بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
ٱقۡتَرَبَتِ ٱلسَّاعَةُ وَٱنشَقَّ ٱلۡقَمَرُ ١Ola lachiweruzo lili pafupi ndipo mwezi wagawanika pakati وَإِن يَرَوۡاْ ءَايَةً يُعۡرِضُواْ وَيَقُولُواْ سِحۡرٌ مُّسۡتَمِرٌّ ٢Koma iwo akaona chozizwitsa, sakhulupirira ndipo amati, “Ichi sichina ayi koma matsenga ozama.” وَكَذَّبُواْ وَٱتَّبَعُوٓاْ أَهۡوَآءَهُمۡۚ وَكُلُّ أَمۡرٍ مُّسۡتَقِرٌّ ٣Iwo amakana choonadi koma amatsatira zilakolako zawo. Koma chinthu chilichonse chili ndi kumaliza kwake وَلَقَدۡ جَآءَهُم مِّنَ ٱلۡأَنۢبَآءِ مَا فِيهِ مُزۡدَجَرٌ ٤Ndithudi uthenga waperekedwa kale kwa iwo umene uli ndi chenjezo حِكۡمَةُۢ بَٰلِغَةٌۖ فَمَا تُغۡنِ ٱلنُّذُرُ ٥Wodzadzidwa ndi nzeru koma machenjezo ake sawathandiza iwo china chilichonse فَتَوَلَّ عَنۡهُمۡۘ يَوۡمَ يَدۡعُ ٱلدَّاعِ إِلَىٰ شَيۡءٍ نُّكُرٍ ٦Kotero iwe, asiye okha. Patsiku limene woitana adzawaitana kudza ku chinthu choopsa خُشَّعًا أَبۡصَٰرُهُمۡ يَخۡرُجُونَ مِنَ ٱلۡأَجۡدَاثِ كَأَنَّهُمۡ جَرَادٌ مُّنتَشِرٌ ٧Iwo adzadza kumeneko ndi nkhope zogwa pansi, kuchokera kumanda awo monga dzombe louluka ponseponse مُّهۡطِعِينَ إِلَى ٱلدَّاعِۖ يَقُولُ ٱلۡكَٰفِرُونَ هَٰذَا يَوۡمٌ عَسِرٌ ٨Adzadza mofulumira kwa oitana anthu osakhulupirira adzati, “Ili ndi tsiku lovuta kwambiri.” ۞ كَذَّبَتۡ قَبۡلَهُمۡ قَوۡمُ نُوحٍ فَكَذَّبُواْ عَبۡدَنَا وَقَالُواْ مَجۡنُونٌ وَٱزۡدُجِرَ ٩Asanadze iwo, anthu a Nowa adakana kapolo wathu ndipo adati, “Uyu ndi munthu wamisala.” Ndipo iwo adamuthamangitsa iye ndi kumunyoza kwambiri فَدَعَا رَبَّهُۥٓ أَنِّي مَغۡلُوبٌ فَٱنتَصِرۡ ١٠Ndipo iye adadandaula kwa Ambuye wake nati, “Ndagonjetsedwa kotero idzani kuti mundithandize.” فَفَتَحۡنَآ أَبۡوَٰبَ ٱلسَّمَآءِ بِمَآءٍ مُّنۡهَمِرٍ ١١Motero Ife tidatsekula makomo a kumwamba, ndipo mvula idagwa nthawi yomweyo وَفَجَّرۡنَا ٱلۡأَرۡضَ عُيُونًا فَٱلۡتَقَى ٱلۡمَآءُ عَلَىٰٓ أَمۡرٍ قَدۡ قُدِرَ ١٢Ndipo tidatumphutsa a kasupe padziko lapansi kotero madzi onse adakumana monga mwa lamulo lathu وَحَمَلۡنَٰهُ عَلَىٰ ذَاتِ أَلۡوَٰحٍ وَدُسُرٍ ١٣Ndipo tidamunyamula iye m’chombo chopangidwandimatabwandichokhomedwandimisomali تَجۡرِي بِأَعۡيُنِنَا جَزَآءً لِّمَن كَانَ كُفِرَ ١٤Chidanyamuka potsogozedwa ndi Ife. Mphotho kwa iye amene adakanidwa وَلَقَد تَّرَكۡنَٰهَآ ءَايَةً فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٍ ١٥Ndithudi tidachisiya icho ngati chizindikiro koma kodi alipo ena amene adzachenjezedwa فَكَيۡفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ ١٦Kodi chilango changa ndi chenjezo langa zidali zalikulu bwanji وَلَقَدۡ يَسَّرۡنَا ٱلۡقُرۡءَانَ لِلذِّكۡرِ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٍ ١٧Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulidziwa ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa كَذَّبَتۡ عَادٌ فَكَيۡفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ ١٨Anthu a Aad adakana. Kodi chilango changa ndi chenjezo langa zidali zoopsa bwanji إِنَّآ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ رِيحًا صَرۡصَرًا فِي يَوۡمِ نَحۡسٍ مُّسۡتَمِرٍّ ١٩Ndithudi Ife tidatumiza mphepo yamkhuntho pa tsiku latsoka losasimbika تَنزِعُ ٱلنَّاسَ كَأَنَّهُمۡ أَعۡجَازُ نَخۡلٍ مُّنقَعِرٍ ٢٠Kugwetsa anthu ngati kuti adali mathunthu a mitengo ya mgwalangwa yozulidwa فَكَيۡفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ ٢١Kodi chilango changa ndipo chenjezo langa zidali zoopsa bwanji وَلَقَدۡ يَسَّرۡنَا ٱلۡقُرۡءَانَ لِلذِّكۡرِ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٍ ٢٢Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa كَذَّبَتۡ ثَمُودُ بِٱلنُّذُرِ ٢٣Anthu a Thamoud adakana machenjezo فَقَالُوٓاْ أَبَشَرًا مِّنَّا وَٰحِدًا نَّتَّبِعُهُۥٓ إِنَّآ إِذًا لَّفِي ضَلَٰلٍ وَسُعُرٍ ٢٤Iwo adati, “Munthu! Mmodzi yekha wochokera ku mtundu wathu kuti timutsatire? Ndithudi ife tikhala olakwa kwambiri ndiponso a misala.” أَءُلۡقِيَ ٱلذِّكۡرُ عَلَيۡهِ مِنۢ بَيۡنِنَا بَلۡ هُوَ كَذَّابٌ أَشِرٌ ٢٥“Kodi ndiye kuti uthenga waperekedwa kwa iye yekha pakati pa ife tonse? Iyayi! Iye ndi wabodza ndi wodzikweza.” سَيَعۡلَمُونَ غَدًا مَّنِ ٱلۡكَذَّابُ ٱلۡأَشِرُ ٢٦Mawa iwo adzadziwa kuti wabodza ndi wodzikweza ndani إِنَّا مُرۡسِلُواْ ٱلنَّاقَةِ فِتۡنَةً لَّهُمۡ فَٱرۡتَقِبۡهُمۡ وَٱصۡطَبِرۡ ٢٧Ndithudi Ife titumiza ngamira yaikazi ngati mayesero kwa iwo. Motero iwe uwapenyetsetse ndipo ukhale wopirira وَنَبِّئۡهُمۡ أَنَّ ٱلۡمَآءَ قِسۡمَةُۢ بَيۡنَهُمۡۖ كُلُّ شِرۡبٍ مُّحۡتَضَرٌ ٢٨Ndipo uwauze kuti azigawana madzi. Ndipo nthawi yomwera madzi idzakhazikitsidwa فَنَادَوۡاْ صَاحِبَهُمۡ فَتَعَاطَىٰ فَعَقَرَ ٢٩Ndipo iwo adaitana m’bale wawo ndipo iye adatulutsa lupanga ndi kuipha فَكَيۡفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ ٣٠Kodi chilango changa ndi chenjezo langa zidali zoopsa bwanji إِنَّآ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ صَيۡحَةً وَٰحِدَةً فَكَانُواْ كَهَشِيمِ ٱلۡمُحۡتَظِرِ ٣١Ndithudi tidawatumizira mfuwu umodzi ndipo onse adali ngati nkhuni zodula zimene munthu womanga mpanda amatola وَلَقَدۡ يَسَّرۡنَا ٱلۡقُرۡءَانَ لِلذِّكۡرِ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٍ ٣٢Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Koma kodi alipo ena amene adzachenjezedwa كَذَّبَتۡ قَوۡمُ لُوطِۭ بِٱلنُّذُرِ ٣٣Anthu a Loti adati chenjezo lathu ndi labodza إِنَّآ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ حَاصِبًا إِلَّآ ءَالَ لُوطٍۖ نَّجَّيۡنَٰهُم بِسَحَرٍ ٣٤Ndithudi Ife tidawatumizira mphepo yonyamula miyala kupatula a pa banja la Loti amene tidawapulumutsa mu ola lomaliza la usiku نِّعۡمَةً مِّنۡ عِندِنَاۚ كَذَٰلِكَ نَجۡزِي مَن شَكَرَ ٣٥Monga chisomo chochokera kwa Ife, motero ndi mmene timalipirira anthu oyamika وَلَقَدۡ أَنذَرَهُم بَطۡشَتَنَا فَتَمَارَوۡاْ بِٱلنُّذُرِ ٣٦Ndithudi iye adawachenjeza za chilango chathu choopsa koma iwo adakana chenjezo lathu وَلَقَدۡ رَٰوَدُوهُ عَن ضَيۡفِهِۦ فَطَمَسۡنَآ أَعۡيُنَهُمۡ فَذُوقُواْ عَذَابِي وَنُذُرِ ٣٧Ndipo, ndithudi, iwo adafuna kuchititsa manyazi alendo ake. Motero Ife tidawachititsa khungu. Kotero inu lawani chilango changa ndi machenjezo anga وَلَقَدۡ صَبَّحَهُم بُكۡرَةً عَذَابٌ مُّسۡتَقِرٌّ ٣٨Ndithudi chilango chowawa chidadza pa iwo nthawi yam’mawa فَذُوقُواْ عَذَابِي وَنُذُرِ ٣٩Kotero inu lawani chilango changa ndi machenjezo anga وَلَقَدۡ يَسَّرۡنَا ٱلۡقُرۡءَانَ لِلذِّكۡرِ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٍ ٤٠Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa وَلَقَدۡ جَآءَ ءَالَ فِرۡعَوۡنَ ٱلنُّذُرُ ٤١Ndipo, ndithudi, machenjezo adadza kwa anthu a Farawo كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا كُلِّهَا فَأَخَذۡنَٰهُمۡ أَخۡذَ عَزِيزٍ مُّقۡتَدِرٍ ٤٢Iwo adati machenjezo athu onse ndi abodza motero tidawaononga ndi chilango champhamvu yochuluka أَكُفَّارُكُمۡ خَيۡرٌ مِّنۡ أُوْلَٰٓئِكُمۡ أَمۡ لَكُم بَرَآءَةٌ فِي ٱلزُّبُرِ ٤٣Kodi anthu anu osakhulupirira ndi abwino kuposa awa? Kapena inu muli ndi chitetezo mu m’mawu a Mulungu أَمۡ يَقُولُونَ نَحۡنُ جَمِيعٌ مُّنتَصِرٌ ٤٤Kodi kapena iwo amati, “Ife ndife ambiri ndipo tidzapambana?” سَيُهۡزَمُ ٱلۡجَمۡعُ وَيُوَلُّونَ ٱلدُّبُرَ ٤٥Tsopano magulu awo ali kupirikitsidwa ndipo iwo ali kuthawa بَلِ ٱلسَّاعَةُ مَوۡعِدُهُمۡ وَٱلسَّاعَةُ أَدۡهَىٰ وَأَمَرُّ ٤٦Iyayi, koma ola lachiweruzo ndi nthawi imene iwo adalonjezedwa ndipo ola limeneli lidzakhala loopsa kwambiri إِنَّ ٱلۡمُجۡرِمِينَ فِي ضَلَٰلٍ وَسُعُرٍ ٤٧Ndithudi anthu osakhulupirira ndi olakwa adzapsya يَوۡمَ يُسۡحَبُونَ فِي ٱلنَّارِ عَلَىٰ وُجُوهِهِمۡ ذُوقُواْ مَسَّ سَقَرَ ٤٨Tsiku limene iwo adzaduduluzidwa pa nkhope zawo kunka ku moto, (zidzanenedwa) “Lawani ululu wa ku Moto.” إِنَّا كُلَّ شَيۡءٍ خَلَقۡنَٰهُ بِقَدَرٍ ٤٩Ndithudi tidalenga chilichonse molingana ndi muyeso wake وَمَآ أَمۡرُنَآ إِلَّا وَٰحِدَةٌ كَلَمۡحِۭ بِٱلۡبَصَرِ ٥٠Ndipo ulamuliro wathu ndi umodzi monga kuphenira kwa diso وَلَقَدۡ أَهۡلَكۡنَآ أَشۡيَاعَكُمۡ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٍ ٥١Ndithudi Ife tidaononga kale anthu onga inu koma kodi alipo amene anga chenjezedwe وَكُلُّ شَيۡءٍ فَعَلُوهُ فِي ٱلزُّبُرِ ٥٢Ndipo zonse zimene adachita zidalembedwa وَكُلُّ صَغِيرٍ وَكَبِيرٍ مُّسۡتَطَرٌ ٥٣Ndipo chilichonse chaching’ono ndi chachikulu chidalembedwa kale إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي جَنَّٰتٍ وَنَهَرٍ ٥٤Ndithudi onse amene amalewa zoipa adzakhala m’kati mwa minda ndi mitsinje فِي مَقۡعَدِ صِدۡقٍ عِندَ مَلِيكٍ مُّقۡتَدِرِۭ ٥٥Ku Paradiso kufupi ndi Mfumu yamphamvu zonse