بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
حمٓ ١Ha mim وَٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُبِينِ ٢Ndilumbira pali Buku limene limafotokoza zinthu mosabisa إِنَّا جَعَلۡنَٰهُ قُرۡءَٰنًا عَرَبِيًّا لَّعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ ٣Ndithudi talipanga ilo kukhala Korani yam’chinenero cha Chiarabu kuti iwe ukhoza kulizindikira وَإِنَّهُۥ فِيٓ أُمِّ ٱلۡكِتَٰبِ لَدَيۡنَا لَعَلِيٌّ حَكِيمٌ ٤Ndithudi ilo lili mu Make Buku limene lili pamaso pathu, lolemekezeka ndi lodzala ndi nzeru أَفَنَضۡرِبُ عَنكُمُ ٱلذِّكۡرَ صَفۡحًا أَن كُنتُمۡ قَوۡمًا مُّسۡرِفِينَ ٥Kodi Ife tisiye kukukumbutsani inu nonse chifukwa chakuti ndinu anthu osasamala ndi oswa malamulo وَكَمۡ أَرۡسَلۡنَا مِن نَّبِيٍّ فِي ٱلۡأَوَّلِينَ ٦Kodi ndi Atumwi angati amene Ife tidatumiza ku mitundu ya anthu akale وَمَا يَأۡتِيهِم مِّن نَّبِيٍّ إِلَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ ٧Ndipo kwa iwo sikunadze Mtumwi amene iwo sadamunyoze فَأَهۡلَكۡنَآ أَشَدَّ مِنۡهُم بَطۡشًا وَمَضَىٰ مَثَلُ ٱلۡأَوَّلِينَ ٨Kotero Ife tidawaononga, anthu amphamvu kuposa awa, ndipo chitsanzo cha anthu onse akale chadutsa وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ لَيَقُولُنَّ خَلَقَهُنَّ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡعَلِيمُ ٩Ndithudi ngati iwe ukawafunsa kuti, “Kodi ndani adalenga kumwamba ndi dziko lapansi?” Iwo, ndithudi, adzakuyankha kuti, “Mwini mphamvu ndi Mwini wodziwa ndiye amene adazilenga.” ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ مَهۡدًا وَجَعَلَ لَكُمۡ فِيهَا سُبُلًا لَّعَلَّكُمۡ تَهۡتَدُونَ ١٠Iye ndi amene adalenga dziko kukhala malo anu a mpumulo ndipo adaika mu ilo njira kuti inu mukhoza kutsogozedwa bwino وَٱلَّذِي نَزَّلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءَۢ بِقَدَرٍ فَأَنشَرۡنَا بِهِۦ بَلۡدَةً مَّيۡتًاۚ كَذَٰلِكَ تُخۡرَجُونَ ١١Ndipo ndiye amene amatumiza mvula kuchokera kumitambo molingana ndi muyeso. Ndipo Ife timadzutsa nthaka imene idali yakufa ndi iyo, kotero nanunso mudzadzutsidwa chimodzimodzi وَٱلَّذِي خَلَقَ ٱلۡأَزۡوَٰجَ كُلَّهَا وَجَعَلَ لَكُم مِّنَ ٱلۡفُلۡكِ وَٱلۡأَنۡعَٰمِ مَا تَرۡكَبُونَ ١٢Ndipo ndiye amene adalenga zinthu ziwiriziwiri ndipo adapanga zombo ndi nyama kuti muzikwera لِتَسۡتَوُۥاْ عَلَىٰ ظُهُورِهِۦ ثُمَّ تَذۡكُرُواْ نِعۡمَةَ رَبِّكُمۡ إِذَا ٱسۡتَوَيۡتُمۡ عَلَيۡهِ وَتَقُولُواْ سُبۡحَٰنَ ٱلَّذِي سَخَّرَ لَنَا هَٰذَا وَمَا كُنَّا لَهُۥ مُقۡرِنِينَ ١٣Kuti inu mukhoza kukhala okhazikika pa misana pawo ndi kukumbukira ubwino