بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
طسٓمٓ ١Ta Sin Mim تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُبِينِ ٢Awa ndi mawu omveka a Buku la Korani لَعَلَّكَ بَٰخِعٌ نَّفۡسَكَ أَلَّا يَكُونُواْ مُؤۡمِنِينَ ٣Iwe mwina ukhoza kudziononga ndi madandaulo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo إِن نَّشَأۡ نُنَزِّلۡ عَلَيۡهِم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ ءَايَةً فَظَلَّتۡ أَعۡنَٰقُهُمۡ لَهَا خَٰضِعِينَ ٤Ngati Ife tifuna, tikhoza kuwavumbulutsira chizindikiro chochokera kumwamba chimene makosi awo adzakhota modzichepetsa وَمَا يَأۡتِيهِم مِّن ذِكۡرٍ مِّنَ ٱلرَّحۡمَٰنِ مُحۡدَثٍ إِلَّا كَانُواْ عَنۡهُ مُعۡرِضِينَ ٥Palibe chenjezo latsopano limene limadza kuchokera kwa Mwini chisoni chosatha koma iwo amalikana فَقَدۡ كَذَّبُواْ فَسَيَأۡتِيهِمۡ أَنۢبَٰٓؤُاْ مَا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ ٦Ndithudi iwo amakana mawu a Mulungu koma nkhani zidzadza kwa iwo zokhudza zinthu zimene iwo amazichita chipongwe أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ إِلَى ٱلۡأَرۡضِ كَمۡ أَنۢبَتۡنَا فِيهَا مِن كُلِّ زَوۡجٍ كَرِيمٍ ٧Kodi iwo saona nthaka, mmene ife tameretsamo mbewu zabwino zosiyanasiyana إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةًۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ ٨Ndithudi m’menemu muli chizindikiro komabe ambiri a iwo sakhulupirira ayi وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ٩Ndithudi Ambuye wako ndiye Mwini mphamvu zonse ndiponso Mwini chisoni chosatha وَإِذۡ نَادَىٰ رَبُّكَ مُوسَىٰٓ أَنِ ٱئۡتِ ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ ١٠Ndipo pamene Ambuye wako adamuitana Mose adanena kuti, “Pita kwa anthu opanda chilungamo.” قَوۡمَ فِرۡعَوۡنَۚ أَلَا يَتَّقُونَ ١١Kodi anthu a Farawo sangaope قَالَ رَبِّ إِنِّيٓ أَخَافُ أَن يُكَذِّبُونِ ١٢Iye adati, “Ambuye wanga! Ndithudi ine ndili kuopa kuti adzandikana.” وَيَضِيقُ صَدۡرِي وَلَا يَنطَلِقُ لِسَانِي فَأَرۡسِلۡ إِلَىٰ هَٰرُونَ ١٣“Ndipondikhozakupsamtimandikulepherakuyankhula. Tumizani Aroni.” وَلَهُمۡ عَلَيَّ ذَنۢبٌ فَأَخَافُ أَن يَقۡتُلُونِ ١٤“Ndipo iwo ali ndi mangawa ndi ine ndipo ndichita mantha kuti akhoza kukandipha.” قَالَ كـَلَّاۖ فَٱذۡهَبَا بِـَٔايَٰتِنَآۖ إِنَّا مَعَكُم مُّسۡتَمِعُونَ ١٥Mulungu adati, “Nkosatheka kutero! Kotero pitani nonse awiri ndi zizindikiro zathu. Ife tidzakhala ndi inu ndipo tidzamva.” فَأۡتِيَا فِرۡعَوۡنَ فَقُولَآ إِنَّا رَسُولُ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ١٦Ndipo mukakafika kwa Farawo mukamuuze kuti, “Ife ndife Atumwi ochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse.” أَنۡ أَرۡسِلۡ مَعَنَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ١٧“Motero alekeni ana a Israyeli kuti apite ndi ife.” قَالَ أَلَمۡ نُرَبِّكَ فِينَا وَلِيدًا وَلَبِثۡتَ فِينَا مِنۡ عُمُرِكَ سِنِينَ ١٨(Farawo) adati, “Kodi ife sitidakurere iwe pamene udali wamng’ono? Ndipo iwe unakhala pakati pathu zaka zambiri.” وَفَعَلۡتَ فَعۡلَتَكَ ٱلَّتِي فَعَلۡتَ وَأَنتَ مِنَ ٱلۡكَٰفِرِينَ ١٩“Ndipo iwe udachita chimene udachita. Ndithudi iwe ndiwe mmodzi wa anthu osathokoza.” قَالَ فَعَلۡتُهَآ إِذًا وَأَنَا۠ مِنَ ٱلضَّآلِّينَ ٢٠(Mose) adati, “Ine ndidachita chimenecho popeza nthawi imeneyo ndidali wosadziwa china chilichonse.” فَفَرَرۡتُ مِنكُمۡ لَمَّا خِفۡتُكُمۡ فَوَهَبَ لِي رَبِّي حُكۡمًا وَجَعَلَنِي مِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ٢١“Motero ine ndidathawa inu nonse pa nthawi imene ndidakuopani koma tsopano Ambuye wanga wandipatsa luntha ndiponso wandipanga ine kukhala mmodzi mwa Atumwi ake.” وَتِلۡكَ نِعۡمَةٌ تَمُنُّهَا عَلَيَّ أَنۡ عَبَّدتَّ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٢٢“Ndipo uwu ndi mwayi umene ubwino wake iwe uli kundinyogodola. Iwe wasandutsa ana a Israyeli kukhala akapolo ako.” قَالَ فِرۡعَوۡنُ وَمَا رَبُّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٢٣Farawo adati, “Kodi Ambuye wa zolengedwa zonse ndani?” قَالَ رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَآۖ إِن كُنتُم مُّوقِنِينَ ٢٤(Mose) adati, “Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo ngati inu mufuna kukhulupirira.” قَالَ لِمَنۡ حَوۡلَهُۥٓ أَلَا تَسۡتَمِعُونَ ٢٥(Farawo) adawafunsa anthu amene adamuzungulira! “Kodi muli kumva zimene ali kunenazi.” قَالَ رَبُّكُمۡ وَرَبُّ ءَابَآئِكُمُ ٱلۡأَوَّلِينَ ٢٦(Mose) adapitiriza kuti, “Ambuye wanu ndiponso Ambuye wa makolo anu akale.” قَالَ إِنَّ رَسُولَكُمُ ٱلَّذِيٓ أُرۡسِلَ إِلَيۡكُمۡ لَمَجۡنُونٌ ٢٧(Farawo) adati, “Ndithudi Mtumwi amene watumizidwa kwa inu ndi wopenga.” قَالَ رَبُّ ٱلۡمَشۡرِقِ وَٱلۡمَغۡرِبِ وَمَا بَيۡنَهُمَآۖ إِن كُنتُمۡ تَعۡقِلُونَ ٢٨(Mose) adati, “Iye ndi Ambuye wa kum’mawa ndi kumadzulo ndi zonse zimene zikhala kumeneko ngati muli ozindikira.” قَالَ لَئِنِ ٱتَّخَذۡتَ إِلَٰهًا غَيۡرِي لَأَجۡعَلَنَّكَ مِنَ ٱلۡمَسۡجُونِينَ ٢٩(Farawo) adayankha kuti, “Ngati iwe utumikira mulungu wina kupatula ine, ndithudi ndikupanga kukhala mmodzi wa anthu okhala ku ndende.” قَالَ أَوَلَوۡ جِئۡتُكَ بِشَيۡءٍ مُّبِينٍ ٣٠(Mose) adafunsa kuti, “Kodi zingakhale choncho ngakhale nditakulangiza chizindikiro choonekeratu? “ قَالَ فَأۡتِ بِهِۦٓ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ ٣١(Farawo) adati, “Tilangize chizindikiro chako ngati zonse zimene unena ndi zoona.” فَأَلۡقَىٰ عَصَاهُ فَإِذَا هِيَ ثُعۡبَانٌ مُّبِينٌ ٣٢Motero Mose adaponya ndodo yake pansi ndipo nthawi yomweyo idasanduka njoka yeniyeni وَنَزَعَ يَدَهُۥ فَإِذَا هِيَ بَيۡضَآءُ لِلنَّٰظِرِينَ ٣٣Ndipo Iye adatulutsa dzanja lake ndipo nthawi yomweyo lidasanduka loyera kwa iwo amene adaliona قَالَ لِلۡمَلَإِ حَوۡلَهُۥٓ إِنَّ هَٰذَا لَسَٰحِرٌ عَلِيمٌ ٣٤Farawo adauza nduna zake kuti, “Ndithudi munthu uyu ndi wodziwa matsenga.” يُرِيدُ أَن يُخۡرِجَكُم مِّنۡ أَرۡضِكُم بِسِحۡرِهِۦ فَمَاذَا تَأۡمُرُونَ ٣٥“Iyeyu afuna kukuchotsani m’dziko lanu ndi matsenga ake. Kodi ulangizi wanu ndi wotani ndipo ukupereka langizo lanji?” قَالُوٓاْ أَرۡجِهۡ وَأَخَاهُ وَٱبۡعَثۡ فِي ٱلۡمَدَآئِنِ حَٰشِرِينَ ٣٦Iwo adati, “Muyambe mwawasunga iye pamodzi ndi m’bale wake kwa kanthawi kochepa. Tumizani mithenga ku mizinda yanu يَأۡتُوكَ بِكُلِّ سَحَّارٍ عَلِيمٍ ٣٧Abweretse kwa inu munthu aliyense yemwe ndi wodziwa matsenga kwambiri.” فَجُمِعَ ٱلسَّحَرَةُ لِمِيقَٰتِ يَوۡمٍ مَّعۡلُومٍ ٣٨Motero anthu amatsengawa adasonkhanitsidwa patsiku lodziwika lomwe adagwirizana وَقِيلَ لِلنَّاسِ هَلۡ أَنتُم مُّجۡتَمِعُونَ ٣٩Ndipo anthu adafunsidwa kuti, “Kodi nonse mudzasonkhana?” لَعَلَّنَا نَتَّبِعُ ٱلسَّحَرَةَ إِن كَانُواْ هُمُ ٱلۡغَٰلِبِينَ ٤٠“Kuti mwina ife tikhoza kudzatsatira a matsenga ngati iwo atapambana.” فَلَمَّا جَآءَ ٱلسَّحَرَةُ قَالُواْ لِفِرۡعَوۡنَ أَئِنَّ لَنَا لَأَجۡرًا إِن كُنَّا نَحۡنُ ٱلۡغَٰلِبِينَ ٤١Ndipo pamene anthu onse amatsenga adadza kwa Farawo, iwo adati kwa Farawo, “Kodi mudzatilipira ngati titapambana?” قَالَ نَعَمۡ وَإِنَّكُمۡ إِذًا لَّمِنَ ٱلۡمُقَرَّبِينَ ٤٢Iye adati, “Inde. Ndipo ndithudi inu mudzakhala kufupi ndi Ine.” قَالَ لَهُم مُّوسَىٰٓ أَلۡقُواْ مَآ أَنتُم مُّلۡقُونَ ٤٣Mose adawauza kuti, “Ponyani pansi chilichonse chimene mufuna kuponya.” فَأَلۡقَوۡاْ حِبَالَهُمۡ وَعِصِيَّهُمۡ وَقَالُواْ بِعِزَّةِ فِرۡعَوۡنَ إِنَّا لَنَحۡنُ ٱلۡغَٰلِبُونَ ٤٤Ndipo iwo adaponya zingwe ndi ndodo zawo ndipo adati: “Mwa mphamvu ya Farawo, ndithudi, ife tipambana.” فَأَلۡقَىٰ مُوسَىٰ عَصَاهُ فَإِذَا هِيَ تَلۡقَفُ مَا يَأۡفِكُونَ ٤٥Ndipo Mose adaponya ndodo yake ndipo nthawi yomweyo idameza zonse zabodza zimene iwo adapanga فَأُلۡقِيَ ٱلسَّحَرَةُ سَٰجِدِينَ ٤٦Ndipo anthu amatsenga onse aja adagwa pansi mogwada قَالُوٓاْ ءَامَنَّا بِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٤٧Iwo adati, “Ife takhulupirira mwa Ambuye wa zolengedwa zonse.” رَبِّ مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ ٤٨“Ambuye wa Mose ndi Aroni” قَالَ ءَامَنتُمۡ لَهُۥ قَبۡلَ أَنۡ ءَاذَنَ لَكُمۡۖ إِنَّهُۥ لَكَبِيرُكُمُ ٱلَّذِي عَلَّمَكُمُ ٱلسِّحۡرَ فَلَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَۚ لَأُقَطِّعَنَّ أَيۡدِيَكُمۡ وَأَرۡجُلَكُم مِّنۡ خِلَٰفٍ وَلَأُصَلِّبَنَّكُمۡ أَجۡمَعِينَ ٤٩Farawo adati, “Kodi inu mwakhulupirira mwa iye pamene ine sindinakupatseni chilolezo? Ndithudi iye ndi mtsogoleri wanu amene adakuphunzitsani matsenga. Ndithudi posachedwapa mudzazindikira. Ndithudi ine ndidzadula manja anu ndi miyendo yanu moisiyanitsa. Ndidzakudulani dzanja lamanja ndi mwendo wamanzere ndiponso ndidzakupachikani pa mtanda.” قَالُواْ لَا ضَيۡرَۖ إِنَّآ إِلَىٰ رَبِّنَا مُنقَلِبُونَ ٥٠Iwo adati, “Zilibe kanthu chifukwa ndithudi ife tidzabwerera kwa Ambuye wathu.” إِنَّا نَطۡمَعُ أَن يَغۡفِرَ لَنَا رَبُّنَا خَطَٰيَٰنَآ أَن كُنَّآ أَوَّلَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٥١“Ndithudi Ife tili ndi chiyembekezo kuti Ambuye wathu adzatikhululukira machimo athu popeza ndife oyamba kukhulupirira.” ۞ وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ أَنۡ أَسۡرِ بِعِبَادِيٓ إِنَّكُم مُّتَّبَعُونَ ٥٢Ndipo tidamulamula Mose kuti, “Nyamuka nthawi ya usiku ndi akapolo anga chifukwa, ndithudi, inu mulondoledwa ndi gulu la adani anu.” فَأَرۡسَلَ فِرۡعَوۡنُ فِي ٱلۡمَدَآئِنِ حَٰشِرِينَ ٥٣Ndipo Farawo adatumiza mithenga ku mizinda yonse إِنَّ هَٰٓؤُلَآءِ لَشِرۡذِمَةٌ قَلِيلُونَ ٥٤“Ndithudi anthu amenewa ndi kagulu ka anthu ochepa.” وَإِنَّهُمۡ لَنَا لَغَآئِظُونَ ٥٥“Ndithudi anthu amenewa atipsetsa mtima.” وَإِنَّا لَجَمِيعٌ حَٰذِرُونَ ٥٦“Ife tonse tili tcheru.” فَأَخۡرَجۡنَٰهُم مِّن جَنَّٰتٍ وَعُيُونٍ ٥٧Ndipo tidawachotsa m’minda ndi mu a kasupe وَكُنُوزٍ وَمَقَامٍ كَرِيمٍ ٥٨Ndiponso m’chuma ndi m’malo alionse olemekezeka كَذَٰلِكَۖ وَأَوۡرَثۡنَٰهَا بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٥٩Kotero tidawapanga ana a Israyeli kukhala alowa m’malo a zinthu za anthu a Farawo فَأَتۡبَعُوهُم مُّشۡرِقِينَ ٦٠Pamene dzuwa linali kutuluka, iwo adalondoledwa ndi adani awo فَلَمَّا تَرَٰٓءَا ٱلۡجَمۡعَانِ قَالَ أَصۡحَٰبُ مُوسَىٰٓ إِنَّا لَمُدۡرَكُونَ ٦١Ndipo pamene magulu awiriwa adaonana wina ndi mnzake, anthu a Mose adati, “Ndithudi atipeza.” قَالَ كـَلَّآۖ إِنَّ مَعِيَ رَبِّي سَيَهۡدِينِ ٦٢Mose adati, “Iyayi. Ndithudi Ambuye wanga ali ndi ine ndipo adzanditsogolera.” فَأَوۡحَيۡنَآ إِلَىٰ مُوسَىٰٓ أَنِ ٱضۡرِب بِّعَصَاكَ ٱلۡبَحۡرَۖ فَٱنفَلَقَ فَكَانَ كُلُّ فِرۡقٍ كَٱلطَّوۡدِ ٱلۡعَظِيمِ ٦٣Ndipo tidalamulira Mose kuti, “Menya madzi a m’nyanja ndi ndodo yako.” Ndipo nyanja idagawanika pakati, mbali iliyonse idali ngati phiri lalikulu وَأَزۡلَفۡنَا ثَمَّ ٱلۡأٓخَرِينَ ٦٤Ndipo anthu a Farawo tidawayandikitsa ndi nyanja ija وَأَنجَيۡنَا مُوسَىٰ وَمَن مَّعَهُۥٓ أَجۡمَعِينَ ٦٥Ndipo Ife tidapulumutsa Mose ndi onse amene adali ndi iye ثُمَّ أَغۡرَقۡنَا ٱلۡأٓخَرِينَ ٦٦Ndipo tidamiza ena إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةًۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ ٦٧Ndithudi mu ichi muli phunziro komabe anthu ambiri sakhulupirira ayi وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ٦٨Ndithudi Ambuye wako! Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha وَٱتۡلُ عَلَيۡهِمۡ نَبَأَ إِبۡرَٰهِيمَ ٦٩Ndipo afotokozere nkhani za Abrahamu إِذۡ قَالَ لِأَبِيهِ وَقَوۡمِهِۦ مَا تَعۡبُدُونَ ٧٠Pamenepo iye adanena kwa abambo ake ndiponso kwa anthu ake kuti, “Kodi ndi chiyani chimene inu muli kupembedza?” قَالُواْ نَعۡبُدُ أَصۡنَامًا فَنَظَلُّ لَهَا عَٰكِفِينَ ٧١Iwo adati, “Timatumikira mafano ndipo timapempha kwa iwo modzipereka kwambiri.” قَالَ هَلۡ يَسۡمَعُونَكُمۡ إِذۡ تَدۡعُونَ ٧٢Ndipo adati, “Kodi iwo amakumvani pamene mumawapempha?” أَوۡ يَنفَعُونَكُمۡ أَوۡ يَضُرُّونَ ٧٣“Kodi amakuthandizani kapena kukuonongani?” قَالُواْ بَلۡ وَجَدۡنَآ ءَابَآءَنَا كَذَٰلِكَ يَفۡعَلُونَ ٧٤Iwo adati, “Iyayi. Koma ife tidawapeza makolo athu akupembedza mafano.” قَالَ أَفَرَءَيۡتُم مَّا كُنتُمۡ تَعۡبُدُونَ ٧٥Iye adati, “Kodi inu muli kuzidziwa zimene muli kuzipembedza?” أَنتُمۡ وَءَابَآؤُكُمُ ٱلۡأَقۡدَمُونَ ٧٦“Inu ndiponso makolo anu akale?” فَإِنَّهُمۡ عَدُوٌّ لِّيٓ إِلَّا رَبَّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٧٧“Ndithudi onse ndi adani anga kupatula Ambuye wachilengedwe.” ٱلَّذِي خَلَقَنِي فَهُوَ يَهۡدِينِ ٧٨“Amene adandipanga ine ndipo ndiye amene amandipatsa chilangizo.” وَٱلَّذِي هُوَ يُطۡعِمُنِي وَيَسۡقِينِ ٧٩“Ndipo ndiye amene amandipatsa chakudya ndi chakumwa.” وَإِذَا مَرِضۡتُ فَهُوَ يَشۡفِينِ ٨٠“Ndipo ndikadwala, ndi Iye amene amandichiza.” وَٱلَّذِي يُمِيتُنِي ثُمَّ يُحۡيِينِ ٨١“Ndipo ndiye amene adzandipangitsa kuti ndife ndi kudzandibwezeranso moyo.” وَٱلَّذِيٓ أَطۡمَعُ أَن يَغۡفِرَ لِي خَطِيٓـَٔتِي يَوۡمَ ٱلدِّينِ ٨٢“Ndi amene ine ndimayembekezera kuti adzandikhululukira machimo anga pa tsiku lachiweruzo” رَبِّ هَبۡ لِي حُكۡمًا وَأَلۡحِقۡنِي بِٱلصَّٰلِحِينَ ٨٣Ambuye ndipatseni luntha ndipo mundilole kuti ndikhale pakati pa anthu ochita zabwino وَٱجۡعَل لِّي لِسَانَ صِدۡقٍ فِي ٱلۡأٓخِرِينَ ٨٤Ndipatseni ulemerero umene udzatchulidwe ndi mibadwo yomwe ikubwera mtsogolo وَٱجۡعَلۡنِي مِن وَرَثَةِ جَنَّةِ ٱلنَّعِيمِ ٨٥Ndipo ndiikeni m’gulu la anthu amene adzakhala kumalo a mtendere a ku Paradiso وَٱغۡفِرۡ لِأَبِيٓ إِنَّهُۥ كَانَ مِنَ ٱلضَّآلِّينَ ٨٦Akhululukireni abambo anga ndithudi iwo ali mmodzi mwa anthu osochera وَلَا تُخۡزِنِي يَوۡمَ يُبۡعَثُونَ ٨٧Musadzandichititse manyazi patsiku limene anthu adzaukitsidwa kwa akufa يَوۡمَ لَا يَنفَعُ مَالٌ وَلَا بَنُونَ ٨٨Tsiku limene chuma ndi ana sizidzathandiza wina aliyense إِلَّا مَنۡ أَتَى ٱللَّهَ بِقَلۡبٍ سَلِيمٍ ٨٩Kupatula yekhayo amene adzadza kwa Mulungu ndi mtima woyera وَأُزۡلِفَتِ ٱلۡجَنَّةُ لِلۡمُتَّقِينَ ٩٠Pamenepo Paradiso idzayandikiritsidwa kwa anthu angwiro وَبُرِّزَتِ ٱلۡجَحِيمُ لِلۡغَاوِينَ ٩١Ndipo Gahena idzaonetsedwa poyera kwa anthu ochimwa وَقِيلَ لَهُمۡ أَيۡنَ مَا كُنتُمۡ تَعۡبُدُونَ ٩٢Mawu adzanenedwa kwa iwo kuti, “Kodi mafano anu aja amene mumatumikira ali kuti?” مِن دُونِ ٱللَّهِ هَلۡ يَنصُرُونَكُمۡ أَوۡ يَنتَصِرُونَ ٩٣Kuwonjezera pa Mulungu weniweni? Kodi iwo akhoza kukuthandizani inu kapena kudzithandiza okha?” فَكُبۡكِبُواْ فِيهَا هُمۡ وَٱلۡغَاوُۥنَ ٩٤Ndipo iwo ndi onse ochimwa adzaponyedwa ku Gahena وَجُنُودُ إِبۡلِيسَ أَجۡمَعُونَ ٩٥Ndiponso pamodzi ndi magulu onse a Satana قَالُواْ وَهُمۡ فِيهَا يَخۡتَصِمُونَ ٩٦Iwo adzati pamene adzakhala ali kukangana kumeneko تَٱللَّهِ إِن كُنَّا لَفِي ضَلَٰلٍ مُّبِينٍ ٩٧“Pali Mulungu, ndithudi, ife tidali ochimwa moonekeratu.” إِذۡ نُسَوِّيكُم بِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٩٨Pamene tidakusandutsani inu kukhala ofanana ndi Ambuye wa zolengedwa zonse وَمَآ أَضَلَّنَآ إِلَّا ٱلۡمُجۡرِمُونَ ٩٩Palibe ena koma anthu ochita zoipa amene adatisocheretsa ife فَمَا لَنَا مِن شَٰفِعِينَ ١٠٠Palibe wina woti angatipepesere ife وَلَا صَدِيقٍ حَمِيمٍ ١٠١Ndiponso palibe bwenzi lenileni فَلَوۡ أَنَّ لَنَا كَرَّةً فَنَكُونَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ١٠٢Koma tikadakhalanso ndi moyo, tikadakhala anthu okhulupirira إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةًۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ ١٠٣Ndithudi mu zimenezi muli chizindikiro koma anthu ambiri sakhulupirira ayi وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ١٠٤Ndithudi Ambuye wanu! Ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha كَذَّبَتۡ قَوۡمُ نُوحٍ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ١٠٥Anthu a m’badwo wa Nowa adakana Atumwi awo إِذۡ قَالَ لَهُمۡ أَخُوهُمۡ نُوحٌ أَلَا تَتَّقُونَ ١٠٦Pamene Nowa adati, “Kodi inu simungaope Mulungu ndi kumumvera Iye?” إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٌ ١٠٧“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu wokhulupirika.” فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ١٠٨“Motero opani Mulungu ndipo mundimvere ine.” وَمَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ١٠٩“Ine sindikupemphani malipiro ena alionse chifukwa palibe wina aliyense amene angandilipire ine kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.” فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ١١٠“Kotero opani