ملة الإسلام

السورة 53 · 62 آية · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

سورة النجم باللغة الشيشيوا

السورة بالعربية مع التفسير استمع إلى سورة النجم (1,299 قارئاً)
مكيةسورة النجم٦٢ آية

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

وَٱلنَّجۡمِ إِذَا هَوَىٰ ١Ndi pali nyenyezi pamene ili kulowa مَا ضَلَّ صَاحِبُكُمۡ وَمَا غَوَىٰ ٢M’bale wanu sadasochere kapena kuti ndi wolakwa وَمَا يَنطِقُ عَنِ ٱلۡهَوَىٰٓ ٣Ndipo iye sayankhula zofuna zake إِنۡ هُوَ إِلَّا وَحۡيٌ يُوحَىٰ ٤Icho ndi chochita kuuzidwa kwa iye عَلَّمَهُۥ شَدِيدُ ٱلۡقُوَىٰ ٥Iye adaphunzitsidwa ndi Iye amene ali ndi mphamvu ذُو مِرَّةٍ فَٱسۡتَوَىٰ ٦Wopanda chilema chilichonse, kotero adadzuka ndi kukhala wokhazikika وَهُوَ بِٱلۡأُفُقِ ٱلۡأَعۡلَىٰ ٧Pamene iye anali patali kwambiri mu mlengalenga ثُمَّ دَنَا فَتَدَلَّىٰ ٨Ndipo adasendera ndi kudza pafupi فَكَانَ قَابَ قَوۡسَيۡنِ أَوۡ أَدۡنَىٰ ٩Ndipo adali pa mtunda wolingana kuponya mipaliro iwiri kapena kucheperapo فَأَوۡحَىٰٓ إِلَىٰ عَبۡدِهِۦ مَآ أَوۡحَىٰ ١٠Motero Iye adaulula Uthenga kwa kapolo wake kudzera mwa Gabriyele مَا كَذَبَ ٱلۡفُؤَادُ مَا رَأَىٰٓ ١١Mtima wake wa Mtumwi siudaname ponena zimene iye adaona أَفَتُمَٰرُونَهُۥ عَلَىٰ مَا يَرَىٰ ١٢Kodi inu mudzatsutsana naye pa zimene iye adaona وَلَقَدۡ رَءَاهُ نَزۡلَةً أُخۡرَىٰ ١٣Ndithudi iye adamuona iye pamene anali kutsika kachiwiri عِندَ سِدۡرَةِ ٱلۡمُنتَهَىٰ ١٤Pafupi ndi mtengo wa Sidrah عِندَهَا جَنَّةُ ٱلۡمَأۡوَىٰٓ ١٥Pafupi pake pali munda womwe ndi malo opumirako إِذۡ يَغۡشَى ٱلسِّدۡرَةَ مَا يَغۡشَىٰ ١٦Ndipo chimene chimaphimba chidakuta mtengo wa Sidrah مَا زَاغَ ٱلۡبَصَرُ وَمَا طَغَىٰ ١٧Maso ake sadayang’ane kumbali kapena kupyola muyeso لَقَدۡ رَأَىٰ مِنۡ ءَايَٰتِ رَبِّهِ ٱلۡكُبۡرَىٰٓ ١٨Ndithudi iye adaona zizindikiro zazikulu kwambiri za Ambuye wake أَفَرَءَيۡتُمُ ٱللَّٰتَ وَٱلۡعُزَّىٰ ١٩Kodi inu maganiza za Lat ndi Uzza وَمَنَوٰةَ ٱلثَّالِثَةَ ٱلۡأُخۡرَىٰٓ ٢٠Ndi Manat wachitatu wamkazi أَلَكُمُ ٱلذَّكَرُ وَلَهُ ٱلۡأُنثَىٰ ٢١Kwa inu amuna ndipo kwa Iye akazi تِلۡكَ إِذًا قِسۡمَةٌ ضِيزَىٰٓ ٢٢Ndithudi kumeneku ndiko kugawa kosalungama إِنۡ هِيَ إِلَّآ أَسۡمَآءٌ سَمَّيۡتُمُوهَآ أَنتُمۡ وَءَابَآؤُكُم مَّآ أَنزَلَ ٱللَّهُ بِهَا مِن سُلۡطَٰنٍۚ إِن يَتَّبِعُونَ إِلَّا ٱلظَّنَّ وَمَا تَهۡوَى ٱلۡأَنفُسُۖ وَلَقَدۡ جَآءَهُم مِّن رَّبِّهِمُ ٱلۡهُدَىٰٓ ٢٣Awa ndi mayina chabe amene inu mwapeka, inu ndi atate anu, amene Mulungu sadakulamuleni ndi pang’ono pomwe. Iwo amangotsatira nkhani zakumva chabe zimene mitima yawo imafuna pamene, ndithudi, kwadza kale kwa iwo ulangizi wochokera kwa Ambuye wawo أَمۡ لِلۡإِنسَٰنِ مَا تَمَنَّىٰ ٢٤Kodi munthu angapeze zonse zimene amafuna فَلِلَّهِ ٱلۡأٓخِرَةُ وَٱلۡأُولَىٰ ٢٥Koma Mulungu ndiye Mwini moyo umene uli nkudza ndi moyo wakale ۞ وَكَم مِّن