Millat al-Islam

Chapter 101 · 11 verses · Khaled Ibrahim Betala

Surah Al-Qaria in Chichewa

Arabic with tafsir Listen to Surah Al-Qaria (1290 reciters)

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

ٱلۡقَارِعَةُ ١“Kugunda kwa phokoso (la Qiyâma) مَا ٱلۡقَارِعَةُ ٢“Kodi kugunda kwa phokosolo ndi chiyani وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلۡقَارِعَةُ ٣“Ndichiyani chingakudziwitse za kugunda kwa phokoso (la Qiyâma komwe kudzawakomole anthu) يَوۡمَ يَكُونُ ٱلنَّاسُ كَٱلۡفَرَاشِ ٱلۡمَبۡثُوثِ ٤“Limenelo ndi tsiku limene anthu adzakhala ngati agulugufe obalalika وَتَكُونُ ٱلۡجِبَالُ كَٱلۡعِهۡنِ ٱلۡمَنفُوشِ ٥“Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya womwazidwa (wongouluka uku ndi uku mumlengalenga) فَأَمَّا مَن ثَقُلَتۡ مَوَٰزِينُهُۥ ٦“Tsono amene muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzalemere (ndikupepuka zoipa) فَهُوَ فِي عِيشَةٍ رَّاضِيَةٍ ٧“Ndiye kuti iye adzakhala mu umoyo wosangalatsa (patsiku la chiweruziro) وَأَمَّا مَنۡ خَفَّتۡ مَوَٰزِينُهُۥ ٨“Ndipo yemwe muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzapepuka (ndi kulemera zoipa) فَأُمُّهُۥ هَاوِيَةٌ ٩“Ndiye kuti mbuto yake ndi ku Hawiya وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا هِيَهۡ ١٠“Kodi ndi chiyani chingakudziwitse za Hawiya نَارٌ حَامِيَةُۢ ١١“Umenewo ndi Moto woyaka mwa ukali

Translation: Khaled Ibrahim Betala.