Mulungu ndipo mundimvere ine.” ۞ قَالُوٓاْ أَنُؤۡمِنُ لَكَ وَٱتَّبَعَكَ ٱلۡأَرۡذَلُونَ ١١١Iwo adati, “Kodi ife tikukhulupirire iwe pamene anthu onyozeka ndiwo amene amakutsatira iwe?” قَالَ وَمَا عِلۡمِي بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ ١١٢Nowa adati, “Kodi ine ndikudziwa chiyani za chimene iwo amachita?” إِنۡ حِسَابُهُمۡ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّيۖ لَوۡ تَشۡعُرُونَ ١١٣“Ambuye wanga ndiye amene akhoza kuweruza ngati mumazindikira.” وَمَآ أَنَا۠ بِطَارِدِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ١١٤“Ndipo ine sindidzathamangitsa anthu okhulupirira moona.” إِنۡ أَنَا۠ إِلَّا نَذِيرٌ مُّبِينٌ ١١٥“Ine ndine wopereka chenjezo poyera.” قَالُواْ لَئِن لَّمۡ تَنتَهِ يَٰنُوحُ لَتَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمَرۡجُومِينَ ١١٦Iwo adati, “Iwe Nowa; ngati siusiya zimene uchita udzaponyedwa miyala.” قَالَ رَبِّ إِنَّ قَوۡمِي كَذَّبُونِ ١١٧Iye adati, “Ambuye wanga! Ndithudi anthu anga akundikana.” فَٱفۡتَحۡ بَيۡنِي وَبَيۡنَهُمۡ فَتۡحًا وَنَجِّنِي وَمَن مَّعِيَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ١١٨Motero weruzani mwachilungamo pakati pa ine ndi iwo. Ndipulumutseni ine pamodzi ndi anthu okhulupirira amene ali ndi ine فَأَنجَيۡنَٰهُ وَمَن مَّعَهُۥ فِي ٱلۡفُلۡكِ ٱلۡمَشۡحُونِ ١١٩Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi iwo amene adali naye m’chombo ثُمَّ أَغۡرَقۡنَا بَعۡدُ ٱلۡبَاقِينَ ١٢٠Ndipo pambuyo pake tidamiza ena onse ndi chigumula إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةًۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ ١٢١Ndithudi mu chimenechi muli phunziro komabe ambiri sakhulupirira وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ١٢٢Ndithudi Ambuye wako ndi Mwini mphamvu ndi Mwini chisoni chosatha كَذَّبَتۡ عَادٌ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ١٢٣Anthu a ku Aad sanakhulupirire Atumwi awo إِذۡ قَالَ لَهُمۡ أَخُوهُمۡ هُودٌ أَلَا تَتَّقُونَ ١٢٤Pamene m’bale wawo Houd adati, “Kodi inu simungakhale ndi mantha ndi Mulungu?” إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٌ ١٢٥“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu wokhulupirika.” فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ١٢٦“opani Mulungu ndipo munditsate ine.” وَمَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ١٢٧“Pa ntchito iyi, ine sindipempha malipiro kuchokera kwa inu chifukwa palibe wina amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.” أَتَبۡنُونَ بِكُلِّ رِيعٍ ءَايَةً تَعۡبَثُونَ ١٢٨“Kodi inu mukumamanga nyumba pamalo paliponse pokwera mofuna kudzisangalatsa?” وَتَتَّخِذُونَ مَصَانِعَ لَعَلَّكُمۡ تَخۡلُدُونَ ١٢٩“Kodi muli kumanga nyumba zokongola ndi zolimba ngati kuti mudzakhalamo mpaka kalekale?” وَإِذَا بَطَشۡتُم بَطَشۡتُمۡ جَبَّارِينَ ١٣٠“Ndipo pamene mumenya anthu mumamenya ngati anthu ankhanza.” فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ١٣١“Motero opani Mulungu, ndipo mundimvere ine.” وَٱتَّقُواْ ٱلَّذِيٓ أَمَدَّكُم بِمَا تَعۡلَمُونَ ١٣٢“Ndipo muopeni Iye amene wakupatsani inu zinthu zonse zimene mumazidziwa.” أَمَدَّكُم بِأَنۡعَٰمٍ وَبَنِينَ ١٣٣“Iye wakupatsani nyama ndi ana,” وَجَنَّٰتٍ وَعُيُونٍ ١٣٤“Ndiponso minda ndi a kasupe;” إِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُمۡ عَذَابَ يَوۡمٍ عَظِيمٍ ١٣٥“Ndithudi ine ndili kuchita mantha ndi chilango chimene chidzadza pa inu pa tsiku loopsa.” قَالُواْ سَوَآءٌ عَلَيۡنَآ أَوَعَظۡتَ أَمۡ لَمۡ تَكُن مِّنَ ٱلۡوَٰعِظِينَ ١٣٦Iwo adati, “Ndi chimodzimodzi kwa ife kaya utilalikira kapena ayi.” إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا خُلُقُ ٱلۡأَوَّلِينَ ١٣٧“Zonse zimene uli kutiopseza nazo ndi chikhalidwe cha anthu amakedzana.” وَمَا نَحۡنُ بِمُعَذَّبِينَ ١٣٨“Ife sitidzalangidwa ayi.” فَكَذَّبُوهُ فَأَهۡلَكۡنَٰهُمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةًۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ ١٣٩Iwo adamukana iye ndipo Ife tidawaononga onse. Ndithudi mu chimenechi muli phunziro koma ambiri sakhulupirira ayi وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ١٤٠Ndithudi Ambuye wako ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha كَذَّبَتۡ ثَمُودُ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ١٤١Anthu a Thamoud adakana Atumwi awo إِذۡ قَالَ لَهُمۡ أَخُوهُمۡ صَٰلِحٌ أَلَا تَتَّقُونَ ١٤٢Pamene m’bale wawo Saleh adati, “Kodi inu simungakhale ndi mantha ndi Mulungu?” إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٌ ١٤٣“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu okhulupirika.” فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ١٤٤“Motero opani Mulungu ndipo mundimvere ine.” وَمَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ١٤٥“Pa ntchito iyi ine sindili kukupemphani malipiro. Palibe wina amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.” أَتُتۡرَكُونَ فِي مَا هَٰهُنَآ ءَامِنِينَ ١٤٦“Kodi inu muganiza kuti mudzasiyidwa mu mtendere wa m’dziko lino?” فِي جَنَّٰتٍ وَعُيُونٍ ١٤٧“M’kati mwa minda ndi a kasupe.” وَزُرُوعٍ وَنَخۡلٍ طَلۡعُهَا هَضِيمٌ ١٤٨“Minda ya chimanga ndi mitengo ya tende imene yapatsa zipatso zambiri.” وَتَنۡحِتُونَ مِنَ ٱلۡجِبَالِ بُيُوتًا فَٰرِهِينَ ١٤٩“Ndipo muboola mapiri ndi kumangamo nyumba zanu mwaukatswiri;” فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ١٥٠“Khalani ndi mantha ndi Mulungu ndipo mundimvere ine.” وَلَا تُطِيعُوٓاْ أَمۡرَ ٱلۡمُسۡرِفِينَ ١٥١“Musamvere malamulo a anthu oononga.” ٱلَّذِينَ يُفۡسِدُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا يُصۡلِحُونَ ١٥٢“Amene amachita zoipa padziko lapansi ndipo sakonza makhalidwe awo.” قَالُوٓاْ إِنَّمَآ أَنتَ مِنَ ٱلۡمُسَحَّرِينَ ١٥٣Iwo adati, “Iwe uli mmodzi mwa olodzedwa.” مَآ أَنتَ إِلَّا بَشَرٌ مِّثۡلُنَا فَأۡتِ بِـَٔايَةٍ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ ١٥٤“Iwe ndiwe munthu wonga ife tomwe. Tilangize chizindikiro ngati zimene ukunenazi ndi zoona” قَالَ هَٰذِهِۦ نَاقَةٌ لَّهَا شِرۡبٌ وَلَكُمۡ شِرۡبُ يَوۡمٍ مَّعۡلُومٍ ١٥٥Iye adati, “Iyi ndi ngamira yaikazi. Iyo idzamwa madzi patsiku lake ndipo inu mudzamwa patsiku lanu lokhazikitsidwa.” وَلَا تَمَسُّوهَا بِسُوٓءٍ فَيَأۡخُذَكُمۡ عَذَابُ يَوۡمٍ عَظِيمٍ ١٥٦“Musaizunze ayi chifukwa mukatero chilango cha tsiku loopsa chidzadza kwa inu.” فَعَقَرُوهَا فَأَصۡبَحُواْ نَٰدِمِينَ ١٥٧Komabe iwo adaipha iyo ndipo adanong’oneza bombono فَأَخَذَهُمُ ٱلۡعَذَابُۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةًۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ ١٥٨Chilango chidawapeza iwo. Ndithudi mu chimenechi muli chizindikiro koma ambiri a iwo sakhulupirira وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ١٥٩Ndithudi Ambuye wako! Indedi ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha كَذَّبَتۡ قَوۡمُ لُوطٍ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ١٦٠Anthu a Loti adakana Atumwi awo إِذۡ قَالَ لَهُمۡ أَخُوهُمۡ لُوطٌ أَلَا تَتَّقُونَ ١٦١Pamene m’bale wawo Loti adati, “Kodi inu simungaope Mulungu?” إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٌ ١٦٢“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu wokhulupirika.” فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ١٦٣“Opani Mulungu ndipo mundimvere ine.” وَمَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ١٦٤“Ine sindili kupempha kuti mundilipire chifukwa cha ichi ayi chifukwa palibe wina amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.” أَتَأۡتُونَ ٱلذُّكۡرَانَ مِنَ ٱلۡعَٰلَمِينَ ١٦٥“Kodi inu mwasankha kuti muzigonana ndi amuna anzanu mwa zolengedwa zonse وَتَذَرُونَ مَا خَلَقَ لَكُمۡ رَبُّكُم مِّنۡ أَزۡوَٰجِكُمۚ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٌ عَادُونَ ١٦٦“Kusiya akazi amene Mulungu adakulengerani? Koma inu ndinu anthu olakwa kwambiri.” قَالُواْ لَئِن لَّمۡ تَنتَهِ يَٰلُوطُ لَتَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡمُخۡرَجِينَ ١٦٧Iwo adati, “Iwe Loti! Ngati siusiya zimenezi ndithudi udzakhala mmodzi mwa othamangitsidwa.” قَالَ إِنِّي لِعَمَلِكُم مِّنَ ٱلۡقَالِينَ ١٦٨Iye adati, “Ine ndili kudana ndi makhalidwe anu.” رَبِّ نَجِّنِي وَأَهۡلِي مِمَّا يَعۡمَلُونَ ١٦٩“Ambuye wanga! Ndipulumutseni ine pamodzi ndi a pabanja langa ku ntchito zawo zoipa.” فَنَجَّيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥٓ أَجۡمَعِينَ ١٧٠Ndipo Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi anthu ake onse إِلَّا عَجُوزًا فِي ٱلۡغَٰبِرِينَ ١٧١Kupatula mayi wokalamba, pakati pa amene adatsalira m’mbuyo ثُمَّ دَمَّرۡنَا ٱلۡأٓخَرِينَ ١٧٢Ndipo Ife tidawaononga kwambiri ena onse وَأَمۡطَرۡنَا عَلَيۡهِم مَّطَرًاۖ فَسَآءَ مَطَرُ ٱلۡمُنذَرِينَ ١٧٣Ndipo choipa chidali chilango cha mvula imene idagwa pa iwo amene adachenjezedwa koma sadamvere إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةًۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ ١٧٤Ndithudi mu ichi muli phunziro koma ambiri a iwo sakhulupirira وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ١٧٥Ndithudi Ambuye wako ndiye mwini mphamvu zonse ndi mwini chisoni chosatha كَذَّبَ أَصۡحَٰبُ لۡـَٔيۡكَةِ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ١٧٦Nawonso anthu okhala m’nkhalango adakana Atumwi إِذۡ قَالَ لَهُمۡ شُعَيۡبٌ أَلَا تَتَّقُونَ ١٧٧Pamene Shaibu adawauza kuti, “Kodi inu simungaope Mulungu?” إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٌ ١٧٨“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu wokhulupirira.” فَٱتَّقُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُونِ ١٧٩“Opani Mulungu ndipo mundimvere ine.” وَمَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍۖ إِنۡ أَجۡرِيَ إِلَّا عَلَىٰ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ١٨٠“Ine sindikupemphani malipiro chifukwa palibe wina aliyense amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.” ۞ أَوۡفُواْ ٱلۡكَيۡلَ وَلَا تَكُونُواْ مِنَ ٱلۡمُخۡسِرِينَ ١٨١“Perekani muyeso oyenera ndipo musachepetse.” وَزِنُواْ بِٱلۡقِسۡطَاسِ ٱلۡمُسۡتَقِيمِ ١٨٢“Yesani ndi miyeso yabwino.” وَلَا تَبۡخَسُواْ ٱلنَّاسَ أَشۡيَآءَهُمۡ وَلَا تَعۡثَوۡاْ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُفۡسِدِينَ ١٨٣“Ndipo musawachepetsere anthu zinthu zawo kapena kulowetsa chisokonezo m’dziko.” وَٱتَّقُواْ ٱلَّذِي خَلَقَكُمۡ وَٱلۡجِبِلَّةَ ٱلۡأَوَّلِينَ ١٨٤“Muopeni Iye amene adakulengani inu ndi mibadwo yakale.” قَالُوٓاْ إِنَّمَآ أَنتَ مِنَ ٱلۡمُسَحَّرِينَ ١٨٥Iwo adati, “Ndithudi iwe walodzedwa.” وَمَآ أَنتَ إِلَّا بَشَرٌ مِّثۡلُنَا وَإِن نَّظُنُّكَ لَمِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ ١٨٦“Iwe ndiwe munthu wolingana ndi ife. Ndithudi ife tili kuganiza kuti iwe uli kunama.” فَأَسۡقِطۡ عَلَيۡنَا كِسَفًا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ ١٨٧“Tigwetsere mtambo kuchokera kumwamba ngati zimene uli kunena ndi zoonadi.” قَالَ رَبِّيٓ أَعۡلَمُ بِمَا تَعۡمَلُونَ ١٨٨Iye adati, “Ambuye wanga amadziwa kwambiri chimene inu mumachita.” فَكَذَّبُوهُ فَأَخَذَهُمۡ عَذَابُ يَوۡمِ ٱلظُّلَّةِۚ إِنَّهُۥ كَانَ عَذَابَ يَوۡمٍ عَظِيمٍ ١٨٩Iwo adamukana iye kotero chilango cha thambo ndi moto chidawaononga. Ichi chidali chilango cha tsiku loopsa إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةًۖ وَمَا كَانَ أَكۡثَرُهُم مُّؤۡمِنِينَ ١٩٠Ndithudi mu chimenechi muli chiphunzitso koma ambiri a iwo sakhulupirira وَإِنَّ رَبَّكَ لَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ ١٩١Ndithudi Ambuye wako ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha وَإِنَّهُۥ لَتَنزِيلُ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ١٩٢Buku lolemekezekali lavumbulutsidwa ndi Ambuye wa zolengedwa zonse نَزَلَ بِهِ ٱلرُّوحُ ٱلۡأَمِينُ ١٩٣Mzimu wokhulupirika udabweretsa Bukuli عَلَىٰ قَلۡبِكَ لِتَكُونَ مِنَ ٱلۡمُنذِرِينَ ١٩٤Ku mtima wako kuti ukhoza kuchenjeza mitundu ya anthu بِلِسَانٍ عَرَبِيٍّ مُّبِينٍ ١٩٥Mu chinenero chomveka cha Chiarabu وَإِنَّهُۥ لَفِي زُبُرِ ٱلۡأَوَّلِينَ ١٩٦Ndithudi lili kupezeka mu mawu a Mulungu akale أَوَلَمۡ يَكُن لَّهُمۡ ءَايَةً أَن يَعۡلَمَهُۥ عُلَمَٰٓؤُاْ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ١٩٧Kodi si chizindikiro kwa iwo kuti anthu ophunzira a ana a Israyeli amalidziwa وَلَوۡ نَزَّلۡنَٰهُ عَلَىٰ بَعۡضِ ٱلۡأَعۡجَمِينَ ١٩٨Ngati Ife tikadaivumbulutsa kwa munthu wa mtundu wina uliwonse yemwesi wa Chiarabu فَقَرَأَهُۥ عَلَيۡهِم مَّا كَانُواْ بِهِۦ مُؤۡمِنِينَ ١٩٩Kuti iye ailakatule kwa iwo ndipo sakadakhulupirira iwo mwa Bukulo كَذَٰلِكَ سَلَكۡنَٰهُ فِي قُلُوبِ ٱلۡمُجۡرِمِينَ ٢٠٠Kotero Ife tidaipanga iyo kuti ilowe m’mitima ya anthu ochitazoipa لَا يُؤۡمِنُونَ بِهِۦ حَتَّىٰ يَرَوُاْ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَلِيمَ ٢٠١Iwosadzakhulupiriramuilompakapamene adzaona chilango chowawa فَيَأۡتِيَهُم بَغۡتَةً وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ ٢٠٢Ndipo icho chidzadza kwa iwo mwadzidzidzi pamene iwo sakudziwa فَيَقُولُواْ هَلۡ نَحۡنُ مُنظَرُونَ ٢٠٣Ndipo iwo adzati, “Kodi ife sitidzapatsidwanso nthawi?” أَفَبِعَذَابِنَا يَسۡتَعۡجِلُونَ ٢٠٤Kodi iwo angafune kuti chilango chathu chidze msanga أَفَرَءَيۡتَ إِن مَّتَّعۡنَٰهُمۡ سِنِينَ ٢٠٥Tandiuza. Ngati Ife titawalola kukhala mu mtendere wa zaka zambiri ثُمَّ جَآءَهُم مَّا كَانُواْ يُوعَدُونَ ٢٠٦Ndipo pambuyo pake chilango chimene chidalonjezedwa chidza pa iwo مَآ أَغۡنَىٰ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يُمَتَّعُونَ ٢٠٧Chisangalalo chawo chimene adapatsidwa chidzakhala chopanda phindu وَمَآ أَهۡلَكۡنَا مِن قَرۡيَةٍ إِلَّا لَهَا مُنذِرُونَ ٢٠٨Palibe mtundu wa anthu umene tidaonongapo kale umene sitidautumizire owachenjeza ذِكۡرَىٰ وَمَا كُنَّا ظَٰلِمِينَ ٢٠٩Monga chenjezo ndipo Ife si ndife opondereza ayi وَمَا تَنَزَّلَتۡ بِهِ ٱلشَّيَٰطِينُ ٢١٠Si a Satana amene adabweretsa Korani ino ayi وَمَا يَنۢبَغِي لَهُمۡ وَمَا يَسۡتَطِيعُونَ ٢١١Si koyenera kwa iwo ndiponso sangathe kutero إِنَّهُمۡ عَنِ ٱلسَّمۡعِ لَمَعۡزُولُونَ ٢١٢Ndithudi iwo amanidwa kumva za Bukuli فَلَا تَدۡعُ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ فَتَكُونَ مِنَ ٱلۡمُعَذَّبِينَ ٢١٣Musapembedze milungu ina kuonjezera pa Mulungu weniweni chifukwa mukatero mudzakhala m’gulu limene lidzalangidwa وَأَنذِرۡ عَشِيرَتَكَ ٱلۡأَقۡرَبِينَ ٢١٤Achenjeze abale ako amene ali pafupi ndi iwe وَٱخۡفِضۡ جَنَاحَكَ لِمَنِ ٱتَّبَعَكَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٢١٥Ndipo onetsa chifundo kwa anthu okhulupirira amene amakutsatira iwe فَإِنۡ عَصَوۡكَ فَقُلۡ إِنِّي بَرِيٓءٌ مِّمَّا تَعۡمَلُونَ ٢١٦Ngati iwo sakumvera iwe, unene kuti, “Ine sindidzaimbidwa mlandu chifukwa cha zimene mumachita.” وَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱلۡعَزِيزِ ٱلرَّحِيمِ ٢١٧Ika chikhulupiriro chako mwa Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha ٱلَّذِي يَرَىٰكَ حِينَ تَقُومُ ٢١٨Amene amakuona pamene umaimirira popemphera وَتَقَلُّبَكَ فِي ٱلسَّٰجِدِينَ ٢١٩Ndi machitidwe ako pakati pa anthu opemphera إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ ٢٢٠Mulungu amamva chilichonse ndipo amadziwa china chilichonse هَلۡ أُنَبِّئُكُمۡ عَلَىٰ مَن تَنَزَّلُ ٱلشَّيَٰطِينُ ٢٢١Kodi ndi kuuzeni za munthu amene Satana amamutsikira تَنَزَّلُ عَلَىٰ كُلِّ أَفَّاكٍ أَثِيمٍ ٢٢٢Iwo amadza pa munthu wabodza ndi wochimwa يُلۡقُونَ ٱلسَّمۡعَ وَأَكۡثَرُهُمۡ كَٰذِبُونَ ٢٢٣Iwo amamvera mabodza okhaokha ndipo komaambiriaiwondiabodza وَٱلشُّعَرَآءُ يَتَّبِعُهُمُ ٱلۡغَاوُۥنَ ٢٢٤Alakatuliamatsatidwandi anthu ochita zoipa أَلَمۡ تَرَ أَنَّهُمۡ فِي كُلِّ وَادٍ يَهِيمُونَ ٢٢٥Kodi simuona kuti iwo amangonena nkhani iliyonse mu zolakatula zawo وَأَنَّهُمۡ يَقُولُونَ مَا لَا يَفۡعَلُونَ ٢٢٦Ndipo iwo amakamba zinthu zimene iwo sachita إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَذَكَرُواْ ٱللَّهَ كَثِيرًا وَٱنتَصَرُواْ مِنۢ بَعۡدِ مَا ظُلِمُواْۗ وَسَيَعۡلَمُ ٱلَّذِينَ ظَلَمُوٓاْ أَيَّ مُنقَلَبٍ يَنقَلِبُونَ ٢٢٧Kupatula okhawo amene akhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino ndi kumakumbukira Mulungu kwambiri ndi kudziteteza pambuyo pa kuponderezedwa. Ndipo iwo amene amachita zoipa adzadziwa chimene chidzawagadabuza