بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
وَيۡلٌ لِّلۡمُطَفِّفِينَ ١Tsoka kwa iwo onse amene amagulitsa malonda awo monyenga ٱلَّذِينَ إِذَا ٱكۡتَالُواْ عَلَى ٱلنَّاسِ يَسۡتَوۡفُونَ ٢Iwo amene amati ena akamawayesera zinthu amafuna kuti zikwanire muyeso wake وَإِذَا كَالُوهُمۡ أَو وَّزَنُوهُمۡ يُخۡسِرُونَ ٣Koma pamene iwo ayesa kapena awayesera anthu ena amawanyenga أَلَا يَظُنُّ أُوْلَٰٓئِكَ أَنَّهُم مَّبۡعُوثُونَ ٤Kodi iwo saganiza kuti adzaukitsidwa kwa akufa لِيَوۡمٍ عَظِيمٍ ٥Patsiku lalikulu يَوۡمَ يَقُومُ ٱلنَّاسُ لِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٦Tsiku limene anthu a mitundu yonse adzaima pamaso pa Ambuye wa zolengedwa zonse كـَلَّآ إِنَّ كِتَٰبَ ٱلۡفُجَّارِ لَفِي سِجِّينٍ ٧Iyayi! Ndithudi chiwerengero cha anthu onse oipa chili mu Sijjin وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا سِجِّينٌ ٨Kodi udzadziwa bwanji Sijjin ndi chiyani كِتَٰبٌ مَّرۡقُومٌ ٩Ili ndi Buku lolembedwa وَيۡلٌ يَوۡمَئِذٍ لِّلۡمُكَذِّبِينَ ١٠Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira ٱلَّذِينَ يُكَذِّبُونَ بِيَوۡمِ ٱلدِّينِ ١١Iwo amene amakana kuti kuli tsiku lachiweruzo وَمَا يُكَذِّبُ بِهِۦٓ إِلَّا كُلُّ مُعۡتَدٍ أَثِيمٍ ١٢Palibe wina amene amalikana tsikuli kupatula munthu wogona m’machimo إِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِ ءَايَٰتُنَا قَالَ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ ١٣Pamene chivumbulutso chathu chinenedwa kwa iye, iye amati: “Izi ndizo nthano za anthu akale.” كـَلَّاۖ بَلۡۜ رَانَ عَلَىٰ قُلُوبِهِم مَّا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ ١٤Iyayi! Koma m’mitima mwawo ndi mokutidwa ndi zintchito zimene amachita كـَلَّآ إِنَّهُمۡ عَن رَّبِّهِمۡ يَوۡمَئِذٍ لَّمَحۡجُوبُونَ ١٥Iyayi! Ndithudi iwo sadzaloledwa kuona Ambuye wawo pa tsikuli ثُمَّ إِنَّهُمۡ لَصَالُواْ ٱلۡجَحِيمِ ١٦Ndipo iwo adzalowa ndi kulawa moto ku Gahena ثُمَّ يُقَالُ هَٰذَا ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تُكَذِّبُونَ ١٧Ndipo kudzanenedwa kwa iwo kuti: “Chimenechi ndicho chilango chija munkachinena kuti sichidzakhalako.” كـَلَّآ إِنَّ كِتَٰبَ ٱلۡأَبۡرَارِ لَفِي عِلِّيِّينَ ١٨Iyayi! Ndithudi chiwerengero cha anthu olungama chimasungidwa mu Illiyyun وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا عِلِّيُّونَ ١٩Kodi mudzadziwa bwanji kuti Illiyin wapamwambayo ndi chiyani كِتَٰبٌ مَّرۡقُومٌ ٢٠Ndi Al Mutaffifin 645 Buku lochita kulembedwa يَشۡهَدُهُ ٱلۡمُقَرَّبُونَ ٢١Limene limaonedwa ndi iwo okhawo amene ali kufupi ndi zofuna za Mulungu إِنَّ ٱلۡأَبۡرَارَ لَفِي نَعِيمٍ ٢٢Ndithudi anthu onse olungama adzakhala ku malo a mtendere عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِ يَنظُرُونَ ٢٣Atakhala pa mipando ya wofowofo ndipo ali kuyang’ana uku ndi uku تَعۡرِفُ فِي وُجُوهِهِمۡ نَضۡرَةَ ٱلنَّعِيمِ ٢٤Ndipo udzaona chisangalalo pa nkhope zawo يُسۡقَوۡنَ مِن رَّحِيقٍ مَّخۡتُومٍ ٢٥Iwo adzapatsidwa kuti amwe vinyo weniweni amene sanatsegulidwepo خِتَٰمُهُۥ مِسۡكٌۚ وَفِي ذَٰلِكَ فَلۡيَتَنَافَسِ ٱلۡمُتَنَٰفِسُونَ ٢٦Womaliza wake adzakhala ndi fungo labwino ndipo pachifukwa cha ichi, aleke onse amene afuna kulimbikira kuti alimbike وَمِزَاجُهُۥ مِن تَسۡنِيمٍ ٢٧Wosakanizidwa ndi madzi a Tasnim عَيۡنًا يَشۡرَبُ بِهَا ٱلۡمُقَرَّبُونَ ٢٨Kasupe amene anthu odala adzakhala ali kumwa إِنَّ ٱلَّذِينَ أَجۡرَمُواْ كَانُواْ مِنَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ يَضۡحَكُونَ ٢٩Ndithudi! Anthu amene amachita zoipa, anali kuwaseka anthu amene anakhulupirira وَإِذَا مَرُّواْ بِهِمۡ يَتَغَامَزُونَ ٣٠Ndi kumacheulana iwo akamadutsa pakati pawo وَإِذَا ٱنقَلَبُوٓاْ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِمُ ٱنقَلَبُواْ فَكِهِينَ ٣١Ndipo iwo amati akabwerera kwa anthu awo amabwera ali kunyoza وَإِذَا رَأَوۡهُمۡ قَالُوٓاْ إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ لَضَآلُّونَ ٣٢Ndipo amati akawaona iwo amati: “Ndithudi awa ndiwo anthu osochera.” وَمَآ أُرۡسِلُواْ عَلَيۡهِمۡ حَٰفِظِينَ ٣٣Pamene iwo sadalamulidwe kuti akhale owayang’anira فَٱلۡيَوۡمَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مِنَ ٱلۡكُفَّارِ يَضۡحَكُونَ ٣٤Koma pa tsikuli anthu okhulupirira adzaseka anthu osakhulupirira عَلَى ٱلۡأَرَآئِكِ يَنظُرُونَ ٣٥Ali pa mipando yawofowofo ndi kumayang’ana هَلۡ ثُوِّبَ ٱلۡكُفَّارُ مَا كَانُواْ يَفۡعَلُونَ ٣٦Kodi anthu osakhulupirira, sanalipidwe mphotho yawo molingana ndi ntchito zawo