بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
إِذَا ٱلسَّمَآءُ ٱنفَطَرَتۡ ١Pamene thambo lidzang’ambika وَإِذَا ٱلۡكَوَاكِبُ ٱنتَثَرَتۡ ٢Pamene nyenyezi zidzagwa ndi kubalalitsidwa وَإِذَا ٱلۡبِحَارُ فُجِّرَتۡ ٣Ndi pamene nyanja zikuluzikulu zidzaphulika وَإِذَا ٱلۡقُبُورُ بُعۡثِرَتۡ ٤Pamene manda adzatseguka عَلِمَتۡ نَفۡسٌ مَّا قَدَّمَتۡ وَأَخَّرَتۡ ٥Pamenepo Mzimu uliwonse udzadziwa chimene udatumiza ndi chimene udasiya m’mbuyo يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡإِنسَٰنُ مَا غَرَّكَ بِرَبِّكَ ٱلۡكَرِيمِ ٦oh Iwe munthu! Kodi ndi chiyani chikukunamiza kuti usiye kutsatira malamulo a Ambuye wako Wolemekezeka ٱلَّذِي خَلَقَكَ فَسَوَّىٰكَ فَعَدَلَكَ ٧Amene adakulenga iwe ndi kukukonza kuti uzioneka bwino monga mmene uonekeramu فِيٓ أَيِّ صُورَةٍ مَّا شَآءَ رَكَّبَكَ ٨Ndi nkhope ina iliyonse imene idamukondweretsa anakulenga iwe كـَلَّا بَلۡ تُكَذِّبُونَ بِٱلدِّينِ ٩Iyayi! Koma inu mukukana kuti kudzakhala tsiku lachiweruzo وَإِنَّ عَلَيۡكُمۡ لَحَٰفِظِينَ ١٠Koma pakati panu pali ena amene ali kukuyang’anirani كِرَامًا كَٰتِبِينَ ١١Olemekezeka ndi odziwa kulemba يَعۡلَمُونَ مَا تَفۡعَلُونَ ١٢Iwo amadziwa chilichonse chimene mumachita إِنَّ ٱلۡأَبۡرَارَ لَفِي نَعِيمٍ ١٣Ndithudi anthu onse angwiro adzakhala mu mtendere وَإِنَّ ٱلۡفُجَّارَ لَفِي جَحِيمٍ ١٤Ndipo, ndithudi, anthu onse oipa adzakhala ku Gahena يَصۡلَوۡنَهَا يَوۡمَ ٱلدِّينِ ١٥Imene iwo adzalowako ndi kulawa malawi ake patsiku lachiweruzo وَمَا هُمۡ عَنۡهَا بِغَآئِبِينَ ١٦Iwo sadzatha kuthawa ayi وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا يَوۡمُ ٱلدِّينِ ١٧Kodi chidzakuuza ndi chiani za tsiku lachiweruzo ثُمَّ مَآ أَدۡرَىٰكَ مَا يَوۡمُ ٱلدِّينِ ١٨Tinenanso kodi chidzakuuza ndi chiani za tsiku lachiweruzo يَوۡمَ لَا تَمۡلِكُ نَفۡسٌ لِّنَفۡسٍ شَيۡـًٔاۖ وَٱلۡأَمۡرُ يَوۡمَئِذٍ لِّلَّهِ ١٩Ndi tsiku limene mzimu uliwonse sudzatha kuthandiza wina aliyense ndipo Mulungu yekha ndiye amene adzaweruza