بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
وَٱلصَّٰٓفَّٰتِ صَفًّا ١Pali iwo amene amasonkhana kukhala pa maudindo osiyanasiyana فَٱلزَّٰجِرَٰتِ زَجۡرًا ٢Pali iwo amene amayendetsa mitambo mwa ubwino فَٱلتَّٰلِيَٰتِ ذِكۡرًا ٣Pali iwo amene amabweretsa m’Buku ndi Korani kuchokera kwa Mulungu kupita nalo kwa anthu ake إِنَّ إِلَٰهَكُمۡ لَوَٰحِدٌ ٤Ndithudi Mulungu wanu ndi mmodzi yekha رَّبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا وَرَبُّ ٱلۡمَشَٰرِقِ ٥Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndi wa zonse zimene zili m’menemo ndi Ambuye wa dera lililonse lotulukira dzuwa إِنَّا زَيَّنَّا ٱلسَّمَآءَ ٱلدُّنۡيَا بِزِينَةٍ ٱلۡكَوَاكِبِ ٦Ndithudi Ife tidakongoletsa mtambo woyandikira kwambiri ndi nyenyezi وَحِفۡظًا مِّن كُلِّ شَيۡطَٰنٍ مَّارِدٍ ٧Ndi kulonda Satana wofukira لَّا يَسَّمَّعُونَ إِلَى ٱلۡمَلَإِ ٱلۡأَعۡلَىٰ وَيُقۡذَفُونَ مِن كُلِّ جَانِبٍ ٨Kotero iwo sangathe kumvetsera zokambidwa za gulu lapamwamba chifukwa iwo amapirikitsidwa kuchokera kumbali iliyonse دُحُورًاۖ وَلَهُمۡ عَذَابٌ وَاصِبٌ ٩Atapirikitsidwa, chawo chidzakhala chilango chosatha إِلَّا مَنۡ خَطِفَ ٱلۡخَطۡفَةَ فَأَتۡبَعَهُۥ شِهَابٌ ثَاقِبٌ ١٠Kupatula yekhayo amene amakwatula zinthu mwakuba, ndipo amathamangitsidwa ndi moto woyaka ndi wowala kwambiri فَٱسۡتَفۡتِهِمۡ أَهُمۡ أَشَدُّ خَلۡقًا أَم مَّنۡ خَلَقۡنَآۚ إِنَّا خَلَقۡنَٰهُم مِّن طِينٍ لَّازِبِۭ ١١Ndipo tawafunsa, “Kodi iwo ndi a mphamvu kuposa zolengedwa zina zimene tidalenga?” Iwo tidawalenga kuchokera ku dothi lonyata la makande بَلۡ عَجِبۡتَ وَيَسۡخَرُونَ ١٢Iyayi, iwe udadabwa pamene iwo anali kunyoza وَإِذَا ذُكِّرُواْ لَا يَذۡكُرُونَ ١٣Ndipo iwo akamaweruzidwa, iwo safuna kuweruzidwa وَإِذَا رَأَوۡاْ ءَايَةً يَسۡتَسۡخِرُونَ ١٤Ndipo iwo akaona chizindikiro chochokera kwa Mulungu amachisandutsa ngati chinthu choseweretsa وَقَالُوٓاْ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا سِحۡرٌ مُّبِينٌ ١٥Ndipo amati, “Ichi si china ayi koma matsenga woonekera poyera.” أَءِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابًا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ ١٦“Chiyani! Ife tikafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, kodi tidzaukitsidwa?” أَوَءَابَآؤُنَا ٱلۡأَوَّلُونَ ١٧“Ndiponso makolo athu amakedzana?” قُلۡ نَعَمۡ وَأَنتُمۡ دَٰخِرُونَ ١٨Nena, “Inde mudzachititsidwa manyazi.” فَإِنَّمَا هِيَ زَجۡرَةٌ وَٰحِدَةٌ فَإِذَا هُمۡ يَنظُرُونَ ١٩Ndipo udzakhala mfuwu umodzi ndipo taona iwo adzakhala ali kupenyetsetsana وَقَالُواْ يَٰوَيۡلَنَا هَٰذَا يَوۡمُ ٱلدِّينِ ٢٠Iwo adzati, “Tsoka kwa ife! Ili ndi tsiku lachiweruzo.” هَٰذَا يَوۡمُ ٱلۡفَصۡلِ ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تُكَذِّبُونَ ٢١“Ili ndi tsiku lachiweruzo limene inu mumati ndi bodza.” ۞ ٱحۡشُرُواْ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ وَأَزۡوَٰجَهُمۡ وَمَا كَانُواْ يَعۡبُدُونَ ٢٢(Kudzanenedwa kuti); “Bweretsani anthu ochimwa pamodzi ndi anzawo ndi zinthu zimene iwo anali kupembedza.” مِن دُونِ ٱللَّهِ فَٱهۡدُوهُمۡ إِلَىٰ صِرَٰطِ ٱلۡجَحِيمِ ٢٣“Kuonjezera pa Mulungu weniweni ndipo atsogolereni ku njira ya kumoto.” وَقِفُوهُمۡۖ إِنَّهُم مَّسۡـُٔولُونَ ٢٤“Ndipo aimitseni. Ndithudi, iwo ayenera kufunsidwa.” مَا لَكُمۡ لَا تَنَاصَرُونَ ٢٥“Kodi mwatani? Nanga ndi chifukwa chiyani inu simuli kuthandizana?” بَلۡ هُمُ ٱلۡيَوۡمَ مُسۡتَسۡلِمُونَ ٢٦Iyayi! Koma iwo lero ndi odzipereka وَأَقۡبَلَ بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٍ يَتَسَآءَلُونَ ٢٧Ndipo iwo adzafunsana wina ndi mnzake قَالُوٓاْ إِنَّكُمۡ كُنتُمۡ تَأۡتُونَنَا عَنِ ٱلۡيَمِينِ ٢٨Iwo adzati, “Ndinu amene munali kubwera kwa ife kuchokera kudzanja lamanja.” قَالُواْ بَل لَّمۡ تَكُونُواْ مُؤۡمِنِينَ ٢٩Iwo adzayankha kuti, “Iyayi, Inuyo simunali okhulupirira.” وَمَا كَانَ لَنَا عَلَيۡكُم مِّن سُلۡطَٰنِۭۖ بَلۡ كُنتُمۡ قَوۡمًا طَٰغِينَ ٣٠“Ndipo ife tidalibe ulamuliro pa inu. Iyayi! Inu mudali osamva.” فَحَقَّ عَلَيۡنَا قَوۡلُ رَبِّنَآۖ إِنَّا لَذَآئِقُونَ ٣١“Kotero chiweruzo cha Ambuye wathu chadza pa ife. Ndithudi tsopano tidzachilawa.” فَأَغۡوَيۡنَٰكُمۡ إِنَّا كُنَّا غَٰوِينَ ٣٢“Choncho ife tidakusocheretsani chifukwa nafenso tidali osochera.” فَإِنَّهُمۡ يَوۡمَئِذٍ فِي ٱلۡعَذَابِ مُشۡتَرِكُونَ ٣٣Ndipo, ndithudi, patsiku limeneli onse adzalandirana chilango pakati pa wina ndi mnzake إِنَّا كَذَٰلِكَ نَفۡعَلُ بِٱلۡمُجۡرِمِينَ ٣٤Ndithudi mmenemo ndi mmene timachitira ndi anthu olakwa إِنَّهُمۡ كَانُوٓاْ إِذَا قِيلَ لَهُمۡ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا ٱللَّهُ يَسۡتَكۡبِرُونَ ٣٥Ndithudi pamene iwo, adauzidwa kuti, “Kulibe mulungu wina koma Mulungu weniweni, iwo anali kudzitukumula.” وَيَقُولُونَ أَئِنَّا لَتَارِكُوٓاْ ءَالِهَتِنَا لِشَاعِرٍ مَّجۡنُونِۭ ٣٦Ndipo adanena kuti, “Kodi ife tisiye milungu yathu chifukwa cha Mlakatuli wamisala?” بَلۡ جَآءَ بِٱلۡحَقِّ وَصَدَّقَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ٣٧Iyayi. Iye wadza ndi choonadi ndipo ali kutsimikizira uthenga wa Atumwi amene adadza kale إِنَّكُمۡ لَذَآئِقُواْ ٱلۡعَذَابِ ٱلۡأَلِيمِ ٣٨Ndithudi, inu mudzalangidwa kwambiri وَمَا تُجۡزَوۡنَ إِلَّا مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ ٣٩Ndipo inu mudzalandira mphotho molingana ndi ntchito zanu إِلَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ ٤٠Kupatula akapolo osankhidwa a Mulungu أُوْلَٰٓئِكَ لَهُمۡ رِزۡقٌ مَّعۡلُومٌ ٤١Kwa iwo mphotho yawo ndi yodziwika فَوَٰكِهُ وَهُم مُّكۡرَمُونَ ٤٢Zipatso ndipo iwo adzalemekezeka kwambiri فِي جَنَّٰتِ ٱلنَّعِيمِ ٤٣M’minda ya chisangalalo عَلَىٰ سُرُرٍ مُّتَقَٰبِلِينَ ٤٤Atakhala pa mipando ya chifumu moyang’anizana يُطَافُ عَلَيۡهِم بِكَأۡسٍ مِّن مَّعِينِۭ ٤٥Pakati pawo padzaperekedwa chikho cha vinyo wabwino بَيۡضَآءَ لَذَّةٍ لِّلشَّٰرِبِينَ ٤٦oyera ndiponso okoma kwa iwo amene amamwa لَا فِيهَا غَوۡلٌ وَلَا هُمۡ عَنۡهَا يُنزَفُونَ ٤٧Simudzakhala mavuto mu icho ndipo sichidzawatopetsa وَعِندَهُمۡ قَٰصِرَٰتُ ٱلطَّرۡفِ عِينٌ ٤٨Ndipo pakati pawo padzakhala akazi angwiro opanda chimasomaso كَأَنَّهُنَّ بَيۡضٌ مَّكۡنُونٌ ٤٩Okhala ngati mazira osamalidwa bwino فَأَقۡبَلَ بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٍ يَتَسَآءَلُونَ ٥٠Ndipo adzadza kwa anzawo ndi kumafunsana wina ndi mnzake قَالَ قَآئِلٌ مِّنۡهُمۡ إِنِّي كَانَ لِي قَرِينٌ ٥١Wina wochokera pakati pawo adzayankhula nati, “Ndithudi ine ndinali ndi bwenzi langa.” يَقُولُ أَءِنَّكَ لَمِنَ ٱلۡمُصَدِّقِينَ ٥٢“Amene amakonda kunena kuti; “Kodi ndiwe mmodzi mwa okhulupirira?” أَءِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابًا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَدِينُونَ ٥٣“Kodi ife tikafa ndi kusanduka dothi ndi mafupa, tidzatengedwa kupita ku chiweruzo قَالَ هَلۡ أَنتُم مُّطَّلِعُونَ ٥٤Iye adati, “Kodi iwe ungaone pansi?” فَٱطَّلَعَ فَرَءَاهُ فِي سَوَآءِ ٱلۡجَحِيمِ ٥٥Motero adayang’ana pansi ndipo adamuona iye ali pakati pa moto wa ku Gahena قَالَ تَٱللَّهِ إِن كِدتَّ لَتُرۡدِينِ ٥٦Iye adati, “Pali Mulungu! Iwe udatsala pang’ono kundipweteka.” وَلَوۡلَا نِعۡمَةُ رَبِّي لَكُنتُ مِنَ ٱلۡمُحۡضَرِينَ ٥٧“Ndipo kukadapanda chisomo cha Ambuye wanga ine, ndithudi, ndikadakhala mmodzi wa iwo.” أَفَمَا نَحۡنُ بِمَيِّتِينَ ٥٨“Kodi ndiye kuti ife sitidzafa?” إِلَّا مَوۡتَتَنَا ٱلۡأُولَىٰ وَمَا نَحۡنُ بِمُعَذَّبِينَ ٥٩“Kupatula kufa koyamba, kodi ife sitidzalangidwa?” إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ ٱلۡفَوۡزُ ٱلۡعَظِيمُ ٦٠Ndithudi uku ndiko kupambana kwenikweni لِمِثۡلِ هَٰذَا فَلۡيَعۡمَلِ ٱلۡعَٰمِلُونَ ٦١Pofuna kupeza zotere, alekereni alimbikire amene akufuna kuti alimbikirewo أَذَٰلِكَ خَيۡرٌ نُّزُلًا أَمۡ شَجَرَةُ ٱلزَّقُّومِ ٦٢Kodi chimenechi ndi chabwino kapena mtengo wa Zaqqum إِنَّا جَعَلۡنَٰهَا فِتۡنَةً لِّلظَّٰلِمِينَ ٦٣Ndithudi tazipanga izi kukhala mayesero kwa anthu olakwa إِنَّهَا شَجَرَةٌ تَخۡرُجُ فِيٓ أَصۡلِ ٱلۡجَحِيمِ ٦٤Ndithudi umenewu ndi mtengo umene umamera pansi pa Gahena طَلۡعُهَا كَأَنَّهُۥ رُءُوسُ ٱلشَّيَٰطِينِ ٦٥Zipatso zake zili ngati mitu ya a Satana فَإِنَّهُمۡ لَأٓكِلُونَ مِنۡهَا فَمَالِـُٔونَ مِنۡهَا ٱلۡبُطُونَ ٦٦Ndithudi iwo adzadya zimenezi ndi kukhutitsa mimba zawo ndi zipatsozo ثُمَّ إِنَّ لَهُمۡ عَلَيۡهَا لَشَوۡبًا مِّنۡ حَمِيمٍ ٦٧Ndithudi iwo akadzadya, adzamwa chakumwa chokonzedwa ndi madzi owira ثُمَّ إِنَّ مَرۡجِعَهُمۡ لَإِلَى ٱلۡجَحِيمِ ٦٨Ndithudi iwo adzapita ku Gahena إِنَّهُمۡ أَلۡفَوۡاْ ءَابَآءَهُمۡ ضَآلِّينَ ٦٩Ndithudi iwo adapeza makolo awo ali osochera فَهُمۡ عَلَىٰٓ ءَاثَٰرِهِمۡ يُهۡرَعُونَ ٧٠Kotero iwo ali kutsatira mapazi awo وَلَقَدۡ ضَلَّ قَبۡلَهُمۡ أَكۡثَرُ ٱلۡأَوَّلِينَ ٧١Ndithudi makolo awo adasochera iwo asanadze وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا فِيهِم مُّنذِرِينَ ٧٢Ndipo, ndithudi, ife tidatumiza Atumwi pakati pawo فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُنذَرِينَ ٧٣Ndipo taona zimene zidadza kwa iwo amene adachenjezedwa إِلَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ ٧٤Kupatula akapolo osankhidwa a Mulungu omwe ndi anthu olungama وَلَقَدۡ نَادَىٰنَا نُوحٌ فَلَنِعۡمَ ٱلۡمُجِيبُونَ ٧٥Ndipo ndithudi Nowa adatipempha Ife ndipo Ife timayankha bwino pa amene amayankha وَنَجَّيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥ مِنَ ٱلۡكَرۡبِ ٱلۡعَظِيمِ ٧٦Ndipo Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi banja lake ku chilango choopsa وَجَعَلۡنَا ذُرِّيَّتَهُۥ هُمُ ٱلۡبَاقِينَ ٧٧Ndipo tidapulumutsanso ana ake وَتَرَكۡنَا عَلَيۡهِ فِي ٱلۡأٓخِرِينَ ٧٨Ndipo tidakhazikitsa ulemu pa iye pakati pa mitundu yonse yamtsogolo سَلَٰمٌ عَلَىٰ نُوحٍ فِي ٱلۡعَٰلَمِينَ ٧٩Mtendere ukhale kwa Nowa kuchokera kwa zolengedwa zonse إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ ٨٠Ndithudi mmenemo ndi mmene timalipirira anthu ochita zabwino إِنَّهُۥ مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٨١Ndithudi iye adali mmodzi mwa akapolo athu okhulupirira ثُمَّ أَغۡرَقۡنَا ٱلۡأٓخَرِينَ ٨٢Ndipo ena onse tidawamiza ۞ وَإِنَّ مِن شِيعَتِهِۦ لَإِبۡرَٰهِيمَ ٨٣Ndithudi pakati pa iwo amene amatsatira njira yake adali Abrahamu إِذۡ جَآءَ رَبَّهُۥ بِقَلۡبٍ سَلِيمٍ ٨٤Pamene iye adadza kwa Ambuye wake ndi mtima woyera إِذۡ قَالَ لِأَبِيهِ وَقَوۡمِهِۦ مَاذَا تَعۡبُدُونَ ٨٥Pamene iye adati kwa atate wake ndi anthu a mtundu wake, “Kodi ndi chiyani chimene inu muli kupembedza?” أَئِفۡكًا ءَالِهَةً دُونَ ٱللَّهِ تُرِيدُونَ ٨٦“Kodi mukufuna milungu yabodza kapena Mulungu weniweni?” فَمَا ظَنُّكُم بِرَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ٨٧“Kodi mukuganiza zotani za Ambuye wa zolengedwa zonse?” فَنَظَرَ نَظۡرَةً فِي ٱلنُّجُومِ ٨٨Ndipo iye adayang’ana nyenyezi فَقَالَ إِنِّي سَقِيمٌ ٨٩Ndipo iye adati, “Ndithudi ndili kudwala.” فَتَوَلَّوۡاْ عَنۡهُ مُدۡبِرِينَ ٩٠Kotero iwo adamusiya ndi kubwerera فَرَاغَ إِلَىٰٓ ءَالِهَتِهِمۡ فَقَالَ أَلَا تَأۡكُلُونَ ٩١Ndipoiyeadayang’anakwamilunguyawonati, “Kodi