wa Ambuye wanu pamene mumakhazikikapo ndi kunena kuti, “Ulemerero ukhale kwa Iye amene adazipanga izo kukhala zopanda mphamvu kwa ife ndipo ife sitikadatha kutero.” وَإِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا لَمُنقَلِبُونَ ١٤“Ndithudi kwa Ambuye wathu ife tidzabwerera.” وَجَعَلُواْ لَهُۥ مِنۡ عِبَادِهِۦ جُزۡءًاۚ إِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ لَكَفُورٌ مُّبِينٌ ١٥Komabe iwo amawapatsa ena mwa akapolo ake gawo lake. Ndithudi munthu ndi wosayamika أَمِ ٱتَّخَذَ مِمَّا يَخۡلُقُ بَنَاتٍ وَأَصۡفَىٰكُم بِٱلۡبَنِينَ ١٦Kodi Iye wadzisankhira ana aakazi kuchokera ku zimene walenga ndipo adakusankhani inu kukhala ndi ana aamuna وَإِذَا بُشِّرَ أَحَدُهُم بِمَا ضَرَبَ لِلرَّحۡمَٰنِ مَثَلًا ظَلَّ وَجۡهُهُۥ مُسۡوَدًّا وَهُوَ كَظِيمٌ ١٧Ndipo ngati wina wa iwo auzidwa nkhani za chimene Iye amati ndi chofanana ndi Mulungu, nkhope yake imada ndipo amakhala wokwiya أَوَمَن يُنَشَّؤُاْ فِي ٱلۡحِلۡيَةِ وَهُوَ فِي ٱلۡخِصَامِ غَيۡرُ مُبِينٍ ١٨Icho ndi chimene chidapangidwa ngati chosangalatsa ndipo pa mtsutso, icho sichingathe kuyankhula bwinobwino وَجَعَلُواْ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ ٱلَّذِينَ هُمۡ عِبَٰدُ ٱلرَّحۡمَٰنِ إِنَٰثًاۚ أَشَهِدُواْ خَلۡقَهُمۡۚ سَتُكۡتَبُ شَهَٰدَتُهُمۡ وَيُسۡـَٔلُونَ ١٩Ndipo iwo amasandutsa angelo amene ali akapolo a Mulungu, kukhala akazi. Kodi iwo adaonerera chilengedwe chawo? Umboni wawo udzalembedwa ndipo iwo adzafunsidwa وَقَالُواْ لَوۡ شَآءَ ٱلرَّحۡمَٰنُ مَا عَبَدۡنَٰهُمۗ مَّا لَهُم بِذَٰلِكَ مِنۡ عِلۡمٍۖ إِنۡ هُمۡ إِلَّا يَخۡرُصُونَ ٢٠Ndipo iwo adati, “Chikadakhala chifuniro cha Mwini Chisoni Chosatha, ife sitikadapembedza milungu ina.” Iwo sadziwa china chilichonse chokhudza chimenechi. Ndipo iwo amangonama chabe أَمۡ ءَاتَيۡنَٰهُمۡ كِتَٰبًا مِّن قَبۡلِهِۦ فَهُم بِهِۦ مُسۡتَمۡسِكُونَ ٢١Kodi kapena Ife tidawapatsa Buku lina ili lisanadze limene iwo ali kukhulupilira بَلۡ قَالُوٓاْ إِنَّا وَجَدۡنَآ ءَابَآءَنَا عَلَىٰٓ أُمَّةٍ وَإِنَّا عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِم مُّهۡتَدُونَ ٢٢Iyayi! Iwo amati, “Ife tidapeza makolo athu ali kutsatira njira ina ndi chipembedzo china chake ndipo ife timatsogozedwa potsatira zimene iwo amachita.” وَكَذَٰلِكَ مَآ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ فِي قَرۡيَةٍ مِّن نَّذِيرٍ إِلَّا قَالَ مُتۡرَفُوهَآ إِنَّا وَجَدۡنَآ ءَابَآءَنَا عَلَىٰٓ أُمَّةٍ وَإِنَّا عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِم مُّقۡتَدُونَ ٢٣Ndipo Ife sitidatumize Mchenjezi iwe usanadze kwa