ملة الإسلام

السورة 27 · 93 آية · Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

سورة النمل باللغة الشيشيوا

السورة بالعربية مع التفسير استمع إلى سورة النمل (1,258 قارئاً)
مكيةسورة النمل٩٣ آية

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

طسٓۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡقُرۡءَانِ وَكِتَابٍ مُّبِينٍ ١Ichi ndi chivumbulutso cha Korani, Buku lofotokoza bwino هُدًى وَبُشۡرَىٰ لِلۡمُؤۡمِنِينَ ٢Malangizo ndi nkhani yosangalatsa kwa anthu okhulupirira ٱلَّذِينَ يُقِيمُونَ ٱلصَّلَوٰةَ وَيُؤۡتُونَ ٱلزَّكَوٰةَ وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ يُوقِنُونَ ٣Amene amapitiriza kupemphera ndipo amapereka msonkho wothandiza anthu osauka ndiponso amakhulupirira kwambiri m’moyo umene uli nkudza إِنَّ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ زَيَّنَّا لَهُمۡ أَعۡمَٰلَهُمۡ فَهُمۡ يَعۡمَهُونَ ٤Ndithudi iwo ndi amene amakana za moyo umene uli nkudza. Ife tazipanga ntchito zawo kuti zioneke ngati zabwino motero iwo amayenda mwakhungu أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ لَهُمۡ سُوٓءُ ٱلۡعَذَابِ وَهُمۡ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ هُمُ ٱلۡأَخۡسَرُونَ ٥Iwo adzalangidwa koposa. Ndipo m’moyo umene uli nkudza, iwo sadzapindula china chilichonse وَإِنَّكَ لَتُلَقَّى ٱلۡقُرۡءَانَ مِن لَّدُنۡ حَكِيمٍ عَلِيمٍ ٦Ndithudi iwe walandira Korani kuchokera kwa Iye amene ali ndi nzeru ndipo amadziwa chilichonse إِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِأَهۡلِهِۦٓ إِنِّيٓ ءَانَسۡتُ نَارًا سَـَٔاتِيكُم مِّنۡهَا بِخَبَرٍ أَوۡ ءَاتِيكُم بِشِهَابٍ قَبَسٍ لَّعَلَّكُمۡ تَصۡطَلُونَ ٧Pamenepo Mose adauza banja lake kuti, “Ine ndili kuona moto. Ine posachedwapa ndikubweretserani nkhani kapena khala la moto kuti mukhoza kuotha.” فَلَمَّا جَآءَهَا نُودِيَ أَنۢ بُورِكَ مَن فِي ٱلنَّارِ وَمَنۡ حَوۡلَهَا وَسُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٨Ndipo pamene iye adafika pamoto paja, mawu adamveka akunena naye kuti, “odalitsidwa ndiye amene ali mu moto uwu ndiponso alionse a pamalo pozungulira. Ulemerero ukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwe zonse.” يَٰمُوسَىٰٓ إِنَّهُۥٓ أَنَا ٱللَّهُ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ ٩“Mose! Ine ndine Mulungu, Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse.” وَأَلۡقِ عَصَاكَۚ فَلَمَّا رَءَاهَا تَهۡتَزُّ كَأَنَّهَا جَآنٌّ وَلَّىٰ مُدۡبِرًا وَلَمۡ يُعَقِّبۡۚ يَٰمُوسَىٰ لَا تَخَفۡ إِنِّي لَا يَخَافُ لَدَيَّ ٱلۡمُرۡسَلُونَ ١٠“Ponya ndodo yako pansi.” Ndipo pamene iye adaona kuti ilikuyenda ngati njoka, adatembenuka ndi kuthawa ndipo sadayang’ane m’mbuyo. “Iwe Mose!” Atumwi anga sachita mantha pamene ali ndi Ine إِلَّا مَن ظَلَمَ ثُمَّ بَدَّلَ حُسۡنَۢا بَعۡدَ سُوٓءٍ فَإِنِّي غَفُورٌ رَّحِيمٌ ١١Akakhala iwo amene amalakwa ndipo amachita zabwino pambuyo pochita zoipa Ine ndine wokhululukira ndiponso wachisoni chosatha وَأَدۡخِلۡ يَدَكَ فِي جَيۡبِكَ تَخۡرُجۡ بَيۡضَآءَ مِنۡ غَيۡرِ سُوٓءٍۖ فِي تِسۡعِ ءَايَٰتٍ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَقَوۡمِهِۦٓۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمًا فَٰسِقِينَ ١٢“Pisa dzanja m’thumba mwako. Litulutse lili loyera ngakhale kuti siudapweteke. Ichi ndi chimodzi cha zizindikiro