بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
صٓۚ وَٱلۡقُرۡءَانِ ذِي ٱلذِّكۡرِ ١Suad. Pali Korani yodzadza ndi chikumbutso بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فِي عِزَّةٍ وَشِقَاقٍ ٢Iyayi! anthu osakhulupirira ali kungodzikundikira ndi kumangotsutsa كَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِن قَبۡلِهِم مِّن قَرۡنٍ فَنَادَواْ وَّلَاتَ حِينَ مَنَاصٍ ٣Kodi ndi mibadwo ingati imene Ife tidaononga iwo asanadze ndipo iyo idalira poona kuti padalibe nthawi yothawa وَعَجِبُوٓاْ أَن جَآءَهُم مُّنذِرٌ مِّنۡهُمۡۖ وَقَالَ ٱلۡكَٰفِرُونَ هَٰذَا سَٰحِرٌ كَذَّابٌ ٤Ndipo iwo ali kudabwa kuti Mtumwi wadza kwa iwo kuchokera pakati pawo. Ndipo anthu osakhulupirira amati, “Uyu ndi munthu wamatsenga ndiponso wabodza!” أَجَعَلَ ٱلۡأٓلِهَةَ إِلَٰهًا وَٰحِدًاۖ إِنَّ هَٰذَا لَشَيۡءٌ عُجَابٌ ٥“Kodi iye wapanga milungu yonse kukhala Mulungu mmodzi? Ndithudi ichi ndi chinthu chachilendo.” وَٱنطَلَقَ ٱلۡمَلَأُ مِنۡهُمۡ أَنِ ٱمۡشُواْ وَٱصۡبِرُواْ عَلَىٰٓ ءَالِهَتِكُمۡۖ إِنَّ هَٰذَا لَشَيۡءٌ يُرَادُ ٦Ndipo atsogoleri awo amachoka monyinyirika nati, “Pitirizani inu ndipo mudzipereke kwathunthu kwa milungu yanu! Ndithudi ichi ndi chinthu choti chikusokonezani.” مَا سَمِعۡنَا بِهَٰذَا فِي ٱلۡمِلَّةِ ٱلۡأٓخِرَةِ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا ٱخۡتِلَٰقٌ ٧“Ife sitidamvepo zimenezi pakati pa anthu akale. Ichi si china koma nkhani zopeka chabe.” أَءُنزِلَ عَلَيۡهِ ٱلذِّكۡرُ مِنۢ بَيۡنِنَاۚ بَلۡ هُمۡ فِي شَكٍّ مِّن ذِكۡرِيۚ بَل لَّمَّا يَذُوقُواْ عَذَابِ ٨“Kodi uthenga wavumbulutsidwa kwa iye yekha pakati pathu?” Iyayi! Koma iwo ali kukayika za uthenga wanga. Iyayi! Iwo sadalawepo chilango changa أَمۡ عِندَهُمۡ خَزَآئِنُ رَحۡمَةِ رَبِّكَ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡوَهَّابِ ٩Kapena iwo ndi nkhokwe za chifundo cha Ambuye wako, Mwini Mphamvu zonse, Mwini kupereka zabwino zonse أَمۡ لَهُم مُّلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَاۖ فَلۡيَرۡتَقُواْ فِي ٱلۡأَسۡبَٰبِ ١٠Kapena iwo ali ndi ulamuliro kumwamba ndi padziko ndi kuti zonse zimene zili m’menemo ndi zawo? Ngati nditero, alekeni iwo kuti akwere mothandizidwa جُندٌ مَّا هُنَالِكَ مَهۡزُومٌ مِّنَ ٱلۡأَحۡزَابِ ١١Iwo adzagonjetsedwa monga magulu akale كَذَّبَتۡ قَبۡلَهُمۡ قَوۡمُ نُوحٍ وَعَادٌ وَفِرۡعَوۡنُ ذُو ٱلۡأَوۡتَادِ ١٢Asanadze iwo, panali ena amene adakana Atumwi. Anthu a Nowa, a Aad, ndi a Farawo, mfumu ya zisonga وَثَمُودُ وَقَوۡمُ لُوطٍ وَأَصۡحَٰبُ لۡـَٔيۡكَةِۚ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلۡأَحۡزَابُ ١٣Thamoud ndi anthu a Loti ndi anthu okhala m’nkhalango, onsewa adali wothandizana إِن كُلٌّ إِلَّا كَذَّبَ ٱلرُّسُلَ فَحَقَّ عِقَابِ ١٤Panalibe mmodzi amene sadanene kuti Atumwi adali abodza, motero chilango changa chinali chowayenera وَمَا يَنظُرُ هَٰٓؤُلَآءِ إِلَّا صَيۡحَةً وَٰحِدَةً مَّا لَهَا مِن فَوَاقٍ ١٥Ndipo awa ali kungodikira kulira kumodzi kokha kumene kuchitike mosachedwa وَقَالُواْ رَبَّنَا عَجِّل لَّنَا قِطَّنَا قَبۡلَ يَوۡمِ ٱلۡحِسَابِ ١٦Iwo amati, “Ambuye wathu, bweretsani msanga kwa ife Buku la ntchito zathu ngakhale nthawi yake siinakwane.” ٱصۡبِرۡ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَٱذۡكُرۡ عَبۡدَنَا دَاوُۥدَ ذَا ٱلۡأَيۡدِۖ إِنَّهُۥٓ أَوَّابٌ ١٧Khala wopirira pa zimene ali kunena ndipo uzikumbukira kapolo wathu Davide, munthu wamphamvu. Ndithudi iye anali kulapa nthawi zonse إِنَّا سَخَّرۡنَا ٱلۡجِبَالَ مَعَهُۥ يُسَبِّحۡنَ بِٱلۡعَشِيِّ وَٱلۡإِشۡرَاقِ ١٨Ndithudi Ife tidauza mapiri kuti aziyimba pamodzi ndi iye mayamiko athu nthawi ya madzulo ndi m’mbandakucha وَٱلطَّيۡرَ مَحۡشُورَةًۖ كُلٌّ لَّهُۥٓ أَوَّابٌ ١٩Ndipo mbalame zidasonkhana, zonse pamodzi ndi iye zidalemekeza Mulungu وَشَدَدۡنَا مُلۡكَهُۥ وَءَاتَيۡنَٰهُ ٱلۡحِكۡمَةَ وَفَصۡلَ ٱلۡخِطَابِ ٢٠Tidalimbikitsa Ufumu wake ndipo tidamupatsa nzeru ndi kuweruza kwabwino m’manenedwe ndi m’chiweruzo ۞ وَهَلۡ أَتَىٰكَ نَبَؤُاْ ٱلۡخَصۡمِ إِذۡ تَسَوَّرُواْ ٱلۡمِحۡرَابَ ٢١Kodi nkhani ya anthu okangana yakupeza iwe? Pamene, iwo adakwera chipupa cha nyumba ndi kulowa mnyumba ya padera إِذۡ دَخَلُواْ عَلَىٰ دَاوُۥدَ فَفَزِعَ مِنۡهُمۡۖ قَالُواْ لَا تَخَفۡۖ خَصۡمَانِ بَغَىٰ بَعۡضُنَا عَلَىٰ بَعۡضٍ فَٱحۡكُم بَيۡنَنَا بِٱلۡحَقِّ وَلَا تُشۡطِطۡ وَٱهۡدِنَآ إِلَىٰ سَوَآءِ ٱلصِّرَٰطِ ٢٢Pamene adalowa kwa Davide, iye adachita mantha ndi iwo ndipo iwo adati, “Usaope. Ife ndife anthu okangana, ndipo wina wa ife wachimwira mnzake motero weruza mwachilungamo ndipo usatiweruze opanda chilungamo koma titsogolere ku njira yoyenera.” إِنَّ هَٰذَآ أَخِي لَهُۥ تِسۡعٌ وَتِسۡعُونَ نَعۡجَةً وَلِيَ نَعۡجَةٌ وَٰحِدَةٌ فَقَالَ أَكۡفِلۡنِيهَا وَعَزَّنِي فِي ٱلۡخِطَابِ ٢٣“Ndithudi uyu ndi m’bale wanga ndipo ali ndi nkhosa makumi asanu ndi anayi kudza mphambu zisanu ndi zinayi pamene ine ndili ndi nkhosa imodzi yokha basi. Komabe iye akuti, ‘Undipatse ine nkhosayo’ ndipo iye adandipambana mu zonena zake.” قَالَ لَقَدۡ ظَلَمَكَ بِسُؤَالِ نَعۡجَتِكَ إِلَىٰ نِعَاجِهِۦۖ وَإِنَّ كَثِيرًا مِّنَ ٱلۡخُلَطَآءِ لَيَبۡغِي بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٍ إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَقَلِيلٌ مَّا هُمۡۗ وَظَنَّ دَاوُۥدُ أَنَّمَا فَتَنَّٰهُ فَٱسۡتَغۡفَرَ رَبَّهُۥ وَخَرَّۤ رَاكِعًاۤ وَأَنَابَ ۩ ٢٤Iye adati, “Ndithudi iye wakulakwira kwambiri pokupempha kuti nkhosa yako imodzi yokha iperekedwe kwa iye kuonjezera pa zimene ali nazo.” Ndithudi anthu ambiri ochitira pamodzi malonda ndi amene akulakwirana wina ndi mnzake. Koma izi sizichitika ndi anthu amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino ndipo anthu otere ndi ochepa. Ndipo Davide adazindikira kuti Ife tidamuyesa iye ndipo adapempha chikhululukiro kwa Ambuye wake ndipo iye adagwa nagunditsa mphumi yake pansi ndi kudza molapa فَغَفَرۡنَا لَهُۥ ذَٰلِكَۖ وَإِنَّ لَهُۥ عِندَنَا لَزُلۡفَىٰ وَحُسۡنَ مَـَٔابٍ ٢٥Kotero Ife tidamukhululukira ndipo ndithudi adali kufupi ndi Ife ndipo ali ndi malo okongola pa nthawi yobwerera يَٰدَاوُۥدُ إِنَّا جَعَلۡنَٰكَ خَلِيفَةً فِي ٱلۡأَرۡضِ فَٱحۡكُم بَيۡنَ ٱلنَّاسِ بِٱلۡحَقِّ وَلَا تَتَّبِعِ ٱلۡهَوَىٰ فَيُضِلَّكَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ يَضِلُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ لَهُمۡ عَذَابٌ شَدِيدُۢ بِمَا نَسُواْ يَوۡمَ ٱلۡحِسَابِ ٢٦Iwe Davide! Ndithudi Ife takukhazika iwe kukhala Kazembe padziko lapansi motero weruza pakati pa anthu mwachilungamo, ndipo usatsatire zilakolako za mtima wako chifukwa zidzakusocheretsa ku njira ya Mulungu. Ndithudi iwo amene asochera ku njira ya Mulungu adzalangidwa kwambiri chifukwa iwo amaiwala za tsiku lachiweruzo وَمَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَآءَ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا بَٰطِلًاۚ ذَٰلِكَ ظَنُّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْۚ فَوَيۡلٌ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ مِنَ ٱلنَّارِ ٢٧Si kuti tidasowa chochita polenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’kati mwake! Amenewo adali maganizo a anthu osakhulupirira! Ndipo tsoka kwa anthu osakhulupirira lochokera ku moto أَمۡ نَجۡعَلُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ كَٱلۡمُفۡسِدِينَ فِي ٱلۡأَرۡضِ أَمۡ نَجۡعَلُ ٱلۡمُتَّقِينَ كَٱلۡفُجَّارِ ٢٨Kodi Ife tingasamale mofanana anthu okhulupirira ndi ochita ntchito zabwino ndi iwo amene amadzetsa chisokonezo pa dziko? Kapena Ife tingasamalire anthu amene amalewa zoipa chimodzimodzi ndi iwo amene amachita zoipa كِتَٰبٌ أَنزَلۡنَٰهُ إِلَيۡكَ مُبَٰرَكٌ لِّيَدَّبَّرُوٓاْ ءَايَٰتِهِۦ وَلِيَتَذَكَّرَ أُوْلُواْ ٱلۡأَلۡبَٰبِ ٢٩Ili ndi Buku limene Ife tatumiza kwa iwe, lodzala ndi madalitso kuti akhoza kuganiza mofatsa pa mavesi ake ndi kuti anthu ozindikira akhoza kukumbukira وَوَهَبۡنَا لِدَاوُۥدَ سُلَيۡمَٰنَۚ نِعۡمَ ٱلۡعَبۡدُ إِنَّهُۥٓ أَوَّابٌ ٣٠Kwa Davide Ife tidamupatsa Solomoni. Kapolo wabwino zedi! Ndithudi iye anali kudzalapa kwa Ife إِذۡ عُرِضَ عَلَيۡهِ بِٱلۡعَشِيِّ ٱلصَّٰفِنَٰتُ ٱلۡجِيَادُ ٣١Ndipo pamene adadza nazo kwa iye, nthawi ya madzulo, Hatchi zophunzitsidwa bwino zamphamvu ndi zoberekedwa bwino فَقَالَ إِنِّيٓ أَحۡبَبۡتُ حُبَّ ٱلۡخَيۡرِ عَن ذِكۡرِ رَبِّي حَتَّىٰ تَوَارَتۡ بِٱلۡحِجَابِ ٣٢Ndipo iye adati, “Ndithudi ine ndidakonda chuma kuposa kukumbukira Ambuye wanga. Mpaka pamene nthawi idatha ndipo dzuwa lidalowa mu mdima.” رُدُّوهَا عَلَيَّۖ فَطَفِقَ مَسۡحَۢا بِٱلسُّوقِ وَٱلۡأَعۡنَاقِ ٣٣Ndipo iye adati “Bweretsani mahatchi kwa ine.” Ndipo iye adayamba kuzisisita miyendo ndi makosi awo وَلَقَدۡ فَتَنَّا سُلَيۡمَٰنَ وَأَلۡقَيۡنَا عَلَىٰ كُرۡسِيِّهِۦ جَسَدًا ثُمَّ أَنَابَ ٣٤Ndipo, ndithudi, Ife tidamuyesa Solomoni ndipo Ife tidaika Satana pa mpando wake wachifumu koma iye adadza kwa Ife modzipereka ndi molapa قَالَ رَبِّ ٱغۡفِرۡ لِي وَهَبۡ لِي مُلۡكًا لَّا يَنۢبَغِي لِأَحَدٍ مِّنۢ بَعۡدِيٓۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡوَهَّابُ ٣٥Iye adati, “Ambuye wanga! Khululukireni ndipo ndipatseni ufumu umene simudzapatsanso wina pambuyo panga chifukwa inu mumapereka zokoma zanu mopanda muyeso.” فَسَخَّرۡنَا لَهُ ٱلرِّيحَ تَجۡرِي بِأَمۡرِهِۦ رُخَآءً حَيۡثُ أَصَابَ ٣٦Ndipo Ife tidamuchepetsera mphamvu yakuti mphepo imvere malamulo ake kuti iziyenda potsatira malamulo ake amene iye adalamula وَٱلشَّيَٰطِينَ كُلَّ بَنَّآءٍ وَغَوَّاصٍ ٣٧Ndiponso a Satana ochokera kwa majini ndi m’misiri aliyense womanga nyumba ndi wodziwa kusambira pa madzi وَءَاخَرِينَ مُقَرَّنِينَ فِي ٱلۡأَصۡفَادِ ٣٨Ndi ena omwe ndi omangidwa ku magoli هَٰذَا عَطَآؤُنَا فَٱمۡنُنۡ أَوۡ أَمۡسِكۡ بِغَيۡرِ حِسَابٍ ٣٩Iyi ndi mphatso yathu yaulere, kotero pereka mowolowa manja kapena kuisunga. Iwe siudzaimbidwa mlandu وَإِنَّ لَهُۥ عِندَنَا لَزُلۡفَىٰ وَحُسۡنَ مَـَٔابٍ ٤٠Ndipo ndithudi iye adali pafupi ndi Ife, ndi kubwera ku malo abwino وَٱذۡكُرۡ عَبۡدَنَآ أَيُّوبَ إِذۡ نَادَىٰ رَبَّهُۥٓ أَنِّي مَسَّنِيَ ٱلشَّيۡطَٰنُ بِنُصۡبٍ وَعَذَابٍ ٤١Ndipo kumbukira kapolo wathu Yobu pamene adapempha kwa Ambuye wake kuti, “Satana wandikundikira mavuto ndi masautso.” ٱرۡكُضۡ بِرِجۡلِكَۖ هَٰذَا مُغۡتَسَلُۢ بَارِدٌ وَشَرَابٌ ٤٢“Menya nthaka ndi phazi lako. Uyu ndi kasupe wa madzi oti usambe, ozizira ndi okoma pakumwa.” وَوَهَبۡنَا لَهُۥٓ أَهۡلَهُۥ وَمِثۡلَهُم مَّعَهُمۡ رَحۡمَةً مِّنَّا وَذِكۡرَىٰ لِأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ ٤٣Ndipo Ife tidamubwezera banja lake ndi kuonjezera chiwerengero chawo ngati chisomo chochokera kwa Ife ndiponso chikumbutso kwa anthu ozindikira وَخُذۡ بِيَدِكَ ضِغۡثًا فَٱضۡرِب بِّهِۦ وَلَا تَحۡنَثۡۗ إِنَّا وَجَدۡنَٰهُ صَابِرًاۚ نِّعۡمَ ٱلۡعَبۡدُ إِنَّهُۥٓ أَوَّابٌ ٤٤Ndipo nyamula m’manja mwako mtolo wa udzu ochepa ndipo mumenye nawo koma usaphwanye lonjezo lako. Ndithudi! Ife tidamupeza ali wopirira kwambiri ndi okhazikika. Ndithudi iye adali Mtumwi wabwino! Ndithudi iye anali kulapa nthawi zonse وَٱذۡكُرۡ عِبَٰدَنَآ إِبۡرَٰهِيمَ وَإِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَ أُوْلِي ٱلۡأَيۡدِي وَٱلۡأَبۡصَٰرِ ٤٥Ndipo kumbukira akapolo athu Abrahamu, Isake, Yakobo ameneadaliodzalandimphamvundiponsoomvetsa zinthu za chipembedzo إِنَّآ أَخۡلَصۡنَٰهُم بِخَالِصَةٍ ذِكۡرَى ٱلدَّارِ ٤٦Ndithudi tidawasankha iwo ndi kuwapatsa chikumbumtima chamoyo umene uli nkudza وَإِنَّهُمۡ عِندَنَا لَمِنَ ٱلۡمُصۡطَفَيۡنَ ٱلۡأَخۡيَارِ ٤٧Ndipo iwo timawaona. Ndithudi ali m’gulu la anthu odziwika ndi abwino وَٱذۡكُرۡ إِسۡمَٰعِيلَ وَٱلۡيَسَعَ وَذَا ٱلۡكِفۡلِۖ وَكُلٌّ مِّنَ ٱلۡأَخۡيَارِ ٤٨Ndipo kumbukira Ishimayeli, Elisa, ndi Dhul-Kifl onse adali m’gulu la anthu ochita zabwino هَٰذَا ذِكۡرٌۚ وَإِنَّ لِلۡمُتَّقِينَ لَحُسۡنَ مَـَٔابٍ ٤٩Ichi ndi chikumbutso, ndithudi, kwa anthu olungama awo ndi malo abwino جَنَّٰتِ عَدۡنٍ مُّفَتَّحَةً لَّهُمُ ٱلۡأَبۡوَٰبُ ٥٠Minda yosatha imene makomo ake adzakhalaotsekulidwakwaiwonthawizonse مُتَّكِـِٔينَ فِيهَا يَدۡعُونَ فِيهَا بِفَٰكِهَةٍ كَثِيرَةٍ وَشَرَابٍ ٥١M’menemo iwo adzakhala mwamtendere ndiponso m’menemo iwo adzaitanitsa zipatso zochuluka ndi zakumwa zokoma ۞ وَعِندَهُمۡ قَٰصِرَٰتُ ٱلطَّرۡفِ أَتۡرَابٌ ٥٢Ndipo pambali pawo padzakhala a namwali angwiro ongoyang’ana maso awo pa amuna ofanana nawo zaka هَٰذَا مَا تُوعَدُونَ لِيَوۡمِ ٱلۡحِسَابِ ٥٣Limeneli ndi lonjezo limene lapatsidwa kwa inu lokhudza tsiku lachiweruzo إِنَّ هَٰذَا لَرِزۡقُنَا مَا لَهُۥ مِن نَّفَادٍ ٥٤Ndithudi zimenezi ndi zokoma zathu kwa inu ndipo sizidzatha ayi هَٰذَاۚ وَإِنَّ لِلطَّٰغِينَ لَشَرَّ مَـَٔابٍ ٥٥Izi zili choncho. Ndipo zoonadi anthu ochita zoipa adzakhala ku malo oipa kupitako جَهَنَّمَ يَصۡلَوۡنَهَا فَبِئۡسَ ٱلۡمِهَادُ ٥٦Gahena! Ndi kumene iwo adzalowa ndipo ndi malo oipa kukhalamo هَٰذَا فَلۡيَذُوقُوهُ حَمِيمٌ وَغَسَّاقٌ ٥٧Izi zili choncho! Kotero alekeni iwo alawe madzi owira ndi mafinya وَءَاخَرُ مِن شَكۡلِهِۦٓ أَزۡوَٰجٌ ٥٨Ndi zilango zina zofanana zawo ndi zina zosiyanasiyana هَٰذَا فَوۡجٌ مُّقۡتَحِمٌ مَّعَكُمۡ لَا مَرۡحَبَۢا بِهِمۡۚ إِنَّهُمۡ صَالُواْ ٱلنَّارِ ٥٩Ili ndi gulu la nkhondo limene lili kulowa ndi inu! Palibe kulandiridwa kwabwino kwa iwo! Ndithudi iwo adzalowa kumoto قَالُواْ بَلۡ أَنتُمۡ لَا مَرۡحَبَۢا بِكُمۡۖ أَنتُمۡ قَدَّمۡتُمُوهُ لَنَاۖ فَبِئۡسَ ٱلۡقَرَارُ ٦٠Iwo adzati, “Iyayi! Inunso. Simulandiridwa ayi. Ndinu amene mudatinyenga ife, kotero awa ndiwo malo oipa kwambiri kukhalako.” قَالُواْ رَبَّنَا مَن قَدَّمَ لَنَا هَٰذَا فَزِدۡهُ عَذَابًا ضِعۡفًا فِي ٱلنَّارِ ٦١Iwo adzati, “Ambuye wathu! Aliyense amene adachititsa kuti zimenezi zidze kwa ife muonjezereni kawiri chilango chake cha kumoto.” وَقَالُواْ مَا لَنَا لَا نَرَىٰ رِجَالًا كُنَّا نَعُدُّهُم مِّنَ ٱلۡأَشۡرَارِ ٦٢Ndipo iwo adzati, “Kodi zachitika bwanji kuti ife sitili kuona anthu amene tinkawawerenga pakati pa anthu ochita choipa?” أَتَّخَذۡنَٰهُمۡ سِخۡرِيًّا أَمۡ زَاغَتۡ عَنۡهُمُ ٱلۡأَبۡصَٰرُ ٦٣Kodi ife timangowanyoza kapena maso athu alephera kuwaona bwinobwino إِنَّ ذَٰلِكَ لَحَقٌّ تَخَاصُمُ أَهۡلِ ٱلنَّارِ ٦٤Ndithudi zimenezi ndi zoona. Zokangana za anthu a ku moto قُلۡ إِنَّمَآ أَنَا۠ مُنذِرٌۖ وَمَا مِنۡ إِلَٰهٍ إِلَّا ٱللَّهُ ٱلۡوَٰحِدُ ٱلۡقَهَّارُ ٦٥Nena, “Ndithudi ine ndine mchenjezi basi ndipo kulibe mulungu wina koma Mulungu mmodzi yekha, wopambama ndi wofunika.” رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡغَفَّٰرُ ٦٦“Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo. Iye ndi wamphamvu zambiri ndi wokhululukira nthawi zonse.” قُلۡ هُوَ نَبَؤٌاْ عَظِيمٌ ٦٧Nena, “Uwu ndi uthenga wofunika kwambiri.” أَنتُمۡ عَنۡهُ مُعۡرِضُونَ ٦٨“Umeneinumulikuukana.” مَا كَانَ لِيَ مِنۡ عِلۡمِۭ بِٱلۡمَلَإِ ٱلۡأَعۡلَىٰٓ إِذۡ يَخۡتَصِمُونَ ٦٩“Inesindidziwazamafumu olemekezeka pamene amatsutsana ndi kukambirana.” إِن يُوحَىٰٓ إِلَيَّ إِلَّآ أَنَّمَآ أَنَا۠ نَذِيرٌ مُّبِينٌ ٧٠“Koma akuti ichi chavumbulutsidwa kwa ine kuti ndine opereka chenjezo lomveka ndiponso poyera.” إِذۡ قَالَ رَبُّكَ لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِنِّي خَٰلِقُۢ بَشَرًا مِّن طِينٍ ٧١Ndipo pamene Ambuye wako adati kwa Angelo, “Ndithudi Ine ndidzalenga munthu kuchokera ku dothi.” فَإِذَا سَوَّيۡتُهُۥ وَنَفَخۡتُ فِيهِ مِن رُّوحِي فَقَعُواْ لَهُۥ سَٰجِدِينَ ٧٢Ndipo ndikatha kumulenga iye ndi kumupumira mzimu wanga kotero igwani nonse ndi kumulambira iye فَسَجَدَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ كُلُّهُمۡ أَجۡمَعُونَ ٧٣Kotero Angelo onse pamodzi adamulambira إِلَّآ إِبۡلِيسَ ٱسۡتَكۡبَرَ وَكَانَ مِنَ ٱلۡكَٰفِرِينَ ٧٤Kupatula Satana, iye anali ndi mwano ndipo iye anali mmodzi wa osakhulupirira قَالَ يَٰٓإِبۡلِيسُ مَا مَنَعَكَ أَن تَسۡجُدَ لِمَا خَلَقۡتُ بِيَدَيَّۖ أَسۡتَكۡبَرۡتَ أَمۡ كُنتَ مِنَ ٱلۡعَالِينَ ٧٥Mulungu adati, “Iwe Satana! Chakuletsa ndi chiyani kulambira munthu amene ndalenga ndi manja anga? Kodi ndiwe wamwano? Kodi kapena iwe ndiwe mmodzi wa apamwamba?” قَالَ أَنَا۠ خَيۡرٌ مِّنۡهُ خَلَقۡتَنِي مِن نَّارٍ وَخَلَقۡتَهُۥ مِن طِينٍ ٧٦Iye adati, “Ine ndine wopambana kuposa iye. Inu mudandilenga ine kuchokera kumoto pamene iye mudamulenga kuchokera ku dothi.” قَالَ فَٱخۡرُجۡ مِنۡهَا فَإِنَّكَ رَجِيمٌ ٧٧Mulungu adati, “Kotero choka pamaso panga chifukwa iwe ndiwe okanidwa ndi otembereredwa.” وَإِنَّ عَلَيۡكَ لَعۡنَتِيٓ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلدِّينِ ٧٨“Ndipo ndithudi matemberero anga adzakhala pa iwe mpaka pa tsiku lachiweruzo.” قَالَ رَبِّ فَأَنظِرۡنِيٓ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ ٧٩Satana adati, “Ambuye wanga! Ndipatseni mpata mpaka patsiku louka kwa akufa.” قَالَ فَإِنَّكَ مِنَ ٱلۡمُنظَرِينَ ٨٠Mulungu adati, “Mpata waperekedwa kwa iwe.” إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡوَقۡتِ ٱلۡمَعۡلُومِ ٨١“Mpaka pa nthawi yomwe idakhazikitsidwa.” قَالَ فَبِعِزَّتِكَ لَأُغۡوِيَنَّهُمۡ أَجۡمَعِينَ ٨٢Satana adati, “Kotero kudzera ku mphamvu zanu, ine ndidzawasocheretsa.” إِلَّا عِبَادَكَ مِنۡهُمُ ٱلۡمُخۡلَصِينَ ٨٣“Kupatula akapolo anu osankhidwa amene ali pakati pawo.” قَالَ فَٱلۡحَقُّ وَٱلۡحَقَّ أَقُولُ ٨٤Mulungu adati, “Ichi ndi choonadi ndipo choonadi ndicho chimene ndimanena.” لَأَمۡلَأَنَّ جَهَنَّمَ مِنكَ وَمِمَّن تَبِعَكَ مِنۡهُمۡ أَجۡمَعِينَ ٨٥“Kuti ndidzadzadza Gahena ndi iwe ndiponso onse amene amakutsatira iwe.” قُلۡ مَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٍ وَمَآ أَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُتَكَلِّفِينَ ٨٦Nena “Ine sindili kukufunsani malipiro chifukwa cha ichi ndiponso ine sindine wodziyenereza.” إِنۡ هُوَ إِلَّا ذِكۡرٌ لِّلۡعَٰلَمِينَ ٨٧“Ichi si china koma chikumbutso kwa anthu a mitundu yonse.” وَلَتَعۡلَمُنَّ نَبَأَهُۥ بَعۡدَ حِينِۭ ٨٨“Ndithudi nonse mudzadziwa choonadi chake nthawi ina.”