ملة الإسلام

السورة 104 · 9 آية · Khaled Ibrahim Betala

سورة الهمزة باللغة الشيشيوا

السورة بالعربية مع التفسير استمع إلى سورة الهمزة (1,287 قارئاً)
مكيةسورة الهمزة٩ آية

بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ

وَيۡلٌ لِّكُلِّ هُمَزَةٍ لُّمَزَةٍ ١“Kuonongeka koopsa kudzampeza aliyense wojeda ndi wonyoza anthu polozera (ndi maso kapena kuyankhula ndi lirime) ٱلَّذِي جَمَعَ مَالًا وَعَدَّدَهُۥ ٢“Yemwe wasonkhanitsa chuma ndikumachiwerengera يَحۡسَبُ أَنَّ مَالَهُۥٓ أَخۡلَدَهُۥ ٣“Akuganiza kuti chuma chakecho chimkhazika (pa dziko) nthawi yaitali (ndikumteteza ku zimene sakuzifuna) كـَلَّاۖ لَيُنۢبَذَنَّ فِي ٱلۡحُطَمَةِ ٤“Sichoncho! (Asiye maganizo amenewo) ndithudi, akaponyedwa ku Moto woononga (chifukwa cha kuipa kwa zochita zake) وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا ٱلۡحُطَمَةُ ٥“Ndi chiyani chingakudziwitse za Moto woonongawu نَارُ ٱللَّهِ ٱلۡمُوقَدَةُ ٦“Umenewu ndi Moto wa Allah woyaka (nthawi zonse, woononga chilichonse choponyedwa mmenemo) ٱلَّتِي تَطَّلِعُ عَلَى ٱلۡأَفۡـِٔدَةِ ٧“Umene umakwera mpaka ku mtima إِنَّهَا عَلَيۡهِم مُّؤۡصَدَةٌ ٨“Ndithu motowo ukawazinga (ndi kuwatsekera makomo) فِي عَمَدٍ مُّمَدَّدَةِۭ ٩“Munsanamira za zitalizitali (kotero kuti sakatha kugwedezeka mmenemo kapena kupulumuka)

الترجمة: Khaled Ibrahim Betala.