zisanu ndi zinayi zimene zidzaonetsedwa kwa Farawo ndi anthu ake. Ndithudi iwo ndi anthu ochimwa kwambiri.” فَلَمَّا جَآءَتۡهُمۡ ءَايَٰتُنَا مُبۡصِرَةً قَالُواْ هَٰذَا سِحۡرٌ مُّبِينٌ ١٣Pamene zizindikiro zathu zooneka bwino zinaonetsedwa kwa iwo, iwo adati, “Uwu ndiwo ufiti weniweni.” وَجَحَدُواْ بِهَا وَٱسۡتَيۡقَنَتۡهَآ أَنفُسُهُمۡ ظُلۡمًا وَعُلُوًّاۚ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُفۡسِدِينَ ١٤Mitima yawo idadziwa kuti zizindikiro zidali zoona koma adazikana izo chifukwa chakulakwa ndiponso kunyada kwawo. Taona zimene zidawaonekera anthu olakwa وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا دَاوُۥدَ وَسُلَيۡمَٰنَ عِلۡمًاۖ وَقَالَا ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي فَضَّلَنَا عَلَىٰ كَثِيرٍ مِّنۡ عِبَادِهِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ١٥Ndithudi Ife tidapereka nzeru kwa Davide ndi Solomoni. Iwo adati, “Kuyamikidwa ndi kwa Iye amene watikweza ife kukhala pamwamba pa akapolo ake ambiri okhulupirira.” وَوَرِثَ سُلَيۡمَٰنُ دَاوُۥدَۖ وَقَالَ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ عُلِّمۡنَا مَنطِقَ ٱلطَّيۡرِ وَأُوتِينَا مِن كُلِّ شَيۡءٍۖ إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ ٱلۡفَضۡلُ ٱلۡمُبِينُ ١٦Solomoniadalowam’malomwaDavide.Iye adati, “Oh inu anthu anga! Ife taphunzitsidwa chiyankhulo cha mbalame ndipo tapatsidwa zinthu zabwino zambiri. Ndithudi ichi ndi chifundo choonekeratu.” وَحُشِرَ لِسُلَيۡمَٰنَ جُنُودُهُۥ مِنَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِ وَٱلطَّيۡرِ فَهُمۡ يُوزَعُونَ ١٧Asirikali a nkhondo a mtundu wa majini, anthu ena ndi mbalame anasonkhanitsidwa pamaso pa Solomoni ndipo adaimitsidwa pa mizere m’magulu osiyanasiyana mogwirizana ndi maudindo حَتَّىٰٓ إِذَآ أَتَوۡاْ عَلَىٰ وَادِ ٱلنَّمۡلِ قَالَتۡ نَمۡلَةٌ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّمۡلُ ٱدۡخُلُواْ مَسَٰكِنَكُمۡ لَا يَحۡطِمَنَّكُمۡ سُلَيۡمَٰنُ وَجُنُودُهُۥ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ ١٨Mpaka pamene iwo anafika pa chigwa cha nyerere, nyerere ina idati, “Oh inu nyerere! Lowani ku maenje anu chifukwa mwina Solomoni pamodzi ndi Asirikali ake, akhoza kukuonongani mosadziwa.” فَتَبَسَّمَ ضَاحِكًا مِّن قَوۡلِهَا وَقَالَ رَبِّ أَوۡزِعۡنِيٓ أَنۡ أَشۡكُرَ نِعۡمَتَكَ ٱلَّتِيٓ أَنۡعَمۡتَ عَلَيَّ وَعَلَىٰ وَٰلِدَيَّ وَأَنۡ أَعۡمَلَ صَٰلِحًا تَرۡضَىٰهُ وَأَدۡخِلۡنِي بِرَحۡمَتِكَ فِي عِبَادِكَ ٱلصَّٰلِحِينَ ١٩Solomoni adamwetulira posangalatsidwa ndi mawu ake ndipo iye adati, “Ndilangizeni Ambuye kuti ndizikuthokozani pa zabwino zonse zimene mwandipatsa ine ndi makolo anga ndiponso kuti ndizichita ntchito zabwino zimene zimakukondweretsani inu. Ndilowetseni ine ku Paradiso kudzera m’chisomo chanu, kuti ndikhale pakati pa akapolo anu angwiro.” وَتَفَقَّدَ ٱلطَّيۡرَ فَقَالَ مَالِيَ لَآ أَرَى ٱلۡهُدۡهُدَ أَمۡ كَانَ مِنَ ٱلۡغَآئِبِينَ ٢٠Iye adayendera mbalame nati, “Kodi mbalame yotchedwa mnthengu ili kuti? Kodi kapena iyo ili pamodzi ndi amene sadabwere?” لَأُعَذِّبَنَّهُۥ عَذَابًا شَدِيدًا أَوۡ لَأَاْذۡبَحَنَّهُۥٓ أَوۡ لَيَأۡتِيَنِّي بِسُلۡطَٰنٍ مُّبِينٍ ٢١“Ndithudi ndidzailanga iyo ndi chilango chowawa kapena ndidzaipha kupatula ngati ibweretsa kwa ine chifukwa chomveka.” فَمَكَثَ غَيۡرَ بَعِيدٍ فَقَالَ أَحَطتُ بِمَا لَمۡ تُحِطۡ بِهِۦ وَجِئۡتُكَ مِن سَبَإِۭ بِنَبَإٍ يَقِينٍ ٢٢Ndipo mbalame ya mnthengu siidachedwe ndipo idati, “Ndadziwa zimene iwe siudziwa ndipo ndikubweretsera nkhani yoona kuchokera ku Saba.” إِنِّي وَجَدتُّ ٱمۡرَأَةً تَمۡلِكُهُمۡ وَأُوتِيَتۡ مِن كُلِّ شَيۡءٍ وَلَهَا عَرۡشٌ عَظِيمٌ ٢٣“Ine ndapeza munthu wamkazi akulamulira iwo ndipo iye wapatsidwa zinthu zonse zomuyenereza ndipo ali ndi Mpando waukulu wachifumu وَجَدتُّهَا وَقَوۡمَهَا يَسۡجُدُونَ لِلشَّمۡسِ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَزَيَّنَ لَهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ أَعۡمَٰلَهُمۡ فَصَدَّهُمۡ عَنِ ٱلسَّبِيلِ فَهُمۡ لَا يَهۡتَدُونَ ٢٤Ndidamupeza iye pamodzi ndi anthu ake ali kupembedza dzuwa moonjezera pa Mulungu ndipo Satana wawakongoletsera ntchito zawo zoipa ndipo wawasocheretsakunjirayoyenerandipoiwosiotsogozedwa bwino.” أَلَّاۤ يَسۡجُدُواْۤ لِلَّهِ ٱلَّذِي يُخۡرِجُ ٱلۡخَبۡءَ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَيَعۡلَمُ مَا تُخۡفُونَ وَمَا تُعۡلِنُونَ ٢٥Ndi kuti sapembedza Mulungu amene amaulula zobisika za kumwamba ndi pa dziko lapansi ndipo Iye amadziwa zimene inu mumabisa ndi zimene mumaulula ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ رَبُّ ٱلۡعَرۡشِ ٱلۡعَظِيمِ ۩ ٢٦Mulungu! Kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Ambuye wa mpando wa Chifumu ۞ قَالَ سَنَنظُرُ أَصَدَقۡتَ أَمۡ كُنتَ مِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ ٢٧Solomoni adati, “Tidzaona posachedwapa ngati zimene ukunena ndi zoona kapena zabodza.” ٱذۡهَب بِّكِتَٰبِي هَٰذَا فَأَلۡقِهۡ إِلَيۡهِمۡ ثُمَّ تَوَلَّ عَنۡهُمۡ فَٱنظُرۡ مَاذَا يَرۡجِعُونَ ٢٨“Pita ukapereke kalata yangayi kwa iwo ndipo ukachoke pang’ono poyembekezera yankho lawo.” قَالَتۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمَلَؤُاْ إِنِّيٓ أُلۡقِيَ إِلَيَّ كِتَٰبٌ كَرِيمٌ ٢٩Mfumukazi ya ku Saba adati, “Oh inu nduna zanga! Ine ndalandira kalata yolemekezeka.” إِنَّهُۥ مِن سُلَيۡمَٰنَ وَإِنَّهُۥ بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ ٣٠Kalatayi ndi yochokera kwa Solomoni ndipo ikuti, “M’dzina la Mulungu, Mwini chifundo ndi Mwini chisoni chosatha.” أَلَّا تَعۡلُواْ عَلَيَّ وَأۡتُونِي مُسۡلِمِينَ ٣١“Usadzikweze kwa ine koma bwerani nonse kwa ine modzipereka.” قَالَتۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمَلَؤُاْ أَفۡتُونِي فِيٓ أَمۡرِي مَا كُنتُ قَاطِعَةً أَمۡرًا حَتَّىٰ تَشۡهَدُونِ ٣٢Iye adati, “oh inu mafumu! Ndipatseni chilangizo chokhudza nkhani iyi ndipo sindilamula china chilichonse pokhapokha inu mutakhalapo.” قَالُواْ نَحۡنُ أُوْلُواْ قُوَّةٍ وَأُوْلُواْ بَأۡسٍ شَدِيدٍ وَٱلۡأَمۡرُ إِلَيۡكِ فَٱنظُرِي مَاذَا تَأۡمُرِينَ ٣٣Iwo adati, “Ife ndife olimba mtima ndiponso odziwa kumenya nkhondo molimba, ndipo nkhani ili kwa iwe. Ndipo udziwe mmene ungalamulire.” قَالَتۡ إِنَّ ٱلۡمُلُوكَ إِذَا دَخَلُواْ قَرۡيَةً أَفۡسَدُوهَا وَجَعَلُوٓاْ أَعِزَّةَ أَهۡلِهَآ أَذِلَّةًۚ وَكَذَٰلِكَ يَفۡعَلُونَ ٣٤Iye adati, “Ndithudi mafumu akalowa mu mzinda amaononga mwaupandu ndi kuwasandutsa anthu olemekezeka kukhala onyozeka. Umo ndi mmene iwo amachitira.” وَإِنِّي مُرۡسِلَةٌ إِلَيۡهِم بِهَدِيَّةٍ فَنَاظِرَةُۢ بِمَ يَرۡجِعُ ٱلۡمُرۡسَلُونَ ٣٥“Koma ine ndiwatumizira mphatso ndipo