مَّلَكٍ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ لَا تُغۡنِي شَفَٰعَتُهُمۡ شَيۡـًٔا إِلَّا مِنۢ بَعۡدِ أَن يَأۡذَنَ ٱللَّهُ لِمَن يَشَآءُ وَيَرۡضَىٰٓ ٢٦Ndipo kuli angelo ambiri amene ali kumwamba amene kukhala pakati kwawo sikudzathandiza chilichonse kupatula pokhapo pamene Mulungu apereka chilolezo kwa amene Iye wamufuna ndi kukondweretsedwa naye إِنَّ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ لَيُسَمُّونَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ تَسۡمِيَةَ ٱلۡأُنثَىٰ ٢٧Ndithudi iwo amene sakhulupirira za m’moyo umene uli nkudza, amatcha angelo ndi mayina achikazi وَمَا لَهُم بِهِۦ مِنۡ عِلۡمٍۖ إِن يَتَّبِعُونَ إِلَّا ٱلظَّنَّۖ وَإِنَّ ٱلظَّنَّ لَا يُغۡنِي مِنَ ٱلۡحَقِّ شَيۡـًٔا ٢٨Pamene iwo sadziwa chilichonse cha izo. Iwo satsatira china chilichonse koma nkhani zabodza ndipo, ndithudi, nkhani zabodza si mlowam’malo wa choonadi فَأَعۡرِضۡ عَن مَّن تَوَلَّىٰ عَن ذِكۡرِنَا وَلَمۡ يُرِدۡ إِلَّا ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا ٢٩Motero mupewe wina aliyense amene salabadira chikumbutso chathu ndipo safuna china chilichonse koma moyo wa padziko lino lapansi ذَٰلِكَ مَبۡلَغُهُم مِّنَ ٱلۡعِلۡمِۚ إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعۡلَمُ بِمَن ضَلَّ عَن سَبِيلِهِۦ وَهُوَ أَعۡلَمُ بِمَنِ ٱهۡتَدَىٰ ٣٠Uko ndiko kuchuluka kwa nzeru zawo. Ndithudi Ambuye wako ndiye amadziwa bwino onse amene amasochera ku njira yoyenera ndipo amadziwa kwambiri iye amene amatsata njira yoyenera وَلِلَّهِ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِ لِيَجۡزِيَ ٱلَّذِينَ أَسَٰٓـُٔواْ بِمَا عَمِلُواْ وَيَجۡزِيَ ٱلَّذِينَ أَحۡسَنُواْ بِٱلۡحُسۡنَى ٣١Ndipo Mulungu ndiye mwini wake wa chilichonse chimene chili kumwamba ndi dziko lapansi, ndipo akhoza kulanga onse amene amachita zoipa molingana ndi ntchito zawo ndiponso kuti akhoza kulipira onse amene amachita zabwino ndi mphotho yabwino kwambiri ٱلَّذِينَ يَجۡتَنِبُونَ كَبَٰٓئِرَ ٱلۡإِثۡمِ وَٱلۡفَوَٰحِشَ إِلَّا ٱللَّمَمَۚ إِنَّ رَبَّكَ وَٰسِعُ ٱلۡمَغۡفِرَةِۚ هُوَ أَعۡلَمُ بِكُمۡ إِذۡ أَنشَأَكُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ وَإِذۡ أَنتُمۡ أَجِنَّةٌ فِي بُطُونِ أُمَّهَٰتِكُمۡۖ فَلَا تُزَكُّوٓاْ أَنفُسَكُمۡۖ هُوَ أَعۡلَمُ بِمَنِ ٱتَّقَىٰٓ ٣٢Iwo amene amapewa machimo a akuluakulu ndi chigololo kupatula machimo a ang’onoang’ono, ndithudi, Ambuye wako ndi Mwini chikhululukiro. Iye amakudziwani bwino pamene amakulengani kuchokera ku dothi ndi pamene mukutidwa m’mimba mwa amayi anu. Motero musadziyeretse nokha. Al Najm 567 Iye amadziwa bwino kwambiri aliyense amene amalewa zoipa أَفَرَءَيۡتَ ٱلَّذِي تَوَلَّىٰ ٣٣Kodi iwe wamuona amene amabwerera m’mbuyo وَأَعۡطَىٰ قَلِيلًا وَأَكۡدَىٰٓ ٣٤Amene adapereka pang’ono ndipo anasiya kupereka أَعِندَهُۥ عِلۡمُ ٱلۡغَيۡبِ فَهُوَ يَرَىٰٓ ٣٥Kodi iye