mapemphero ndi kupereka chothandiza nacho anthu osauka ndipo adali, kwa Ambuye wake, wokondedwa وَٱذۡكُرۡ فِي ٱلۡكِتَٰبِ إِدۡرِيسَۚ إِنَّهُۥ كَانَ صِدِّيقًا نَّبِيًّا ٥٦Ndipo kumbukira za Idrissa. Iye adali munthu wonena zoona ndi Mtumwi وَرَفَعۡنَٰهُ مَكَانًا عَلِيًّا ٥٧Ife tidamukweza kukhala malo a pamwamba أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ أَنۡعَمَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِم مِّنَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ مِن ذُرِّيَّةِ ءَادَمَ وَمِمَّنۡ حَمَلۡنَا مَعَ نُوحٍ وَمِن ذُرِّيَّةِ إِبۡرَٰهِيمَ وَإِسۡرَٰٓءِيلَ وَمِمَّنۡ هَدَيۡنَا وَٱجۡتَبَيۡنَآۚ إِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُ ٱلرَّحۡمَٰنِ خَرُّواْۤ سُجَّدًاۤ وَبُكِيًّا ۩ ٥٨Awa ndi anthu amene Mulungu adawaonetsera chisomo chake. Atumwi ochokera ku m’badwo wa Adamu ndi iwo amene tidawatenga pamodzi m’chombo ndi Nowa. Ana a Abrahamu, a Israyeli ndi iwo amene Ife tawatsogolera ndi kuwasankha. Pamene zivumbulutso za Mwini chisoni chosatha zinali kulakatulidwa kwa iwo, iwo adali kugwa nkhope zawo pansi ndi kumalira ۞ فَخَلَفَ مِنۢ بَعۡدِهِمۡ خَلۡفٌ أَضَاعُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَٱتَّبَعُواْ ٱلشَّهَوَٰتِۖ فَسَوۡفَ يَلۡقَوۡنَ غَيًّا ٥٩Koma mibadwo ya anthu imene inadza iwo atachoka idanyoza mapemphero ndi kutsatira zilakolako zawo. Ndithudi awa adzakumana ndi mavuto إِلَّا مَن تَابَ وَءَامَنَ وَعَمِلَ صَٰلِحًا فَأُوْلَٰٓئِكَ يَدۡخُلُونَ ٱلۡجَنَّةَ وَلَا يُظۡلَمُونَ شَيۡـًٔا ٦٠Kupatula amene alapa machimo ndi kukhulupirira choonadi ndi kumachita ntchito zabwino. Iwo adzalowa ku Paradiso ndipo sadzaponderezedwa m’chilichonse جَنَّٰتِ عَدۡنٍ ٱلَّتِي وَعَدَ ٱلرَّحۡمَٰنُ عِبَادَهُۥ بِٱلۡغَيۡبِۚ إِنَّهُۥ كَانَ وَعۡدُهُۥ مَأۡتِيًّا ٦١Iwo adzakhala m’minda ya Edeni mpaka muyaya, imene Mwini chisoni chosatha adalonjeza akapolo ake ngakhale kuti iwo sadaione. Ndithudi lonjezo lake lidzakwaniritsidwa لَّا يَسۡمَعُونَ فِيهَا لَغۡوًا إِلَّا سَلَٰمًاۖ وَلَهُمۡ رِزۡقُهُمۡ فِيهَا بُكۡرَةً وَعَشِيًّا ٦٢Kumeneko iwo sadzamva zinthu zopanda pake koma mawu a mtendere okha, ndipo chakudya chidzapatsidwa kwa iwo m’mawa ndi madzulo تِلۡكَ ٱلۡجَنَّةُ ٱلَّتِي نُورِثُ مِنۡ عِبَادِنَا مَن كَانَ تَقِيًّا ٦٣Imeneyo ndiyo Paradiso imene tidzawapatsa akapolo athu omwe anali kuopa Mulungu وَمَا نَتَنَزَّلُ إِلَّا بِأَمۡرِ رَبِّكَۖ لَهُۥ مَا بَيۡنَ أَيۡدِينَا وَمَا خَلۡفَنَا وَمَا بَيۡنَ ذَٰلِكَۚ وَمَا كَانَ رَبُّكَ نَسِيًّا ٦٤Ife sititsika kuchoka kumwamba pokhapokha ngati taloledwa ndi Ambuye wako. Iye ndiye mwini wa zinthu zonse zimene zili pamaso pathu, kumbuyo kwathu ndi zonse zimene zili pakati pa zimenezi. Ndipo Ambuye wako saiwala رَّبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا فَٱعۡبُدۡهُ وَٱصۡطَبِرۡ لِعِبَٰدَتِهِۦۚ هَلۡ تَعۡلَمُ لَهُۥ سَمِيًّا ٦٥Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo. Kotero m’pembedze Iye yekha ndipo khala wopirira pamapemphero ake. Kodi ukudziwa wina amene ali ndi dzina ngati la Iye وَيَقُولُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَءِذَا مَا مِتُّ لَسَوۡفَ أُخۡرَجُ حَيًّا ٦٦Munthu amati, “Pamene ine nditafa kodi ndidzaukitsidwa ndi kukhalanso ndi moyo?” أَوَلَا يَذۡكُرُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَنَّا خَلَقۡنَٰهُ مِن قَبۡلُ وَلَمۡ يَكُ شَيۡـًٔا ٦٧Kodi munthu sakumbukira kuti tidamulenga iye pamene poyamba sadali chinthu china chilichonse فَوَرَبِّكَ لَنَحۡشُرَنَّهُمۡ وَٱلشَّيَٰطِينَ ثُمَّ لَنُحۡضِرَنَّهُمۡ حَوۡلَ جَهَنَّمَ جِثِيًّا ٦٨Motero pali Ambuye wako; ndithudi Tidzawasonkhanitsa pamodzi ndi a Satana ndipo onse tidzawabweretsa m’mphepete mwa Gahena atagwada ثُمَّ لَنَنزِعَنَّ مِن كُلِّ شِيعَةٍ أَيُّهُمۡ أَشَدُّ عَلَى ٱلرَّحۡمَٰنِ عِتِيًّا ٦٩Ndipo mwachoonadi tidzachotsa mugulu lililonse onse amene adanyoza Mulungu kwambiri ثُمَّ لَنَحۡنُ أَعۡلَمُ بِٱلَّذِينَ هُمۡ أَوۡلَىٰ بِهَا صِلِيًّا ٧٠Ndithudi Ife tilikuwadziwa kwambiri amene ali oyenera kuotchedwa وَإِن مِّنكُمۡ إِلَّا وَارِدُهَاۚ كَانَ عَلَىٰ رَبِّكَ حَتۡمًا مَّقۡضِيًّا ٧١Palibe wina wa inu amene sadzapita kumbali ya Moto. Limeneli ndilo lamulo la mphamvu la Ambuye wanu ثُمَّ نُنَجِّي ٱلَّذِينَ ٱتَّقَواْ وَّنَذَرُ ٱلظَّٰلِمِينَ فِيهَا جِثِيًّا ٧٢Ndipo Ife tidzapulumutsa onse amene amaopa ndi kuwasiya ochita zoipa, atagwada, kuti amve ululu wake وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُنَا بَيِّنَٰتٍ قَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَيُّ ٱلۡفَرِيقَيۡنِ خَيۡرٌ مَّقَامًا وَأَحۡسَنُ نَدِيًّا ٧٣Pamene zivumbulutso zathu zilakatulidwa momveka kwa iwo, anthu osakhulupirira amanena kwa anthu okhulupirira kuti, “Kodi ndi gulu liti pa magulu awiriwa limene lili ndi malo abwino okhala ndi anthu apamwamba?” وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّن قَرۡنٍ هُمۡ أَحۡسَنُ أَثَٰثًا وَرِءۡيًا ٧٤Kodi ndi mibadwo ingati yakale imene tidaononga iwo asanadze, mibadwo imene idali ndi zinthu zabwino ndiponso zokongola قُلۡ مَن كَانَ فِي ٱلضَّلَٰلَةِ فَلۡيَمۡدُدۡ لَهُ ٱلرَّحۡمَٰنُ مَدًّاۚ حَتَّىٰٓ إِذَا رَأَوۡاْ مَا يُوعَدُونَ إِمَّا ٱلۡعَذَابَ وَإِمَّا ٱلسَّاعَةَ فَسَيَعۡلَمُونَ مَنۡ هُوَ شَرٌّ مَّكَانًا وَأَضۡعَفُ جُندًا ٧٥Nena, “Aliyense amene alakwa, Mwini chisoni chosatha adzawaonjezera nthawi, mpaka pamene adzaone zomwe adalonjezedwa. Kaya ndi chilango kapena ola lomaliza, pamenepo ndiye adzadziwa kuti ndani amene ali mwini wa malo oipa ndi gulu lankhondo lofoka.” وَيَزِيدُ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ٱهۡتَدَوۡاْ هُدًىۗ وَٱلۡبَٰقِيَٰتُ ٱلصَّٰلِحَٰتُ خَيۡرٌ عِندَ رَبِّكَ ثَوَابًا وَخَيۡرٌ مَّرَدًّا ٧٦Mulungu amapitiriza kutsogolera iwo amene atsatira njira yoyenera. Ntchito zabwino zimene zili ndi malipiro osatha zili ndi mphotho yabwino pamaso pa Ambuye wako ndiponso zotsatira zake ndi zabwino أَفَرَءَيۡتَ ٱلَّذِي كَفَرَ بِـَٔايَٰتِنَا وَقَالَ لَأُوتَيَنَّ مَالًا وَوَلَدًا ٧٧Kodi mwamuona munthu amene akana zivumbulutso zathu ndipo amanena kuti, “Ine, ndithudi, ndidzapatsidwa chuma ndi ana?” أَطَّلَعَ ٱلۡغَيۡبَ أَمِ ٱتَّخَذَ عِندَ ٱلرَّحۡمَٰنِ عَهۡدًا ٧٨Kodi iye waziona zinthu zosaoneka kapena Mwini chisoni chosatha wamupatsa lonjezo lotere كـَلَّاۚ سَنَكۡتُبُ مَا يَقُولُ وَنَمُدُّ لَهُۥ مِنَ ٱلۡعَذَابِ مَدًّا ٧٩Osatheka! Ife tidzalemba zimene akunena ndi kuchipanga chilango chake kukhala chachitali وَنَرِثُهُۥ مَا يَقُولُ وَيَأۡتِينَا فَرۡدًا ٨٠Zonse zimene azilankhula iye zidzabwerera kwa Ife ndipo adzadza pamaso pathu yekha وَٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ ءَالِهَةً لِّيَكُونُواْ لَهُمۡ عِزًّا ٨١Anthu osakhulupirira adadzisankhira milungu ina kuti iwapatse mphamvu ndi ulemerero كـَلَّاۚ سَيَكۡفُرُونَ بِعِبَادَتِهِمۡ وَيَكُونُونَ عَلَيۡهِمۡ ضِدًّا ٨٢Ayi. Koma milunguyo idzakana kupembedza kwawo ndipo idzakhala adani awo أَلَمۡ تَرَ أَنَّآ أَرۡسَلۡنَا ٱلشَّيَٰطِينَ عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ تَؤُزُّهُمۡ أَزًّا ٨٣Kodi siudaone kuti timatumiza kwa anthu osakhulupirira a Satana amene amawaonetsa zinthu zoti achimwe nazo فَلَا تَعۡجَلۡ عَلَيۡهِمۡۖ إِنَّمَا نَعُدُّ لَهُمۡ عَدًّا ٨٤Kotero musafulumize kuwapemphera chionongeko, ndithudi, tikuwawerengera masiku awo يَوۡمَ نَحۡشُرُ ٱلۡمُتَّقِينَ إِلَى