ndidzaona yankho limene a Kazembe anga adzabwere nalo.” فَلَمَّا جَآءَ سُلَيۡمَٰنَ قَالَ أَتُمِدُّونَنِ بِمَالٍ فَمَآ ءَاتَىٰنِۦَ ٱللَّهُ خَيۡرٌ مِّمَّآ ءَاتَىٰكُمۚ بَلۡ أَنتُم بِهَدِيَّتِكُمۡ تَفۡرَحُونَ ٣٦Ndipo pamene akazembe adadza kwa Solomoni, iye adati, “Kodi muli kundipatsa chuma chambiri? Icho chimene Mulungu wandipatsa ine ndi chabwino kuposa chuma chonse chimene wakupatsani inu. Koma inu mumasangalala ndi mphatso zanu.” ٱرۡجِعۡ إِلَيۡهِمۡ فَلَنَأۡتِيَنَّهُم بِجُنُودٍ لَّا قِبَلَ لَهُم بِهَا وَلَنُخۡرِجَنَّهُم مِّنۡهَآ أَذِلَّةً وَهُمۡ صَٰغِرُونَ ٣٧“Bwererani kwa iwo. Ife tidzapita kwa iwo ndi magulu ankhondo amene iwo sangathe kuwagonjetsa ndipo tidzawathamangitsa m’dziko lawo mochititsa manyazi ndipo iwo adzanyozeka.” قَالَ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمَلَؤُاْ أَيُّكُمۡ يَأۡتِينِي بِعَرۡشِهَا قَبۡلَ أَن يَأۡتُونِي مُسۡلِمِينَ ٣٨Iye adati, “oh inu mafumu! Kodi ndani amene angandibweretsere mpando wake wachifumu iwo asanabwerekwainemogonja?” قَالَ عِفۡرِيتٌ مِّنَ ٱلۡجِنِّ أَنَا۠ ءَاتِيكَ بِهِۦ قَبۡلَ أَن تَقُومَ مِن مَّقَامِكَۖ وَإِنِّي عَلَيۡهِ لَقَوِيٌّ أَمِينٌ ٣٩Winawamphamvu, amene adalimmodziwamajiniadati,“Inendidzakubweretseraniinu musadanyamuke pa mpando wanu. Ine ndili ndi mphamvu zonyamulira mpando ndiponso ndine wokhulupirika.” قَالَ ٱلَّذِي عِندَهُۥ عِلۡمٌ مِّنَ ٱلۡكِتَٰبِ أَنَا۠ ءَاتِيكَ بِهِۦ قَبۡلَ أَن يَرۡتَدَّ إِلَيۡكَ طَرۡفُكَۚ فَلَمَّا رَءَاهُ مُسۡتَقِرًّا عِندَهُۥ قَالَ هَٰذَا مِن فَضۡلِ رَبِّي لِيَبۡلُوَنِيٓ ءَأَشۡكُرُ أَمۡ أَكۡفُرُۖ وَمَن شَكَرَ فَإِنَّمَا يَشۡكُرُ لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن كَفَرَ فَإِنَّ رَبِّي غَنِيٌّ كَرِيمٌ ٤٠Koma wina amene anali kudziwa Mawu a Mulungu adati “Ine ndidzakubweretserani msanga musadaphenire maso anu.” Ndipo pamene iye adaona kuti mpando wabwera kwa iye adati, “Ichi ndi chisomo cha Ambuye wanga kuti andiyese ngati ndikuthokoza kapena sindikuthokoza. Ndipo aliyense amene athokoza atero podzipezera yekha zabwino. Ndipo amene sathokoza ndithu, Ambuye wanga ali ndi zonse ndipo ndi Wolemekezeka.” قَالَ نَكِّرُواْ لَهَا عَرۡشَهَا نَنظُرۡ أَتَهۡتَدِيٓ أَمۡ تَكُونُ مِنَ ٱلَّذِينَ لَا يَهۡتَدُونَ ٤١Ndipo iye adati, “Sinthani mpando wake wachifumu kuti tione ngati iye akhoza kuuzindikira kapena ayi.” فَلَمَّا جَآءَتۡ قِيلَ أَهَٰكَذَا عَرۡشُكِۖ قَالَتۡ كَأَنَّهُۥ هُوَۚ وَأُوتِينَا ٱلۡعِلۡمَ مِن قَبۡلِهَا وَكُنَّا مُسۡلِمِينَ ٤٢Ndipo pamene mfumukazi inadza kwa Solomoni idafunsidwa kuti, “Kodi mpando wako wachifumu ndi otere?” Iye adati, “Ukukhala ngati umenewu” ndipo ife tinadziwa kale ndipo tagonja kwa Mulungu mwamtendere.” وَصَدَّهَا مَا كَانَت تَّعۡبُدُ مِن دُونِ ٱللَّهِۖ إِنَّهَا كَانَتۡ مِن قَوۡمٍ كَٰفِرِينَ ٤٣Zinthu zimene amapembedza zoonjezera pa Mulungu ndi zimene zamusokoneza. Iye adali mmodzi wa anthu osakhulupirira قِيلَ لَهَا ٱدۡخُلِي ٱلصَّرۡحَۖ فَلَمَّا رَأَتۡهُ حَسِبَتۡهُ لُجَّةً وَكَشَفَتۡ عَن سَاقَيۡهَاۚ قَالَ إِنَّهُۥ صَرۡحٌ مُّمَرَّدٌ مِّن قَوَارِيرَۗ قَالَتۡ رَبِّ إِنِّي ظَلَمۡتُ نَفۡسِي وَأَسۡلَمۡتُ مَعَ سُلَيۡمَٰنَ لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٤٤Iye adauzidwa kuti, “Lowa mnyumba yachifumu.” Ndipo pamene iye anaiona iyo, adaganiza kuti ndi dziwe la madzi