amadziwa za zinthu zobisika kuti akhoza kuziona أَمۡ لَمۡ يُنَبَّأۡ بِمَا فِي صُحُفِ مُوسَىٰ ٣٦Kodi kapena iye sadauzidwe za mawu amene ali m’mabuku a Mose وَإِبۡرَٰهِيمَ ٱلَّذِي وَفَّىٰٓ ٣٧Ndiponso za Abrahamu amene adakwaniritsa malamulo أَلَّا تَزِرُ وَازِرَةٌ وِزۡرَ أُخۡرَىٰ ٣٨Kuti palibe munthu amene adzasenza katundu wa mnzake وَأَن لَّيۡسَ لِلۡإِنسَٰنِ إِلَّا مَا سَعَىٰ ٣٩Ndipo kuti munthu sadzapeza chilichonse kupatula chimene wachigwirira ntchito وَأَنَّ سَعۡيَهُۥ سَوۡفَ يُرَىٰ ٤٠Ndipo kuti ntchito zake zidzaoneka ثُمَّ يُجۡزَىٰهُ ٱلۡجَزَآءَ ٱلۡأَوۡفَىٰ ٤١Pamenepo iye adzalipidwa malipiro ake oyenera وَأَنَّ إِلَىٰ رَبِّكَ ٱلۡمُنتَهَىٰ ٤٢Ndipo kuti kwa Ambuye wanu ndi kumene nonse mudzapita وَأَنَّهُۥ هُوَ أَضۡحَكَ وَأَبۡكَىٰ ٤٣Ndipo kuti Ndiye amene amawachititsa anthu kuseka ndi kuwaliritsa وَأَنَّهُۥ هُوَ أَمَاتَ وَأَحۡيَا ٤٤Ndipo kuti Ndiye amene amapereka imfa ndi moyo وَأَنَّهُۥ خَلَقَ ٱلزَّوۡجَيۡنِ ٱلذَّكَرَ وَٱلۡأُنثَىٰ ٤٥Ndiponso kuti Iye adalenga zinthu ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi مِن نُّطۡفَةٍ إِذَا تُمۡنَىٰ ٤٦Kuchokera ku madontho a umuna umene umatuluka وَأَنَّ عَلَيۡهِ ٱلنَّشۡأَةَ ٱلۡأُخۡرَىٰ ٤٧Ndipo kuti kwa Iye kuli chilengedwe chachiwiri وَأَنَّهُۥ هُوَ أَغۡنَىٰ وَأَقۡنَىٰ ٤٨Ndipo kuti Ndiye amene amapereka chuma ndi chisangalalo وَأَنَّهُۥ هُوَ رَبُّ ٱلشِّعۡرَىٰ ٤٩Ndipo kuti Iye ndiye Ambuye wa nyenyezi yamphamvu yotchedwa Sirius وَأَنَّهُۥٓ أَهۡلَكَ عَادًا ٱلۡأُولَىٰ ٥٠Kuti ndiye amene adaononga anthu akale a mphamvu kwambiri a mtundu wa a Aad kale وَثَمُودَاْ فَمَآ أَبۡقَىٰ ٥١Ndi anthu a mtundu wa a Thamoud. Ndipo Iye sadasiye wina aliyense وَقَوۡمَ نُوحٍ مِّن قَبۡلُۖ إِنَّهُمۡ كَانُواْ هُمۡ أَظۡلَمَ وَأَطۡغَىٰ ٥٢Ndi anthu a Nowa amakedzana ndithudi iwo adali osalungama ndi oswa malamulo mwamwano وَٱلۡمُؤۡتَفِكَةَ أَهۡوَىٰ ٥٣Ndipo iye adaononga mizinda yomwe idali yogonjetsedwa فَغَشَّىٰهَا مَا غَشَّىٰ ٥٤Kotero iwo adawavundikira nd chimene chidawavundikira فَبِأَيِّ ءَالَآءِ رَبِّكَ تَتَمَارَىٰ ٥٥Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wako zimene udzazikayikira هَٰذَا نَذِيرٌ مِّنَ ٱلنُّذُرِ ٱلۡأُولَىٰٓ ٥٦Uyu ndi mchenjezi wotsatizana ndi achenjezi a makedzana أَزِفَتِ ٱلۡأٓزِفَةُ ٥٧Tsiku louka kwa akufa lili pafupi لَيۡسَ لَهَا مِن دُونِ ٱللَّهِ كَاشِفَةٌ ٥٨Palibe wina kupatula Mulungu amene akhoza kulipherera أَفَمِنۡ هَٰذَا ٱلۡحَدِيثِ تَعۡجَبُونَ ٥٩Kodi inu mulikudabwa pa zimene zili kulakatulidwa وَتَضۡحَكُونَ وَلَا تَبۡكُونَ ٦٠Ndipo inu muli kuseka m’malo mwakulira وَأَنتُمۡ سَٰمِدُونَ ٦١Ndi kumapitirizabe kuchita zinthu zopanda pake فَٱسۡجُدُواْۤ لِلَّهِۤ وَٱعۡبُدُواْ ۩ ٦٢Motero gunditsani nkhope zanu pansi ndipo pembedzani Mulungu mmodzi yekha

الترجمة: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.