ٱلرَّحۡمَٰنِ وَفۡدًا ٨٥Tsiku limenetidzasonkhanitsaanthuolungamam’magulu kufika pamaso pa Ambuye wachisoni kudzalandira ulemu وَنَسُوقُ ٱلۡمُجۡرِمِينَ إِلَىٰ جَهَنَّمَ وِرۡدًا ٨٦Ndipo tidzawakusa anthu oipa kupita ku moto wa ku Gahena ali ndi ludzu lodetsa nkhawa لَّا يَمۡلِكُونَ ٱلشَّفَٰعَةَ إِلَّا مَنِ ٱتَّخَذَ عِندَ ٱلرَّحۡمَٰنِ عَهۡدًا ٨٧Palibe amene adzakhala ndi mphamvu zodandaula kupatula yekhayo amene walandira chilolezo cha Mwini chisoni chosatha وَقَالُواْ ٱتَّخَذَ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَلَدًا ٨٨Iwo amati, “Mwini chisoni chosatha wabala mwana wamwamuna.” لَّقَدۡ جِئۡتُمۡ شَيۡـًٔا إِدًّا ٨٩Ndithudi mwanena chinthu choipitsitsa تَكَادُ ٱلسَّمَٰوَٰتُ يَتَفَطَّرۡنَ مِنۡهُ وَتَنشَقُّ ٱلۡأَرۡضُ وَتَخِرُّ ٱلۡجِبَالُ هَدًّا ٩٠Pafupifupi kumwamba kumafuna kung’ambika chifukwa cha mawu amenewa ndipo nthaka imafuna kugawikana ndi mapiri kugudubuzika ndi kuonongeka أَن دَعَوۡاْ لِلرَّحۡمَٰنِ وَلَدًا ٩١Chifukwa chonena Mwini Chisoni Chosatha ali ndi mwana wamwamuna وَمَا يَنۢبَغِي لِلرَّحۡمَٰنِ أَن يَتَّخِذَ وَلَدًا ٩٢Si zoyenera kwa Mwini chisoni chosatha kuti akhale ndi mwana إِن كُلُّ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ إِلَّآ ءَاتِي ٱلرَّحۡمَٰنِ عَبۡدًا ٩٣Palibe china chilichonse chimene chili kumwamba kapena pa dziko lapansi chimene chimabwera kwa Mwini chisoni chosatha kupatula ngati kapolo لَّقَدۡ أَحۡصَىٰهُمۡ وَعَدَّهُمۡ عَدًّا ٩٤Iye wasunga chiwerengero cha zolengedwa zake zonse وَكُلُّهُمۡ ءَاتِيهِ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ فَرۡدًا ٩٥Ndipo onse, mmodzimmodzi, adzabwerera kwa Iye pa tsiku la kuuka kwa akufa إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ سَيَجۡعَلُ لَهُمُ ٱلرَّحۡمَٰنُ وُدًّا ٩٦Ndithudi amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, Mwini chisoni chosatha adzawakonda فَإِنَّمَا يَسَّرۡنَٰهُ بِلِسَانِكَ لِتُبَشِّرَ بِهِ ٱلۡمُتَّقِينَ وَتُنذِرَ بِهِۦ قَوۡمًا لُّدًّا ٩٧Motero Ife tapanga iyo kukhala yosavuta ya m’chiyankhulo chako kuti upeleke nkhani yabwino kwa anthu oopa ndi kuchenjeza ndi ilo anthu otsutsa وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا قَبۡلَهُم مِّن قَرۡنٍ هَلۡ تُحِسُّ مِنۡهُم مِّنۡ أَحَدٍ أَوۡ تَسۡمَعُ لَهُمۡ رِكۡزَۢا ٩٨Kodi ndi mibadwo ingati imene Ife tidaononga kale iwo asanadze? Kodi uli kumuona mmodzi aliyense wa iwo kapena kumva manong’onong’o ochokera kwa iwo