anthu ena, koma achuma amene anali kukhala pakati pawo ankati; “Ife tidapeza makolo athu ali kutsatira njira yina ndi chipembedzo china chake ndipo ndithudi ife tidzatsatira zimene iwo anali kuchita.” ۞ قَٰلَ أَوَلَوۡ جِئۡتُكُم بِأَهۡدَىٰ مِمَّا وَجَدتُّمۡ عَلَيۡهِ ءَابَآءَكُمۡۖ قَالُوٓاْ إِنَّا بِمَآ أُرۡسِلۡتُم بِهِۦ كَٰفِرُونَ ٢٤Iye adati; “Ngakhale kuti ine nditakubweretserani langizo labwino loposa limene mukuti mudapeza makolo anu ali kutsatira?” Iwo adati, “Ndithudi ife sitikhulupirira zimene iwe ukuti watumizidwa.” فَٱنتَقَمۡنَا مِنۡهُمۡۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُكَذِّبِينَ ٢٥Kotero Ife tidagwetsa chilango pa iwo ndipo taona mmene chinalili chimaliziro cha iwo amene adakana choonadi وَإِذۡ قَالَ إِبۡرَٰهِيمُ لِأَبِيهِ وَقَوۡمِهِۦٓ إِنَّنِي بَرَآءٌ مِّمَّا تَعۡبُدُونَ ٢٦Ndipo Abrahamu adawauza abambo ake pamodzi ndi anthu ake kuti, “Ndithudi ine ndili kudzipatula ku zimene inu mupembedza.” إِلَّا ٱلَّذِي فَطَرَنِي فَإِنَّهُۥ سَيَهۡدِينِ ٢٧“Kupatula yekhayo amene adandilenga ine ndipo, ndithudi, Iye adzanditsogolera.” وَجَعَلَهَا كَلِمَةَۢ بَاقِيَةً فِي عَقِبِهِۦ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ ٢٨Ndipo adawapanga mawu kuti akhazikike mwa iwo amene adadza iye atachoka kuti akhoza kubwerera بَلۡ مَتَّعۡتُ هَٰٓؤُلَآءِ وَءَابَآءَهُمۡ حَتَّىٰ جَآءَهُمُ ٱلۡحَقُّ وَرَسُولٌ مُّبِينٌ ٢٩Iyayi! Koma Ine ndidawapatsa ,iwo ndiponso makolo awo, chisangalalo mpaka pamene choonadi chidadza kwa iwo ndi Mtumwi amene anali kuwafotokozera zonse momveka وَلَمَّا جَآءَهُمُ ٱلۡحَقُّ قَالُواْ هَٰذَا سِحۡرٌ وَإِنَّا بِهِۦ كَٰفِرُونَ ٣٠Koma pamene choonadi chidadza pa iwo, iwo adati, “Awa ndi matsenga ndipo ife sitikhulupirira mwa iwo.” وَقَالُواْ لَوۡلَا نُزِّلَ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانُ عَلَىٰ رَجُلٍ مِّنَ ٱلۡقَرۡيَتَيۡنِ عَظِيمٍ ٣١Ndipo iwo amati: “Bwanji Korani iyi siidatumizidwe kwa munthu wina wotchuka wochokera ku Mzinda wina pakati pa Mizinda iwiri?” أَهُمۡ يَقۡسِمُونَ رَحۡمَتَ رَبِّكَۚ نَحۡنُ قَسَمۡنَا بَيۡنَهُم مَّعِيشَتَهُمۡ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَرَفَعۡنَا بَعۡضَهُمۡ فَوۡقَ بَعۡضٍ دَرَجَٰتٍ لِّيَتَّخِذَ بَعۡضُهُم بَعۡضًا سُخۡرِيًّاۗ وَرَحۡمَتُ رَبِّكَ خَيۡرٌ مِّمَّا يَجۡمَعُونَ ٣٢Kodi ndiwo amene akhoza kugawa gawo lina la chisomo cha Ambuye wako? Ndife amene timagawa pakati pawo chakudya chawo cha moyo uno ndipo tawakweza ena kukhala apamwamba kuposa anzawo kotero kuti akhoza kulemba ntchito anzawo. Koma chisoni cha Ambuye wako ndi chabwino kwambiri kuposa chuma chimene amasonkhanitsa وَلَوۡلَآ أَن يَكُونَ ٱلنَّاسُ أُمَّةً وَٰحِدَةً لَّجَعَلۡنَا لِمَن يَكۡفُرُ بِٱلرَّحۡمَٰنِ لِبُيُوتِهِمۡ سُقُفًا مِّن فِضَّةٍ وَمَعَارِجَ عَلَيۡهَا يَظۡهَرُونَ ٣٣Ndipo zikadakhala kuti anthu onse anali a chipembedzo chimodzi, ndithudi, Ife tikadawapatsa onse amene sakhulupirira mwa Mulungu madenga a siliva kuti aike pa nyumba zawo ndi pa makwerero oti azikwererapo وَلِبُيُوتِهِمۡ أَبۡوَٰبًا وَسُرُرًا عَلَيۡهَا يَتَّكِـُٔونَ ٣٤Ndipo nyumba, zitseko ndi mipando, zonse zikadakhala za siliva kuti azikhalapo وَزُخۡرُفًاۚ وَإِن كُلُّ ذَٰلِكَ لَمَّا مَتَٰعُ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَٱلۡأٓخِرَةُ عِندَ رَبِّكَ لِلۡمُتَّقِينَ ٣٥Ndipo zipangizo zina zikadakhala za golide. Komabe zonsezi sizikadakhala chinthu china koma chisangalalo cha m’moyo uno. Ndipo moyo umene uli nkudza, umene uli ndi Ambuye wako, ndi wa anthu ochita ntchito zabwino وَمَن يَعۡشُ عَن ذِكۡرِ ٱلرَّحۡمَٰنِ نُقَيِّضۡ لَهُۥ شَيۡطَٰنًا فَهُوَ لَهُۥ قَرِينٌ ٣٦Aliyense amene asiya kukumbukira Mwini chisoni chosatha, Ife timamusankhira iye Satana kuti akhale bwenzi lake la pamtima وَإِنَّهُمۡ لَيَصُدُّونَهُمۡ عَنِ ٱلسَّبِيلِ وَيَحۡسَبُونَ أَنَّهُم مُّهۡتَدُونَ ٣٧Ndipo, ndithudi, iwo amangowasokoneza ku njira yoyenera koma iwo amaganiza kuti ali kutsogozedwa bwino حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَنَا قَالَ يَٰلَيۡتَ بَيۡنِي وَبَيۡنَكَ بُعۡدَ ٱلۡمَشۡرِقَيۡنِ فَبِئۡسَ ٱلۡقَرِينُ ٣٨Mpaka pamene wotereyu abwerera kwa Ife, iye amati, pomuuza bwenzi lake la pamtima, “Kukadakhala kuti pakati pa ine ndi iwe panali mtunda wotalika monga kutalikirana kwa kum’mawa kuwiri!” Bwenzi loipa lenileni وَلَن يَنفَعَكُمُ ٱلۡيَوۡمَ إِذ ظَّلَمۡتُمۡ أَنَّكُمۡ فِي ٱلۡعَذَابِ مُشۡتَرِكُونَ ٣٩Ndipo popeza inu munali kuchita zoipa, lero sizidzakuthandizani popeza nonse ndinu olandira chilango أَفَأَنتَ تُسۡمِعُ ٱلصُّمَّ أَوۡ تَهۡدِي ٱلۡعُمۡيَ وَمَن كَانَ فِي ضَلَٰلٍ مُّبِينٍ ٤٠Kodi iwe ungawapange agonthi kumva kapena kutsogolera anthu akhungu kapena kutsogolera iye amene ndi ochimwa فَإِمَّا نَذۡهَبَنَّ بِكَ فَإِنَّا مِنۡهُم مُّنتَقِمُونَ ٤١Ndipo Ife tikakutenga, Ife, ndithudi, tidzagwetsa chilango chathu pa iwo أَوۡ نُرِيَنَّكَ ٱلَّذِي وَعَدۡنَٰهُمۡ فَإِنَّا عَلَيۡهِم مُّقۡتَدِرُونَ ٤٢Kapena ngati Ife titakuonetsa zina zimene tawalonjeza iwo, ndipo ndithudi, Ife tili ndi mphamvu pa zinthu zonse فَٱسۡتَمۡسِكۡ بِٱلَّذِيٓ أُوحِيَ إِلَيۡكَۖ إِنَّكَ عَلَىٰ صِرَٰطٍ مُّسۡتَقِيمٍ ٤٣Kotero gwiritsa chimene chavumbulutsidwa kwa iwe. Ndithudi iwe uli pa njira yoyenera وَإِنَّهُۥ لَذِكۡرٌ لَّكَ وَلِقَوۡمِكَۖ وَسَوۡفَ تُسۡـَٔلُونَ ٤٤Ndipo ndithudi Ichi ndi chikumbutso kwa iwe ndi kwa anthu ako ndipo posachedwapa mudzafunsidwa وَسۡـَٔلۡ مَنۡ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ مِن رُّسُلِنَآ أَجَعَلۡنَا مِن دُونِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ءَالِهَةً يُعۡبَدُونَ ٤٥Ndipo afunse iwo za Atumwi athu amene Ife tidawatuma iwe usanabadwe. Kodi Ife tidasankha milungu ina yoti izipembedzedwa yoonjezera pa Mwini Chisoni Chosatha وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ فَقَالَ إِنِّي رَسُولُ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٤٦Ndipo, ndithudi, Ife tidamutumiza Mose ndi uthenga wathu kwa Farawo ndi mafumu ake ndipo iye adati, “Ndithudi ine ndine Mtumwi wa Ambuye wa zolengedwa zonse.” فَلَمَّا جَآءَهُم بِـَٔايَٰتِنَآ إِذَا هُم مِّنۡهَا يَضۡحَكُونَ ٤٧Koma pamene iye adadza kwa iwo ndi zizindikiro zathu zooneka, iwo adaziseka zizindikirozo وَمَا نُرِيهِم مِّنۡ ءَايَةٍ إِلَّا هِيَ أَكۡبَرُ مِنۡ أُخۡتِهَاۖ وَأَخَذۡنَٰهُم بِٱلۡعَذَابِ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ ٤٨Tidawaonetsa zizindikiro zosiyanasiyana, chilichonse chopambana chinzake, ndipo Ife tidawapatsa chilango kuti akhoza kutembenuka وَقَالُواْ يَٰٓأَيُّهَ ٱلسَّاحِرُ ٱدۡعُ لَنَا رَبَّكَ بِمَا عَهِدَ عِندَكَ إِنَّنَا لَمُهۡتَدُونَ ٤٩Ndipo iwo adati, “oh iwe munthu wamatsenga! Mupemphe Ambuye wako m’malo mwathu, molingana ndi lonjezo limene Iye adapanga ndi iwe. Ndithudi ife tidzatsatira njira yoyenera.” فَلَمَّا كَشَفۡنَا عَنۡهُمُ ٱلۡعَذَابَ إِذَا هُمۡ يَنكُثُونَ ٥٠Koma pamene tidawachotsera chilango, iwo adaphwanya lonjezo lawo وَنَادَىٰ فِرۡعَوۡنُ فِي قَوۡمِهِۦ قَالَ يَٰقَوۡمِ أَلَيۡسَ لِي مُلۡكُ مِصۡرَ وَهَٰذِهِ ٱلۡأَنۡهَٰرُ تَجۡرِي مِن تَحۡتِيٓۚ أَفَلَا تُبۡصِرُونَ ٥١Ndipo Farawo adalengeza pamaso pa anthu ake kuti, “Oh inu anthu anga! Kodi Ufumu wa dziko la Aiguputo si wanga? Nanga mitsinje imene ilikuyenda pansi pa mapazi anga, kodi simuli kuiona?” أَمۡ أَنَا۠ خَيۡرٌ مِّنۡ هَٰذَا ٱلَّذِي هُوَ مَهِينٌ وَلَا يَكَادُ يُبِينُ ٥٢“Kodi ine sindine wopambana kwambiri kuposa munthu wonyozeka amene ali kukanika kuyankhula momveka?” فَلَوۡلَآ أُلۡقِيَ عَلَيۡهِ أَسۡوِرَةٌ مِّن ذَهَبٍ أَوۡ جَآءَ مَعَهُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ مُقۡتَرِنِينَ ٥٣“Nanga ndi chifukwa chiyani iye sadavekedwe zigwinjiri za golide kapena bwanji silinadze ndi iye gulu la angelo lomuperekeza?” فَٱسۡتَخَفَّ قَوۡمَهُۥ فَأَطَاعُوهُۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمًا فَٰسِقِينَ ٥٤Motero iye adawapusitsa anthu ake ndipo iwo amamumvera iye. Ndithudi iwo adali anthu onyoza فَلَمَّآ ءَاسَفُونَا ٱنتَقَمۡنَا مِنۡهُمۡ فَأَغۡرَقۡنَٰهُمۡ أَجۡمَعِينَ ٥٥Ndipo pamene iwo adatikwiyitsa, Ife tidawagwetsera chilango ndipo onse tidawamiza m’madzi فَجَعَلۡنَٰهُمۡ سَلَفًا وَمَثَلًا لِّلۡأٓخِرِينَ ٥٦Ndipo tidawapanga iwo kukhala phunziro kwa mibadwo yam’tsogolo ۞ وَلَمَّا ضُرِبَ ٱبۡنُ مَرۡيَمَ مَثَلًا إِذَا قَوۡمُكَ مِنۡهُ يَصِدُّونَ ٥٧Ndipo pamene mwana wamwamuna wa Maria atchulidwa ngati chitsanzo, taona! Anthu ako amaseka وَقَالُوٓاْ ءَأَٰلِهَتُنَا خَيۡرٌ أَمۡ هُوَۚ مَا ضَرَبُوهُ لَكَ إِلَّا جَدَلَۢاۚ بَلۡ هُمۡ قَوۡمٌ خَصِمُونَ ٥٨Ndipo iwo amati, “Kodi milungu yathu ndiyo yopambana kapena iyeyo ndiye wopambana?” Izi amangozinena kwa iwe ndi cholinga chofuna mikangano ndipo iwo ndi anthu amwano إِنۡ هُوَ إِلَّا عَبۡدٌ أَنۡعَمۡنَا عَلَيۡهِ وَجَعَلۡنَٰهُ مَثَلًا لِّبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٥٩Iye sadali wina koma kapolo wathu amene tidamulangiza chisomo chathu, ndipo tidamupanga Iye kukhala chitsanzo kwa ana a Israyeli وَلَوۡ نَشَآءُ لَجَعَلۡنَا مِنكُم مَّلَٰٓئِكَةً فِي ٱلۡأَرۡضِ يَخۡلُفُونَ ٦٠Ndipo tikadafuna tikadapanga ena a inu kukhala angelo kuti akhale padziko m’malo mwanu وَإِنَّهُۥ لَعِلۡمٌ لِّلسَّاعَةِ فَلَا تَمۡتَرُنَّ بِهَا وَٱتَّبِعُونِۚ هَٰذَا صِرَٰطٌ مُّسۡتَقِيمٌ ٦١Ndithudi ichi ndi chizindikiro cha ola, kotero musakayike za ilo ndipo nditsateni ine. Iyo ndiyo njira yoyenera وَلَا يَصُدَّنَّكُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُۖ إِنَّهُۥ لَكُمۡ عَدُوٌّ مُّبِينٌ ٦٢Ndipo musalole kuti Satana akutchinjirizeni chifukwa, ndithudi, iye ndi mdani wanu weniweni وَلَمَّا جَآءَ عِيسَىٰ بِٱلۡبَيِّنَٰتِ قَالَ قَدۡ جِئۡتُكُم بِٱلۡحِكۡمَةِ وَلِأُبَيِّنَ لَكُم بَعۡضَ ٱلَّذِي تَخۡتَلِفُونَ فِيهِۖ فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ٦٣Pamene Yesu adadza ndi zizindikiro zooneka adati, “Tsopano ndadza kwa inu ndi luntha ndi cholinga chokuuzani tsatanetsatane za fundo zina zimene mumatsutsana. Motero opani Mulungu ndipo mundimvere ine.” إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ رَبِّي وَرَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُوهُۚ هَٰذَا صِرَٰطٌ مُّسۡتَقِيمٌ ٦٤“Ndithudi Mulungu! Ndiye Ambuye wanga ndi Ambuye wanu. Motero mutumikireni Iye. Imeneyi ndiyo njira yoyenera.” فَٱخۡتَلَفَ ٱلۡأَحۡزَابُ مِنۢ بَيۡنِهِمۡۖ فَوَيۡلٌ لِّلَّذِينَ ظَلَمُواْ مِنۡ عَذَابِ يَوۡمٍ أَلِيمٍ ٦٥Koma magulu ena a pakati pawo adapatukana, kotero tsoka kwa iwo amene adali oipa chifukwa cha chilango chowawa chimene chidzadza pa iwo patsiku la masautso هَلۡ يَنظُرُونَ إِلَّا ٱلسَّاعَةَ أَن تَأۡتِيَهُم بَغۡتَةً وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ ٦٦Kodi iwo ali kungodikira kuti ola lidzadza pa iwo mwadzidzidzi pamene iwo sali kudziwa ٱلۡأَخِلَّآءُ يَوۡمَئِذِۭ بَعۡضُهُمۡ لِبَعۡضٍ عَدُوٌّ إِلَّا ٱلۡمُتَّقِينَ ٦٧Abwenzi patsiku limeneli adzasanduka adani kupatula okhawo amene amalewa zoipa يَٰعِبَادِ لَا خَوۡفٌ عَلَيۡكُمُ ٱلۡيَوۡمَ وَلَآ أَنتُمۡ تَحۡزَنُونَ ٦٨oh inu akapolo anga! Palibe chochititsa mantha kwa inu lero lino ndipo simudzamva chisoni ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَكَانُواْ مُسۡلِمِينَ ٦٩Inu amene mwakhulupirira chivumbulutso chathu ndipo munali Asilamu ٱدۡخُلُواْ ٱلۡجَنَّةَ أَنتُمۡ وَأَزۡوَٰجُكُمۡ تُحۡبَرُونَ ٧٠Lowani m’Paradiso, inu pamodzi ndi akazi anu ndipo mudzasangalatsidwa يُطَافُ عَلَيۡهِم بِصِحَافٍ مِّن ذَهَبٍ وَأَكۡوَابٍۖ وَفِيهَا مَا تَشۡتَهِيهِ ٱلۡأَنفُسُ وَتَلَذُّ ٱلۡأَعۡيُنُۖ وَأَنتُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ ٧١Mbale za golide ndi zikho zomwera zidzaperekedwa kwa iwo ndipo mu izo mudzakhala zimene mitima yawo inali kulakalaka ndi ponso zosangalala kuziona. Ndipo inu mudzakhala momwemo mpaka kalekale وَتِلۡكَ ٱلۡجَنَّةُ ٱلَّتِيٓ أُورِثۡتُمُوهَا بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ ٧٢Ndipo uwu ndi munda umene mwapatsidwa kuti mukhalemo chifukwa cha zimene mudachita لَكُمۡ فِيهَا فَٰكِهَةٌ كَثِيرَةٌ مِّنۡهَا تَأۡكُلُونَ ٧٣M’menemo mudzapeza zipatso zochuluka zimene muzidzadya إِنَّ ٱلۡمُجۡرِمِينَ فِي عَذَابِ جَهَنَّمَ خَٰلِدُونَ ٧٤Ndithudi onse osakhulupirira adzakhala ku moto wa ku Gahena mpaka kalekale لَا يُفَتَّرُ عَنۡهُمۡ وَهُمۡ فِيهِ مُبۡلِسُونَ ٧٥Chilango chawo sichidzachepetsedwa ndipo adzasowa chonena chifukwa adzakhala ndi mantha وَمَا ظَلَمۡنَٰهُمۡ وَلَٰكِن كَانُواْ هُمُ ٱلظَّٰلِمِينَ ٧٦Ife sitidawalakwire koma iwo adadzilakwitsa okha وَنَادَوۡاْ يَٰمَٰلِكُ لِيَقۡضِ عَلَيۡنَا رَبُّكَۖ قَالَ إِنَّكُم مَّٰكِثُونَ ٧٧Ndipo iwo adzalira kuti, “Oh Maliki! Muuze Ambuye wako kuti atimalize ife! Ndipo iye adzati, “Ndithudi inu mudzakhalabe ndi moyo.” لَقَدۡ جِئۡنَٰكُم بِٱلۡحَقِّ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَكُمۡ لِلۡحَقِّ كَٰرِهُونَ ٧٨Ndithudi Ife tabweretsa choonadi kwa iwe koma ambiri a inu mumadana ndi choonadi أَمۡ أَبۡرَمُوٓاْ أَمۡرًا فَإِنَّا مُبۡرِمُونَ ٧٩Kapene iwo ali ndi chikonzekero china? Motero nafenso tili kukonzeka أَمۡ يَحۡسَبُونَ أَنَّا لَا نَسۡمَعُ سِرَّهُمۡ وَنَجۡوَىٰهُمۚ بَلَىٰ وَرُسُلُنَا لَدَيۡهِمۡ يَكۡتُبُونَ ٨٠Kapena iwo amaganiza kuti Ife sitikumva zimene amabisa ndi nkhani zawo za chinsinsi? Ndithudi Ife timamva ndipo Atumwi athu amene ali pakati pawo amalemba chilichonse قُلۡ إِن كَانَ لِلرَّحۡمَٰنِ وَلَدٌ فَأَنَا۠ أَوَّلُ ٱلۡعَٰبِدِينَ ٨١Nena, “Ngati Mwini Chisoni Chosatha akadakhala ndi Mwana, ine ndikadakhala woyamba kumupembedza.” سُبۡحَٰنَ رَبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ رَبِّ ٱلۡعَرۡشِ عَمَّا يَصِفُونَ ٨٢“Ulemerero ukhale kwa Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, Ambuye Mwini mpando wachifumu! Iye akhale pamwamba pa zimene amukundukira Iye.” فَذَرۡهُمۡ يَخُوضُواْ وَيَلۡعَبُواْ حَتَّىٰ يُلَٰقُواْ يَوۡمَهُمُ ٱلَّذِي يُوعَدُونَ ٨٣Kotero aleke kuti ayambe kuyankhula zinthu zopanda pake ndi kusewera mpaka pamene akumana ndi tsiku limene amaopsedwa nalo وَهُوَ ٱلَّذِي فِي ٱلسَّمَآءِ إِلَٰهٌ وَفِي ٱلۡأَرۡضِ إِلَٰهٌۚ وَهُوَ ٱلۡحَكِيمُ ٱلۡعَلِيمُ ٨٤Iye ndiye Mulungu wakumwamba ndi Mulungu wa padziko lapansi ndipo Iye ndi waluntha ndi wodziwa chinthu china chilichonse وَتَبَارَكَ ٱلَّذِي لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا وَعِندَهُۥ عِلۡمُ ٱلسَّاعَةِ وَإِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ ٨٥Ndipo wodala ndi Mwini Ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo. Iye ndiye amene amadziwa ola lachiweruzo ndipo kwa Iye ndi kumene nonse mudzabwerera وَلَا يَمۡلِكُ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ مِن دُونِهِ ٱلشَّفَٰعَةَ إِلَّا مَن شَهِدَ بِٱلۡحَقِّ وَهُمۡ يَعۡلَمُونَ ٨٦Ndipo onse amene amawapembedza oonjezera pa Mulungu alibe mphamvu yowaimirira kupatula yekhayo amene amachitira umboni woona ndiye amene iwo amamudziwa وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَهُمۡ لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُۖ فَأَنَّىٰ يُؤۡفَكُونَ ٨٧Ndipo ngati iwe utawafunsa kuti kodi adawalenga ndani? Ndithudi iwo adzayankha kuti, “Mulungu.” Nanga ndi chifukwa chiyani amasiya choonadi وَقِيلِهِۦ يَٰرَبِّ إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ قَوۡمٌ لَّا يُؤۡمِنُونَ ٨٨Ndi zonena zake kuti, “Ambuye wanga! Ndithudi awa ndi anthu amene safuna kukhulupirira.” فَٱصۡفَحۡ عَنۡهُمۡ وَقُلۡ سَلَٰمٌۚ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ ٨٩Kotero asiye okha ndipo nena, “Mtendere!” Koma iwo adzadziwa posachedwapa