ndipo miyendo yake adaionetsa poyera. Solomoni adati, “Iyi ndi nyumba yachifumu yomatidwa ndi magalasi.” Iye adati, “Ambuye, ine ndalakwira mzimu wanga. Tsopano ndili kudzipereka pamodzi ndi Solomoni kwa Mulungu, Ambuye wazolengedwa zonse.” وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَآ إِلَىٰ ثَمُودَ أَخَاهُمۡ صَٰلِحًا أَنِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ فَإِذَا هُمۡ فَرِيقَانِ يَخۡتَصِمُونَ ٤٥A Thamoud, ndithudi, tidawatumizira m’bale wawo Saleh, amene adati, “Muzipembedza Mulungu basi.” Koma iwo adagawikana m’magulu awiri okangana قَالَ يَٰقَوۡمِ لِمَ تَسۡتَعۡجِلُونَ بِٱلسَّيِّئَةِ قَبۡلَ ٱلۡحَسَنَةِۖ لَوۡلَا تَسۡتَغۡفِرُونَ ٱللَّهَ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ ٤٦Iye adati, “Anthu anga! Kodi bwanji mufuna kubweretsa choipa msanga musanabweretse chabwino? Nanga ndi chifukwa chiyani simupempha chikhululukiro kwa Mulungu kuti mukhoza kupeza chisomo chake?” قَالُواْ ٱطَّيَّرۡنَا بِكَ وَبِمَن مَّعَكَۚ قَالَ طَٰٓئِرُكُمۡ عِندَ ٱللَّهِۖ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٌ تُفۡتَنُونَ ٤٧Iwo adati, “Ife tili kuona choipa chochokera kwa iwe ndiponso kwa anthu amene amakutsatira iwe.” Iye adati, “Choipa chimene muli kuchiona chili kuchokera kwa Mulungu. Inu ndinu anthu amene muli kuyesedwa.” وَكَانَ فِي ٱلۡمَدِينَةِ تِسۡعَةُ رَهۡطٍ يُفۡسِدُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا يُصۡلِحُونَ ٤٨M’mizinda mwawo mudali anthu asanu ndi anayi amene anali kuchita zoipa mdziko ndipo samachita zabwino ayi قَالُواْ تَقَاسَمُواْ بِٱللَّهِ لَنُبَيِّتَنَّهُۥ وَأَهۡلَهُۥ ثُمَّ لَنَقُولَنَّ لِوَلِيِّهِۦ مَا شَهِدۡنَا مَهۡلِكَ أَهۡلِهِۦ وَإِنَّا لَصَٰدِقُونَ ٤٩Iwo adati, “Tiyeni tonse tilumbire, dzina la Mulungu, kuti timuphe nthawi ya usiku pamodzi ndi a pabanja lake lonse. Ndipo tidzawauza abale ake kuti, “Ife kudalibe pamene iwo anali kuphedwa. Ndipo zimene tili kunena ndi zoona zokhazokha.” وَمَكَرُواْ مَكۡرًا وَمَكَرۡنَا مَكۡرًا وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ ٥٠Iwo adachita chiwembu ndipo nafenso tidachita chiwembu iwo osadziwa chilichonse فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ مَكۡرِهِمۡ أَنَّا دَمَّرۡنَٰهُمۡ وَقَوۡمَهُمۡ أَجۡمَعِينَ ٥١Ndipo taona zotsatira zake za chiwembu chawo. Ife tidawaonongeratu pamodzi ndi anthu awo onse فَتِلۡكَ بُيُوتُهُمۡ خَاوِيَةَۢ بِمَا ظَلَمُوٓاْۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةً لِّقَوۡمٍ يَعۡلَمُونَ ٥٢Chifukwa chakuti iwo adalakwa, nyumba zawo zimene anali kukhalamo tsopano ndi mabwinja. Ndithudi m’zimenezi muli zizindikiro kwa anthu ozindikira وَأَنجَيۡنَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَكَانُواْ يَتَّقُونَ ٥٣Ndipo Ife tidapulumutsa anthu onse okhulupirira ndipo anali kuopa Mulungu وَلُوطًا إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِۦٓ أَتَأۡتُونَ ٱلۡفَٰحِشَةَ وَأَنتُمۡ تُبۡصِرُونَ ٥٤Loti kwa anthu ake, “Kodi inu mukuchita zinthu zochititsa manyazi pamene muli kuona?” أَئِنَّكُمۡ لَتَأۡتُونَ ٱلرِّجَالَ شَهۡوَةً مِّن دُونِ ٱلنِّسَآءِۚ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٌ تَجۡهَلُونَ ٥٥“Kodi inu muli kuchita chiwerewere ndi amuna anzanu pokwaniritsa zilakolako zanu ndi kusiya akazi? Inu ndinu mbuli basi.”

