ملة الإسلام

السورة 73 · 20 آية · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

سورة المزمل باللغة الشيشيوا

السورة بالعربية مع التفسير استمع إلى سورة المزمل (1,296 قارئاً)
مكيةسورة المزمل٢٠ آية

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمُزَّمِّلُ ١Oh iwe amene wadzikulunga m’chovala قُمِ ٱلَّيۡلَ إِلَّا قَلِيلًا ٢Dzuka usiku onse kupatula kwanthawi kochepa نِّصۡفَهُۥٓ أَوِ ٱنقُصۡ مِنۡهُ قَلِيلًا ٣Theka la usikuwo kapena kanthawi kocheperako أَوۡ زِدۡ عَلَيۡهِ وَرَتِّلِ ٱلۡقُرۡءَانَ تَرۡتِيلًا ٤Kapena kwa kanthawi kochulukirapo ndipo lakatula Korani modekha ndi modukizadukiza monga mmene umayenera kuchitikira إِنَّا سَنُلۡقِي عَلَيۡكَ قَوۡلًا ثَقِيلًا ٥Ndithudi, Ife tidzakutumizira Mawu a mphamvu إِنَّ نَاشِئَةَ ٱلَّيۡلِ هِيَ أَشَدُّ وَطۡـًٔا وَأَقۡوَمُ قِيلًا ٦Ndithudi kuuka nthawi ya usiku ndi kovuta, ndipo mau amatchulidwa bwino إِنَّ لَكَ فِي ٱلنَّهَارِ سَبۡحًا طَوِيلًا ٧Ndithudi, iwe masana umatangwanika kwambiri وَٱذۡكُرِ ٱسۡمَ رَبِّكَ وَتَبَتَّلۡ إِلَيۡهِ تَبۡتِيلًا ٨Ndipo uzikumbukira dzina la Ambuye wako ndipo udzipereke kwathunthu kwa Iye رَّبُّ ٱلۡمَشۡرِقِ وَٱلۡمَغۡرِبِ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ فَٱتَّخِذۡهُ وَكِيلًا ٩Iye ndiye Ambuye wa kum’mawa ndi wa kumadzulo. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Mulandire Iye kuti akhale Mtetezi wako وَٱصۡبِرۡ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَٱهۡجُرۡهُمۡ هَجۡرًا جَمِيلًا ١٠Pirira pa zonse zimene ali kunena ndipo siyana nawo mwaulemu وَذَرۡنِي وَٱلۡمُكَذِّبِينَ أُوْلِي ٱلنَّعۡمَةِ وَمَهِّلۡهُمۡ قَلِيلًا ١١Undisiyire Ine onse amene amakana choonadi nthawi zonse ndipo pirira ndi iwo pakanthawi kochepa إِنَّ لَدَيۡنَآ أَنكَالًا وَجَحِيمًا ١٢Ife, ndithudi, tili ndi unyolo ndipo tawasungira moto wosatha kuuzima وَطَعَامًا ذَا غُصَّةٍ وَعَذَابًا أَلِيمًا ١٣Ndi chakudya chotsamwitsa ndi chilango chowawa يَوۡمَ تَرۡجُفُ ٱلۡأَرۡضُ وَٱلۡجِبَالُ وَكَانَتِ ٱلۡجِبَالُ كَثِيبًا مَّهِيلًا ١٤Patsiku limene dziko ndi mapiri zidzagwedezeka kwambiri ndipo mapiri adzakhala mulu wa mchenga wotaika umene umatuluka kupansi إِنَّآ أَرۡسَلۡنَآ إِلَيۡكُمۡ رَسُولًا شَٰهِدًا عَلَيۡكُمۡ كَمَآ أَرۡسَلۡنَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ رَسُولًا ١٥Ndithudi Ife tatumiza Mtumwi kukhala umboni wokutsutsani monga momwe tidatumizira Mtumwi kwa Farao فَعَصَىٰ فِرۡعَوۡنُ ٱلرَّسُولَ فَأَخَذۡنَٰهُ أَخۡذًا وَبِيلًا ١٦Koma Farao sadamumvere Mtumwi ndipo Ife tidamulanga ndi chilango choopsa فَكَيۡفَ تَتَّقُونَ إِن كَفَرۡتُمۡ يَوۡمًا يَجۡعَلُ ٱلۡوِلۡدَٰنَ شِيبًا ١٧Kodi ngati inu simukhulupirira, mudzalithawa bwanji tsiku limene lidzachititsa ana anu a ang’ono kukhala ndi imvi ٱلسَّمَآءُ مُنفَطِرُۢ بِهِۦۚ كَانَ وَعۡدُهُۥ مَفۡعُولًا ١٨Tsiku limene thambo la kumwamba lidzang’ambika pakati. Ndithudi lonjezo la Mulungu lidzakwaniritsidwa إِنَّ هَٰذِهِۦ تَذۡكِرَةٌۖ فَمَن شَآءَ ٱتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِۦ سَبِيلًا ١٩Ndithudi ili ndi chenjezo chabe, motero musiyeni aliyense amene afuna kuti atsatire njira yoyenera yonka kwa Ambuye wake kuti aitsatire ۞ إِنَّ رَبَّكَ يَعۡلَمُ أَنَّكَ تَقُومُ أَدۡنَىٰ مِن ثُلُثَيِ ٱلَّيۡلِ وَنِصۡفَهُۥ وَثُلُثَهُۥ وَطَآئِفَةٌ مِّنَ ٱلَّذِينَ مَعَكَۚ وَٱللَّهُ يُقَدِّرُ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَۚ عَلِمَ أَن لَّن تُحۡصُوهُ فَتَابَ عَلَيۡكُمۡۖ فَٱقۡرَءُواْ مَا تَيَسَّرَ مِنَ ٱلۡقُرۡءَانِۚ عَلِمَ أَن سَيَكُونُ مِنكُم مَّرۡضَىٰ وَءَاخَرُونَ يَضۡرِبُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ يَبۡتَغُونَ مِن فَضۡلِ ٱللَّهِ وَءَاخَرُونَ يُقَٰتِلُونَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِۖ فَٱقۡرَءُواْ مَا تَيَسَّرَ مِنۡهُۚ وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَ وَأَقۡرِضُواْ ٱللَّهَ قَرۡضًا حَسَنًاۚ وَمَا تُقَدِّمُواْ لِأَنفُسِكُم مِّنۡ خَيۡرٍ تَجِدُوهُ عِندَ ٱللَّهِ هُوَ خَيۡرًا وَأَعۡظَمَ أَجۡرًاۚ وَٱسۡتَغۡفِرُواْ ٱللَّهَۖ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمُۢ ٢٠NdithudiAmbuye wako amadziwa kuti nthawi zina iwe umakhala tcheru mphindi ziwiri pakati pa mphindi zitatu za usiku, mwina theka la usiku ndipo nthawi zina mphindi imodzi pakati pa mphindi zitatu za usiku, monga momwe gulu lina la anthu amene ali nawe. Ndipo Mulungu ndiye amene amasiyanitsa usiku ndi usana. Iye amadziwa kuti siungathe kupemphera mphindi zonse ndipo wakuyang’ana mwachisoni. Kotero lakatula magawo ena a Korani amene angakhale apafupi kwa iwe. Iye amadziwa kuti pakati panu pali anthu odwala ndi ena amene ali kupita uku ndi uku padziko kufunafuna zokoma za Mulungu ndi ena amene ali kumenya nkhondo m’njira ya Mulungu. Motero lakatula, mawu a m’Korani, amene ungathe kulakatula, ndipo pitiriza kupemphera ndipo pereka msonkho wothandiza anthu osauka ndipo kongoza ngongole yabwino kwa Mulungu ndipo chabwino chilichonse chimene muli kutsogoza, mudzachipeza kwa Mulungu, chitasungidwa bwino ndipo mudzalandira mphotho ya mtengo wapatali kuchokera kwa Iye. Ndipo pempha chikhululukiro kwa Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wa chisoni chosatha

الترجمة: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.