ملة الإسلام

السورة 75 · 40 آية · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

سورة القيامة باللغة الشيشيوا

السورة بالعربية مع التفسير استمع إلى سورة القيامة (1,389 قارئاً)
مكيةسورة القيامة٤٠ آية

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

لَآ أُقۡسِمُ بِيَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ ١Ine ndilumbira pali tsiku lachiweruzo وَلَآ أُقۡسِمُ بِٱلنَّفۡسِ ٱللَّوَّامَةِ ٢Ndipo ndilumbira pali munthu amene amadzidzudzula yekha أَيَحۡسَبُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَلَّن نَّجۡمَعَ عِظَامَهُۥ ٣Kodi munthu amaganiza kuti Ife sitidzalumikiza mafupa ake بَلَىٰ قَٰدِرِينَ عَلَىٰٓ أَن نُّسَوِّيَ بَنَانَهُۥ ٤Inde Ife tikhoza kulumikiza mwaubwino nsonga za zala zake بَلۡ يُرِيدُ ٱلۡإِنسَٰنُ لِيَفۡجُرَ أَمَامَهُۥ ٥Ngakhale tero, munthu amafuna kupitiliza kuchita zoipa يَسۡـَٔلُ أَيَّانَ يَوۡمُ ٱلۡقِيَٰمَةِ ٦Iye amafunsa: “Kodi zimenezi zidzachitika liti?” فَإِذَا بَرِقَ ٱلۡبَصَرُ ٧Motero pamene maso adzathodwa وَخَسَفَ ٱلۡقَمَرُ ٨Ndipo pamene mwezi udetsedwa وَجُمِعَ ٱلشَّمۡسُ وَٱلۡقَمَرُ ٩Pamene dzuwa ndi mwezi zidzakumana يَقُولُ ٱلۡإِنسَٰنُ يَوۡمَئِذٍ أَيۡنَ ٱلۡمَفَرُّ ١٠Patsikuli munthu adzafunsa kuti: “Kodi ndithawira kuti tsopano?” كـَلَّا لَا وَزَرَ ١١Iai! Kulibe malo othawirako إِلَىٰ رَبِّكَ يَوۡمَئِذٍ ٱلۡمُسۡتَقَرُّ ١٢Ndi kwa Ambuye wako kokha kumene kudzakhala kothawira يُنَبَّؤُاْ ٱلۡإِنسَٰنُ يَوۡمَئِذِۭ بِمَا قَدَّمَ وَأَخَّرَ ١٣Patsiku limeneli, munthu adzauzidwa zonse zimene adachita kuyambira poyamba mpaka pomaliza بَلِ ٱلۡإِنسَٰنُ عَلَىٰ نَفۡسِهِۦ بَصِيرَةٌ ١٤Iai! Munthu adzadzichitira umboni wodzineneza yekha وَلَوۡ أَلۡقَىٰ مَعَاذِيرَهُۥ ١٥Ngakhale kuti iye azidzayesa kudzipulumutsa yekha لَا تُحَرِّكۡ بِهِۦ لِسَانَكَ لِتَعۡجَلَ بِهِۦٓ ١٦Usagwedeze lilime lako zokhudza Korani ponena mofulumira إِنَّ عَلَيۡنَا جَمۡعَهُۥ وَقُرۡءَانَهُۥ ١٧Ndi udindo wathu kuisonkhanitsa ndi kukupatsa nzeru kuilakatula iyo فَإِذَا قَرَأۡنَٰهُ فَٱتَّبِعۡ قُرۡءَانَهُۥ ١٨Ndipo pamene talakatula, tsatira mwandondomeko kalakatulidwe kake ثُمَّ إِنَّ عَلَيۡنَا بَيَانَهُۥ ١٩Ndi udindo wathu kukufotokozera tanthauzo lake كـَلَّا بَلۡ تُحِبُّونَ ٱلۡعَاجِلَةَ ٢٠Iyayi!Komainumukondamoyowothamsanga وَتَذَرُونَ ٱلۡأٓخِرَةَ ٢١Ndipo simufuna kulabadira za moyo umene uli nkudza وُجُوهٌ يَوۡمَئِذٍ نَّاضِرَةٌ ٢٢Nkhope zina, pa tsiku limeneli, zidzakhala zowala ndi chisangalalo إِلَىٰ رَبِّهَا نَاظِرَةٌ ٢٣Zili kuyang’ana kwa Ambuye wawo وَوُجُوهٌ يَوۡمَئِذِۭ بَاسِرَةٌ ٢٤Ndipo nkhope zina, patsiku limeneli, zidzakhala zachisoni تَظُنُّ أَن يُفۡعَلَ بِهَا فَاقِرَةٌ ٢٥Pozindikira kuti chilango chowawa chidzagwa pa iwo كـَلَّآ إِذَا بَلَغَتِ ٱلتَّرَاقِيَ ٢٦Iyayi, pamene ufika mpaka pa khosi وَقِيلَ مَنۡۜ رَاقٍ ٢٧Ndipo kudzanenedwa kuti: “Kodi palibe woti angamuchize ndi kumupulumutsa ku imfa?” وَظَنَّ أَنَّهُ ٱلۡفِرَاقُ ٢٨Ndipo iye adzadziwa kuti awa ndi mathero a moyo wake وَٱلۡتَفَّتِ ٱلسَّاقُ بِٱلسَّاقِ ٢٩Ndipo mwendo udzatembenuzika pa unzake إِلَىٰ رَبِّكَ يَوۡمَئِذٍ ٱلۡمَسَاقُ ٣٠Tsiku limeneli zonse zidzabwerera kwa Ambuye wako فَلَا صَدَّقَ وَلَا صَلَّىٰ ٣١Iye sanali kuvomereza chilungamo kapena kupemphera وَلَٰكِن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ ٣٢Koma m’malo mwake adakana choonadi ndi kubwerera m’mbuyo ثُمَّ ذَهَبَ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ يَتَمَطَّىٰٓ ٣٣Ndipo iye anapita kubanja lake monyada ali kudziyamikila yekha أَوۡلَىٰ لَكَ فَأَوۡلَىٰ ٣٤Tsoka kwa iwe. Ndiponso tsoka kwa iwe ثُمَّ أَوۡلَىٰ لَكَ فَأَوۡلَىٰٓ ٣٥Kachiwiri tsoka lili pafupi ndi iwe, tsopano tsoka lili pafupi أَيَحۡسَبُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَن يُتۡرَكَ سُدًى ٣٦Kodi munthu amaganiza kuti tidzangomulekerera kuti azichita chilichonse chimene afuna أَلَمۡ يَكُ نُطۡفَةً مِّن مَّنِيٍّ يُمۡنَىٰ ٣٧Kodi iye sanali dontho la umuna limene lidatuluka ثُمَّ كَانَ عَلَقَةً فَخَلَقَ فَسَوَّىٰ ٣٨Ndipo iye adakhala kam’bulu ka magazi. Ndipo Mulungu adamuumba ndipo adamukonza m’maonekedwe okongola فَجَعَلَ مِنۡهُ ٱلزَّوۡجَيۡنِ ٱلذَّكَرَ وَٱلۡأُنثَىٰٓ ٣٩Ndipo adamulenga m’mitundu iwiri, mwamuna ndi mkazi أَلَيۡسَ ذَٰلِكَ بِقَٰدِرٍ عَلَىٰٓ أَن يُحۡـِۧيَ ٱلۡمَوۡتَىٰ ٤٠Kodi Iye alibe mphamvu yopereka moyo kwa anthu akufa

الترجمة: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.