الجزء العشرون

۞ فَمَا كَانَ جَوَابَ قَوۡمِهِۦٓ إِلَّآ أَن قَالُوٓاْ أَخۡرِجُوٓاْ ءَالَ لُوطٍ مِّن قَرۡيَتِكُمۡۖ إِنَّهُمۡ أُنَاسٌ يَتَطَهَّرُونَ ٥٦“Yankho lawo silidali lina koma kuti, “Chotsani anthu a Loti mu mzinda wanu. Awa ndi anthu amene afuna kudziyeretsa.” فَأَنجَيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥٓ إِلَّا ٱمۡرَأَتَهُۥ قَدَّرۡنَٰهَا مِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ ٥٧Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi anthu ake kupatula mkazi wake amene adatsalira m’chilango وَأَمۡطَرۡنَا عَلَيۡهِم مَّطَرًاۖ فَسَآءَ مَطَرُ ٱلۡمُنذَرِينَ ٥٨Ndipo tidawalasa iwo ndi mvula ya miyala imene idagwa pa iwo. Ndi mvula yoipa imene idagwera iwo amene adachenjezedwa قُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ وَسَلَٰمٌ عَلَىٰ عِبَادِهِ ٱلَّذِينَ ٱصۡطَفَىٰٓۗ ءَآللَّهُ خَيۡرٌ أَمَّا يُشۡرِكُونَ ٥٩Nena, “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu ndipo mtendere ukhale pa Atumwi ake amene Iye wawasankha. Kodi wabwino ndani Mulungu kapena mafano amene amawapembedza yoonjezera pa Mulungu?” أَمَّنۡ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَأَنزَلَ لَكُم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءً فَأَنۢبَتۡنَا بِهِۦ حَدَآئِقَ ذَاتَ بَهۡجَةٍ مَّا كَانَ لَكُمۡ أَن تُنۢبِتُواْ شَجَرَهَآۗ أَءِلَٰهٌ مَّعَ ٱللَّهِۚ بَلۡ هُمۡ قَوۡمٌ يَعۡدِلُونَ ٦٠Kapena wabwino ndi Iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi kukutumizirani mvula kuchokera kumwamba ndi kubweretsa minda ya chisangalalo? Iwo sangathe kumeretsa mitengo. Kodi pali milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni? Koma iwo ndi anthu amene amafanizira ena ake kukhala ofanana ndi Mulungu أَمَّن جَعَلَ ٱلۡأَرۡضَ قَرَارًا وَجَعَلَ خِلَٰلَهَآ أَنۡهَٰرًا وَجَعَلَ لَهَا رَوَٰسِيَ وَجَعَلَ بَيۡنَ ٱلۡبَحۡرَيۡنِ حَاجِزًاۗ أَءِلَٰهٌ مَّعَ ٱللَّهِۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ ٦١Kapena Iye amene adakhazikitsa dziko ndi kulithirira ilo ndi mitsinje ya madzi oyenda; ndipo wakhazikitsa mapiri pa dziko ndipo waika malire pakati pa nyanja ziwiri. Kodi pali mulungu wina woonjezera pa Mulungu weniweni? Koma ambiri a iwo ndi osadziwa أَمَّن يُجِيبُ ٱلۡمُضۡطَرَّ إِذَا دَعَاهُ وَيَكۡشِفُ ٱلسُّوٓءَ وَيَجۡعَلُكُمۡ خُلَفَآءَ ٱلۡأَرۡضِۗ أَءِلَٰهٌ مَّعَ ٱللَّهِۚ قَلِيلًا مَّا تَذَكَّرُونَ ٦٢Kapena Iye amene amayankha mapemphero a munthu opanikizika pamene amupempha Iye ndipo amamuchotsera mavuto. Ndiyetu amene wakupatsani dziko lapansi kuti muzikhalamo. Kodi pali mulungu winanso woonjezera pa Mulungu weniweni? Ndi zazing’ono zimene mumakumbukira أَمَّن يَهۡدِيكُمۡ فِي ظُلُمَٰتِ ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِ وَمَن يُرۡسِلُ ٱلرِّيَٰحَ بُشۡرَۢا بَيۡنَ يَدَيۡ رَحۡمَتِهِۦٓۗ أَءِلَٰهٌ مَّعَ ٱللَّهِۚ تَعَٰلَى ٱللَّهُ عَمَّا يُشۡرِكُونَ ٦٣Kapena ndi Iye amene amakutsogolerani mu mdima pa mtunda kapena pa nyanja ndipo amatumiza mphepo ngati yonyamula uthenga wabwino wa chisomo chake. Kodi pali mulungu winanso woonjezera pa Mulungu weniweni? Mulungu ndi wapamwamba kuposa zimene amamufanizira nazo أَمَّن يَبۡدَؤُاْ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥ وَمَن يَرۡزُقُكُم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِۗ أَءِلَٰهٌ مَّعَ ٱللَّهِۚ قُلۡ هَاتُواْ بُرۡهَٰنَكُمۡ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ ٦٤Kapena Iye amene poyambirira adapanga zolengedwa ndiponso amene adzatidzutsanso kukhala ndi moyo m’moyo umene uli nkudza ndiponso amene amakupatsani chakudya kuchokera ku nthaka ndi kumwamba? Kodi pali mulungu winanso woonjezera pa Mulungu weniweni? Nena, “Tionetseni chizindikiro chanu ngati zimene mukunenazi ndi zoonadi.” قُل لَّا يَعۡلَمُ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ ٱلۡغَيۡبَ إِلَّا ٱللَّهُۚ وَمَا يَشۡعُرُونَ أَيَّانَ يُبۡعَثُونَ ٦٥Nena, “Palibe amene ali kumwamba kapena pa dziko lapansi amene amadziwa zobisika kupatula Mulungu. Ndiponso anthu sadziwa nthawi imene adzaukitsidwa kukhalanso ndi moyo.” بَلِ ٱدَّٰرَكَ عِلۡمُهُمۡ فِي ٱلۡأٓخِرَةِۚ بَلۡ هُمۡ فِي شَكٍّ مِّنۡهَاۖ بَلۡ هُم مِّنۡهَا عَمُونَ ٦٦Kodi kuzindikira kwawo m’moyo umene uli nkudza kwakwaniritsidwa? Iwo ndi okaika pa zamoyo umene uli nkudza ndipo maso awo ndi otsekeka pa za iwo وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ أَءِذَا كُنَّا تُرَٰبًا وَءَابَآؤُنَآ أَئِنَّا لَمُخۡرَجُونَ ٦٧Anthu osakhulupirira adati, “Kodi pamene ife ndi makolo anthu, tisanduka dothi tidzaukitsidwanso?” لَقَدۡ وُعِدۡنَا هَٰذَا نَحۡنُ وَءَابَآؤُنَا مِن قَبۡلُ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّآ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ ٦٨“Ndithudi ife tidalonjezedwa ndiponso makolo athu. Ichi si china ayi koma nkhani zopanda pake za anthu akale.” قُلۡ سِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَٱنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُجۡرِمِينَ ٦٩Nena, “Pitani pa dziko lonse lapansi ndipo mukaone zimene zidawaonekera anthu ochimwa.” وَلَا تَحۡزَنۡ عَلَيۡهِمۡ وَلَا تَكُن فِي ضَيۡقٍ مِّمَّا يَمۡكُرُونَ ٧٠Usachite chisoni kapena kuvutika mu mtima chifukwa cha ziwembu zimene apanga وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ ٧١Ndipo iwo amati, “Kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa liti ngati zimene muli kunenazi ndi zoona?” قُلۡ عَسَىٰٓ أَن يَكُونَ رَدِفَ لَكُم بَعۡضُ ٱلَّذِي تَسۡتَعۡجِلُونَ ٧٢Nena, “Mwina gawo lina la zimene muli kufuna kuti zidze msanga zili pafupi kudza.” وَإِنَّ رَبَّكَ لَذُو فَضۡلٍ عَلَى ٱلنَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَشۡكُرُونَ ٧٣Ndipo, ndithudi, Ambuye wako ndi wokoma mtima kwa anthu, koma ambiri a iwo sathokoza ayi وَإِنَّ رَبَّكَ لَيَعۡلَمُ مَا تُكِنُّ صُدُورُهُمۡ وَمَا يُعۡلِنُونَ ٧٤Ndipo, ndithudi, Ambuye wako amadziwa zonse zimene zimabisika m’mitima mwawo ndiponso zonse zimene amaulula وَمَا مِنۡ غَآئِبَةٍ فِي ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِ إِلَّا فِي كِتَٰبٍ مُّبِينٍ ٧٥Kulibe chinsinsi kumwamba kapena padziko lapansi chimene sichidalembedwe mu Buku lake lolemekezeka إِنَّ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانَ يَقُصُّ عَلَىٰ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ أَكۡثَرَ ٱلَّذِي هُمۡ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ ٧٦Buku la Korani lili kuwauza ana a Israyeli zambiri zimene iwo amatsutsana وَإِنَّهُۥ لَهُدًى وَرَحۡمَةٌ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ ٧٧Ndipo limeneli ndi chenjezo ndiponso madalitso kwa anthu okhulupirira m’choonadi إِنَّ رَبَّكَ يَقۡضِي بَيۡنَهُم بِحُكۡمِهِۦۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡعَلِيمُ ٧٨Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo ndi chiweruzo chake. Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini kudziwa za chinthu china chilichonse فَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱللَّهِۖ إِنَّكَ عَلَى ٱلۡحَقِّ ٱلۡمُبِينِ ٧٩Kotero iwe ika chikhulupiriro chako mwa Mulungu chifukwa iwe uli pa choonadi chenicheni إِنَّكَ لَا تُسۡمِعُ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَلَا تُسۡمِعُ ٱلصُّمَّ ٱلدُّعَآءَ إِذَا وَلَّوۡاْ مُدۡبِرِينَ ٨٠Ndithudi iwe siungathe kumupanga munthu wakufa kuti amve ndiponso siungathe kumupanga munthu osamva kuti amve kuitana kwako pamene iye atembenuka وَمَآ أَنتَ بِهَٰدِي ٱلۡعُمۡيِ عَن ضَلَٰلَتِهِمۡۖ إِن تُسۡمِعُ إِلَّا مَن يُؤۡمِنُ بِـَٔايَٰتِنَا فَهُم مُّسۡلِمُونَ ٨١Si udindo wako kutsogolera anthu a khungu kuti aleke kusochera. Palibe munthu amene adzakumvera kupatula okhawo amene amakhulupirira mu chivumbulutso chathu ndipo amadzipereka kwathunthu ۞ وَإِذَا وَقَعَ ٱلۡقَوۡلُ عَلَيۡهِمۡ أَخۡرَجۡنَا لَهُمۡ دَآبَّةً مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ تُكَلِّمُهُمۡ أَنَّ ٱلنَّاسَ كَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا لَا يُوقِنُونَ ٨٢Patsiku limene chiweruzo chathu chidzayandikira kwa osakhulupirira, Ife tidzawabweretsera chinyama chimene chidzayankhula nawo kuchokera ku dziko lapansi chifukwa munthu sanakhulupirire chivumbulutso chathu وَيَوۡمَ نَحۡشُرُ مِن كُلِّ أُمَّةٍ فَوۡجًا مِّمَّن يُكَذِّبُ بِـَٔايَٰتِنَا فَهُمۡ يُوزَعُونَ ٨٣Patsiku limeneli, tidzasonkhanitsa kuchokera ku mtundu uliwonse gululaanthuamenesadakhulupirirechivumbulutsochathu. Iwo adzasonkhanitsidwa ndi kuikidwa m’mizere حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءُو قَالَ أَكَذَّبۡتُم بِـَٔايَٰتِي وَلَمۡ تُحِيطُواْ بِهَا عِلۡمًا أَمَّاذَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ ٨٤Mpaka pamene adzafike pamalo a chiweruzo, Mulungu adzati, “Kodi inu mudakana chivumbulutso changa ngakhale kuti inu simumadziwa chilichonse cha chivumbulutsocho? Kodi ndi chiyani mumachita?” وَوَقَعَ ٱلۡقَوۡلُ عَلَيۡهِم بِمَا ظَلَمُواْ فَهُمۡ لَا يَنطِقُونَ ٨٥Chionongeko chidzadza pa iwo chifukwa cha zoipa zawo ndipo iwo adzasowa chowiringula أَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّا جَعَلۡنَا ٱلَّيۡلَ لِيَسۡكُنُواْ فِيهِ وَٱلنَّهَارَ مُبۡصِرًاۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٍ لِّقَوۡمٍ يُؤۡمِنُونَ ٨٦Kodi iwo saona mmene tidakonzera usiku kuti ukhale mpumulo ndi masana kuti uziwapatsa kuwala? Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira وَيَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِ فَفَزِعَ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ إِلَّا مَن شَآءَ ٱللَّهُۚ وَكُلٌّ أَتَوۡهُ دَٰخِرِينَ ٨٧Patsikulimeneli, lipengalidzalizidwandipoonseamene amakhala kumwamba ndi padziko lapansi adzagwidwa ndi mantha kupatula okhawo amene Mulungu adzafuna kuwapatula mu zimene zi. Onse adzabwera kwa Iye modzichepetsa وَتَرَى ٱلۡجِبَالَ تَحۡسَبُهَا جَامِدَةً وَهِيَ تَمُرُّ مَرَّ ٱلسَّحَابِۚ صُنۡعَ ٱللَّهِ ٱلَّذِيٓ أَتۡقَنَ كُلَّ شَيۡءٍۚ إِنَّهُۥ خَبِيرُۢ بِمَا تَفۡعَلُونَ ٨٨Iwe udzaona mapiri ndi kuwaganizira kuti ndi okhazikika koma iwo adzayenda ngati mmene mitambo imachitira. Uwu ndi mchitidwe wa Mulungu amene wakonza bwino lomwe chinthu chilichonse. Ndithudi Iye amadziwa bwino zonse zomwe mumachita مَن جَآءَ بِٱلۡحَسَنَةِ فَلَهُۥ خَيۡرٌ مِّنۡهَا وَهُم مِّن فَزَعٍ يَوۡمَئِذٍ ءَامِنُونَ ٨٩Iwo amene achita zabwino adzalandira mphotho imene ili yabwino ndipo adzakhala osakhudzidwa ndi zochititsa mantha za tsiku limeneli وَمَن جَآءَ بِٱلسَّيِّئَةِ فَكُبَّتۡ وُجُوهُهُمۡ فِي ٱلنَّارِ هَلۡ تُجۡزَوۡنَ إِلَّا مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ ٩٠Koma iwo amene achita zoipa adzaduduluzidwa pa mphumi zawo kunka ku moto. “Kodi inu simudzalandira malipiro ofanana ndi ntchito zanu?” إِنَّمَآ أُمِرۡتُ أَنۡ أَعۡبُدَ رَبَّ هَٰذِهِ ٱلۡبَلۡدَةِ ٱلَّذِي حَرَّمَهَا وَلَهُۥ كُلُّ شَيۡءٍۖ وَأُمِرۡتُ أَنۡ أَكُونَ مِنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ ٩١Nena, “Ine ndalamulidwa kutumikira Ambuye wa mzinda uno umene waupanga kuti ukhale Woyera. Zinthu zonse ndi zake. Ndipo ndalamulidwa kukhala mmodzi mwa odzipereka.” وَأَنۡ أَتۡلُوَاْ ٱلۡقُرۡءَانَۖ فَمَنِ ٱهۡتَدَىٰ فَإِنَّمَا يَهۡتَدِي لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن ضَلَّ فَقُلۡ إِنَّمَآ أَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُنذِرِينَ ٩٢Ndipo ndalamulidwa kuwerenga Buku la Korani. Aliyense amene atsatira njira yoyenera atero podzithandiza yekha. Kwa iye amene asochera nena “Ine si ndine kanthu kena koma mmodzi wa iwo ochenjeza anthu.” وَقُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ سَيُرِيكُمۡ ءَايَٰتِهِۦ فَتَعۡرِفُونَهَاۚ وَمَا رَبُّكَ بِغَٰفِلٍ عَمَّا تَعۡمَلُونَ ٩٣Ndipo nena, “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu! Iye adzakulangizani zizindikiro zake ndipo inu mudzazizindikira. Ambuye wanu saiwala zimene mumachita.”

الترجمة: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula.