بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
حمٓ ١Ha Mim وَٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُبِينِ ٢Ndilumbira pali Buku limene limanena zoona إِنَّآ أَنزَلۡنَٰهُ فِي لَيۡلَةٍ مُّبَٰرَكَةٍۚ إِنَّا كُنَّا مُنذِرِينَ ٣Ife tidalivumbulutsa ilo mu usiku wodalitsika. Ndithudi Ife tili kupitirizabe kuchenjeza فِيهَا يُفۡرَقُ كُلُّ أَمۡرٍ حَكِيمٍ ٤Mu umenewu, ntchito iliyonse ili kuonetsedwa poyera أَمۡرًا مِّنۡ عِندِنَآۚ إِنَّا كُنَّا مُرۡسِلِينَ ٥Lamulo lochokera kwa Ife, ndithudi Ife timatumiza رَحۡمَةً مِّن رَّبِّكَۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ ٦Chifundo chochokera kwa Ambuye wako, ndithudi Iye ndi wakumva ndi wodziwa رَبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَآۖ إِن كُنتُم مُّوقِنِينَ ٧Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo, ngati inu nonse mutakhala ndi chikhulupiriro chenicheni لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ يُحۡيِۦ وَيُمِيتُۖ رَبُّكُمۡ وَرَبُّ ءَابَآئِكُمُ ٱلۡأَوَّلِينَ ٨Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Ndipo ndiye amene amapereka moyo ndi imfa. Ambuye wako ndi Ambuye wa makolo ako amene adanka kale بَلۡ هُمۡ فِي شَكٍّ يَلۡعَبُونَ ٩Iyayi! Iwo amakayika, amasewerera فَٱرۡتَقِبۡ يَوۡمَ تَأۡتِي ٱلسَّمَآءُ بِدُخَانٍ مُّبِينٍ ١٠Motero dikirani tsiku limene kumwamba kudzatsitsa utsi wooneka يَغۡشَى ٱلنَّاسَۖ هَٰذَا عَذَابٌ أَلِيمٌ ١١Umene udzazungulira anthu ndipo chimenechi ndi chilango chowawa رَّبَّنَا ٱكۡشِفۡ عَنَّا ٱلۡعَذَابَ إِنَّا مُؤۡمِنُونَ ١٢Iwo adzati, “Ambuye wathu! Tichotsereni chilango ichi chifukwa tsopano takhulupirira.” أَنَّىٰ لَهُمُ ٱلذِّكۡرَىٰ وَقَدۡ جَآءَهُمۡ رَسُولٌ مُّبِينٌ ١٣Kodi iwo angachenjezedwe bwanji pamene kunadza kale Mtumwi amene anali kuwauza choonadi ثُمَّ تَوَلَّوۡاْ عَنۡهُ وَقَالُواْ مُعَلَّمٌ مَّجۡنُونٌ ١٤Iwo adamutembenukira ndi kumati, “Munthu wophunzitsidwa ndi anthu ena, munthu wamisala.” إِنَّا كَاشِفُواْ ٱلۡعَذَابِ قَلِيلًاۚ إِنَّكُمۡ عَآئِدُونَ ١٥Ndithudi Ife tidzachotsa chilango pa kanthawi kochepa koma ndithudi inu mudzabwerera يَوۡمَ نَبۡطِشُ ٱلۡبَطۡشَةَ ٱلۡكُبۡرَىٰٓ إِنَّا مُنتَقِمُونَ ١٦Patsiku limene Ife tidzakugwirani mwamphamvu. Ndithudi tidzawabwezera chilango choyenera ۞ وَلَقَدۡ فَتَنَّا قَبۡلَهُمۡ قَوۡمَ فِرۡعَوۡنَ وَجَآءَهُمۡ رَسُولٌ كَرِيمٌ ١٧Ndipo, ndithudi, tidawayesa anthu a Farawo, iwo asanabadwe, ndipo kudadza kwa iwo Mtumwi wolemekezeka أَنۡ أَدُّوٓاْ إِلَيَّ عِبَادَ ٱللَّهِۖ إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٌ ١٨Naati “Bweretsani kwa ine akapolo a Mulungu.” “Ndithudi ine ndine Mtumwi wokhulupirika kwa inu.” وَأَن لَّا تَعۡلُواْ عَلَى ٱللَّهِۖ إِنِّيٓ ءَاتِيكُم بِسُلۡطَٰنٍ مُّبِينٍ ١٩“Ndipo musachitire mwano Mulungu. Ndithudi ine ndadza kwa inu ndi ulamuliro wooneka.” وَإِنِّي عُذۡتُ بِرَبِّي وَرَبِّكُمۡ أَن تَرۡجُمُونِ ٢٠“Ndipo ndithudi ine ndapempha chitetezo cha Ambuye wanga ndi Ambuye wanu kuti musandiononge.” وَإِن لَّمۡ تُؤۡمِنُواْ لِي فَٱعۡتَزِلُونِ ٢١“Koma ngati inu simundikhulupirira ine, ndiye mundisiye ndekha.” فَدَعَا رَبَّهُۥٓ أَنَّ هَٰٓؤُلَآءِ قَوۡمٌ مُّجۡرِمُونَ ٢٢Ndipo iye anati kwa Ambuye wake, “Anthu awa ndi ochimwa.” فَأَسۡرِ بِعِبَادِي لَيۡلًا إِنَّكُم مُّتَّبَعُونَ ٢٣Choka iwe ndi akapolo anga nthawi yausiku. Ndithudi iwe udzalondoledwa وَٱتۡرُكِ ٱلۡبَحۡرَ رَهۡوًاۖ إِنَّهُمۡ جُندٌ مُّغۡرَقُونَ ٢٤“Ileke nyanja kukhala monga mmene ili. Ndithudi iwo ndi anthu amene adzamizidwa.” كَمۡ تَرَكُواْ مِن جَنَّٰتٍ وَعُيُونٍ ٢٥Kodi ndi minda ingati ndiponso a kasupe angati amene iwo adasiya وَزُرُوعٍ وَمَقَامٍ كَرِيمٍ ٢٦Ndi minda ya chimanga ndi malo olemekezeka وَنَعۡمَةٍ كَانُواْ فِيهَا فَٰكِهِينَ ٢٧Ndi zinthu zabwino zimene amasangalala nazo كَذَٰلِكَۖ وَأَوۡرَثۡنَٰهَا قَوۡمًا ءَاخَرِينَ ٢٨Kotero zinali choncho. Ndipo Ife tidawasankha anthu ena kuti atenge zinthu zawo فَمَا بَكَتۡ عَلَيۡهِمُ ٱلسَّمَآءُ وَٱلۡأَرۡضُ وَمَا كَانُواْ مُنظَرِينَ ٢٩Kumwamba kapena dziko lapansi silidakhetse msozi chifukwa cha iwo ndipo iwo sadapatsidwe mpumulo وَلَقَدۡ نَجَّيۡنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ مِنَ ٱلۡعَذَابِ ٱلۡمُهِينِ ٣٠Ndithudi tidapulumutsa ana a Israyeli ku chilango chochititsa manyazi مِن فِرۡعَوۡنَۚ إِنَّهُۥ كَانَ عَالِيًا مِّنَ ٱلۡمُسۡرِفِينَ ٣١Chimene chidaperekedwa ndi Farawo. Ndithudi iye adali wamwano ndi mmodzi wa anthu oswa malamulo وَلَقَدِ ٱخۡتَرۡنَٰهُمۡ عَلَىٰ عِلۡمٍ عَلَى ٱلۡعَٰلَمِينَ ٣٢Ndithudi tidawasankha iwo kuti akhale ndi nzeru kuposa mitundu ina وَءَاتَيۡنَٰهُم مِّنَ ٱلۡأٓيَٰتِ مَا فِيهِ بَلَٰٓؤٌاْ مُّبِينٌ ٣٣Ndipo tidawapatsa chivumbulutso chimene chidali ndi mayesero ooneka إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ لَيَقُولُونَ ٣٤Ndithudi iwo akuti إِنۡ هِيَ إِلَّا مَوۡتَتُنَا ٱلۡأُولَىٰ وَمَا نَحۡنُ بِمُنشَرِينَ ٣٥“Palibe china chilichonse kupatula imfa yathu yoyamba ndipo ife sitidzaukitsidwa kwa akufa.” فَأۡتُواْ بِـَٔابَآئِنَآ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ ٣٦“Kotero bweretsa makolo athu ngati zimene ukunena ndi zoona!” أَهُمۡ خَيۡرٌ أَمۡ قَوۡمُ تُبَّعٍ وَٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ أَهۡلَكۡنَٰهُمۡۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ مُجۡرِمِينَ ٣٧Kodi awa ndi opambana kuposa anthu a Tubba ndi iwo amene adalipo kale? Ife tidawaononga onse ndipo iwo adali olakwa وَمَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا لَٰعِبِينَ ٣٨Ndipo ife sitidalenge kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo mwamasewera مَا خَلَقۡنَٰهُمَآ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ ٣٩Ife sitidazilenge zonsezi kupatula mwachoonadi ndipo ambiri a iwo sadziwa إِنَّ يَوۡمَ ٱلۡفَصۡلِ مِيقَٰتُهُمۡ أَجۡمَعِينَ ٤٠Ndithudi tsiku lachimaliziro ndi tsiku lomaliza kwa iwo onse يَوۡمَ لَا يُغۡنِي مَوۡلًى عَن مَّوۡلًى شَيۡـًٔا وَلَا هُمۡ يُنصَرُونَ ٤١Ndi tsiku limene bwenzi sadzakumbukira bwenzi ake ndipo sadzalandira chithandizo إِلَّا مَن رَّحِمَ ٱللَّهُۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ٤٢Kupatula yekhawo amene waonetsedwa chisomo cha Mulungu. Ndithudi Iye ndiye Mwini mphamvu ndi Mwini chisoni chosatha إِنَّ شَجَرَتَ ٱلزَّقُّومِ ٤٣Ndithudi mtengo wa Zaqqum طَعَامُ ٱلۡأَثِيمِ ٤٤Udzakhala chakudya cha anthu ochimwa كَٱلۡمُهۡلِ يَغۡلِي فِي ٱلۡبُطُونِ ٤٥Monga mafuta owira, chidzabwata m’mimba mwawo كَغَلۡيِ ٱلۡحَمِيمِ ٤٦Monga ngati madzi ogaduka خُذُوهُ فَٱعۡتِلُوهُ إِلَىٰ سَوَآءِ ٱلۡجَحِيمِ ٤٧“Mugwire iye ndipo mududuzireni m’kati mwa Gahena.” ثُمَّ صُبُّواْ فَوۡقَ رَأۡسِهِۦ مِنۡ عَذَابِ ٱلۡحَمِيمِ ٤٨Ndipo thirani pamutu pake chilango cha madzi owira ذُقۡ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡكَرِيمُ ٤٩“Lawani ichi! Ndithudi inu munali amphamvu ndi aulemu.” إِنَّ هَٰذَا مَا كُنتُم بِهِۦ تَمۡتَرُونَ ٥٠“Ndithudi! Ichi ndicho chimene munali kukayika.” إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي مَقَامٍ أَمِينٍ ٥١“Ndithudi! Iwo amene amalewa zoipa adzakhala kumalo otetezedwa.” فِي جَنَّٰتٍ وَعُيُونٍ ٥٢Pakati pa minda ndi a kasupe يَلۡبَسُونَ مِن سُندُسٍ وَإِسۡتَبۡرَقٍ مُّتَقَٰبِلِينَ ٥٣Iwo atavala Silika wokhuthala ndi wokongola, atakhala moyang’anizana كَذَٰلِكَ وَزَوَّجۡنَٰهُم بِحُورٍ عِينٍ ٥٤Kotero zidzakhala choncho ndipo Ife tidzawakwatitsa kwa akazi a maso aakuluakulu okongola يَدۡعُونَ فِيهَا بِكُلِّ فَٰكِهَةٍ ءَامِنِينَ ٥٥Iwo adzaitanitsa chipatso cha mtundu uliwonse mwamtendere ndi mokhazikika لَا يَذُوقُونَ فِيهَا ٱلۡمَوۡتَ إِلَّا ٱلۡمَوۡتَةَ ٱلۡأُولَىٰۖ وَوَقَىٰهُمۡ عَذَابَ ٱلۡجَحِيمِ ٥٦Ndipo iwo sadzalawa imfa kupatula imfa yoyamba ndipo Iye adzawapulumutsa ku chilango chowawa cha Gahena فَضۡلًا مِّن رَّبِّكَۚ ذَٰلِكَ هُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ ٥٧Chisomo chochokera kwa Ambuye wako! Chimenechi chidzakhala chinthu chopambana kwambiri فَإِنَّمَا يَسَّرۡنَٰهُ بِلِسَانِكَ لَعَلَّهُمۡ يَتَذَكَّرُونَ ٥٨Ndithudi Ife taipanga Koraniyi kukhala yapafupi m’chiyankhulo chako ndi cholinga chakuti mwina angathe kukumbukira فَٱرۡتَقِبۡ إِنَّهُم مُّرۡتَقِبُونَ ٥٩Kotero iwe dikira chifukwa nawonso ali kudikira