inu simudya?” مَا لَكُمۡ لَا تَنطِقُونَ ٩٢“Kodi bwanji inu simuyankhula?” فَرَاغَ عَلَيۡهِمۡ ضَرۡبَۢا بِٱلۡيَمِينِ ٩٣Ndipo iye adadza pafupi ndi iyo ndi kuigwetsa ndi dzanja lake lamanja فَأَقۡبَلُوٓاْ إِلَيۡهِ يَزِفُّونَ ٩٤Nthawi yomweyo wopembedza mafano adadza kwa iye mwamsangamsanga قَالَ أَتَعۡبُدُونَ مَا تَنۡحِتُونَ ٩٥Iye adati, “Kodi mumapembedza zinthu zimene inu mwasema?” وَٱللَّهُ خَلَقَكُمۡ وَمَا تَعۡمَلُونَ ٩٦“Pamene Mulungu ndiye amene adakulengani inu pamodzi ndi zosemasema zanuzi!” قَالُواْ ٱبۡنُواْ لَهُۥ بُنۡيَٰنًا فَأَلۡقُوهُ فِي ٱلۡجَحِيمِ ٩٧Iwo adati, “Mupangireni ng’anjo ndipo muponyeni m’moto woyaka!” فَأَرَادُواْ بِهِۦ كَيۡدًا فَجَعَلۡنَٰهُمُ ٱلۡأَسۡفَلِينَ ٩٨Iwo adachita chiwembu koma Ife tidawachititsa manyazi وَقَالَ إِنِّي ذَاهِبٌ إِلَىٰ رَبِّي سَيَهۡدِينِ ٩٩Ndipo iye adati, “Ine ndithawira kwa Ambuye wanga. Ndipo Iye adzanditsogolera ine.” رَبِّ هَبۡ لِي مِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ ١٠٠“Ambuye wanga! Ndipatseni ana kuchokera kwa ochita ntchito zabwino.” فَبَشَّرۡنَٰهُ بِغُلَٰمٍ حَلِيمٍ ١٠١Ndipo Ife tidamuuza nkhani yabwino ya mwana wamwamuna wopirira فَلَمَّا بَلَغَ مَعَهُ ٱلسَّعۡيَ قَالَ يَٰبُنَيَّ إِنِّيٓ أَرَىٰ فِي ٱلۡمَنَامِ أَنِّيٓ أَذۡبَحُكَ فَٱنظُرۡ مَاذَا تَرَىٰۚ قَالَ يَٰٓأَبَتِ ٱفۡعَلۡ مَا تُؤۡمَرُۖ سَتَجِدُنِيٓ إِن شَآءَ ٱللَّهُ مِنَ ٱلصَّٰبِرِينَ ١٠٢Ndipo pamene iye adakula mofika pa msinkhu woti angathe kuthandiza abambo ake, iye adati: “Mwana wanga! Ndithudi ine ndalota ndili kukupha ngati nsembe. Taganiza zimene uli kuziona.” Iye adati, “Atate wanga! Inu chitani monga momwe mwalamulidwira. Ngati Mulungu afuna, mudzandipeza ine wopirira!” فَلَمَّآ أَسۡلَمَا وَتَلَّهُۥ لِلۡجَبِينِ ١٠٣Ndipo pamene onse adadzipereka, ndipo adamugoneka iye chafufumimba وَنَٰدَيۡنَٰهُ أَن يَٰٓإِبۡرَٰهِيمُ ١٠٤Ndipo Ife tidamuitana ndipo tidati, “Iwe Abrahamu!” قَدۡ صَدَّقۡتَ ٱلرُّءۡيَآۚ إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ ١٠٥“Ndithudi wakwaniritsa maloto ako.” Ndithudi mmenemo ndi mmene timaperekera mphotho kwa anthu ochita zabwino إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ ٱلۡبَلَٰٓؤُاْ ٱلۡمُبِينُ ١٠٦Ndithudi awa adali mayesero oonekeratu وَفَدَيۡنَٰهُ بِذِبۡحٍ عَظِيمٍ ١٠٧Ndipo tidamupatsa iye nsembe yaikulu وَتَرَكۡنَا عَلَيۡهِ فِي ٱلۡأٓخِرِينَ ١٠٨Ndipo Ife tidakhazikitsa ulemu pa iye pakati pa mibadwo yamtsogolo سَلَٰمٌ عَلَىٰٓ إِبۡرَٰهِيمَ ١٠٩Mtendere ukhale pa Abrahamu كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ ١١٠Mmenemo ndi mmene timalipira mphotho kwa anthu ochita zabwino إِنَّهُۥ مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ١١١Ndithudi iye adali mmodzi wa akapolo athu okhulupirira وَبَشَّرۡنَٰهُ بِإِسۡحَٰقَ نَبِيًّا مِّنَ ٱلصَّٰلِحِينَ ١١٢Ndipo Ife tidamuuza nkhani yabwino ya Isake, Mtumwi, wochokera pakati pa anthu okhulupirira وَبَٰرَكۡنَا عَلَيۡهِ وَعَلَىٰٓ إِسۡحَٰقَۚ وَمِن ذُرِّيَّتِهِمَا مُحۡسِنٌ وَظَالِمٌ لِّنَفۡسِهِۦ مُبِينٌ ١١٣Ndipo Ife tidaika madalitso athu pa iye ndi pa Isake. Ndipo pakati pa ana awo pali ena ochita ntchito zabwino ndi ena amene ndi olakwa ndipo amadzipondereza okha وَلَقَدۡ مَنَنَّا عَلَىٰ مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ ١١٤Ndipo, ndithudi, Ife tidaonetsa chisomo chathu kwa Mose ndi Aroni وَنَجَّيۡنَٰهُمَا وَقَوۡمَهُمَا مِنَ ٱلۡكَرۡبِ ٱلۡعَظِيمِ ١١٥Ndipo tidawapulumutsa onse pamodzi ndi anthu awo ku mavuto oopsa وَنَصَرۡنَٰهُمۡ فَكَانُواْ هُمُ ٱلۡغَٰلِبِينَ ١١٦Ndipo Ife tidawathandiza kotero adali opambana وَءَاتَيۡنَٰهُمَا ٱلۡكِتَٰبَ ٱلۡمُسۡتَبِينَ ١١٧Ndipo Ife tidawapatsa Buku Lopatulika limene limathandiza kufotokoza zinthu momveka bwino وَهَدَيۡنَٰهُمَا ٱلصِّرَٰطَ ٱلۡمُسۡتَقِيمَ ١١٨Ndipo Ife tidawatsogolera ku njira yoyenera وَتَرَكۡنَا عَلَيۡهِمَا فِي ٱلۡأٓخِرِينَ ١١٩Ndipo Ife tidakhazikitsa ulemu kwa iwo pakati pa mibadwo ya mtsogolo سَلَٰمٌ عَلَىٰ مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ ١٢٠“Mtendere ukhale pa Mose ndi Aroni.” إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ ١٢١Ndithudi mmenemo ndi mmene timaperekera mphotho kwa anthu ochita ntchito zabwino إِنَّهُمَا مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ١٢٢Ndithudi onse adali akapolo athu okhulupirira وَإِنَّ إِلۡيَاسَ لَمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ١٢٣Ndithudi Eliya anali mmodzi wa Atumwi إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِۦٓ أَلَا تَتَّقُونَ ١٢٤Pamene, iye adati kwa anthu ake, “Kodi inu simungaope Mulungu?” أَتَدۡعُونَ بَعۡلًا وَتَذَرُونَ أَحۡسَنَ ٱلۡخَٰلِقِينَ ١٢٥“Kodi muli kupembedza Bala ndi kusiya kupembedza Namalenga?” ٱللَّهَ رَبَّكُمۡ وَرَبَّ ءَابَآئِكُمُ ٱلۡأَوَّلِينَ ١٢٦“Mulungu, Ambuye wanu ndi Ambuye wa makolo anu akale?” فَكَذَّبُوهُ فَإِنَّهُمۡ لَمُحۡضَرُونَ ١٢٧Koma iwo adamukana iye ndipo ndithudi, iwo adzatengedwa إِلَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ ١٢٨Kupatula akapolo osankhidwa a Mulungu وَتَرَكۡنَا عَلَيۡهِ فِي ٱلۡأٓخِرِينَ ١٢٩Ndithudi tidakhazikitsa ulemu kwa iye pakati pa mibadwo ya patsogolo سَلَٰمٌ عَلَىٰٓ إِلۡ يَاسِينَ ١٣٠“Mtendere ukhale ndi Eliya.” إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ ١٣١Ndithudi mmenemo ndi mmene timaperekera mphotho kwa anthu ochita ntchito zabwino إِنَّهُۥ مِنۡ عِبَادِنَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ١٣٢Ndithudi iye adali mmodzi wa akopolo athu okhulupirira وَإِنَّ لُوطًا لَّمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ١٣٣Ndipo Loti adali mmodzi wa Atumwi إِذۡ نَجَّيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥٓ أَجۡمَعِينَ ١٣٤Pamene, Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi onse omutsatira إِلَّا عَجُوزًا فِي ٱلۡغَٰبِرِينَ ١٣٥Kupatula mayi mmodzi wokalamba amene adali m’gulu la anthu otsalira m’mbuyo ثُمَّ دَمَّرۡنَا ٱلۡأٓخَرِينَ ١٣٦Ndipo Ife tidawaononga onse وَإِنَّكُمۡ لَتَمُرُّونَ عَلَيۡهِم مُّصۡبِحِينَ ١٣٧Ndithudi inu mumawadutsa nthawi ya m’mawa وَبِٱلَّيۡلِۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ ١٣٨Ndi nthawi yausiku, kodi inu simungazindikire وَإِنَّ يُونُسَ لَمِنَ ٱلۡمُرۡسَلِينَ ١٣٩Ndipo, ndithudi, Yona adali mmodzi wa Atumwi إِذۡ أَبَقَ إِلَى ٱلۡفُلۡكِ ٱلۡمَشۡحُونِ ١٤٠Pamene iye adathawa kupita ku chombo chodzadza kwambiri ndi katundu فَسَاهَمَ فَكَانَ مِنَ ٱلۡمُدۡحَضِينَ ١٤١Iye adachita nawo mayere koma iye adali mmodzi wa olephera فَٱلۡتَقَمَهُ ٱلۡحُوتُ وَهُوَ مُلِيمٌ ١٤٢Ndipo nsomba idamumeza iye chifukwa adalakwa فَلَوۡلَآ أَنَّهُۥ كَانَ مِنَ ٱلۡمُسَبِّحِينَ ١٤٣Koma kukadakhala kuti sadapemphe chikhululukiro cha Mulungu wolemekezeka لَلَبِثَ فِي بَطۡنِهِۦٓ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ ١٤٤Ndithudi iye akadakhalabe m’mimba mwa nsomba mpaka tsiku la kuuka kwa akufa ۞ فَنَبَذۡنَٰهُ بِٱلۡعَرَآءِ وَهُوَ سَقِيمٌ ١٤٥Koma Ife tidakamuponya pa mtunda pamene iye anali kudwala وَأَنۢبَتۡنَا عَلَيۡهِ شَجَرَةً مِّن يَقۡطِينٍ ١٤٦Ndipo Ife tidameretsa chitsamba cha chipanda kuti chimere pamwamba pake وَأَرۡسَلۡنَٰهُ إِلَىٰ مِاْئَةِ أَلۡفٍ أَوۡ يَزِيدُونَ ١٤٧Ndipo tidamutumiza kwa anthu zikwi makumi khumi kapena kuposa apa فَـَٔامَنُواْ فَمَتَّعۡنَٰهُمۡ إِلَىٰ حِينٍ ١٤٨Ndipo onse adakhulupirira ndipo Ife tidawapatsa chisangalalo cha kanthawi kochepa فَٱسۡتَفۡتِهِمۡ أَلِرَبِّكَ ٱلۡبَنَاتُ وَلَهُمُ ٱلۡبَنُونَ ١٤٩Ndipo tsopano afunseni kuti, “Kodi Ambuye wako ali ndi ana أَمۡ خَلَقۡنَا ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ إِنَٰثًا وَهُمۡ شَٰهِدُونَ ١٥٠Kapena kuti Ife tidalenga angelo kukhala akazi pamene iwo anali kuona أَلَآ إِنَّهُم مِّنۡ إِفۡكِهِمۡ لَيَقُولُونَ ١٥١Kodi iwo sanena zabodza pamene amati وَلَدَ ٱللَّهُ وَإِنَّهُمۡ لَكَٰذِبُونَ ١٥٢“Mulungu wabereka mwana?” Ndithudi iwo ndi abodza أَصۡطَفَى ٱلۡبَنَاتِ عَلَى ٱلۡبَنِينَ ١٥٣Kodi iye adasankha ana aakazi m’malo mwa ana aamuna مَا لَكُمۡ كَيۡفَ تَحۡكُمُونَ ١٥٤Kodi mwatani? Kodi mumaweruza bwanji أَفَلَا تَذَكَّرُونَ ١٥٥Kodi simungaganize bwino أَمۡ لَكُمۡ سُلۡطَٰنٌ مُّبِينٌ ١٥٦Kapena kodi inu muli ndi ulamuliro weniweni فَأۡتُواْ بِكِتَٰبِكُمۡ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ ١٥٧Kotero bweretsani Buku lanu ngati ndinu olungama وَجَعَلُواْ بَيۡنَهُۥ وَبَيۡنَ ٱلۡجِنَّةِ نَسَبًاۚ وَلَقَدۡ عَلِمَتِ ٱلۡجِنَّةُ إِنَّهُمۡ لَمُحۡضَرُونَ ١٥٨Ndipo iwo akhazikitsa ubale pakati pa Mulungu ndi majini. Koma majini amadziwa kuti iwo adzatengedwa kupita kwa Iye سُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ عَمَّا يَصِفُونَ ١٥٩Ulemerero ukhale kwa Mulungu. Iye ali pamwamba pa zimene amamuyerekeza nazo إِلَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ ١٦٠Kupatula akapolo a Mulungu, amene Iye amasankha فَإِنَّكُمۡ وَمَا تَعۡبُدُونَ ١٦١Ndithudi inu pamodzi ndi zimene mupembedza مَآ أَنتُمۡ عَلَيۡهِ بِفَٰتِنِينَ ١٦٢Simungathe kusocheza wina aliyense إِلَّا مَنۡ هُوَ صَالِ ٱلۡجَحِيمِ ١٦٣Kupatula okhawo amene adzapita ku moto wa ku Gahena وَمَا مِنَّآ إِلَّا لَهُۥ مَقَامٌ مَّعۡلُومٌ ١٦٤Aliyense wa Ife ali ndi malo ake ake وَإِنَّا لَنَحۡنُ ٱلصَّآفُّونَ ١٦٥Ndithudi ndife amene timaima pa mizere kupemphera وَإِنَّا لَنَحۡنُ ٱلۡمُسَبِّحُونَ ١٦٦Ndipo, ndithudi, ndife amene timamulemekeza وَإِن كَانُواْ لَيَقُولُونَ ١٦٧Ndipo, ndithudi, iwo anali kunena kuti لَوۡ أَنَّ عِندَنَا ذِكۡرًا مِّنَ ٱلۡأَوَّلِينَ ١٦٨“Tikadakhala ndi chikumbutso monga chomwe chinali ndi anthu akale.” لَكُنَّا عِبَادَ ٱللَّهِ ٱلۡمُخۡلَصِينَ ١٦٩“Ife, ndithudi, tidakhala akapolo osankhidwa a Mulungu.” فَكَفَرُواْ بِهِۦۖ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ ١٧٠Koma iwo sakhulupilira mu izi komabe iwo adzadziwa وَلَقَدۡ سَبَقَتۡ كَلِمَتُنَا لِعِبَادِنَا ٱلۡمُرۡسَلِينَ ١٧١Ndithudi mawu athu adatsogola kwa akapolo athu omwe ndi Atumwi athu إِنَّهُمۡ لَهُمُ ٱلۡمَنصُورُونَ ١٧٢Kuti iwo, ndithudi, adzathandizidwa وَإِنَّ جُندَنَا لَهُمُ ٱلۡغَٰلِبُونَ ١٧٣Ndipo, ndithudi, gulu lathu lokha lidzakhala lopambana فَتَوَلَّ عَنۡهُمۡ حَتَّىٰ حِينٍ ١٧٤Kotero uyambe wawasiya okha kwa kanthawi kochepa وَأَبۡصِرۡهُمۡ فَسَوۡفَ يُبۡصِرُونَ ١٧٥Ndipo uwaone ndipo iwo adzadzioneranso أَفَبِعَذَابِنَا يَسۡتَعۡجِلُونَ ١٧٦Kodi iwo afuna kufulumizitsa chilango chathu فَإِذَا نَزَلَ بِسَاحَتِهِمۡ فَسَآءَ صَبَاحُ ٱلۡمُنذَرِينَ ١٧٧Koma pamene icho chidzadza pa iwo, udzakhala m’mawa woipa kwa iwo amene adachenjezedwa وَتَوَلَّ عَنۡهُمۡ حَتَّىٰ حِينٍ ١٧٨Kotero uyambe wawasiya okha kwa kanthawi kochepa وَأَبۡصِرۡ فَسَوۡفَ يُبۡصِرُونَ ١٧٩Ndipo uwaone ndipo nawo adzaona سُبۡحَٰنَ رَبِّكَ رَبِّ ٱلۡعِزَّةِ عَمَّا يَصِفُونَ ١٨٠Ulemerero ukhale kwa Ambuye wako, Ambuye wolemekezeka ndi wamphamvu, kuposa zimene ali kumukundikira وَسَلَٰمٌ عَلَى ٱلۡمُرۡسَلِينَ ١٨١Ndipo mtendere ukhale kwa Atumwi onse وَٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ ١٨٢Ndipo kuyamikidwa ndi kuthokoza konse kukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse